Kodi Kumvera Kuli Koyenera Nthaŵi Zonse?
“KODI wandimva?” amayi afuula kwa Johnnie wachichepere pamene iye akutuluka panja pa chitseko. Ayi, iwo sakufufuza kumva kwa Johnnie. Iwo akutsimikizira kuti iye adzawamvera iwo ndi kubwera panyumba panthaŵi yoyenera.
Ndithudi, kumva ndi kumvera ziri zogwirizana mwathithithi. Sichiri chodabwitsa, chotero, kuti m’zinenero zoyambirira za Baibulo, mawu osonyeza kumvera anali kugwirizana ndi kumva. Koma ndi kwa ndani kumene tiyenera kupereka khutu lomvetsera? Kodi tiyenera kupereka kumvera kwa aliyense yemwe akafuna iko? Ndipo kodi kumvera kuli koyenera nthaŵi zonse?
Pamene Kumvera kuli Koyenera
Kumvera kwa Mlengi wathu, Yehova Mulungu, nthaŵi zonse kuli koyenera. Monga Mpangi wathu ndi Magwero a moyo, iye ali ndi chifuno choyambirira cha kumvera kwa zolengedwa zake. (Masalmo 95:6, 7) Monga Wolamulira Wamkulukulu, Yehova amaperekanso ulamuliro wake kwa ena omwe amakwaniritsa miyezo yake, ndipo ichi chimapangitsa kumvera kwathu kwa iwo kukhala koyenerera. Yemwe ali patsogolo kwambiri pakati pa anthu oterewo ali Yesu Kristu. Kuyambira 1914 iye wakhala Mfumu yoikidwa ya Mulungu ya Ufumu wa kumwamba “kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu ndi anthu amanenedwe onse, amtumikire.” (Danieli 7:13, 14) M’kuwonjezerapo, monga Mutu wa mpingo Wachikristu, Yesu wapereka ulamuliro kwa ena mmenemo, kupanga kumvera kwathu kwa abusa ochepera amenewo kuli koyenerera.—Ahebri 13:17.
Yehova wakhazikitsanso malamulo m’chigwirizano ndi nkhani ya kumvera mkati mwa banja. Ana akuchenjezedwa ‘kukhala omvera kwa makolo awo m’chigwirizano ndi Ambuye,’ ndipo akazi akuuzidwa kukhala “ogonjera kwa amuna awo monga Ambuye.” (Aefeso 5:21–6:3) Akristu amakumbutsidwanso “kugonjera kwa akulu ndi aulamuliro.” (Tito 3:1) Mu zonsezi, ngakhale kuli tero, kodi kumvera kwathu kufunikira kukhala kotheratu? Kodi kuli koyenera nthaŵi zonse?
Pamene Kumvera Sikuli Koyenera
Ndithudi, kumvetsera kwa awo omwe sanapatsidwe ulamuliro kuchokera kwa Yehova kungatulukepo m’tsoka. Mwamuna woyambirira, Adamu, “anamvetsera” kwa liwu la Hava ndi kugwirizana naye m’kudya kuchokera ku mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa. (Genesis 3:17) Nchiyani chimene chinali chotulukapo chake? “Pakuti monga mwa kusamvera kwa munthu mmodzi ambiri anayesedwa ochimwa.” (Aroma 5:19) Ndi chotulukapo chochititsa tsoka chotani kumvetsera kwa munthu wolakwika.
Kodi nthaŵi zonse chimakhala choyenera, ngakhale kuli tero, kumvetsera kwa awo omwe apatsidwa malo aulamuliro? Osati ngati iwo akuyesera kugwiritsira ntchito ulamuliro wawo m’njira yosakhala yaumulungu. Mwachitsanzo, m’chigwirizano ndi prinsipulo la kumvera “ambuye m’lingaliro la kuthupi,” tiyenera kukhala omvera kwa otilemba ntchito athu. Koma bwanji ngati oterowo atilamulira ife kuchita chinachake chotsutsana ndi malamulo a Mulungu wamphamvuyonse? Chimene Paulo ananena potsatira chimasonyeza njira yoyenera: “Si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima.” (Aefeso 6:5, 6) Pa chochitika china, Petro ndi atumwi ena ananena kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”—Machitidwe 5:29.
Prinsipulo lofananalo limagwira ntchito mkati mwa banja. Mosayamikira zifuno zaumulungu, mwamuna wake sangavomereze za chikhumbo cha mkazi wake kupezeka pa misonkhano ya Chikristu mokhazikika. Tangoyerekezani kuti iye anaika chitsenderezo pa iye, ngakhale kufikira ku chiŵaŵa, monga mmene zimakhalira nthaŵi zina, kumletsa iye kupita ku misonkhano ya Chikristu. Nchiyani chimene iye akayenera kuchita? Ngati iye akafunikira kusiya, iye angaike m’tsoka uzimu wake, limodzinso ndi uja wa banja lake, ndi kutaya chiyembekezo cha moyo wosatha. Kodi sichikakhala chabwinopo kumvera Yehova, akumazindikira kuti palibe munthu, osati ngakhale mwamuna wake, amene wapatsidwa ulamuliro wa kupyola lamulo la ‘osaleka kusonkhana kwathu pamodzi’?—Ahebri 10:25.
Mwamuna wa Miyoko anatsutsa kuti ndalama zake zinali “kuwonongedwa” mwa kupezekapo kwake pa misonkhano imene iye sanavomereze. Potsirizira pake, iye analeka kupereka ndalama za panyumba, ndipo Miyoko anayenera kuyenda mtunda wa ora limodzi kupita ku Nyumba ya Ufumu.
Kodi iye anagonjera? Ayi. Iye anafikira Yehova m’pemphero ndi kulinganiza mkhalidwe wake. Akumazindikira chifukwa cha chitsutso cha mwamuna wake, Miyoko analingalira kutenga ntchito yopereka manyuzipepala. Mwamuna wake anavomereza, kokha ngati iye adzamupatsako theka la malipiro ake.
Kachiŵirinso, iye anapemphera kuti ngati chiri chifuno cha Yehova, iye apatsidwe njira ya pafupipo. Kaŵirikaŵiri, chimatenga chaka kapena kuposerapo kupeza chimene munthu afuna. Koma, modabwitsa, mkati mwa milungu isanu ndi umodzi Miyoko anapatsidwa njira pafupi ndi nyumba yake. Wolimbikitsidwa ndi lingaliro lakuti Yehova anamva mapemphero ake, iye anagwira ntchito kuyambira 4:30 mpaka 6:00 m’mawa uliwonse. Mwakuwona ichi, mkhalidwe wa mwamuna wake pang’onopang’ono unasitha, ndipo anakhala wogwirizana. Monga mmene zikuchitikira kwa Miyoko, yemwe mokhazikika amatumikira monga mpainiya wothandizira, kulingalira ndi kulinganiza mikhalidwe yake, kupemphera ponena za icho ndipo kenaka kugwirirapo ntchito motsimikizirika, inu nanunso mudzapeza kuti ichi chidzatulukapo dalitso la Yehova.
Ndithudi, pangakhale zifukwa zapadera kaamba ka zimene mwamuna wosakhulupirira angafunsire mkazi wake kuphonya msonkhano Wachikristu. Iye angachite ichi popanda cholinga cha kunyalanyaza kulambira kwake ndi utumiki kwa Yehova Mulungu. Kumvetsetsa maprinsipulo ophatikizidwa kudzathandiza mkazi Wachikristu kugamulapo molondola mogwirizana ndi mkhalidwe wake wapadera.
Kutenga nkhaniyo patsogolo pang’ono, bwanji ngati mwamuna wake amletsa iye kuti sayenera kutenga ana awo ku misonkhano ya Chikristu? Iye akudziŵa, ndithudi, kuti ngakhale kuti mwamuna wake savomereza umutu wa Kristu, iye ali mutu wa banjalo. (1 Akorinto 11:3) Ndipo komabe, iyenso amasunga mu mtima ubwino wauzimu wa ana ake, limodzinso ndi chikhumbo chake cha kukhala womvera kwa Yehova. Icho ndithudi chiri chiyeso cha chikhulupiriro chake kukhalilira ku mathayo ake m’mbali zonsezi. Kupemphera kwa Yehova kaamba ka nzeru ndi kuzindikira ndithudi kudzathandiza. (Yakobo 1:5; Afilipi 4:6, 7) Mwaluntha kulingalira ndi mwamuna wake ndi kulankhula mwachikondi, kusonyeza mzimu wofatsa ndi wodzichepetsa, kungathandizenso kuthetsa tsokalo.—Akolose 4:6; 1 Petro 3:1-5.
Mkazi Wachikristu mu Yamato, Japan, anayang’anizana ndi mkhalidwe woterowo pamene mwamuna wake anamletsa iye kutenga ana awo atatu ku misonkhano. Nchiyani chimene iye akanachita? Iye mwaluntha anaphunzitsa ana ake kunyumba, ndipo pamene iwo anali a akulu kupanga zosankha zawo, aliyense anatenga kaimidwe kaamba ka Yehova ndi kuyamba kupezekapo pa misonkhano. Atakwiitsidwa, mwamunayo anawathamangitsa iwo onse m’nyumba yake.
Mkaziyo anapeza ntchito ndi kukhala kwa kanthaŵi m’nyumba ya mlongo. Koma iye sanaisiire nkhaniyo pamenepo. Iye ankabwereranso kukakonza nyumba ya mwamunayo ndi kuphika zakudya zake. Pomalizira, pambuyo pa mwezi umodzi kapena kuposerapo, mwamunayo anawatenganso iwo ndi kuleka kuwatsutsa iwo. Inali mphoto yotani nanga kaamba ka njira yake yokhulupirika!
“Yesani Mawu Ouziridwa”
Bwanji ponena za ulamuliro mu mpingo Wachikristu? Popeza awo amene ali m’malo amathayo ali oikidwa ndi kugwira ntchito kwa mzimu woyera ndipo iwo amazika uphungu wawo ndi chenjezo pa Mawu a Mulungu, tingakhale otsimikizira kuti kumvera ulamuliro woikidwa mu mpingo Wachikristu kuli koyenera. (Machitidwe 20:28; Ahebri 13:17) Koma sichitanthauza kuti timamvera ulamuliro woterowo popanda kupereka lingaliro ku chimene chanenedwa. Nchifukwa ninji?
Mtumwi Yohane anapereka uphunguwu: “Musakhulupirira mawu onse ouziridwa, koma yesani mawu ouziridwa kuwona ngati achokera kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1, NW) Ichi sichitanthauza kuti tiyenera kukaikira mawu onse amene ena atiuza. M’malomwake, timasunga m’malingaliro mawu a Paulo pa Agalatiya 1:8: “Koma ngakhale ife, kapena mngelo wochokera kumwamba, ngati akakulalikireni uthenga wabwino wosati umene takulalikirani ife, akhale wotembereredwa.”
Kodi chidziŵitso chimene chiri pamaso pathu chiri chosiyana ndi chimene taphunzitsidwa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? Kodi munthu wobukitsa uthenga umenewo akulankhula kulemekeza dzina la Yehova, kapena kodi iye akuyesera kudzikweza iyemwini? Kodi chidziŵitsocho chiri m’chigwirizano ndi ziphunzitso zonse za Baibulo? Awa ndi mafunso amene adzatithandiza ife ‘m’kuyesa’ chirichonse chimene chingamveke chokaikirika. Tikuchenjezedwa “kutsimikizira zinthu zonse; kugwiritsitsa ku chimene chiri chabwino.”—Mateyu 24:45; 1 Atesalonika 5:21.
Nkhani yosangalatsa m’nsongayi iri ija ya Woweruza Gideoni. Kuti atsimikizire kuti Yehova akakhala naye, Gideoni anapereka chiyeso: “Tawonani, ndidzaika chikopa cha ubweya popunthira tirigu,” iye anauza Yehova. “Pakakhala mame pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pouma, pamenepo ndidzadziŵa kuti mudzapulumutsa Israyeli ndi dzanja langa.” Pamene Yehova anapangitsa icho kuchitika monga mmene anafunsira, Gideoni anafuna chitsimikiziro chowonjezereka: “Paume pachikopa pokha, ndi panthaka ponse pakhale mame.”—Oweruza 6:37-39.
Kodi Gideoni anali wonkitsa ndi kuchenjera kapena wokaikira mopambanitsa? Mwachiwonekere ayi, chifukwa Yehova anavomereza pempho lake nthaŵi zonse ziŵiri ndipo anachita monga momwe anafunsira. Gideoni anafuna kutsimikizira kuyenera kwa mkhalidwe wake. Popeza analibe Mawu olembedwa a Mulungu monga mmene tiri nawo ife, imeneyo inali njira yokha yokhutiritsa ya Gideoni ya “kutsimikizira.” Komabe, pamene iye analandira chitsimikizirocho, iye anapereka chimvero chosamalitsa ku malamulo ochokera kwa Yehova ngakhale kuti kupereka amuna 300 molimbana ndi gulu la adani la 135,000 kukanawoneka monga kudzipha kuchokera pakawonedwe ka munthu. (Oweruza 7:7; 8:10) Kodi timasonyeza mkhalidwe wofananawo mwa kufufuza m’Mawu a Mulungu kaamba ka chimene kwenikweni chiri chifuno cha Yehova ndipo kenaka kumamatira ku icho?
Chosankha Chanzeru Koposa
Yehova samatiyembekezera ife kusonyeza kukhulupirira kwa khungu. Iye samafuna kuchokera kwa ife mtundu wa chimvero chimene wophunzitsa amachipeza kuchokera kwa nyama mwa chomangira chapamutu kapena mkwapulo. Chimenecho ndicho chifukwa chake iye anauza Davide: “Musakhale monga kavalo kapena ngati buru, wopanda nzeru. Zomangira zawo ndizo cham’kamwa ndi chapamutu zakuwakokera.” (Masalmo 32:9) M’malomwake, Yehova watipatsa ife kuthekera kwa kuganizira ndi kulingalira kotero kuti, kutazikidwa pa kumvetsetsa, tingasankhe kumvera iye.
Mu chiJapanese, liwu lakuti kiku (kumva) limaphatikiza tanthauzo osati kokha la kumvetsera ndi kumvera komanso la kugamulapo kuti kaya chinthucho chiri chabwino kapena choipa. Pamene winawake alankhula kwa ife, chiri chabwino kumvetsera m’lingaliro limeneli kotero kuti pamene timvera, tichite tero osati kokha mwa kumvera koma mwa kusankha. Pamene Atate wathu wa kumwamba, Yehova Mulungu, alankhula, kaya kupyolera mwa Mawu ake, Baibulo, kapena kupyolera m’gulu lake la padziko lapansi, chiri chofunika kwambiri kwa ife kumvetsera ndi kumvera, mwakutero kutsimikizira kuti tiri alambiri omvera omwe sanyalanyaza chikumbutso cha chikondi: “Kodi unandimva?”
[Chithunzi patsamba 29]
Ndi kwandani kumene tiyenera kumvetsera?
[Chithunzi patsamba 31]
Gideoni anafufuza chifuno cha Yehova ndi kum’mvera iye