Pitirizanibe Kukhala Ndimoyo Monga Ana a Mulungu
“Yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.”—1 Yohane 3:10.
1, 2. Pamene tikupitirizabe kuphunzira Yohane Woyamba, kodi ndiuphungu wotani wamtumwiyo umene tidzapenda?
YEHOVA ali ndi banja lachilengedwe chonse, ndipo anthu ena tsopano ali mbali yake. Iwo ali ana a Mulungu. Koma kodi iwo amasiyana motani ndi ena?
2 M’kalata yake yoyamba youziridwa ndi Mulungu, Mtumwi Yohane akusonyeza anthu oyanjidwa kwambiri amenewa. Iye akuperekanso uphungu umene umawathandiza kupitirizabe kukhala ndi moyo monga ana a Mulungu. Ndipo zimene anena zidzapindulitsa Mboni zodzipatulira zonse za Yehova.
Chikondi cha Mulungu Nchachikulu Chotani!
3. Kodi ndimotani mmene ena apangidwira kukhala “ana a Mulungu” ndipo kodi dziko limawawona motani?
3 Yohane akutchula chiyembekezo cha Akristu odzozedwa. (Werengani 1 Yohane 3: 1-3.) Nchikondi chachikulu chotani nanga chimene Yehova wasonyeza mwa kuwalandira iwo monga ana auzimu, kuwapanga kukhala “ana a Mulungu”! (Aroma 5:8-10) Mzimu wawo waumulungu, zonulirapo zawo, ndi ziyembekezo nzosadziwika ndi “dziko”—chimangidwe cha anthu osalungama. Chimangidwe chaudziko chotero chimada Kristu ndi otsatira ake ndipo chotero Atate yemwe. (Yohane 15:17-25) Chotero dziko lingadziwe odzozedwawo monga anthu koma osati monga ana a Mulungu chifukwa chakuti ‘silinafikire pa kudziwa’ Yehova.—1 Akorinto 2:14.
4. Kodi nchiyani chimene aliyense wokhala ndi chiyembekezo chakumwamba ayenera kuchita?
4 Pakali pano, odzozedwawo ali ana a Mulungu. ‘Koma,’ akutero Yohane, “sichinawoneke chimene tidzakhala” pambuyo pa kufa m’kukhulupirika ndi kuukitsidwira ku moyo wakumwamba ndi matupi auzimu. (Afilipi 3: 20, 21) Komabe, pamene Mulungu ‘awoneka,’ iwo adzakhala “ofanana ndi iye” ndipo ‘adzamuwona iye monga momwe ali,’ monga “Yehova Mzimuyo.” (2 Akorinto 3:17, 18) Aliyense wokhala ndi “chiyembekezo ichi” cha moyo ayenera kusonkhezeredwa kudziyeretsa “monga iyeyu [Yehova] ali woyera. Ngakhale kuti odzozedwawo tsopano ali opanda ungwiro, ayenera kukhala ndi moyo mwanjira imene iri yogwirizana ndi chiyembekezo chawo cha kuwona Mulungu wangwiro, woyera m’gawo lakumwamba.—Salmo 99:5, 9; 2 Akorinto 7:1.
Kusonyeza Chilungamo
5, 6. Kodi munthu aliyense wochita uchimo mwachizolowezi akuchitanji pamaso pa Mulungu, koma pamfundoyi, kodi nchiyani chimene chiri chowona ponena za otsalawo “ogwirizana” ndi Yesu Kristu?
5 Kukhala ndi moyo monga ana a Mulungu kumatanthauzanso kuchita chilungamo. (Werengani 1 Yohane 3:4, 5.) “Yense wakuchita tchimo achitanso kusayeruzika” m’maso mwa Yehova, amene malamulo ake amaswedwa ndi wochimwayo. (Yesaya 33:22; Yakobo 4:12) ‘Tchimo lonse ndilo kusayeruzika,’ kuswedwa kwa malamulo a Mulungu. Kuchita chizolowezi chauchimo kuli kosiyana ndi mzimu Wachikristu, ndipo tiri okondwera kuti Yesu Kristu “anawonekera” monga munthu “kuchotsa machimo athu.” Popeza kuti ‘mwa iye mulibe uchimo,’ anali wokhoza kupereka kwa Mulungu nsembe yochotsa machimo yokhutiritsa kotheratu.—Yesaya 53:11, 12; Ahebri 7: 26-28; 1 Petro 2:22-25.
6 “Yense wakukhala mwa iye [Mwanayo] sachimwa.” (Werengani 1 Yohane 3:6.) Pokhala opanda ungwiro, ife nthawi zina tingachimwe. Koma kuchimwa sindiko chizolowezi kwa awo amene ali m’chigwirizano ndi Mwanayo ndipo mwakutero ogwirizana ndi Atate. Ozolowera kuchita uchimo “sanawone” Yesu ndi diso lachikhulupiriro; ndiponso ochimwa dala otero monga ampatuko ‘samadziwa’ ndi kuzindikira Kristu monga “Mwanawankhosa wa Mulungu” wotetezera uchimo.—Yohane 1:36.
7, 8. Mogwirizana ndi kunena kwa 1 Yohane 3: 7, 8, kodi wozolowera kuchita uchimo dala amachokera kwayani, koma Mwana wa Mulungu “anasonyezedwa” kudzachita chiyani pamfundoyi?
7 Yohane Akuchenjeza motsutsana ndi kusokeretsedwa. (Werengani 1 Yohane 3:7, 8.) “Munthu asasokeretse inu,” akutero mtumwiyo, akuwonjezera kuti: “Iye wakuchita cholungama [mwa kusunga chilamulo cha Mulungu] ali wolungama, monga iyeyu [Yesu Kristu] ali wolungama.” Mkhalidwe wathu wauchimo umatilepheretsa kukhala olungama pamlingo umodzimodziwo monga Wopereka Chitsanzo Wamkuluyo. Koma mwa kukoma mtima kwapadera kwa Yehova otsatira odzozedwa a Yesu tsopano angapitirizebe kukhala ndi moyo monga ana a Mulungu.
8 Wozolowera kuchimwa dala ali “wochokera mwa Mdyerekezi,” amene wakhala akuchimwa “kuyambira pachiyambi” pa ntchito yake yodzisankhira yopandukira Yehova. Koma Mwana wa Mulungu ‘anawonekera’ kuti “akawononge” “ntchito” za Satana zopititsa patsogolo uchimo ndi mphulupulu. Izi zimaphatikizapo kumasula ziyambukiro za imfa ya Adamu mwa kutetezera uchimo kupyolera mwa Kristu ndi kuukitsidwa kwa awo amene ali m’manda (Hadesi), kuphatikizaponso kuphwanyidwa kwa mutu wa Satana. (Genesis 3:15; 1 Akorinto 15:26) Pakali pano, otsalira odzozedwa, ndi “khamu lalikulu,” tipewetu chizolowezi chauchimo ndi chisalungamo.
Sungani Chilamulo cha Mulungu
9. Kodi ndim’lingaliro lotani m’limene Mkristu wobadwa ndi mzimu sangakhalire ndi “chizolowezi cha kuchita uchimo,” ndipo nchifukwa ninjiizi ziri choncho?
9 Kenako Yohane akulekanitsa pakati pa ana a Mulungu ndi a Mdyerekezi. (Werengani 1 Yohane 3:9-12.) Aliyense “wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo,” kapena kuuzolowera. “Mbewu ya Yehova,” kapena “mzimu woyera umene umapatsa munthuyo “kubadwa kwatsopano” ku chiyembekezo cha kumwamba, umakhalabe mwa munthuyo kusiyapo ngati awukaniza ndipo motero ‘kuumvetsa chisoni’ mzimuwo, kotero kuti Mulungu amauchotsa. (1 Petro 1:3, 4, 18, 19, 23; Aefeso 4:30) Kupitirizabe kukhala mmodzi wa ana a Mulungu, Mkristu wodzozedwa ndi Mulungu ‘sakhoza kuchimwa mwachizolowezi.’ Monga ‘cholengedwa chatsopano’ chokhala ndi “umunthu watsopano,” iye amayesayesa kutsutsana ndi uchimo. Iye ‘wawonjoka ku chivundi cha m’dzikoli napyola chilakolako,’ ndipo iye saali wochimwa wozolowera mu mtima mwake.—2 Akorinto 5:16, 17; Akolose 3: 5-11; 2 Petro 1:4.
10. Kodi ndiiti imene iri njira imodzi yolekanitsira pakati pa ana a Mulungu ndi ana a Mdyerekezi?
10 Njira imodzi yolekanitsira pakati pa ana a Mulungu ndi a Mdyerekezi ndi iyi: “Yense wosachita chilungamo saali wochokera kwa Mulungu.” Chisalungamo chiri chowanda kwambiri pakati pa ana a Mdyerekezi kotero kuti iwo “akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tawo tiwachokera,” izi ndizo zimene ampatuko akanakonda kuchitira Akristu okhulupirika.—Miyambo 4:14-16.
11. (a) Kodi ndiiti imene iri njira ina yodziwira awo amene saali ana a Mulungu? (b) Kusinkhasinkha panjira ya Kaini kuyenera kutisonkhezera kuchitanji?
11 Ndiponso, iye wosakonda mbale wake [sachokera kwa Mulungu].” Kwenikweni, “uthenga” umene taumva “kuyambira pachiyambi” pa miyoyo yathu monga Mboni za Yehova ngwakuti “tikondane wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34) Chotero ife sitiri “monga Kaini,”amene anasonyeza kuti anali “wochokera kwa woipayo” mwa ‘kupha mbale wake’ mwa mkhalidwe wachiwawa wa kuchita mbanda wa Satana. (Genesis 4:2-10; Yohane 8:44) Kaini anapha Abele “popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.” Ndithudi, kusinkhasinkha panjira ya Kaini kuyenera kutisonkhezera kupewa udani wofananawo pa abale athu auzimu.
Kukonda “m’Ntchito ndi m’Chowonadi”
12. Kodi “timadziwa bwanji kuti tapyola imfa kumka kumoyo,” ndipo ichi chimatanthauzanji?
12 Ngati tinati titsanzire Kaini tikanakhala akufa mwauzimu. (Werengani 1 Yohane 3: 13-15.) Iye anada mbale wake kwambiri kotero kuti anamupha, ndipo sitikudabwa kuti dziko mofananamo likutida, chifukwa chakuti Yesu adaneneratu ichi. (Marko 13:13) Koma “tidziwa [kapena tiri ndi chidaliro chakuti] tapyola imfa [yauzimu] kumka kumoyo [wosatha], chifukwa chakuti timakonda abale,” mboni zinzathu za Yehova. Chifukwa cha kukonda abale kumeneku, limodzi ndi kukhulupirira Kristu, sitirinso ‘akufa’ m’machimo ndi mphulupulu, koma Mulungu wachotsa pa ife themberero Lake, ndipo taukitsidwa ku imfa yauzimu, tikumapatsidwa chiyembekezo cha moyo wosatha. (Yohane 5:24; Aefeso 2:1-7) Ampatuko opanda chikondiwo alibe chiyembekezo chotero, chifukwa chakuti “iye amene sakonda akhala mu imfa [yauzimu].”
13. Ngati timuda mbale wathu, kodi nchifukwa ninji tiyenera kupanga nkhaniyi kukhala ya pemphero?
13 Ndithudi, “yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu.” Sipangachitidwe mbanda yakuthupi (monga pamene Kaini anapha Abele chifukwa cha njiru ndi udani, ) Koma waudaniyo akanakonda kuti mbale wake wauzimu asakhale wamoyo. Popeza kuti Yehova amawerenga mtima, waudaniyo ngwotsutsidwa. (Miyambo 21:2; yerekezerani ndi Mateyu 5:21, 22. ) Palibe “wakupha munthu,” kapena wakuda wokhulupirira mnzake wotero, amene ali “ndi moyo wosatha wa kukhala mwa iye.” Chotero ngati tida Mboni inzathu iriyonse mobisa, kodi sitiyenera kupempherera chithandizo cha Yehova kuti tisinthe mkhalidwe wathu kuti tikhale ndi mzimu wakukonda abale?
14. Kodi nkumlingo wotani kuumene timafunsidwa kusonyeza chikondi kwa abale?
14 Ngati titi tipitirizebe kukhala ana a Mulungu, tiyenera kusonyeza kukonda abale mwa mawu ndi ntchito. (Werengani 1 Yohane 3:16-18.) Izi ziyenera kukhala zotheka, chifukwa chakuti “tizindikira chikondi, popeza iye [Yesu Kristu] anapereka moyo wake [kapena, “umoyo”] chifukwa cha ife.” Popeza kuti Yesu anasonyeza chikondi chachikulu motero, ife tiyenera kusonyeza chikondi chopanda mpeni kumphasa chimodzimodzicho (Chigiriki a·gaʹpe) kwa okhulupirira anzathu. Mwachitsanzo, m’nthawi za chizunzo, timakhala ndi thayo la “kupereka moyo wathu chifukwa cha abale,” monga mom we Priska ndi Akwila ‘anaperekera khosi lawo chifukwa cha moyo wanga [wa mtumwi Paulo].’—Aroma 16:3, 4; Yohane 15:12, 13.
15. Ngati mbale ali wosowa ndipo ife tiri nacho “chuma cha dziko lino chochirikizira moyo,” kodi chikondi chimatifunikiritsa ife kuchita chiyani?
15 Ngati tikanapereka miyoyo yathu kaamba ka abale athu, tiyenera kukhala ofunitsitsa kusafunsira zinthu zambiri kwa iwo. Tinene kuti tiri ndi “chuma cha dzikoli chochirikizira moyo”—ndalama, chakudya, zovala, ndi zina zotero zotheketsedwa ndi dziko. Tingathe ‘kuwona’ mbale wosowa, sitimawona kokha mkhalidwe panthawi ndi nthawi koma timauyang’anitsitsa. Mkhalidwe wake ungachititse “chitseko” cha “zinsoni,” kapena malingaliro akuya mopambanitsa, kutsegulidwa. Koma bwanji ngati titseka “chitseko” chimenecho mwa kulola dyera kulepheretsa cholinga chathu cha kumthandiza? Pamenepo “chikondi cha Mulungu” chikhala mwa ife bwanji?Sikuli kokwanira kungolankhula kokha za kukonda abale. Monga ana a Mulungu, tiyenera kuchisonyeza “m’ntchito ndi m’chowonadi.” Mwachitsanzo, ngati mbale ali wanjala, afunikira chakudya, osampatsa mawu okha.—Yakobo 2:14-17.
Mitima Imene Simatitsutsa
16. (a) Kodi ndimotani mmene Mulungu aliri “wamkulu kuposa mitima yathu”? (b) Mogwirizana ndi kunena kwa Yohane, kodi nchifukwa ninji Yehova amayankha mapemphero athu?
16 Kenako Yohane akusonya zitsimikiziro zakuti ndife ana a Mulungu. (Werengani 1 Yohane 3:19-24. ) “Umo tidzazindikira kuti tiri ochokera m’chowonadi” ndipo sitiri mikhole yonyengedwa ndi ampatuko “mwa ichi”—chenicheni chakuti tikusonyeza kukonda abale. Motero ‘titsimikizira Imitima yathu’ pamaso pa Mulungu. (Salmo 119:11) Ngati mitima yathu ititsutsa, mwinamwake chifukwa chakuti tikulingalira kuti sitinasonyeze olambira anzathu chikondi chokwanira, kumbukirani kuti “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.” Iye ngwachifundo chifukwa chakuti akuzindikira ‘kukonda kwathu abale kopanda chinyengoko,’ kumenyana kwathu ndi uchimo, ndi zoyesayesa zathu kukhala ndi moyo mwanjira yomkondweretsa. (1 Petro 1:22; Salmo 103:10-14) “Mtima wathu ukapanda kutitsutsa” chifukwa chakuti pali ntchito zotsimikizira kukonda kwathu abale, ndipo sitiri ndi liwongo la uchimo wobisika, ‘tiri nawo ufulu wa kulankhula ndi Mulungu’ m’pemphero. (Salmo 19:12) Ndipo iye amayankha mapemphero athu chifukwa chakuti tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.”
17. Kodi “malamulo” a Mulungu amaphatikizapo zofunika ziwiri ziti?
17 Ngati tiyembekezera kuti mapemphero athu ayankhidwe, tiyenera kusunga “malamulo” a Mulungu ophatikizapo zofunika ziwiri izi: (1) Tiyenera kukhulupirira “dzina” la Yesu, kulandira dipo ndi kuvomereza ufumu wake woperekedwa ndi Mulungu. (Afilipi 2: 9-11) (2) Tiyeneranso “kukondana wina ndi mnzake” monga momwedi Yesu analamulira. (Yohane 15:12, 17) Ndithudi, aliyense wokhulupirira dzina la Kristu ayenera kukonda ena onse osonyeza chikhulupiriro chotero.
18. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova ali “m’chigwirizano ndi ife”?
18 Munthu wosunga malamulo a Mulungu “akhala mwa iye,” ali wogwirizana ndi Yehova. (Yerekezerani ndi Yohane 17:20, 21. ) Koma kodi ndimotani mmene “timapezera chidziwitso” chakuti Mulungu ali “m’chigwirizano ndi ife”? Timadziwa ichi “mwa mzimu [woyera] umene anatipatsa ife.” Kukhala ndi mzimu woyera wa Mulungu ndi mphamvu ya kusonyeza zipatso zake, kuphatikizapo kukonda abale, kumatsimikizira kuti tiri m’chigwirizano ndi Yehova.—Agalatiya 5:22, 23.
Khalani Odikira!
19, 20. Kodi nchifukwa ninji tiyenera ‘kuyesa mawu onse ouziridwa,’ ndipo nchithandizo chotani chimene Yohane akupereka pamfundo ino?
19 Kenako Yohane akusonyeza mmene tiyenera kukhalira odikira. (Werengani 1 Yohane 4:1.) Sitiyenera kukhulupirira mzimu uliwonse, kapena “mawu ouziridwa” koma tiyenera ‘kuyesa mizimu kuti tiwone ngati ichokera kwa Mulungu.’ Chifukwa ninji? “Popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m’dziko lapansi” Kwakukulukulu ena a aphunzitsi onyenga amenewa panthawiyo anali kuyendayenda akumagwirizana ndi mipingo yosiyanasiyana nafunafuna “kukopa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:29, 30, NW; 2 Yohane 7) Chotero okhulupirika anafunikira kudikira.
20 Akristu ena a m’zaka za zana loyamba anali ndi ‘luntha la kudziwa mawu ouziridwa,’ mphatso yozizwitsa ya mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu imene mwachiwonekere inawakhozetsa kudziwa kuti kaya mawu ouziridwawo ana chokera kwa Yehova kapena ayi. (1 Akorinto 12:4, 10) Koma chenjezo la Yohane likuwonekera kukhala logwira ntchito kwa Akristu onse ndipo nlothandiza lerolino pamene ampatuko ayesayesa kuwononga chikhulupiriro cha Mboni za Yehova. Ngakhale kuti mphatso ya ‘kuzindikira mawu ouziridwa’ inapita, mawu a Yohane akupereka njira yodziwira kuti kaya aphunzitsiwo akusonkhezeredwa ndi mzimu wa Mulungu ndi zisonkhezero zauchiwanda.
21. Kodi ndinjira imodzi yotani imene inali yoyesera “mawu ouziridwa”?
21 Tamverani njira imodzi yoyesera. (Werengani 1 Yohane 4:2, 3.) “Mzimu uliwonse umene uvomereza kuti Yesu Kristu anadza m’thupi uchokera mwa Mulungu.” Timavomereza kuti Yesu kalero anadza monga munthu ndipo ali Mwana wa Mulungu, ndipo chikhulupiriro chathu chimatisonkhezera kuphunzitsa ena chowonadi chotero. (Mateyu 3: 16, 17; 17:5; 20:28; 28:19, 20) “Ndipo mzimu uliwonse umene suuvomereza Yesu suuchokera kwa Mulungu.” Mmalo mwake, “uwo ndiwo mzimu wa wokana Kristu” wotsutsa Kristu ndi ziphunzitso Zamalemba zonena za iye. Mwachiwonekere, Yohane ndi atumwi ena adachenjeza kuti ‘mawu ouziridwa a wokana Kristu’ analinkudza. (2 Akorinto 11:3, 4; 2 Petro 2:1) Popeza kuti panthawiyo aphunzitsi onyenga anali kuwopseza Akristu owona, Yohane akananena kuti, “ulimo m’dziko lapansi.”
22. Kodi ndinjira ina yotani yoyesera “mawu ouziridwa”?
22 Njira ina yodziwira ‘mawu ouziridwa’ ndiyo kuwona amene amawamvetsera. (Werengani 1 Yohane 4:4-6.) Monga atumiki a Yehova, ife ‘tagonjetsa,’ kapena kulaka, aphunzitsi onyenga, kulakika pa zoyesayesa zawo za kutichotsa pa chowonadi cha Mulungu. Chilakiko chauzimu chimenechi chakhala chotheka chifukwa cha Mulungu, amene ali ‘m’chigwirizano’ ndi Akristu okhulupirica, ‘amene ali wamkulu kwambiri kuposa iye Mdyerekezi] amene ali wogwirizana ndi dzito,’ kapena anthu osalungama. (2 Akorinto 4:4) Chifukwa chakuti ampatuko “achokera m’dziko” ndipo ali ndi mzimu wake woipawo, “alankhula monga ochokera m’dziko lapansi, ndipo dziko lapansi liwamvera.” Popeza kuti tiri nawo mzimu wa Yehova, tingathe kuzindikira mpangidwe wauchiwanda wa “mawu awo ouziridwa” ndipo chifukwa chake timawakana.
23. Kodi ndani amene amatimvetsera nazindikira kuti timatsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu?
23 Koma timadziwa kuti “ndife ochokera mwa Mulungu” chifukwa chakuti “iye amene azindikira Mulungu atimvera.” Anthu onga nkhosa amazindikira kuti timaphunzitsa chowonadi chochokera m’Mawu a Mulungu. (Yerekezerani ndi Yohane 10:4, 5, 16, 26, 27. ) Ndithudi, “iye wosachokera mwa Mulungu satimvera ife.” Aneneri onyega kapena aphunzitsi sanamvetsere kwa Yohane, kapena kwa ena amene ‘anachokera mwa Mulungu’ ndipo anapereka chilangizo cholama chauzimu. Chotero “momwemo tizindikira mzimu wa chowonadi, ndi mzimu wa chisokeretso.” Ife amene tapanga banja la olambira a Yehova timalankhula “chinenero changwiro” chowonadi Chamalemba choperekedwa kupyolera mu gulu la Mulungu. (Zefaniya 3:9) Ndipo kuchokera m’zimene timanena, kuli kwachiwonekere kwa anthu onga nkhosa kuti ife timatsogozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.
24. Kodi kenako Yohane adzasonyezanji?
24 Pamfundo ino, Yohane akupereka zofunika zazikulu zimene tiyenera kufikitsa ngati titi tipitirizebe kuyenda monga ana a Mulungu. Kenako adzatisonyeza chifukwa chake tiyenera nthawi zonse kusonyeza chikondi ndi chikhulupiriro.
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi ndimotani mmene ena amapangidwira kukhala “ana a Mulungu”?
◻ Kodi tingalekanitse motani pakati pa ana a Mulungu ndi a Mdyerekezi?
◻ Kodi kusinkhasinkha pa njira ya Kaini kuyenera kutisonkhezera kuchita chiyani?
◻ Kodi ndikumlingo wotani kumene tiyenera kusonyeza kukonda abale?
◻ Kodi ndimotani mmene “mawu ouziridwa” angayesedwere?
[Chithunzi pa tsamba 11]
Kusinkhasinkha pa njira ya Kaini kuyenera kutisonkhezera kupewa kudana ndi abale athu alionse
[Chithunzi pa tsamba 12]
Olambira Yehova amalankhula “chinenero changwiro” cha chowonadi Chamalemba choperekedwa kupyolera