Mutu 15
Kodi Nchifukwa Ninji Kudera Nkhaŵa ndi Anthu Ena?
1. (a) Kodi nchiyani chimene chachititsa anthu ambiri kusamalira za iwo okha ndi kusadera nkhaŵa ndi anthu ena? (b) Kodi nchiyani chimene chakhala choturukapo chake?
KUDERA NKHAŴA ndi ena kopanda dyera kuli kosoŵa lerolino. Ngakhale kuli kwakuti munthu aliyense amabadwa ali ndi kukhoza kusonyeza chikondi, pamene ena mosayenerera afunafuna phindu la iwo eni kapena pamene zoyesayesa za munthuwe zakusonyeza chikondi zikumvedwa molakwa, munthuyo angaganize kuti kuli bwinopo kungosamalira za iyemwini. Ena, powona kuti anthu amene amadyera masuku pamutu anthu anzawo akulemerera mwakuthupi, angalingalire kuti imeneyi ndiyo njira yopezera chipambano. Choturukapo chake nchakuti anthu ambiri ali ndi mkhalidwe wakusadalira ndipo ali ndi mabwenzi enieni oŵerengeka, ngati alipo. Kodi nchiyani chimene chimachititsa mkhalidwe wosakondweretsa wazinthu umenewu?
2. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera muzu wavutolo? (b) Kodi kudziŵa Mulungu kumatanthauzanji?
2 Chikondi chikusoŵeka, mtundu wachikondi chimene chiri chodera nkhaŵa kwenikweni ndi thanzi losatha la anthu ena. Ndipo kodi nchifukwa ninji chikusoŵeka? Pofika pamuzu penipeni pavutolo, Baibulo limalongosola kuti: “Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Ndithudi, anthu ambiri ofuna zawo zokha amadzinenera kukhala akukhulupilira Mulungu ngakhale kufika kutchalitchi. Koma chenicheni ndicho chakuti iwo sakudziwa kwenikweni Mulungu. Kudziŵa Mulungu kumatanthauza kuzoloŵerana bwino ndi umunthu wake, kuzindikira ulamuliro wake, ndiyeno kuchita mogwirizana ndi zimene timadziŵa ponena za iye. (Yeremiya 22:16; Tito 1:16) Chotero, pamenepa, kuti tipeze chisangalalo chowona m’moyo chimene chimadza kokha pamene munthu asonyeza chikondi ndi kuchilandira, tiyenera kufika pakudziŵa Mulungu bwino lomwe ndi kugwiritsira ntchito zimene timaphunzira.
3. Kodi Mulungu wasonyeza motani chikondi chake chachikulu kaamba ka anthu?
3 “Umo chinawoneka chikondi cha Mulungu ponena za ife, kuti Mulungu anamtumiza Mwana wake wobadwa yekha, aloŵe m’dziko, kuti tipeze moyo kupyolera mwa iye. Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu [choyamba], koma kuti iye anatikonda ife, ndipo anatumiza Mwana wake akhale nsembe yachiwombolo chifukwa cha machimo athu. Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda ife kotero, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.” (1 Yohane 4:9-11) Mulungu sanalole mkhalidwe wopanda chikondi wa anthu kuziralitsa chikondi chake. Monga momwe kwalongosoledwera pa Aroma 5:8 kuti: “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Kristu adatifera ife.”
4. Kodi chimenecho chimakuchititsani inumwini kumva bwanji kulinga kwa Mulungu?
4 Kodi ndianthu angati amene mumawakonda kwambiri kotero kuti mukawataira moyo wanu—anthu amene sanakuchitireni kanthu kalikonse? Ngati muli kholo, kodi pali yani amene inu mukakhala wofunitsitsa kuti mwana wanu amfere? Umenewu ndiwo mtundu wachikondi chimene Mulungu anachisonyeza. (Yohane 3:16) Kodi kuzindikira zimenezi kumakuchititsani kulingalira motani kulinga kwa Mulungu? Ngati ife tiyamikiradi zimene iye wachita, tidzapeza kuti sikolemetsa kumvera malamulo ake.—1 Yohane 5:3.
5. (a) Kodi nchiyani chimene chiri “lamulo latsopano” limene Yesu anapereka kwa ophunzira ake? (b) Kodi ndimotani mmene kudzipereka kwathu kwa Mulungu monga wolamulira kukuloŵetsedweramo? (c) Pamenepa, kodi kumvera “lamulo latsopano” limeneli kumafunikiritsa chiyani?
5 Pausikuwo imfa yake isanachitike Yesu anapatsa ophunzira ake limodzi lamalamulo amenewo. Likawadziŵikitsa kukhala osiyana ndi mbali yotsala yadziko. Iye anati: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake.” Lamulo la Yesu linali “latsopano” m’chakuti anali kunena za kukonda ena, osati kokha monga momwe anadzikondera, koma “monga ndakonda inu”—kukhala ofunitsitsa kuferana. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:16) Mtundu umenewu wachikondi umasonyeza kudzipereka kwathu kwa Mulungu mwakutsimikizira kukhala bodza kudzinenera kwa Mdyerekezi kwakuti palibe munthu akamvera Mulungu ngati kutero kunaika pangozi moyo wake. (Yobu 2:1-10) Mwachiwonekere, kumvera “lamulo latsopano” iri kumafunikira kuderana nkhaŵa kwambiri.—Yakobo 1:27; 2:15, 16; 1 Atesalonika 2:8.
6. Kodi chikondi chiyenera kusonyezedwanso kwayani, ndipo chifukwa ninji?
6 Koma Kristu anafera dziko la anthu, osati ophunzira ake okha. Chotero Malemba amalimbikitsa kuti: “Monga tiri nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo apabanja lachikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Mipata ya ‘kuchitira onse chokoma’ imabuka tsiku ndi tsiku. Pamene chikondi chathu sichiri chochepa, koma chamataya ndi chowoloŵa manja, timatsanzira Mulungu, popeza ‘amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa abwino, navumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.’—Mateyu 5:43-48.
Kulemekeza Munthu ndi Chuma cha Ena
7. Kodi nchiyani chimene chingasonkhezere mmene tikuchitira kwa munthu ndi chuma cha ena?
7 Tikukhala ndi moyo mkati mwadziko lopanda chikondi. Mwinamwake inu mukudziŵa kuti nthawi zonse simumakhala olingalira ena monga momwe mukadakhalira. Koma ngati munthu ati atumikire Mulungu, pali kufunika kwa kuyesayesa mosamalitsa kuti iye ‘asandulize maganizo ake.’ (Aroma 12:1, 2) Afunikira kusintha ganizo lake kulinga kwa anthu ndi chuma cha ena.
8. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kusalemekeza chuma cha ena kofalikira? (b) Kodi ndi uphungu wotani umene uli m’Baibulo, ngati utsatiridwa, ungaletse munthu kusachita zinthu zoterozo?
8 M’madera ena muli kusalemekeza kwakukulu chuma cha ena. Kaamba ka chikondwerero chabe, ana amawononga ponse paŵiri chuma cha anthu ndi chaboma. Kapena mwadala amaipitsa zinthu zimene ena azigwirira ntchito zolimba kuti azipeze. Anthu ena angasonyeze kuwopsedwa ndi kusakaza koteroko, komabe iwo amakuthandizira mwakutaya zinyalala m’mapaki, pamakwalala kapena m’nyumba za anthu onse. Kodi machitachita amenewa ngogwirizana ndi chilangizo cha Yesu chakuti: “Chifukwa chake zinthu zirizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero”? (Mateyu 7:12) Khalidwe lopanda chikondi lotero limasonyeza kuti munthuyo sali wogwirizana kotheratu ndi chifuno cha Mulungu chakuti dziko lapansi lino likhale paradaiso.
9. (a) Kodi ndimotani mmene kuba kumayambukirira miyoyo ya onse? (b) Kodi nchifukwa ninji kuba kuli kolakwa m’maso mwa Mulungu?
9 M’malo ambiri, kudera nkhawa ndi moyo wanu ndi chuma kumachititsa zitseko kukhomedwa ndi maloko, mazenera oikidwa mipiringidzo yachitsulo, ndi agalu olondera kukhala ofala. Masitolo amakweza mitengo kuti akwichize zobedwa. Koma kuba sikudzakhala ndi malo m’Dongosolo Latsopano la Mulungu. Chifukwa chake, alionse oyembekezera kukhalamo ayenera kuphunzira tsopano kukhala ndi moyo mwanjira imene imathandizira kuchititsa chisungiko cha anthu anzawo. Baibulo limasonyeza kuti “mphatso” ya Mulungu njakuti munthu awone “zabwino kaamba ka ntchito yake yonse yolimba.” Chotero kuli kulakwa kuyesa kum’mana zotulukapo za ntchito yake. (Mlaliki 3:13; 5:18) Anthu ambiri amene kale anali osawona mtima asintha. Sikokha kuti iwo amapewa kuba koma iwo aphunziranso chisangalalo chakupatsa ena. (Machitidwe 20:35) Pokhala ndi chikhumbo chakukondweretsa Mulungu, iwo akulabadira zimene zalembedwa pa Aefeso 4:28 kuti: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza osoŵa.”
10. (a) Mwanjira imene timalankhulira ndi ena, kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuwalingalira? (b) Kodi nchiyani chimene chidzathandiza munthu kuphunzira kusonyeza chikondi m’njira imeneyi?
10 Kaŵirikaŵiri, makamaka pamene zinthu sizikuyenda bwino, chimene ena afunikira sindicho kanthu kena ka kuthupi, koma amafunikira chifundo. Komabe, kodi nchiyani chimene chimachitika m’mikhalidwe kumene zophophonya za munthu ziwonekera? Pangakhale mawu amkwiyo, kutukwana, kapena mawu odula. Ngakhale ena amene amazindikira kuti njirayi njolakwa amalephera kulamulira lirime lawo. Kodi ndimotani mmene munthu angagonjetsere chizoloŵezi chotero? Kwakukulukulu, chimene chikusoŵeka ndicho chikondi, ndipo chimenecho chimasonyeza kufunika kwa kufika pakudziŵa Mulungu. Pamene munthu afikira pakuzindikira ukulu wa chifundo cha Mulungu pa iye, adzakupeza kukhala kosavuta kwambiri kukhululukira ena. Iye angayambedi kuwona njira zothandizira wolakwayo, akumapereka chithandizo chokoma mtima ncholinga chakuwongokera.—Mateyu 18:21-35; Aefeso 4:31–5:2.
11. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukhala otukwana m’kulankhula kwathu ngakhale pamene ena ali osakoma mtima kwa ife?
11 Nzowona kuti anthu ena sangagwiritsire ntchito uphungu wabwino kwambiri uwu wochokera m’Mawu a Mulungu umenewu m’zochita zawo ndi ife. Mosasamala kanthu za zisonkhezero zathu zamtima, nthawi zina tingapeze kuti tikuchitiridwa moipa. Kodi pamenepo tidzachitanji? Baibulo limalangiza kuti: “Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.” (Aroma 12:17-21; 1 Petro 2:21-23) Kukoma mtima kwathu kosalekeza m’nthawi yokwanira kungafeŵetse mkhalidwe wawo ndi kutulutsa mikhalidwe yawo yabwino kwambiri. Mulimonse mmene angachitire, pamene tipirizabe kusonyeza chifundo, tikusonyeza kuti tikuchirikiza njira ya Mulungu ya kulamula, imene iri yozikidwa pa chikondi.
Kugonjetsa Tsankhu Laufuko, Lautundu, la Anthu
12, 13. Kodi ndimotani mmene Baibulo limathandizira munthu kuchotsa malingaliro alionse atsankho laufuko, lautundu, kapena lamakhalidwe a anthu?
12 Munthu amene ali ndi chikondi chenicheni samasonkhezeredwa ndi fuko, mawonekedwe akhungu, utundu, kapena mkhalidwe wa kutchuka kwa munthu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti iye amazindikira chowonadi cha Baibulo chakuti “[Mulungu] anapanga kuchokera mwa munthu mmodzi mtundu uliwonse wa anthu.” (Machitidwe 17:26, NW) Chifukwa cha chimenecho anthu onse ali achibale. Palibe fuko lirilonse limene mwachibadwa liri lapamwamba kuposa lina.
13 Palibe aliyense amene ali ndi chifukwa chirichonse chonyadira chifukwa cha makolo ake, fuko, kawonekedwe ka khungu, mtundu kapena malo ake m’moyo. “Onse anachimwa, naperewera paulemelero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Chifukwa chake munthu aliyense amadalira pa nsembe yadipo ya Kristu. Ndipo Baibulo limasonyeza kuti awo amene adzasiidwa kupyola “chisatso chachikulu” akuchokera mu “mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.”—Chivumbulutso 7:9, 14-17.
14. Kodi nchifukwa ninji kuchitiridwa moipa kwa munthu sikuli maziko enieni akuchitira tsankho motsutsana ndi anthu afuko lina kapena mtundu?
14 Poyesa kulungamitsa tsankho lake, munthu angakumbukire chokumana nacho choipa chimene iye anali nacho ndi munthu wina wafuko lina kapena mtundu wina. Koma kodi aliyense wafuko limenelo kapena mtundu analoŵetsedwa m’cholakwacho? Ndipo kodi anthu afuko kapena mtundu wamunthuwe sanakhale ndi liwongo la chinthu chofananacho? Ngati tikuyembekezera kukhala ndi moyo m’Dongosolo Latsopano la mtendere la Mulungu, tifunikira kuchotsa m’mitima yathu kunyada kulikonse kumene kumatichititsa kudana ndi anthu ena.
15. Ngati mawu a munthu ponena za fuko kapena mtundu akanakhumudwitsa wokhulupirira mnzake, kodi ndimotani mmene ichi chikayambukirira kaimidwe ka iyemwini pamaso pa Mulungu ndi Kristu?
15 Chimene chiri m’mitima yathu nthawi ina chimawonekera m’kulankhula kwathu. Monga momwe Kristu Yesu ananenera kuti: “M’kamwa . . . mungolankhula mwakuchuluka kwamtima wake.” (Luka 6:45) Bwanji ngati kulankhula kosonyeza tsankho kukakhumudwitsa munthu wina amene anali kusonyeza chikondwerero m’gulu la Yehova? Nkhaniyo njowopsa kwambiri kotero kuti Yesu anachenjeza kuti: “Yense yemwe adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupilira ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukoloŵekedwe m’khosi mwake, naponyedwe iye m’nyanja.”—Marko 9:42.
16. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kupanda tsankho kumene tiyenera kusonyeza anthu ena?
16 Akristu ali ndi thayo losonyeza chikondwerero chachikondi mwa ena mosasamala kanthu za fuko lawo, mtundu, kapena kutchuka. (Yakobo 2:1-9) Monga momwe Yesu analimbikitsira kuti: “Pamene ukonza phwando uitane aumphaŵi, opunduka, otsimphina, akhungu; ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho.” (Luka 14:13, 14) Mwakukhala ndi mtundu uwu wakudera nkhaŵa ndi anthu ena, timasonyeza mikhalidwe yachikondi ya Atate wathu wakumwamba.
Nkhaŵa Yachikondi Kaamba ka Ubwino Wosatha wa Ena
17. (a) Kodi ndichinthu chamtengo wapatali koposa chotani chimene tingagaŵane ndi ena? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonkhezeredwa kuchita motero?
17 Nkhaŵa yathu kaamba ka ena siyenera kukhala yolekezera pazosoŵa zawo zakuthupi. Ndiponso chikondi chathu sichikakhala chokwanira kokha chifukwa chakuti tinali okoma mtima kwa anthu amitundu yonse. Kuti moyo ukhale ndi tanthauzo lenileni, anthu afunikira kudziŵa Yehova ndi zifuno zake. M’pemphero kwa Atate wake, Yesu anati: “Ichi chitanthauza moyo wosatha, kulandira kwawo chidziŵitso cha inu, Mulungu yekha, ndi cha uyo amene munamtuma, Yesu Kristu.” (Yohane 17:3, NW) Ngati mwaŵerenga bukhu lino kuyambira kuchiyambi, mukudziŵa mmene mungapezere mfupo imeneyo. Mwadziwonera nokha zimene Malemba amaneneratu ponena za “chisautso chachikulu,” ndi maumboni owoneka amene amatsimikizira kuyandikira kwake. Mukudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chiyembekezo chokha cha anthu. Koma kodi kukonda Yehova ndi mtundu wa anthu kumakusonkhezerani kugaŵana chidziŵitso chofunikachi ndi ena?
18. (a) Pa Mateyu 24:14, kodi ndintchito yotani imene Yesu anaineneratu kaamba ka tsiku lathu? (b) Kodi tiyenera kuwona motani kukhalamo ndi phande?
18 Polankhula za “mapeto adongosolo lazinthu,” Yesu ananeneratu kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:3, 14, NW) Ha ndimwaŵi wotani nanga kuimira Mfumu yolamulira chilengedwe chonse, Yehova iyemwini, pamene munthuyo akukhala ndi phande mu ‘kuchitira umboni’ kumeneku! Mwaŵi wakukhala ndi phande ntchito yapadera imeneyi uli chitsegukire, koma osati kwanthawi yaitali kwambiri.
19. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulola lingaliro lirilonse la kusakhala kwathu ndi luso kutilepheretsa kukhala ndi phande m’ntchito imeneyi?
19 Polingalira chiyembekezo cha kukhala ndi phande mu “umboni ku mitundu yonse,” kuli bwino kuzindikira kuti sindilo luso lamunthu mwini limene limachititsa zoturukapo kuuthengawo koma Mulungu. (Machitidwe 16:14; 1 Akorinto 3:6) Ngati mwasonkhezeredwa ndi mtima wofunitsitsa, Yehova angakhoze kukugwiritsirani ntchito kukwaniritsa chifuniro chake. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera: “Ndipo kulimbika kotero kwa Mulungu tiri nako mwa Kristu: sikuti tiri okwanira mwa ife tokha, kuyesera kanthu kena monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kukuchokera kwa Mulungu.”—2 Akorinto 3:4-6.
20. (a) Kodi aliyense adzalabadira bwino lomwe mbiri yabwino? (b) Kodi ndiubwino wotani umene umachitidwa mwakulalikira kwa anthu amene ali amphwayi kapena ngakhale otsutsa?
20 Ndithudi, sitiyenera kuyembekezera kuti, munthu aliyense adzalabadira moyanja. Ambiri adzakhala amphwayi. Ena adzatsutsa. Komabe iwo angasinthe. Saulo wa ku Tariso, amene nthawi ina anali wozunza Akristu anakhala mtumwi wachangu wa Yesu. (1 Timoteo 1:12, 13) Kaya ena akudziŵa kapena ayi, iwo afunikira uthenga wa Ufumu. Chotero tifunikira kukhala odera nawo nkhawa, tiri ofunitsitsa kuyesayesa kwamtima wonse kaamba ka ubwino wawo wosatha. (1 Atesalonika 2:7, 8) Ngakhale ngati iwo sakufuna uthenga wa Ufumu, ubwino umachitidwabe. Umboni umaperekedwa, dzina la Yehova limakwezedwa, ‘kulekanitsidwa’ kwa anthu kuli nkuchitidwa, ndipo timasonyeza kukhulupirika kwa ife eni kwa Yehova.—Mateyu 25:31-33.
Kudera Nkhawa ndi Zimene Zikuchitikira Banja la Inumwini
21. Kodi ndithayo lotani limene mutu wabanja uli nalo ponena za thanzi lauzimu la banja lake?
21 Zoyesayesa zanu za kuthandiza ena kupindula ndi makonzedwe achikondi a Yehova ziyeneranso kulunjikitsidwa kubanja la inumwini. Mwachitsanzo, mutu wabanja uli ndi thayo la kukula kwauzimu kwabanja lake. Kumeneku kumasonkhezeredwa mwachindunji ndi kukhazikika m’makonzedwe ake akukambitsirana kwabanja Mawu a Mulungu. Ndipo pamene mapemphero a atate kaamba ka banja asonyeza kuzipereka kwambiri ndi chiyamikiro, limeneli lingaumbe mkhalidwe wabanja lonse.
22. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa atate kulanga ana ake, ndipo kodi nchiyani chimene chiyenera kumsonkhezera?
22 Thayo lake limaphatikizaponso kupereka chilango. Pamene mavuto abuka, kungawonekere kukhala kosavuta kwambiri kuwanyalanyaza. Koma ngati chilango chiperekedwa kokha pamene atateyo wakwiya, kapena ngati mavuto asamaliridwa kokha pamene iwo akhala aakulu, kanthu kena kakusoŵeka. Miyambo 13:24 imati: ‘Atate amene amakonda mwana wake wamwamuna ndiye amene amamuyambiza kumlanga.’ Chifukwa chake atate wachikondi amapereka chilango mosasintha. Modekha amalongosolera ana ake zinthu ndipo amalingalira zopereŵera zamaganizo, zamalingaliro, ndi zakuthupi za aliyense. (Aefeso 6:4; Akolose 3:21) Ngati inu ndinu atate, kodi muli ndi chikondi chamtundu umenewo kwa ana anu? Kodi muli wofunitsitsa kusenza thayo limeneli, mukumayang’anitsitsa osati kokha paubwino wabanja watsopano lino komanso mtsogolo?—Miyambo 23:13, 14; 29:17.
23. Kodi ndimotani mmene mayi angathandizire kulinga ku ubwino wauzimu wa banja lake?
23 Nayenso, mkazi, angathandize banjalo kwambiri. Kugwirizana kwake ndi mwamuna wake ndi kugwiritsira ntchito kwake nthawi mwanzeru kuumba miyoyo ya ana mwanjira yaumulungu kaŵirikaŵiri kumasonyezedwa mu mkhalidwe ndi lingaliro la ana. (Miyambo 29:15) Ngakhale m’banja mmene mulibe atate, kuphunzitsa kosamalitsa kochokera m’Baibulo kophatikizidwa ndi chitsanzo chabwino kwambiri kumatulutsa zoturukapo zabwino.
24. (a) Ngati wakumana ndi chitsutso chochokera kwa mnzake wa muukwati, kodi ndinkhani yotani imene wokhulupulirayo ayenera kuikumbukira? (b) Pansi pamikhalidwe yoteroyo, kodi ndimotani mmene chikondi chikasonyezedwera kwa mnzanu wosakhulupilirayo?
24 Koma bwanji ngati atate amene ali m’banja salandira Mawu a Mulungu, kapena ngakhale kuzunza mkazi wake? Kodi mkaziyo ayenera kuchitanji? Ngati iye amakonda Yehova, iye ndithudi sadzafulatira Iye. Ndiye Satana amene ananena kuti anthu akasiya Mulungu ngati atavutitsidwa. Ndithudi mkaziyo safuna kuchita zikhumbo za Satana. (Yobu 2:1-5; Miyambo 27:11) Panthawi imodzimodziyo, Baibulo limamfulumiza kufunafuna ubwino wosatha wa mwamuna wake. Kuleka chimene iye akudziŵa kukhala chowonadi kukatanthauza kutaikiridwa ndi moyo wamuyaya kwa aŵiriwo. Koma ngati iye aima nji m’chikhulupiliro chake, angathandize mwamunayo kupeza chipulumutso. (1 Akorinto 7:10-16; 1 Petro 3:1, 2) Ndiponso, mwakupitirizabe kulemekeza zowinda zake zaukwati, ngakhale m’vuto, iye amasonyeza kulemekeza kwake kwambiri Woyambitsa ukwati, Yehova Mulungu.
25. Kodi ndimotani mmene chosankha chakholo chimayambukilira ziyembekezo za moyo za ana?
25 Chifukwa china champhamvu kwakholo lokhulupilira chakukhalira wokhulupirika kwa Mulungu poyang’anizana ndi chitsutso ndicho ana. Mulungu amapereka chitsimikiziro chakuti ana achichepere a atumiki ake odzipereka adzatetezeredwa kupyola “chisautso chachikulu” chirinkudza. Ngakhale ngati kholo limodzi lokha liri mtumiki wa Yehova, Iye amaŵerengera ana achichepere oterowo kukhala “oyera.” (1 Akorinto 7:14) Koma ngati khololo ‘lileka’ kuchita chifuniro cha Mulungu, pamenepo chiyani? Kholo loterolo likataya osati kaamba ka ilo lokha, komanso kaamba ka ana aang’onowo, kaimidwe kovomerezeka pamaso pa Mulungu. (Ahebri 12:25) Ha kumeneku kukakhala kutaikiridwa kowopsa kotani nanga!
26. Kuti tichite mopindulitsa kwenikweni kwa ife eni ndi ena, kodi tifunikira kuchita chiyani?
26 Pamenepa, ziribe kanthu kuti ndi mbali yamoyo yotani imene tikulingalira, kuli kowoneka kuti tifunikira kulingalira osati kokha ife eni koma enanso. Tidzalandira chikondi ngati tisankha chizolowezi chakusonyeza chikondi kwa ena. (Luka 6:38) Koma kuti tisonyeze chikondi chopanda mpeni kumphasa, ndi kusasokeretsedwa ndi kulingalira kwa anthu osawona patali, tifunikira kudziwa Yehova ndi kukhala ndi unansi wabwino ndi iye. Komabe, kuchita kwathu motero, kumalowetsamo chosankha chimene ife aliyense payekha tiyenera kupanga.
[Chithunzi patsamba 171]
Mtundu wachikondi chimene atumiki a Yehova ayenera kukhala nacho chimawapatsa thayo lakusonyeza chifundo chenicheni kwa ena mosasamala kanthu za fuko, mtundu, kapena kutchuka