Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’makalata a Yohane ndi Yuda
MTUMWI Yohane analemba makalata ake atatu ali ku Efeso cha mu 98 C.E., ndipo makalata amenewa ali cha kumapeto kwa Malemba ouziridwa. Makalata awiri oyambirira, amalimbikitsa Akhristu kupitirizabe kuyenda m’kuunika ndiponso kupewa mpatuko. M’kalata yachitatu, Yohane akulimbikitsa Akhristu kuyenda m’choonadi ndiponso kukhala ogwirizana.
Panthawi imene anali ku Palestina, mwina cha mu 65 C.E., Yuda, m’bale wake wa Yesu analembanso kalata yochenjeza Akhristu anzake za anthu oipa amene analowa mu mpingo. Iye anawalangizanso za mmene angakanire makhalidwe oipa a anthuwo. Kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili m’makalata a Yohane ndi Yuda, kungatithandize kukhala olimba m’chikhulupiriro ngakhale tikukumana ndi mavuto.—Aheb. 4:12.
PITIRIZANI KUYENDA M’KUUNIKA, M’CHIKONDI NDIPONSO MWA CHIKHULUPIRIRO
Kalata yoyamba ya Yohane analembera mpingo wonse wachikhristu, ndipo ili ndi malangizo abwino othandiza Akhristu kupewa mpatuko, kukhalabe olimba m’choonadi ndiponso kuti azichita chilungamo. Ikutsindikanso kufunika kopitiriza kuyenda m’kuunika, m’chikondi ndiponso mwa chikhulupiriro.
Yohane analemba kuti: “Ngati tikuyenda m’kuunika monganso iye [Mulungu] ali m’kuunika, tikukhala mu umodzi wina ndi mnzake.” Popeza kuti Mulungu ndiye chimake cha chikondi, mtumwiyu ananenanso kuti: “Tiyeni tipitirize kukondana.” “Kukonda Mulungu” kumatichititsa “kusunga malamulo ake,” ndipo timagonjetsa dziko mwa ‘kukhulupirira kwathu’ Yehova Mulungu, Mawu ake ndiponso Mwana wake.—1 Yoh. 1:7; 4:7; 5:3, 4.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:2; 4:10—Kodi Yesu ndi “nsembe yachiyanjanitso” m’njira yotani? Kuyanjanitsa kumatanthauza kuchita zinthu zothandiza anthu kuti agwirizane. Yesu anapereka moyo wake monga nsembe yachiyanjanitso ndipo mwakuchita zimenezi, anakwaniritsa chilungamo changwiro. Mulungu anasonyeza kuti ndi wachifundo kudzera mwa nsembe imeneyo, ndipo anthu amene angakhulupirire Yesu amakhululukidwa machimo awo.—Yoh. 3:16; Aroma 6:23.
2:7, 8—Kodi lamulo “lakale” ndiponso “latsopano” limene Yohane akunena ndi liti? Yohane akunena za lamulo lokhudza chikondi cha pa abale chololera kuvutikira ena. (Yoh. 13:34 ) Lamuloli akulitchula kuti ndi “lakale” chifukwa chakuti Yesu anali atalipereka kale zaka zoposa 60, Yohane asanalembe kalata yake youziridwa yoyamba. Choncho Akhristuwa anakhala ndi lamuloli “kuyambira pachiyambi” pa moyo wawo wachikhristu. Lamuloli akulitchanso kuti ndi “latsopano” chifukwa chakuti limafuna zambiri kuwonjezera pa ‘kukonda mnansi wako monga umadzikondera wekha.’ Limafuna kuti munthu akhale ndi chikondi chololera kuvutikira ena.—Lev. 19:18; Yoh. 15:12, 13.
3:2—N’chiyani chimene ‘sichinaonekebe’ kwa Akhristu odzozedwa, ndipo kodi ndani amene iwo ‘adzamuona mmene alili’? Iwo sanaonebe mmene adzakhalire akadzaukitsidwa kupita kumwamba ali ndi matupi auzimu. (Afil. 3:20, 21) Komabe, Akhristu odzozedwa amadziwa kuti Mulungu ‘akadzaonekera, [iwo] adzakhala monga iye, chifukwa adzamuona mmene alili,’ monga “Mzimu.”—2 Akor. 3:17, 18.
5:5-8—Kodi madzi, magazi ndi mzimu zimachitira umboni motani kuti “Yesu ndi Mwana wa Mulungu”? Madzi anam’chitira umboni chifukwa chakuti Yesu atabatizidwa m’madzi, Yehova anasonyeza kuti amam’konda monga Mwana wake. (Mat. 3:17) Komanso magazi a Yesu, [kapena kuti moyo wake,] omwe anaperekedwa ngati “dipo lolinganiza m’malo mwa onse,” anasonyeza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu. (1 Tim. 2:5, 6) Ndipo mzimu woyera unachitira umboni kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu pamene unatsikira pa iye pa ubatizo wake. Mzimuwu unam’thandiza ‘kuyendayenda m’dziko, kuchita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.’—Yoh. 1:29-34; Mac. 10:38.
Zimene Tikuphunzirapo:
2:9-11; 3:15. Mkhristu akalekerera chinthu kapena munthu aliyense kumulepheretsa kuti asamakondenso abale ake, ndiye kuti akuyenda mumdima wauzimu, ndipo sakudziwa kumene akulowera.
PITIRIZANI ‘KUYENDA M’CHOONADI’
Yohane anayamba kulemba kalata yake yachiwiri ndi mawu akuti: “Ineyo monga mkulu, ndikulembera mayi wosankhika ndiponso ana ake.” Ndipo anafotokoza kuti anali wosangalala chifukwa anapeza “ena mwa ana [a mayiyo] akuyenda m’choonadi.”—2 Yoh. 1, 4.
Atawalimbikitsa kuti azikondana, Yohane analembanso kuti: “Chikondi chimenechi chimatanthauza kuti tiziyendabe motsatira malamulo ake.” Iye anawachenjezanso za “wonyenga . . . ndi wokana Khristu.”—2 Yoh. 5-7.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1, 13—Kodi “mayi wosankhika” ndani? N’kutheka kuti Yohane ankanena za mayi winawake wotchedwa Kyria. Dzina limeneli ndi mawu a Chigiriki otanthauza “mayi.” Mwina anagwiritsa ntchito mawuwo mophiphiritsa potchula mpingo winawake, n’cholinga choti anthu amene ankazunza Akhristu asazindikire. Ngati ankanenadi za mpingo, ndiye kuti ana a mayiyo anali anthu a mumpingowo ndipo ‘ana a m’bale wake,’ ayenera kuti anaimira anthu a mumpingo wina.
7—Kodi “kubwera” kwa Yesu kumene Yohane ananena pa lembali ndi kuti, nanga onyenga “amatsutsa” motani zimenezi? “Kubwera” kwa Yesu, kumene Yohane ananena si kubwera kosaoneka kumene kunali m’tsogolo. Koma anali kunena za kubwera kwake monga munthu ndiponso za kudzozedwa kwake n’kukhala Khristu. (1 Yoh. 4:2) Anthu onyenga amatsutsa za kubwera kwake monga munthu. Mwinanso amakana kuti Yesu anakhalapo komanso kuti anadzozedwa ndi mzimu woyera.
Zimene Tikuphunzirapo:
2, 4. Kudziwa kwathu “choonadi,” cha m’Baibulo chimene ndi maziko a ziphunzitso zachikhristu, komanso kugwiritsa ntchito mfundo zake m’moyo wathu, n’kofunika kwambiri kuti tidzapulumuke.—3 Yoh. 3, 4.
7—Ngati tikufuna kupitiriza kupindula ndi “kukoma mtima kwa m’chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi kwa Yesu Khristu,” komanso kupitiriza kukhala m’gulu lachikondi la okhulupirira anzathu, tiyenera ‘kusamala’ moyo wathu wauzimu ndi kukana aliyense ‘wosakhalabe m’chiphunzitso cha Khristu.’—2 Yoh. 3.
KHALANI “ANTCHITO ANZATHU M’CHOONADI”
Kalata yachitatu ya Yohane inali yopita kwa Gayo, amene anali mnzake. Iye anati: “Palibe chondisangalatsa koposa zinthu zimenezi, kumva kuti ana anga akuyendabe m’choonadi.”—3 Yoh. 4.
Yohane anayamikira Gayo chifukwa ‘chogwira ntchito mokhulupirika’ pothandiza abale ochezera mipingo. Mtumwiyu anati: “Tili ndi udindo wolandira bwino anthu oterowo ndi kuwachereza, kuti akhale antchito anzathu m’choonadi.”—3 Yoh. 5-8.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
11—N’chifukwa chiyani anthu ena amachita zinthu zoipa? Anthu ena amalephera kuzindikira kuti kuli Mulungu chifukwa chakuti alibe chikhulupiriro cholimba m’choonadi. Popeza kuti iwo sangamuone, amachita zinthu ngati kuti Mulunguyo sakuwaona.—Ezek. 9:9.
14—Kodi “mabwenzi” otchulidwa palembali ndi ndani? Palembali mawu akuti “mabwenzi” sakungonena za anthu okhawo amene amagwirizana kwambiri, koma Yohane anali kunenanso za anthu ena onse okhulupirira.
Zimene Tikuphunzirapo:
4. Akhristu okhwima mwauzimu amasangalala kwambiri akamaona achinyamata mu mpingo akupitiriza ‘kuyenda m’choonadi.’ Nawonso makolo amene athandiza ana awo kukhala okonda zinthu zauzimu, amakhala ndi chimwemwe chachikulu.
5-8. Ena mwa anthu amene amachita khama kuthandiza abale awo chifukwa chowakonda komanso chokonda Yehova, ndi oyang’anira oyendayenda, amishonale, otumikira pa Beteli kapena m’maofesi a nthambi ndiponso amene akuchita upainiya. Tiyenera kuwalimbikitsa anthu amenewa ndiponso kutsanzira chikhulupiriro chawo.
9-12. Tiyenera kutsanzira chikhulupiriro cha Demetiriyo osati Diotirefe yemwe ankakonda kujeda abale.
“KHALANIBE M’CHIKONDI CHA MULUNGU”
Yuda anafotokoza kuti anthu ena analowerera mu mpingo ndipo anali “okonda kung’ung’udza, okonda kudandaula za moyo wawo, ongotsatira zilakolako zawo.” Ndipo iwo ‘anali kulankhula modzitukumula, akumatamanda anthu ena.’—Yuda 4, 16.
Kodi Akhristu angatani kuti asatengere makhalidwe oipa? Yuda analemba kuti: “Okondedwa, kumbukirani mawu amene atumwi a Ambuye wathu Yesu Khristu ananena kalero.” Iye analembanso kuti: “Khalanibe m’chikondi cha Mulungu.”—Yuda 17-21.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
3, 4—N’chifukwa chiyani Yuda analimbikitsa Akhristu kuti ‘amenye zolimba nkhondo ya chikhulupiriro’? Chinali chifukwa chakuti ‘anthu ena analowa mozemba mumpingo.’ Anthu amenewa ‘anatenga kukoma mtima kwa m’chisomo kwa Mulungu wathu kukhala chifukwa cha khalidwe lotayirira.’
20, 21—Kodi tingatani kuti ‘tikhalebe m’chikondi cha Mulungu’? Tingachite zimenezi m’njira zitatu: (1) mwa kuyesetsa kuchita zinthu zogwirizana ndi ‘chikhulupiriro chathu choyera kopambana,’ pophunzira Mawu a Mulungu ndiponso kulalikira mwakhama; (2) “kupemphera m’mphamvu ya mzimu woyera”; kapena kuti motsogoleredwa ndi mzimuwo ndiponso (3) kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Khristu imene ingatithandize kupeza moyo wosatha.—Yoh. 3:16, 36.
Zimene Tikuphunzirapo:
5-7. Kodi anthu oipa angazembe chiweruzo cha Yehova? Zimenezi n’zosatheka. Umboni wake uli m’zitsanzo zitatu zotichenjeza zimene Yuda analemba.
8-10. Tiyenera kutsanzira chitsanzo cha Mikayeli mkulu wa angelo mwa kulemekeza anthu amene Mulungu wawapatsa udindo.
12. Anthu ampatuko amene amanamizira kuti ndi achikondi, ndi oopsa ngati mmene miyala ya pansi panyanja ilili kwa anthu oyenda pa sitima kapena osambira. Aphunzitsi onyenga angaoneke ngati owolowa manja, koma kwenikweni ali ngati mitambo yopanda madzi ndiponso sakonda n’komwe choonadi. Anthu amenewa alinso ngati mitengo yakufa yomwe singabereke zipatso. Adzazulidwa ngati mitengo n’kuwonongedwa. Choncho tiyenera kupewa anthu ampatuko.
22, 23. Akhristu oona amadana ndi zoipa. Anthu achikulire mwauzimu, makamaka akulu, amathandiza mwauzimu anthu “ena amene akukayikakayika,” pofuna kuwapulumutsa pamoto wa chiwonongeko chosatha.
[Zithunzi patsamba 28]
Madzi, mzimu ndi magazi zinachitira umboni kuti “Yesu ndi Mwana wa Mulungu”