MUTU 1
Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 YOHANE 5:3.
1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani mumakonda Yehova Mulungu?
KODI mumam’konda Mulungu? Ngati munadzipereka kale kwa Yehova Mulungu, mungayankhe motsimikiza kuti inde, ndipo mpake kutero. Mwachibadwa anthufe timakonda Yehova. Timakonda Mulungu chifukwa chakuti iyeyo ndi amene anayamba kutikonda. Baibulo limanena kuti: “Timasonyeza chikondi, chifukwa iye [Yehova] ndi amene anayamba kutikonda.”—1 Yohane 4:19.
2 Zoonadi, Yehova ndi amene anayamba kutikonda. Mwachitsanzo, anatipatsa dziko lapansi lokongola kuti tizikhalamo ndiponso amatipatsa zinthu zofunikira pa moyo. (Mateyu 5:43-48) Iye amatipatsanso zosowa zathu zauzimu, zomwe ndi zofunikira kwambiri. Mwachitsanzo, anatipatsa Mawu ake Baibulo, komanso amatiuza kuti tizipemphera kwa iye ndipo amatitsimikizira kuti amamvetsera mapemphero athu ndi kutipatsa mzimu wake woyera kuti uzitithandiza. (Salimo 65:2; Luka 11:13) Koposa zonse, anatitumizira Mwana wake wokondedwa kudzatiwombola ku uchimo ndi imfa. Kunena zoona, Yehova watisonyeza chikondi chachikulu kwambiri—Werengani Yohane 3:16; Aroma 5:8.
3. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu apitirize kutikonda? (b) Kodi ndi funso lofunika liti limene tiyenera kuliganizira, nanga yankho lake tingalipeze kuti?
3 Yehova ndi wofunitsitsa kupitiriza kutikonda mpaka kalekale. Komabe zili ndi ife kusankha kuchita zinthu zoti apitirizebe kutikonda kapena ayi. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: ‘Pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani . . . pamene mukuyembekezera kuti . . . mulandire moyo wosatha.’ (Yuda 21) Mawu akuti “pitirizani,” akusonyeza kuti tiyenera kuchita zinazake kuti Mulungu apitirizebe kutikonda. Tiyenera kusonyeza mwa zochita zathu kuti timam’konda Yehova. Funso lofunika kwambiri kuliganizira pamenepa ndi lakuti: ‘Kodi ineyo ndingasonyeze bwanji kuti ndimakonda Mulungu?’ Yankho la funso limeneli likupezeka m’mawu ouziridwa a mtumwi Yohane akuti: “Chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Tiyeni tione bwinobwino tanthauzo la mawu amenewa, chifukwa atithandiza kudziwa mmene tingasonyezere Mulungu wathu kuti timam’konda kwambiri.
ZIMENE “KUKONDA MULUNGU KUMATANTHAUZA”
4, 5. Fotokozani mmene munayambira kukonda Yehova.
4 Kodi mtumwi Yohane ankaganiza chiyani pamene analemba mawu ali pamwambawa? Musanayankhe funso limeneli, tayesani kukumbukira nthawi imene munayamba kukonda Yehova.
5 Taganizirani nthawi imene munayamba kuphunzira choonadi chonena za Yehova ndi zolinga zake komanso pamene munayamba kumukhulupirira. Munadziwa kuti munabadwa ndi uchimo ndipo simunali pa ubwenzi ndi Mulungu, koma Yehova anakutsegulirani njira kudzera mwa Khristu kuti mudzakhale angwiro komanso mudzapeze moyo wosatha umene Adamu anautaya. (Mateyu 20:28; Aroma 5:12, 18) Kenako munayamba kumvetsa kuti zimene Yehova anachita potumiza Mwana wake wokondedwa kwambiri kuti adzakufereni zinasonyeza kuti amakukondani kwambiri. Zimenezi zinakukhudzani mtima ndipo munayamba kukonda Mulungu chifukwa anakusonyezani chikondi chachikulu.—Werengani 1 Yohane 4:9, 10.
6. Kodi tingasonyeze bwanji chikondi chenicheni, nanga kodi kukonda Mulungu kunakulimbikitsani kuchita chiyani?
6 Komabe zimenezo zinali chiyambi chabe chokonda Yehova kuchokera pansi pa mtima. Kukonda Yehova kuchokera pansi pa mtima, kumafuna zambiri osati kungonena kuti, “Ndimakonda Yehova.” Mofanana ndi chikhulupiriro, chikondi chenicheni chimaonekeramu zochita zathu. (Yakobo 2:26) Timasonyeza chikondi pochita zinthu zimene zimakondweretsa munthu amene timamukondayo. Choncho, pamene chikondi chanu pa Yehova chinayamba kukula mumtima mwanu, munayamba kufunitsitsa kuchita zinthu zokondweretsa Atate wanu wakumwamba. Kodi ndinu Mboni yobatizidwa? Ngati zili choncho, kudzipereka komanso chikondi chanu chochokera pansi pa mtima chinakupangitsani kusankha chinthu chofunika kwambiri m’moyo wanu. Munadzipereka kwa Yehova kuti muchite chifuniro chake, kenako munabatizidwa posonyeza kudzipereka kwanu. (Werengani Aroma 14:7, 8.) Mtumwi Yohane anafotokozanso chimene muyenera kuchita kuti mukwaniritse lonjezo limeneli, lomwe munapanga kwa Yehova.
“KUSUNGA MALAMULO AKE”
7. Kodi ena mwa malamulo a Mulungu ndi ati, ndipo kodi kusunga malamulo amenewa kumaphatikizapo chiyani?
7 Yohane anafotokoza kuti kukonda Mulungu kumatanthauza “kusunga malamulo ake.” Kodi malamulo a Mulungu amenewa ndi ati? Yehova amatipatsa malamulo osiyanasiyana kudzera m’Mawu ake, Baibulo. Mwachitsanzo, iye amaletsa makhalidwe monga kumwa mwauchidakwa, dama, kupembedza mafano, kuba ndi kunama. (1 Akorinto 5:11; 6:18; 10:14; Aefeso 4:28; Akolose 3:9) Kusunga malamulo a Mulungu kumaphatikizapo kutsatira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino pa moyo wathu.
8, 9. Kodi tingadziwe bwanji zimene zimakondweretsa Yehova pa nkhani zimene zilibe malamulo ake m’Baibulo? Perekani chitsanzo.
8 Komabe, kuti tikondweretse Yehova, tifunikira kuchita zambiri kuwonjezera pa kutsatira malamulo amene anatchulidwa m’Baibulo. Yehova sanachite kutipatsa malamulo pa chilichonse chimene timachita. Choncho, tsiku lililonse timakumana ndi nkhani zimene zilibe malamulo ake m’Baibulo. Zikatero, kodi tingadziwe bwanji zimene zingakondweretse Yehova? M’Baibulo muli nkhani zimene zingatithandize kudziwa bwinobwino mmene Mulungu amaganizira. Choncho, tikamaphunzira Baibulo timadziwa zimene Yehova amakonda komanso zimene amadana nazo. (Werengani Salimo 97:10; Miyambo 6:16-19) Timayamba kudziwa makhalidwe ndi zochita zimene zimamukondweretsa. Tikamaphunzira zambiri zokhudza makhalidwe a Yehova komanso zochita zake, timatha kusankha ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi maganizo ake. Zimenezi zikutanthauza kuti, ngakhale kuti m’Baibulo mulibe lamulo lokhudza nkhani inayake, tingathe kudziwabe “chifuniro cha Yehova.”—Aefeso 5:17.
9 Mwachitsanzo, m’Baibulo mulibe malamulo oletsa kuonera mavidiyo ndi mapulogalamu a pa TV oonetsa zachiwawa kapena zachiwerewere. Komabe, n’zachidziwikire kuti kuonera zimenezi si koyenera. Timadziwa mmene Yehova amaonera zinthu zimenezi. Mawu ake amanena kuti: “[Yehova] amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” (Salimo 11:5) Baibulo limanenanso kuti: “Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.” (Aheberi 13:4) Tikamaganizira mawu ouziridwa amenewa, tingathe kuzindikira chifuniro cha Yehova. Choncho, timasankha kusaonera zinthu zimene zimasonyeza makhalidwe amene Mulungu wathu amadana nawo. Tikudziwa kuti Yehova amasangalala tikamapewa zinthu zonyansa zimene dzikoli limaziona ngati zosangalatsa zabwinobwino.a
10, 11. Kodi n’chifukwa chiyani timasankha kumvera Yehova, ndipo kumvera kwathu kuyenera kukhala kotani?
10 Kodi chifukwa chenicheni chimene timasungira malamulo a Mulungu n’chiyani? N’chifukwa chiyani timafuna kuti tsiku lililonse tizichita zinthu zimene tikudziwa kuti ndi zogwirizana ndi maganizo a Mulungu? Timachita zimenezi osati chabe chifukwa choopa kudzalangidwa kapena chifukwa chongofuna kupewa mavuto amene amagwera anthu osachita chifuniro cha Mulungu. (Agalatiya 6:7) M’malomwake, timaona kuti kumvera Yehova ndi mwayi wamtengo wapatali chifukwa kumatipatsa mpata womusonyeza kuti timamukonda. Mofanana ndi mwana amene amafuna kusangalatsa bambo ake, ifenso timafuna kusangalatsa Yehova. (Salimo 5:12) Iye ndi Atate wathu ndipo timamukonda. Chimene chimatisangalatsa kwambiri kapena kutibweretsera mtendere wa mumtima ndi kudziwa kuti tikuchita zinthu zokondweretsa Yehova.—Miyambo 12:2.
11 Choncho, timamvera Yehova nthawi zonse popanda kunyinyirika.b Sitichita kusankha kumvera malamulo amene akutikomera n’kusiya amene sakutikomera. Koma timamvera “mochokera pansi pa mtima.” (Aroma 6:17) Mumtima mwathu timamva ngati wamasalimo amene ananena kuti: “Ndidzakondwera ndi malamulo anu, amene ndimawakonda.” (Salimo 119:47) Zoonadi, timakonda kumvera Yehova. Timadziwa kuti iye ndi woyenera kumumvera ndiponso amafuna kuti tizimumvera ndi mtima wathu wonse. (Deuteronomo 12:32) Timafuna kukhala ngati Nowa yemwe anali munthu wokhulupirika ndipo anasonyeza kuti ankakonda Mulungu pomumvera kwa zaka zambirimbiri. Ndipo Baibulo limati: “Nowa anachita zonse motsatira zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi momwemo.” Ifenso timafuna kuti Yehova azitiona kuti ndife anthu omvera.—Genesis 6:22.
12. Kodi mtima wa Yehova umakondwera tikamamumvera motani?
12 Kodi Yehova amamva bwanji tikamamumvera mwakufuna kwathu? Mawu ake amanena kuti tikamatero, ‘timakondweretsa mtima’ wake. (Miyambo 27:11) Kodi n’zoonadi kuti tikamamvera timakondweretsa mtima wa Ambuye Wamkulu Koposa m’chilengedwe chonse? Inde. Ndipo Yehova ali ndi chifukwa chabwino chokhalira wokondwera ndi zimenezi. Tikutero chifukwa iye anatilenga ndi ufulu wosankha. Izi zikutanthauza kuti tingathe kusankha kumumvera kapena ayi. (Deuteronomo 30:15, 16, 19, 20) Choncho, tikasankha kumvera Yehova mwakufuna kwathu, ndipo ngati tasankha zimenezi chifukwa cha chikondi chathu chochokera pansi pa mtima, Atate wathu wakumwamba amakondwera kwambiri. (Miyambo 11:20) Komanso tikatero, ndiye kuti tasankha moyo wabwino kwambiri.
“MALAMULO AKEWO NDI OSALEMETSA”
13, 14. Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘malamulo a Mulungu ndi osalemetsa,’ ndipo tingayerekezere bwanji zimenezi?
13 Mtumwi Yohane akutiuza mfundo yolimbikitsa yokhudza malamulo a Yehova. Iye akuti: “Malamulo akewo ndi osalemetsa.”c Malamulo a Yehova si opanikiza kapena opondereza. Malamulo ake si oti munthu wopanda ungwiro angalephere kuwatsatira.
14 Tiyeni tiyerekezere kuti mnzanu akusamuka ndipo wakupemphani kuti mumuthandize kunyamula katundu. Pali katundu wambiri wofunika kusamutsidwa. Katundu wina ndi wopepuka woti munthu mmodzi angathe kunyamula bwinobwino, koma wina ndi wolemera kwambiri woti munthu mmodzi sanganyamule. Ndiye mnzanuyo akukusankhirani katundu woti munyamule. Kodi iye angakuuzeni kuti munyamule katundu amene akudziwa kuti simungathe kunyamula? Ayi. Iye sangafune kuti munyamule nokha katundu wolemera poopera kuti mungavulale. Mofanana ndi zimenezi, Mulungu wathu wachikondi komanso wokoma mtima sangatiuze kuti tisunge malamulo ovuta kuwatsatira. (Deuteronomo 30:11-14) Iye sangayese ngakhale pang’ono kutiuza kuti tinyamule katundu wolemera choncho. Yehova amadziwa zimene sitingathe kuchita chifukwa “akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.”—Salimo 103:14.
15. Kodi n’chifukwa chiyani tili ndi chikhulupiriro chakuti malamulo a Yehova amatipindulitsa kwambiri?
15 Malamulo a Yehova ndi osalemetsa ngakhale pang’ono ndipo amatipindulitsa kwambiri. (Werengani Yesaya 48:17.) N’chifukwa chake Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova anatilamula kuti tizitsatira malangizo onsewa, tiziopa Yehova Mulungu wathu, ndi kupindula nthawi zonse, kuti tikhale ndi moyo monga mmene zilili lero.” (Deuteronomo 6:24) Ifenso tili ndi chikhulupiriro chakuti potipatsa malamulo ake, Yehova amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino mpaka kalekale. Iye sangatilamule kuchita zinthu zimene zingatibweretsere mavuto. Yehova ndi Mulungu wanzeru zopanda malire. (Aroma 11:33) Choncho, iye amadziwa zinthu zimene zingatithandize kwambiri. Komanso Yehova ndiye chikondi. (1 Yohane 4:8) Iye amanena ndi kuchita zinthu zonse chifukwa cha chikondi, lomwe ndi khalidwe lake lalikulu. Malamulo ake onse amene amapereka kwa atumiki ake amawapereka chifukwa cha chikondi.
16. Ngakhale kuti m’dziko loipali timalimbana ndi zinthu zokopa komanso thupi lathu lopanda ungwiro, zingatheke bwanji kuti tikhalebe omvera?
16 Koma zimenezi sizikutanthauza kuti kumvera Mulungu n’kosavuta. Tikutero chifukwa chakuti timalimbana ndi zinthu zokopa za m’dzikoli, limene “lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Ndipo timalimbananso ndi thupi lathu lopanda ungwiro, limene limatichititsa kuphwanya malamulo a Mulungu. (Aroma 7:21-25) Koma ngati timakonda kwambiri Mulungu, tingathe kupambana nkhondoyi. Anthu amene amasonyeza kuti amakonda Yehova pokhala omvera amadalitsidwa. Iye amapereka mzimu wake woyera “kwa anthu omumvera monga wolamulira.” (Machitidwe 5:32) Mzimu umenewo umabala zipatso zabwino kwambiri mwa ife, ndipo zipatso zimenezo ndi makhalidwe apamwamba amene angatithandize kukhalabe omvera.—Agalatiya 5:22, 23.
17, 18. (a) Kodi m’bukuli tikambirana chiyani, ndipo pamene tikukambirana tiyenera kukumbukira zinthu ziti? (b) Kodi mutu wotsatira ufotokoza chiyani?
17 M’bukuli, tikambirana mfundo za Yehova ndi malamulo ake komanso nkhani zina zambiri zimene zingatithandize kudziwa chifuniro chake. Pamene tikukambirana, tikumbukire kuti Yehova satikakamiza kumvera malamulo ake ndiponso mfundo zake. Iye amafuna kuti tizimumvera mwakufuna kwathu komanso mochokera pansi pa mtima. Tisaiwalenso kuti Yehova amatiuza kuchita zinthu zimene zingatipatse madalitso ochuluka panopa komanso moyo wosatha m’tsogolo. Chinanso, tiziona kuti kumvera Yehova ndi mtima wathu wonse, ndi mwayi wamtengo wapatali chifukwa kumatipatsa mpata wosonyeza kuti timamukonda kwambiri.
18 Pofuna kutithandiza kusiyanitsa chabwino ndi choipa, Yehova mwachikondi anatipatsa chikumbumtima. Koma kuti chikumbumtima chathu chikhale chodalirika, tifunika kuchiphunzitsa. Mutu wotsatira ufotokoza zimenezi.
b Mizimu yoipa ingathenso kumvera koma monyinyirika. Mwachitsanzo, pamene Yesu analamula kuti ziwanda zituluke mwa anthu ogwidwa ndi mizimu yoipayi, ziwandazo zinazindikira mphamvu imene Yesu anali nayo ndipo zinamumvera koma monyinyirika.—Maliko 1:27; 5:7-13.
c Mawu akuti ‘olemetsa’ anagwiritsidwanso ntchito pa Mateyu 23:4, pofotokoza za “akatundu olemera,” omwe ndi miyambo ya anthu komanso malamulo ambirimbiri amene alembi ndi Afarisi ankakakamiza anthu wamba kuti azitsatira. Mawu omwewanso anatanthauziridwa kuti ‘kupondereza’ pa Machitidwe 20:29, 30, ndipo amanena za ampatuko opondereza amene anayamba “kulankhula zinthu zopotoka” pofuna kusocheretsa ena.