-
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?Nsanja ya Olonda—1997 | January 15
-
-
“Malamulo Ake Sali Olemetsa”
4-6. (a) Kodi tanthauzo lenileni nlotani la liwu lachigiriki lotembenuzidwa “cholemetsa”? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kunena kuti malamulo a Mulungu sali olemetsa?
4 “Kusunga malamulo ake.” Zimenezo makamaka nzimene Mulungu akufuna kwa ife. Kodi iye akupempha zopambanitsa? Kutalitali! Mtumwi Yohane akutiuza kanthu kena kolimbikitsa kwambiri ponena za malamulo a Mulungu, kapena zofuna zake. Analemba kuti: ‘Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.’—1 Yohane 5:3.
5 Liwu lachigiriki lotembenuzidwa “olemetsa” kwenikweni limatanthauza “cholemera.” Lingatanthauze chinthu chovuta kuchita kapena kukwaniritsa. Pa Mateyu 23:4, liwulo lagwiritsiridwa ntchito kufotokoza “akatundu olemera,” malamulo ndi miyambo yopangidwa ndi anthu, zimene alembi ndi Afarisi anaika pa anthu. Kodi mukumvetsa lingaliro limene mtumwi Yohane wokalambayo akupereka? Malamulo a Mulungu sali mtolo wolemetsa, ndipo sali ovuta kwambiri kwa ife kuwamvera. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:11.) M’malo mwake, pamene tikonda Mulungu, kukwaniritsa zofuna zake kumatipatsa chimwemwe. Kumatipatsa mwaŵi wamtengo wapatali wa kusonyeza chikondi chathu kwa Yehova.
-
-
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?Nsanja ya Olonda—1997 | January 15
-
-
12. Kodi mungafotokoze motani chifukwa chake kuloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu ndi zifuno zake sikuli mtolo wolemetsa?
12 Kodi kuloŵetsa chidziŵitso chotero chonena za Mulungu ndi zifuno zake kuli mtolo wolemetsa? Kutalitali! Kodi mukukumbukira mmene munamvera nthaŵi yoyamba pamene munadziŵa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, kuti Ufumu wake udzabwezeretsa Paradaiso padziko lapansi pano, kuti anapereka Mwana wake wokondedwa monga dipo la machimo athu, limodzinso ndi mfundo zina za choonadi chamtengo wapatali? Kodi simunamve ngati kukuchotsani chophimba cha kupulukira moti munayamba kuona zinthu bwinobwino? Kuloŵetsa chidziŵitso chonena za Mulungu si mtolo wolemetsa ayi. Kuli kosangalatsa!—Salmo 1:1-3; 119:97.
-
-
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?Nsanja ya Olonda—1997 | January 15
-
-
16. Fotokozani chifukwa chake sikuli mtolo wolemetsa kufika pa miyezo ya Mulungu ya khalidwe labwino ndi kulandira choonadi chake.
16 Kodi ndi mtolo wolemetsa kwa ife kufika pa miyezo ya Mulungu ya khalidwe labwino ndi choonadi chake? Osati ngati tilingalira za mapindu ake—maukwati mmene mwamuna ndi mkazi amakondana ndi kukhulupirirana m’malo mwa maukwati osweka chifukwa cha kusakhulupirika; nyumba mmene ana amamva kukhala okondedwa ndi ofunika kwa makolo awo m’malo mwa mabanja amene ana amamva kukhala osakondedwa, onyanyalidwa, ndi osafunika; chikumbumtima choyera ndi thanzi labwino m’malo mwa kumva liwongo ndi thupi kusakazidwa ndi AIDS kapena matenda ena opatsirana mwa kugonana. Ndithudi, zimene Yehova amafuna sizimatimanitsa kalikonse kamene tifunikira kuti tikondwere nawo moyo!—Deuteronomo 10:12, 13.
-
-
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?Nsanja ya Olonda—1997 | January 15
-
-
19. Fotokozani mmene timapindulira mwa kulemekeza moyo ndi mwazi.
19 Kodi ndi mtolo wolemetsa kwa ife kulemekeza moyo ndi mwazi monga zinthu zopatulika? Kutalitali! Tangolingalirani. Kodi ndi mtolo wolemetsa kupeŵa kansa ya kumapapu yochititsidwa ndi kusuta fodya? Kodi ndi mtolo wolemetsa kupeŵa kugodomala maganizo ndi thupi ndi anamgoneka oononga? Kodi ndi mtolo wolemetsa kupeŵa AIDS, hepatitis, kapena nthenda iliyonse yopatsidwa mwa kuikidwa mwazi? Mwachionekere, kupeŵa kwathu zizoloŵezi ndi machitachita oipa otero kuli kotipindulitsadi.—Yesaya 48:17.
20. Kodi banja lina linapindula motani mwa kukhala ndi kaonedwe ka Mulungu ka moyo?
20 Talingalirani chochitikachi. Zaka zingapo zapitazo, mkazi wina Mboni wa pathupi pa miyezi ngati itatu ndi theka anayamba kukha mwazi tsiku lina madzulo ndipo anamfulumizira ku chipatala. Dokotala atampima, mkaziyo anamumva akuuza nesi wina kuti adzafunikira kuchotsa mimbayo. Podziŵa mmene Yehova amaonera moyo wa mwana wosabadwa, iye anakana zolimba kuchotsa mimba, akumauza dokotalayo kuti: “Ngati ali wamoyo, msiyeni!” Anapitiriza kukha mwazi nthaŵi zina, koma patapita miyezi ingapo anabala mwana wamwamuna wathanzi miyezi isanakwane, amene tsopano ali ndi zaka 17. Mkaziyo anati: “Tinamuuza mwana wathu zonsezi, ndipo anati ali ndi mwaŵi kuti sanatayidwe. Amadziŵa kuti kutumikira kwathu Yehova ndiko kokha kwachititsa kuti akhalepobe ndi moyo.” Kunena zoona, kuona moyo mmene Mulungu amauonera sikunali mtolo wolemetsa pa banjali!
-
-
Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?Nsanja ya Olonda—1997 | January 15
-
-
23, 24. Kodi tingachitire chitsanzo motani kusonyeza kuti sikuli mtolo wolemetsa kutumikira Yehova limodzi ndi anthu ake olinganizidwa?
23 Kodi ndi mtolo wolemetsa kutumikira Yehova limodzi ndi anthu ake olinganizidwa? Kutalitali! M’malo mwake, ndi mwaŵi wamtengo wapatali kukhala ndi chikondi ndi chichirikizo cha banja la padziko lonse la abale ndi alongo achikristu! (1 Petro 2:17) Tayerekezerani kuti mwapulumuka ngozi ya chombo chomwe chasweka ndipo muli m’madzi, mukulimbikira kusambira. Pamene muona kuti mukulephera, mungoona dzanja likufika kwa inu kuchokera m’bwato lopulumutsira. Inde, alipo opulumuka ena! M’bwato lopulumutsiralo, mulandizana kupalasa ndi ena kulinga kumtunda, mukumatola opulumuka ena m’njira.
-