Sonyezani Chikondi ndi Chikhulupiriro Nthaŵi Zonse
“lye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu. . . . Ndipo ichi ndi chilako tililaka nacho dziko lapansi ndicho chikhulupiriro chathu.”—1 YOHANE 4:16; 5:4.
1, 2. Kodi ndimikhalidwe yotani imene yagogomezeredwa kwakukulukulu pa 1 Yohane 4: 7-5:21?
YEHOVA ndiye munthuyo wotchulidwa monga chikondi, ndipo awo okhumba kumkondweretsa ayenera kusonyeza mkhalidwe wa Mulungu umenewu. Mtumwi Yohane akumveketsa izi m’mbali yomalizira ya kalata yake yoyamba youziridwa.
2 Akristu owona ayeneranso kusonyeza chikhulupiriro. Kuli kokha mwanjirayi kuti iwo angathe kugonjetsa dziko nakhalabe otetezereka m’chiyanjo cha Yehova. Pamenepa, pamene tikuphunzira mbali yomalizira ya kalata ya Yohane, tiyeni tipende mwapemphero kufunika kwa kusonyeza chikondi ndi chikhulupiriro.
‘Tiyeni Tikondane’
3, 4. Kodi ndiunansi wotani umene kusonyeza chikondi kuli nako ndi kudziwa kwathu Mulungu?
3 Yohane akugogomezera kufunika kwa chikondi. (Werengani 1 Yohane 4:7, 8.) “Okondedwa” Achikristu akulimbikitsidwa “kupitirizabe kukondana wina ndi mnzake, chifukwa chakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu,” Yehova ndiye magwero ake. “Yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu [monga munthu wobadwa ndi mzimu] namzindikira Mulungu,” pokhala wozolowerana ndi mikhalidwe ya Yehova ndi zifuno ndi mmene amasonyezera chikondi. Lerolino “kudziwa Mulungu” kumeneko kwafikiridwanso ndi a “khamu lalikulu” a “nkhosa zina” za Kristu.
4 Kudziwa Mulungu kumatanthauzadi kuzindikira mikhalidwe yake, kumkonda kotheratu, ndi kumamatira kwa iye monga Mfumu yathu. Koma “iye wosakonda sazindikira Mulungu.” Awo amene samasonyeza chikondi Chachikristu “sazindikira Mulungu chifukwa Mulungu ndiye chikondi.” Inde, chikondi ndicho mkhalidwe waukulu wa Yehova, wowoneka m’makonzedwe ake auzimu ndi akuthupi kwa anthu.
5. Kodi ndiuti umene uli umboni waukulu koposa wakuti “Mulungu ndiye chikondi”?
5 Kenako pakutchulidwa umboni waukulu koposa wakuti “Mulungu ndiye chikondi.” (Werengani 1 Yohane 4:9, 10.) Yohane akuti: “Umo chidawoneka chikondi cha Mulungu mwa ife [monga ochimwa oyenerera imfa], kuti Mulungu anamtuma Mwana wake wobadwa yekha alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.” Yesu ali “Mwana wobadwa yekha” wa Yehova m’chakuti anali wolengedwa yekha mwachindunji wa Mulungu. (Yohane 1: 1-3, 14; Akolose 1:13-16) Ndipo Yesu ‘anatumidwa kulowa m’dziko lapansi’ mwa kukhala munthu, akumasenza utumiki wake poyera, ndiyeno kufa imfa yopereka nsembe. (Yohane 11:27; 12:46) ‘Kupeza moyo wosatha kupyolera mwa iye,’ kaya kumwamba kapena padziko lapansi, kumafunikiritsa chikhulupiriro m’mtengo wa nsembe yake ya dipo.
6. Pamene ife tinali chikhalirebe ochimwa kodindani amene sanakonde Mulungu, kodi iye anachitanji?
6 Tinali chikhalirebe ochimwa amene sanakonde Mulungu pamene “iye anatikonda ife natumiza Mwana wake akhale chiwombolo chifukwa cha machimo athu.” Nsembe ya Kristu inatitheketsa kufikira kubwezeretsedwa m’maunansi olungama ndi Mulungu. (Aroma 3:24, 25; Ahebri 2:17) Kodi mumayamikira kusonyezedwa kwakukulu kumeneku kwa chikondi chapadera kochitidwa ndi Atate wathu wakumwamba?
7. (a) Popeza kuti sitingathe kunena kuti timakonda Yehova chifukwa chakukhala titamuwonapo, kodi ndimotani mmene tingasonyezere kutitimamkonda? (b) Kusonyeza kwathu kukonda abale kumatsimikizira chiyani?
7 Chikondi cha Mulungu kwa ife chiyenera kuyambukira mkhalidwe wathu kulinga kwa ena. (Werengani 1 Yohane 4:11-13.) Popeza kuti iye anatikonda pamene ife tinali chikhalirebe ochimwa “ifenso tiyenera kukonda wina ndi mnzake.” Pakati pa anthu, “palibe munthu aliyense amene anawona Mulungu.” Chotero sitingathe kunena kuti timakonda Yehova chifukwa cha kukhala titamuwona. (Eksodo 33: 20; Yohane 1:18; 4:24) Komabe, mwa kusonyeza chikondi, timasonyeza kuti timakonda Magwero a mkhalidwe uwu. Kukonda kwathu abale kumatsimikizira kuti “Mulungu akhala mwa ife, ndi chikondi chake chikhala changwiro,” kapena kusonyezedwa mokwanira, mwa ife. Ndipo timazindikira kuti “tikhala mwa iye” Yehova “chifukwa anatipatsako mzimu wake.” Kusonyeza kwathu kukonda abale kumatsimikizira kuti mzimu wa Yehova umagwira ntchito mkati mwathu, chifukwa chakuti chikondi ndicho chimodzi cha zipatso zake. (Agalatiya 5: 22, 23) Ichi chimasonyeza kuti tidziwa Mulungu ndipo tiri ndi chiyanjo chake.
8. Kodi ndiumboni wowonjezereka wotani umene ulipo wakuti tiri ‘m’chigiwirizano ndi Mulungu’?
8 Pali umboni wowonjezereka wakuti ife tiri “mwa Mulungu.” (Werengani 1 Yohane 4:14-16a.) Pokhala ‘titawona’ zimene Yesu anachita padziko lapansi ndi mmene anavutikira mmalo mwa anthu, Yohane akanakhoza ‘kuchitira umboni wakuti Atate anatumiza Mwana Wake kukhala Mpulumutsi wa dziko’ la anthu ochimwa. (Yohane 4:42; 12:47) Ndiponso, ‘Mulungu amakhalabe m’chigwirizano ndi ife ndipo ife ndi iye’ ngati tivomereza ndi mtima wonse kuti Yesu Kristu ali Mwana wake. Izi zimafunikiritsa kusonyeza chikhulupiriro ndi kupereka umboni wapoyera wakuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. (Yohane 3:36; Aroma 10:10) Chidaliro chathu mu “chikondicho Mulungu ali nacho pa ife” chimapereka umboni wowonjezereka wakuti ife amene tiri a otsalira odzozedwa ndi a “nkhosa zina” tiri m’chigwirizano ndi Yehova.
9. (a) Ndim’lingaliro lotani m’limene kukonda Mulungu ‘kungapangidwe kukhala kwangwiro,’ ndipo ichi chidzayambukira motani unansi wa thu ndi ena? (b) Kodi chikondi “changwiro” chimapititsa patsogolo chiyani?
9 Kenako Yohane akusonyeza kuti chikondi chingathe ‘kukhala changwiro’ (Werengani 1 Yohane 4:16b, 17.) Tikukumbutsidwa kuti “Mulungu ndiye chikondi.” Chifukwa chakuti ife ‘tikhalabe m’chikondi,’ mwa kusonyeza chipatso ichi chamzimu wa Mulungu, ‘timakhalabe m’chigwirizano ndi Mulungu.’ Ngati chikondi chathu kwa Yehova “chakhala changwiro,” pokhala chitafikira mlingo wokwanira kwa iye, tidzakonda okhulupirira anzathu. (Yerekezerani ndi vesi 12.) Chikondi “changwiro” chimapititsanso patsogolo ‘ufulu wa kulankhula’ ndi Mulungu m’pemphero tsopano ndi “m’tsiku la mlandu” limene liri logwirizanitsidwa ndi ku khalapo kwa Kristu. Pamenepo awo osonyeza chikondi chotero sadzakhala ndi chifukwa cha kuchitira mantha akuti chiweruzo cha Mulungu chidzakhala chowatsutsa. Ngati tisonyeza chikondi, m’lingaliro limenelo “monga iyeyo [Yesu] ali, momwemo tiri ife m’dziko lino lapansi.” Inde, tiri ofanana naye m’kukhala ndi chiyanjo monga ana a Mulungu m’dziko lino la anthu okhala paudani ndi Mulungu.
10. Kodi awo amene chikondi chawo chapangidwa kukhala “changwiro” samakhala nchiyani?
10 Awo amene chikondi chawo chapangidwa kukhala “changwiro” samachita mantha ogwirizanitsidwa ndi pemphero. (Werengani 1 Yohane 4:18, 19.) “Mantha ali nacho chilango” chimene chingatilepheretse kuyandikira Yehova mwaufulu. Chotero ngati tiri ndi mantha otero, ‘sitinapangidwe angwiro m’chikondi.’Koma ngati tapangidwa “angwiro m’chikondi,” mkhalidwe uwu umadzadza mitima yathu, umatisonkhezera kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo umatisonkhezera kukhala pafupi ndi Atate wathu wakumwamba m’pemphero. Ndithudi ife tiri ndi chifukwa chabwino cha kukondera Yehova ndi kupemphera kwa iye, pakuti monga momwe Yohane akunenera, ‘tikonda, chifukwa chakuti anayamba iye kutikonda.’
11. Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kuti timvere lamulo lakuti “Iye wokonda Mulungu akondenso mbale wake”?
11 Ndithudi, sikuli kokwanira kungonena kokha kuti timakonda Mulungu. (Werengani 1 Yohane 4:20, 21.) Aliyense wakunena kuti “ndikonda Mulungu” pamene akudana ndi mbale wake wauzimu “ali wabodza.” Popeza kuti tingathe kuwona mbale wathu ndi kuwona zikhoterero zake zaumulungu, kumkonda kuyenera kukhala kosavutirapo kwambiri kuposa kukonda Mulungu wosawonekayo. Ndithudi, “iye wosakonda mbale wake amene wamuwona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuwona.” Chotero kuli kwanzeru kuti timvere “lamulo” limeneli lakuti: “Iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.”
Kodi Ndani Amene Amalaka Dziko?
12. Popeza kuti timakonda Mulungu, kodi nchikondi china chotani chimene tingayembekezeredwe kukhala nacho?
12 Kenako Yohane akusonyeza chimene kwenikweni kukonda Mulungu kumatanthauza. (Werengani 1 Yohane 5:1-5.) Choyamba, mtumwiyo akusonyeza kuti “yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Kristu,” (Mesiya kapena Wodzozedwayo wa Yehova) “wabadwa kuchokera kwa Mulungu,” kapena wabadwa ndi mzimu wa Yehova. Ndiponso, aliyense amene amakonda Wobalayo, Yehova, amakonda munthu ali yense “amene anabadwa wochokera mwa iyeyo.” Inde, ana onse odzozedwa a Mulungu amamkonda ndipo angayembekezeredwe kukondana. Kukonda abale kotero kukusonyezedwanso ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” lokhala ndi ziyembekezo za padziko lapansi.—Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9.
13. (a) Kodi nchifukwa ninji malamulo a Mulungu saali “olemetsa” kwa ife? (b) Kodi ndimotanimmene ‘timalilakira dziko’?
13 ‘Tizindikira kuti tikonda ana a Mulung pamene tikonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake.’ Kwenikweni, ‘kukonda Mulungu kumatanthauza kuti tisunge malamulo ake.’ Popeza kuti timakonda Mulungu ndi chilungamo, tiri achimwemwe kusunga malamulo ake. Yohane akunena kuti malamulowo saali “olemetsa” kwa ife “pakuti chirichonse chobadwa mwa Mulungu chililaka dziko lapansi.” “Chirichonse” chingatanthauze mphamvu yoperekedwa ndi Mulungu ya ‘kulakira dziko,’ kapena kulakika pa chimangidwe cha anthu chosalungama limodzi ndi mayeso ake a kuswa malamulo a Yehova. (Yohane 16:33) “Ichi ndichilako tililaka nacho dziko lapansi” ndicho “chikhulupiriro chathu” mwa Mulungu, Mawu ake ndi Mwana wake. Ngati tiri ndi “chikhulupiriro chakuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu,” ‘timalilaka dziko’ mwa kukana maganizo ake olakwika ndi achisembwere ndi mwa kusunga malamulo a Mulungu.
14. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anadzera “mwa madzi”? (b) Kodi Kristu anasonyeza motani kukhala Mwana wa Mulungu “ndi mwazi”? (c) Kodi mzimu woyera ‘umachitira umboni’ mo tani za Yesu Kristu?
14 Popeza kuti kukhulupirira Yesu kuli kofunika kwambiri kuti tikhale ‘olaka dziko,’ Yohane akutchula umboni woperekedwa wonena za Kristu ndi “atatu a kuchita umboni.” (Werengani 1 Yohane 5:6-8.) Choyamba Yohane akunena kuti Yesu “anadza mwa madzi.” Pamene Yesu anabatizidwa m’madzi kusonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu, Yehova analengeza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3: 17) Kristu anasonyezedwanso kukhala Mwana wa Mulungu “ndi mwazi” umene anatsanulira mu imfa yake monga dipo. (1 Timoteo 2:5, 6) Kwakukulukulu, Yohane akuti, “mzimu [woyera] ndiye wakuchita umboni, chifukwa mzimu ndiye chowonadi.” Kutsika kwa mzimu pa Yesu paubatizo wake kunamtsimikizira kukhala Mwana wa Mulungu. (Mateyu 3:16; Yohane 1: 29-34) Mzimu wa Yehova unakhozetsa Yesu kukwaniritsa ntchito yake ndi kuchita ntchito zamphamvu. (Yohane 10:37, 38; Machitidwe 10:38) Mwamzimu, Mulungu anachititsa mdima wapadera, chivomezi, ndi kung’ambika kwa chisalu chochinga cha m’kachisi pamene Yesu anafa, ndiyeno mwa mzimu umodzimodziwo Mulungu anamuukitsa.—Mateyu 27: 45-54.
15. Kodi ndani amene ali “atatu a kuchita umboni”?
15 Motero “pali atatu a kuchita umboni” wa chenicheni chakuti Yesu ali Mwana wa Mulungu. Amenewa ndiwo (1) mzimu woyera, (2) madzi aubatizo wa Yesu ndi chimene unaimira (kudzipereka kwa iyemwini kwa Yehova), ndi (3) mwazi umene anautsanulira mu imfa monga dipo. Atatu amenewa “ali amodzi” m’kupereka umboni wakuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu, mwa amene tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chowona ngati titi tilandire moyo wamuyaya.—Yerekezerani ndi Deuteronomo 19:15.
Umboni Wochitidwa ndi Mulungu
16. Kodi ndimotani mmene Yehova wachitira umboni ponena za Yesu?
16 Mulungu mwiniyo wachitira umboni wonena za Mwana wake. (Werengani 1 Yohane 5:9-12.) “Ngati tilandira umboni [kukhala wowona] kwa anthu [opanda ungwiro], [monga momwe mwachizolowezi timachitira pokambitsirana ndi m’bwalo lamilandu], umboni wa Mulungu uposa.” (Yohane 8:17, 18) Popeza kuti ‘Mulungu sangathe kunama,’ tingathe kuika chidaliro chotheratu mu ‘umboni umene waupereka ponena za Mwana wake.’ Ndipo Yehova wanena kuti Yesu Kristu ali Mwana wake. (Tito 1:2; Mateyu 3:17; 17:5) Ndiponso, Mulungu anali mchirikizi wa “atatu a kuchita umboni” ndiko kuti, mzimu Wake woyera, madzi aubatizo wa Yesu, ndi mwazi wokhetsedwa wa Kristu.
17. Kodi ndiiti imene iri njira yokha mwa imene chipulumutso chiri chotheka?
17 “lye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboni mwa iye,” kapena “mwa iyemwini,” chifukwa chakuti umboni wonse umamkhutiritsa kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu. Koma “wosakhulipirira Mulungu” monga mboni yodalirika yonena za Mwana Wake amapangitsa Yehova kuwonekera kukhala wabodza. Ndithudi, kuchuluka kwa umboni woperekedwa nkwakuti “Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wake.” Kuli kokha kudzera mwa Yesu monga Mwana wa Mulungu kuti chipulumutso kumoyo wamuyaya chiri chotheka. (Yohane 11:25, 26; 14:6; 17:1-3) Chotero “iye wakukhala ndi Mwana” mwa kumkhulupirira ali ndi mphotho yachisomo ya moyo wamuyaya. (Yohane 20:31) Koma “moyo uwu” sudzapatsidwa kwa aliyense wopanda chikhulupiriro mwa Yesu monga Mwana wa Mulungu.
Pemphero Limagwira Ntchito!
18. Kodi nchifukwa ninji Yohane analemba “zinthu izi”?
18 Kenako Yohane akupereka chifuno chachikulu cha kalata yake ndipo akulongosola pemphero. (Werengani 1 Yohane 5:13-15.) Iye walemba ‘zinthu izi’ kotero kuti kudziwike kuti ‘tiri ndi moyo wosatha.’ Ichi ndicho chikhutiro chathu cha iwo a kukhulupirira “m’dzina” la Mwana wa Mulungu. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 3:23.) Ndipo ampatuko, amene saali athu, sangathe kuwononga chikhulupiriro chimenecho.—1 Yohane 2:18, 19.
19. (a) Mogwirizana ndi kunena kwa 1 Yohane 5:14, 15, kodi ndi ‘chidaliro’ chotani chimene tiri nacho kulinga kwa Mulungu? (b) Kodi nziti zimene ziri zinthu zina zimene moyenerera tingapempherere?
19 Ife tiri ndi “chidaliro” kwa Mulungu, kapena “kulimbika mtima,” kwakuti mosasamala kanthu chimene tipempha m’pemphero “monga mwa chifuniro chake, atimvera. ” Moyenerera timapempherera zinthu zonga kulemekezedwa kwa dzina la Yehova, mzimu wake, nzeru yaumulungu, ndi kulanditsidwa kwa woipayo. (Mateyu 6:9, 13; Luka 11:13; Yakobo 1:5-8) Ndipo “tidziwa kuti tiri nazo izi tazipempha kwa iye,” “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.
20, 21. (a) Kodi nchiyani chimene chiri “tchimo losati la kuimfa”? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kulakwa kupempherera “tchimo la kuimfa”?
20 Kenako Yohane akulankhula za pemphero ndi mitundu iwiri yauchimo. (Werengani 1 Yohane 5:16, 17.) “Tchimo losati la kuimfa” siriri ladala, ndipo sikukanakhala kulakwa kupempherera wochita cholakwa wolapa kuti akhululukidwe. (Machitidwe 2:36-38; 3:19; Yakobo 5:13-18) Koma kukakhala kulakwa kupempherera “tchimo la kuimfa” chifukwa chakuti limeneli liri kuchimwira dala mzimu woyera, kaamba ka limene chikhululukiro chiri chosatheka (Mateyu 12:22-32; Ahebri 6:4-6; 10:26-31) Ochimwa otero amapita ku Gehena, amakumana ndi chiwonongeko chosatha mu “imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 21:8; Mateyu 23:15) Chotero pamene kuli kwakuti Yehova ndiye Woweruza womalizira, ife sitimafunikira kuputa kusamkondweretsa mwa kupempherera wochimwa ngati pali umboni wosonyeza kuti iye ali ndi liwongo la “tchimo la kuimfa” ladala.
21 Chifukwa chake, “wina [makamaka mkulu wodzozedwa ndi mzimu] akawona mbale wake alimkuchimwa tchimo losati la kuimfa [“imfa yachiwiri”], apemphere Mulungu, ndipo iye [Mulungu] adzampatsira moyo [wochimwayo],” akumampulumutsa ku chiwonongeko chamuyaya. Ndithudi, “chosalungama chirichonse chiri uchimo,” kapena kuphonya chizindikiro malingana ndi muyezo wolungama wa Mulungu. ‘Komabe pali uchimo umene sumachititsa imfa’ chifukwa chakuti umachokera m’kupanda kwathu ungwiro, ngati tiri olapa, uchimowo umakwiriridwa ndi nsembe ya Kristu.
Mfundo Zazikulu za Kalata ya Yohane
22. Kodi ndani amene ‘samagwiritsitsa zolimba’ pa Mkristu wokhulupirika, ndipo kodi munthu wotero angapempherere chiyani ndi chidaliro?
22 Tsopano Yohane akufotokoza mwachidule mfundo zazikulu m’kalata yake. (Werengani 1 Yohane 5:18-21.) Aliyense “wobadwa kuchokera mwa Mulungu” monga Mkristu wodzozedwa ndi mzimu “sachimwa.” Yesu Kristu, “Wobadwa kuchokera mwa Mulungu” mwa mzimu woyera, ‘amyang’anira, ndipo woipayo [Satana] samamgwiritsitsa zolimba.’ Mkristu wodzozedwa wokhulupirika wotero angathe kupemphera mwachidaliro kaamba ka chilanditso kuchokera kwa woipayo ndipo angathe, mogwiritsira ntchito ‘chishyango chachikulu cha chikhulupiriro,’ kupewa chivulazo chauzimu chochokera ku ‘mivi yoyaka moto’ ya Satana.—Mateyu 6:13; Aefeso 6:16.
23. Kodi ndimotani mmene ‘dziko lonse limagonera m’mphamvu ya woipayo’?
23 Popeza kuti odzozedwawo ali ndi umboni wakuti ali ana auzimu a Yehova, iwo angathe kunena kuti, “Tidziwa kuti tiri ife ochokera mwa Mulungu.” Chenicheni chakuti iwo amakhulupirira Kristu ndipo saali ndi chizolowezi cha uchimo chimatsimikizira kuti ali ana a Mulungu amene Satana wakhala wosakhoza ‘kuwagwiritsitsa.’ “Ndipo dziko lonse lapansi [anthu osalungama] ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (Aefeso 2:1, 2; Chivumbulutso 12:9) Dziko limagonjera ku chisonkhezero choipa cha Satana ndi ulamuliro, silimapanga kuyesayesa kuwonjoka kotero kuti lichite chifuniro cha Mulungu.
24. Kodi ndikumlingo wotani ku umene Yesu ‘watipatsira chidziwitso’?
24 Aphunzitsi ena onyenga anaumirira pa kunena kuti Kristu sanadze m’thupi. (2 Yohane 7) Koma maumboni otchulidwa m’kalata iyi amakhozetsa Yohane kunena kuti, “Tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika.” (1 Yohane 1: 1-4; 5:5-8) Ndiponso, Yesu ‘anatipatsa ife chidziwitso,’ kapena “chizindikiro cha maganizo,” kotero kuti “tizindikire wowonayo,” chidziwitso chopita patsogolo cha Mulungu. (Mateyu 11:27) Chotero ‘tiri m’chigwirizano ndi wowonayo [Yehova Mulungu], kudzera mwa Mwana wake Yesu Kristu.’—Yerekezerani ndi Yohane 17:20, 21.
25. Monga Akristu, kodi ndimotani mmene tingagwiritsirire ntchito uphungu wa pa 1 Yohane 5:21?
25 Okhala m’chigwirizano ndi Mulungu wowona, Yehova, kaya akhale otsalira odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” amafuna kumkondweretsa m’njira iriyonse. Koma mayeso akulowe tsedwa m’kulambira mafano analipo m’zaka za zana loyamba, monga momwedi aliri lerolino. Chotero moyenerera Yohane akumaliza kalata yake mwa kupereka uphungu wautate wakuti: “Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano.” Monga Akristu, sitimaweramira mafano. (Eksodo 20:4-6) Timadziwanso kuti kukakhala kulakwa kudziikira ife eni, chisangalalo, kapena kanthu kena kalikonse mmalo a Mulungu. (2 Timoteo 3:1, 2, 4) Ndipo kudzipatulira kwathu kwa iye kumakaniza kulambira kwathu “chirombo” chandale zadziko ndi “fano” lake. (Chivumbulutso 13:14-18; 14:9-12) Chotero ncholinga cha kukondweretsa Atate wathu wakumwamba ndi kulandira mphatso yake ya moyo wosatha, tiyeni titsimikizire m’chitsimikizo chathu cha kupewa kulambira mafano konse, osakulola konse kuwononga unansi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova kudzera mwa Yesu Kristu
Chithandizo Chokhalitsa kwa Ife
26. Kodi ndiziti zimene ziri mbali zina zofunika za Yohane Woyamba?
26 Kalata yoyamba youziridwa ya Yohane inathandiza Akristu oyambirira kukaniza kulambira mafano. Inawakhozetsa kugonjetsa mabodza a ampatuko, ndipo imatumikira chifuno chofananacho lerolino. Mwachitsanzo, imatsimikizira kuti Yesu anali munthu nafa kukhala “nsembe ya dipo” kaamba ka machimo athu. Kalatayo imasonyeza “okana Kristu” ndi kulekanitsa pakati pa ana a Mulungu ndi a Mdyerekezi. Imasonyeza mmene tingayesere “mawu ouziridwa” kuwona kuti kaya akuchokera kwa Yehova kapena ayi. Ndiponso, mawu a Yohane amatikhutiritsa kuti “Mulungu ndiye chikondi,” kuti chikhulupiriro chowona chimalaka dziko, ndi kuti Yehova amamva mapemphero a Mboni zake zokhulupirika.
27. Kodi ndim’njira zotani m’zimene kalata yoyamba youziridwa ndi Mulungu ya Yohane imatithandizira?
27 Poyang’anizana ndi mayeso a dziko, nkwanzeru chotani nanga kukumbukira chenjezo la Yohane lotsutsa kukonda dziko! Ngati mavuto athu angapereke vuto paunansi wathu ndi okhulupirira anzathu ena, mawu a mtumwiyo angatikumbutse kuti tingadzitsimikizire kukhala okonda Mulungu mwa kusonyeza abale chikondi. Mwa chithandizo cha Mulungu ndi mwa kugwiritsira ntchito uphungu wa Yohane, tingathe kupewa kuchita chizolowezi cha uchimo ndi kusunga chikhulupiriro chimene chimalaka dziko. Chotero tiyeni tisonyeze chiyamikiro chathu kaamba ka kalata youziridwa iyi pamene tikupitirizabe kuyenda m’kuunika kwa Mulungu, tikumapitirizabe kukhala ndi moyo monga ana a Mulungu ndi kusonyeza chikondi ndi chikhulupiriro nthawi zonse ku ulemerero wa Atate wathu wakumwamba, Yehova.
Kodi Mukanayankha Motani?
◻ Ngati tikonda Yehova, kodi uku kuyenera kuyambukira motani unansi wathu ndi okhulupirira anzathu?
◻ Kodi ndimotani mmene ‘tingalakire dziko’?
◻ Kodi ndani amene ali “atatu a kuchita umboni” wonena za Mwana wa Mulungu?
◻ Ponena za pemphero, kodi ‘nchidaliro’ chotani chimene tiri nacho?
◻ Kodi Yohane Woyamba angatithandize ife m’njira zotani?
[Mawu Otsindika patsamba 15]
Popeza kuti Yehova anatikonda pamene tinali chikhalire ochimwa, ‘tiri ndi thayo la kukondana win a mnzake’
[Mawu Otsindika patsamba 16]
Kukhulupirira kwathu Mulungu, Mawu ake, ndi Mwana wake wobadwa yekha kumatikhozetsa ife ‘kulaka dziko’
[Chithunzi pa tsamba 18]
Mzimu woyera, madzi aubatizo wa Yesu, mwazi wake, wokhetsedwa, ndi Yehova iyemwini anachitira umboni wakuti Yesu Kristu ndiye Mwana wa Mulungu