Zimene Owerenga Amafunsa
N’chifukwa Chiyani Mulungu Sayankha Mapemphero Ena?
Tonsefe tingathe kupemphera kwa Mulungu. Mofanana ndi bambo wachikondi amene amafuna kuti ana ake azilankhula naye momasuka, Yehova Mulungu amafuna kuti tizipemphera kwa iye. Komanso mofanana ndi bambo aliyense wanzeru, Mulungu sayankha zopempha zonse ndipo ali ndi zifukwa zomveka zochitira zimenezi. Kodi zifukwazo n’zachinsinsi kapena zinatchulidwa m’Baibulo?
Mtumwi Yohane anati: “Ndipo ife timam’dalira kuti chilichonse chimene tingapemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Motero zopempha zathu ziyenera kugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Anthu ena amapempha zinthu zosemphana ndi chifuniro cha Mulungu. Mwachitsanzo, ena amapempha kuti awine njuga kapena mpikisano wina uliwonse. Enanso amapempherera zinthu zimene akufuna kuzigwiritsa ntchito molakwika. Wophunzira Yakobe ananena kuti tisamachite zimenezi. Iye anati: “Mumapempha koma simulandira, chifukwa mukupempha ndi cholinga choipa, kuti mukakhutiritse zilakolako za matupi anu.”—Yakobe 4:3.
Tayerekezerani kuti pali matimu awiri amene akufuna kusewera mpira. Timu iliyonse ikupemphera kuti iwine. N’zosatheka kuti Mulungu ayankhe mapemphero otsutsanawo. N’chimodzimodzinso ndi anthu amene amapemphera kwa Mulungu kuti asilikali a mbali yawo apambane pankhondo. Mulungu sangayankhenso mapemphero oterewa.
Mulungu sayankha mapemphero a anthu amene safuna kutsatira malamulo ake. Panthawi ina Yehova anauza anthu amene ankamutumikira mwachinyengo kuti: “Pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.” (Yesaya 1:15) Baibulo limanenanso kuti: “Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.”—Miyambo 28:9.
Komabe nthawi zonse Yehova amamvetsera mapemphero a anthu amene amayesetsa kumutumikira mogwirizana ndi chifuniro chake. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti iye angawapatse chilichonse chimene angapemphe? Ayi. Taonani zitsanzo za m’Malemba zotsatirazi.
Mose ankagwirizana kwambiri ndi Mulungu kuposa munthu aliyense wa m’nthawi yake, koma nayenso anafunika kupemphera “mogwirizana ndi chifuniro [cha Mulungu].” Mosemphana ndi chifuniro cha Mulungu Mose anapempha Mulungu kuti amulowetse m’dziko la Kanani. Iye anati: “Ndiwoloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordano.” Izi zisanachitike Mose anachimwa ndipo anauzidwa kuti sadzalowa m’dzikolo. Motero m’malo molola zimene Mose anapempha, Yehova anamuyankha kuti: “Chikukwanire, usawonjezenso kunena ndi ine za chinthuchi.”—Deuteronomo 3:25, 26; 32:51.
Nayenso Mtumwi Paulo anapempha Mulungu kuti am’chotsere vuto limene iye anati ndi “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7) N’kutheka kuti “munga” umenewu unali vuto la maso kapena kuvutitsidwa mobwerezabwereza ndi anthu otsutsa komanso “abale onyenga.” (2 Akorinto 11:26; Agalatiya 4:14, 15) Paulo analemba kuti: “Katatu konse ndinachonderera Ambuye kuti mungawu undichoke.” Koma Mulungu anadziwa kuti Paulo akapitirizabe kulalikira ngakhale akuvutika ndi “munga m’thupi,” zikanasonyezeratu kuti Mulungu ndi wamphamvu komanso kuti Paulo amakhulupirira kwambiri Mulungu. Choncho m’malo mochita zimene Paulo anapempha, Mulungu anamuyankha kuti: “Mphamvu yanga imakhala yokwanira m’kufooka.”—2 Akorinto 12:8, 9.
Mosiyana ndi anthufe, Mulungu amadziwa bwino ngati zinthu zimene tapempha zili zothandizadi kwa ife. Nthawi zonse Yehova amayankha mapemphero mokomera ifeyo komanso mogwirizana ndi chifuniro chake chimene chafotokozedwa m’Baibulo.