PHUNZIRO 52
Tizivala Ndi Kudzikongoletsa Moyenera
Tonsefe timasankha zimene tikufuna kuvala komanso mmene tikufuna kudzikongoletsera. Komabe, tikamatsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza nkhaniyi, tingamavale zovala zimene timakonda koma zomwe sizingakhumudwitse Yehova. Tiyeni tione zina mwa mfundo zimenezi.
1. Ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuti tizisankha kuvala ndi kudzikongoletsa moyenera?
Tiyenera kusankha “zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru” ndipo nthawi zonse tizioneka bwino kuti anthu ena aziona kuti ndife anthu amene “amalemekeza Mulungu.” (1 Timoteyo 2:9, 10) Tiyeni tione mfundo 4 izi: (1) Zovala zathu zizikhala “zoyenera.” Mwina munaona kuti pamisonkhano yathu timavala mosiyanasiyana. Komabe, zomwe timavala komanso mmene timametera kapena kukonzera tsitsi lathu, zimasonyeza kuti timalemekeza Mulungu amene timamulambira. (2) Kuvala “mwaulemu” kumatanthauza kupewa kuvala zovala zimene zingachititse anthu kuganizira zachiwerewere, kapenanso kuti azingoganizira za ifeyo basi. (3) Timasonyezanso kuti timavala “mwanzeru” tikamapewa kumangotengera sitayiro iliyonse yatsopano yakavalidwe ndi kudzikongoletsa. (4) Timayesetsa kuti nthawi zonse tizioneka monga anthu amene “amalemekeza Mulungu” moti anthu ena sangavutike kuzindikira kuti timalambira Mulungu woona.—1 Akorinto 10:31.
2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira abale ndi alongo athu tikamasankha zomwe tikufuna kuvala?
N’zoona kuti tili ndi ufulu wosankha zimene tikufuna kuvala, komabe ndi bwino kuganizira mmene kavalidwe kathu kangakhudzire anthu ena. Timapewa kukhumudwitsa ena ndipo timayesetsa “kuwakondweretsa pa zinthu zabwino zowalimbikitsa.”—Werengani Aroma 15:1, 2.
3. Kodi kavalidwe kathu kangathandize bwanji anthu ena kuti ayambe kuphunzira za Yehova?
Ngakhale kuti nthawi zonse timavala bwino, koma timayesetsa kuvala bwino kwambiri tikamapezeka pamisonkhano yampingo komanso tikamalalikira uthenga wabwino. Sitimafuna kuti anthu ena alephere kumvetsera uthenga wabwino chifukwa cha mmene tavalira. M’malomwake, timafuna kuti kaonekedwe kathu kazithandiza anthu ena kukopeka ndi uthenga wabwino ndiponso ‘kuti kazikometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu.’—Tito 2:10.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zimene tingachite kuti anthu ena asamavutike kuzindikira kuti ndife Akhristu akamaona mmene timavalira ndi kudzikongoletsera.
4. Tikamaoneka bwino timalemekeza Yehova
Kodi ndi chifukwa chachikulu chiti chimene chiyenera kutipangitsa kuti tizisamala ndi mmene timaonekera? Werengani Salimo 47:2, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi kukumbukira kuti timaimira Yehova kungatithandize bwanji tikamasankha zomwe tikufuna kuvala?
Kodi mukuona kuti ndi nzeru kuganizira mmene timaonekera tikakhala pamisonkhano komanso tikamalalikira? N’chifukwa chiyani mukutero?
5. Zimene tingachite kuti tizivala ndi kudzikongoletsa moyenera
Zovala zathu zizikhala zoyera ndiponso zoyenera malo amene tili, kaya zikhale zodula kapena zotchipa. Werengani 1 Akorinto 10:24 ndi 1 Timoteyo 2:9, 10. Kenako, mukambirane chifukwa chake tiyenera kupewa kuvala zovala . . .
zakuda kapena zosalongosoka.
zothina, zoonekera mkati kapenanso zomwe zingachititse anthu ena kuganizira zachiwerewere.
Ngakhale kuti Akhristu masiku ano satsatira chilamulo cha Mose, angadziwe maganizo a Yehova pa nkhani yakavalidwe kuchokera m’Chilamulochi. Werengani Deuteronomo 22:5, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuvala ndi kudzikongoletsa m’njira imene imachititsa kuti amuna azioneka ngati akazi kapenanso akazi azioneka ngati amuna?
Werengani 1 Akorinto 10:32, 33 ndi 1 Yohane 2:15, 16, kenako mukambirane mafunso awa:
N’chifukwa chiyani ndi bwino kuganizira mmene kaonekedwe kathu kangakhudzire anthu am’dera lathu kapenanso amumpingo wathu?
Kodi kumene mumakhala, anthu amakonda kuvala ndi kudzikongoletsa m’njira yotani?
Kodi mumaona kuti ena mwa masitayilowo sangakhale oyenera kwa Mkhristu? N’chifukwa chiyani mukutero?
ZIMENE ENA AMANENA: “Ndi ufulu wanga kuvala chilichonse chomwe ndikufuna.”
Kodi nanunso mumaona choncho? N’chifukwa chiyani mukutero?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Tikamasankha bwino zomwe tikufuna kuvala komanso mmene tingadzikongoletsere, timasonyeza kuti timalemekeza Yehova ndi anthu ena.
Kubwereza
N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizivala komanso kudzikongoletsa moyenera?
Kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize kuti tizisankha mwanzeru zimene tikufuna kuvala komanso mmene tingadzikongoletsere?
Kodi mmene timavalira ndi kudzikongoletsera zingachititse kuti anthu ena aziona bwanji kulambira kwathu?
ONANI ZINANSO
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zomwe ena angaganize akaona zimene mumavala.
“Kodi Ndimakonda Kuvala Zovala Zotani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani chifukwa chake muyenera kumaganiza kaye musanasankhe kukhala ndi matatuu.
“Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yodzilemba Matatuu?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani mfundo zinanso zomwe zingatithandize posankha zochita.
“Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?” (Nsanja ya Olonda, September 2016)