Kodi Choonadi N’chamtengo Wapatali Motani kwa Inu?
“Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—YOHANE 8:32.
1. Kodi kugwiritsa ntchito kwa liwu lakuti “choonadi” kwa Pilato kunasiyana motani ndi mmene Yesu analigwiritsira ntchito liwuli?
“CHOONADI n’chiyani?” Pilato pofunsa funso limeneli, zikuoneka kuti anangochita chidwi ndi choonadi mulingaliro wamba. Koma Yesu anali atangonena kumene kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37, 38) Mosiyana ndi Pilato, Yesu anali kunena za choonadi cha Mulungu.
Mmene Dziko Limaonera Choonadi
2. Kodi ndi mawu ati a Yesu amene akusonyeza kuti choonadi n’chamtengo wapatali?
2 Paulo anati: “Si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Tinganenenso chimodzimodzi pa nkhani ya choonadi. Anthu ambiri ngakhale atapatsidwa mwayi wodziŵa choonadi cha m’Baibulo, amachinyalanyaza mwadala. Komatu choonadi n’chamtengo wapatali. Yesu anati: “Mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32)
3. Kodi tifunika kumvera malangizo ati pankhani ya ziphunzitso zonyenga?
3 Mtumwi Paulo ananena kuti choonadi sichikanapezeka mu nzeru ndi miyambo ya anthu. (Akolose 2:8) Inde, ziphunzitso zimenezo n’zonyenga. Paulo anachenjeza Akristu a ku Efeso kuti ngati akanakhulupirira nzeru ndi miyambo ya anthu imeneyi, akanakhala ngati makanda auzimu “ogwedezekagwedezeka . . . ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la [“chinyengo cha,” NW] anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusokeretsa.” (Aefeso 4:14) Lerolino, “chinyengo cha anthu” akuchilimbikitsa mwa mabodza a anthu amene amatsutsa choonadi cha Mulungu. Mabodza ameneŵa mochenjera amapotoza choonadi n’kukhala bodza ndipo amalimbikitsa mabodza kukhala choonadi. Kuti tipeze choonadi m’kati mwa chinyengo chimenechi, tifunika kuphunzira Malemba mwakhama.
Akristu ndi Dziko
4. Kodi choonadi chikupezeka kwa yani, ndipo amene achilandira afunika kuchita chiyani?
4 Yesu Kristu ponena za anthu amene anakhala ophunzira ake, anapemphera kwa Yehova kuti: “Patulani iwo m’choonadi; mawu anu ndi choonadi.” (Yohane 17:17) Anthu otereŵa adzapatulidwa kuti atumikire Yehova ndi kudziŵikitsa dzina lake ndi ufumu wake. (Mateyu 6:9, 10; 24:14) Ngakhale kuti si onse amene ali nacho, choonadi cha Yehova chikupezeka monga mphatso yaulere kwa onse amene akuchifunafuna, a mtundu uliwonse, fuko lililonse ndiponso chikhalidwe chilichonse. Mtumwi Petro anati: “Ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.
5. N’chifukwa chiyani nthaŵi zambiri Akristu amazunzidwa?
5 Akristu amauza anthu ena choonadi cha m’Baibulo koma si anthu onse amene amawalandira. Yesu anachenjeza kuti: “Adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Pofotokoza za vesi limeneli, mtsogoleri wina wa chipembedzo wa ku Ireland, John R. Cotter analemba mu 1817 kuti: “Kuyesetsa kwawo [kwa Akristu] koti asinthe miyoyo ya anthu mwa kulalikira kwawo, m’malo moti kuwachititse anthu kuyamikira, kudzawachititsa kudana nawo ndi kuwazunza ophunzirawo chifukwa chovumbula zoipa za anthuwo.” Anthu ozunzaŵa ‘salandira chikondi cha choonadi kuti akapulumutsidwe.’ N’chifukwa chake, “Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza; kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.”—2 Atesalonika 2:10-12.
6. Kodi Mkristu sayenera kulakalaka chiyani?
6 Mtumwi Yohane akulangiza Akristu amene akukhala m’dziko laudanili kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. . . . Chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.” (1 Yohane 2:15, 16) Yohane ponena kuti “chilichonse,” sakupatulapo kanthu. N’chifukwa chake sitiyenera kulakalaka chilichonse chimene dzikoli limapereka chimene chingatipatutse pa choonadi. Kumvera langizo la Yohane kudzalimbikitsa kwambiri miyoyo yathu. Motani?
7. Kodi kudziŵa choonadi kwalimbikitsa motani anthu oongoka mtima?
7 M’chaka cha 2001, Mboni za Yehova padziko lonse zinali kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba oposa 4,500,000 mwezi uliwonse, kulangiza anthu ndi magulu mmene Mulungu amafunira kuti tizikhalira. Zotsatira zake zinali zakuti anthu 263,431 anabatizidwa. Ophunzira ameneŵa anaona choonadi kukhala cha mtengo wapatali ndipo anasiya mayanjano oipa ndi njira zosayenera zonyozetsa Mulungu zimene zafala m’dziko lino. Kuyambira pamene anabatizidwa, iwo apitirizabe kutsatira miyezo ya Yehova imene anakhazikitsira Akristu onse. (Aefeso 5:5) Kodi choonadi n’chamtengo wapatali motero kwa inu?
Yehova Amatisamalira
8. Kodi Yehova amachita motani ndi kudzipatulira kwathu, ndipo n’chifukwa chiyani n’kwanzeru ‘kuthanga tafuna Ufumu’?
8 Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, Yehova mwachifundo amavomereza kudzipatulira kwathu. Tinganene kuti amadzichepetsa kuti atiyandikizitse kwa iye. Motero iye amatiphunzitsa kuti tikweze zolinga ndi zofuna zathu. (Salmo 113:6-8) Panthaŵi imodzimodziyo, Yehova amatilola kukhala naye pa ubale weniweni, ndipo amalonjeza kuti atisamalira ngati ‘tithanga tafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.’ Ngati tichita zimenezi ndi kudziteteza tokha mwauzimu, iye akutilonjeza kuti: “Zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.”—Mateyu 6:33.
9. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndani, ndipo Yehova amatisamalira motani kudzera mwa “kapolo” ameneyu?
9 Yesu Kristu anasankha ophunzira ake 12 ndipo anaika maziko a mpingo wa Akristu odzozedwa amene kenako anadzatchedwa “Israyeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 21:9, 14) Patapita nthaŵi, Israyeli wa Mulunguyo anadzam’fotokoza kukhala “Eklesia [“mpingo,” NW] wa Mulungu wamoyo, mzati ndi m’chirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:15) Yesu anadziŵikitsa anthu a mumpingo umenewo kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndiponso monga “mdindo wokhulupirika ndi wanzeru.” Yesu ananena kuti mtumiki wokhulupirika ameneyo adzakhala ndi udindo wopatsa Akristu “zakudya panthaŵi yake.” (Mateyu 24:3, 45-47; Luka 12:42) Popanda chakudya, titha kufa. Mofananamo, ngati sitidya chakudya chauzimu, tidzafooka ndi kufa mwauzimu. Motero, kukhalapo kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi umboni winanso wakuti Yehova amatisamalira. Tiyenitu nthaŵi zonse tiziyamikira chakudya chauzimu cha mtengo wapatali chimene timalandira kudzera mwa “kapolo” ameneyo.—Mateyu 5:3.
10. N’chifukwa chiyani n’kofunika kwambiri kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse?
10 Kudya chakudya chauzimu kumaphatikizapo phunziro laumwini. Kumafunanso kucheza ndi Akristu ena ndi kupezeka pa misonkhano yampingo. Kodi mukukumbukira bwinobwino zimene munadya miyezi isanu ndi umodzi, kapena ngakhale milungu isanu ndi umodzi yapitayo? Mwina ayi. Komabe, kaya munadya chiyani, chakudyacho chinakupatsani zofunika m’thupi kuti mukhale ndi moyo. Ndipo kuyambira nthaŵi imeneyo muyeneranso kuti mwadyapo chakudya chofanana ndi chimenecho. Zimenezi n’chimodzimodzinso ndi chakudya chauzimu chimene timalandira pa misonkhano yachikristu. Mwina sitikumbukira zonse zimene tamva pa misonkhano. Ndipo mosakayika, nkhani zimene mwamvazo ziyenera kuti zinakambidwapo nthaŵi zambiri. Komabe, chimenecho n’chakudya chauzimu chomwe chili chofunika kwambiri pa moyo wathu. Misonkhano yathu nthaŵi zonse imapereka chakudya chabwino chauzimu, chimene timalandira panthaŵi yoyenera.
11. Kodi tili ndi udindo wotani pamene tili pa misonkhano yachikristu?
11 Kupezeka pamisonkhano yachikristu kumatipatsanso udindo. Akristu akulangizidwa ‘kudandaulirana,’ kufulumiza anzathu a mumpingo ku “chikondano ndi ntchito zabwino.” Kukonzekera kwathu, kupezekapo, ndiponso kutenga nawo mbali pa misonkhano yonse yachikristu kumalimbikitsa chikhulupiriro chathu ndiponso kumalimbikitsa anthu ena. (Ahebri 10:23-25) Monga ana aang’ono amene mwina sangakonde chakudya chambiri, anthu ena angafunike kuwalimbikitsa nthaŵi zonse kuti adye chakudya chauzimu. (Aefeso 4:13) Kumakhala kusonyeza chikondi kuwalimbikitsa motero ngati chilimbikitsocho chikufunikira n’cholinga choti anthu oterowo apite patsogolo mwauzimu n’kukhala Akristu okhwima, amene Paulo analemba za iwo kuti: “Chakudya chotafuna chili cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloŵeretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”—Ahebri 5:14.
Kudzisamalira Tokha Mwauzimu
12. Kodi ndani amene ali ndi udindo wonse kuti tipitirizebe kuyenda m’choonadi? Fotokozani.
12 Mnzathu amene takwatirana naye kapena makolo athu angatilimbikitse kuyendabe m’choonadi. Akulu mumpingo nawonso angatibuse monga nkhosa zimene apatsidwa kuti aziyang’anire. (Machitidwe 20:28) Koma kodi ndani amene ali ndi udindo wonse ngati tikufuna kuti tipitirizebe kuyenda m’choonadi? Kunena zoona, udindowu ndi wa munthu aliyense payekha. Ndipo zimenezi ziyenera kukhala choncho pamene zinthu zili bwino komanso panthaŵi zovuta. Taonani chochitika chotsatirachi.
13, 14. Monga mmene taonera pa zimene zinachitikira kamwana ka nkhosa, kodi tingapeze bwanji thandizo lauzimu limene tikufunikira?
13 Ku Scotland, tiana ta nkhosa tina tinali kudya msipu pamene kamwana kena kanasokera kuseri kwa phiri ndipo kanatsetsereka n’kugwera pa mwala wina umene unali m’munsi. Sikanavulale, koma kanali ndi mantha ndipo kanalephera kukwera kuti kabwerere kumene kanali. Ndiyeno kanayamba kulira kwambiri. Mayi wake anamva ndipo nayenso anayamba kulira mpaka pamene mbusa anabwera n’kukachotsa kamwana ka nkhosako.
14 Onani mmene zinthu zinayendera. Kamwanako kanalira kuti kathandizidwe, mayi wake anawonjezera kulirako, ndipo mbusa atadziŵa anachitapo kanthu mwamsanga kuti apulumutse kamwanako. Ngati kamwana ka nkhosa ndi mayi wake zingazindikire kuti zili pangozi ndipo n’kupempha thandizo mwamsanga, kodi ife sitingachitenso chimodzimodzi tikakhumudwa mwauzimu kapena tikakumana ndi ngozi zosayembekezeka za m’dziko la Satanali? (Yakobo 5:14, 15; 1 Petro 5:8) Tifunika kutero, makamaka ngati sitikudziŵa zambiri mwina chifukwa chakuti ndife achichepere kapena ndife achatsopano m’choonadi.
Kutsatira Malangizo a Mulungu Kumabweretsa Chimwemwe
15. Kodi mkazi wina anamva bwanji atayamba kusonkhana ndi mpingo wachikristu?
15 Taganizirani phindu la kumvetsa Baibulo ndi mtendere wamaganizo zimene anthu amene akutumikira Mulungu wa choonadi amapeza. Mkazi wina wa zaka 70 amene ankapita ku Tchalitchi cha England kuyambira ali wamng’ono anavomera kuphunzira Baibulo ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Posakhalitsa, iye anaphunzira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo anayankha nawo kuti “Amen” pa mapemphero okhudza mtima operekedwa ku Nyumba ya Ufumu ya kumeneko. Iye anafotokoza kuchokera pansi pa mtima kuti: “Mmalo moona Mulungu ngati woti anthufe sitingam’fikire, mumakhala ngati mukum’bweretsa pakati pathu ngati bwenzi lenileni. Zimenezi sizinandichitikirepo kuyambira kale.” Mosakayika, munthu wachidwi ameneyu sadzaiwala mmene choonadi chinamukhudzira kwa nthaŵi yoyamba. Tiyenitu nafenso tisaiŵale mmene choonadi chinalili cha mtengo wapatali kwa ife titachilandira kumene.
16. (a) Kodi chingachitike n’chiyani ngati kufunafuna chuma kukhala cholinga chathu chachikulu m’moyo? (b) Kodi chimwemwe chenicheni tingachipeze bwanji?
16 Anthu ambiri amakhulupirira kuti atakhala ndi ndalama zambiri angakhale osangalala kwambiri. Komabe, ngati kufunafuna ndalama kukhala cholinga chathu chachikulu m’moyo, tingavutike ndi “zosautsa maganizo zosaneneka.” (1 Timoteo 6:10, Phillips) Taganizani kuchuluka kwa anthu amene amagula matikiti a lotale, kuwononga ndalama m’nyumba za juga, kumwaza ndalama mosasamala mumsika wogulitsa makampani, kuganiza kuti awina ndalama zambiri. Anthu ochepetsetsa okha ndi amene amawina ndalama zambiri zimene anali kuyembekezera. Ndiponso, nthaŵi zambiri ngakhale amene apeza ndalama zambiriwo, amapeza kuti kulemera kwawo kwadzidzidziko sikuwabweretsera chimwemwe. Mosiyana ndi zimenezi, chimwemwe chenicheni chimapezeka mwa kuchita zimene Yehova amafuna, kugwira ntchito limodzi ndi mpingo wachikristu motsogozedwa ndi mzimu wa Yehova ndiponso mothandizidwa ndi angelo ake. (Salmo 1:1-3; 84:4, 5; 89:15) Tikachita zimenezi, tingapeze madalitso osayembekezeka. Kodi choonadi n’chamtengo wapatali kwa inu moti chingakubweretsereni madalitso amenewo?
17. Kodi kukhala kwa Petro m’nyumba ya Simoni wofufuta zikopa, kunasonyeza kuti mtumwiyu anali ndi mtima wotani?
17 Taganizani zimene mtumwi Petro anakumana nazo. M’chaka cha 36 C.E., anayenda ulendo waumishonale kupita ku Chigwa cha Sarona. Anaima ku Luda, kumene anachiritsa Eneya wamanjenje ndipo kenako anapitirira ku doko la Yopa. Kumeneko iye anaukitsa Dorika. Machitidwe 9:43 amatiuza kuti: “Ndipo kunali, kuti anakhala iye m’Yopa masiku ambiri ndi munthu Simoni wofufuta zikopa.” Kankhani kochepa kameneka kakusonyeza kuti Petro analibe mtima wa tsankho pamene anali kutumikira anthu mumzinda umenewo. Motani? Katswiri wina wamaphunziro a Baibulo, Frederic W. Farrar analemba kuti: “Wotsatira kwambiri Chilamulo Chapakamwa [cha Mose] sakanalola kukhala m’nyumba ya munthu wofufuta zikopa. Kuona tsiku ndi tsiku zikopa ndi nyama zakufa zosiyanasiyana zofunika pantchito imeneyi, ndiponso zipangizo zimene zinkafunikira, zinali zodetsa ndiponso zonyansa kwambiri kwa munthu wotsatira kwambiri Chilamulo.” Ngakhale kukanakhala kuti ‘nyumba yake ya m’mbali mwa nyanja’ sinayandikane kwambiri ndi kumene ankafufutira zikopa, Simoni ankachita nawo ‘malonda omwe ena anali kuwanyansa ndipo motero anali kuchotsa ulemu wa anthu amene anali kuchita nawo malondawo,’ anatero Farrar.—Machitidwe 10:6.
18, 19. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Petro anakayikakayika pa masomphenya amene anaona? (b) Kodi Petro analandira madalitso osayembekezeka otani?
18 Petro wopanda tsankhoyu anavomera kuchereza kwa Simoni, ndipo ali komweko analandira mosayembekezeka malangizo ochokera kwa Mulungu. Anaona masomphenya mmene anauzidwa kudya nyama zodetsedwa malinga ndi chilamulo cha Ayuda. Petro anakana kuti sanadye “kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.” Koma anauzidwa katatu konse kuti: “Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba.” N’zomveka kuti ‘Petro mwa yekha anakayikakayika kuti masomphenya adawaona akuti chiyani.’—Machitidwe 10:5-17; 11:7-10.
19 Petro sankadziŵa kuti dzulo lake ku Kaisareya, pa mtunda wa makilomita 50 kuchokera ku Yopa, Wakunja wina dzina lake Korneliyo anaonanso masomphenya. Mngelo wa Yehova anauza Korneliyo kuti atume antchito akaitane Petro kunyumba ya Simoni wofufuta zikopa. Korneliyo anatumiza antchito ake kunyumba ya Simoni, ndipo Petro anatsagana nawo kupita ku Kaisareya. Atafika kumeneko, analalikira kwa Korneliyo pamodzi ndi achibale ndi mabwenzi ake. Zotsatira zake zinali zakuti iwo anakhala Akunja osadulidwa oyamba kulandira mzimu woyera monga oloŵa Ufumu. Ngakhale kuti anthuwo anali osadulidwa, onse amene anamva mawu a Petro anabatizidwa. Zimenezi zinatsegula njira yoti anthu amitundu, amene Ayuda ankawaona ngati odetsedwa, akhale mbali ya mpingo wachikristu. (Machitidwe 10:1-48; 11:18) Umenewutu unali mwayi waukulu kwa Petro ndipo zonsezi zinachitika chifukwa chakuti choonadi chinali cha mtengo wapatali kwa iye ndipo chinam’chititsa kumvera malangizo a Yehova ndi kuchitapo kanthu mwachikhulupiriro.
20. Kodi Mulungu amatithandiza motani tikaika choonadi patsogolo m’moyo wathu?
20 Paulo anati: ‘Ndi kuchita zoona [“Ndi kulankhula choonadi,” NW] mwa chikondi tikakule m’zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Kristu.’ (Aefeso 4:15) Inde, choonadi chidzatibweretsera chimwemwe chosasimbika pakalipano ngati tichiika patsogolo m’moyo wathu ndi kulola kuti Yehova atsogolere mapazi athu mwa mzimu wake woyera. Ndiponso kumbukirani kuti angelo opatulika akutithandiza pa ntchito yathu yolalikira. (Chivumbulutso 14:6, 7; 22:6) Tili ndi mwayitu kwambiri kuti pali otithandiza pa ntchito imene Yehova watipatsa kuti tichite. Kukhalabe okhulupirika kudzatichititsa kutamanda Yehova, Mulungu wa choonadi, mpaka muyaya. Kodi pangakhalenso chabwino china choposa kuchita zimenezi?—Yohane 17:3.
Kodi Taphunzira Chiyani?
• N’chifukwa chiyani ambiri salandira choonadi?
• Kodi Akristu afunika kuona motani zinthu za m’dziko la Satana?
• Kodi misonkhano tiziiona motani, ndipo chifukwa chiyani?
• Kodi tili ndi udindo wotani podzisamalira tokha mwauzimu?
[Mapu/Chithunzi patsamba 18]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
NYANJA YAIKULU
Kaisareya
CHIGWA CHA SARONA
Yopa
Luda
Yerusalemu
[Chithunzi]
Petro anatsatira malangizo a Mulungu ndipo anapeza madalitso osayembekezeka
[Mawu a Chithunzi]
Mapu: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.
[Chithunzi patsamba 13]
Yesu anachitira umboni choonadi
[Chithunzi patsamba 15]
Monga chakudya chakuthupi, chakudya chauzimu n’chofunika kwambiri kuti tikhale ndi moyo