Pitirizani Kuyenda m’Kuunika kwa Umulungu
Panthawi imene mpingo udzaphunzira nkhani ino ndi ziwiri zotsatizana nayo, wochititsa phunziro ayenera kuchititsa mbali zolembedwa za Yohane Woyamba kuwerengedwa ngati nthawi ilola
“Mulungu ndiye kuunika.—1 YOHANE 1:5.
1, 2. Kodi Yohane Woyamba analembedwa liti ndipo kuti, ndipo amagwira ntchito kwa ayani?
MBONI ZA YEHOVA ziri zothokoza kaamba ka kuunika kwa umulungu ndipo ziri ndi cholinga cha kupitirizabe kuyendamo. Komabe, kutero sikuli kosavuta, chifukwa chakuti ngakhale ophunzira oyambirira aYesu Kristu anayang’anizana ndi mpatuko. Koma atumwi okhulupirika a Yesu analetsakufalikira kwake, ndipo munthu amene ‘anali monga choletsa’ anali mtumwi Yohane. (2 Atesalonika 2:1-12) Monga mwamuna wokalamba kwambiri wokhala m’Efeso kapena chapafupipo pafupifupi 98 C.E., iye analemba kalata yake yoyamba youziridwa ndi Mulungu. Uphungu wake unathandiza Akristu a m’zaka za zana loyamba kupitirizabe kuyenda m’kuunika kwa umulungu. Koma bwanji za ife?
2 Mawu a Yohane ali othandiza mofananamo kwa Akristu a m’zaka za zana la 20. Chotero m’phunziro lanu la nkhani ino ndi ziwiri zotsatira, tsimikizirani kuwerenga mbali zonse zolembedwa za kalata yake yoyamba youziridwa pamene zikuphunziridwa. M’kalata ya mtumwiyo ndi ndemanga zimene ife tanenapo, a mlowa mmalo a dzina monga “ti” ndi “ife” kwakukulukulu amasonya kwa otsatira odzozedwa a Yesu. Koma malamulo a makhalidwe abwino aakulu ophatikizapo chilungamo, chikondi, chikhulupiriro, ndi zina zotero, amagwiranso ntchito kwa Akristu okhala ndi ziyembekezo za padziko lapansi.
Kugawana Kumene Kumadzetsa Chisangalalo
3. Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wakuti Mwana wa Mulungu analikodi, anavutika, ndipo anafa monga munthu, ndipo nchifukwa ninji iye amatchedwa “mawu a moyo”?
3 Choyamba Yohane akulankhula za “kugawana” kwachisangalalo. (Werengani 1 Yohane 1:1-4.) Yesu, “mawu a moyo,” anali ndi Yehova ‘kuyambira pachiyambi’ monga cholengedwa chachisamba cha Mulungu, kupyolera mwa amene ‘zinthu zonse zinalengedwa.’ (Akolose 1:15, 16) Ampatuko ena a m’zaka za zana loyamba ananena kuti anali opanda uchimo ndipo analandula malo oyenerera a Kristu m’kakonzedwe kaumulungu. Koma atumwi a Yesu anamumva akulankhula, anamvetsera kwa iye mwachidwi, ndipo anamkhudza. Anazindikira kuti mphamvu ya Mulungu inali kugwira ntchito kupyolera mwa iye. Chotero panali umboni wochokera kumboni zowona ndi maso wakuti iye anali Mwana wa Mulungu amene adakhala moyo, navutika, naafa monga munthu. Iye ndiye “mawu a moyo” chifukwa chakuti “moyo [wosatha] unawonetsedwa” kupyolera mwa Yesu, mwa amene Mulungu anagawira dipo.—Aroma 6:23; 2 Timoteo 1:9, 10.
4. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa mwa mawu akutiwo “kugawana” kumene odzozedwa ali nako?
4 Mwa zimene atumwi ananena ndi kulemba, ‘anachitira umboni’ za munthu wopanda uchimoyo Yesu Kristu. Yohane ‘anasimba’ nkhani zotero kotero kuti odzozedwawo ‘agawane,’ kapena kuyanjana, ndi olowa nyumba ena a Ufumu, limodzi ndi Atate, ndi Mwana Wake. ‘Kugawana’ uku kumatanthauza chigwirizano ndi kuchititsa chisangalalo chachikulu. (Salmo 133:1-2; Yohane 17:20, 21) Ampatuko amene amada atsamwali apapitapo muutumiki wa Yehova alibenso mayanjano otero ndi Mulungu ndi Kristu.
“Mulungu Ndiye Kuunika”
5. Kodi ndi “uthenga” wotani umene atumwi analandira kuchokera kwa Yesu, ndipo ndimotani mmene umayambukirira khalidwe la Mboni za Yehova?
5 Wolongosoledwa pambuyo pake ndiwo “uthenga” umene atumwi analandira kuchokera kwa Yesu. (Werengani 1 Yohane 1:5-7.) Ndiwo uwu: “Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima [mulibe chivundi, chisembwere, mabodza, kapena choipa].” Chotero Mboni za Yehova zimakana zizolowezi zauchimo zonse zogwirizanitsidwa ndi mdima. (Yobu 24:14-16; Yohane 3:19-21; Aroma 13: 11-14; 2 Akorinto 6:14; 1 Atesalonika 5:6-9) Popeza kuti ampatuko ena sanakhulupirire kuti ntchito zauchimo ziriko, iwo anali m’mdima wauzimu. Iwo ananena kuti anali ndi chidziwitso chachinsinsi, koma Mulungu ndiye kuunika, osati chinsinsi chamdima. Amapereka kuunika kwauzimu kokha kwa mboni zake zokhulupirika.—Mateyu 5:14-16; 1 Petro 2:9.
6. Ngati ‘tigwiritsira ntchito chowonadi,’ kodi tiri ndi dalitso lotani?
6 Tikati kuti “tiyanjana” ndi Mulungu koma “tiyenda m’mdima,” tikumakhala moyo m’mphulupulu, “tinama, ndipo sitichita chowonadi,” kapena kukhala ndi moyo mogwirizana nacho. Koma ngati tilondola njira imene iri yogwirizana ndi chowonadi tiri m’kuunika, monga momwedi Mulungu aliri. “Tiyanjana” ndi Akristu anzathu, amene onse ali ogwirizana m’chiphunzitso, m’lingaliro lauzimu, m’ntchito yopanga ophunzira, ndi mbali zina za kulambira kwangwiro.
7. Kodi nchifukwa ninji mwazi wa Yesu ‘ungatiyeretse kuuchimo wonse’?
7 Mosiyana ndi ampatuko ena oyambirira, ife amene ‘tiyenda m’kuunika’ timavomereza kuti uchimo ndiwo chidetso. Mwazi wa YesU ‘umatiyeretsa ku machimo onse’ chifukwa chakuti sitiri ochimwa dala. (Mateyu 12:31, 32) Ndithudi, tiri othokoza, kuti Mulungu amasonyeza chifundo ngakhale kwa Akristu ochimwa koma olapa.—Salmo 103:8-14; Mika 7:18, 19.
Maziko Achitetezero
8, 9. (a) Kodi Yehova adzatikhululukira pamaziko otani? (b) Ponena za uchimo, kodi nchiyani chimene ampatuko ena anali kunena, ndipo nchifukwa ninji iwo anali olakwa?
8 Kenako Yohane akutchula. maziko a kuyeretsedwa kuuchimo. (Werengani 1 Yohane 1 :8-2:2.) Tikati kuti “tiribe uchimo,” tikulandula chenicheni chakuti zolengedwa zonse zopanda imgwiro nzochimwa, ndipo “mwa ife mulibe chowonadi.” (Aroma 5:12) Koma Mulungu ali “wokhulupirika” ndipo amatikhululukira “ngati tivomereza machimo athu” kwa iye ndi mkhalidwe wolapa umene umatisonkhezera kusiya kuchita cholakwa. (Miyambo 28:13) Mulungu anati ponena za a m’pangano latsopano: “Zoipa zawo sindidzazikumbukanso.” (Yeremiya 31:31-34; Ahebri 8:7-12) Powakhululukira, iye ngwokhulupirika kulbnjezolo.
9 Ndiponso, Mulungu ali “wolungama,” amene nthawi zonse amamamatira kumiyezo yake yachilungamo. Iye wakwaniritsa chilungamo kupyolera mwa dipo ndipo angathe ‘kukhululukira machimo athu ndi kutiyeretsa tonse ku chisalungamo’ ngati tivomereza machimo athu mokhulupirira nsembe ya Yesu. (Ahebri 9:11-15) Mwa imfa yake Mesiya anasenza machimo athu, monga momwedi mbuzi yonyamula uchimo inatumizidwira kuchipululu pa Tsiku la Chitetezero. (Levitiko 16:20-22; Yesaya 53:5, 8, 11, NW; 1 Petro 2:24) Ampatuko ena ananena kuti, “sitinachimwe,” motero ‘kupangitsa Yehova kukhala wabodza.’ Koma ‘Mulungu . . . sanganame,’ ndipo Mawu ake amasonyeza kuti anthu opanda ungwiro onse ngochimwa. (Tito 1:2; Mlaliki 7:20; Aroma 3:23) Eya, kunena kuti “sitinachimwe” kukanatanthauza kuti mawu a Mulungu saali “mwa ife,” saali m’mitima yathu!—Yerekezerani ndi Ahebri 8:10.
10. Kodi ndi m’njira yotani mu imene Yesu aliri “nsembe yotetezera”?
10 Yohane akulemba “zinthii zimenezi” ponena za uchimo, chikhululukiro, ndi kuyeretsedwa kotero kuti tisazolowere kuchita uchimo. Mawu ake ayenera kutisonkhezera kuyesayesa mwaphamphu kusachimwa. (1 Akorinto 15:34) Koma ngati tichita “uchimo” ndipo tiri olapa, tiri naye “nkhoswe kwa Atate”—“Yesu Kristu, wolungama,” amene amatipembedzera machimo athu kwa Mulungu. (Ahebri 7:26; yerekezerani ndi Yohane 17:9, 15, NW.) Yesu ndiye ‘nsembe yotetezera.” Imfa yake inakwaniritsa chiweruzo cholungama nitheketsa Mulungu kusonyeza chifundo ndi kuchotsa liwongo la uchimo kwa Aisrayeli auzimu ndi “dziko lonse,” kuphatikizapo “khamu lalikulu.” (Aroma 6:23; Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 7:4-14) Tikuyiyamikira chotani nanga nsembe imeneyi!
Mverani Mulungu ndi Kusonyeza Chikondi
11. Kodi ndi mwaumboni wotani umene timadziwa nawo kuti tiri mu “chigwirizano ndi” Mulungu?
11 Kuti tipitirize kuyenda m’kuunika kwa umulungu, tiyenera kumvera Yehova. (Werengani 1 Yohane 2:3-6.) Tikuzindikira kuti ‘tafikira pa kudziwa’ Mulungu, kumuyamikira ndi mikhalidwe yake, ngati “tipitirizabe kusunga malamulo ake.” Aliyense wonena kuti amadziwa Yehova koma nalephera kummvera “ali wabodza.” Mmalo mwake, “chikondi cha Mulungu chapangidwa kukhala changwiro,” kapena chokwanira, ngati timvera mawu ake. ‘Mwa umboni uwu’ wa kumvera ndi kukonda Mulungu, tidziwa kuti tiri ‘ogwirizana naye.’ Ndipo tiri ndi thayo la kuyenda monga momwe anachitira Mwana wake, m’ntchito ya kupanga ophunzira, muunansi wathu ndi ena, ndi zina zotero.
12. Kodi ndi “lamulo lakale” liti limene Akristu ali nalo, ndipo ndimotani mmene liririnso “latsopano”?
12 Chikondi cha pa abale chirinso chofunika. (Werengani 1 Yohane 2:7, 8.) Yohane akulemba “lamulo lakale” limene okhulupirika anali nalo “kuyambira pachiyambi” cha miyoyo yawo monga Akristu. Liri “lakale” chifukwa chakuti Yesu adalipereka zaka zambiri kalero pamene anauza ophunzira ake ‘kukondana wina ndi mnzake monga momwedi iye anali atawakondera.’ (Yohane 13:34) Komabe iro lirinso “latsopano” chifukwa chakuti limachita zambiri kuposa zimene Chilamulo chinafuna kukonda mnansi ndipo limafunikiritsa kufunitsitsa kulepa moyo wa munthuwe mmalo mwa okhulupirira anzako. (Levitiko 19:18; Yohane 15:12, 13) Popeza kuti chikondi chathu chopanda mpeni kumphasacho chimatsimikizira kuti kugwirizana ndi “lamulo latsopano” limeneli ndiko ‘chowonadi ponse pawiri kwa Kristu ndi kwa ife, mdima ukupitirira ndipo kuunika kowona kukuwala kale’ pakati pathu.
13. Mogwirizana ndi kunena kwa 1 Yohane 2: 9-11, kodi ndani amene ali “m’kuunika” ndipo ndani amene saali?
13 Komabe, kodi ndani amene kwenikweni ali “m’kuunika”? (Werengani 1 Yohane 2:9-11.) Eya, “iye amene anena kuti ali m’kuunika, namuda mbale wake” ali mu mdima wauzimu “kufikira tsopano.” Koma “iye amene akonda mbale wake akhala m’kuunika,” ndipo kwa iye kulibe “chokhumudwitsa.” Panopa liwu Lachigiriki likupereka lingaliro lamsampha wa nyama woikidwa nyambo ndipo likutanthauza kanthu kena kamene kangachititse kugwera muuchimo. Kwenikweni, wodzinenera kukhala Mkristu amene amada mbale wake “sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.” (Mateyu 13:13-15) Kodi tchenjezo limeneli lidzakusonkhezerani kupewa mdima wauzimu mwa kukana kulola mavuto a inu mwini, mabodza a ampatuko, kapena kanthu kena kalikonse kuwononga chikondi chanu chaubale?
Maziko a Chidaliro
14. Kodi ndani amene ali “tiana” ndi “atate” otchulidwa ndi Yohane?
14 Kenako Yohane akusonyeza chidaliro mwa “tiana [tochepa],” mwachiwonekere akutanthauza mpingo wathunthu. (Werengani 1 Yohane 2:12-14.) Machimo athu akhululukidwa ‘m’dzina la Kristu,’ chifukwa chakuti kuli kupyolera mwa iye yekha kuti Mulungu anapangitsa chipulumutso kukhala chotheka. (Machitidwe 4:12) Odzozedwawo “amadziwa Atate” chifukwa chakuti iye anawabala mwa mzimu wake. Ena ali “atate”—mwachiwonekere okhulupirira achikulire, achidziwitso kwambiri, ndi okula msinkhu mwauzimu. Iwo amadziwa Yesu, amene analiko “kuyambira pachiyambi” m’chakuti Mulungu analenga iye asanalenge zinthu zonse.
15. (a) Ndani amene ali “anyamata” amene Yohane analembera, ndipo kodi ndimotani mmene iwo “alakira woipayo”? (b) Perekani chitsanzo cha mmene ‘tingalakire’ Satana lerolino.
15 “Anyamata” amene Yohane akusonyako angakhale Akristu achichepere kwambiri, okhala ndi chidziwitso chochepa. Iwo “agonjetsa woipayo,” Satana, mwa kusagonjera ku ‘machenjera’ ake. (2 Akorinto 2:11) Mwachitsanzo, lerolino kumeneku kukanaphatikizapo kupewa zosangulutsa zonyansa, nyimbo zodzutsa chilakolako, ndi mabukhu onyansa, zimene zingathe kufooketsa malamulo a makhalidwe abwino Achikristu ndi kutulukira m’kugwera m’chisembwere. “Anyamatawo” ali olakika pa Satana chifukwa chakuti “ngamphamvu” mwauzimu ndipo “mawu a Mulungu akhalabe” mwa iwo. Tikhaletu ofanana nawo mwa kuvomereza makonzedwe auzimu a Mulungu, kukana mpatuko, ndi kupitirizabe kuyenda m’kuunika kwa Mulungu.
Chikondi Chimene Sitiyenera Kukhala Nacho
16. Kodi nchikondi chotani chimene sitiyenera kukhala nacho, koma nchiyani chimene chikakhala chowona ponena za ife ngati tinali ndi malingaliro ndi ziganizo za dziko?
16 Kaya ndife Akristu achicheperepo kapena achikulire, pali chikondi chimene sitiyenera kukhala nacho. (Werengani 1 Yohane 2:15-17) Sitiyenera ‘kukonda dziko kapena chirichonse mu iro.’ Mmalo mwake, tifunikira kupewa kukhala ochitidwa mawanga ndi chivundi cha anthu osalungama ndipo sitiyenera kupuma “mzimu” wake, kapena kusonkhezeredwa ndi mkhalidwe wake wofunga wauchimo. (Aefeso 2:1, 2; Yakobo 1:27) Ngati tinati tikhale ndi malingaliro ndi zikhumbo za dziko, “chikondi cha Atate” sichikanakhala mwa ife. (Yakobo 4:4) Imeneyo iridi mfundo yofunika mwapemphero, kodi sichoncho?
17. Kodi ndizilakolako za dziko zotani zimene Akristu sayenera kukhutiritsa?
17 “Chirichonse cha m’dziko lapansi” sichichokera kwa Mulungu. Chimenechi chimaphatikizapo “chilakolako chathupi,” chimene kukhutiritsidwa kwake kungatanthauze kukondweretsa zilakolako zauchimo zonga ngati zilakolako zodetsa zachisembwere. (1 Akorinto 6:15-20; Agalatiya 5:19-21) Ndiponso choyenera kupewedwa ndicho kugonjera ku “chilakolako cha maso.” Chipatso choletsedwacho cholakalakika chinakopa Hava, ndipo kuyang’anitsitsa Betiseba kwa Davide pamene anali kusamba kunatsogolera ku uchimo waukulu. (Genesis 3:6; 2 Samueli 11:2-17) Pamenepa, kuti tipitirizebe kuyenda m’kuunika kwa Mulungu, tiyenera kupewa zosangulutsa zoluluzika ndi zinthu zina zimene ziri zosonkhezera ku chilakolako cha uchimo ndi kuipsa mtima.—Miyambo 2:10-22; 4:20-27.
18. Kodi nchifukwa ninji “matamandidwe a moyo” ali opanda pake, ndipo kodi iwo amalephera kudzetsa chiyani?
18 Ndiponso a m’dziko lapansi ndiwo “matamandidwe a moyo.” Munthu wonyada anganyadire chuma chake, zovala zake, ndi zina zotero, zimene zonsezo zingathe kutayika. ‘Kudziwonetsera kwake’ kungachititse chidwi anthu ena ndi kudzetsa zitamando za kanthawi koma osati dalitso la Mulungu.—Mateyu 6: 2, 5, 16, 19-21; Yakobo 4:16.
19. Kodi nchiyani chimene chidzachitikira dziko lino, ndipo chenicheni chimenechi chiyenera kutiyambukira motani?
19 Kumbukirani kuti “dziko lapansi lipita” ndipo lidzawonongedwa. (2 Petro 3:6) Zilakolako zake ndi ziyembekezo zidzawonongeka limodzi nalo, monga momwe adzachitira olikonda. “Koma,” akutero Yohane, “iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.” Chotero tiyeni tisunge chonulirapo cha moyo wamuyaya mwa ‘kukaniza zilakolako zadziko’ ndi kupitirizabe kuyenda m’kuunika kwa umulungu.—Tito 2:11-14.
Chenjerani ndi Mpatuko
20. Kodi “otsutsana ndi Kristu” anatchedwa chiyani, ndipo kuwonekera kwawo kunatsimikizira kuyandikira kwa chiyani?
20 Tsopano Yohane akuchenjeza za okana Kristu. (Werengani 1 Yohane 2:18, 19.) Iye akukumbutsa okhulupirira anzake kuti iwo ‘anamva kuchokera kwa atumwi kuti okana Kristu analinkudza.’ Kuwonekera kwa “okana Kristu ambiri” kunatsimikizira kuti inali “nthawi yotsiriza,” mbali yomalizira ya nyengo ya atumwi. Ngakhale kuli kwakuti ‘otsutsa Kristu’ amenewo anapanga gulu la “okana Kristu,” anthu alionse paokha ambiri okana Kristu anayeserera kulambira Mulungu, koma “sanali a ife” ndipo anasiya Chikristu chowona. Tiri okondwera kuti kuchoka kapena kuchotsedwa kwa otere lerolino kumatetezera kuipitsidwa kwa mpingo.
21. Kodi nchifukwa ninji Akristu odzozedwa ndi mzimu ali ndi “chidziwitso,” ndipo ndi “chowonadi” chotani chimene amadziwa?
21 Malingaliro a ampatuko amakanidwa ndi Akristu okhulupirika obadwa ndi mzimu. Popeza kuti ‘kudzozedwa kochokera kwa woyerayo,’ Yehova, kumawathandiza kuzindikira Mawu ake, ‘iwo onse ali ndi chidziwitso.’ (Werengani 1 Yohane 2:20, 21.) Ndithudi iwo amadziwa “chowonadi” chimene chimaphatikizapo Yesu Kristu, pamene kuli kwakuti ampatuko ali ndi malingaliro olakwika onena za iye. Popeza kuti “kulibe bodza lochokera kwa chowonadi,” okonda Yehova onse amakana malingaliro abodza otero ndi awo amene amawachirikiza.
22. Kodi nchiyani chimene C. T. Russell anachita pamene mmodzi wa mabwenzi ake oyambirira anakana dipo?
22 Ndi iko komwe, “wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu saali Kristu,” Wodzozedwa wa Mulungu? (Werengani 1 Yohane 2: 22-25.) Eya, ‘yense wa kukana Atate ndi Mwanayo ndiye wokana Kristu’! Mokondweretsa, pamene tsamwali woyambirira wa wophunzira Baibulo Charles T. Russell anakana kukhulupirira dipo, Russell anasiya kuyanjana naye nayamba kufalitsa magazini ano, amene nthawi zonse alengeza chowonadi chonena za chiyambi cha Kristu, mbali Yaumesiya, ndi utumiki wachikondi monga “nsembe yoyanjanitsa.”
23. Kodi ndimotani mmene ‘kuvomereza Mwana’ kumayambukirira unansi wathu ndi Mulungu, ndi ziyembekezo zathu?
23 Ampatuko amene amakana Kristu, Yehova saali Bwenzi lawo. (Yohane 5:23) Koma ife amene ‘timavomereza Mwanayo poyera tiri naye Atate,’ pokhala muunansi woyanjidwa ndi Mulungu. (Mateyu 10:32, 33) Otsatira oyambirira okhulupirika a Yesu anamamatira ku zimene adamva ponena za Mwana wa Mulungu “kuyambira pachiyambi” cha miyoyo yawo monga Akristu. Ndipo ngati chowonadi chimodzimodzicho chiri m’mitima yathu, tidzakhala “m’chigwirizano” ndi onse awiri Mulungu ndi Kristu ndipo tidzalandira ‘chinthu cholonjezedwacho’, moyo wosatha.—Yohane 17:3.
Ophunzitsidwa ndi Yehova Mulungu
24. Kodi ndani amene ali “odzozedwa” ndi mzimu woyera, ndipo nchifukwa ninji iwo “safunikira aliyense kuwaphunzitsa”?
24 Kuyenda m’kuunika kwa umulungu ndi kusasochezedwa ndi ampatuko, tifunikira malangizo oyenerera auzimu. (Werengani 1 Yohane 2:26-29.) Obadwa ndi mzimuwo ali “odzozedwa” ndi mzimu woyera, afikiranso kudziwa Mulungu ndi Mwana wake, ndipo ‘sasowa kuti wina [wampatuko] awaphunzitse.’ Mwa kuwadzoza kwake ndi mzimu, Mulungu ‘akuphunzitsa’ Aisrayeli auzimu “za zinthu zonse” zofunika kumlambira movomerezeka. (Yohane 4:23, 24; 6:45) Tiri okondwera kuti monga Mboni za Yehova timalandira malangizo auzimu otero kuchokera kwa Mulungu kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45-47.
25, 26. (a) Kodi nchifukwa ninji odzozedwawo ali ndi “ufulu wa kulankhula”? (b) Kodi kumatanthauzanji ‘kugwiritsira ntchito chilungamo’?
25 Yohane akusonkhezera odzozedwa ophunzitsidwa bwino ‘kukhalabe m’chigwirizano ndi’ Mulungu. Mofananamo ‘ogwirizana’ ndi Yehova ali pa chigwirizano ndi Mwana wake. (Yohane 14:19-21) Chigwirizano chotero chikulimbikitsidwa kotero kuti ‘pamene iye [Kristu] akawonekera tikakhale nako kulimbika mtima osachita manyazi kwa iye pa kudza kwake,’ ndiko kuti, pa kukhalapo kwake.
26 Popeza kuli kwakuti ife tsopano tiri mkati mwa “kukhala pafupi” kwa Yesu kodi tingatsimikizire motani kuti tiribe kanthu kakuchita nako manyazi ndipo tikuyendadi m’kuunika kwa Mulungu? Mwa ‘kugwiritsira ntchito chilungamo.’ ‘Ngati tidziwa kuti Mulungu ali wolungama,’ akutero Yohane, ‘tidziwa kuti aliyense wakuchita chilungamo wabadwa kuchokera kwa iye.’ ‘Kuchita chilungamo’ kumatanthauza kumvera malamulo a Mulungu, kupewa chisalungamo, ndi kukhala ndi phande m’ntchito zabwino kwambirizo monga kupanga ophunzira ndi kuthandiza okhulupirira anzathu. (Marko 13:10; Afilipi 4:14-19; 1 Timoteo 6:17, 18) “Kubadwa” ndi Mulungu kumatanthauza kukhala “wobadwanso” monga ana ake auzimu.—Yohane 3:3-8.
27. Kodi nchiyani chimene kenako mtumwi Yohane adzatisonyeza?
27 Chotero Yohane wasonyeza mmene tingapitirizire kuyenda m’kuunika kwa umulungu. Kenako akusonyeza mmene tingakhalire ndi moyo monga ana a Mulungu. Kodi izi zimafunikiritsa chiyani?
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi ndiumboni wotani umene Yohane amapereka wakuti mwana wa Mulungu analiko, anavutika, ndipo anafa monga munthu?
◻ Kodi ndim’njira yotani mu imene Yesu Kristu aliri “nsembe yotetezera”?
◻ Kodi ndilamulo lotani limene Akristu ali nalo limene liri ponse pawiri “lakale” ndi “latsopano”?
◻ Kodi nchiyani chimene chidzachitikira dziko lino, ndipo ichi chiyenera kutiyambukira motani monga Akristu?
◻ Kodi odzozedwa angatsimikizirire motani kuti akuyenda m’kuunika kwa umulungu?
[Mawu Otsindika patsamba 28]
Kodi mukusonyeza chiyamikiro kaamba ka nsembe ya Yesu?