Oyang’anira Oyendayenda—Mphatso mwa Amuna
“Mmene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende, naninkha zaufulu kwa anthu [“mphatso mwa amuna,” NW].”—AEFESO 4:8.
1. Kodi ndi ntchito yotani imene inalengezedwa m’magazini ano mu 1894?
ZAKA zana limodzi zapitazo, Nsanja ya Olonda inalengeza kanthu kena katsopano. Kanthuko kanafotokozedwa kukhala “Mbali Ina ya Ntchito.” Kodi ntchito yatsopano imeneyo inali yotani? Inali chiyambi chamakono cha ntchito ya oyang’anira oyendayenda. Kope lachingelezi la September 1, 1894 la magazini ano linafotokoza kuti kuyambira nthaŵiyo abale oyenerera adzakhala akuchezetsa magulu a Ophunzira Baibulo ‘ndi cholinga chowamangirira m’choonadi.’
2. Kodi oyang’anira madera ndi a zigawo ali ndi mathayo otani?
2 M’zaka za zana loyamba C.E., mipingo yachikristu inali kuchezetsedwa ndi oyang’anira onga Paulo ndi Barnaba. Amuna okhulupirika ameneŵa anali ndi cholinga ‘chomangirira’ mipingoyo. (2 Akorinto 10:8) Lerolino, ndife odala pokhala ndi amuna zikwi zambiri amene akuchita zimenezo mwadongosolo. Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lawaika kukhala oyang’anira madera ndi a zigawo. Woyang’anira dera amatumikira mipingo pafupifupi 20, mlungu umodzi pampingo umodzi pafupifupi kaŵiri pachaka, akumapenda zolembedwa, kukamba nkhani, ndi kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda ndi ofalitsa a Ufumu a kumaloko. Woyang’anira chigawo amakhala tcheyamani wa msonkhano wadera uliwonse wa pachaka wa madera angapo, amakhala ndi phande mu utumiki wakumunda ndi mipingo ya pamalo a msonkhano, ndipo amapereka chilimbikitso m’nkhani zozikidwa pa Baibulo.
Mzimu Wawo Wodzimana
3. Kodi nchifukwa ninji oyang’anira oyendayenda ayenera kukhala ndi mzimu wodzimana?
3 Oyang’anira oyendayenda amakhala paulendo nthaŵi zonse. Zimenezo pazokha zimafuna mzimu wodzimana. Kuyenda ulendo kuchokera ku mpingo wina kumka ku winanso nthaŵi zambiri kungakhale kovuta, koma amuna ameneŵa ndi akazi awo amatero ndi mtima wachimwemwe. Woyang’anira dera wina anati: “Mkazi wanga amandichirikiza kwambiri ndipo samadandaula . . . Ndiyenera kumthokoza chifukwa cha mzimu wake wodzimana.” Oyang’anira madera ena amayenda ulendo makilomita 1,000 pochoka ku mpingo wina kumka ku wina. Ambiri amayendetsa galimoto, koma ena amapita kumalo osiyanasiyana ndi zoyendera za onse, njinga, pakavalo, kapena ndi miyendo. Woyang’anira dera wina wachiafirika amayenda ngakhale m’madzi kudutsa mtsinje mkazi wake ali pamapeŵa ake kuti akafike ku mpingo wina. Pamaulendo ake aumishonale, mtumwi Paulo anapirira ndi kutentha ndi kuzizira, njala ndi ludzu, kusoŵa tulo usiku, ngozi zamitundumitundu, ndi zizunzo zachiwawa. Analinso ndi “chalabadiro cha [“nkhaŵa ya,” NW] mipingo yonse”—imene oyang’anira oyendayenda onse amakhala nayo lerolino.—2 Akorinto 11:23-29.
4. Kodi zovuta za thanzi zingakhale ndi chiyambukiro chotani pa moyo wa oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo?
4 Monga momwe Timoteo mnzake wa Paulo analili, oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo nthaŵi zina amakhala ndi zovuta za thanzi. (1 Timoteo 5:23) Zimenezi zimawonjezera chipsinjo pa iwo. Mkazi wa woyang’anira dera wina akufotokoza kuti: “Ndimavutika kwambiri kukhala ndi abale nthaŵi zonse pamene sindikumva bwino. Kuchokera pamene ndinaleka kusamba, kuteroko kwakhala kondivuta kwambiri. Kulongedza katundu wathu yense kokha mlungu ndi mlungu ndi kusamukira kwina ndi vuto lalikulu. Nthaŵi zambiri, ndimayamba ndaima kaye ndi kupemphera kwa Yehova kuti andipatse nyonga ya kupitiriza.”
5. Mosasamala kanthu za mayesero amitundumitundu, kodi ndi mzimu wotani umene wasonyezedwa ndi oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo?
5 Mosasamala kanthu za zovuta za thanzi ndi mayesero ena, oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo amapeza chimwemwe mu utumiki wawo ndipo amasonyeza chikondi chodzimana. Ena aika moyo wawo pangozi kuti apereke thandizo lauzimu panthaŵi ya chizunzo kapena ya nkhondo. Pochezetsa mipingo, iwo asonyeza mzimu wonga uja wa Paulo, amene anauza Akristu a ku Tesalonika kuti: “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha; kotero ife poliralira inu, tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si uthenga wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.”—1 Atesalonika 2:7, 8.
6, 7. Kodi ndi chisonkhezero chabwino chotani chimene oyang’anira oyendayenda ogwira ntchito zolimba angapereke?
6 Monga akulu ena mumpingo wachikristu, oyang’anira oyendayenda amakhala “akuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.” Akulu onse otero ayenera ‘kuyesedwa oyenera ulemu woŵirikiza.’ (1 Timoteo 5:17) Chitsanzo chawo chingakhale chopindulitsa ngati, pambuyo ‘poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo titsanza chikhulupiriro chawo.’—Ahebri 13:7.
7 Kodi akulu oyendayenda ena akhala ndi chiyambukiro chotani pa ena? “Mbale P—— anandithandiza kwambiri chotani nanga m’moyo wanga!” Mboni ina ya Yehova inalemba motero. “Anali woyang’anira woyendayenda m’Mexico kuyambira 1960 ndi mtsogolo mwake. Monga mwana, ndinali kuyembekezera mwachidwi ndi mwachimwemwe kufika kwake. Pamene ndinali ndi zaka khumi, iye anandiuza kuti, ‘Iwenso udzakhala woyang’anira dera.’ Pazaka zovuta zaunyamata, ndinkamfunafuna nthaŵi zambiri chifukwa nthaŵi zonse anali kunena mawu anzeru. Nkhaŵa yake yaikulu inali kuŵeta gulu! Tsopano pokhala ndine woyang’anira dera, nthaŵi zonse ndimayesa kupatula nthaŵi yocheza ndi achichepere ndi kuwasonyeza zonulirapo zateokrase monga momwe iye anachitira kwa ine. Ngakhale pazaka zake zomaliza za moyo wake, mosasamala kanthu za kudwala mtima, Mbale P—— nthaŵi zonse anayesayesa kuuza munthu mawu olimbikitsa. Kutangotsala tsiku limodzi iye asanafe mu February 1995, anapita nane ku tsiku la msonkhano wapadera ndipo anasonyeza mbale wina amene ali wolemba mapulani zonulirapo zabwino. Pomwepo mbaleyo anafunsira utumiki wa pa Beteli.”
Amayamikiridwa
8. Kodi “mphatso mwa amuna” zofotokozedwa mu Aefeso chaputala 4 ndani, ndipo kodi amaupindulitsa motani mpingo?
8 Oyang’anira oyendayenda ndi akulu ena amene akhala ndi magawo a utumiki mwa chisomo cha Mulungu amatchedwa “mphatso mwa amuna.” Monga woimira Yehova ndi Mutu wa mpingo, Yesu wapereka amuna auzimu ameneŵa kuti atimangirire aliyense payekha ndi kuti tifikire uchikulire. (Aefeso 4:8-15) Mphatso iliyonse imayenera kuyamikiridwa. Zimenezi zili choncho makamaka ndi mphatso imene imatilimbitsa kuti tipitirizebe kutumikira Yehova. Nangano, ndi motani mmene tingasonyezere chiyamikiro kaamba ka ntchito ya oyang’anira oyendayenda? Kodi ndi m’njira ziti zimene tingasonyezere kuti ‘timakondabe amuna ameneŵa’?—Afilipi 2:29, NW.
9. Kodi ndi m’njira zotani zimene tingasonyezere chiyamikiro kwa oyang’anira oyendayenda?
9 Pamene chilengezo cha kuchezetsa kwa woyang’anira dera chiperekedwa, tingayambe kupanga makonzedwe a kukhala ndi phande lokwanira m’zochita za mpingo za mlunguwo. Mwinamwake tingapatule nthaŵi yochirikizira makonzedwe a utumiki wakumunda paulendowo. Tingathe kutumikira monga apainiya othandiza mwezi umenewo. Ndithudi, tidzafuna kugwiritsira ntchito malingaliro a woyang’anira dera kuti tiwongolere utumiki wathu. Mzimu wolabadira umenewo udzatipindulitsa ndipo udzampatsa chitsimikizo chakuti ulendo wake ngwothandiza. Inde, oyang’anira oyendayenda amachezetsa mipingo kuti atimangirire, koma nawonso amafunikira kuwamangirira mwauzimu. Nthaŵi zina Paulo anafunikira chilimbikitso, ndipo iye nthaŵi zambiri anapempha Akristu anzake kumpempherera. (Machitidwe 28:15; Aroma 15:30-32; 2 Akorinto 1:11; Akolose 4:2, 3; 1 Atesalonika 5:25) Mofananamo oyang’anira oyendayenda amakono amafunikira mapemphero athu ndi chilimbikitso.
10. Kodi tingathandize motani kuti ntchito ya woyang’anira woyendayenda ikhale yosangalatsa?
10 Kodi tauzapo woyang’anira dera ndi mkazi wake mmene timayamikirira kuchezetsa kwawo? Kodi timamyamikira kaamba ka uphungu wothandiza umene amatipatsa? Kodi timamdziŵitsa pamene malingaliro ake a utumiki wakumunda awonjezera chimwemwe chathu mu utumiki? Ngati timatero, zimenezo zidzathandiza kuchititsa ntchito yake kukhala yosangalatsa. (Ahebri 13:17) Woyang’anira dera wina ku Spain anasimba makamaka za mmene amakondera makalata oyamikira amene amalandira atachezetsa mipingo. “Timasunga makhadi ameneŵa ndi kuwaŵerenga pamene tikumva kulefuka,” iye akutero. “Amatilimbikitsa kwenikweni.”
11. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kudziŵitsa akazi a oyang’anira madera ndi a zigawo kuti timawakonda ndi kuwayamikira?
11 Mkazi wa woyang’anira woyendayenda amapinduladi ndi mawu oyamikira. Iye wadzimana kwambiri kuti athandize mwamuna wake mu utumiki wakumunda umenewo. Alongo okhulupirika ameneŵa amalepa chikhumbo cha chibadwa cha kukhala ndi nyumba zawo ndiponso, nthaŵi zambiri, chija cha kukhala ndi ana. Mwana wamkazi wa Yefita anali mmodzi wa atumiki a Yehova amene mwaufulu analepa mwaŵi wa kukhala ndi mwamuna ndi banja chifukwa cha choŵinda chimene atate wake anapanga. (Oweruza 11:30-39) Kodi kudzimana kwake kunaonedwa motani? Oweruza 11:40 amati: “Ana aakazi a Israyeli akamuka chaka ndi chaka kumliririra [“kumthokoza,” NW] mwana wa Yefita wa ku Gileadi, masiku anayi pa chaka.” Zimakhala bwino chotani nanga pamene sitiiŵala kuuza akazi a oyang’anira madera ndi a zigawo kuti timawakonda ndi kuwayamikira!
“Musaiŵale Kuchereza Alendo”
12, 13. (a) Kodi ndi maziko ati a m’Malemba amene alipo okhalira wochereza kwa oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo? (b) Sonyezani mmene kuchereza alendo kumeneko kungakhalire kopindulitsa kumbali zonse ziŵiri.
12 Kuchereza alendo ndiko njira ina yosonyezera chikondi ndi chiyamikiro kwa awo amene ali m’ntchito yoyendayenda yachikristu. (Ahebri 13:2) Mtumwi Yohane anathokoza Gayo chifukwa chochereza awo ochezetsa mipingo monga amishonale oyendayenda. Yohane analemba kuti: “Wokondedwa, uchita chokhulupirika nacho chilichonse, uwachitira abale ndi alendo omwe; amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wawo koyenera Mulungu, udzachita bwino: pakuti chifukwa cha dzinali anatuluka, osalandira kanthu kwa amitundu. Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana nacho choonadi.” (3 Yohane 5-8) Lerolino, tingapititse patsogolo ntchito yolalikira Ufumu mwa kuchereza mofananamo oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo. Zoonadi, akulu a kumaloko ayenera kutsimikizira kuti malo ogona ali okhutiritsa, koma woyang’anira chigawo wina anati: “Kuyanjana kwathu ndi abale sikuyenera kudalira pa amene angatichitire kanthu. Sitimafuna nkomwe kupereka chithunzi chimenecho. Tiyenera kulandira mwaufulu kuchereza kwa aliyense wa abale athu, wolemera kapena wosauka.”
13 Kuchereza alendo kungakhale kopindulitsa kumbali zonse ziŵiri. “M’banja lathu, tinali ndi mwambo wa kuitanira oyang’anira oyendayenda kudzakhala nafe,” Jorge, yemwe kale anali woyang’anira dera koma tsopano akutumikira pa Beteli, akukumbukira motero. “Ndikhulupirira kuti maulendo ameneŵa anandithandiza kwambiri koposa mmene ndinaganizira panthaŵiyo. Pazaka zanga za kusinkhuka, ndinali ndi zothetsa nzeru zauzimu. Amayi anada nkhaŵa ndi zimenezi koma sanadziŵe mmene akanandithandizira choncho anapempha woyang’anira dera kuti alankhule nane. Poyamba ndinali kumpeŵa, popeza ndinali kuwopa kuti adzandinena. Komano potsirizira pake mkhalidwe wake waubwenzi unandikopa. Tsiku lina Lolemba anandipempha kukadya naye chakudya, ndipo ndinamuuza zakukhosi chifukwa ndinatsimikiza kuti anali kundimvetsa. Anamvetsera mosamalitsa. Malingaliro ake otsatirika anagwiradi ntchito, ndipo ndinayamba kukula mwauzimu.”
14. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala oyamikira osati osuliza akulu oyendayenda?
14 Woyang’anira woyendayenda amayesa kukhala wothandiza mwauzimu kwa achichepere ndi achikulire omwe. Pamenepatu, tiyenera kusonyeza chiyamikiro chathu kaamba ka khama lake. Komabe, bwanji ngati tikanamsuliza chifukwa cha zofooka zake kapena kumyerekezera mosayenerera ndi ena amene achezetsapo mpingo wathu? Ndithudi zimenezo zingamlefule kwambiri. Paulo sanalimbikitsidwe pamene anamva kuti ntchito yake inali kusulizidwa. Mwachionekere, Akristu ena a ku Korinto anali kulankhula zoipa ponena za kaonekedwe kake ndi luso lake la kulankhula. Iye mwiniyo anagwira mawu osuliza amenewo kuti: “Akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mawu ake ngachabe.” (2 Akorinto 10:10) Komabe, nkosangalatsa kuti nthaŵi zambiri oyang’anira oyendayenda amamva mawu oyamikira achikondi.
15, 16. Kodi oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo amakhudzidwa motani ndi chikondi ndi changu chosonyezedwa ndi okhulupirira anzawo?
15 Woyang’anira dera wina ku Latin America amayenda tsiku lonse m’tinjira tamatope kuti akachezetse abale ake ndi alongo auzimu okhala m’dera lolamuliridwa ndi zigaŵenga. “Kumakhudza mtima kuona mmene abale amayamikirira kuchezetsako,” akulemba motero. “Ngakhale kuti ndimavutika kuti ndikafike kumeneko, ndikumayang’anizana ndi ngozi zambiri ndi zovuta, zonsezo zimafupidwa ndi chikondi ndi changu chosonyezedwa ndi abalewo.”
16 Woyang’anira dera wina mu Afirika akulemba kuti: “Chifukwa cha chikondi chimene abale anatisonyeza, tinalikonda kwambiri gawo la Tanzania! Abale anali okonzekera kuphunzira kwa ife, ndipo anakondwa kukhala nafe m’nyumba zawo.” Panali unansi wachikondi ndi wachimwemwe pakati pa mtumwi Paulo ndi banja lachikristu la Akula ndi Priska. Kwenikweni, Paulo anati za iwo: “Mulankhule Priska ndi Akula, antchito anzanga m’Kristu Yesu, amene anapereka khosi lawo chifukwa cha moyo wanga; amene ndiwayamika, siine ndekha, komanso mipingo yonse ya Ambuye ya kwa anthu amitundu.” (Aroma 16:3, 4) Oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo amayamikira kukhala ndi Aakula ndi Apriska amakono monga mabwenzi awo amene amayesetsa kuchereza alendo ndi kusonyeza ubwenzi.
Kulimbitsa Mipingo
17. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti makonzedwe a oyang’anira oyendayenda ali anzeru, ndipo kodi iwo amapeza kuti malangizo awo?
17 Yesu anati: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Nzeru ya makonzedwe a oyang’anira oyendayenda imaonekera m’njira yakuti iwo amathandizira kulimbitsa mipingo ya anthu a Mulungu. Paulendo wachiŵiri wa Paulo wa umishonale, iye ndi Sila anakhoza “kupyola pa Suriya ndi Kilikiya, nakhazikitsa [“akumalimbitsa,” NW] mipingo.” Buku la Machitidwe limatiuza kuti: “Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu. Kotero mipingoyo inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiŵerengo chawo tsiku ndi tsiku.” (Machitidwe 15:40, 41; 16:4, 5) Oyang’anira oyendayenda amakono amalandira malangizo auzimu mwa Malemba ndi zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” monga momwe zimakhalira kwa Akristu ena onse.—Mateyu 24:45.
18. Kodi oyang’anira oyendayenda amalimbitsa motani mipingo?
18 Inde, akulu oyendayenda ayenera kupitiriza kudya pagome lauzimu la Yehova. Ayenera kuzidziŵa bwino njira ndi zitsogozo zimene gulu la Mulungu limatsatira. Pamenepo amuna amenewo angakhaledi dalitso kwambiri kwa ena. Mwa chitsanzo chawo chabwino cha changu mu utumiki wakumunda, angathandize okhulupirira anzawo kuwongolera utumiki wachikristu. Nkhani zozikidwa pa Baibulo zokambidwa ndi akulu ameneŵa ochezetsa zimamangirira omvetsera mwauzimu. Mwa kuthandiza ena kutsatira uphungu wa Mawu a Mulungu, kutumikira mogwirizana ndi anthu a Yehova padziko lonse lapansi, ndi kugwiritsira ntchito zogaŵira zauzimu zoperekedwa ndi Mulungu mwa “kapolo wokhulupirika,” oyang’anira oyendayenda amalimbitsa mipingo imene amakhala ndi mwaŵi wa kuitumikira.
19. Kodi ndi mafunso otani amene atsala kuti ayankhidwe?
19 Pamene gulu la Yehova linayambitsa ntchito ya akulu oyendayenda pakati pa Ophunzira Baibulo pafupifupi zaka zana limodzi zapitazo, magazini ano anati: “Tidzayang’anira zotulukapo zake ndi chitsogozo chowonjezereka cha Ambuye.” Chitsogozo cha Yehova chaonekera bwino lomwe. Chifukwa cha dalitso lake ndi uyang’aniro wa Bungwe Lolamulira, ntchito imeneyi yafutukuka ndi kuwongoleredwa pazaka zambiri. Chotero, mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi ikulimbikitsidwa m’chikhulupiriro ndi kukula m’chiŵerengero tsiku ndi tsiku. Mwachionekere, Yehova akudalitsa mzimu wodzimana wa mphatso mwa amuna zimenezi. Koma kodi oyang’anira oyendayenda angachite motani ntchito yawo mwachipambano? Kodi zolinga zawo nzotani? Kodi angadzetse motani mapindu ochuluka?
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi mathayo ena a oyang’anira madera ndi a zigawo ngotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji oyang’anira oyendayenda afunikira kukhala ndi mzimu wodzimana?
◻ Kodi chiyamikiro chingasonyezedwe motani pa ntchito ya akulu oyendayenda ndi akazi awo?
◻ Kodi oyang’anira oyendayenda angachitenji kuti alimbikitse mipingo m’chikhulupiriro?
[Chithunzi patsamba 10]
Kukhala pamaulendo kumafuna mzimu wodzimana
[Chithunzi patsamba 13]
Kodi mwachereza oyang’anira oyendayenda ndi akazi awo?