Kuchereza Alendo Kwachikristu m’Dziko Logaŵanikana
“Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale [antchito anzawo m’choonadi, NW].”—3 YOHANE 8.
1. Kodi ndi mphatso zabwino koposa zotani zimene Mlengi wapatsa anthu?
“MUNTHU alibe kanthu kabwino pansi pano, koma kudya ndi kumwa, ndi kusekera; ndi kuti zimenezi zikhalebe naye m’vuto lake masiku onse a moyo wake umene Mulungu wampatsa pansi pano.” (Mlaliki 8:15) Ndi mawu amenewo mlaliki wachihebri wakaleyo akutiuza kuti Yehova Mulungu samangofuna zolengedwa zake zaumunthu kusangalala ndi kukhala ndi chimwemwe komanso amapereka njira yoti zikhalire motero. M’mbiri yonse ya anthu chikhumbo chimodzi chofala pakati pa anthu kulikonse chikuoneka kuti ndicho kukhala achimwemwe ndi kukhala ndi nthaŵi zosangalatsa.
2. (a) Kodi anthu apotoza motani chifuno cha Yehova kwa iwo? (b) Chotulukapo chake nchiyani?
2 Lerolino tikukhala m’chitaganya chokondetsa zokondweretsa mmene anthu ali otanganitsidwa ndi kulondola zokondweretsa ndi zosangalatsa. Anthu ochuluka akhala “odzikonda okha, . . . okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu,” monga momwe Baibulo linaneneratu. (2 Timoteo 3:1-4) Komabe, kumeneku ndi kupotoza moipitsitsa chifuno cha Yehova Mulungu. Pamene kulondola zosangalatsa kukhala chonulirapo chachikulu, kapena pamene kudzikhutiritsa kukhala cholinga chachikulu, sipamakhala kukhutira koona, ndipo ‘zonse zimakhala zachabe ndi kungosautsa mtima.’ (Mlaliki 1:14; 2:11) Chifukwa cha zimenezi dziko nlodzaza ndi anthu osungulumwa ndi ogwiritsidwa mwala, zimene, pambuyo pake, zimachititsa mavuto ambiri m’chitaganya. (Miyambo 18:1) Anthu samakhulupirirana ndipo amakhala ogaŵanikana monga mafuko, mitundu, pa makhalidwe, ndi pa za chuma.
3. Kodi chimwemwe ndi chikhutiro chenicheni tingachipeze motani?
3 Zinthu zikanakhala zosiyana chotani nanga anthu akanatsanzira njira ya Yehova ya kuchita ndi ena—kukhala okoma mtima, ooloŵa manja, ochereza alendo! Iye ananena momveka kuti chinsinsi cha chimwemwe chenicheni sichili pa kuyesa kukhutiritsa zikhumbo zathu. M’malo mwake, mfungulo yake ndi iyi: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Kuti tipeze chimwemwe ndi chikhutiro chenicheni, tiyenera kugonjetsa zopinga ndi magaŵano amene angatitsekereze. Ndipo tiyenera kukhala aufulu ndi awo amene akutumikira Yehova limodzi nafe. Nkofunika kuti timve uphunguwu: “Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale [antchito anzawo m’choonadi, NW].” (3 Yohane 8) Kusonyeza mkhalidwe wochereza alendo kwa ouyenerera, kufika pamlingo umene mikhalidwe yathu ilola, kumapindulitsa paŵiri—kumapindulitsa opatsa ndi olandira omwe. Chotero, kodi ndani amene ali pakati pa oyenerera amene tiyenera “kulandira”?
‘Chezani ndi Ana Amasiye ndi Akazi Amasiye’
4. Kodi ndi kusintha kotani m’maunansi a banja kumene kukuoneka ngakhale pakati pa ena a anthu a Yehova?
4 Mabanja okhazikika ndi maukwati achimwemwe si ofala lerolino. Ziŵerengero zomakwera za zisudzulo ndi chiŵerengero chomawonjezereka cha anakubala osakwatiwa kuzungulira dziko zasintha kwambiri banja la mwambo. Choncho, ambiri amene akhala Mboni za Yehova m’zaka zaposachedwapa amachokera m’mabanja osweka. Iwo mwinamwake ngosudzulidwa kapena opatukana ndi anzawo a muukwati, kapena amakhala m’mabanja a kholo limodzi. Ndiponso, monga momwe Yesu ananeneratu, choonadi chimene anaphunzitsa chachititsa kugaŵanikana m’mabanja ambiri.—Mateyu 10:34-37; Luka 12:51-53.
5. Kodi nchiyani chimene Yesu ananena chimene chingakhale cholimbikitsa kwa okhala m’mabanja ogaŵanikana?
5 Timasangalala kuona atsopano akuima mochirimika kumbali ya choonadi, ndipo kaŵirikaŵiri timawatonthoza ndi lonjezo lolimbikitsa la Yesu lakuti: “Ndinena ndi inu ndithu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amayi, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha ine, ndi chifukwa cha uthenga wabwinowo, amene sadzalandira makumi khumi tsopano nthaŵi ino, nyumba, ndi abale, ndi alongo, ndi amayi, ndi ana, ndi minda, pamodzi ndi mazunzo; ndipo nthaŵi ilinkudza, moyo wosatha.”—Marko 10:29, 30.
6. Kodi tingakhale motani ‘abale, alongo, amayi, ndi ana’ kwa “ana amasiye ndi akazi amasiye” amene ali pakati pathu?
6 Komabe, kodi ‘abale ndi alongo, ndi amayi, ndi ana’ ameneŵa ndani? Kungoona anthu ambiri pa Nyumba ya Ufumu, nthaŵi zambiri zana limodzi kapena kuposapo, amene amadzitcha abale ndi alongo sikumachititsa munthu pamenepo kuona ameneŵa monga abale, alongo, amayi ndi ana ake. Talingalirani za mfundoyi: Wophunzira Yakobo akutikumbutsa kuti, kuti kulambira kwathu kukhale kolandirika kwa Yehova, tiyenera ‘kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chawo, ndi kudzisungira ife eni osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.’ (Yakobo 1:27) Zimenezo zikutanthauza kuti sitiyenera kulola malingaliro akudziko a kunyada chifukwa cha chuma ndi chifukwa cha kukhala apamwamba kutsekereza chifundo chathu kwa “ana amasiye ndi akazi amasiye” ameneŵa. M’malo mwake tiyenera kuyamba ndife kukulitsa ubwenzi wathu kwa iwo ndi kuwachereza.
7. (a) Kodi chifuno chenicheni chocherezera “ana amasiye ndi akazi amasiye” nchiyani? (b) Ndani angakhalenso ndi phande pa kusonyeza mkhalidwe wa kuchereza alendo kwachikristu?
7 Kusonyeza mkhalidwe wa kuchereza alendo kwa “ana amasiye ndi akazi amasiye” sikumafuna nthaŵi zonse kuwapatsa zinthu zakuthupi zimene akusoŵa. Kwenikweni mabanja a kholo limodzi kapena mabanja ogaŵanikana pa chipembedzo samakhala ndi vuto la ndalama. Komabe, mayanjano abwino, kukhala monga banja limodzi, kuyanjana ndi anthu amisinkhu yosiyanasiyana, ndi kugaŵana zinthu zabwino zauzimu—zimenezi ndizo mbali za moyo zimene amakonda. Chotero, pokumbukira kuti chofunika si chochitika chambambande, koma mzimu wachikondi ndi umodzi, nkwabwino chotani nanga kuti, nthaŵi zina, ngakhale “ana amasiye ndi akazi amasiye” angakhale ndi phande pa kusonyeza mkhalidwe wochereza alendo kwa Akristu anzawo!—Yerekezerani ndi 1 Mafumu 17:8-16.
Kodi Pali Ochokera Kwina Pakati Pathu?
8. Kodi ndi kusintha kotani kumene kukuoneka m’mipingo yambiri ya Mboni za Yehova?
8 Tikukhala m’nthaŵi ya kusamuka kwa anthu ambiri. “Anthu oposa 100 miliyoni kuzungulira dziko akukhala m’maiko mmene saali nzika zake, ndipo 23 miliyoni amachotsedwa panyumba zawo m’maiko awo,” ikutero World Press Review. Chotulukapo chake cha zimenezi chakhala chakuti m’madera ambiri, makamaka m’mizinda yaikulu, mipingo ya anthu a Yehova imene panthaŵi ina inkakhala kwakukulukulu ndi fuko limodzi kapena anthu a m’dziko limodzi tsopano ili ndi anthu ochokera ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi. Mwinamwake ndi mmene zilili kwanuko. Komabe, kodi ndi motani mmene tiyenera kuonera “alendo” ndi “ochokera kwina” ameneŵa, monga mmene dziko limawatchera, amene chinenero chawo, miyambo, ndi moyo wawo zingakhale zosiyana ndi zathu?
9. Kodi ndi msampha waukulu wotani umene ungatikole ponena za kaonedwe kathu ka “alendo” ndi “ochokera kwina” amene amadza mumpingo wachikristu?
9 Kunena mosavuta, sitiyenera kulola malingaliro alionse owopa alendo ndi kuwada kutichititsa kuganiza kuti ife m’njira ina yake ndife oyenerera kwambiri mwaŵi wa kudziŵa choonadi kuposa aja amene anachokera ku dziko lina kapena limene amati nlachikunja; kapenanso sitiyenera kuganiza kuti alendo ameneŵa akutilanda Nyumba ya Ufumu kapena zinthu zina. Mtumwi Paulo anakumbutsa Akristu achiyuda a m’zaka za zana loyamba, amene anali ndi malingaliro ameneŵa, kuti palibe analidi woyenerera; chinali chisomo cha Mulungu chimene chinatheketsa aliyense kupeza chipulumutso. (Aroma 3:9-12, 23, 24) Tiyenera kukhala achimwemwe kuti chisomo cha Mulungu chikufikira anthu ambiri tsopano amene, m’njira ina yake, analibe mwaŵi wa kumva uthenga wabwino. (1 Timoteo 2:4) Kodi tingasonyeze motani kuti chikondi chathu pa iwo nchenicheni?
10. Kodi tingasonyeze motani kuti tili ochereza alendo enieni kwa “ochokera kwina” amene ali pakati pathu?
10 Tingatsatire uphungu wa Paulo wakuti: “Mulandirane wina ndi mnzake, monganso Kristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.” (Aroma 15:7) Pozindikira kuti kaŵirikaŵiri anthu ochokera ku maiko ena kapena makulidwe osiyana amasoŵa zinthu zofunika, tiyenera kuwakomera mtima ndi kuwadera nkhaŵa ngati tingathe kuchita zimenezo. Tiyenera kuwalandira pakati pathu, kukhala ndi aliyense wa iwo “monga wa m’dziko momwemo,” ndi ‘kumkonda monga tidzikonda tokha.’ (Levitiko 19:34) Zimenezi zingakhale zovuta kuchita, koma tidzapambana ngati tikumbukira uphungu wakuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.”—Aroma 12:2.
Gaŵanani ndi Oyera Mtima
11, 12. Kodi ndi chisamaliro chapadera chotani chimene chinaperekedwa pa atumiki ena a Yehova (a) mu Israyeli wakale (b) m’zaka za zana loyamba?
11 Pakati pa awo amene ali oyenereradi chisamaliro ndi kuchereza alendo kwathu pali Akristu okula msinkhu amene amagwiritsa ntchito kaamba ka ubwino wathu wauzimu. Yehova anapanga makonzedwe apadera a ansembe ndi Alevi mu Israyeli wakale. (Numeri 18:25-29) M’zaka za zana loyamba, Akristu analimbikitsidwanso kusamalira aja amene anali kutumikira pamathayo apadera. Nkhani ya pa 3 Yohane 5-8 ikutipatsa chithunzi cha chomangira cholimba cha chikondi chimene chinali pakati pa Akristu oyambirira.
12 Mtumwi Yohane wokalambayo anayamikira kwambiri kukoma mtima ndi kuchereza alendo kumene Gayo anasonyeza kwa abale ena oyendayenda amene anatumidwa kukachezera mpingo. Abale ameneŵa— kuphatikizapo Demetriyo amene zikuoneka ngati ndiye anapereka kalatayo—anali alendo kapena osadziŵana ndi Gayo poyamba. Koma analandiridwa bwino popeza “chifukwa cha dzinali [la Mulungu] anatuluka.” Yohane anafotokoza motere: “Chifukwa chake ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale [antchito anzawo m’choonadi, NW].”—3 Yohane 1, 7, 8.
13. Kodi ndani pakati pathu lerolino amene makamaka ayenera ‘kulandiridwa’?
13 Lerolino, m’gulu la Yehova, pali ambiri amene akugwiritsa ntchito kaamba ka gulu lonse la abale. Ameneŵa amaphatikizapo oyang’anira oyendayenda, amene amathera nthaŵi ndi nyonga yawo pa kumangirira mipingo mlungu ndi mlungu; amishonale, amene amasiya mabanja ndi mabwenzi kuti akalalikire ku maiko achilendo; awo amene amatumikira panyumba za Beteli kapena maofesi anthambi, amene amapereka mautumiki awo modzifunira kuti achirikize ntchito ya padziko lonse ya kulalikira; ndi aja amene ali mu utumiki waupainiya, amene amathera nthaŵi ndi nyonga yawo yaikulu mu utumiki wakumunda. Kwenikweni, onseŵa amagwiritsa ntchito, osati kuti adzipezere ulemu kapena phindu, koma chifukwa cha kukonda kwawo ubale wachikristu ndi Yehova. Iwo ngwoyenerera kuti ife tiwatsanzire chifukwa cha kudzipereka kwawo kwa mtima wonse ndipo ayeneradi ‘kulandiridwa.’
14. (a) Kodi timakhala motani Akristu abwino kwambiri pamene tichereza okhulupirika? (b) Kodi nchifukwa ninji Yesu ananena kuti Mariya anasankha “dera lokoma”?
14 Pamene ‘tilandira otere,’ mtumwi Yohane anatero, ‘timakhala antchito anzawo m’choonadi.’ Chotero timakhala Akristu abwinopo m’njira ina yake. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti ntchito zachikristu zimaphatikizapo kuchitira okhulupirira anzathu zabwino. (Miyambo 3:27, 28; 1 Yohane 3:18) Palinso mapindu ena. Pamene Mariya ndi Marita analandira Yesu m’nyumba mwawo, Marita anafuna kukhala wochereza alendo wabwino mwa kukonzera Yesu “zinthu zambiri.” Mariya anasonyeza kuchereza alendo m’njira yosiyana. Iye ‘anakhala pa mapazi a Ambuye, namva mawu ake,’ ndipo Yesu anamyamikira kaamba ka kusankha “dera lokoma.” (Luka 10:38-42) Kaŵirikaŵiri kulankhulana ndi kukambitsirana ndi awo amene ali ndi zaka zambiri za chidziŵitso kumakhala kwapadera pamene ticheza nawo madzulo.—Aroma 1:11, 12.
Pa Zochitika Zapadera
15. Kodi ndi zochitika zapadera ziti zimene zingakhale nthaŵi zosangalatsa kwa anthu a Yehova?
15 Ngakhale kuti Akristu oona samatsatira miyambo yofala kapena kusunga maholide ndi mapwando akudziko, pali nthaŵi pamene amakumana kuti ayanjane wina ndi mnzake. Mwachitsanzo, Yesu anapezeka pa phwando la ukwati ku Kana ndipo anawonjezera chisangalalo pa chochitikacho mwa kuchita chozizwitsa chake choyamba kumeneko. (Yohane 2:1-11) Momwemonso lerolino, anthu a Yehova amakhala pamodzi ndi kusangalala pa zochitika zapadera zofananazo, ndipo phwando loyenera limawonjezera chimwemwe pa zochitika zimenezi. Komabe, kodi nchiyani chimene chili choyenera?
16. Kodi ndi zitsogozo zotani zimene tili nazo ponena za khalidwe labwino ngakhale pa zochitika zapadera?
16 Mwa kuphunzira kwathu Baibulo, timadziŵa khalidwe loyenera kwa Akristu, ndipo timatsatira limeneli nthaŵi zonse. (Aroma 13:12-14; Agalatiya 5:19-21; Aefeso 5:3-5) Macheza, kaya a pa mapwando aukwati kapena pa chochitika china chilichonse, samatipatsa ufulu wa kunyalanyaza miyezo yathu yachikristu kapena wa kuchita chinachake chimene sitingachite masiku onse: ndiponso sitimakhala ndi thayo la kutsatira miyambo yonse ya m’dziko limene timakhala. Yambiri ya imeneyi yazikidwa pa machitachita onyenga achipembedzo kapena pa miyambo, ndipo ina imaloŵetsamo khalidwe losavomerezeka konse kwa Akristu.—1 Petro 4:3, 4.
17. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zikusonyeza kuti phwando la ukwati ku Kana linali lolinganizidwa ndi loyang’aniridwa bwino? (b) Nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yesu anayanja chochitika chimenecho?
17 Titaŵerenga Yohane 2:1-11, timaona mosavuta kuti chochitikacho chinali chambambande ndi kuti panalinso oitanidwa ambiri. Komabe, Yesu ndi ophunzira ake anali alendo ‘oitanidwa’; sanafikepo mwadzidzidzi, ngakhale kuti ena a iwo mwinamwake anali achibale a mwini phwando. Timaonanso kuti panali awo amene anali “atumiki” limodzinso ndi “mkulu,” amene anali kupereka malangizo pa zimene zinali kuperekedwa kwa anthu kapena kuchitidwa. Zonsezi zikusonyeza kuti chochitikacho chinali cholinganizidwa bwino ndi choyang’aniridwa bwino. Nkhaniyo imatha mwa kunena kuti mwa zimene anachita paphwandolo, Yesu ‘anaonetsera ulemerero wake.’ Kodi akanasankha chochitikacho kuti akachitireko zimenezo chikanakhala phwando laphokoso ndi losalamulirika? Mosakayikira ayi.
18. Kodi nchiyani chimene chiyenera kulingaliridwa mwamphamvu pa kucheza kulikonse?
18 Ndiyeno, bwanji ponena za zochitika zilizonse zapadera zimene tingachitire m’nyumba mwathu? Tiyenera kukumbukira kuti chifuno cha kulandira ena mwa kuwachereza ndicho chakuti tonsefe ‘tikhale antchito anzawo m’choonadi.’ Chotero, sikokwanira kungotcha chochitikacho kukhala chochitika cha “Mboni.” Funso lingafunsidwe kuti, Kodi kwenikweni chili umboni wa amene ife tili ndi zimene timakhulupirira? Sitiyenera konse kuona zochitika zimenezi monga mpata woonera pamene tingafike kupikisana ndi dziko pa njira zake, pa kuloŵerera ‘m’chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, ndi matamandidwe a moyo.’ (1 Yohane 2:15, 16) M’malo mwake, zochitika zimenezi ziyenera kusonyeza bwino ntchito yathu monga Mboni za Yehova, ndipo tiyenera kutsimikizira kuti zimene tikuchita zikudzetsa ulemerero ndi ulemu kwa Yehova.—Mateyu 5:16; 1 Akorinto 10:31-33.
‘Cherezani Mosadandaula’
19. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ‘ocherezana wina ndi mnzake, osadandaula’?
19 Pamene mikhalidwe ya dziko ikuipaipabe ndipo anthu akugaŵanikana kuposa ndi kale lonse, tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tilimbitse chomangira cholimba chimene chili pakati pa Akristu oona. (Akolose 3:14) Kuti tichite chimenechi tiyenera kukhala ndi ‘chikondano chenicheni mwa ife tokha,’ monga momwe mtumwi Petro anatilimbikitsira. Ndiyeno, mwa mawu olimbikitsa kuchigwiritsira ntchito, anawonjezera kuti: “Mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula.” (1 Petro 4:7-9) Kodi tili ofunitsitsa kuyambirira kukhala wochereza kwa abale athu, kulimbikira kukhala okoma mtima ndi othandiza? Kapena kodi timadandaula pakakhala mpata umenewu? Ngati timatero, tikutsekereza chimwemwe chimene tingakhale nacho ndiponso timataya mphotho ya chimwemwe kaamba ka kuchita zabwino.—Miyambo 3:27; Machitidwe 20:35.
20. Kodi tidzakhala ndi madalitso otani ngati tili ndi chizoloŵezi cha kuchereza alendo m’dziko logaŵanikali?
20 Kugwira ntchito pamodzi ndi Akristu anzathu, kukhala okoma mtima ndi kucherezana wina ndi mnzake, kudzabweretsa madalitso ochuluka. (Mateyu 10:40-42) Kwa otereŵa Yehova analonjeza kuti “adzawachitira mthunzi, sadzamvanso njala, kapena ludzu.” Kukhala mumthunzi wa Yehova ndiko kutetezeredwa ndi kucherezedwa ndi iye. (Chivumbulutso 7:15, 16; Yesaya 25:6) Inde, patsogolopa tikuyembekezera kucherezedwa ndi Yehova kosatha.—Salmo 27:4; 61:3, 4.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nchiyani chimene sitiyenera kunyalanyaza ngati tikufuna kupeza chimwemwe ndi chikhutiro chenicheni?
◻ Kodi “ana amasiye ndi akazi amasiye” ndani, ndipo kodi tiyenera ‘kucheza nawo’ motani?
◻ Kodi “alendo” ndi “ochokera kwina” amene ali pakati pathu tiyenera kuwaona motani?
◻ Kodi ndani amene ayenera chisamaliro chapadera lerolino?
◻ Kodi zochitika zapadera ziyenera kusonyeza motani mzimu weniweni wa kuchereza alendo?
[Zithunzi pamasamba 16, 17]
Pa mapwando tingakhale ochereza kwa ochokera kwina, ana amasiye, aja okhala mu utumiki wanthaŵi zonse, ndi oitanidwa ena