‘Mulungu Adzatsiriza Kuphunzitsidwa Kwanu’
WOTHAMANGA amene akukonzekera kaamba ka chochitika chapadera ayenera kudziphunzitsa kwamphamvu. Iye amafunikira kulipanga thupi lake m’mkhalidwe wabwino kotero kuti patsiku lalikulu limenelo, iye akapereka kachitidwe kake kabwino koposa kothekera. Akristu, nawonso, ayenera kuphunzitsidwa kwamphamvu koma ndi chonulirapo chosiyana. Mtumwi Paulo anati: “Dziphunzitseni ndi kupembedza Mulungu monga chonulirapo chanu.”—1 Timoteo 4:7, NW.
Chotero, Mkristu ayenera kudzisunga iye mwini mu mkhalidwe wabwino mwauzimu. Monga mmene wothamanga amamangirira thupi lake, Mkristu amamangirira mphamvu yake yauzimu ndi chipiriro. Iye amachita ichi mwakuphunzira Mawu a Mulungu Baibulo, mwapemphero, mwakuyanjana mokhazikika ndi Akristu anzake, ndi mwakupanga chisonyezero chapoyera cha chikhulupiriro chake.
Wothamanga kawirikawiri amakhala ndi mphunzitsi, ndipo Akristu, nawonso, ali ndi mphunzitsi. Ndani? Palibe wina woposa Yehova Mulungu iye mwini! Mtumwi Petro analoza kudera nkhawa kwa Yehova kaamba ka programs ya kuphunzitsa ya Kristu, akumalemba: “Mulungu wa kukoma mtima konse kwapadera, . . . iye mwini adzatsiriza kuphunzitsidwa kwanu, adzakulimbikitsani, adzakukhalitsani amphamvu.” (1 Petro 5:10, NW) Kodi ndi kuphunzitsa kotani kumene Yehova amatipatsa ife? Kwa mitundu yosiyanasiyana, ndipo konse kuli kofunika ngati tikufuna kukhalabe mu mkhalidwe wabwino monga Akristu.
Chilango Chachindunji
Petro iye mwini analandira kuphunzitsidwa kuchokera kwa Yehova. Tingaphunzire zambiri kuchokera ku chokumana nacho chake. Nthawi zina kuphunzitsidwa kwa Petro kunali kopweteka. Tangolingalirani ndimotani mmene Petro anamverera pamene anayesa kumukhwethemula Yesu ku kupita kupyola mu chifuno cha Mulungu, ndipo Yesu anayankha: “Pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; ndiwe chokhumudwitsa ine; chifukwa susamalira za Mulungu, koma za anthu.” (Mateyu 16:23) Tangolingalirani, kachiwirinso, mmene anamverera zaka zambiri pambuyo pake pamene kuwopa munthu kunamtsogolera iye kuchita mopanda nzeru. Mtumwi Paulo anapereka chilango cha Yehova pa chochitikika chimenecho: “Koma pamene Kefa [Petro] anadza ku Antiokeya ndinatsutsana naye pamaso pake, pakuti anatsutsika wolakwa.”—Agalatiya 2:11-14.
Mosasamala kanthu za chimenecho, pa zochitika zonse ziwiri Yehova anali kuphunzitsa Petro. Iye anaphunzira kuti “chilango chiri chonse pakuchitika sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Kulandira zidzudzulo zamphamvu zimenezo monga chilango chochokera kwa Yehova kunamthandiza Petro kupeza kawonedwe kabwino ka zinthu ndipo kunamuphunzitsa iye mu mikhalidwe yofunikira ya Chikristu ya chifatso ndi kudzichepetsa.—-Miyambo 3:34; 15:33.
Kusamalira Mikhalidwe
Yehova angatiphunzitse ife mwakulola mikhalidwe kubuka yomwe iri yovuta kuisamalira—nthawi zina imeneyi imakhala mkati mwa mpingo Wachikristu. Timakula monga Akristu pamene tipemphera kaamba ka chitsogozo, kugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo amene taphunzira, ndi kuwona ndimotani mmene kuŵagwiritsira ntchito maprinsipulo amenewo kuti nthawi zome njira yabwino koposa.
Petro anaphatikizidwa mu kuwombana kwaumunthu komwe kunabuka pakati pa atumwi a Yesu. Pamene tiwerenga mbiri ya chimenechi, chiri chosangalatsa kuwona ndimotani mmene Yesu anagwiritsira ntchito kuwombana kumeneku—komwe kunalidi chotulukapo cha kupanda ungwiro ndi kusazolowera—mwawi wa kuphunzitsira otsatira ake mu mikhalidwe yoyenera ya Chikristu ya chikondi, kudzichepetsa, ndi kukhululukira.—Mateyu 18:15-17, 21, 22; Luka 22:24-27.
Paulo anachitiranso umboni kuwombana kwaumunthu. (Machitidwe 15:36-40; Afilipi 4:2) Iye analongosola ndimotani mmene mavuto oterowo amapatsira Akristu mwawi wa kulandira kupbunzitsidwa: “Loleranani wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni nokha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake, monganso [Yehova, NW] anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”—Akolose 3:13, 14.
Mu zana loyamba, ngozi yowopsya kwambiri inawoneka pakati pa Akristu. Petro anachenjeza ponena za iyo: [“Padzakhala aphunzitsi onyenga pakati panu. Amenewo adzalowetsamo mwkachetechete mipatuko yowononga ndipo, NW] adzakana ngakhale Ambuye amene adawagula, akumadzidzetsera chiwonongeko chofulumira. Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zawo; chifukwa cha iwo njira ya chowonadi idzanenedwa zamwano.” (2 Petro 2: 1, 2) Chokumana nacho chimenechi chidzatulukamo mu chiwonongeko cha “aphunzitsi onyenga” osalapa. (2 Petro 2:3) Koma bwanji ponena za awo amene anakhala okhulupirika? Chokumana nacho chikawaphunzitsa iwo ‘kutsitsimutsa mtima wawo wowona ndi kuwakumbutsa.’ (2 Petro 3:1) Kugalamuka kwawo mu kuchinjiriza kulowerera kwa ziphunzitso zonyenga kukaitanira pa iwo kubwereramo mu zifukwa za chikhulupiriro chawo. Pamene iwo anawona zotulukapo zoipa za kachitidwe ka “aphunzitsi onyenga,” chidaliro chawo mu chowonadi cha Chikristu chikakhala champhamvu koposa.—2 Petro 3:3-7. ,
Mwachitsanzo, mu mpingo umodzi mtumwi Yohane wachikulire anatsutsidwa ndi Diotrefe, munthu wonyada yemwe anali ndi ulemu wochepera kaamba ka ulamuliro wa Yohane ndi amene sanakane kokha kulandira athenga otumizidwa ndi Yohane koma angakhale anayesera kuwachotsa mu mpingo awo amene anatero. Ichi chingakhale chinali chopweteka kwambiri kwa Akristu owona mu mpingo umodzi ndi Diotrefe. Koma chinawapatsa iwo mwawi wa kusonyeza kuti iwo sanali ‘otsanzira choipa’ ndipo chotero kulandira kuphunzitsidwa kwapamwamba mu kukhulupirika kwa Yehova ndi ku Ulamuliro wa atumwi.—3 Yohane 9-12.
Mkuchita ndi Osakhala Akristu
Yesu ananena kuti otsatira ake sanali mbali yadziko lapansi. (Yohane 17:16) Kugonjera koyambirira kwa Akristu kuli kulinga kwa Yehova ndi Ufumu wake. Iye amayesera kusunga kaimidwe kapamwamba ka makhalidwe abwino a Mulungu, chotero zikondwerero zake ndi zodera nkhaŵa zake zenizeni ziri zosiyana ndi zija za dziko. Komabe, Mkristu ayenera kukhala mu dziko, ndipo ichi mosakaikira chimapangitsa kukwinjika. Petro, mkati mwa uminisitala wake wautali, angakhale anawona nthawi zochuluka pamene Akristu anayenera kupanga zosankha zovuta, kulinganiza zofuna za dziko ndi zofunsidwa za chikumbumtima chawo. Mu kalata yoyamba ya Petro, iye anapereka uphungu wabwino, wokhoza kugwirirapo ntchito ponena za ndimotani mmene ichi chingachitidwire kotero kuti Akristu akhale ndi “chikumbumtima chabwino.”—1 Petro 2:13-20; 3:1-6, 16.
Komabe, monga Akristu timayang’ana kutsogolo kunthawi pamene sitidzafunikira kulingalira zofuna za dongosolo iri lakachitidwe kazinthu. Koma panthawi ino tikuphunzitsidwa mu chipiriro ndi kuloledwa kusonyeza kukhulupirika kwathu pamaso pa ziyeso ndi zisonkhezero zopanda umulungu. Pamene tikuzolowerana mwakugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo mu mikhalidwe yosiyanasiyana ndipo molimba mtima kuchita m’njira imene tonsefe tikudziwa kuti Yehova akutifuna ife kuchita, tikuphunzitsidwanso mu nzeru yeniyeni ndi kulimbamtima. Tangolingalirani ponena zandi kuphunzitsidwa kowonjezereka kotani kumene tidzakhala titalandira chifukwa cha kukhala titakhala mu dongosolo iri lakachitidwe kazinthu ndipo mwachipambano kusamalira mavuto ambiri ovuta!
Pansi pa Chizunzo
Pamene Petro analankhula ponena za kuphunzitsidwa kwathu ndi Mulungu, iye mwapadera anali kuloza ku chizunzo. Iye anasonyeza kuti Akristu ayenera kuyembekezera chizunzo: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”—1 Petro 5:8; onaninso 2 Timoteo 3:12.
Petro anali woyeneretsedwa kulankhula ponena za ichi chifukwa iye mwaumwini anavutika ndi chizunzo. Mu masiku oyambirira a mpingo wa Chikristu, iye ndi atumwi ena anakwapulidwa ndi kulamuliridwa kuleka kulalikira. Chivomerezo chawo? Iwo “anapita kuchokera kubwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.”—Machitidwe 5:41.
Chotero, Petro analankhula kuchokera ku chokumana nacho, limodzi ndi pansi pa kuuziridwa, pamene iye anati: “Koma popeza mulawana ndi Kristu zowawa zake, kondwerani; kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu. Mukatonzedwa padzina la Kristu, odala inu; pakuti mzimu wa ulemerero, ndi mzimu wa Mulungu upuma painu.”—1 Petro 4:13, 14.
Inde, chizunzo chotheratu chingatumikire monga mtundu wa kuphunzitsa. Pansi pa icho, Mkristu amaphunzira kudalira mowonjezereka pa mzimu wa Mulungu. Chikhulupiriro chake chimakulitsa “mkhalidwe woyesedwa.” (1 Petro 1:7) Iye amaphunzitsidwa kulimbamtima kozikidwa pa mphamvu ya Yehova. (2 Timoteo 1:7) Iye amakulitsa kupirira koleza mtima, ndipo mofanana ndi Yesu, iye ‘amaphunzira kumvera kupyolera mu zinthu anavutika nazo.’—Ahebri 5:8; 1 Petro 2:23, 24.
Yehova Amatsiriza Kuphunzitsidwa Kwathu
Komabe, mavuto ovuta kwambiri, kuphatikizapo chizunzo, chimene Akristu amapirira sizimabwera kuchokera kwa Mulungu. Yakobo anapereka uphungu: “Munthu poyesedwa, asanena, ‘ndiyesedwa ndi Mulungu.’ Pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Mavuto angabuke kuchokera ku zoyambitsa zochuluka, kuphatikizapo pamene anthu apanga zophophonya kapena kuchita zolakwa mwakufuna kwawo. Komabe, popeza zinthu zoterozo zimachitika, Yehova amazigwiritsira ntchito kuphunzitsa atumiki ake mu mikhalidwe yofunika kwambiri ya Chikristu.
Yakobo, Yeremiya, Petro, Paulo, ndi onse a atumiki a Mulungu mu nthawi ya Baibulo anaphunzitsidwa mu njira imeneyi. Ife, nafenso, pamene tiyang’anizana ndi mikhalidwe yovuta yosiyanasiyana, tiyenera kuiwona iyo monga magwero akuphunzira ololedwa ndi Yehova. Mwakuyang’anizana nawo kwathu mu mphamvu ya Yehova, tidzaphunzitsidwa kumvera, nzeru, kudzichepetsa, kulimbamtima, chikondi, kulekerera, ndi mikhalidwe ina yambiri yowonjezereka.—Yerekezani ndi Yakobo 1:2-4.
Tikulimbikitsidwa, nafenso, mwakudziwa kuti mbali imeneyi ya kuphunzitsidwa kwathu tsiku lina idzatha. Chotero, Petro anatonthoza Akristu anzake, akumati: “Koma mutavutika kanthawi, Mulungu wakukoma mtima konse kwapadera, amene anakuitanirani ku uleme rero wake wosatha mogwirizana ndi Kristu, iye mwini adzatsiriza kuphunzitsidwa kwanu, adzakulimbikitsani, adzakukhalitsani amphamvu.” (1 Petro 5:10, NW) Mawu amenewo amagwira ntchito ndi mphamvu yofananayo kwa “khamu lalikulu” lomwe likuyang’ana kutsogolo ku moyo wosatha mu Paradaiso wa dziko lapansi.
Lingaliro limenelo mwa ilo lokha liyenera kutithandiza ife kugonjera molezamtima ku zokumana nazo zophunzitsa zimenezi, kukhala otsimikizira kusagonjera. Chotero, tidzakumana ndi chowonandi cha mawu olimbikitsa a Paulo: “Motero tiyeni tisaleke kuchita chimene chiri chabwino, pakuti mu nyengo yokwanira tidzatuta tikapanda kulema.”—Agalatiya 6:9, NW.