“Mulimbanetu Chifukwa cha Chikhulupiriro”!
“Mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.”—YUDA 3.
1. Kodi Akristu oona lerolino ali pankhondo inayake iti?
NTHAŴI zonse asilikali amakhala ndi moyo wovuta kwambiri pankhondo. Talingalirani za kuvala zovala zonse zankhondo ndi zida zake ndiyeno kuyenda mtunda wamakilomita osaŵerengeka mosasamala kanthu za machedwe, kuchita maphunziro otopetsa kotheratu a kugwiritsira ntchito zida zankhondo, kapena kudzitetezera ku zinthu zonse zimene zingawatayitse moyo kapena kuwavulaza. Komabe, Akristu oona samenya nawo nkhondo za amitundu. (Yesaya 2:2-4; Yohane 17:14) Ngakhale zili tero, sitiyenera kuiŵala kuti tonsefe tili pankhondo inayake. Satana ali paudani waukulu ndi Yesu Kristu ndiponso otsatira ake a padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:17) Onse amene amasankha kutumikira Yehova Mulungu, kwenikweni, amaloŵa usilikali womenya nkhondo yauzimu.—2 Akorinto 10:4.
2. Kodi Yuda akuifotokoza motani nkhondo ya Akristu, ndipo kalata yake ingatithandize motani kupirira m’nkhondoyo?
2 Nchifukwa chakedi, mbale wa Yesu wa atate wina, Yuda, analemba kuti: “Okondedwa, pakuchita changu chonse chakukulemberani za chipulumutso cha ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro chapatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.” (Yuda 3) Pamene Yuda akulimbikitsa Akristu kuti ‘alimbanetu,’ iye akugwiritsira ntchito mawu ofanana ndi mawu akuti ‘nsautso.’ Inde, kulimbana kumeneku kungakhale kovuta, ngakhalenso kosautsa! Kodi nthaŵi zina mumavutika kupirira pankhondo imeneyi? Kalata ya Yuda yaifupi koma yamphamvu ingatithandize. Iyo imatilimbikitsa kukana khalidwe loipa, kulemekeza ulamuliro woikidwa ndi Mulungu, ndi kudzisunga ife eni m’chikondi cha Mulungu. Tiyeni tione mmene tingagwiritsirire ntchito uphungu umenewu.
Kanani Khalidwe Loipa
3. Kodi ndi mkhalidwe uti mumpingo wachikristu wa m’tsiku la Yuda umene unali wofunika chisamaliro cha mwamsanga?
3 Yuda anaona kuti si Akristu anzake onse amene anali kupambana m’nkhondo yolimbana ndi Satana. Gulu la Akristulo linali mumkhalidwe wina wofunika kuusamalira mwamsanga. Amuna oipa “anakwaŵira m’tseri,” analemba motero Yuda. Amuna ameneŵa anali kuchirikiza khalidwe loipa mwamachenjera. Ndipo mochenjera anali kupeza chodzikhululukira pazochita zawo, “kusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa.” (Yuda 4) Mwinamwake, monga anthu akale otchedwa ma Gnostic, iwo ankaganiza kuti munthu akamachimwa kwambiri, amalandiranso chisomo cha Mulungu chochuluka—choncho, kwenikweni, kuli bwino kuchimwa kwambiri! Kapenanso ankaganiza kuti Mulungu wachifundo sangawalange. Mulimonse mmene zinalili, iwo sanali olondola.—1 Akorinto 3:19.
4. Kodi Yuda akutchula zitsanzo za m’Malemba zitatu ziti za ziweruzo zakale za Yehova?
4 Yuda akutsutsa malingaliro awo oipawo mwa kutchula zitsanzo zitatu za ziweruzo za Yehova m’nthaŵi zakale: kwa Aisrayeli amene anali “osakhulupirira”; kwa “angelo amene sanasunga chikhalidwe chawo choyamba” kuti akachimwe ndi akazi; ndiponso kwa anthu a m’Sodomu ndi Gomora, amene ‘adadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo.’ (Yuda 5-7; Genesis 6:2-4; 19:4-25; Numeri 14:35) Pazochitika zonsezo, Yehova anapereka chiweruzo choŵaŵa kwa ochimwawo.
5. Kodi Yuda akugwira mawu mneneri wakale uti, ndipo kodi ulosi umenewo unasonyeza motani kuti udzakwaniritsidwadi?
5 Kenako, Yuda akutchula chiweruzo chachikulu kwambiri. Akugwira mawu ulosi wa Enoke—nkhani yopezeka pano pokha m’Malemba onse ouziridwa.a (Yuda 14, 15) Enoke analosera nthaŵi pamene Yehova adzaweruza anthu onse osaopa Mulungu pamodzi ndi zochita zawo zopanda umulungu. Komano, Enoke analankhula monga kuti zinachitika kale, popeza kuti ziweruzo za Mulungu zinali zotsimikizirika zedi monga kuti zinachitika kale. Anthu ayenera kuti ananyoza Enoke ndipo kenako Nowa, koma onyoza onse ameneŵo anafa ndi madzi pa Chigumula cha dziko lonse.
6. (a) Kodi Akristu a m’nthaŵi ya Yuda anafunikira kukumbutsidwa za chiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulabadira zikumbutso za Yuda?
6 Kodi Yuda analemberanji za ziŵeruzo za Mulungu zimenezi? Chifukwa anadziŵa kuti ena amene anali m’mipingo yachikristu m’tsiku lake anali kuchita machimo onyansa ndiponso oyenerera chilango monga amene anachititsa ziŵeruzo zakale zimenezo. Choncho, Yuda analemba kuti mipingo iyenera kukumbutsidwa za choonadi china choyambirira chauzimu. (Yuda 5) Iwo mwachionekere anaiŵala kuti Yehova Mulungu anali kuona zochita zawo. Inde, iye amaona pamene atumiki ake akuswa malamulo ake mwadala, kudzidetsa iwo okha ndi kudetsa ena. (Miyambo 15:3) Zochita zimenezi zimampweteketsa mtima kwabasi. (Genesis 6:6; Salmo 78:40) Nkoopsa kuona kuti anthu wambafe tingakhudze mtima wa Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse. Masiku onse amationa, ndipo pamene tichita zonse zimene tingathe kuti titsatire mapazi a Mwana wake, Yesu Kristu, ndiye kuti khalidwe lathu limasangalatsa mtima wake. Choncho, tiyeni tisakane konse zikumbutso monga zimene Yuda akupereka koma tizilabadire.—Miyambo 27:11; 1 Petro 2:21.
7. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kuti awo amene amachita machimo aakulu apemphe thandizo mwamsanga? (b) Kodi ife tonse tingalipeŵe motani khalidwe loipa?
7 Yehova samangoona chabe komanso amachitapo kanthu. Pokhala Mulungu wachilungamo, iye amalanga ochimwa—panthaŵi yake. (1 Timoteo 5:24) Awo amene amaganiza kuti ziweruzo zake zangokhala mbiri yakale ndi kuti iye sasamala za zoipa zimene iwo akuchita akungodzinyenga. Nkofunika zedi kuti onse lerolino amene amachita khalidwe loipa apemphe thandizo mwamsanga kwa akulu achikristu! (Yakobo 5:14, 15) Tonsefe tikudziŵa bwino kuopsa kwa ngozi ya khalidwe loipa m’nkhondo yathu yauzimu. Chaka chilichonse pamakhala ophedwa—anthu amene amachotsedwa pakati pathu, ambiri a iwo chifukwa chobwerezabwereza khalidwe loipa. Tiyenera kutsimikizadi mtima kukana ziyeso zimene zimafuna kutiloŵetsa mumkhalidwe umenewo.—Yerekezerani ndi Mateyu 26:41.
Lemekezani Ulamuliro Woikidwa ndi Mulungu
8. Kodi “maulemerero” otchulidwa pa Yuda 8 anali ndani?
8 Vuto lina limene Yuda akutchula ndilo la kusalemekeza ulamuliro woikidwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, m’vesi 8 iye akuimba mlandu anthu oipa amodzimodziwo kuti ‘achitira mwano maulemerero.’ Kodi “maulemerero” amenewo anali ndani? Anali anthu opanda ungwiro, koma anali ndi maudindo amene mzimu woyera wa Yehova unawapatsa. Mwachitsanzo, mipingo inali ndi akulu, amene anali ndi udindo woŵeta gulu la Mulungu. (1 Petro 5:2) Kunalinso oyang’anira oyendayenda, monga mtumwi Paulo. Ndiponso bungwe la akulu ku Yerusalemu linali bungwe lolamulira, limene linali kupanga zosankha zokhudza mipingo yonse yachikristu. (Machitidwe 15:6) Yuda anada nkhaŵa kwambiri kuti ena m’mipingomo anali kuchitira mwano, ngakhale kutukwana anthu ameneŵa.
9. Kodi Yuda akutchula zitsanzo ziti zokhudza kusalemekeza ulamuliro?
9 Potsutsa zonena zopanda ulemu zimenezo, m’vesi 11, Yuda akutchula zitsanzo zinanso zitatu monga zokumbutsa: Kaini, Balamu, ndi Kora. Kaini ananyalanyaza uphungu wachikondi wa Yehova natsata njira yake ya udani wambanda modzifunira. (Genesis 4:4-8) Balamu analandira machenjezo obwerezabwereza amene mosakayika konse anachokera kumagwero osakhala a munthu—ngakhale bulu wake weniweniyo analankhula naye! Koma Balamu mwadyera anapitirizabe kuchitira anthu a Mulungu chiwembu. (Numeri 22:28, 32-34; Deuteronomo 23:5) Kora anali ndi udindo wake, koma sanakhutire nawo. Anasonkhezera anthu kuti apandukire munthu wofatsa woposa anthu onse padziko lapansi, Mose.—Numeri 12:3; 16:1-3, 32.
10. Kodi ena lerolino angagwere motani mumsampha wa ‘kuchitira mwano maulemerero,’ ndipo nchifukwa ninji tiyenera kupeŵa kulankhula zinthu zoterozo?
10 Zitsanzo zimenezi zikutiphunzitsa momvekadi kuti tiyenera kumvera uphungu ndi kulemekeza awo amene Yehova akuwagwiritsira ntchito m’maudindo! (Ahebri 13:17) Kuwapeza zolakwa akulu oikidwa nkwapafupi kwambiri, popeza kuti iwonso ngopanda ungwiro monga momwe tonsefe tilili opanda ungwiro. Koma ngati tingosumika maganizo athu pa zolakwa zawo ndi kuwanyozera, kodi sitingakhale ‘tikuchitira mwano maulemerero’? M’vesi 10, Yuda akutchula za awo amene ‘achitira mwano zimene sazidziŵa.’ Nthaŵi zina, ena amatsutsa chigamulo chimene bungwe la akulu lapanga kapena chimene komiti ya chiweruzo yapanga. Komabe, iwo samadziŵa mfundo zonse zimene akulu anapenda kuti apange chigamulo chimenecho. Choncho, amalankhuliranji zamwano pazinthu zimene sakuzidziŵa? (Miyambo 18:13) Awo amene amalimbikira kulankhula zinthu zoipa zimenezo angachititse magaŵano mumpingo ndipo nthaŵi zina tingawayerekezere ndi “miyala yaikulu [yoopsa] yobisika pansi pa madzi” pamisonkhano ya okhulupirira anzawo. (Yuda 12, 16, 19, NW) Sitikufuna konse kuika ena pangozi yauzimu. M’malo mwake, aliyense wa ife atsimikize mtima kuyamikira amuna amaudindo ameneŵa kaamba ka ntchito yawo ndi kudzipereka kwawo ku gulu la Mulungu.—1 Timoteo 5:17.
11. Kodi nchifukwa ninji Mikayeli anapeŵa kupereka chiweruzo kwa Satana?
11 Yuda akutchula chitsanzo cha munthu amene analemekeza ulamuliro woikidwa. Analemba kuti: “Mikayeli mkulu wa angelo, pakuchita makani ndi Mdyerekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumtchulira chifukwa chomchitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.” (Yuda 9) Nkhani yochititsa chidwi imeneyi, yopezeka m’buku la Yuda mokha m’Malemba ouziridwa, imatiphunzitsa maphunziro aŵiri aakulu. Choyamba, imatiphunzitsa kusiyira Yehova chiweruzo. Satana mwachionekere anafuna kugwiritsira ntchito thupi la munthu wokhulupirikayo Mose molakwa kuti asonkhezere kulambira konyenga. Ngwoipa chotani nanga! Komabe, Mikayeli modzichepetsa anapeŵa kupereka chiweruzo, popeza kuti Yehova yekha ndiye anali ndi mphamvu imeneyo. Koposa kotani nanga kuti ifeyo tizipeŵa kuweruza anthu okhulupirika amene akuyesa kutumikira Yehova.
12. Kodi amene ali ndi maudindo mumpingo wachikristu angaphunzireponji pachitsanzo cha Mikayeli?
12 Chachiŵiri, awo amene ali ndi ulamuliro winawake mumpingo angatengeponso phunziro kwa Mikayeli. Ndi iko komwe, ngakhale kuti Mikayeli anali “mkulu wa angelo,” iye sanagwiritsire ntchito udindo wake waukuluwo molakwa, ngakhale ataputidwa. Akulu okhulupirika amatsatira chitsanzo chimenecho mosamalitsa, akumadziŵa kuti kugwiritsira ntchito ulamuliro wawo molakwa sikumapereka ulemu ku uchifumu wa Yehova. Kalata ya Yuda inatchula zambiri ponena za anthu amene anali ndi udindo m’mipingo koma amene anagwiritsira ntchito mphamvu yawo molakwa. Mwachitsanzo, m’mavesi 12 mpaka 14, Yuda analemba motsutsa zedi “[abusa NW] akudziŵeta okha opanda mantha.” (Yerekezerani ndi Ezekieli 34:7-10.) M’mawu ena, cholinga chawo choyamba chinali cha kudzipindulitsa iwo okha, osati kupindulitsa gulu la Yehova. Akulu lerolino angaphunzirepo zambiri pa zitsanzo zoipa zimenezo. Ndithudi, mawu a Yuda pano akupereka chithunzi choonekera bwino cha zimene sitiyenera kukhala. Tikakhala adyera, sitingakhale asilikali a Kristu; timatanganitsidwa kwambiri ndi kumenyera nkhondo zinthu zaumwini. M’malo mwake, tiyeni tonse titsatire mawu a Yesu akuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
“Mudzisunge Nokha m’Chikondi cha Mulungu”
13. Kodi nchifukwa ninji tonsefe tiyenera kuyesetsadi kukhalabe m’chikondi cha Mulungu?
13 Chakumapeto kwa kalata yake, Yuda akupereka uphungu wachikondiwu: “Mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu.” (Yuda 21) Palibe chimene chidzatithandiza kumenya nkhondo ya Akristuyi kuposa chinthu chimenechi, kukhalabe okondedwa ndi Yehova Mulungu. Ndi iko komwe, chikondi ndicho mkhalidwe waukulu wa Yehova. (1 Yohane 4:8) Paulo analembera Akristu a ku Roma kuti: “Ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:38, 39) Komano, kodi tingakhalebe motani m’chikondi chimenecho? Nazi zinthu zitatu zimene tingachite, malinga nkunena kwa Yuda.
14, 15. (a) Kodi kudzimangirira tokha ‘pachikhulupiriro chathu choyeretsetsa’ kumatanthauzanji? (b) Kodi tingazipende motani zovala zathu zankhondo zauzimu?
14 Choyamba, Yuda akutiuza kupitirizabe kudzimangirira tokha pa ‘chikhulupiriro choyeretsetsa.’ (Yuda 20) Monga momwe tinaonera m’nkhani yoyambayo, imeneyi ndi ntchito yosalekeza. Tili ngati nyumba zofuna kulimbitsidwa mowonjezerekawonjezereka kuti zisagwe ndi mkuntho womakulakulabe. (Yerekezerani ndi Mateyu 7:24, 25.) Choncho tisadzidalire mopambanitsa. M’malo mwake, tiyeni tione pamene tingadzimangirire pamaziko a chikhulupiriro chathu, kukhala olimba kwambiri, asilikali okhulupirika kwambiri a Kristu. Mwachitsanzo, tingapende mbali za zovala zankhondo zauzimu zofotokozedwa pa Aefeso 6:11-18.
15 Kodi zovala zathu zankhondo zauzimu nzotani? Kodi “chikopa [chathu] cha chikhulupiriro” ncholimba mokwanira? Tikamakumbukira zaka zapitazi, kodi tikuona zizindikiro za kufooka, monga kuphonyaphonya misonkhano, kusoŵa changu cha utumiki, kapena kusoŵa changu cha phunziro laumwini? Zizindikiro zimenezo nzoopsa! Tiyenera kuchitapo kanthu tsopano kuti tidzimangirire ndi kudzilimbitsa m’choonadi.—1 Timoteo 4:15; 2 Timoteo 4:2; Ahebri 10:24, 25.
16. Kodi kupemphera mu mzimu woyera kumatanthauzanji, ndipo ndi chinthu chiti chimene tiyenera kumpempha Yehova nthaŵi zonse?
16 Njira yachiŵiri yokhalirabe m’chikondi cha Mulungu ndiyo kupitirizabe “kupemphera mu Mzimu Woyera.” (Yuda 20) Zimenezo zikutanthauza kupemphera mosonkhezeredwa ndi mzimu wa Yehova ndiponso mogwirizana ndi Mawu ake ouziridwa ndi mzimu. Pemphero lili njira yofunika kwambiri yoyandikirira kwa Yehova mwaumwini ndiponso yosonyezera kudzipereka kwathu. Tisanyalanyaze konse mwaŵi waukulu umenewu! Ndipo pamene tipemphera, tingapemphe—tingonena kuti, nthaŵi zonse tizipempha—mzimu woyera. (Luka 11:13) Ndiyo mphamvu yaikulu koposa imene tingapeze. Pokhala ndi thandizo limenelo, tingakhalebe m’chikondi cha Mulungu ndi kupirira monga asilikali a Kristu.
17. (a) Kodi nchifukwa ninji chitsanzo cha Yuda pankhani ya chifundo chili chothandiza kwambiri? (b) Kodi aliyense wa ife angapitirize motani kusonyeza chifundo?
17 Chachitatu, Yuda akutilimbikitsa kupitiriza kusonyeza chifundo. (Yuda 22) Chitsanzo chake pankhaniyi nchothandiza kwambiri. Ndipotu iye anali ndi nkhaŵa yoyenera chifukwa cha zoipa, khalidwe loipa, ndi mpatuko umene unali kuloŵa mumpingo wachikristu. Komabe, sanataye mtima, kuganiza kuti mwina nthaŵizo zinali zoipa kwambiri moti sangasonyeze mkhalidwe “wabwino” umenewo monga chifundo. Ayi, iye analimbikitsa abale ake kupitirizabe kusonyeza chifundo monga momwe angathere, kukambitsirana mwachifundo ndi amene akukayikira ngakhalenso “kuwakwatula kumoto” awo amene anali pafupi kuloŵa m’tchimo. (Yuda 23; Agalatiya 6:1) Ndi uphungu wabwino chotani nanga kwa akulu a m’nthaŵi zovutazi! Iwonso amafunitsitsa kusonyeza chifundo ngati nkoyenera, pamenenso amakhala olimba ngati kutero nkofunika. Tonsefe tiyeneranso kusonyezana chifundo. Mwachitsanzo, m’malo mosunga chinthu kukhosi pamilandu yaing’ono, tiyenera kukhala okhululukira mwaufulu.—Akolose 3:13.
18. Kodi tingakhale motani otsimikiza za chilakiko pankhondo yathu yauzimu?
18 Nkhondo imene tikumenyayi siyaing’ono ayi. Monga momwe Yuda akunenera, ili “nkhondo yamphamvu.” (Yuda 3, NW) Adani athu ngamphamvu. Osati Satana yekha koma dziko lake loipa ndi zofooka za ife eni zonse zikumenyana nafe nkhondo. Komabe, tiyenera kukhala otsimikiza kotheratu za chilakiko! Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tili kumbali ya Yehova. Yuda akumaliza kalata yake ndi chikumbutso chakuti Yehova ngwoyenereradi “ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthaŵi, ndi tsopano, ndi kufikira nthaŵi zonse. Amen.” (Yuda 25) Kodi limeneli si lingaliro lodzutsa chidwi? Choncho, kodi pangakhalenso kukayikira kulikonse kuti Mulungu mmodzimodziyu “akhoza kukudikirani, [kuti] mungakhumudwe”? (Yuda 24) Kutalitali! Aliyense wa ife akhale wotsimikiza mtima kukana khalidwe loipa, kulemekeza ulamuliro woikidwa ndi Mulungu, ndiponso kudzisunga iyemwini m’chikondi cha Mulungu. Mwakutero, tidzakhala ndi chipambano chaulemerero pamodzi.
[Mawu a M’munsi]
a Ofufuza ena amanena kuti Yuda anali kugwira mawu buku lopanda umboni lotchedwa kuti Buku la Enoke. Komabe, R. C. H. Lenski akuti: “Tikufunsa kuti: ‘Kodi buku lankhani zosiyanasiyana limeneli, Buku la Enoke, linachokera kuti?’ Buku limeneli linangosonkhanitsa nkhani zosiyanasiyana, ndipo palibe amene angatsimikizire za madeti a zigawo zake zosiyanasiyana . . . ; palibe amene ali ndi umboni wakuti mawu ake ena sanatengedwe kwa Yuda iye mwini.”
Mafunso Obwereza
◻ Kodi kalata ya Yuda ikutiphunzitsa motani kukana khalidwe loipa?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kulemekeza ulamuliro woikidwa ndi Mulungu?
◻ Kodi nchifukwa ninji kugwiritsira ntchito molakwa ulamuliro wa mumpingo kuli kulakwa kwambiri?
◻ Kodi tingachitenji kuti tikhalebe m’chikondi cha Mulungu?
[Chithunzi patsamba 15]
Mosiyana ndi asilikali a Roma, Akristu ali pankhondo yauzimu
[Chithunzi patsamba 18]
Abusa achikristu samatumikira chifukwa chadyera, koma chifukwa cha chikondi