Khalanibe ndi “Chiyembekezo cha Chipulumutso” Choŵala!
‘Valani . . . chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso.’—1 ATESALONIKA 5:8.
1. Kodi “chiyembekezo cha chipulumutso” chimathandiza motani kupirira?
CHIYEMBEKEZO cha kupulumutsidwa chingam’thandize munthu kupirirabe ngakhale m’mikhalidwe yosautsa kwambiri. Wopulumuka m’chombo chosweka amene angamayandame paphaka angapirire kwanthaŵi yaitali ngati akudziŵa kuti odzam’pulumutsa ali pafupi kufika. Mofananamo, kwa zaka mazana ambiri, kuyembekeza “chipulumutso cha Yehova” kwalimbikitsa amuna ndi akazi achikhulupiriro m’nthaŵi za nsautso, ndipo chiyembekezo chimenechi sichinawagwiritsepo fuŵa lamoto. (Eksodo 14:13; Salmo 3:8; Aroma 5:5; 9:33) Mtumwi Paulo anayerekezera “chiyembekezo cha chipulumutso” chimenechi ndi “chisoti” pa zovala zankhondo za m’Kristu. (1 Atesalonika 5:8; Aefeso 6:17) Inde, chidaliro chathu mwa Mulungu chakuti adzatipulumutsa chimateteza luntha lathu la kulingalira, ndi kutithandiza kukhalabe ndi chiyembekezo mosasamala kanthu za mavuto, chitsutso, ndi mayesero.
2. Kodi “chiyembekezo cha chipulumutso” n’chofunika kwambiri m’njira ziti pa kulambira koona?
2 “Anthu achikunja, [dziko lozinga Akristu a m’zaka za zana loyamba] analibe chiyembekezo chilichonse cha m’tsogolo,” ikutero The International Standard Bible Encyclopedia. (Aefeso 2:12; 1 Atesalonika 4:13) Komabe, “chiyembekezo cha chipulumutso” n’chofunika kwambiri pa kulambira koona. Motani? Choyamba, chipulumutso cha atumiki a Yehova n’chogwirizana ndi dzina lakelo. Wamasalmo Asafu anapemphera kuti: “Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni.” (Salmo 79:9; Ezekieli 20:9) Komanso, kukhala ndi chidaliro pa madalitso olonjezedwa a Yehova n’kofunika kuti tikhale naye pa ubwenzi wabwino. Paulo anafotokoza motere: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Ndiyeno Paulo anapitiriza kufotokoza kuti cholinga chachikulu chomwe Yesu anabwerera kudziko lapansi chinali kudzapulumutsa ochimwa olapa. Iye anati: “Mawuŵa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ochimwa.” (1 Timoteo 1:15) Ndipo mtumwi Petro ananena za chipulumutso kuti ndicho ‘chitsiriziro cha [kapena kuti, zotsatira za] chikhulupiriro chathu.’ (1 Petro 1:9) Mwachionekere, kuyembekezera chipulumutso n’koyenera. Koma kodi chipulumutsocho n’chiyani kwenikweni? Ndipo chofunika n’chiyani kuti munthu achipeze?
Kodi Chipulumutso N’chiyani?
3. Kodi atumiki a Yehova a m’nthaŵi zakale analandira chipulumutso chotani?
3 M’Malemba Achihebri, “chipulumutso” kaŵirikaŵiri chimatanthauza kupulumutsa kapena kulanditsa ku chitsenderezo kapena ku imfa yamwadzidzidzi, yomvetsa chisoni kwambiri. Mwachitsanzo, potchula Yehova kuti “Mpulumutsi,” Davide anati: “Mulungu wa thanthwe langa, . . . populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa. Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera tim’tamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.” (2 Samueli 22:2-4) Davide anadziŵa kuti Yehova amamvetsera pamene atumiki Ake okhulupirika am’fuulira iye kuti awathandize.—Salmo 31:22, 23; 145:19.
4. Kodi atumiki a Yehova omwe analiko Chikristu chisanakhaleko anali ndi chiyembekezo chotani cha m’tsogolo?
4 Atumiki a Yehova omwe analiko Chikristu chisanakhaleko analinso ndi chiyembekezo cha moyo wam’tsogolo. (Yobu 14:13-15; Yesaya 25:8; Danieli 12:13) Kwenikweni, ochuluka mwa malonjezo a chipulumutso opezeka m’Malemba Achihebri anali kulosera chipulumutso chachikulu—chipulumutso chotsogolera ku moyo wosatha. (Yesaya 49:6, 8; Machitidwe 13:47; 2 Akorinto 6:2) M’masiku a Yesu, Ayuda ochuluka anali kuyembekezera moyo wosatha, komano iwo anakana kulandira Yesu monga kiyi yokwaniritsira ziyembekezo zawozo. Yesu anauza atsogoleri achipembedzo am’nthaŵi yake kuti: “Musanthula m’Malemba, popeza muyesa kuti momwemo muli nawo moyo wosatha; ndipo akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo.”—Yohane 5:39.
5. Kodi chipulumutso kwenikweni chimatanthauzanji?
5 Kupyolera mwa Yesu, Mulungu anavumbula tanthauzo lonse la chipulumutso. Ilo limaphatikiza kumasulidwa kuchoka ku ulamuliro wa uchimo, kuchoka m’nsinga za chipembedzo chonyenga, kuchoka m’dziko lolamulidwa ndi Satana, kuchoka ku kuopa munthu, ngakhalenso kuchoka m’mantha a imfa. (Yohane 17:16; Aroma 8:2; Akolose 1:13; Chivumbulutso 18:2, 4) Pambuyo pake, kwa atumiki okhulupirika a Mulungu, kupulumutsidwa ndi Mulungu sikunangotanthauza kuwomboledwa kokha ku chitsenderezo ndi kupsinjika maganizo ayi, koma kunatanthauzanso mwayi wokhala ndi moyo wosatha. (Yohane 6:40; 17:3) Yesu anaphunzitsa kuti kwa “kagulu kankhosa,” chipulumutso chikutanthauza kuukitsidwira kwawo ku moyo wakumwamba kukalamulira limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake. (Luka 12:32) Kwa mtundu wonse wa anthu, chipulumutso chikutanthauza kubwezeretsedwa kwa moyo wangwiro ndi ubwenzi ndi Mulungu zomwe Adamu ndi Hava anali kusangalala nazo m’munda wa Edene asanachimwe. (Machitidwe 3:21; Aefeso 1:10) Kukhala ndi moyo wosatha m’mikhalidwe ya paradaiso yoteroyo ndicho chinali chifuno choyambirira cha Mulungu ku mtundu wa anthu. (Genesis 1:28; Marko 10:30) Komano, kodi kubwezeretsa mikhalidwe imeneyo n’kotheka motani?
Maziko a Chipulumutso—Dipo
6, 7. Ndi mbali yotani imene Yesu anachita pa chipulumutso chathu?
6 Chipulumutso chosatha n’chotheka kupyolera m‘nsembe ya dipo ya Kristu yokha basi. Chifukwa chiyani? Baibulo limafotokoza bwino kuti Adamu atachimwa, ‘anadzigulitsa’ yekha limodzi ndi mbadwa zake zonse zam’tsogolo, kuphatikiza ifeyo, ku uchimo—potero anachititsa dipo kukhala loyenera ngati mtundu wa anthu ukanati ukhale ndi chiyembekezo china chilichonse chodalirika. (Aroma 5:14, 15; 7:14) Mfundo yakuti Mulungu adzakonzera mtundu wa anthu dipo inachitiridwa chithunzi ndi nsembe zanyama zoperekedwa m’nthaŵi ya Chilamulo cha Mose. (Ahebri 10:1-10; 1 Yohane 2:2) Nsembe ya Yesu ndiyo inakwaniritsa zithunzi zaulosi zimenezo. Yesu asanabadwe, mngelo wa Yehova analengeza kuti: “Iyeyo adzapulumutsa anthu ake kumachimo awo.”—Mateyu 1:21; Ahebri 2:10.
7 Yesu anabadwa mozizwitsa kwa namwaliyo Mariya, ndipo monga Mwana wa Mulungu, sanalandira imfa kuchokera kwa Adamu. Popeza kuti sanalandira imfa, ndi kuti moyo wake unali wangwiro ndi wokhulupirika, n’zomwe zinapatsa moyo wakewo mtengo woyenerera kuti akhoze kuwombola mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa. (Yohane 8:36; 1 Akorinto 15:22) Mosiyana ndi anthu ena onse, Yesu sanali woyenerera kufa chifukwa cha uchimo. Iyeyu mofunitsitsa anadza kudziko lapansi “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Popeza kuti anachitadi zimenezo, Yesu yemwe tsopano n’ngwoukitsidwa ndi wokwezeka pampando wachifumu ali ndi mphamvu zonse zopereka chipulumutso kwa onse ochita zofuna za Mulungu.—Chivumbulutso 12:10.
Kodi Chofunika N’chiyani Kuti Tilandire Chipulumutso?
8, 9. (a) Kodi Yesu anayankha motani funso la wolamulira wachinyamata wachuma lokhudza chipulumutso? (b) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito motani mpata umenewu kuphunzitsa ophunzira ake?
8 Panthaŵi inayake, wolamulira wina wachinyamata wachuma m’Israyeli anafunsa Yesu kuti: “Ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” (Marko 10:17) Funso lakelo liyenera kuti linasonyeza malingaliro achiyuda omwe anali ofala kwambiri m’nthaŵi yake. Malingalirowo anali akuti Mulungu amafuna ntchito zabwino zamtundu winawake ndi kuti mwa kuchita zochuluka mwa ntchitozo, m’pamene munthu angalandire chipulumutso kuchokera kwa Mulungu. Komabe kudzipereka kwamtundu umenewu kungayambe ndi zolinga zadyera. Ntchito zoterozo zinalephera kupereka chiyembekezo chodalirika cha chipulumutso, chifukwa chakuti palibe munthu wopanda ungwiro amene kwenikweni angafikire miyezo ya Mulungu.
9 Poyankha funso la mwamuna uja, mwachidule Yesu anam’kumbutsa kuti ayenera kumvera malamulo a Mulungu. Wolamulira wachinyamatayo mwamsanga anam’tsimikizira Yesu kuti wakhala akusunga malamulowa kuyambira ubwana wake. Yankho lakelo linasonkhezera chikondi cha Yesu pa iye. Yesu ananena naye: “Chinthu chimodzi chikusoŵa: Pita, gulitsa zonse uli nazo, nuzipereke kwa anthu aumphaŵi, ndipo chuma udzakhala nacho m’mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.” Koma mnyamatayo anachoka ali wachisoni “pakuti anali mwini chuma chambiri.” Zitatha izi Yesu ananena motsindika kwa ophunzira ake kuti kumamatira kotheratu ku chuma chadziko lino kumatseka njira ya kuchipulumutso. Iye anawonjezera kuti palibe munthu adzalandira chipulumutso m’mphamvu za iye yekha. Koma Yesu anapitirizabe kuwatsimikizira kuti: “Sikutheka ndi anthu, koma kutheka ndi Mulungu; pakuti zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.” (Marko 10:18-27; Luka 18:18-23) Kodi chipulumutso n’chotheka motani?
10. Kodi tiyenera kukwaniritsa ziyeneretso zotani kuti tikapeze chipulumutso?
10 Chipulumutso ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, koma siibwera mwachisawawa. (Aroma 6:23) Pali ziyeneretso zinazake zikuluzikulu zomwe munthu aliyense afunikira kuzikwaniritsa kuti ayenerere kulandira mphatso imeneyo. Yesu anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Kenako mtumwi Yohane anawonjezera kuti: “Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo.” (Yohane 3:16, 36) Ndithudi, Mulungu amafuna kuti munthu aliyense amene akuyembekezera kulandira chipulumutso chosatha akhale wokhulupirira ndi womvera. Aliyense payekha ayenera kusankha kuvomereza dipo ndi kutsatira m’mapazi a Yesu.
11. Kodi munthu wopanda ungwiro angavomerezedwe motani ndi Yehova?
11 Popeza kuti ndife opanda ungwiro, sindife omvera mwachibadwa ndipo n’kosatheka kuti nthaŵi zonse tikhale omvera. N’chifukwa chaketu Yehova anapereka dipo kuphimba machimo athu. Ngakhale kuti zili choncho, n’kofunika kuti tiyesetse mosalekeza kukhala mogwirizana ndi njira za Mulungu. Monga momwe Yesu anauzira wolamulira wachinyamata wachuma uja, nafenso tifunikira kusunga malamulo a Mulungu. Kuchita zimenezo kumatipanga osati kungokhala chabe ovomerezeka kwa Mulungu komanso kukhala ndi chimwemwe chochuluka, chifukwa chakuti “malamulo ake sali olemetsa;” malamulo ake ‘amalimbikitsa.’ (1 Yohane 5:3; Miyambo 3:1, 8, NW) Komabe, si chapafupi kugwiritsa chiyembekezo cha chipulumutso.
“Mulimbanetu Chifukwa cha Chikhulupiriro”
12. Kodi chiyembekezo cha chipulumutso chingalimbitse motani Mkristu kupeŵa zilakolako za mikhalidwe yoipa?
12 Wophunzira Yuda anafuna kulembera Akristu oyambirirawo za “chipulumutso cha [iwo onse].” Komabe, mikhalidwe yoipa yomwe inali yofala kwambiri m’nthaŵiyo inam’sonkhezera kulangiza abale akewo kuti ‘alimbanetu chifukwa cha chikhulupiriro.’ Inde, kukhala ndi chikhulupiriro, kumamatira ku chikhulupiriro choona chachikristu, ndi kumvera pamene zonse zikuyenda mwa taŵataŵa, sizokwanira kuti munthu akapeze chipulumutso. Kudzipereka kwathu kwa Yehova kuyenera kukhala kwamphamvu zedi kotero kuti kutithandize kupirira mayesero ndi zisonkhezero za mikhalidwe yoipa. Komano, chiwerewere chadzaoneni ndi kusaweruzika kosaneneka, kuchitira mwano aulamuliro, magawano, ndi kukayikakayika zinali kuwononga maganizo ndi khalidwe labwino la mpingo wa m’zaka za zana loyamba. Powathandiza kuthetsa zizoloŵezi zimenezo, Yuda anauza Akristu anzakewo kukumbukira cholinga chawo akumati: “Okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu, ndi kulindira chifundo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.” (Yuda 3, 4, 8, 19-21) Chiyembekezo cha kupeza chipulumutso chikanawalimbitsa pa kuyesetsa kwawo zolimba kukhalabe amakhalidwe oyera.
13. Kodi tingasonyeze motani kuti sitinalandire chisomo cha Mulungu kwachabe?
13 Yehova Mulungu amayembekezera mikhalidwe yopereka zitsanzo zabwino mwa anthu amene iye adzawapatsa chipulumutso. (1 Akorinto 6:9, 10) Komabe kumamatira ku miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino, sikutanthauza kuweruza ena. Si ndife amene tidzagamula chiweruzo chosatha cha munthu mnzathu. M’malo mwake, Mulungu ndiye adzatero, monga momwe Paulo anauzira Agiriki ku Atene kuti: “Anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu”—Yesu Kristu. (Machitidwe 17:31; Yohane 5:22) Ngati tikukhala ndi chikhulupiriro mu dipo la Yesu tilibetu chifukwa chilichonse choopera tsiku la chiweruzo likudzalo. (Ahebri 10:38, 39) Chinthu chofunika ndicho ‘kusalandira chisomo cha Mulungu [kuyanjidwa kwathu ndi iye kudzera m’dipo] kwachabe’ mwa kulola kukodwa m’misampha ya malingaliro ndi makhalidwe oipa. (2 Akorinto 6:1) Kuwonjeza pamenepo, mwa kuthandiza ena kupeza chipulumutso, timasonyeza kuti sitinalandire chisomo cha Mulungu kwachabe. Kodi tingawathandize motani?
Kuuza Ena Chiyembekezo cha Chipulumutso
14, 15. Kodi Yesu anatuma yani kukafalitsa uthenga wabwino wa chipulumutso?
14 Pogwira mawu mneneri Yoweli, Paulo analemba kuti: “Amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.” Ndiyeno anawonjezera kuti: “Ndipo iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanam’khulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” Atalemba mavesi ena angapo, Paulo anatchula mfundo yakuti chikhulupiriro sichibwera mosayembekezera; m’malo mwake, icho “chidza ndi mbiri” yomwe ndi “mawu a Kristu.”—Aroma 10:13, 14, 17; Yoweli 2:32.
15 Kodi ndani yemwe adzapititsa “mawu a Kristu” ku mitundu ya anthu? Yesu wapereka ntchito imeneyo kwa ophunzira ake—awo amene aphunzitsidwa kale “mawu” amenewo. (Mateyu 24:14; 28:19, 20; Yohane 17:20) Pamene titangwanika ndi ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira, ndiye kuti tikuchita zenizenizo zimene mtumwi Paulo analemba, panthaŵi ino akumagwira mawu Yesaya. Iye anati: “Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” Ngakhale ambiri samalandira uthenga wabwino umene timawatengera, mapazi athu ‘n’ngokometsetsa ndithu’ kwa Yehova.—Aroma 10:15; Yesaya 52:7.
16, 17. Kodi ntchito yathu yolalikirayi imakwaniritsa zifuno ziŵiri ziti?
16 Kugwira ntchito imeneyi kumakwaniritsa zifuno ziŵiri zofunika kwambiri. Chifuno choyamba, uthenga wabwino uyenera kulalikidwa kotero kuti dzina la Mulungu likwezeke ndi kuti awo amene akufuna chipulumutso adziŵe komwe angachipeze. Paulo anamvetsa bwino mtundu umenewu wa ntchito. Iye anafotokoza kuti: “Pakuti kotero anatilamulira Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.” Chotero, monga ophunzira a Kristu, aliyense wa ife ayenera kuchitapo gawo lake mwa kutenga uthenga wa chipulumutso ndi kuupereka kwa anthu.—Machitidwe 13:47; Yesaya 49:6.
17 Chifuno chachiŵiri, kulalikira uthenga wabwino kumayala maziko a chiweruzo cholungama cha Mulungu. Ponena za chiweruzo chimenecho, Yesu anati: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pachimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” Ngakhale kuti kuweruza ndi kulekanitsako zidzachitika “pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake,” ntchito yolalikira ikupereka mwayi kwa anthu lerolino wozindikira abale auzimu a Kristu ndi kuti agwire nawo ntchito limodzi powachirikiza komanso kaamba ka chipulumutso chawo chosatha.—Mateyu 25:31-46.
Khalanibe ndi “Chiyembekezo Chokwanira”
18. M’motani momwe tingakhalire ndi “chiyembekezo cha chipulumutso” chathu chidakali choŵala?
18 Kutenga kwathu mbali mokangalika m’ntchito yolalikira kulinso njira yotithandiza kukhalabe ndi chiyembekezo choŵala. Paulo analemba kuti: “Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.” (Ahebri 6:11) Chotero aliyense wa ife, avaletu “chisoti chili chiyembekezo cha chipulumutso,” potero tikumakumbukira kuti “Mulungu sanatiika ife tilawe mkwiyo, komatu kuti tilandire chipulumutso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Atesalonika 5:8, 9) Tikumbukirenso chilimbikitso cha Petro chakuti: “Mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani odziletsa. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa madalitso amene mudzalandire.” (1 Petro 1:13, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chichewa Chamakono) Onse ochita zimenezo adzaona “chiyembekezo cha chipulumutso” chawo chikukwaniritsidwa kotheratu!
19. Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?
19 Padakali pano, kodi nthaŵi yotsala ya dongosolo lino tiyenera kuiona motani? Kodi tingagwiritse ntchito motani nthaŵi imeneyo kuti tipeze chipulumutso chathu ndi cha ena? Tidzakambirana mafunso ameneŵa m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungalongosole?
• N’chifukwa chiyani “chiyembekezo cha chipulumutso” chathu chiyenera chikhalebe choŵala?
• Kodi chipulumutso chimaphatikizapo chiyani?
• Kodi tiyenera kuchitanji kuti tikalandire mphatso ya chipulumutso?
• Kodi ntchito yathu yolalikira imakwaniritsa chiyani mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu?
[Zithunzi patsamba 10]
Chipulumutso chimatanthauza zambiri kuposa kungoomboledwa chabe ku chiwonongeko