Mkazi Wachigololo wa Mbiri Yoipa—Chiwonongeko Chake
“[Lemekezani Ya, anthu inu! “NW”] Chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali owona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsya dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo.”—CHIBVUMBULUTSO 19:1, 2.
1. Ndimotani mmene mkazi wachigololo wamkulu wachitira chigololo ndi “mafumu a dziko,” ndipo ndi kuchiyani kumene ichi chatulukapo?
ZONSE zomwe takhala tikukambitsirana ziri zosamalitsa mokwanira. Ngakhale kuli tero, tiyenera kuwona kuti Chibvumbulutso 17:2 chimalankhulanso ponena za dama la mkazi wachigololo ndi “mafumu a dziko.” Ngakhale kuti wavutika ndi kugwa, iye adakali bwenzi lenileni la dziko, ndipo akuyesera kulamulira atsogoleri a dziko kupeza mapindu ake. (Yakobo 4:4) Chigololo chauzimu chimenechi, chophatikizapo unansi woipa pakati pa Babulo Wamkulu ndi olamulira a ndale zadziko, chatulukapo mu imfa yosayembekezeredwa ya anthu opanda liwongo mamiliyoni makumi angapo! Chinali choipa mokwanira kuti mkazi wachigololo wamkuluyo anaphatikizidwa m’mbali zonse ziŵiri za kumenyana mu Nkhondo ya Dziko ya I. Koma machimo ake m’chigwirizano ndi Nkhondo ya Dziko ya II motsimikizirika “anawunjikizana kufikira m’Mwamba”! (Chibvumbulutso 18:5) Nchifukwa ninji tikunena tero?
2. (a) Ndimotani mmene Franz von Papen anathandizira Adolf Hitler kukhala wolamulira wa Germany, ndipo ndimotani mmene wolamulira wapapitapo wa ku Germany analongosolera kutsanuliridwa kwa chisomo cha upapa kumeneko? (b) M’Chigwirizano cha pakati pa Boma la Nazi ndi Vatican, ndi nsonga ziŵiri zotani zimene zinasungidwa za chinsinsi? (Onani mawu am’munsi.)
2 Chabwino, kutenga chitsanzo chimodzi, ndimotani mmene Adolf Hitler wankhanza anakhalira nduna yaikulu ya boma—ndi wolamulira wotsendereza ufulu—wa Germany? Chinali kupyolera m’kugwirizana kwa ndale zadziko kwa kutsanuliridwa kwa chisomo cha upapa kumene wolamulira wa papitapo wa ku Germany, Kurt von Schleicher, anakulongosola kukhala “mtundu wa wopereka wotsatira ku amene Yudasi Isikariote ali woyera.” Uyu anali Franz von Papen, yemwe anatsogoza Kachitidwe ka Chikatolika ndi atsogoleri mu indastri kutsutsa chikomyunizimu ndi kugwirizanitsa Germany pansi pa Hitler. Monga mbali ya malonda ogulitsa, von Papen anapangidwa wolamulira wachiŵiri. Hitler anatumiza nthumwi zotsogozedwa ndi von Papen ku Roma kukakambitsirana chigwirizano pakati pa Boma la Nazi ndi Vatican. Papa Pius XI ananena kwa nthumwi za ku Germany zimenezo mmene analiri wokondweretsedwa kuti “Boma la Germany tsopano linali patsogolo pake ndi mwamuna yemwe mosagonjera anali wotsutsa Chikomyunizimu,” ndipo pa July 20, 1933, pa mwambo wokometseredwa mu Vatican, Cardinal Pacelli (yemwe posachedwa anafunikira kukhala Papa Pius XII) anasaina chigwirizanocho.a
3. (a) Nchiyani chimene katswiri wa mbiri yakale ananena ponena za Chigwirizano pakati pa Boma la Nazi ndi Vatican? (b) Mkati mwa kukondwerera pa Vatican, ndi ulemu wotani womwe unaperekedwa kwa Franz von Papen? (c) Ndi thayo lotani limene Franz von Papen anachita m’kutengedwa kwa Austria kochitidwa ndi Nazi?
3 Katswiri wa mbiri yakale mmodzi akulemba kuti: “Chigwirizano [ndi Vatican] chinali chilakiko chachikulu kaamba ka Hitler. Icho chinampatsa iye chirikizo loyamba la makhalidwe lomwe iye analandira kuchokera ku dziko lakunja, ndipo ichi kuchokera ku magwero okwezeka kwenikweni.” Mkati mwa madyerero pa Vatican, Pacelli anafunsira von Papen kukometsera upapa wopambana wa Mtanda Waukulu wa Lamulo la Pius.b Winston Churchill, m’bukhu lake The Gathering Storm, lofalitsidwa mu 1948, akunena mmene von Papen mowonjezereka anagwiritsira ntchito “kutchuka kwake monga m’Katolika wabwino” kupeza chichirikizo cha tchalitchi kaamba ka kulandidwa kwa Austria kochitidwa ndi Nazi. Mu 1938, m’kulemekeza tsiku lobadwa la Hitler, Cardinal Innitzer analamula kuti matchalitchi onse a ku Austria akweze mbendera ya swastika, kuliza mabelu awo, ndi kupemphera kaamba ka wolamulira wotsendereza ufulu wa Nazi.
4, 5. (a) Nchifukwa ninji liwongo la mwazi loipitsitsa limakhala pa Vatican? (b) Ndimotani mmene abishopu a Chikatolika a ku Germany anaperekera chirikizo lapoyera kwa Hitler?
4 Chotero liwongo la mwazi loipitsitsa limakhala pa Vatican! Monga mbali yotsogolera ya Babulo Wamkulu, iyo inathandiza mwapadera m’kuika Hitler mu mphamvu ndi kumpatsa iye chirikizo “laumwini.” Vatican inapitirizanso kuvomereza mochenjera ku nkhanza za Hitler. Mkati mwa nthaŵi yaitali ya zaka khumi za upandu wa Nazi, papa wa Chiroma anakhalabe chete pamene mazana a zikwi za asilikali a Chikatolika ankamenyana ndi kufa kaamba ka ulemerero wa ulamuliro wa Nazi ndipo pamene mamiliyoni a osakhala ndi mwaŵi ena ankasungunulidwa m’zipinda za gas za Hitler.
5 Abishopu a Chikatolika a ku Germany anakhozanso kupereka chirikizo lapoyera kwa Hitler. Pa tsiku limodzimodzilo limene Japan, mnzake wa nthaŵi ya nkhondo wa Germany pa nthaŵiyo, inapanga kuwukira kozembera pa Pearl Harbor, The New York Times inanyamula ripoti iri: “Msonkhano wa Abishopu a Chikatolika a ku Germany wochitidwa mu Fulda wayamikira kuyambitsidwa kwapadera kwa ‘pemphero lankhondo’ lomwe lidzafunikira kuŵerengedwa pa chiyambi ndi pamapeto pa mautumiki aumulungu onse. Pempherolo limafunsira Mulungu kudalitsa zida zankhondo za ku Germany ndi chipambano ndi kupereka chitetezero ku miyoyo ndi umoyo wa asilikali onse. Abishopuwo mowonjezereka anachenjeza atsogoleri a chipembedzo a Chikatolika kupitirizabe ndi kukumbukira pa ulaliki wapadera wa pa Sande chifupifupi kamodzi pa mwezi asilikali ankhondo a ku Germany ‘omwe ali pa mtunda, pa nyanja ndi m’mlengalenga.’”
6. Dziko likanapulumutsidwa kuwawa kolulira kotani ndi nkhalwe ngati panalibe chigololo chauzimu pakati pa Vatican ndi Anazi?
6 Ngati panalibe kachitidwe ka chikondi pakati pa Vatican ndi Anazi, dziko likanapulumutsidwa kuwawa kwa kukhala ndi mamiliyoni ochulukira a asilikali ndi anthu wamba akumaphedwa m’nkhondo, kwa mamiliyoni asanu ndi imodzi a Ayuda ophedwa kaamba ka kusakhala a Aryan, ndi—a mtengo wapatali koposa m’maso mwa Yehova—zikwi zingapo za Mboni zake, ponse paŵiri za odzozedwa ndi “nkhosa zina,” zovutika ndi nkhalwe zokulira, pokhala ndi Mboni zambiri zikumafa m’misasa yachibalo ya Nazi.—Yohane 10:10, 16.
Kuyang’ana Kosamalitsa kwa Mkazi Wachigololoyo
7. Ndimotani mmene mtumwi Yohane akulongosolera kawonedwe kake kosamalitsa ka mkazi wachigololo wamkulu?
7 Ndi oyenerera chotani nanga mmene aliri masomphenya omwe motsatira akufutukuka mu ulosi wa Chibvumbulutso! Kutembenukira ku mutu 17, versi 3 kufika ku 5, tikupeza Yohane akunena za mngelo kuti: “Ndipo ananditenga kumka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinawona mkazi alinkukhala pachirombo chofiiritsa, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi. Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golidi, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m’dzanja lake chikho chagolidi chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake, ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, chinsinsi, Babulo Wamkulu, amayi wa achigololo ndi wa zonyansitsa za dziko.”
8. (a) Nchiyani chimene mkazi wachigololo wamkulu akunyamula m’chikho chake cha golidi, mwakutero kudzizindikiritsa iyemwini? (b) Ndimotani mmene Babulo Wamkulu mophiphiritsira ali “wovekedwa mu chofiira ndi chobiriŵira” ndi wokometseredwa ndi “golidi ndi miyala ya mtengo wapatali”?
8 Pano Yohane akuwona Babulo Wamkulu pa malo apafupi. Mkaziyo mowonadi ali wa m’chipululu chimenecho, pakati pa zirombo za kuthengo zomwe zimakhala mmenemo. Mkazi wachigololo wamkulu ameneyu akuzindikiritsidwa momvekera bwino ndi chimene iye akunyamula m’chikho chake, ngakhale kuti monyenga chikuwoneka cha mtengo wapatali kuchokera chakunja. Iye akumwa mbali yomwe iri yodetsedwa kuchokera ku kawonedwe ka Mulungu. Ubwenzi wake ndi dziko, ziphunzitso zake zonyenga, kulolera kwake kwa makhalidwe, kusanganizana kwake ndi mphamvu za ndale zadziko—palibe nchimodzi chonse cha izi chomwe chimalekereredwa ndi Yehova, “woweruza wa dziko lonse lapansi.” (Genesis 18:22-26; Chibvumbulutso 18:21, 24) Eya, ndi mokongola chotani nanga mmene amadzikometsera iyemwini! Ali wotchuka kwambiri kaamba ka zimango zake zazikulu zopempherera ndi kamangidwe kake kocheutsa ndi mazenera a magalasi opakidwa utoto, kukometsera kwa mosonkhanira mwake ndi miyala ya mtengo wapatali ndi nyumba zolambiriramo, akachisi ake olemekezedwa ndi tiakachisi. Chowona ku mafashoni osiyanasiyana oikidwa ndi mkazi wachigololo wamkulu, ansembe ake ndi odzipereka ku chipembedzo mwa lumbiro avekedwa minjiro ya mtengo yofiira, yobiriŵira, ndi saffron.—Chibvumbulutso 17:1.
9. Babulo Wamkulu ali ndi mbiri yakale yaitali yotani ya liwongo la mwazi, ndipo ndimotani mmene Yohane molondola akutsirizira kulongosola kwake kwa iye?
9 Cha mlandu kwambiri, ngakhale ndi tero, chiri liwongo lake la mwazi. Yehova ali ndi mlandu wokhalapo kwa nthaŵi yaitali wofunika kuthetsedwa pa nsonga imeneyo! Mkaziyo wachirikiza olamulira otsendereza ufulu omwe ali ndi ludzu la mwazi a nthaŵi zamakono, ndipo mbiri yake yonyansa imabwerera kumbuyo kupyola mazana, kupyola m’nkhondo za chipembedzo, Kufufuzafufuza, Nkhondo za Chikristu, inde, kufika kumbuyo ku kuphedwera chikhulupiriro kwa ena a atumwi ndi kuphedwa kwa Mwana weniweni wa Mulungu, Ambuye Yesu Kristu, ndi kupitirira. (Machitidwe 3:15; Ahebri 11:36, 37) Wonjezerani ku zonsezi kuphedwa kwa Mboni za Yehova m’zaka za posachedwapa mwa kuwombera mfuti, kupachikidwa, nkhwangwa, makina odulira mitu, lupanga, ndi kuzunzidwa kwa uchinyama m’ndende ndi m’misasa yachibalo. Nchosadabwitsa kuti Yohane akumaliza kulongosola kwake mwa kunena kuti: “Ndipo ndinawona mkazi woledzera ndi mwazi wa oyera mtima, ndi mwazi wa mboni za Yesu”!—Chibvumbulutso 17:6.
‘Chinsinsi cha Mkazi ndi Chirombo’
10. (a) Ndimotani mmene mkazi wachigololo wamkulu wazunzira Mboni za Yehova kupyola kufika ku tsiku lino? (b) Ndi mtundu wotani wa atsogoleri umene atsogoleri achipembedzo a Babulo Wamkulu ali?
10 Yohane “anadabwa ndi kuzizwa kwakukulu” pa chimene anawona. Lerolino, nafenso timadabwa! Mkati mwa ma 1930 ndi ma 1940, mkazi wachigololo wamkulu anagwiritsira ntchito Kachitidwe ka Chikatolika ndi chiŵembu cha ndale zadziko kuzunza ndi kuletsa mboni zokhulupirika za Yehova. Kufikira ku tsiku lino, kumene angachite chisonkhezero chokwanira, Babulo Wamkulu wapitirizabe kulepheretsa, kuletsa, ndi kunenera monama ntchito ya Mboni za Yehova, zomwe zimalalikira chiyembekezo cha ulemerero cha Ufumu wa Mulungu. Mwa kusunga mazana a mamiliyoni a anthu mu ukapolo m’magulu a chipembedzo a mkazi wachigololo wamkulu, atsogoleri ake a chipembedzo amatumikira monga ‘atsogoleri akhungu a anthu akhungu,’ akumawatsogolera kulinga ku mbuna ya chiwonongeko. Nchosatheka, nchosatheka m’pang’ono pomwe kuti mkazi wachigololo wambiri yoipayu anganene ndi mtumwi Paulo kuti: “Ndikuitanani kuchitira umboni . . . kuti ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.”—Mateyu 15:7-9, 14; 23:13; Machitidwe 20:26.
11, 12. Nchiyani chomwe chiri chinsinsi cha “chirombo chofiiritsa” chomwe chikunyamula mkazi wachigololo wa mbiri yoipa, ndipo ndi kuwunikira kotani kumene Mboni za Yehova zinalandira pa chinsinsichi mu 1942?
11 Akumawona kudabwitsidwa kwa Yohane, mngelo anati kwa iye: “Uzizwa chifukwa ninji? Ine ndidzakuwuza iwe chinsinsi cha mkazi, ndi cha chirombo chakumbereka iye, chokhala nayo mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi.” (Chibvumbulutso 17:7) Kodi “chirombo” chimenechi nchiyani? Zoposa zaka 600 kumayambiriro, mneneri Danieli anawona zirombo za masomphenya, ndipo chinalongosoledwa kwa iye kuti izi zinaimira “mafumu,” kapena ulamuliro wa ndale zadziko pano pa dziko lapansi. (Danieli 7:2-8, 17; 8:2-8, 19-22) Yohane pano akuwona m’masomphenya kusanganizana kwa maulamuliro oterowo—“chirombo chofiiritsa.” Ichi ndi Chigwirizano cha Mitundu chopangidwa ndi anthu chimene chinawonekera pa chochitika cha dziko mu 1920 koma chinagwera mu phompho la kusagwira ntchito pamene Nkhondo ya Dziko ya II inawulika mu 1939. Nchiyani, ngakhale ndi tero, chimene chiri “chinsinsi cha mkazi ndi chirombo”?
12 Ndi chitsogozo chaumulungu, Mboni za Yehova zinalandira kuwunikira pa chinsinsi chimenecho mu 1942. Nkhondo ya Dziko ya II pa nthaŵiyo inali kufika pachimake chake, ndipo ambiri anaganiza kuti ikakula kufikira kukhala Armagedo. Koma Yehova anali ndi lingaliro losiyanako! Panali padakali ntchito yambiri kaamba ka Mboni zake kuichita! Pa Msonkhano wawo wa Teokratiki ya Dziko Latsopano wa September 18-20, 1942, ndi mzinda wapakati Cleveland, Ohio, wolumikizidwa ndi lamya ku malo ena 51 mu United States, Nathan H. Knorr, prezidenti wa Watch Tower Society, anapereka nkhani yapoyera pa, “Mtendere—Kodi Ungakhalitse?” Mu iyo iye anabwereramo mu Chibvumbulutso 17:8, chimene chimanena za “chirombo chofiiritsa” kuti “chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m’phompho, ndi kunka kuchitayiko.” Anasonyeza mmene Chigwirizano cha Mitundu “chinaliko” kuchokera mu 1920 kufika mu 1939. Kenaka mkhalidwe wa “kulibe” unafikiridwa chifukwa cha kufa kwa Chigwirizanocho. Koma pambuyo pa Nkhondo ya Dziko ya II, kusanganiza kumeneku kwa mitundu kukatuluka m’phompho. Kodi ulosi wonenedweratuwo wozikidwa pa Baibulo unakwaniritsidwa? Mowonadi unatero! Mu 1945 “chirombo” cha mitundu yonse chinatuluka kuchoka m’phompho lake la kusagwira ntchito monga Mitundu Yogwirizana.
13. Ndimotani mmene Babulo Wamkulu wapitirizira kutsatira njira zake zonga mkazi wachigololo ndi “chirombo” cha UN?
13 Babulo Wamkulu, ngakhale kuti anafooketsedwa ndi kugwa kwake, wapitirizabe kutsatira njira zake za chigololo ndi “chirombo” cha UN. Mwachitsanzo, mu June 1965, nduna zolemekezeka kuchokera ku nthambi zisanu ndi ziŵiri zotsogolera za dziko za chipembedzo, zotchedwa Zachikristu ndi zosakhala Zachikristu, zinanenedwa kuimira theka limodzi la chiŵerengero cha anthu a dziko, omasonkhana mu San Francisco kukondwerera chaka cha kubadwa cha 20 cha UN.c M’chaka chimodzimodzicho, Papa Paul VI analongosola UN kukhala “chiyembekezo chotsirizira cha chimvano ndi mtendere,” ndipo pambuyo pake Papa John Paul II analongosola chiyembekezo chake kuti “Mitundu Yogwirizana idzapitirizabe kukhala bungwe lamphamvu la mtendere ndi chilungamo.” Mu 1986 ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga unatenga chitsogozo m’kuchirikiza Chaka cha UN cha Mtendere wa Mitundu yonse. Koma kodi mtendere wowona ndi chisungiko zinabwera monga yankho ku mapemphero awo a chipembedzo? Kutalitali ndi icho! Mitundu yochulukira, yomwe ndi ziŵalo za UN ikusonyeza kuti iribe chikondi chenicheni kaamba ka mkazi wachigololo wamkulu.
Kugwetsa Mkazi wa Chigololoyo
14. Ndi utumiki wapadera wotani umene “chirombo” cha UN chidzayenera kuchita, ndipo ndimotani mmene ichi chalongosoledwera ndi mngelo wa Mulungu?
14 M’kupita kwa nthaŵi, “chirombo chofiiritsa” chenichenicho chiyenera kupita ku chiwonongeko. Koma ichi chisanachitike, ndipo ngakhale chiwukiro chake chotsirizira cha uchirombo pa anthu a Mulungu chisanakhale, chirombo cha UN chimenecho chiri ndi ntchito yapadera ya kuichita. Yehova akuika ‘malingaliro ake m’mitima ya chirombo ndi nyanga zake zankhondo.’ Ndi chotulukapo chotani? Mngelo wa Mulungu akuyankha kuti: “Ndipo nyanga khumi udaziwona, ndi chirombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsyereza ndi moto.” “Anadzilemekeza iyemwini ndi kukhala m’kudyerera kwake,” (NW) koma tsopano zonsezi zatembenuzidwa. Kusonkhezera kwake zimango zabwino za chipembedzo ndi chuma chake chachikulu sizidzampulumutsa iye. Monga mmene mngelo akulengezera: “Chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi [kusoweka kwa chakudya, NW] ndipo adzapsyerera ndi moto; chifukwa [Yehova, NW] Mulungu woweruza ndiye wolimba.”—Chibvumbulutso 17:16, 17; 18:7, 8.
15. Ndimotani mmene atsamwali a ndale zadziko a mkazi wachigololo, limodzi ndi osonkhezera a malonda akulu, adzachitira ku kunyazitsidwa kwake?
15 Atsamwali ake a ndale zadziko adzadzuma pa kuzimiririka kwake, akumalengeza kuti: “Tsoka, tsoka, mudzi waukuluwo, Babulo, mudzi wolimba! pakuti mu ora limodzi chafika chiweruziro chanu.” Mofananamo, osonkhezera malonda akulu, omwe anapanga mapindu osawona mtima ndi iye, “nadzalira, ndi kuchita chifundo; nadzanena, ‘Tsoka, tsoka, . . . pakuti mu ora limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere.’”—Chibvumbulutso 18:9-17.
16. Ndi kuyankha kotani kumene anthu a Mulungu adzapanga ku chiwonongeko cha mkazi wachigololo wamkulu, ndipo ndimotani mmene Chibvumbulutso chikutsimikizira ichi?
16 Ngakhale kuli tero, ndi kuvomereza kotani kumene anthu ake a Mulungu adzapanga? Zonsezi nzophatikizidwa m’mawu a mngelo: “Kondwera pa iye, m’mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.” Ndi kuponyedwa kwa mwamsanga Babulo Wamkulu adzakhala ataponyedwa pansi, sadzatonzanso poyera dzina la Yehova. Chiwonongeko cha mkazi wachigololo wamkulu chidzaitanira kaamba ka kukondwerera ndi nyimbo za chipambano m’kutamanda Yehova. Monga yoyambirira ya ndandanda ya nyimbo za aleluya, kuvomereza kwa chisangalalo kudzamveka: “[Lemekezani Ya, anthu inu! NW] Chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali owona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsya dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake a mkaziyo.”—Chibvumbulutso 18:20–19:3.
17. Pambuyo pa kuvumbulidwa kwa mkazi wachigololo wamkulu, ndimotani mmene machitidwe a chiweruzo a Mulungu akupitirizira ku mathedwe?
17 Machitidwe a chiweruzo a Mulungu adzachitika mofulumira mpaka kumapeto pamene “Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye,” Kristu Yesu, aponda “moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse” pa Armagedo. Pamenepo adzagwetsa olamulira oipa ndi otsalira ena a gulu la Satana pa dziko lapansi. Mbalame zakudya zinthu zakufa zidzadya mitembo yawo. (Chibvumbulutso 16:14, 16; 19:11-21) Ndi achimwemwe chotani nanga mmene tiyenera kukhalira kuti nthaŵi yoikidwiratu ya Mulungu iri pafupi kaamba ka kuchotsapo pa dziko lathu lapansi lokongola chinthu chirichonse chimene chiri chosayera, chonyansa, ndi choipitsa!
18. Nchiyani chomwe chiri kufika pachimake kokulira kwa bukhu la Chibvumbulutso?
18 Kodi chimenecho ndicho chimake cha bukhu la Chibvumbulutso? Ayi, sichinafike! Popeza kuti ndi kumalizidwa kwa chiwukiriro cha a 144,000 kukwera kumwamba, ukwati wa Mwanawankhosa uchitidwa. “Mkwatibwi” wake, wokometseredwa kaamba ka mwamuna wake, ali wokhazikitsidwa “m’miyamba yatsopano,” ndipo kuchkera kumeneko atsika, mophiphiritsira, monga mthandizi wa Mkwati wake m’kuchita chifuniro cha Yehova ‘kupanga zinthu zonse zatsopano.’ Kukongla kwauzimu kwa mkwatibwiyo kuli kuja kwa mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, umene Yehova Mulungu Wamphamvuyonse awunikira ndi ulemerero wake, ndipo Mwanawankhosa ali nyali yake. (Chibvumbulutso 21:1-5, 9-11, 23) Chotero pano Chibvumbulutso chikufikira pachimake chachikulu, ndi dzina la Yehova litayeretsedwa ndipo Mwanawankhosa, Kristu Yesu, limodzinso ndi mkwatibwi wake, Yerusalemu Watsopano, akubwera kudalitsa mtundu wa anthu omvera ndi moyo wosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi.
19. (a) Pambali pa kutuluka m’Babulo Wamkulu, nchiyani chinanso chomwe chiri chofunika ku chipulumbutso? (b) Ndi chiitano chofulumira chotani chomwe chidakali chotseguka, ndipo nchiyani chomwe chiyenera kukhala chivomerezo chathu?
19 Kodi mwagalamuka ku umthira kuŵiri wa chipembedzo chonyenga ndi kutuluka m’Babulo Wamkulu? Ndipo kodi mwatenga sitepi lotsatira la kubwera kwa Yehova Mulungu, kupyolera mwa Kristu Yesu, m’kudzipereka kwa mtima wonse kotsogolera ku ubatizo? Ichinso chiri chofunika kwambiri ku chipulumutso! Pamene nthaŵi yoikidwiratu kaamba ka kupereka chiweruzo chotsirizira cha Yehova iyandikira, chiitano chimvekera ndi kufulumira kwa mwamsanga: “Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, ‘Idzani!’” Lolani kuti onse omwe amalabadira chiitano chimenecho apereke miyoyo yawo kwa Yehova ndi kukhala achangu m’kunena kuti “Idzani!” kwa enanso. Inde, “wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chibvumbulutso 22:17) Chiitano chidakali chotsegukabe. Mudzakhala achimwemwe ndithudi ngati mutenga kaimidwe kanu ndi kusungirira kaimidwe kameneko pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu ndi Mwanawankhosa monga mmodzi wa anthu odzipereka a Yehova, obatizidwa. Nthaŵi yoikidwiratu iri pafupi kwambiri kuposa mmene mungaganizire! Inde, chimake chokulira cha Chibvumbulutso chiri pafupi!
Monga chotsirizira ku Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu uno, wotsogoza ayenera kuitana kaamba ka kuŵerengedwa kwa Chigamulo chotsatirachi ndi kubwerera mu icho ndi thandizo la mafunso omwe aperekedwa. Ichindi Chigamulo chomwe chinaperekedwa kuzungulira dziko lonse pa Msonkhano Wachigawo wa “Chilungamo Chaumulungu” wa Mboni za Yehova mu 1988, pamapeto pa nkhani yakuti “ ‘Mkazi Wachigololo’ wa Mbiri Yoipa—Kugwa Kwake ndi Chiwonongeko.”
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka zifukwa zokziwikiratu, nsonga ziŵiri za Chigwirizanocho zinasungidwa mwachinsinsi pa nthaŵiyo, izi zomachita ndi chimvano chopita patsogolo motsutsana ndi Soviet Union ndi ntchito za ansembe a Chikatolika olembedwa ntchito m’gulu lankhondo la Hitler. Kulembedwa koteroko kunali kuswa Pangano la pa Versailles (1919) ku limene Germany inali yomamatirabe; chidziŵitso chapoyera cha nsonga zimenezi chikanakhoza kusokoneza osaina a pa Versailles ena.
b Franz von Papen anali pakati pa Anazi omwe anazengedwa mlandu monga apandu a nkhondo pa Nuremberg, Germany, kumapeto kwa ma 1940. Iye anamasulidwa koma pambuyo pake anapanga lamulo lolimba kuchokera ku bwalo lamilandu lotsutsa chinazi la ku Germany. Pambuyo pakebe, mu 1959, iye anapangidwa kukhala Papal Privy Chamberlain.
c Kuchitira ndemanga pa kusonkhanako, Papa Paul VI ananena kuti: “Ndi molondola mowonadi chotani nanga ndi moyenerera mmene kuliri kuti kufikira kwa chipembedzo kaamba ka mtendere kwaphatikizidwa pakati pa mapwando osaiwalika a kusaina Tchata cha Mitundu Yogwirizana zaka makumi aŵiri zapitazo.”
[Bokosi patsamba 11]
KUKHALA CHETE KWA PAPA
M’bukhu lake Franz von Papen--His Life and Times, lofalitsidwa mu 1939, H. W. Blood-Ryan akulongosola m’tsatanetsatane kuzizwitsidwa kumene kutsanuliridwa kwa chisomo cha upapa kumeneku kunabweretsa Hitler ku mphamvu ndi kukambitsirana chigwirizano cha Vatican ndi Anazi. Ponena za kupha koipa kwa chisawawa, komwe kunaphatikizapo Ayuda, Mboni za Yehova, ndi ena, mkonziyo akunena kuti: “Nchifukwa ninji Pacelli [Papa Pius XII] anakhala chete? Chifukwa chakuti m’kukonzekera kwa von Papen kaamba ka Ulamuliro Woyera wa Roma wa anthu a ku Germany a Kumadzulo iye anawona mtsogolo Tchalitchi cha Katolika champhamvuko, chokhala ndi Vatican ikumabweranso ku mpando wa mphamvu ya ulamuliro . . . Pacelli mmodzimodziyo tsopano akutsanulira mphamvu ya nkhalwe yauzimu pa miyoyo mamiliyoni angapo, komabe mwa pang’ono kachitidwe kakachetechete kanakwezedwa pa nkhalwe ndi chizunzo cha Hitler. . . . Pamene ndikulemba mizera imeneyi, masiku atatu a kupha apita kale ndipo palibe pemphero lomwe ladza kuchokera ku Vatican kaamba ka miyoyo ya omenyanawo, theka la amene ali Akatolika. Kubwezera kudzakhala koipitsitsa pamene anthu amenewa, pokhala atalandidwa zisonkhezero zonse za dziko lapansi, adzaimirira pamaso pa Mulungu wawo, Yemwe adzafunsa kaamba ka kuŵerengera. Kodi nchiyani chomwe chingakhale chodzikhululukira chawo? Palibe nchimodzi chomwe!”
[Bokosi patsamba 15]
KULOŴETSEDWAMO KWA VATICAN
The New York Times ya March 6, 1988, inasimba kuti Vatican inayembekezera kupereŵera kwa chiŵerengero cha ndalama zoyembekezeredwa kuwonongedwa cha $61.8 miliyoni kaamba ka 1988. Pepalalo linalongosola kuti: “Chowonongedwa chachikulu chimodzi moyerekeza chinaphatikiza lonjezo lopangidwa mu 1984 la kulipira chifupifupi $250 miliyoni kwa okongongoletsa a Banco Ambrosiano. Vatican inali yoloŵetsedwamo mwakuya ndi banki ya Milan kugwa kwake kusanakhale mu 1982.” Inali yoloŵetsedwamo mwakuya chotero mu nkhani yochititsa manyazi imeneyi, ndithudi, kotero kuti Vatican yakana molimba mtima kupereka ku maulamuliro nduna zapamwamba zitatu za Vatican, kuphatikizapo bishopu wamkulu wa ku America, kukaimirira kaamba ka kuzengedwa mlandu m’mabwalo amilandu a ku Italy!
[Zithunzi patsamba 12]
Vatican imagawana liwongo la mwazi loipitsitsa ndi von Papen ndi Hitler
[Mawu a Chithunzi]
UPI/Bettmann Newsphotos
UPI/Bettmann Newsphotos
[Zithunzi patsamba 15]
M’malo molengeza Ufumu wa Mulungu, apapa alengeza UN kukhala ‘chiyembekezo chotsirizira cha mtendere’
[Mawu a Chithunzi]
Zithunzi zamkati: UN photos