Padzatsala Chipembedzo Chimodzi
TAYEREKEZERANI mmene zinthu zikanakhalira ngati anthu onse padziko lapansi anali ogwirizana pa chipembedzo chimodzi, pa kulambira Mulungu woona yekha koyera kumodzi. Zimenezo zikanadzetsa umodzi chotani nanga! Sipakanakhalanso kulimbana kwa zipembedzo, ndewu, kapena nkhondo. Kodi zimenezi ndi loto chabe? Ayi. Masomphenya a mtumwi Yohane a chiwonongeko cha mkazi wachigololo, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, amasonyeza kuti padzatsala mtundu wina wa kulambira iye atawonongedwa. Uti?
Mawu amene Yohane anamva ochokera kumwamba akutithandiza kudziŵa: “Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.” (Chivumbulutso 18:4) Nkwachionekere panopa kuti Mulungu mwini akulankhula kwa anthu ake. Onani kuti sakulamula anthu ake kugwirizana ndi mkazi wachigololoyo pantchito yachimvano yoyesa kumpulumutsa mwa kumthandiza kusintha moyo wake kuti ukhale wabwino. Ayi, kulibe mankhwala ake. Chifukwa chake, akuwalamula kutuluka mwa iye ndi kukhala patali naye kuti asadetsedwe ndi machimo ake aakulu ndi kuti potsirizira pake apeŵe kuweruzidwa ndi kuwonongedwa pamodzi naye.
Lamulo lochokera kumwamba la ‘kutuluka mmenemo’ limathandizanso ofunafuna choonadi oona mtima kudziŵa anthu a Mulungu. Iwo angadzifunse kuti, ‘Kodi ndi anthu ati padziko lapansi lerolino amene alabadira lamulo la kuchoka m’chipembedzo chilichonse, gulu, kapena bungwe la olambira ogwirizana ndi “Babulo Wamkulu”? (Chivumbulutso 18:2, NW) Ndi anthu ati padziko lapansi lerolino amene amasuka ku ziphunzitso zonse zachibabulo, zikhulupiriro zake, machitachita, ndi miyambo?’ Kodi angakhale yani kusiyapo Mboni za Yehova? Pakati pa Mboni 5.2 miliyoni m’maiko oposa 230, onse amene anali kugwirizana ndi chipembedzo china chachibabulo, kaya mwa kubadwiramo kapena kutembenuka, achisiyiratu—nthaŵi zina ngakhale pali chiletso ndi chitsutso cha achibale, mabwenzi, ndi atsogoleri achipembedzo.
Mwachitsanzo Henry, mwamuna wina wa ku South Africa, amene anali msungachuma wa tchalitchi chake ndipo anali wodzipereka kwambiri. Koma anali kufunafuna choonadi, ndipo tsiku lina analandira phunziro la Baibulo lapanyumba laulere lochititsidwa ndi Mboni za Yehova. M’kupita kwa nthaŵi, atasankha kukhala Mboni, anauza pasitala wake, amenenso anali wachinansi wake wapafupi, kuti anafuna kusiya tchalitchi chake.
Pasitalayo anadabwa kwambiri ndipo pambuyo pake anatenga woyang’anira ndi mamembala ena a tchalitchi kupita nawo kwa Henry. Iwo anamfunsa chimene anasiyira tchalitchi chawo ndi kukhala membala wa chipembedzo chimene, malinga ndi kunena kwawo, chilibe mzimu woyera wa Mulungu. “Poyamba, ndinachita mantha kuti ndiwayankhe,” anatero Henry, “chifukwa nthaŵi zonse anali kundilimbikitsa kwambiri. Koma ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize, ndipo ananditheketsa kuti ndipereke chifukwa chotsatira: ‘Pa zipembedzo zonse za padziko, kodi nchiti chokha chimene nthaŵi zonse chimagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, Yehova? Kodi si Mboni za Yehova? Kodi mukuganiza kuti Mulungu akanawalola kutenga dzina lake popanda kuwapatsanso mzimu wake woyera?’” Akuluakulu a tchalitchiwo analephera kutsutsa lingaliro lake, ndipo Henry tsopano ali mmodzi wa Mboni za Yehova.
Chotero pamene mawu ochokera kumwamba alamula kuti: “Tulukani m’menemo,” kuli kumene mungapite. (Chivumbulutso 18:4) Alipo anthu, olambira Mulungu woona, Yehova, amene mungathaŵireko. Mamiliyoni ambiri athaŵa. Podziŵika monga Mboni za Yehova, iwo amapanga ubale wachikristu wa dziko lonse, wolinganizidwa m’mipingo yoposa 78,600, ndipo tsopano akuona chiwonjezeko chachikulu koposa m’mbiri yawo. Abatiza anthu oposa 1,200,000 pazaka zinayi zapitazo! Asanabatizidwe, onsewa anamaliza kosi yotsitsimula mwauzimu ya phunziro la Baibulo, imene inawatheketsa kupanga chosankha chotsimikizirika chaumwini cha kusiya kugwirizana ndi zipembedzo zina zilizonse.—Zefaniya 2:2, 3.
Ngati simunapezekepobe pamsonkhano wa Mboni za Yehova pa imodzi ya Nyumba zawo za Ufumu, bwanji osachita tero mlungu uno? Mwina mudzachita nazo chidwi kwambiri zimene mudzaona ndi kumva. Ndipo ngati mukufuna kumvetsa Baibulo, bwanji osapempha mmodzi wa Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu, monga momwe ena mamiliyoni ambiri achitira? Ngati pemphero lanu nlakuti mupeze chidziŵitso chenicheni cha Mawu a Mulungu limodzi ndi moyo wogwirizana ndi Mawuwo, pemphero lanu lidzayankhidwa.
[Zithunzi patsamba 8]
Mamiliyoni ambiri akutembenukira ku kulambira Yehova Mulungu