Mutu 38
Tamandani Ya Chifukwa cha Ziweruzo Zake
1. Kodi Yohane anamva mawu otani “ofuula kumwamba ngati mawu a khamu lalikulu”?
ZIDZAKHALA zosangalatsa kwambiri Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, choncho m’pake kuti Yohane anamva mawu achisangalalo otamanda Mulungu kumwamba. Iye anati: “Zimenezi zitatha, ndinamva mawu ofuula kumwamba ngati mawu a khamu lalikulu, akuti: ‘Aleluya!a Chipulumutso, ulemerero, ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu, chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama. Pakuti iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi dama lake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.’ Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: ‘Aleluya!b Utsi wochokera kwa iye udzafuka kwamuyaya.’”—Chivumbulutso 19:1-3.
2. (a) Kodi mawu akuti “Aleluya!” amatanthauza chiyani, ndipo zoti Yohane anamva mawuwa kawiri konse pandime imeneyi zikusonyeza chiyani? (b) Kodi ndani amene adzalandire ulemerero chifukwa chowononga Babulo Wamkulu? Fotokozani.
2 Mawu akuti “Aleluya!” amatanthauza “Tamandani Ya, anthu inu!” ndipo “Ya” ndi chidule cha dzina la Mulungu lakuti Yehova. Zimenezi zikutikumbutsa mawu amene wamasalimo analemba, akuti: “Chopuma chilichonse chitamande Ya. Tamandani Ya, anthu inu!” (Salimo 150:6) Pandime imeneyi m’masomphenya a m’Chivumbulutsowa, Yohane anamva zolengedwa za kumwamba zikuimba mosangalala nyimbo yomwe zinatchulamo mawu akuti “Aleluya!” kawiri konse, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu anapitiriza kuulula choonadi chake. Mulungu amene watchulidwa m’Malemba Achigiriki ndi yemweyonso amene anatchulidwa m’Malemba Achiheberi ndipo dzina lake ndi Yehova. Mulungu amene anachititsa kuti Babulo wakale awonongedwe ndi yemweyonso amene adzaweruze ndi kuwononga Babulo Wamkulu. Ulemerero wonse udzapita kwa iye chifukwa chochita zimenezi. Mphamvu zimene zidzachititse kuti Babulo Wamkulu awonongedwe zidzachokera kwa Mulungu ameneyu osati kwa mayiko amene adzawagwiritse ntchito powononga Babuloyu. Choncho, ndi Yehova yekha amene adzatipulumutse.—Yesaya 12:2; Chivumbulutso 4:11; 7:10, 12.
3. N’chifukwa chiyani hule lalikulu lija lili loyenera kupatsidwa chilango?
3 Kodi n’chifukwa chiyani hule lalikululi lili loyenera kupatsidwa chilangochi? Malinga ndi chilamulo chimene Yehova anapatsa Nowa, ndiponso mtundu wonse wa anthu kudzera mwa Nowayo, munthu wopha dala mnzake ayenera kuphedwa. Lamulo limeneli linabwerezedwanso m’Chilamulo cha Mulungu kwa Aisiraeli. (Genesis 9:6; Numeri 35:20, 21) Komanso pa Chilamulo cha Mose chimenechi, munthu akachita chigololo chenicheni kapena chauzimu ankafunika kuphedwa. (Levitiko 20:10; Deuteronomo 13:1-5) Kwa zaka masauzande ambiri, Babulo Wamkulu wakhala ndi mlandu wa magazi, ndiponso wachita dama lalikulu. Mwachitsanzo, chifukwa chakuti tchalitchi cha Katolika chimaletsa ansembe ake kukwatira, ambiri a iwo amachita dama lonyansa, ndipo ochuluka akutenga matenda a Edzi masiku ano. (1 Akorinto 6:9, 10; 1 Timoteyo 4:1-3) Koma machimo ake akuluakulu, omwe “aunjikana mpaka kumwamba,” ndi okhudza dama lake lonyansa lauzimu chifukwa iye amaphunzitsa mabodza komanso amagwirizana ndi atsogoleri a ndale omwe amachita zachinyengo. (Chivumbulutso 18:5) Iye akadzalandira chilango chake chomaliza, gulu la zolengedwa zakumwamba zija lidzatchula kachiwiri mawu akuti Aleluya m’nyimbo yawo.
4. Kodi mfundo yakuti utsi wa Babulo Wamkulu “udzafuka kwamuyaya” ikutanthauza chiyani?
4 Babulo Wamkulu adzatenthedwa ngati mzinda wogonjetsedwa, ndipo utsi wake “udzafuka kwamuyaya.” Asilikali akagonjetsa mzinda weniweni ndi kuutentha ndi moto, utsi umapitiriza kufuka mpaka phulusa lonse litazizira. Ngati munthu wina atayesa kumanganso mzindawo ukufukabe utsi, akhoza kupsa. Popeza utsi wa Babulo Wamkulu “udzafuka kwamuyaya” akadzapatsidwa chiweruzo chake chomaliza, palibe munthu yemwe adzamangenso mzinda wochimwawo. Zipembedzo zonyenga zidzawonongedwa ndipo sizidzakhalaponso. M’pake kuti zolengedwa zakumwamba zija zidzaimba kuti Aleluya!—Yerekezerani ndi Yesaya 34:5, 9, 10.
5. (a) Kodi akulu 24 ndi zamoyo zinayi ananena chiyani ndipo anachita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani nyimbo zimenezi zokhala ndi mawu akuti Aleluya, zili zokoma kwambiri kuposa nyimbo zilizonse zokhala ndi mawu akuti Aleluya zimene zimaimbidwa m’Matchalitchi Achikhristu?
5 M’masomphenya ena m’mbuyomu, Yohane anaona zamoyo zinayi zitazungulira mpando wachifumu pamodzi ndi akulu 24, omwe akuimira olowa Ufumu ali m’malo awo aulemerero kumwamba. (Chivumbulutso 4:8-11) Koma tsopano Yohane anaonanso zamoyo zinayizi ndi akulu 24 aja akuimba nyimbo mofuula kwambiri n’kutchula kachitatu mawu akuti Aleluya posangalala ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu. Yohane akufotokoza kuti: “Ndipo akulu 24 ndi zamoyo zinayi zija, anagwada pansi ndi kuwerama, n’kulambira Mulungu wokhala pampando wachifumu, ndi mawu akuti: ‘Ame! Aleluya!’”c (Chivumbulutso 19:4) Choncho nyimbo yofuula imeneyi yokhala ndi mawu akuti Aleluya, ikuwonjezera pa “nyimbo yatsopano” yotamanda Mwanawankhosa. (Chivumbulutso 5:8, 9) Iwo akuimba nyimbo yokondwerera kupambanayi, ndipo akupereka ulemerero wonse kwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chifukwa wapambana n’kugonjetseratu hule lalikulu lija, lomwe ndi Babulo Wamkulu. Nyimbo zimene gulu lakumwambali likuimba n’kutchulamo mawu akuti Aleluya, n’zokoma kwambiri kuposa nyimbo zilizonse zokhala ndi mawu akuti Aleluya zimene zimaimbidwa m’Matchalitchi Achikhristu. Matchalitchiwa salemekeza Yehova, kapena kuti Ya, koma m’malo mwake amamunyoza. Anthu achinyengo amene amaimba nyimbo zimenezi, zomwe zimanyoza dzina la Yehova, adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso.
6. Kodi panamveka “mawu” a ndani, ndipo mawuwo akulimbikitsa kuchita chiyani, nanga ndi ndani amene akumvera mawu amenewa?
6 Mu 1918, Yehova anayamba kupereka mphoto kwa anthu ‘oopa dzina lake, olemekezeka ndi onyozeka omwe.’ Oyambirira mwa anthu amenewa anali Akhristu odzozedwa amene anafa ali okhulupirika, ndipo iye anawaukitsa n’kuwaika m’malo awo kumwamba m’gulu la akulu 24. (Chivumbulutso 11:18) Enanso anayamba kuimba nawo nyimbo zokhala ndi mawu akuti Aleluya zimenezi, chifukwa Yohane akutiuza kuti: “Komanso, kunamveka mawu ochokera kumpando wachifumu akuti: ‘Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapolo ake, inu omuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe.’” (Chivumbulutso 19:5) Amenewa ndi “mawu” a Womulankhulira wa Yehova, yemwe ndi Mwana wake Yesu Khristu, amene waima “pafupi ndi mpando wachifumu.” (Chivumbulutso 5:6) Nyimbozi sikuti zikuimbidwa kumwamba kokha, koma zikuimbidwanso padziko lapansi ndi ‘akapolo ake onse,’ ndipo Akhristu odzozedwa ndi omwe akutsogolera. Anthu onsewa akuimba nawo nyimbozi mosangalala pomvera lamulo lakuti: “Muzitamanda Mulungu wathu.”
7. Kodi Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, ndani amene azidzatamanda Yehova?
7 Zoonadi, a khamu lalikulu alinso m’gulu la akapolo amenewa. Kuyambira mu 1935, iwo anayamba kutuluka mu Babulo Wamkulu ndipo aona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu lakuti: “Yehova adzadalitsa anthu omuopa, adzadalitsa onsewo [olemekezeka ndi onyozeka omwe] osasiyapo aliyense.” (Salimo 115:13) Babulo yemwe ali ngati hule akadzawonongedwa, mamiliyoni ambiri a khamu lalikulu adzayamba ‘kutamanda nawo Mulungu wathu’ mogwirizana ndi Akhristu odzozedwa komanso gulu lonse la zolengedwa zakumwamba. Kenako anthu amene adzaukitsidwe padziko lapansi, kaya poyamba anali olemekezeka kapena onyozeka, nawonso adzaimba nawo nyimbo zokhala ndi mawu akuti Aleluya akadzamva kuti Babulo Wamkulu anawonongedwa ndipo anatheratu. (Chivumbulutso 20:12, 15) Yehova yekha ndiye adzatamandidwe chifukwa adzakhala atapambana kwambiri pogonjetsa hule lakalekale limeneli.
8. Kodi nyimbo zimene Yohane anamva zikuimbidwa kumwamba ziyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani panopa Babulo Wamkulu asanawonongedwe?
8 Zimenezi zikutilimbikitsa kwambiri kuti tizigwira ntchito ya Mulungu mwakhama masiku ano. Choncho, atumiki onse a Ya ayenera kudzipereka ndi mtima wawo wonse komanso moyo wawo wonse pogwira ntchito yolengeza ziweruzo za Mulungu komanso madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse. Iwo ayenera kuchita zimenezi panopa Babulo Wamkulu asanagonjetsedwe ndi kuwonongedwa.—Yesaya 61:1-3; 1 Akorinto 15:58.
Tamandani Ya Chifukwa Yehova Ndi Mfumu
9. N’chifukwa chiyani mawu omaliza akuti Aleluya anaimbidwa mwamphamvu komanso mosangalatsa kwambiri?
9 Yohane akupitiriza kutiuza zifukwa zinanso zotichititsa kusangalala. Iye anati: “Kenako ndinamva mawu ngati a khamu lalikulu, omveka ngati mkokomo wa madzi ambiri ndi mabingu amphamvu. Mawuwo anati: ‘Aleluya,d chifukwa Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulira monga mfumu.’” (Chivumbulutso 19:6) Mawu omaliza akuti Aleluya amenewa ndi omwe akuchititsa kuti uthengawu ukhale wochokera kumbali zonse zinayi. Mawu ochokera kumwambawa ndi omveka mokoma kuposa nyimbo iliyonse imene inaimbidwapo ndi anthu, ndi amphamvu kwambiri kuposa mathithi alionse a padziko lapansi, ndiponso ndi ochititsa mantha zedi kuposa mvula iliyonse ya mabingu yomwe inagwapo. Zolengedwa zambirimbiri zakumwamba ndi zomwe zinaimba mawuwa posangalala kuti “Yehova Mulungu wathu, Wamphamvuyonse, wayamba kulamulira monga mfumu.”
10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, Yehova adzayamba kulamulira monga mfumu?
10 Koma kodi mawu akuti Yehova wayamba kulamulira akutanthauza chiyani? Padutsa zaka masauzande ambiri kuchokera pamene wamasalimo ananena kuti: “Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale.” (Salimo 74:12) Ngakhale pa nthawiyo, Yehova anali ali kale mfumu kuyambira kalekale. Nanga n’chifukwa chiyani nyimboyi ikuti “Yehova . . . wayamba kulamulira monga mfumu”? Zimenezi zikutanthauza kuti Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, Yehova sadzakhalanso ndi mdani ameneyu, yemwe amapikisana naye ndiponso amasokoneza anthu kuti asamvere Mulungu monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. Choncho sipadzakhalanso zipembedzo zonyenga zimene zimalimbikitsa olamulira a padzikoli kuti azitsutsana ndi Mulungu. Babulo wakale atagonjetsedwa n’kusakhalanso wolamulira wamphamvu kwambiri padziko lonse, Ziyoni anamva uthenga wokondwerera kupambana, wakuti: “Mulungu wako wakhala mfumu.” (Yesaya 52:7) Ufumu wa Mulungu utabadwa mu 1914, akulu 24 ananena kuti: “Tikukuyamikani inu Yehova, Mulungu . . . chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu ndi kuyamba kulamulira monga mfumu.” (Chivumbulutso 11:17) Tsopano Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, padzamvekanso mawu ofuula akuti: “Yehova . . . wayamba kulamulira monga mfumu.” Sipadzakhalanso mulungu aliyense wopangidwa ndi anthu amene azidzapikisana ndi Mulungu woona Yehova, yemwe ndi wolamulira wa chilengedwe chonse.
Ukwati wa Mwanawankhosa Wayandikira
11, 12. (a) Kodi anthu a mumzinda wakale wa Yerusalemu ankaona bwanji anthu a ku Babulo, ndipo potsatira chitsanzo chimenechi, Yerusalemu Watsopano amaona bwanji Babulo Wamkulu? (b) Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, kodi gulu la zolengedwa zakumwamba lidzaimba nyimbo yotani ndipo lidzalengeza chiyani?
11 Anthu a ku Yerusalemu, malo amene kunali kachisi wolambiriramo Yehova, ankaona anthu a ku Babulo, omwe anali olambira mafano, kuti anali ‘adani awo.’ (Mika 7:8) Nawonso “mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano,” womwe wapangidwa ndi anthu 144,000 amene ali ngati mkwatibwi, uli ndi zifukwa zomveka zoonera Babulo Wamkulu kuti ndi mdani wake. (Chivumbulutso 21:2) Koma posachedwapa hule lalikululi liona zakuda chifukwa liwonongedwa n’kutheratu, ndipo anthu ake ochita zamizimu ndi okhulupirira nyenyezi adzalephera kulipulumutsa. (Yerekezerani ndi Yesaya 47:1, 11-13.) Zimenezi zikutanthauza kuti olambira oona adzapambana.
12 Hule lonyansa lija lomwe ndi Babulo Wamkulu likadzawonongedwa n’kusakhalaponso mpaka kalekale, tsopano maso onse adzakhala pa namwali wosadetsedwa, yemwe ndi mkwatibwi wa Mwanawankhosa. Choncho, gulu la zolengedwa zakumwamba lija lidzaimba mosangalala kwambiri nyimbo yotamanda Yehova, kuti: “Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya. Timupatse ulemerero, chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa [ndipo wakonzeka]. Iye waloledwa kuvala zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, pakuti zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.”—Chivumbulutso 19:7, 8.
13. Kodi ndi zinthu ziti zimene zakhala zikuchitika kwa zaka zambirimbiri pokonzekera ukwati wa Mwanawankhosa?
13 Mwachikondi, kwa zaka zambirimbiri Yesu wakhala akukonzekera ukwati wakumwambawu. (Mateyu 28:20; 2 Akorinto 11:2) Yesu wakhala akuyeretsa a 144,000, omwe ndi Isiraeli wauzimu, n’cholinga choti “iyeyo alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zotero, koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.” (Aefeso 5:25-27) Akhristu odzozedwa akuyembekezera “mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba.” Choncho zinali zofunikiradi kuti Mkhristu wodzozedwa aliyense avule umunthu wake wakale ndi ntchito zake zonse, n’kuvala umunthu watsopano wogwirizana ndi Chikhristu, ndiponso kuchita ntchito zolungama ‘ndi moyo wake wonse ngati kuti akuchitira Yehova.’—Afilipi 3:8, 13, 14; Akolose 3:9, 10, 23.
14. Kodi Satana wachita zotani poyesetsa kuti adetse anthu omwe adzakhale m’gulu la mkwatibwi wa Mwanawankhosa?
14 Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., Satana wakhala akugwiritsa ntchito Babulo Wamkulu ngati chida chake poyesetsa kuti adetse anthu omwe adzakhale m’gulu la mkwatibwi wa Mwanawankhosa. Pomafika kumapeto kwa zaka za m’nthawi ya atumwi, iye anali atafesa mbewu ya chipembedzo chachibabulo mumpingo wachikhristu. (1 Akorinto 15:12; 2 Timoteyo 2:18; Chivumbulutso 2:6, 14, 20) Pofotokoza za anthu amene ankapotoza chikhulupiriro choona, mtumwi Paulo ananena kuti: “Pakuti amuna oterowo ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzisandutsa atumwi a Khristu. Ndipo zimenezo n’zosadabwitsa, popeza ngakhale Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” (2 Akorinto 11:13, 14) Kwa zaka mahandiredi ambiri kuchokera m’nthawi ya atumwi, Matchalitchi Achikhristu ampatuko mofanana ndi Babulo Wamkulu yense, akhala akudziveka zovala zapamwamba komanso zamtengo wapatali. Zovala zimenezi ndi “zovala zofiirira ndi zofiira kwambiri . . . ndi golide, ndi mwala winawake wamtengo wapatali, ndiponso ngale.” (Chivumbulutso 17:4) Atsogoleri a matchalitchiwa komanso apapa ankagwirizana kwambiri ndi mafumu, monga Constantine ndi Charlemagne, omwe anapha anthu ambiri. Ndithudi, Matchalitchi Achikhristu sanayambe avalapo “ntchito zolungama za oyera.” Popeza matchalitchiwa ndi mkwatibwi wachinyengo, iwo ndi chida chachikulu chimene Satana akuchigwiritsa ntchito ponyenga anthu. Koma posachedwapa, iwo awonongedwa ndipo sadzakhalaponso.
Mkazi wa Mwanawankhosa Wakonzeka
15. Kodi kuikidwa chidindo kumachitika motani, ndipo Mkhristu wodzozedwa aliyense ayenera kuchita chiyani?
15 Choncho masiku ano, pamene zaka pafupifupi 2,000 zadutsa kuchokera nthawi imene Yesu anabwera padziko lapansi, Akhristu onse a 144,000 amene ali ngati mkwatibwi akonzeka. Koma kodi ndi nthawi iti pamene tinganenedi kuti ‘mkazi wa Mwanawankhosa wadzikongoletsa ndipo wakonzeka’? Kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E., mwapang’onopang’ono Akhristu odzozedwa okhulupirika anayamba ‘kuikidwa chidindo cha mzimu woyera wolonjezedwawo’ podikira kubwera kwa ‘tsiku limene adzamasulidwe ndi dipo.’ Pofotokoza zimenezi, mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu “watiikanso chidindo chake chotitsimikizira ndipo watipatsa m’mitima mwathu chikole cha madalitso am’tsogolo, ndicho mzimu.” (Aefeso 1:13; 4:30; 2 Akorinto 1:22) Mkhristu wodzozedwa aliyense ndi ‘woitanidwa komanso wosankhidwa mwapadera’ ndipo ayenera kusonyeza kuti ndi ‘wokhulupirika.’—Chivumbulutso 17:14.
16. (a) Kodi ntchito yoika chidindo pa mtumwi Paulo inatha liti, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (b) Kodi ndi nthawi iti pamene mkazi wa Mwanawankhosa adzamalize ‘kudzikongoletsa ndi kukonzekera’?
16 Paulo atakumana ndi mayesero osiyanasiyana kwa zaka zambiri, pomalizira pake ananena kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. Ndasunga chikhulupiriro. Kuyambira panopa mpaka m’tsogolo, andisungira chisoti chachifumu chachilungamo. Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa mphotoyo m’tsikulo. Sadzapatsa ine ndekha ayi, komanso onse amene akhala akuyembekezera kuti iye adzaonekere.” (2 Timoteyo 4:7, 8) Pa nthawiyi, zikuoneka kuti ntchito yoika chidindo pa mtumwiyu inali itatha ngakhale kuti iye anali adakali padziko lapansi ndipo ankayembekezera kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Mofanana ndi zimenezi, nthawi idzafika pamene Akhristu a 144,000 amene adakali ndi moyo padziko lapansi, aliyense payekha, adzaikidwa chidindo posonyeza kuti iwo ndi anthu a Yehova. (2 Timoteyo 2:19) Zimenezi zikadzachitika, mkazi wa Mwanawankhosa adzakhala atamaliza kudzikongoletsa ndi kukonzekera. Ndipotu ambiri mwa anthu 144,000 adzakhala atalandira kale mphoto yawo kumwamba ndipo amene adzakhale adakali padziko lapansili, Mulungu adzakhala atawavomereza ndiponso atawaika chidindo komaliza posonyeza kuti iwo ndi okhulupirika.
17. Kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzachitika liti?
17 Pa nthawiyi mogwirizana ndi ndondomeko imene Yehova akuyendera, ntchito yodinda chidindo Akhristu onse a 144,000 ikadzatha, angelo adzamasula mphepo zinayi za chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 7:1-3) Poyamba, chiweruzo chidzaperekedwa kwa Babulo Wamkulu yemwe ali ngati hule. Kenako Khristu yemwe adzakhale atapambana pa nkhondo adzawononga mwamsanga mbali zonse zotsala za gulu la Satana padziko lapansili pa Aramagedo. Kenako adzaponya Satana ndi ziwanda zake kuphompho. (Chivumbulutso 19:11–20:3) Ngati pa nthawiyo Akhristu ena odzozedwa adzakhale adakali padziko lapansi, n’zosakayikitsa kuti adzalandira mphoto yawo kumwamba Khristu akadzangomaliza kugonjetsa adani ake. Kumwambako, iwo akakhala m’gulu la anthu amene akupanga mkwatibwi, pamodzi ndi anzawo amene anapita kale. Kenako, pa nthawi imene Mulungu anakonzeratu, ukwati wa Mwanawankhosa udzachitika.
18. Kodi Salimo 45 likusonyeza bwanji ndondomeko ya mmene zinthu zokhudzana ndi ukwati wa Mwanawankhosa zidzachitikire?
18 Mawu aulosi amene ali mu Salimo 45 analongosola bwino ndondomeko ya mmene zinthu zidzachitikire. Choyamba Mfumu yomwe inaikidwa pampando idzakwera pahatchi n’kupita kukagonjetsa adani ake. (Vesi 1-7) Kenako ukwati udzachitika ndipo mkwatibwi wakumwamba adzaperekezedwa ndi anamwali anzake apadziko lapansi, omwe ndi a khamu lalikulu. (Vesi 8-15) Ndiyeno ukwatiwu ukadzachitika padzatuluka zipatso, zomwe ndi anthu omwe adzaukitsidwe n’kukhala angwiro ndipo azidzayang’aniridwa ndi “akalonga padziko lonse lapansi.” (Vesi 16, 17) Zimenezi zikusonyezeratu kuti ukwati wa Mwanawankhosa udzabweretsa madalitso ambiri.
Odala Ndiwo Amene Aitanidwa
19. Kodi chinthu chachinayi mwa zinthu 7 zotchulidwa m’buku la Chivumbulutso zokhudzana ndi anthu odala n’chiti, ndipo ndani amene adzasangalale nawo?
19 Tsopano Yohane akutiuza chinthu chachinayi mwa zinthu 7 zotchulidwa m’buku la Chivumbulutso zonena za anthu odala. Iye anati: “Mngeloyo anandiuza kuti: ‘Lemba: Odala ndiwo amene aitanidwa ku phwando la chakudya chamadzulo la ukwati wa Mwanawankhosa.’ Anandiuzanso kuti: ‘Awa ndi mawu oona a Mulungu.’” (Chivumbulutso 19:9)e Anthu amene aitanidwa ku “phwando la chakudya chamadzulo la ukwati wa Mwanawankhosa” ali m’gulu la mkwatibwi. (Yerekezerani ndi Mateyu 22:1-14.) Anthu onse omwe ali m’gulu la mkwatibwili, omwe ndi odzozedwa, ndi odala kapena kuti osangalala, chifukwa anaitanidwa. Ambiri mwa anthuwa anapita kale kumwamba, kumalo omwe kukachitikire phwando la chakudya chamadzulo la ukwati. Ndipo odzozedwa omwe adakali padziko lapansili nawonso ndi osangalala chifukwa anaitanidwa, ndipo ali ndi malo awo ku phwando la chakudya chamadzuloli. (Yohane 14:1-3; 1 Petulo 1:3-9) Anthu onse odzozedwa akadzapita kumwamba, gulu lonse la mkwatibwi logwirizanali, lidzasangalala pamodzi ndi Mwanawankhosa pa ukwati wosangalatsa kwambiriwu.
20. (a) Kodi mawu akuti, “awa ndi mawu oona a Mulungu,” akusonyeza chiyani? (b) Kodi Yohane anatani atamva mawu amene mngelo uja analankhula, nanga mngeloyo ananena chiyani ataona zimenezo?
20 Mngelo uja anawonjezera kuti, “awa ndi mawu oona a Mulungu.” Mawu akuti “oona” amenewa anamasuliridwa kuchokera ku mawu achigiriki (a·le·thi·nosʹ) ndipo amatanthauza kuti chinthu ndi “chenicheni” kapena “chodalirika.” Mawuwa ndi oona ndiponso odalirika chifukwa kwenikweni akuchokera kwa Yehova. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 4:1-3; Chivumbulutso 21:5; 22:6.) Popeza Yohane ali m’gulu la anthu oitanidwa ku phwando la ukwatili, ayenera kuti anasangalala kwambiri atamva zimenezi ndiponso ataganizira za madalitso amene gulu la mkwatibwi limeneli lidzalandire. Zimenezi zinamukhudza kwambiri mumtima moti mpaka anapatsidwa nazo uphungu ndi mngelo uja. Yohane akufotokoza kuti: “Pamenepo ndinagwada pansi n’kuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire. Koma iye anandiuza kuti: ‘Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu. Lambira Mulungu.’”—Chivumbulutso 19:10a.
21. (a) Kodi buku la Chivumbulutso limatiululira chiyani pa nkhani ya angelo? (b) Kodi Akhristu ayenera kuwaona motani angelo?
21 M’buku lonse la Chivumbulutso muli umboni wamphamvu wosonyeza kuti angelo ndi okhulupirika komanso akhama kwambiri. Iwo ndi mbali ya njira imene Mulungu amagwiritsa ntchito poulula choonadi chake. (Chivumbulutso 1:1) Angelo amathandizanso anthu pogwira ntchito yolalikira uthenga wabwino ndiponso pokhuthula miliri yophiphiritsa. (Chivumbulutso 14:6, 7; 16:1) Komanso angelo anamenya nkhondo kumwamba pamodzi ndi Yesu n’kuchotsako Satana ndi angelo ake, ndipo m’tsogolo muno, adzamenyanso nkhondo pamodzi ndi Yesu pa Aramagedo. (Chivumbulutso 12:7; 19:11-14) Kuwonjezera pa zonsezi, angelo ali ndi mwayi wapadera chifukwa amatha kufika pamaso pa Yehova weniweniyo. (Mateyu 18:10; Chivumbulutso 15:6) Ngakhale zili choncho, angelo ndi odzichepetsa ndipo angokhala akapolo chabe a Mulungu. M’gulu la olambira oona, anthu salambira angelo ngakhale pang’ono. Komanso salambira Mulungu kudzera mwa angelo, kapena kudzera mwa anthu amene amaonedwa kuti ndi oyera. (Akolose 2:18) Akhristu amalambira Yehova yekha ndipo amapemphera kwa iye kudzera m’dzina la Yesu.—Yohane 14:12, 13.
Udindo wa Yesu Mogwirizana ndi Ulosi
22. Kodi mngelo uja anamuuza chiyani Yohane, ndipo zimene anamuuzazo zikutanthauza chiyani?
22 Kenako mngelo uja anati: “Pakuti kuchitira umboni za Yesu ndiko cholinga cha maulosi.” (Chivumbulutso 19:10b) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti maulosi onse ouziridwa analembedwa chifukwa cha Yesu ndiponso chifukwa cha udindo umene iye ali nawo pokwaniritsa zolinga za Yehova. Ulosi woyamba wa m’Baibulo unalonjeza zoti kudzabwera mbewu. (Genesis 3:15) Ndipo Yesu ndi amene anadzakhala Mbewu imeneyo. Zinthu zotsatira zimene Mulungu anaulula zinapereka umboni wochuluka wotsimikizira kuti lonjezo limeneli ndi loona. Mwachitsanzo, mtumwi Petulo anauza Koneliyo, yemwe anali wokhulupirira koma sanali Myuda, kuti: “Aneneri onse amachitira umboni za [Yesu].” (Machitidwe 10:43) Patapita zaka pafupifupi 20, mtumwi Paulo anati: “Malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani, akhala Inde kudzera mwa [Yesu].” (2 Akorinto 1:20) Komanso patapita zaka zina 43, nayenso Yohane anatikumbutsa kuti: ‘Choonadi chinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu.’—Yohane 1:17.
23. N’chifukwa chiyani udindo ndi ulamuliro waukulu umene Yesu ali nawo sukusonyeza kuti iye amalambiridwa m’malo mwa Yehova?
23 Kodi zimenezi zikusonyeza kuti mwanjira inayake Yesu akulambiridwa m’malo mwa Yehova? Ayi. Kumbukirani chenjezo limene mngelo uja anapereka. Iye analimbikitsa Yohane kuti: “Lambira Mulungu.” Komanso Yesu sanayesepo n’komwe kupikisana ndi Yehova. (Afilipi 2:6) N’zoona kuti angelo onse anauzidwa kuti ‘agwadire Yesu,’ ndiponso chilengedwe chonse chiyenera kuzindikira udindo waukulu umene iye ali nawo, kuti ‘m’dzina la Yesu, onse apinde mawondo awo.’ Koma onani kuti vesili likuti zimenezi ziyenera kuchitika “polemekeza Mulungu Atate,” komanso molamulidwa ndi Mulunguyo. (Aheberi 1:6; Afilipi 2:9-11) Yehova anapatsa Yesu udindo waukulu, ndipo tikamasonyeza kuti tikulemekeza udindo umenewo, timapereka ulemerero kwa Mulungu. Ngati tingakane kugonjera ulamuliro wa Yesu, ndiye kuti tikukana Yehova Mulungu weniweniyo.—Salimo 2:11, 12.
24. Kodi ndi zinthu ziwiri zikuluzikulu ziti zimene tiyenera kuziganizira, nanga ndi mawu otani amene tiyenera kunena?
24 Choncho, tiyeni tonse tinene mogwirizana mawu oyambirira a pa Salimo 146 mpaka 150, akuti: “Tamandani Ya, anthu inu!” Tiyeni tipitirize kugwirizana ndi magulu akumwamba aja poimba mofuula nyimbo zokhala ndi mawu akuti Aleluya pamene tikuyembekezera kuti Yehova agonjetse Babulo Wamkulu, yemwe ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. Ndiponso tipitirizebe kusangalala kwambiri pamene ukwati wa Mwanawankhosa ukuyandikira.
[Mawu a M’munsi]
a Onani mawu a m’munsi pa Chivumbulutso 19:1.
b Onani mawu a m’munsi pa Chivumbulutso 19:1.
c Onani mawu a m’munsi pa Chivumbulutso 19:1.
d Onani mawu a m’munsi pa Chivumbulutso 19:1.
e Onaninso Chivumbulutso 1:3; 14:13; 16:15.
[Bokosi patsamba 273]
“Kalata Yopita ku Sodomu ndi Gomora”
Nkhani yokhala ndi mutu womwe uli pamwambawu inatuluka m’nyuzipepala ina ya ku London (Daily Telegraph) pa November 12, 1987. Nkhaniyi inafotokoza mfundo zimene sinodi yaikulu ya mpingo wa Church of England inkakambirana pofuna kuchotsa m’tchalitchichi anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha. Godfrey Barker, yemwe analemba nkhaniyi m’nyuzipepalayi ananena kuti: “Dzulo Bishopu Wamkulu wa ku Canterbury wanena mwamanyazi mmene akuonera zinthu, kuti: ‘Ngati Paulo Woyera akanalemba kalata yopita ku mpingo wa Church of England, sitikudziwa kuti akanalemba zotani m’kalata imeneyo.’” A Barker anapitiriza kufotokoza kuti: “Ndikuona kuti kalatayi ikanakhaka ngati kalata yopita ku Sodomu ndi Gomora, ndipo Dr Runcie [bishopu wamkulu] akuganiza kuti uthenga wake ukanafanana ndi wa pa Aroma chaputala 1.”
Wolemba nkhaniyi anagwira mawu a Paulo omwe ali pa Aroma 1:26-32 akuti: “Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zamanyazi za kugonana, . . . amuna ndi amuna anzawo, kuchitirana zonyansa. . . . Ngakhale kuti amalidziwa bwino lamulo lolungama la Mulungu, lakuti amene amachita zinthu zimenezi n’ngoyenera imfa, iwo amapitiriza kuzichita. Kuwonjezera apo, amagwirizananso ndi anthu amene amachita zimenezo.” Pomaliza iye ananena kuti: “Paulo Woyera ankada nkhawa kwambiri ndi makhalidwe onyansa a anthu wamba mumpingo. Koma Dr Runcie akuda nkhawa chifukwa amene akuchita makhalidwe onyansawa ndi atsogoleri a chipembedzocho.”
Kodi n’chifukwa chiyani bishopu wamkuluyu anathedwa nzeru chonchi? Nyuzipepala ina ya ku London (Daily Mail ) ya pa October 22, 1987, inali ndi nkhani zikuluzikulu zimene zinanena kuti: “‘Pa atsogoleri atatu alionse a Church of England, mmodzi amagonana ndi amuna anzake.’ . . . Ndiponso maganizo ofuna kuchotsa m’tchalitchichi anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha, ‘angachititse kuti mpingo wa Church of England utheretu.’” Nkhanizi zinagwira mawu a munthu wina yemwe ankati ndi m’busa, amenenso anali mlembi wa kagulu ka Akhristu olimbikitsa kuti anthu azikwatirana amuna kapena akazi okhaokha. M’busayu ananena kuti: “Ngati sinodi ya mpingo wa Church of England itavomereza maganizo oti ichotse anthu ogonana amuna kapena akazi okhaokha, ndiye kuti kutha kwa tchalitchi kungakhale komweko, ndipo Bishopu Wamkulu wa ku Canterbury akudziwa zimenezi. Tikuganiza kuti pa atsogoleri 100 alionse a mpingo wa Church of England, 30 kapena 40 amagonana amuna okhaokha. Ndipo atsogoleri amenewa ndi amene amachita zambiri potumikira m’matchalitchi athu.” Chiwerengero cha anthu amene amapita ku tchalitchi chikucheperachepera, ndipo mosakayikira zimenezi zikusonyeza kuti mwa zina anthu akuipidwa ndi kuchuluka kwa atsogoleri awo amene amagonana amuna kapena akazi okhaokha.
Kodi sinodi ya mpingowu inagwirizana chiyani pa nkhaniyi? Atsogoleri 388 a mpingowu (omwe ndi atsogoleri 95 pa atsogoleri 100 alionse) anavomereza mfundo yakuti sinodi ingonyalanyaza nkhaniyi. Pa nkhani imeneyi, magazini ina (The Economist) ya pa November 14, 1987, inanena kuti: “Mpingo wa Church of England umadana ndi khalidwe logonana amuna kapena akazi okhaokha, koma sudana nalo kwambiri. Sinodi yaikulu yomwenso imakhala ngati nyumba ya malamulo ya mpingowu, mlungu uno inakambirana za atsogoleri a tchalitchichi amene amagonana amuna okhaokha. Sinodiyi yagwirizana kuti kugonana amuna kapena akazi okhaokha si tchimo ndipo n’kosiyana ndi dama komanso chigololo. Iwo ananena kuti ochita zimenezi ‘amangolephera pang’ono chabe kutsatira mfundo yakuti anthu amene ali m’banja okha ndi amene amayenera kugonana posonyeza kugwirizana ndi kukondana kwawo.’” Posiyanitsa zimene ananena Bishopu Wamkulu wa ku Canterbury ndi mawu osapita m’mbali a mtumwi Paulo opezeka pa Aroma 1:26, 27, magaziniyi inalemba mawu a Paulo pamwamba pa mawu akuti “Paulo Woyera sankaopa kunena maganizo ake.”
Yesu Khristu nayenso sankaopa kunena maganizo ake, ndipo anawanena mosapita m’mbali. Iye ananena kuti “chilango cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako” poyerekezera ndi cha anthu opembedza amene sankafuna kumvetsera uthenga wake. (Mateyu 11:23, 24) Palembali Yesu anagwiritsa ntchito mawu okokomeza pofuna kusonyeza kuti atsogoleri a chipembedzo amenewo, omwe anakana Mwana wa Mulungu ndi zimene ankaphunzitsa, anali ndi mlandu waukulu kuposa anthu a ku Sodomu. Lemba la Yuda 7 limanena kuti anthu a ku Sodomuwo ‘analandira chilango cha moto wosatha,’ kutanthauza chiwonongeko chamuyaya. (Mateyu 25:41, 46) Anthu amene amati ndi atsogoleri achikhristu nawonso adzalandira chiweruzo choopsa. Anthu amenewa ndi atsogoleri akhungu ndipo akusocheretsa nkhosa zawo zakhungu kuti zisamatsatire mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino zokhazikitsidwa ndi Ufumu wa Mulungu. M’malomwake akuziphunzitsa makhalidwe oipa ndi otayirira a m’dzikoli. (Mateyu 15:14) Ponena za chipembedzo chonyenga, kapena kuti Babulo Wamkulu, mngelo wochokera kumwamba akufuula mwamphamvu polengeza uthenga wochenjeza anthu kuti achitepo kanthu mwamsanga. Iye akuti: “Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.”—Chivumbulutso 18:2, 4.
[Zithunzi patsamba 275]
Kumwamba kunamveka mawu akuti Aleluya kanayi konse, potamanda Ya chifukwa chogonjetseratu Babulo Wamkulu