Zinthu Zimene Khristu Adzachita Akabwera
“CHIWAWA KU SÃO PAULO.” Umu ndi mmene magazini yotchedwa Veja inafotokozera masiku anayi a m’mwezi wa May 2006. Panthawi imeneyi, magulu oyambitsa ziwawa anasokoneza zinthu m’mzinda waukulu ndi wolemera wa ku Brazil. Panyengo yonse ya chiwawachi apolisi, akuba ndi anthu wamba pafupifupi 150 anaphedwa.
Nkhani zokhudza chiwawa zikulembedwa kwambiri m’manyuzipepala m’madera ambiri padziko lonse. Olamulira akuoneka kuti alephera kuthetsa chiwawa. Dziko lathu likupitirizabe kukhala loopsa kwambiri kukhalamo. Mwina mwataya mtima chifukwa choti kulikonse komwe mungapite mukumva za uthenga woipa wokhawokha. Komabe, nthawi yoti zinthu zisinthe yayandikira.
Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera Ufumu wa Mulungu ndi kuti chifuniro cha Mulungu chichitike “monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mateyo 6:9, 10) Ufumu umenewu ndi boma limene Khristu Yesu ndiye Mfumu yake yosankhidwa ndi Mulungu. Bomali lidzathetsa mavuto onse a anthu. Koma kuti Ufumu wa Mulungu usinthe zinthu padziko lapansi, ulamuliro wa anthu ufunika kulowedwa m’malo ndi ulamuliro wa Khristu. Izitu n’zimene Khristu adzachita akabwera.
Kodi Kusintha Zinthu Kudzachitika Mwamtendere?
Kodi mayiko adzagonjera ulamuliro wa Khristu mwamtendere? Mtumwi Yohane anaona masomphenya omwe akutipatsa yankho. Yohane anati: “Ndinaona chilombo [magulu andale adziko], mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi [Yesu] wokwera pa kavalo uja ndi gulu lake la nkhondo.” (Chivumbulutso 19:19) Kodi n’chiyani chidzachitikira mafumu adziko pankhondo imeneyi? Ponena za Mfumu yosankhidwa ya Yehova, Baibulo limati ‘idzawathyola ndi ndodo yachitsulo; idzawaphwanya monga mbiya ya woumba.’ (Salmo 2:9) Andale onse adzawaphwanyiratu. Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kutha maufumu [a anthu] onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Nanga bwanji anthu amene amatsutsa Ufumu wa Mulungu? “Pa vumbulutso la Ambuye Yesu, kuchokera kumwamba ndi angelo ake amphamvu m’moto wa lawilawi,” Yesu akuoneka kuti ‘akubwezera chilango kwa osadziwa Mulungu ndi kwa osamvera uthenga wabwino.’ (2 Atesalonika 1:7, 8) Lemba la Miyambo 2:22, limati: “Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”
Ponena za kubwera kwa Khristu, Baibulo limati: “Taonani! Akubwera ndi mitambo, ndipo diso lililonse lidzamuona.” (Chivumbulutso 1:7) Anthu sadzamuona ndi maso awo enieni. Kuchokera nthawi imene Yesu anapita kumwamba anakhala ndi thupi lauzimu. Iye “amakhala m’kuwala kosafikirika, [ndipo] palibe munthu ndi mmodzi yemwe anamuonapo kapena angamuone.”—1 Timoteyo 6:16.
Yesu sakufunikira kukhala ndi thupi laumunthu kuti anthu padziko lapansi amuone. Izi zili monga mmene Yehova sanafunikire kuonekera pamene anakantha Aiguputo ndi Milili Khumi m’masiku a Mose. Anthu panthawiyo sanakayikire kuti Yehova ndi yemwe ankachititsa mililiyo, ndipo iwo sakanachitira mwina koma kuvomereza mphamvu zake. (Eksodo 12:31) Mofananamo, pamene Khristu akadzayamba kugwira ntchito monga Wakupha woikidwa ndi Mulungu, anthu oipa adzakakamizika kuona kapena kuzindikira kuti Mulungu akugwiritsa ntchito Yesu kuwaweruza. Iwo adzadziwa zimenezi chifukwa choti anthu adzakhala atachenjezedwa. Ndithudi, “diso lililonse lidzamuona [Yesu], . . . ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa ndi chisoni chifukwa cha iye.”—Chivumbulutso 1:7.
Kuti padziko lapansi pakhale mtendere ndiponso zinthu ziyambe kuyenda bwino, anthu oipa pamodzi ndi ulamuliro wawo afunikira kuwonongedwa kaye. Khristu adzachita zimenezi. Ndiyeno adzalamulira zinthu zonse padziko lapansi ndipo padzakhala kusintha kwakukulu.
Kubwezeretsa Zinthu Kumene Kudzabweretse Madalitso
Mtumwi Petulo analankhula za “kubwezeretsa zinthu zonse, kumene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera akale.” (Machitidwe 3:21) Kubwezeretsa kumeneku kumaphatikizapo kusintha zinthu komwe kudzachitike padziko lapansi Khristu akamadzalamulira. Mneneri Yesaya yemwe anakhalako zaka za m’ma 700 B.C.E., anali mmodzi mwa aneneri amene Mulungu anawauza za “kubwezeretsa zinthu zonse.” Iye ananeneratu kuti Yesu Khristu, “Kalonga wa Mtendere,” adzabwezeretsa mtendere padziko lapansi. Ponena za ulamuliro wa Khristu, ulosi wa Yesaya umati: “Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.” (Yesaya 9:6, 7) Yesu adzaphunzitsa anthu padziko lapansi kukhala mwamtendere. Anthu omwe adzakhale padziko lapansi ‘adzakondwera nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:11.
Kodi umphawi ndi njala zidzakhalako Khristu akamadzalamulira? Yesaya anati: “Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.” (Yesaya 25:6) Wamasalmo anaimba kuti: “Mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.” (Salmo 72:16) Ndipo ponena za anthu omwe adzakhale padziko lapansi, Baibulo limati: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; pakuti monga masiku amtengo adzakhala masiku a anthu anga; ndi osankhidwa anga adzasangalala nthawi zambiri ndi ntchito za manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.
Yesaya ananeneratu za kutha kwa matenda ndi imfa. Kudzera mwa Yesaya, Mulungu anati: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzayimba.” (Yesaya 35:5, 6) Ndiyeno “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Mulungu ‘adzameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’—Yesaya 25:8.
Nanga bwanji za akufa omwe “ali m’manda a chikumbutso”? (Yohane 5:28, 29) Yesaya analosera kuti: ‘Akufa anu adzakhala ndi moyo . . . adzauka.’ (Yesaya 26:19) Ndithudi, anthu omwe akugona mu imfa adzakhalanso ndi moyo.
“Mulungu Ndiye Mpando Wako Wachifumu kwa Muyaya”
Kubwera kwa Khristu kudzasinthiratu dziko lonse lapansili. Dziko lapansi lidzakhala paradaiso wokongola, ndipo anthu adzagwirizana pakulambira Mulungu woona. Kodi tingatsimikize kuti Yesu Khristu adzachotsadi kuipa padziko lapansi ndi kubweretsa chilungamo?
Taganizirani za yemwe wapereka mphamvu ndi ulamuliro kwa Yesu. Pofotokoza za Mwana, Baibulo limati: “Mulungu ndiye mpando wako wachifumu kwa muyaya ndi muyaya, ndipo ndodo ya ufumu wako ili ndodo ya chilungamo. Unakonda chilungamo, unadana ndi kusamvera malamulo.” (Aheberi 1:8, 9) Mpando wachifumu wa Yesu, kutanthauza udindo kapena ulamuliro wake, n’ngochokera kwa Yehova. Mulungu ndiye anayambitsa ndiponso kupereka ulamuliro umenewu. Palibe mavuto omwe Yesu adzalephere kuwathetsa.
Yesu ataukitsidwa anauza ophunzira ake kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyo 28:18) Lemba la 1 Petulo 3:22, limati: “Angelo ndi maulamuliro ndi mphamvu zinakhala pansi pake.” Palibe mphamvu kapena ulamuliro umene ungapambane polimbana ndi Yesu. Palibe chomwe chingam’letse kubweretsa madalitso osatha kwa anthu.
Mmene Kubwera kwa Khristu Kumakhudzira Anthu
Mu kalata yomwe analembera Atesalonika, mtumwi Paulo anati: “Timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu za chikhulupiriro, ndi ntchito zanu za chikondi. Timateronso pokumbukira chipiriro chimene muli nacho chifukwa cha chiyembekezo chanu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.” (1 Atesalonika 1:3) Paulo anasonyeza kuti tikamayembekezera Yesu Khristu, ntchito zathu zidzabala zipatso ndiponso tidzapirira. Kuyembekeza kumeneku kumatanthauza kukhulupirira kuti Khristu adzabwera ndiponso kuti kubwera kwakeko kudzakonza njira yoti zinthu zisinthe. Chiyembekezo chimenechi chingathandize Akhristu oona kupirirabe ngakhale zinthu zitavuta chotani.
Mwachitsanzo, taganizirani zomwe zinachitikira Carlos, yemwe amakhala ku São Paulo, m’dziko la Brazil. Mu August 2003, Carlos anapezeka ndi matenda a khansa. Kuchokera nthawi imeneyo, iye amuchita maopaleshoni 8 omwe anam’pangitsa kuti azivutikabe kwambiri. Koma iye akupitirizabe kulimbikitsa anthu ena. Mwachitsanzo, polalikira m’msewu wodutsa kutsogolo kwa chipatala chachikulu, anakumana ndi wa Mboni za Yehova wina, yemwe mwamuna mwake ankalandira chithandizo cha mankhwala a khansa. Chifukwa choti Carlos anavutikapo ndi matenda a khansa, anatha kulimbikitsa banjali. Pambuyo pake banjali linanena kuti linalimbikitsidwa kwambiri ndi zomwe anakambirana. Motero, Carlos anaona kuti mawu a Paulo awa n’ngoona: “[Mulungu] amatitonthoza m’masautso athu onse, kuti tikathe kutonthoza amene ali m’masautso a mtundu uliwonse mwa chitonthozo chimene nafenso Mulungu akutitonthoza nacho.”—2 Akorinto 1:4.
Kodi n’chiyani chomwe chimathandiza Carlos kuti akhale ndi mphamvu zolimbikitsa anthu ena ngakhale kuti nayenso akudwala? Chiyembekezo choti Khristu adzabwera ndiponso zonse zimene Khristuyo adzachite zimalimbikitsa Carlos kupitiriza “kuchita zabwino.”—Agalatiya 6:9.
Taganiziraninso za Samuel, yemwe mng’ono wake anaphedwa pafupi ndi nyumba ya bambo awo. Mng’ono wakeyu anaomberedwa zipolopolo 10. Mtembo wake unakhala panjira kwa maola 8 pamene apolisi ankafufuza zachiwembuchi. Samuel samaiwala zomwe zinachitika tsiku limeneli. Koma amalimbikitsidwa ndi chiyembekezo choti Khristu adzathetsa kuipa konse padzikoli ndiponso kuti adzalamulira mwachilungamo ndi kubweretsa madalitso. M’maganizo mwake, Samuel amadziona akukumbatira mng’ono wake ataukitsidwa mu Paradaiso padziko lapansi.—Machitidwe 24:15.
Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?
Chiyembekezo choti Khristu adzabwera ndiponso adzasintha zinthu chidzakulimbikitsani kwambiri. Yesu Khristu adzachotsa zinthu zonse zomwe zimayambitsa mavuto athu ndiponso zoipa zomwe zimatisautsa.
Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mudzalandire madalitso omwe ulamuliro wa Khristu udzabweretse? Phunzirani mwakhama Mawu a Mulungu, Baibulo. Popemphera kwa Atate wake, Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” (Yohane 17:3) Khalani ndi cholinga chofufuza bwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Mboni za Yehova za ku dera lanulo zidzasangalala kukuthandizani pankhani imeneyi. Tikukupemphani mwachikondi kuti mulankhule nazo kapena mulembere kalata ofalitsa magazini ino.
[Zithunzi patsamba 7]
Kubwera kwa Khristu kudzasinthiratu dziko lonse lapansili
[Mawu a Chithunzi]
Inset, background only: Rhino and Lion Park, Gauteng, South Africa