Mutu 40
Mutu wa Njoka Udzaphwanyidwa
Masomphenya 14—Chivumbulutso 20:1-10
Nkhani yake: Satana kuponyedwa kuphompho, Ulamuliro wa Zaka 1,000, kuyesedwa komaliza kwa anthu, ndiponso kuwonongedwa kwa Satana
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuchokera pamapeto pa chisautso chachikulu mpaka pamene Satana adzawonongedwe
1. Kodi ulosi woyambirira wa m’Baibulo wakhala ukukwaniritsidwa motani?
KODI mukukumbukira ulosi woyambirira wa m’Baibulo? Yehova Mulungu ananena ulosi umenewu pamene anauza Njoka kuti: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.” (Genesis 3:15) Tsopano kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu kwatsala pang’ono kufika pachimake. Taona kale zimene Satana wakhala akuchita polimbana ndi mbali ya kumwamba ya gulu la Yehova, yomwe ili ngati mkazi. (Chivumbulutso 12:1, 9) Mbewu ya padziko lapansi ya Njoka, yomwe ikuphatikizapo zipembedzo, anthu a ndale, ndiponso amalonda akuluakulu, yakhala ikuzunza kwambiri mbewu ya mkazi, yomwe ndi Yesu Khristu pamodzi ndi otsatira ake odzozedwa a 144,000 padziko lapansili. (Yohane 8:37, 44; Agalatiya 3:16, 29) Ndipotu Satana anachititsa kuti Yesu aphedwe mwankhanza kwambiri. Koma zimenezi zinangokhala ngati chilonda cha pachidendene chifukwa Mulungu anaukitsa Mwana wake wokhulupirikayu patsiku lachitatu.—Machitidwe 10:38-40.
2. Kodi Njoka idzaphwanyidwa bwanji, ndipo n’chiyani chidzachitikire mbewu yapadziko lapansi ya Njoka?
2 Nanga bwanji za Njoka ndi mbewu yake? Cha m’ma 56 C.E., mtumwi Paulo analemba kalata yaitali yopita kwa Akhristu a ku Roma. Kumapeto kwa kalata yakeyo, iye anawalimbikitsa kuti: “Mulungu amene amapatsa mtendere aphwanya Satana pansi pa mapazi anu posachedwapa.” (Aroma 16:20) Apa Paulo sankatanthauza kuti Satana adzangovulazidwa chabe, koma adzaphwanyidwa. Mawu achigiriki amene iye anagwiritsa ntchito palembali (syn·triʹbo) amatanthauza kuphwanyiratu chinthu mpaka kuchinyenyeratu, kuchipondaponda, kapena kuchiwonongeratu pochiphwanyaphwanya. Ndipotu anthu omwe ndi mbewu ya Njoka akhala akukanthidwa kwambiri ndi miliri m’tsiku la Ambuye ndipo zimenezi zidzafika pachimake pa chisautso chachikulu. Pa nthawiyo, Babulo Wamkulu, maulamuliro a ndale, komanso anthu amalonda pamodzi ndi magulu a asilikali, adzaphwanyidwiratu. (Chivumbulutso chaputala 18 ndi 19) Choncho, Yehova adzathetsa chidani cha pakati pa mbewu ziwirizi. Mbewu ya mkazi wa Mulungu idzapambana pogonjetsa mbewu ya padziko lapansi ya Njoka ndipo mbewu yoipayi sidzakhalaponso.
Satana Adzaponyedwa Kuphompho
3. Kodi Yohane akutiuza kuti n’chiyani chidzachitikire Satana?
3 Nanga n’chiyani chidzachitikire Satana ndi ziwanda zake? Yohane akutiuza kuti: “Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Kenako anagwira chinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000. Ndipo anamuponyera m’phompho ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1,000. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa.”—Chivumbulutso 20:1-3.
4. Kodi mngelo amene ali ndi kiyi wa paphompho ndani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?
4 Kodi mngelo ameneyu ndani? Ayenera kuti ali ndi mphamvu zambiri chifukwa adzatha kuchotsa mdani wamkulu wa Yehova. Komanso iye ali ndi “kiyi wa paphompho ndi unyolo waukulu.” Zimenezi zikutikumbutsa masomphenya ena amene taona m’mbuyomu. Tinaona kuti mfumu ya dzombe ikutchedwanso “mngelo wa phompho.” (Chivumbulutso 9:11) Apa tikuonanso Yesu Khristu amene ali mu ulemerero wake, akupereka chilango kwa Satana. M’pake kuti iye akuchita zimenezi chifukwa amatsogolera pa ntchito yosonyeza kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Mkulu wa angeloyu anachotsa Satana kumwamba, adzaweruza Babulo Wamkulu, ndiponso adzawononga “mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo” pa Aramagedo. Ndipo n’zachidziwikire kuti iye sangasiyire mngelo wina waudindo wocheperapo kuti agwire ntchito yoponya Satana kuphompho, yomwe ndi yofunika kwambiri.—Chivumbulutso 12:7-9; 18:1, 2; 19:11-21.
5. Kodi mngelo wa phompho adzachita chiyani ndi Satana Mdyerekezi, ndipo adzachita zimenezi chifukwa chiyani?
5 Pamene chinjoka chachikulu chofiira chinachotsedwa kumwamba n’kuponyedwa padziko lapansi, chinatchulidwa kuti “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:3, 9) Tsopano pamene chizidzagwidwa kuti chiponyedwe m’phompho, chidzatchulidwanso ndi dzina lake lonse kuti “chinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana.” Satana, yemwe ndi njoka yoopsa, adzamangidwa ndi unyolo n’kuponyedwa “m’phompho.” Iye amafunitsitsa kumeza ndi kunyenga atumiki a Mulungu komanso amakonda kutsutsa Mulungu ndi kumunamizira. Phompholi lidzatsekedwa zolimba “kuti [Satana] asasocheretsenso mitundu ya anthu,” ndipo iye adzakhala m’phomphomo kwa zaka 1,000. Pa nthawi yonseyi, iye sadzatha kusokoneza anthu chifukwa adzangokhala ngati mkaidi amene waponyedwa m’ndende yamdima yapansi. Pamenepa mngelo wa phompho adzakhala atatsekera Satana kuti asasokoneze mwanjira iliyonse Ufumu wa chilungamo, ndipo anthu adzakhala pa mtendere.
6. (a) Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti ziwanda nazonso zidzaponyedwa kuphompho? (b) Zimenezi zikadzachitika, n’chiyani chidzayambe?
6 Nanga n’chiyani chomwe chidzachitike kwa ziwanda? Nazonso ‘azisungira chiweruzo.’ (2 Petulo 2:4) M’Baibulo, Satana amatchedwanso “Belezebule wolamulira wa ziwanda.” (Luka 11:15, 18; Mateyu 10:25) Tikaganizira za nthawi yaitali imene ziwanda zakhala zikugwirizana ndi Satana, m’pomveka kuti nazonso zidzapatsidwe chilango chofanana ndi cha Satana. Ndipo kwa nthawi yaitali, ziwanda zakhala zikuchita mantha zikaganizira za phompho. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yesu anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda, ndipo “ziwandazo zinali kumuchonderera kuti asazilamule kuti zipite kuphompho.” (Luka 8:31) Choncho Satana akamadzaponyedwa kuphompho, n’zachidziwikire kuti angelo ake adzaponyedwa naye limodzi kuphomphoko. (Yerekezerani ndi Yesaya 24:21, 22.) Satana ndi ziwanda zake akadzaponyedwa kuphompho, Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Khristu udzayamba.
7. (a) Kodi chidzachitike n’chiyani kwa Satana ndi ziwanda zake akadzaponyedwa kuphompho, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (b) Kodi Manda ndi ofanana ndi phompho? (Onani mawu a m’munsi.)
7 Kodi Satana ndi ziwanda zake akadzaponyedwa kuphompho, adzakhalabe ndi mphamvu zochita zinthu zosiyanasiyana? Takumbukirani za chilombo chofiira kwambiri cha mitu 7 chimene “chinalipo, tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho.” (Chivumbulutso 17:8) Chilombocho ‘panalibe’ pa nthawi imene chinali kuphompho. Zili choncho chifukwa sichinkatha kugwira ntchito kapena kuchita china chilichonse, moti chinali ngati chakufa. Mofanana ndi zimenezi, mtumwi Paulo ponena za Yesu anati: “‘Kodi ndani adzatsikira kuphompho?’ kuti akaukitse Khristu kwa akufa.” (Aroma 10:7) Pamene anali kuphomphoko, Yesu anali wakufa.a Choncho m’pomveka kunena kuti Satana ndi ziwanda zake adzakhala ngati akufa chifukwa sadzatha kuchita chilichonse kwa zaka 1,000 zimene adzakhale kuphompho. Imeneyi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri kwa anthu okonda chilungamo.
Opambana pa Nkhondo Adzakhala Oweruza kwa Zaka 1,000
8, 9. Kodi tsopano Yohane akutiuza zotani zokhudza anthu amene anawaona atakhala m’mipando yachifumu, ndipo ena mwa anthu amenewo ndi ndani?
8 Zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa kanthawi kochepa. Chifukwa chiyani? Tisanadziwe yankho la funso limeneli, Yohane akutiuza kaye zinthu zina zimene zidzachitike kumayambiriro kwa zaka 1,000 zimenezi. Iye anati: “Kenako ndinaona mipando yachifumu ndi amene anakhalapo. Iwo anapatsidwa mphamvu yoweruza.” (Chivumbulutso 20:4a) Yohane akutiuza kuti anaona anthu omwe anakhala m’mipando yachifumu kumwamba komanso anali ndi mphamvu zolamulira pamodzi ndi Yesu, yemwe ali mu ulemerero wake. Kodi anthu amenewa ndani?
9 Anthu amenewa ndi “oyera” omwe Danieli anawafotokoza kuti akulamulira mu Ufumu wa Mulungu pamodzi ndi winawake “wooneka ngati mwana wa munthu.” (Danieli 7:13, 14, 18) Anthu amenewa ndi akulu 24 omwe aja, amene anakhala pamipando yachifumu kumwamba kuzungulira mpando wachifumu wa Yehova. (Chivumbulutso 4:4) Ena mwa anthu amene ali m’gulu limeneli ndi atumwi 12 a Yesu, amene iye anawalonjeza kuti: “Pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wachifumu waulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.” (Mateyu 19:28) Nayenso Paulo pamodzi ndi Akhristu a ku Korinto amene anakhalabe okhulupirika, ali m’gulu limeneli. (1 Akorinto 4:8; 6:2, 3) Enanso amene ali m’gululi ndi Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya omwe anapambana pa nkhondo.—Chivumbulutso 3:21.
10. (a) Kodi tsopano Yohane anawafotokoza bwanji mafumu okwana 144,000? (b) Tikatengera zimene Yohane anatiuza m’mbuyomu, kodi ena mwa mafumu 144,000 amenewo ndani?
10 Opambana pa nkhondo odzozedwawa awakonzera mipando yachifumu yokwana 144,000. “Iwowa anagulidwa kuchokera mwa anthu, monga zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 14:1, 4) Yohane akupitiriza kutiuza kuti: “Ndiyeno ndinaona miyoyo ya amene anaphedwa ndi nkhwangwa chifukwa cha kuchitira umboni za Yesu, ndi kulankhula za Mulungu. Ndinaonanso anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake, ndipo sanalandire chizindikiro pamphumi pawo ndi padzanja pawo.” (Chivumbulutso 20:4b) Choncho ena mwa mafumu amenewo ndi Akhristu odzozedwa amene anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, ndipo m’mbuyomu pamene mngelo ankamatula chidindo chachisanu, iwo anafunsa Yehova kuti adzadikira mpaka liti iye asanapereke chilango kwa adani amene anakhetsa magazi awo. Pa nthawi imeneyo, iwo anapatsidwa mkanjo woyera ndipo anauzidwa kuti ayembekezere kwa kanthawi pang’ono. Koma posachedwapa Mulungu abwezera adani amene anakhetsa magazi a oyerawo. Iye adzachita zimenezi powononga Babulo Wamkulu, komanso pogwiritsa ntchito Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye kuti awononge mitundu yonse ya anthu, ndi kuponya Satana kuphompho.—Chivumbulutso 6:9-11; 17:16; 19:15, 16.
11. (a) Kodi mawu akuti “anaphedwa ndi nkhwangwa” akutanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti a 144,000 onse amafa imfa ya nsembe?
11 Kodi anthu onse a 144,000 omwe ndi oweruza komanso mafumu “anaphedwa ndi nkhwangwa”? Zikuoneka kuti ndi ochepa okha amene anachitadi kuphedwa ndi nkhwangwa. Choncho zikuoneka kuti mawu amenewa akuimira Akhristu onse odzozedwa amene anapirira mpaka kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo.b (Mateyu 10:22, 28) Sitikukayikira kuti Satana akanakonda kuti odzozedwa onse aphedwe ndi nkhwangwa, koma si abale onse odzozedwa a Yesu amene amachita kuphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ambiri mwa iwo amamwalira chifukwa cha matenda kapena ukalamba. Komabe, odzozedwa amenewa nawonso ali m’gulu limene Yohane anaonali, ndipo tinganene kuti onsewa imfa yawo imakhala yansembe. (Aroma 6:3-5) Kuwonjezera pamenepo, aliyense wa iwo sakhala mbali ya dziko. Choncho onse amadedwa ndi dziko ndipo tinganene kuti dzikoli limawaona kuti ndi akufa. (Yohane 15:19; 1 Akorinto 4:13) Palibe ngakhale mmodzi mwa anthu amenewa amene amalambira chilombo kapena chifaniziro chake, ndipo pomwalira, aliyense wa iwo amakhala alibe chidindo cha chilombo. Onsewa amamwalira atapambana pa nkhondo.—1 Yohane 5:4; Chivumbulutso 2:7; 3:12; 12:11.
12. Kodi Yohane ananena chiyani za mafumu okwana 144,000, ndipo iwo anayamba liti kuukitsidwa?
12 Tsopano Yohane anaona opambana pa nkhondo amenewa alinso ndi moyo. Iye anati: “Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:4c) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti oweruza amenewa sadzaukitsidwa mpaka mitundu ya anthu idzawonongedwe komanso Satana ndi ziwanda zake adzaponyedwe kuphompho? Ayi si choncho. Ambiri a iwo anaukitsidwa kale, ndipo pa Aramagedo iwo limodzi ndi Yesu adzakwera pamahatchi n’kupita kukawononga mitundu ya anthu. (Chivumbulutso 2:26, 27; 19:14) Paulo nayenso anasonyeza kuti anthu amenewa anayamba kuukitsidwa nthawi ya kukhalapo kwa Yesu itangoyamba kumene mu 1914, komanso anasonyeza kuti ena anaukitsidwa moyambirira poyerekezera ndi ena. (1 Akorinto 15:51-54; 1 Atesalonika 4:15-17) Choncho, kuukitsidwa kwa anthu a m’gulu limeneli kwakhala kukuchitika kwa nthawi yaitali pamene aliyense wa iwo wakhala akukalandira payekha kumwamba mphatso ya moyo umene sungafe.—2 Atesalonika 1:7; 2 Petulo 3:11-14.
13. (a) Kodi zaka 1,000 zimene a 144,000 adzakhale akulamulira ndi nthawi yaitali bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani tikutero? (b) Kodi Papias wa ku Herapoli ankaona kuti zaka 1,000 ndi nthawi yaitali bwanji? (Onani mawu a m’munsi.)
13 Mafumu amenewa adzalamulira ndi kuweruza anthu kwa zaka 1,000. Kodi zaka 1,000 zimenezi ndi zenizeni kapena ndi nthawi yaitali yophiphiritsa yomwe sikudziwika bwinobwino kutalika kwake? Mawu akuti “masauzande” angatanthauze chiwerengero chachikulu chimene sichikudziwika, monga momwe zilili pa 1 Samueli 21:11. Koma m’chaputala 20 cha buku la Chivumbulutso, chiwerengero cha “1,000” ndi chenicheni osati chophiphiritsa, ndipo chatchulidwa maulendo atatu pa Chivumbulutso 20:5-7 pamene akunena za “zaka 1,000.” Paulo ananena kuti nthawi yachiweruzo imeneyi ndi “tsiku,” pamene ananena kuti: “[Mulungu] wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu.” (Machitidwe 17:31) Popeza kuti Petulo ananena kuti kwa Yehova tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, n’zosadabwitsa kuti tsiku lopereka chiweruzo limeneli ndi la zaka 1,000 zenizeni.c—2 Petulo 3:8.
Akufa Enawo
14. (a) Kodi Yohane anawonjezera mawu oti chiyani okhudza “akufa enawo”? (b) Kodi zimene mtumwi Paulo ananena zikutithandiza bwanji kumvetsa mawu akuti ‘kukhalanso ndi moyo’?
14 Koma kodi mafumu amenewa adzaweruza ndani ngati, malinga ndi zimene mtumwi Yohane ananena, “(akufa enawo sanakhalenso ndi moyo kufikira zitatha zaka 1,000)”? (Chivumbulutso 20:5a) Apanso tiyenera kuona tanthauzo la mawu akuti ‘kukhalanso ndi moyo’ malinga ndi nkhani yake. Mawu amenewa angakhale ndi matanthauzo osiyanasiyana m’nkhani zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ponena za Akhristu anzake odzozedwa, Paulo anati: “Mulungu anapangitsa inuyo kukhala amoyo pamene munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu.” (Aefeso 2:1) Zoonadi, ngakhale m’nthawi ya atumwi, Mulungu anapangitsa Akhristu odzozedwa ndi mzimu “kukhala amoyo,” ndipo ankawaona kuti ndi olungama chifukwa chokhulupirira nsembe ya Yesu.—Aroma 3:23, 24.
15. (a) Kodi Mulungu ankaona bwanji mboni za Yehova zimene zinakhalapo mpingo wachikhristu usanayambe? (b) Kodi a nkhosa zina ‘adzakhalanso ndi moyo’ m’njira yotani, ndipo ndi liti pamene adzalandiredi dziko lapansi?
15 Mofanana ndi zimenezi, mboni za Yehova zimene zinakhalapo mpingo wachikhristu usanayambe zinkaonedwa kuti ndi zolungama ndiponso zinali mabwenzi a Mulungu. Choncho Baibulo limanena kuti Abulahamu, Isaki ndi Yakobo anali “amoyo” ngakhale kuti iwo anali atamwalira. (Mateyu 22:31, 32; Yakobo 2:21, 23) Komabe, anthu amenewa pamodzi ndi ena onse amene adzaukitsidwe, adzafunika kusintha pang’onopang’ono n’kukhala angwiro. Komanso okhulupirika onse a khamu lalikulu la nkhosa zina amene adzapulumuke pa Aramagedo n’kulowa m’dziko latsopano, pamodzi ndi ana awo amene adzabadwe m’dziko latsopanolo, nawonso adzafunika kusintha n’kukhala angwiro. Yesu Khristu pamodzi ndi mafumu komanso ansembe amene azidzalamulira naye limodzi pa Tsiku la Chiweruzo la zaka 1,000, ndi amene adzathandize anthuwa kusintha n’kukhala angwiro pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Yesuyo. Pamene Tsiku limeneli lizidzatha, “akufa enawo” ‘adzakhalanso ndi moyo,’ kutanthauza kuti adzakhala anthu angwiro. Kutsogoloku, tiona kuti anthu amenewa adzayesedwa komaliza, koma poyesedwapo adzakhala ali anthu angwiro. Akadzapambana mayesero amenewo, Mulungu adzawaona kuti ndi oyenera kukhala ndi moyo wosatha, ndipo adzakhala anthu olungamadi. Lonjezo lonse lakuti, “olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya,” lidzakwaniritsidwa kwa iwo. (Salimo 37:29) Zoonadi, anthu omvera akuyembekezera zinthu zosangalatsa m’tsogolomu.
Kuuka Koyamba kwa Akufa
16. Kodi Yohane anafotokoza bwanji kuuka kwa akufa kwa anthu amene adzalamulire monga mafumu limodzi ndi Khristu, ndipo n’chifukwa chiyani ananena zimenezo?
16 Ponena za amene “anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu,” Yohane analemba kuti: “Uku ndi kuuka koyamba kwa akufa.” (Chivumbulutso 20:5b) N’chifukwa chiyani kuuka kumeneku kuli koyamba? Kumeneku ndi “kuuka koyamba kwa akufa” tikatengera pa nthawi, chifukwa chakuti oukitsidwawo ndi “zipatso zoyambirira zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 14:4) Komanso kuuka kumeneko n’koyamba tikaona kufunika kwake, chifukwa oukitsidwawo adzalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wa kumwamba ndiponso adzaweruza anthu a mitundu yonse. Pomaliza, kuukaku kukutchedwanso koyamba chifukwa cha moyo umene anthu oukitsidwawo amalandira. Kupatulapo Yesu Khristu yekha, oukitsidwa pa kuuka koyambaku ndi okhawo amene Baibulo limanena kuti amapatsidwa moyo umene sungafe.—1 Akorinto 15:53; 1 Timoteyo 6:16.
17. (a) Kodi Yohane anafotokoza bwanji madalitso amene Akhristu odzozedwa akuyembekezera? (b) Kodi “imfa yachiwiri” n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani “ilibe ulamuliro” pa opambana pa nkhondo a 144,000?
17 Akhristu odzozedwawa akuyembekezeradi kudzalandira madalitso ochuluka. Yohane ananena kuti: “Wodala ndi woyera ndiye aliyense wouka nawo pa kuuka koyamba. Pa iwo, imfa yachiwiri ilibe ulamuliro.” (Chivumbulutso 20:6a) Mogwirizana ndi zimene Yesu analonjeza Akhristu a ku Simuna, Akhristu opambana pa nkhondo amene ‘adzauke nawo pa kuuka koyamba’ sadzakhudzidwa ndi “imfa yachiwiri,” imene ikuimira kuwonongedwa popanda chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. (Chivumbulutso 2:11; 20:14) Imfa yachiwiri “ilibe ulamuliro” pa opambana pa nkhondowo chifukwa chakuti adzavala matupi osawonongeka komanso adzakhala ndi moyo umene sungafe.—1 Akorinto 15:53.
18. Kodi Yohane ananena chiyani za olamulira atsopano adziko lapansi, ndipo olamulirawa adzachita chiyani?
18 Ulamuliro wa mafumu amenewa udzakhala wosiyana kwambiri ndi ulamuliro wa mafumu a padziko lapansi pa nthawi ya ulamuliro wa Satana ino. Mafumu a padziko lapansiwa akati alamulira kwa nthawi yaitali amangolamulira zaka 50 kapena 60 zokha, ndipo ambiri a iwo amangolamulira zaka zochepa chabe. Ambiri mwa mafumuwa amazunza kwambiri anthu. Ndipo n’zosatheka kuti anthu apindule kwamuyaya ndi maulamuliro amene amangosinthasintha komanso mfundo zawo zimene zimangosinthasintha. Mosiyana ndi olamulira amenewa, Yohane ananena za olamulira atsopano adziko lapansi kuti: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.” (Chivumbulutso 20:6b) Yesu pamodzi ndi olamulira amenewa adzapanga boma limene lidzalamulire kwa zaka 1,000, ndipo pa nthawiyi sipadzakhalanso boma lina. Iwo adzakhala ansembe ndipo adzathandiza anthu omvera kuti akhale angwiro mwauzimu, akhale ndi makhalidwe angwiro komanso kuti akhale ndi matupi angwiro. Iwo adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito nsembe yangwiro imene Yesu anapereka. Ulamuliro wawo monga mafumu udzathandiza kuti anthu padziko lonse akhale olungama komanso oyera potengera Yehova. Ntchito imene iwo limodzi ndi Yesu adzagwire kwa zaka 1,000 monga oweruza, idzathandiza kwambiri anthu omvera kuti pamapeto pake adzathe kukhala ndi moyo wosatha.—Yohane 3:16.
Mayesero Omaliza
19. Kodi Ulamuliro wa Zaka 1,000 ukamadzafika kumapeto, dziko lapansi lidzakhala lili bwanji, nanga anthu adzakhala ali otani, ndipo pa nthawiyi Yesu adzachita chiyani?
19 Ulamuliro wa Zaka 1,000 ukamadzafika kumapeto, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso weniweni mofanana ndi munda woyambirira wa Edeni uja. Sipadzafunikanso kuti anthu angwiro akhale ndi mkulu wa ansembe woti aziwalankhulira kwa Mulungu, chifukwa chakuti uchimo umene tinatengera kwa Adamu udzakhala utachotsedwa ndipo imfa, yomwe ndi mdani womaliza, kudzakhala kulibe. Pamenepa Ufumu wa Khristu udzakhala utakwaniritsa cholinga cha Mulungu choti dziko lonse lapansi likhale ndi boma limodzi. Pa nthawiyi, Yesu “adzapereka ufumu kwa Mulungu wake ndi Atate wake.”—1 Akorinto 15:22-26; Aroma 15:12.
20. Kodi Yohane akutiuza kuti chidzachitike n’chiyani ikadzafika nthawi ya mayesero omaliza?
20 Kenako nthawi ya mayesero omaliza idzafika. Popeza kuti anthu padziko lonse adzakhala angwiro, kodi iwo adzapitiriza kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, mosiyana ndi anthu oyambirira amene anali m’munda wa Edeni? Yohane akutiuza zimene zidzachitike, kuti: “Tsopano zikadzangotha zaka 1,000, Satana adzamasulidwa m’ndende yake, ndipo adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi, ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kunkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa kunyanja. Iwo adzayenda n’kufalikira mpaka kumbali zonse za dziko lapansi, kenako adzazungulira msasa wa oyera, ndi mzinda wokondedwa.”—Chivumbulutso 20:7-9a.
21. Kodi Satana adzachita chiyani poyesa komaliza kunyenga anthu, ndipo n’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti anthu ena adzam’tsatira ngakhale pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000?
21 Kodi zinthu zidzatha bwanji Satana akadzayamba kunyenga anthu komaliza? Iye adzanyenga “mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi,” ndipo adzaitsogolera “kunkhondo.” Kodi padzapezeka aliyense wokhala kumbali ya Satana pambuyo pa zaka 1,000 za ulamuliro wa Mulungu, womwe udzakhale wosangalatsa komanso wabwino kwambiri? Musaiwale kuti Satana anatha kusocheretsa anthu angwiro, Adamu ndi Hava, pamene iwo ankasangalala ndi moyo m’Paradaiso m’munda wa Edeni. Iye anathanso kusocheretsa angelo akumwamba, ngakhale kuti iwo anaona zotsatira zoipa za kugalukira Mulungu kumene kunachitika m’munda wa Edeni. (2 Petulo 2:4; Yuda 6) Choncho, tisadabwe ndi mfundo yakuti anthu ena angwiro adzanyengedwa n’kuyamba kutsatira Satana ngakhale pambuyo pa zaka 1,000 za ulamuliro wosangalatsa wa Ufumu wa Mulungu.
22. (a) Kodi mawu akuti “mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi” akutanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani anthu opanduka akutchedwa “Gogi ndi Magogi”?
22 Baibulo limanena kuti anthu opandukawa ndi “mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi.” Zimenezi sizikutanthauza kuti anthu adzakhala atagawikananso n’kukhala mayiko osiyanasiyana odzilamulira okha. Koma zikungosonyeza kuti anthuwo adzadzilekanitsa ndi anthu olungama ndiponso okhulupirika a Yehova, ndipo adzasonyeza mtima woipa umene mitundu ya anthu ikusonyeza masiku ano. Iwo ‘adzaganiza zochita chiwembu choipa kwambiri,’ ngati mmene anachitira Gogi wa ku Magogi wotchulidwa mu ulosi wa Ezekieli. Cholinga chawo chidzakhala kuthetsa ulamuliro wa boma la Mulungu padziko lapansi. (Ezekieli 38:3, 10-12) N’chifukwa chake iwo akutchedwa “Gogi ndi Magogi.”
23. Kodi mfundo yakuti anthu amene adzapandukire Mulungu adzakhala ochuluka “ngati mchenga wa kunyanja” ikusonyeza chiyani?
23 Anthu amene adzagwirizane ndi Satana popandukira Mulungu adzakhala ochuluka “ngati mchenga wa kunyanja.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti adzakhala anthu angati? Chiwerengero chawo si chodziwikiratu. (Yerekezerani ndi Yoswa 11:4; Oweruza 7:12.) Chiwerengero cha anthu amenewa chidzadalira zimene munthu aliyense payekha adzachite, Satana akadzayamba kunyenga anthu. Koma mosakayikira anthu amenewa adzakhala ambiri ndithu, chifukwa adzakhulupirira ndi mtima wonse kuti akhoza kugonjetsa “msasa wa oyera, ndi mzinda wokondedwa.”
24. (a) Kodi “mzinda wokondedwa” n’chiyani, ndipo udzazunguliridwa bwanji? (b) Kodi “msasa wa oyera” ukuimira chiyani?
24 “Mzinda wokondedwa” umenewu uyenera kuti ndi mzinda umene Yesu Khristu amene ali mu ulemerero wake, anautchula polankhula ndi otsatira ake pa Chivumbulutso 3:12. Iye anautchula kuti “mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano, wotsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga.” Popeza kuti mzindawu ukuimira gulu lakumwamba, kodi gulu la anthu oukira apadziko lapansiwo ‘adzauzungulira’ bwanji? Iwo adzachita zimenezi pozungulira “msasa wa oyera.” Popeza msasa umakhala kunja kwa mzinda, ndiye kuti “msasa wa oyera” uyenera kuti ukuimira anthu okhulupirika amene ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova padziko lapansi, komwe ndi kunja kwa Yerusalemu Watsopano, yemwe ali kumwamba. Satana ndi anthu ake ogalukirawo akadzaukira anthu okhulupirika, Ambuye Yesu adzaona kuti akuukira Ambuyewo. (Mateyu 25:40, 45) “Mitundu ya anthu” imeneyo idzafunitsitsa kuchotseratu zonse zimene Yerusalemu Watsopano wakumwamba adzakhale atachita posintha dziko lapansili kuti likhale paradaiso. Choncho poukira “msasa wa oyera,” iwo adzakhalanso akuukira “mzinda wokondedwa.”
Nyanja Yamoto ndi Sulufule
25. Kodi Yohane anati ogalukira aja akadzaukira “msasa wa oyera” zotsatira zake zidzakhala zotani, ndipo zimenezi zidzatanthauza chiyani kwa Satana?
25 Kodi Satana adzapambana pa kuukira kwake komalizaku? Ayi sadzapambana. Iye adzalephera mofanana ndi mmene adzalepherere Gogi wa ku Magogi akadzaukira Isiraeli wauzimu m’nthawi yathu ino. (Ezekieli 38:18-23) Yohane anafotokoza momveka bwino zimene zidzachitike. Iye anati: “Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba ndi kuwapsereza. Mdyerekezi, amene anali kuwasocheretsa, adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilombo ndi mneneri wonyenga uja.” (Chivumbulutso 20:9b-10a) M’malo mongoponyedwa kuphompho, pa nthawiyi Satana, yemwe ndi njoka yakale ija, adzaphwanyidwa ndi kuwonongedweratu moti sadzakhalaponso ndipo zidzangokhala ngati wawonongedwa ndi moto.
26. N’chifukwa chiyani ‘nyanja yamoto ndi sulufule’ singakhale malo enieni ozunzirako anthu?
26 Taona kale kuti ‘nyanja yamoto ndi sulufule’ singakhale nyanja yeniyeni kumene anthu amakazunzika. (Chivumbulutso 19:20) Kuti Satana azunzike koopsa m’nyanja imeneyi kwamuyaya, Yehova angafunike kuti amusungebe ndi moyo. Komatu moyo ndi mphatso, osati chilango. Imfa ndiye chilango cha uchimo, ndipo malinga ndi zimene Baibulo limanena, akufa sangamve kupweteka. (Aroma 6:23; Mlaliki 9:5, 10) Komanso tiona kutsogoloku m’buku la Chivumbulutso kuti imfa komanso Manda zidzaponyedwa m’nyanja yomweyi yamoto ndi sulufule. Ndipo n’zodziwikiratu kuti imfa ndi Manda sizingamve kupweteka.—Chivumbulutso 20:14.
27. Kodi zimene zinachitikira mizinda ya Sodomu ndi Gomora zikutithandiza bwanji kumvetsa mawu akuti ‘nyanja yamoto ndi sulufule’?
27 Zonsezi zikutsimikizira mfundo yakuti nyanja yamoto ndi sulufule ndi yophiphiritsa. Komanso, moto ndi sulufule zomwe zatchulidwazi zikutikumbutsa zimene zinachitikira mizinda yakale ya Sodomu ndi Gomora, imene Mulungu anaiwononga chifukwa cha zinthu zoipa kwambiri zimene anthu akumeneko ankachita. Nthawi itakwana, “Yehova anavumbitsa sulufule ndi moto kuchokera kwa Yehova kumwamba, kuvumbira pa Sodomu ndi Gomora.” (Genesis 19:24) Zimene zinachitikira mizinda iwiriyi zimatchedwa “chilango cha moto wosatha.” (Yuda 7) Komatu mizinda iwiriyi sinazunzike kwamuyaya. M’malomwake, inafafanizidwiratu pamodzi ndi anthu ake oipawo, ndipo sinamangidwenso mpaka lero. Panopa mizinda imeneyi kulibenso, ndipo palibe amene anganene motsimikiza malo amene inali.
28. Kodi nyanja yamoto ndi sulufule n’chiyani, ndipo ikusiyana bwanji ndi imfa, Manda ndi phompho?
28 Mogwirizana ndi zimenezi, Baibulo limafotokoza lokha tanthauzo la nyanja yamoto ndi sulufule, kuti: “Nyanja yamoto imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 20:14) N’zoonekeratu kuti nyanja imeneyi n’chimodzimodzi ndi Gehena amene Yesu ananena, yemwe ndi malo kumene anthu oipa amawonongedwa, osati kuzunzidwa kwamuyaya. (Mateyu 10:28) Choncho nyanjayi ikuimira chiwonongeko chotheratu chopanda chiyembekezo chakuti owonongedwawo adzaukitsidwa. Ndipotu Baibulo limanena kuti pali makiyi a imfa, Manda ndi phompho, koma silitchula za makiyi otsegulira nyanja yamoto ndi sulufule. (Chivumbulutso 1:18; 20:1) Izi zikutanthauza kuti nyanjayi sidzatulutsa aliyense amene ali mmenemo.—Yerekezerani ndi Maliko 9:43-47.
Adzazunzidwa Usana ndi Usiku Kwamuyaya
29, 30. Kodi Yohane ananena chiyani zokhudza Mdyerekezi komanso chilombo ndi mneneri wonyenga, ndipo zimenezi zikutanthauza chiyani?
29 Pofotokoza zimene zidzachitikire Mdyerekezi, chilombo, komanso mneneri wonyenga, tsopano Yohane akutiuza kuti: “Ndipo iwo adzazunzidwa usana ndi usiku kwamuyaya.” (Chivumbulutso 20:10b) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Monga tanenera kale, sitinganene kuti zinthu zophiphiritsa, monga chilombo, mneneri wonyenga, komanso imfa ndi Manda, zingazunzikedi. Choncho, palibe chifukwa chokhulupirira kuti Satana adzazunzika kwamuyaya, chifukwa iye adzawonongedwa.
30 Mawu achigiriki (ba·sa·niʹzo) amene palembali anawamasulira kuti “adzazunzidwa” amatanthauza “kuyesa (zitsulo) pogwiritsa ntchito mwala woyesera.” Tanthauzo lachiwiri ndi “kufunsa munthu mafunso kwinaku akumuzunza.” (The New Thayer’s Greek-English Lexicon of the New Testament) Popeza mawu achigiriki amenewa agwiritsidwa ntchito palembali, zikusonyeza kuti zimene zidzachitikire Satana zidzakhala umboni wotsimikizira kwamuyaya kuti Yehova ndi woyenera kulamulira ndipo ulamuliro wakewo ndi wolungama. Nkhani imeneyi yokhudza ulamuliro idzakhala itathetsedwa mpaka kalekale. Ngati wina atadzatsutsanso mfundo yakuti Yehova ndiye woyenera kulamulira, sipadzafunikanso kuti padutse nthawi yaitali kuti Yehovayo asonyeze kuti wotsutsayo ndi wolakwa.—Yerekezerani ndi Salimo 92:1, 15.
31. Kodi mawu awiri achigiriki ofanana ndi mawu ena amene amatanthauza ‘kuzunza’ angatithandize bwanji kumvetsa chilango chimene Satana Mdyerekezi adzalandire?
31 Kuwonjezera pamenepo, mawu enanso achigiriki ofanana ndi amenewa, (ba·sa·ni·stesʹ) amene amatanthauza ‘wozunza,’ m’Baibulo anawamasuliranso kuti ‘woyang’anira ndende.’ (Mateyu 18:34, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Mogwirizana ndi zimenezi, Satana adzaponyedwa m’nyanja yamoto ndipo adzakhala ngati amutsekera m’ndende yomwe sadzatulutsidwamo, koma adzakhala mmenemo kwamuyaya. Komanso, Baibulo lachigiriki la Septuagint, limene Yohane ankalidziwa bwino kwambiri, linagwiritsa ntchito mawu ena ofanana ndi amenewa (baʹsa·nos) ponena za kuzunzika mochititsa manyazi mpaka kufa. (Ezekieli 32:24, 30) Zimenezi zikutithandiza kuona kuti chilango chimene Satana adzalandire chidzakhala imfa yochititsa manyazi komanso yopanda chiyembekezo chilichonse, m’nyanja yamoto ndi sulufule. Ndipo ntchito zake zidzapita naye limodzi.—1 Yohane 3:8.
32. Kodi ziwanda zidzalandira chilango chotani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?
32 Koma ziwanda sizikutchulidwa palembali. Kodi zidzamasulidwa limodzi ndi Satana pambuyo pa zaka 1,000 ndiyeno kenako n’kupatsidwa chilango cha imfa yopanda chiyembekezo chilichonse pamodzi ndi Satanayo? Umboni ukusonyeza kuti zidzakhaladi choncho. Mwachitsanzo, m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu ananena kuti mbuzi zidzapita “kumoto wosatha wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake.” (Mateyu 25:41) Mawu akuti “kumoto wosatha” ayenera kuti akutanthauza nyanja yamoto ndi sulufule, mmene Satana adzaponyedwe. Pajatu angelo a Mdyerekezi anathamangitsidwa kumwamba n’kuponyedwa kudziko lapansi limodzi ndi Mdyerekeziyo. Ndipo zikuoneka kuti kumayambiriro kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000, iwo adzaponyedwa kuphompho limodzi ndi Mdyerekezi. Choncho m’pomvekanso kunena kuti angelo amenewa adzawonongedwa limodzi ndi Mdyerekezi m’nyanja yamoto ndi sulufule.—Mateyu 8:29.
33. Kodi ulosi wa pa Genesis 3:15 udzakwaniritsidwa bwanji wonse, ndipo tsopano mzimu wa Yehova unathandiza Yohane kulemba nkhani yofunika kwambiri iti?
33 Zimenezi zikadzachitika, ndiye kuti ulosi wonse wa pa Genesis 3:15 udzakhala utakwaniritsidwa. Satana akadzaponyedwa m’nyanja yamoto, adzafa ngati njoka imene mutu wake wanyenyedwa ndi chidendene chachitsulo. Ndipo iye ndi ziwanda zake sadzakhalaponso. Choncho buku la Chivumbulutso silikutchulanso Mdyerekezi ndi ziwanda zake. Pambuyo poti ulosiwu wasonyeza kuti Mdyerekezi ndi ziwanda zake adzawonongedwa, tsopano mzimu wa Yehova unathandiza Yohane kulemba nkhani yofunika kwambiri kwa anthu amene akuyembekezera kudzakhala m’dziko lapansi latsopano. Nkhani yake ndi yokhudza funso lakuti, kodi ulamuliro wakumwamba wa “Mfumu ya mafumu,” ndi “oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika,” udzachitira anthu chiyani? (Chivumbulutso 17:14) Poyankha funso limeneli, Yohane akubwerera m’mbuyo n’kutifotokozera zimene zidzachitike kuchiyambi kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000.
[Mawu a M’munsi]
a Malemba ena amanena kuti Yesu anali m’Manda pa nthawi imene anali wakufa. (Machitidwe 2:31) Komabe tisaganize kuti nthawi zonse tanthauzo la mawu akuti Manda limafanana ndi tanthauzo la mawu akuti phompho. Baibulo limatiuza kuti Satana komanso chilombo adzaponyedwa kuphompho. Koma limasonyeza kuti amene amapita ku Manda ndi anthu okha ndipo amagona mu imfa, kuyembekezera kudzaukitsidwa.—Yobu 14:13; Chivumbulutso 20:13.
b Zikuoneka kuti nkhwangwa (Chigiriki peʹle·kus) ndi chida chimene chinkagwiritsidwa ntchito popha munthu ku Roma, ngakhale kuti pofika m’nthawi ya Yohane anthu ankagwiritsa ntchito kwambiri lupanga. (Machitidwe 12:2) Choncho mawu achigiriki (pe·pe·le·kis·meʹnon) amene palembali anawamasulira kuti “anaphedwa ndi nkhwangwa” akungotanthauza “kuphedwa.”
c Anthu amakhulupirira kuti Papias wa ku Herapoli, anaphunzitsidwa mfundo zina za m’Baibulo ndi ophunzira a Yohane, yemwe analemba buku la Chivumbulutso. N’zochititsa chidwi kuti Eusebius, wolemba mbiri yakale wa m’zaka za m’ma 300 C.E., ananena kuti Papias ankakhulupirira kuti Khristu adzalamulira kwa zaka 1,000 zenizeni (ngakhale kuti Eusebius ankamutsutsa kwambiri pa mfundo imeneyi).—The History of the Church, Eusebius, III, 39.
[Chithunzi patsamba 293]
Nyanja Yakufa. N’kutheka kuti mizinda ya Sodomu ndi Gomora inali kumeneku
[Zithunzi patsamba 294]
“Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene”