-
Kodi Tsiku la Chiweruzo N’chiyani?Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
-
-
APa Chivumbulutso 20:11, 12, timawerenga mawu amene mtumwi Yohane analemba ofotokoza za Tsiku la Chiweruzo, akuti: “Ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera, ndi amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake, ndipo malo a zimenezi sanapezekenso. Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inafunyululidwa. Koma mpukutu wina unafunyululidwa, ndiwo mpukutu wa moyo. Ndipo akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.” Kodi amene adzagwire ntchito yoweruzayi ndi ndani?
-
-
Kodi Tsiku la Chiweruzo N’chiyani?Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
-
-
Mu zaka 1,000 zimenezi, Yesu Khristu ‘adzaweruza amoyo ndi akufa.’ (2 Timoteyo 4:1) “Amoyo” akuimira “khamu lalikulu la anthu” amene adzapulumuke pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 7:9-17) Koma mtumwi Yohane anaonanso “akufa . . . ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo” kuti aweruzidwe. Mogwirizana ndi zimene Yesu analonjeza, “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [a Khristu] ndipo adzatuluka,” kapena kuti adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Koma kodi azidzayang’ana chiyani poweruza anthuwa?
Malinga ndi masomphenya amene Yohane anaona, “mipukutu inafunyululidwa” ndipo “akufa anaweruzidwa malinga ndi zolembedwa m’mipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.” (Chivumbulutso 20:12) Kodi m’mipukutuyi munalembedwa zimene anthuwo ankachita asanamwalire? Ayi, anthuwa sadzaweruzidwa potengera zimene ankachita asanamwalire. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Chifukwa Baibulo limanena kuti: “Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu amene adzaukitsidwe adzakhala atakhululukidwa machimo awo onse. Ndiye kuti zimene zalembedwa m’mipukutuyi zikuimira malangizo amene Mulungu adzapereke pa nthawiyo. Kuti akhale ndi moyo kwamuyaya, anthu amene adzapulumuke Aramagedo ndiponso amene adzaukitsidwe, adzayenera kutsatira malamulo a Mulungu, kuphatikizapo malamulo atsopano amene Yehova adzapereke m’zaka 1,000 zimenezi. Choncho, anthu adzaweruzidwa potengera zimene azidzachita mkati mwa Tsiku la Chiweruzo.
-