Chimveni Chowonadi Chonse!
“SINDINALIWONEPO konse dzinalo m’Baibulo langa,” anatero Francisco. Dzina lakuti Yehova linali litangotchulidwa m’kukambitsirana ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Zowona, iye sakanatha kuwona dzina la Mulungulo m’Baibulo lake, kope la mu 1969 la Portuguese Almeida. Dzina lakuti Yehova mulibemo mmenemo. Monga Mkatolika wa ku Brazil, Francisco amapezeka pa Misa mokhazikika pa Sande ndipo amasangalala kuŵerenga Baibulo kunyumba. Koma dzina lakuti Yehova linamuzizwitsa.
Kodi Mulungu Ndani?
Mlungu wotsatira, Mboniyo inabweretsa kope lina la Almeida. Iwo anayerekeza makope aŵiriwo pa Salmo 83:18. Ndipo kodi iwo anapezanji? Mwawonatu, m’kope la 1966 limeneli, lembali limaŵerengedwa motere: “Inuyo, inu nokha amene dzina lakuti YEHOVA nlanu, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi”! Komabe, m’kope la 1969, m’malo mwakuti “YEHOVA” liwu lakuti “AMBUYE” lagwiritsiridwa ntchito. “Simwawona nanga, anasintha chinachake pano,” inatero Mboniyo, ndiyeno inafunsa kuti: “Kunena zowona liwu lakuti ‘Ambuye’ sidzina, kodi sichoncho?” “Inde,” anatero Francisco. Mokwiya pang’ono, iye anawonjezera kuti: “Kodi iwo anachitiranji chimenechi?”
Ichi chinatsegula njira ya kufufuza pang’ono ponena za dzina la Mulungu. Mwachitsanzo, Francisco anadziŵa kuti mogwirizana ndi The Catholic Encyclopedia (ya mu 1910), Yehova ndilo “dzina laumwini la Mulungu m’Chipangano Chakale.” Iye anadziŵanso kuti “m’Chipangano Chakale,” chimene kwakukulukulu chinalembedwa m’chinenero cha Chihebri, dzina limenelo limawoneka pafupifupi nthaŵi 7,000. Palibe wotembenuza amene ali ndi mphamvu ya kusintha dzina laumwini la Yehova kukhala dzina laulemu losatsimikiza lakuti Ambuye. Francisco anafuna chowonadi chonena za dzina la Yehova, ndipo anachipeza m’Baibulo lenilenilo ndiponso kupyolera m’kufufuza kotsogozedwa bwino.
Kodi Malo a Yesu Ngwotani?
Monga momwe tafotokozera m’nkhani yapitayo, zipembedzo zadziko zasukulutsa chowonadi chambiri. Mwamalunji, muuminisitala wawo wakunyumba ndi nyumba, Mboni za Yehova zimakhala ndi mwaŵi wodziwa zimene anthu amakhulupirira. Ndithudi, ichi chingasiyane ku malo ndi malo, koma malingaliro ena ngofala. Mwachitsanzo, pamene afunsidwa kuti, ‘Kodi Mulungu ndani?’ eninyumba ena amati, ‘Yesu.’ Mwakutero iwo amatanthauza kuti Yesu ndiye Mulungu Wamphamvuyonse. Koma kodi lingaliro limeneli limaimira chowonadi?
Talingalirani nsonga zotsatirazi. Yesu anapemphera kwa Atate wake motere: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Kodi mwawona kuti Yesu analozera osati kwa iyemwini koma kwa Atate wake wakumwamba kukhala “Mulungu woona yekha”? Chotero, ophunzira oyambirira a Yesu anali olondola pamene anati kwa iye: “Zoonadi, ndinu Mwana wa Mulungu.” Yesu mwiniyo anati: “Ndiri Mwana wa Mulungu.” Chotero, chowonadi nchakuti Yesu sali Mulungu Wamphamvuyonse, koma iye ndi Mwana wa Yehova Mulungu.—Mateyu 14:33; Yohane 10:36.
Kodi Mtsogolo mwa Dziko Lapansi Ndimotani?
Bwanji ponena za mtsogolo mwa mbadwo uno ndi dziko lapansili? John F. Kennedy, malemu presidenti wa United States, polankhula ku UN General Assembly anati: “Tiri ndi mphamvu yopanga mbadwo uwu wa anthu kukhala wabwino koposa m’mbiri yadziko—kapena kuupanga kukhala womalizira.” Atsogoleri adziko amakono mwachiwonekere akulingalira mofanana. Zimene Mboni za Yehova zimamva kaŵirikaŵiri muuminisitala wawo nzakuti pamapeto adziko, pulaneti ya Dziko Lapansi lidzawonongedwa ndi moto kapena nkhondo yanyukliya. Pochilikiza chikhulupiriro chimenechi, ena amasonya ku Chibvumbulutso 21:1, pamene pamati: ‘Ndipo ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.’
Kaŵirikaŵiri Baibulo limagwiritsira ntchito liwu lakuti “dziko” mophiphiritsira, kulozera kwa anthu. Chitsanzo chikupezeka pa Genesis 11:1, pamene pamati: ‘Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.’ (Onaninso 1 Mafumu 2:1, 2; Salmo 96:1.) Pa Chibvumbulutso 21:1, “dziko loyamba” silikulozera ku pulaneti lino ayi, koma ku chitanganya cha anthu oipa chomwe chidzawonongedwa. Ichi chidzatsegula njira kaamba ka kubwezeretsedwa kwa Paradaiso pa dziko lapansi. (Luka 23:43; 2 Atesalonika 1:6-9; Chibvumbulutso 21:4) Ndipo ichi chimamvana ndi Baibulo lonse, limene limasonyeza kuti dziko lapansi lenileni silidzawonongedwa konse. Mwachitsanzo, pa Salmo 104:5 pamalongosola kuti Mulungu ‘anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse.’ (Yerekezerani ndi Mlaliki 1:4.) Ndithudi, Yehova ‘analiumba dziko lapansi kuti akhalemo anthu’ kosatha.—Yesaya 45:18.
Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kumva Chowonadi Chonse?
Zomwe zakambidwazo n’zitsanzo zokha za malingaliro olakwa amene ngofala kwambiri lerolino. Komabe, pamene mwininyumba ali wofunitsitsa kukambitsirana, monga momwe zinaliri ndi Francisco, Mboni za Yehova zimakondweretsedwa kuti mjira njotseguka yokambitsirana chowonadi Chamalemba.
Kusamva chowonadi chonse kungatsogolere ku zotulukapo zomvetsa chisoni. Kuti tifotokoze mwafanizo: Pamene Yesu anali padziko lapansi, ambiri anaumirizidwa kukhulupirira kuti iye anali kokha mwana wina wa Mariya ndi Yosefe, yemwe kalelo anali wopala matabwa wa ku Nazarete. Chotero, sanamsamale kwenikweni. Ku mlingo winawake, iwo anali olondola. Yesu adali mwana wa Mariya, amene kukhala ndi pakati kwake kunachitika mwa mzimu woyera. Iye adali mwana wolera wa Yosefe, ndipo anagwiradi ntchito monga wopala matabwa. (Marko 6:3) Komabe, kodi chimenecho chinali chowonadi chonse chonena za iye? Kutalitali! Iye adalidi Mesiya ndi woyembekezera kukhala “Mfumu ya mafumu”! (Chibvumbulutso 17:14; Luka 1:32-35; Machitidwe 2:36) Kusamva chowonadi chonse chonena za Yesu kunatsogoza anthu ambiri kuphonya mwaŵi wosadzabwerezedwanso—kusangalala ndi kuyanjana kwaumwini ndi Yesu padziko lapansi.
Santhulani Chowonadi Chonse
Mzinda wa Bereya (tsopano wotchedwa Véroia) m’Makedoniya wakale ngotchuka kwambiri kwa oŵerenga Baibulo chifukwa cha mkhalidwe woyamikirika wa nzika zake za m’zaka za zana loyamba. Kodi mkhalidwewo unali wotani? Mbiriyo ikufotokoza kuti: ‘Analandira mawu [olalikidwa ndi mtumwi Paulo] ndi kufunitsitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.’ Kodi panatulukanji? ‘Ambiri a iwo anakhulupira; ndi akazi a Chihelene omveka, ndi amuna, osati oŵerengeka.’—Machitidwe 17:11, 12.
Woyamikiridwanso koposa unali mkhalidwe wa aneneri akale a Mulungu. Iwo “anafunafuna nasanthula” za chipulumutso chomwe chinkadza kupyolera mwa Mesiya. (1 Petro 1:10) Mulungu anadalitsa zoyesayesa zawo. Pamenepo, nchachidziŵikire kuti palibe njira zachidule. Kusanthula mosamalitsa ndi kufunafuna ziphunzitso moumirira—iyi ndiyo njira yakuchimverera chowonadi chonse cha m’Baibulo!
Inu mungazizwe kuti, ‘Kodi ndiyambire pati?’ Pambuyo poŵerenga mabuku ena Achikristu, mkazi wina wokhala m’Brazil analemba motere: “Ife [iye ndi mwamuna wake] mofulumira tinazindikira kuti tinafunikira chidziŵitso cha mtundu woterowo chowonjezereka, kupeza mayankho ku mafunso ambiri amene tidali nawo . . . Chonde, kodi ndingapeze motani Baibulo ndi mabuku ena amene adzandithandiza kudziŵa zambiri ponena za Atate wathu wakumwamba?” Iye adali panjira yolondola: kuŵerenga Baibulo limodzi ndi mabuku olongosola Baibulo. Ngati nanunso mukufuna kumva chowonadi chonse, tsegulirani mtima wanu kwa Yehova Mulungu ndi kumpempha thandizo lake. Ndipo chonde tamverani mawu olimbikitsa awa: ‘Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse.’—Yakobo 1:5, 6.
Anthu mamiliyoni ambiri akukambitsirana Baibulo ndi Mboni za Yehova, mwakutero akufunafuna ndi kusanthula mosamalitsa kaamba ka chowonadi. Kudziŵa ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso choterocho cha Mulungu woona ndi Yesu Kristu kumatanthauza moyo wosatha. (Yohane 17:3) Limenelo lingakhale dalitso lanu lalikulu ngati musanthula mwakhama ndikumva chowonadi chonse.
[Chithunzi patsamba 7]
Chowonadi chonse chonena za Yesu chinali chakuti iye anali Mesiya, osati kokha wopala matabwa