Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Ngozi Zadzidzidzi?
Yankho la m’Baibulo
Mulungu si amene amachititsa ngozi zadzidzidzi zimene timaonazi ndipo amamva chisoni akaona anthu omwe akhudzidwa nazo. Ngozizi ndi chimodzi mwa zinthu zomwe zimachititsa anthu kuvutika ndipo posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzazithetsa. Koma panopa, Mulungu amatonthoza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi.—2 Akorinto 1:3.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti ngozi zadzidzidzi si chilango chochokera kwa Mulungu?
Kodi ngozi zadzidzidzi ndi chizindikiro choti tikukhala m’masiku otsiriza?
Kodi Mulungu amawathandiza bwanji anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi?
Kodi m’Baibulo muli mfundo zomwe zingatithandize kukonzekera ngozi zadzidzidzi?
Mavesi a m’Baibulo omwe angathandize anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi
N’chifukwa chiyani tinganene kuti ngozi zadzidzidzi si chilango chochokera kwa Mulungu?
Mmene ngozi zadzidzidzi zimachitikira, n’zosiyana kwambiri ndi mmene Yehova ankagwiritsira ntchito mphamvu zake popereka chiweruzo. Tikutero chifukwa:
Ngozi zadzidzidzi zimapha komanso kuvulaza aliyense, kaya akhale wabwino kapena woipa. Mosiyana ndi zimenezi, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu akafuna kupereka chilango, ankawononga anthu oipa okha. Mwachitsanzo, Mulungu atawononga mzinda wa Sodomu ndi Gomora anapulumutsa Loti ndi ana ake aakazi awiri. (Genesis 19:29, 30) Nthawi imeneyo Mulungu ankadziwa zimene zinali mumtima mwa munthu aliyense ndipo anawononga anthu omwe anawaona kuti ndi woipa.—Genesis 18:23-32; 1 Samueli 16:7.
Ngozi zadzidzidzi zimachitika mosayembekezereka. Komabe Mulungu akafuna kuwononga anthu oipa, ankawachenjeza kaye. Anthuwo akamvera, ankatha kupulumuka.—Genesis 7:1-5; Mateyu 24:38, 39.
Zochita za anthu zikhozanso kuyambitsa ngozi zadzidzidzi. Zili choncho chifukwa anthu ena amawononga chilengedwe ndipo ena amamanga nyumba zawo m’madera omwe nthawi zambiri kumachitika zivomezi, madzi amasefukira komanso kumene nyengo yake ndi yoipa kwambiri. (Chivumbulutso 11:18) Choncho si bwino kuimba Mulungu mlandu ngati anthu akukumana ndi mavuto chifukwa cha zosankha zawo.—Miyambo 19:3.
Kodi ngozi zadzidzidzi ndi chizindikiro choti tikukhala m’masiku otsiriza?
Inde. Baibulo linaneneratu kuti “mapeto a nthawi ino” kapena kuti “masiku otsiriza” ano, kudzakhala mavuto ambiri. (Mateyu 24:3; 2 Timoteyo 3:1) Mwachitsanzo, ponena za nthawi yathu ino Yesu ananena kuti: “Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.” (Mateyu 24:7) Koma posachedwapa Mulungu adzachotsa zonse zomwe zimachititsa kuti anthu azivutika, kuphatikizapo ngozi zadzidzidzi.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi Mulungu amawathandiza bwanji anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi?
Amagwiritsa ntchito Mawu ake potonthoza anthu okhudzidwawo. Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amatikonda komanso amamva chisoni akationa tikuvutika. (Yesaya 63:9; 1 Petulo 5:6, 7) Baibulo limanenanso za nthawi imene Yehova adzakwaniritse lonjezo lake pochotsa ngozi zadzidzidzi.—Onani kabokosi kakuti, “Mavesi a m’Baibulo omwe tingagwiritse ntchito pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi.”
Amagwiritsa ntchito atumiki ake pothandiza okhudzidwawo. Mulungu amagwiritsa ntchito atumiki ake kuti azitengera chitsanzo cha Yesu. Baibulo linaneneratu kuti Yesu akadzabwera adzalimbikitsa “anthu osweka mtima” komanso adzatonthoza “anthu onse olira.” (Yesaya 61:1, 2) Atumiki a Mulungu amayesetsa kuchitanso chimodzimodzi.—Yohane 13:15.
Mulungu amagwiritsanso ntchito atumiki ake popereka thandizo la chakudya, zovala, malo ogona ndi zinthu zina zofunikira kwa anthu omwe akhudzidwa ndi ngozi zadzidzidzi.—Machitidwe 11:28-30; Agalatiya 6:10.
Kodi m’Baibulo muli mfundo zomwe zingatithandize kukonzekera ngozi zadzidzidzi?
Inde. Ngakhale kuti Baibulo silinalembedwe n’cholinga chotithandiza kudziwa mmene tingakonzekerere ngozi zadzidzidzi, lili ndi mfundo zothandiza pa nkhaniyi. Mwachitsanzo limatithandiza:
Kudziwiratu zoyenera kuchita ngozi zadzidzidzi zisanachitike. Baibulo limanena kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Choncho ndi bwino kukonzekereratu madzi asanafike m’khosi. Zimenezi zingaphatikizepo kusonkhanitsa zinthu zofunika kwambiri zomwe mungadzazigwiritse ntchito ngati patachitika ngozi yadzidzidzi komanso kukambirana ndi achibale anu za malo omwe mungadzakumane.
Kuona moyo kukhala ofunika kuposa katundu. Baibulo limanena kuti: “Sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu.” (1 Timoteyo 6:7, 8) Tizikhala okonzeka kusiya nyumba yathu komanso katundu wathu n’cholinga choti tidzakwanitse kuthawa ngati patachitika ngozi. Nthawi zonse tizikumbukira kuti moyo wathu ndi wofunika kwambiri kuposa chilichonse chomwe tili nacho.—Mateyu 6:25.