YANDIKIRANI MULUNGU
“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”
Kodi mumalakalaka inuyo ndi banja lanu mutakhala ndi moyo wabwino? Kodi mumafuna mutakhala m’dziko lopanda imfa komanso mavuto ena? Dziwani kuti n’zotheka kukhala m’dziko loterolo. Tikutero chifukwa, cholinga cha Yehova Mulungu n’choti posachedwapa dzikoli lidzakhale latsopano komanso muzidzakhala anthu olungama okhaokha. Taonani zimene Baibulo likunena pofotokoza mmene cholinga chake chimenechi chidzakwaniritsidwire, pa Chivumbulutso 21:3-5.—Werengani.
“[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.” (Chivumbulutso 21:4) Kodi ndi misozi yotani imene Mulungu adzapukute? Imeneyi si misozi yomwe imatuluka chifukwa choti munthu wasangalala kwambiri kapena imene imatuluka poteteza maso athu. Apa Mulungu akulonjeza kudzapukuta misozi imene imatuluka chifukwa cha mavuto kapena chisoni. Ndipo sikuti Mulungu adzangoumitsa misoziyi, koma adzachotsa zonse zimene zimachititsa munthu kulira.
“Imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) Palibe chimene chimapangitsa anthu kulira kwambiri kuposa imfa. Yehova adzachititsa kuti anthu asamafenso. Kodi adzachita bwanji zimenezi? Iye adzachotsa chimene chimayambitsa imfa chomwe ndi uchimo wochokera kwa Adamu. (Aroma 5:12) Yehova adzathandiza anthu omvera kuti akhalenso angwiro pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo la Yesu.a Kenako imfa, yomwe ndi mdani womalizira, “idzawonongedwa.” (1 Akorinto 15:26) Zikadzatere anthu okhulupirika adzakhala ndi moyo wabwino komanso wosatha ngati mmene Mulungu ankafunira poyamba.
“Sipadzakhalanso . . . kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) Izi zikutanthauza kuti kupweteka kwa mtundu uliwonse kumene kumapangitsa kuti anthu azivutika, sikudzakhalaponso. Mavuto amenewa amabwera chifukwa cha uchimo komanso chifukwa choti anthufe si ife angwiro.
Posachedwapa anthu sadzaliranso chifukwa cha chisoni, sikudzakhalanso imfa komanso zowawa zilizonse. Koma mwina mungafunse kuti, ‘Kodi zimene Mulungu walonjezazi zidzachitikira kumwamba?’ Ayi ndithu. N’chifukwa chiyani tikutero? Choyamba, onani kuti mawu oyamba pa mavesiwa akunena kuti: “Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu,” ndipo anthu amakhala padziko lapansi. (Chivumbulutso 21:3) Chachiwiri, lonjezoli likunena za dziko limene “imfa sidzakhalaponso,” kusonyeza kuti poyamba imfayo inalipo. Kumwamba kulibe imfa, koma padziko lapansi pano m’pamene anthu akhala akumwalira kuyambira kalekale. Choncho n’zodziwikiratu kuti lonjezo la Mulungu lonena za dziko lopanda mavuto, lidzakwaniritsidwa padziko lapansi pano osati kumwamba.
Mulungu adzapukuta misozi yonse imene anthu akhala akutulutsa kwa nthawi yaitali polira chifukwa cha chisoni
Yehova amafuna kuti tizikhulupirira lonjezo lake lokhudza dziko latsopano lolungama. Atangomaliza kunena za madalitso amenewa, ananena mawu osonyeza kuti lonjezoli ndi lodalirika. Iye anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” Ananenanso kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.” (Chivumbulutso 21:5) Tikukupemphani kuti muphunzire zimene inuyo ndi banja lanu mungachite kuti mudzakhale m’gulu la anthu amene adzaone kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Mulungu limeneli.
Mavesi amene mungawerenge mu December
1 Petulo 1-5; 2 Petulo 1-3; 1 Yohane 1-5; 2 Yohane 1-13; 3 Yohane 1-14–Chivumbulutso 1-22
a Kuti mudziwe zambiri zokhudza nsembe ya dipo la Yesu, werengani mutu 5 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.