-
Kupanga Zinthu Zonse Kukhala ZatsopanoNsanja ya Olonda—1987
-
-
Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano
“Ndipo lye wakukhala pa mpando wachifumu anati, ‘Taonani! ndichita zonse zikhale zatsopano.’ Ndipo ananena, ‘Talemba, pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.’”—CHIVUMBULUTSO 21:5
1, 2. (a) Kodi ndi funso lotani limene Solomo anapereka zaka zikwi zitatu zapita? (b) Ndi chiyani, lerolino, chimene chimawoneka chotsutsana ndi mawu a Solomo?
“PALIBE kanthu katsopano pansi pano.” Awo anali mawu a Mfumu yanzeru Solomo. Kupitiriza, iye anafunsa: “Kodi pali kanthu unganene kuti: ‘Taona katsopano aka’?” (Mlaliki 1:9, 10) Kodi ndimotani mmene tingayankhire funso limenelo lerolino?
2 Kodi sayansi ndi maphunziro azopangapanga sanabweretse zinthu zambiri zatsopano mkati mwa zana lino la 20? Tangoyang’anani pa dziko la ulendo, ndi ndege zake za majeti, magalimoto ake okhala ndi mphamvu yapamwamba, ndi masitima ake a buleti. Ndipo kenaka pali kupita patsogolo kochititsa chidwi, kwa kulankhulana kwa pa maulendo aatali, kugwiritsira ntchito kwa masetilaiti omazungulira, ndi kuikidwa kwa zombo za m’mwamba zomwe mchenicheni zafikitsa anthu pa mwezi. Ndipo bwanji ponena za zogwiritsira ntchito zamakono za m’khitchini, mafriji, ndi makina ochapira zovala omwe akupezeka m’nyumba zambiri?Anthu ena angakhale oyedzamira ku kunena kuti: ‘Chifukwa ninji, pali chiri chonse chatsopano pansi pa thambo!’
3. Kodi ndi m’khalidwe woopsa wotani umene wapangidwa pansi pano “pansi pa thambo”? (Luka 21:25, 26; Masalmo 53:1)
3 Koma tadikirani pang’ono! Pali china chake chonyansa, chosokoneza, chomwe chiyenera kuwonedwa pansi pa thambo. Kodi chimenecho nchiyani? Nchiyani, dziko lapansi lakhala msasa wazida za nkhondo! Ichi chinayamba mu 1914 pamene Nkhondo Yadziko I inabuka. Kwanthawi yoyamba, mfuti zachiwaya, ndege, mathanki, ndi sitima zoyenda pansi pa madzi zinagwiritsidwa ntchito mu nkhondo. Mu zaka zochepera 30 Nkhondo Yadziko II inatsatira. Iyo inali yowononga moyo ndi katundu kuwirikiza nthawi zinayi monga mmene inaliri nkhondo ya dziko yoyamba. Iyo inapanga kugwiritsira ntchito kwa zinthu zosakaza kwambiri—zipolopolo zowaza moto, mabomba a napalm, ndipo pomalizira bomba la atomiki— mtsogoleri wa zida za nyukiliya zauchiwanda zomwe tsopano zikuwopseza kupulumuka kwenikweni kwa mtundu wa munthu pano pa dziko lapansi.
4. (a) Kodi ndi kukachitidwe kati ka zinthu komwe Solomo analoza m’kulankhula kuti “palibe chatsopano”? (b) Kodi ndimotani mmene nzeru ya Mulungu ndi chikondi chimawonekera mu zimene iye wachita, ndi zimene iye adzachita “pansi pa thambo”?
4 Kodi mowonadi tinganene, ndiyeno, kuti “palibe chiri chonse chatsopano pansi pa thambo”? Inde, tingatero, popeza zopangidwa zonsezi zimabwera kuchokera m’dziko la zinthu za kuthupi mu limene munthu wakhala akukhala nthawi zonse. Ngakhale pamene munthu aphulitsa zipangizo zosakanizidwa ndi haidrogeni, icho sichiri chatsopano. Kusakanizidwa kwa haidrogeni kwakhala kukuchitika mkati mwa dzuwa kwa zaka mabiliyoni. Awa ali magwero a kuwala kokhazikika kwamphamvu yomwe imawalitsa, kufunditsa, ndi kupatsa moyo ku dziko lathu lapansi. Kuwala kochokera ku dzuwa nakonso kumagwirizana ndi mtundu womwe umapezeka mu mitengo yobiriwira, kumapanga shuga ndi sitalichi zomwe ziri magwero a chakudya kaamba ka zamoyo zosawerengeka zotizinga ife. Tingakkhale oyamikira chotani nanga kuti Mlengi wa nzeru zonse wa dziko lapansi anakonza kutulutsidwa kopindulitsa kwamphamvu ya nyukiliya yolinganizidwa imeneyi kaamba ka dziko lathu! (Masalmo 104: 24) Ngakhale kuti anthu opanda umulungu amakonzekera kugwiritsira ntchito zipangizo za nyukiliya kaamba ka kupha kwa chisawawa, mwachimwemwe Mulungu “adzawononga iwo akuwononga dziko.”—Chivumbulutso 11:18.
5. (a) Kodi ndi chifukwa ninji Solomo anali wolondola mkunena kuti: “Palibe chiri chonse chatsopano pansi pa thambo”? (b) Kodi ndimotani mmene njira ya moyo ya anthu opanda ungwiro imasonyezera mawu a Solomo?
5 Solomo analondola m’kunena kwake: “Palibe chiri chonse chatsopano pansi pa thambo.” Popeza palibe chiri chonse chatsopano ponena za zinthu, magwero a mphamvu, ndi malamulo achilengedwe omwe amapanga maziko kaamba ka kachitidwe ka zinthu ka kuthupi ka dziko. Izi zonse kuyambira kale zinakhala mbali ya chilengedwe cha Mulungu. (Masalmo 24:1; Chivumbulutso 4:11) Palibe chiri chonse chatsopano mukuwala ndi kulowa kwa dzuwa, mu kakhalidwe ka nyengo, ndi kuzungulira kwa chilengedwe kaamba ka kutsirira ndi kukonzanso dziko. Ndipo ponena za njira ya moyo ya anthu opanda ungwiro akufa, palibe china chiri chonse chatsopano, mosasamala kanthu za kusintha kwa mafashoni. Ngakhale mu masosaite okhupuka, moyo kwa ambiri umakhala wobwerezabwereza, ndipo ku utali “wotopetsa.” Mu zaka zina 70 kapena 80, munthu wodetsedwa ndi chimo ‘amayenda ku nyumba yake yamuyaya’—manda. Monga mmene Solomo ananenera icho: “Chomwe chinawoneka, chidzawonekanso; ndi chomwe chinachitidwa, chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.”—Mlaliki 1:4-9; 12:5.
“Chilengedwe Chatsopano” Pansi pa Thambo
6. (a) Kodi nchifukwa ninji zinthu zolengedwa zatsopano zakuthupi siziyenera kuyembekezeredwa posachedwapa mtsogolo? (b) Ndimotani ndipo ndi liti pamene Yehova anabweretsera china chake “chatsopano pansi pa thambo”?
6 Zowonadi, mnjira ya kuthupi “palibe chiri chonse chatsopano pansi pa thambo”; Yehova sadzabwerezanso zotulutsidwa za kuthupi zatsopano mkati mwa tsiku la zaka 7, 000 la kupuma ku ntchito yake yachilengedwe. Koma china chake chatsopano chawoneka pansi pa thambo. Ndi liti? Munali mu chaka cha 2 B. C.E. pamene mngelo wa Yehova anawonekera mwadzidzidzi kwa abusa odzichepetsa pafupi ndi Betelehemu kukapanga chilengezo chatsopano chodzutsa maganizo. Iye anati: “Taonani! Ndikuuzani inu uthenga wabwino wa chikondwero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse, pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.” Khamu la angelo oyera anagwirizana naye iye mkulemekeza Mulungu ndi kunena kuti: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.”—Luka 2:8-14.
7. (a) Ndi chinthu chatsopano chiti chomwe chinachitika pa ubatizo wa Yesu? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anatsegulira njira kaamba ka zochitika zowonjezereka?
7 Pa zaka 30 za kubadwa, Mpulumutsi ameneyu anabatizidwa m’madzi a Yordani. Mwamsanga, chinthu china chatsopano chinachitika pansi pa thambo. Luka 3:21, 22 amalongosola ichi mu mawu awa: “Pamene [Yesu] anali kupemphera, panatseguka pathambo, ndipo Mzimu Woyera anatsika ndimawonekedwe a thupi lake ngati nkhunda, nadza pa iye; ndipo munaturuka mawu m’thambo, ndi kuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, mwa iwe ndikondwera.’” Pansonga imeneyi Yesu anakhala “cholengedwa chatsopano,” Mwana wobadwa ndi mzimu wa Mulungu. (2 Akorinto 5: 17) Mkati mwa zaka zitatu ndi theka zotsatira, Yesu anapereka umboni wamphamvu ku Ufumu wa Mulungu, kusonkhanitsa ophunzira ake oyambirira. Kenaka, mu 33 C.E., pambuyo pa imfa yake yansembe ndi kuukitsidwa kwake monga mzimu, Yesu anawoneka “pamaso pa Mulungu” kutsegula njira kaamba ka zochitika zosangalatsa zowonjezereka pansi pano “pansi pa thambo.”—Ahebri 9:24; 1 Petro 3:18.
8. Kodi ndimotani mmene “chilengedwe chatsopano” chinabweretsedwera?
8 Pa tsiku la Pentekoste mchaka chimenecho, Yesu anayamba kutsanulira mzimu woyera pa ophunzira ake okhulupirika, kusonyeza kuti iwo abwezeredwa mchigwirizano ndi iye monga ana a Mulungu. Mtumwi Paulo akulankhula za “chilengedwe chatsopano” chimenechi pa 2 Akorinto 5:17, 18, kumati: “Chifukwa chache ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, tawonani, zakhala zatsopano. Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Kristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso.”
9. Kodi ndi cholinga chotani chimene “chilengedwe chatsopano” chimakwaniritsa?
9 Mtumwi Petro akulankhula ponena za chilengedwe chatsopano, chimenechi akumati: “Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu amwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa.” (1 Petro 2:9) Pamene ali pano pa dziko lapansi, ansembe achifumu mwachangu alalikira “zinthu zokwezeka za Mulungu” ponena za zifuno za Ufumu wake. Awo a mu “chilengedwe chatsopano” amene amaliza njira yawo yosunga umphumphu padziko lapansi amaukitsidwa pambuyo pa kufika kwa Yesu ku kachisi wa Yehova—Machitidwe 2:11; Aroma 8:14-17; Malaki 3:1, 2.
“Kulenganso”
10. (a) Kodi nchiyani chimene Yesu ananena ponena za “kulenganso”? (b) Kodi ndi mu chiyani mmene awo “amchilengedwe chatsopano” akuitanidwa kugawanamo?
10 Komabe, kodi “chilengedwe chatsopano” chimenechi choyamba ndi Yesu Kristu chiri chinthu chokha “chatsopano” chomwe chinawoneka “pansi pa thambo”? Kutalitali! Pamene anali pano pa dziko lapansi, Yesu anauza ophunzira ake: “Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m’kubadwanso, pamene Mwana wamunthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.” (Mateyu 19:28) “Kagulu kankhosa” ka ophunzira a Yesu oyesedwa ndi kuvomerezedwa—144, 000 a iwo—akuitanidwa kugawana ndi Yesu mu Ufumu wake ndi “kukhala pa mipando kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.”—Luka 12:32; 22:28-30; Chivumbulutso 14:1-5.
11. Kodi ndi mbali ziwiri ziti za nsembe ya Yesu nzomwe zinasonyezedwa pa Tsiku Lachitetezero, ndipo motani?
11 Ndi ndani, pamenepo, amene ali “mafuko khumi ndi awiri”? Kakonzedwe kamene Yehova anapanga kaamba ka Tsiku Lachitetezero mu Israyeli wakale kamapereka chizindikiritso. Chaka chiri chonse, pa tsiku la khumi la mwezi wa chisanu ndi chiwiri, wansembe wa mkulu anafunikira kupereka nsembe ya ng’ombe ya mphongo monga nsembe yauchimo “mmalo mwa iye mwini ndi mbumba yake.” Ichi chinaimira nsembe ya Yesu monga yogwiritsidwa ntchito kwa “mbumba yake” ya ansembe. Koma bwanji ponena za Aisrayeli ena? Wansembe wamkulu kenaka anaponya maere pa mbuzi ziwiri. Imodzi ya izo iye anapha monga “mbuzi ya nsembe ya machimo, yomwe iri kaamba ka anthu.” Pambuyo pa kulapa machimo a anthu pa mbuzi yachiŵiri, iye anaitumiza iyo kuchipululu. Kutaidwa kwa mbuzi ziwiri kumeneko mwakutero kunaimira kukhetsedwa kwa mwazi wa moyo wa Yesu mu nsembe ndi kutenga kwake kotheratu kwa machimo amtundu wonse wa anthu mmalo mwa awo amnyumba yake ya unsembe.—Levitiko 16: 6-10, 15.
12. Kodi ndimotani mmene bukhu lotanthauzira mawu limodzi limalongosolela tanthauzo la “kulenganso”?
12 “Mafuko khumi ndi aŵiri Aisrayeli” ali ndi chizindikiro chofananacho pa Mateyu 19:28. Pano kagwiritsidwe ka ntchito kali kofutukulidwa kupyola ansembe ogulidwa ndi mzimu a Yesu kuphatikizapo ena onse a mtundu wa anthu. An Expository Dictionary of New Testament Words, ya W. E. Vine, imalongosola liwu la Chigriki logwiritsidwa ntchito pano kaamba ka “kulenganso,” pa. lin. ge. ne. si’a, monga “kubadwa kwatsopano . . . kubadwanso kwauzimu,” ndipo likuwonjezera: “Mu Mat[eyu] 19:28 liwulo lagwiritsidwa ntchito, mu ulaliki wa Ambuye, mulingaliro lokulirapo la ‘kubwezeretsedwa kwa zinthu zonse,’ (Machitidwe 3:21, R. V. ), pamene, monga chotulukapo cha Kubweranso Kwa chiwiri kwa Kristu, Yehova anakhazikitsa Mfumu Yake pa phiri Lake loyera la Zioni. (Mas. 2:6). . . Mwakutero chidzakwaniritsidwa chiombolo cha dziko kuchokera ku mphamvu ndi kunyenga kwa Satana ndi kuchokera kwa olamulira amitundu ankhalwe ndi okana chikristu.”
13. (a) Kodi ndimotani mmene matembenuzidwe osiyanasiyana a Baibulo asonyezera tanthauzo la pa. lin-ge. ne. si’a? (b) Chotero, kodi nchiyani chimene chidzachitika “pansi pa thambo”?
13 Mchigwirizano ndi ichi, matembenuzidwe a Baibulo pano amagwiritsira ntchito pa. lin. ge. ne. si’a mosiyasiyana monga: kubadwanso, dziko latsopano, kubadwa kwatsopano, dziko lobadwa latsopano, dziko lomwe lidzakhala, Chilengedwe chatsopano, dongosolo latsopano la moyo, mbadwo watsopano. Kodi mukumvetsetsa icho? “Mafuko khumi ndi awiri Aisrayeli,” kuimira anthu onse a mtundu wa anthu, adzayenera kuweruzidwa ndi Kristu ndi ansembe ake omvera. Ichi chidzakhala mchigwirizano ndi kubadwanso, kukonzedwanso kokulira kumene Yehova anakukonzekeretsa kaamba ka dziko iri lapansi pano “pansi pa thambo.”
“Nthawi za Kukonzanso”
14. (a) Malinga ndi Machitidwe 3:20, 21, Yesu ayenera kudikira kaamba ka chiyani? (b) Ndimotani ndipo ndi liti pamene Yesu anakhazikitsidwa monga Mfumu?
14 Kodi ndi liti pamene kubadwanso kumeneku kumachitika? Pa Machitidwe 3:20, 21, Petro analankhula za “Yesu, amene thambo lakumwamba liyenera kumlandira kufikira nthawi zakukonzanso zinthu zonse, zimene Mulungu analankhula za izo m’kamwa mwa aneneri ake oyera [akale, NW].” Ichi chimaloza ku kudikira kwa Yesu kudzanja lamanja la Mulungu kumwamba kufikira “nthawi zawo za anthu akunja zitakwanira.” (Luka 21:24; Masalmo 110:1, 2) Kenaka, mu 1914, Yehova moonadi ‘anakhazikitsa Mfumu yake pa Zioni, phiri lake loyera.’ Kodi ndi kukonzanso kwa mtundu wanji nanga kumene kumachitika?—Masalmo 2:6.
15. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika “pansi pa thambo” kutsatira kukhazikitsidwa monga mfumu kwa Yesu? (b) Ndimotani mmene Mateyu 25:31-34 ndi Yesaya 11:6-9 akukwaniritsidwira?
15 Choyamba, chinthu chatsopano chikuwonedwa pansi pa thambo, mchakuti ansembe otsalira okhulupirira a Kristu—omalizira a “chilengedwe chatsopano”—asonkhanitsidwa ndi kukhazikitsidwa kugwira ntchito mu ‘kulalikira mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu wokhazikitsidwa.’ Kenaka, “khamu lalikulu” lasonkhanitsidwa “kuchokera ku mitundu yonse” kaamba ka kusungidwa kupyola “chisautso chachikulu.” (Mateyu 24:14; Chivumbulutso 7:9, 14) Pa nthawi ino Mfumu yokhazikitsidwa, Yesu Kristu, akulekanitsa anthu kuchokera kwa wina ndi mnzace, monga mmene mbusa alekanitsira nkhosa ndi mbuzi. “Nkhosa” ali awo amene akudzisonyeza iwo eni olungama kulinga kwa Mfumu ndi abale ake ogulidwa ndi mzimu “chilengedwe chatsopano.” Chotero “nkhosa” zimenezi zikuitanidwa kulowa mu moyo wosatha mu Ufumu wa Yehova pa dziko lapansi. Padakali pano, iwo amasangalala ndi paradaiso wauzimu wobwezeretsedwapano pa dziko lapansi.—Mateyu 25:31-34, 46; Yesaya 11:6-9.
16. (a) Kodi ndi chiweruzo chotani chimene chiripo tsopano? (b) Kodi ndi chiweruzo chowonjezereka chotani chimene chidzatenga malo pambuyo pa Armagedo?
16 Kuweruzidwa kwa mitundu ndi kwa “nkhosa” pa nthawi ino kuli ponena za kuyenera kwa kupuluinuka mkati mwa “chisautso chachikulu.” (Mateyu 24:21, 22) Komabe, kodi chiweruzo chimenechi ndi chomwe chatchulidwa mu Mateyu 19:28? Ayi, popeza kuweruza kopitirirapo kudzachitidwa ndi Kristu ndi ansembe ake pambuyo pa chisautso. Kudzakhala kuweruza kophiphiritsira, kwa “mafuko khumi ndi awiri Aisrayeli,” anthu osati ansembe achifumu. Unyinji wa “khumi ndi awiri” umasonyeza kutheratu kwa awo amtundu wa anthu omwe adzaweruzidwa. Ichi chimaphatikizamo opulumuka a “chisautso chachikulu,” mbadwa zomwe adzakhala nazo, ndi mabiliyoni a anthu omwe adzabwera pa dziko lapansi mu chiukiriro.
17. Kodi ndi ndani amene adzaweruzidwa, ndipo malinga ndi “zochita” ziti?
17 Ponena za ichi, Paulo ananena pa Machitidwe 17:31 kuti Mulungu “anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; [Kristu Yesu] napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.” Pamapeto pa Armagedo “dziko lokhalidwa ndi anthu,” lopangidwa ndi mtundu onse wa anthu womwe udzakhalako pa dziko, siudzaweruzidwa malinga ndi machimo omwe anapangidwa kumbuyoko mkati mwa dongosolo iri la zinthu. Mmalo mwake, iwo “adzaweruzidwa aliyense payekha malinga ndi zochita zawo” zochitidwa mu dziko latsopano pamene adziyeneretsa iwo eni pa chopereka cha dipo la Kristu.—Chivumbulutso 20: 13; Mateyu 20:28; 1 Yohane 2:2.
18. (a) Monga kwasonyezedwa ndi Yesaya, kodi nchiyani chomwe chidzawoneka “pansi pa thambo”? (b) Kodi ndi mawu ati alonjezo omwe akukwaniritsidwa, ndipo nchiyani chimene tingayembekezere ku nthawi zosatha mtsogolo? (Aroma8:21)
18 Ndi zinthu zodabwitsa zotani zimene zidzawoneka pansi pa thambo pa nthawi imeneyo! Paradaiso wauzimu adzafutukuka kukhala paradaiso weni weni, m’kukwaniritsidwa kwa chifuno choyambirira cha Yehova kulinga ku dziko iri lapansi. Mulungu wathu amatiuza ife kuti ‘dziko lapansi liri choikapo mapazi ake,’ malo opatulika pa amene iye ayenera kulambiridwa, ndipo iye akulengeza “ndidzachitira malo amapazi anga ulemerero.” (Yesaya 66:1; 60:13) Chotero pano pansi pa thambo, dziko lapansi lidzapangidwa kukhala paradaiso waulemerero, munda wosangalatsa, mu umene anthu angwiro, amtendere, ndi ogwirizana ku nthawi yosatha adzalemekeza Mulungu wawo ndi Mlengi. “Okhulupirika ndi oona” ali mawu osangalatsa alonjezo a Yehova: “Taonani! ndichita zinthu zonse zikhale zatsopano”! (Chivumbulutso 21:5) Ndipo ku nthawi yosatha mtsogolo, ndi zinthu zolengedwa zatsopano zosangalatsa zotani zimene Mulungu wathu wachikondi adzabweretsa pano pansi pa thambo kusangalatsa banja lake la mtundu wa anthu!
-
-
Kupanga Zinthu Zonse Kukhala ZatsopanoNsanja ya Olonda—1987
-
-
[Chithunzi patsamba 29]
Ndi ndemanga yochititsa mantha yotani nanga imene ikuchitidwa ponena za komwe kumatchedwa kupita patsogolo komwe dziko tsopano likuwononga ndalama zokwanira madola 1. 9 miiiyoni pa zida za nkhondo mphindi iri yonse! Izi ziri zoposa zoyenera kukwaniritsa kaamba ka kudyetsa, kuveka, ndi kumangira nyumba awo onse a mtundu wa anthu omwe akukhala mu umphawi lerolino. Ku mbali ina, kuunjikidwa kwa mabomba a megatoni kungawononge anthu onse padziko lapansi—mabiliyoni asanu—kuwirikiza nthawi 12. Koma kukunenedwa kuti theka la miiiyoni la ubongo wabwino koposa wa mdziko umagwiritsidwa ntchito mkupititsa patsogolo zida zowononga koposa.
-