Mutu 43
Mzinda Wokongola Kwambiri
Masomphenya 16—Chivumbulutso 21:9–22:5
Nkhani yake: Kufotokoza Yerusalemu Watsopano
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Chisautso chachikulu chitadutsa ndipo Satana ataponyedwa kuphompho
1, 2. (a) Kodi mngelo anam’tengera kuti Yohane kukamuonetsa Yerusalemu Watsopano, ndipo zimene anaona kumeneko zikusiyana bwanji ndi zimene anaona m’mbuyomu? (b) N’chifukwa chiyani amenewa ali mapeto osangalatsa kwambiri a masomphenya a m’Chivumbulutso?
M’MBUYOMU tinaona kuti mngelo anatengera Yohane kuchipululu kuti akamuonetse Babulo Wamkulu. Tsopano mngelo winanso wofanana ndi ameneyu anatengera Yohane kuphiri lalitali. Zimene anaona kumeneko n’zosiyana kwambiri ndi zimene anaona kuchipululu kuja. Kuphiriko sanaone mzinda wodetsedwa komanso wachiwerewere, wofanana ndi hule lachibabulo lija. Koma anaona Yerusalemu Watsopano, mzinda wosadetsedwa, wauzimu komanso woyera, ukutsika kuchokera kumwamba.—Chivumbulutso 17:1, 5.
2 Ngakhale Yerusalemu wapadziko lapansi analibe ulemerero ngati umenewu. Yohane akutiuza kuti: “Ndipo kunabwera mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliri 7 yotsiriza. Iye anandiuza kuti: ‘Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.’ Choncho, mu mphamvu ya mzimu, ananditengera kuphiri lalikulu ndi lalitali, ndipo anandionetsa mzinda woyera, Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, uli ndi ulemerero wa Mulungu.” (Chivumbulutso 21:9-11a) Pamene anali paphiri lalitalilo, Yohane anatha kuona bwino kwambiri mbali zonse za mzinda wokongolawo. Anthu okhulupirika akhala akuyembekezera mzinda umenewu kungoyambira pamene anthu anachimwa n’kuyamba kufa. Tsopano Yohane anaona mzinda umenewu, womwe anthu anakhala akuuyembekezera kwa nthawi yaitali. (Aroma 8:19; 1 Akorinto 15:22, 23; Aheberi 11:39, 40) Umenewu ndi mzinda wauzimu wokongola kwambiri, wopangidwa ndi a 144,000 okhulupirika omwe anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. Mzindawu ndi wokongola kwambiri chifukwa ndi woyera ndiponso ukuonetsa ulemerero wa Yehova. Amenewatu ndi mapeto osangalatsa kwambiri a masomphenya a m’Chivumbulutso.
3. Kodi Yohane anati chiyani pofotokoza kukongola kwa Yerusalemu Watsopano?
3 Yerusalemu Watsopano ndi mzinda wokongola mogometsa kwambiri. Yohane anati: “Unali wonyezimira ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi. Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, ndipo unali ndi zipata 12. Pazipatazo panali angelo 12, ndipo panalembedwa mayina a mafuko 12 a ana a Isiraeli. Kum’mawa kwa mzindawo kunali zipata zitatu, kumpoto zipata zitatu, kum’mwera zipata zitatu, ndipo kumadzulo kwake zipata zitatu. Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko yokwana 12, ndipo pamiyalayo panali mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:11b-14) M’pake kuti Yohane ataona mzindawo, chinthu choyamba chimene anafotokoza chinali chokhudza kuwala ndi kunyezimira kwake. Yerusalemu Watsopano ndi wowala ngati mkwatibwi, ndipo kuwala kumeneku kukumupangitsa kuti akhale mkwatibwi woyenerera wa Khristu. Mzindawu unali wonyezimira, ndipo zimenezi n’zoyenera chifukwa unamangidwa ndi “Atate wa zounikira zonse zakuthambo.”—Yakobo 1:17.
4. N’chiyani chikusonyeza kuti Yerusalemu Watsopano si mtundu wa Aisiraeli enieni?
4 Pazipata 12 za mzindawo panalembedwa mayina a mafuko 12 a Isiraeli. Zimenezi zikusonyeza kuti mzinda wophiphiritsawu unapangidwa ndi anthu 144,000, amene anadindidwa chidindo, “ochokera m’fuko lililonse la ana a Isiraeli.” (Chivumbulutso 7:4-8) Mofanana ndi zimenezi, pamiyala yomangira maziko a mzindawu panalembedwa mayina a atumwi 12 a Mwanawankhosa. Choncho, Yerusalemu Watsopano sakuimira mtundu wa Aisiraeli enieni ochokera mwa ana 12 a Yakobo. Koma akuimira Isiraeli wauzimu, amene wamangidwa pa maziko a “atumwi ndi aneneri.”—Aefeso 2:20.
5. Kodi “mpanda waukulu ndi wautali” wa Yerusalemu Watsopano ukuimira chiyani? Nanga mfundo yakuti pakhomo lililonse lolowera mumzindawo panaikidwa angelo ikutanthauza chiyani?
5 Mzinda wophiphiritsawu uli ndi mpanda waukulu. Kalekale anthu ankamanga mipanda kuzungulira mizinda kuti adani asathe kulowamo. Yerusalemu Watsopano ali ndi “mpanda waukulu ndi wautali,” kusonyeza kuti ndi wotetezeka mwauzimu. Mumzindawu simungalowe aliyense wodana ndi chilungamo, wodetsedwa kapena wachinyengo. (Chivumbulutso 21:27) Koma aliyense amene akuloledwa kulowa mumzinda wokongolawu, amakhala ngati akulowa m’Paradaiso. (Chivumbulutso 2:7) Adamu atathamangitsidwa m’Paradaiso, Mulungu anaika akerubi kutsogolo kwa mundawo kuti anthu odetsedwa asalowemo. (Genesis 3:24) Mofanana ndi zimenezi, angelo anaikidwa pakhomo lililonse lolowera mumzinda woyera wa Yerusalemu kuti mzindawo ukhale wotetezeka mwauzimu. Zoonadi, m’masiku onse otsiriza ano, angelo akhala akulondera mpingo wa Akhristu odzozedwa, umene udzakhale Yerusalemu Watsopano, kuti usaipitsidwe ndi zikhulupiriro zachibabulo.—Mateyu 13:41.
Anayeza Mzindawo
6. (a) Kodi Yohane anati chiyani pofotokoza ntchito yoyeza mzinda, ndipo kuyezedwa kwa mzindawu kukusonyeza chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti mzindawo unayezedwa “malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo” mwina ikutanthauza chiyani? (Onani mawu a m’munsi.)
6 Yohane akupitiriza kufotokoza kuti: “Tsopano amene anali kundilankhula uja ananyamula bango lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, zipata zake, ndi mpanda wake. Mzindawo unali ndi mbali zinayi zofanana kutalika kwake. M’litali mwake n’chimodzimodzi ndi m’lifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawo ndi bangolo, ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000 kuuzungulira. M’litali mwake, m’lifupi mwake, ndi msinkhu wake, n’zofanana. Anayezanso mpanda wake, ndipo unali wautali mikono 144, malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo.” (Chivumbulutso 21:15-17) Pamene nyumba yopatulika ya pakachisi inayezedwa, zinatsimikizira kuti zolinga za Yehova zokhudza nyumbayo zidzakwaniritsidwa. (Chivumbulutso 11:1) Tsopano pamene mngelo akuyeza Yerusalemu Watsopano zikusonyeza kuti zolinga za Yehova zokhudza mzinda waulemererowu sizingasinthe.a
7. Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi kukula kwa mzindawo?
7 Mzindawu ndi wochititsa chidwi kwambiri chifukwa mbali zake zonse n’zazitali mofanana. M’litali, m’lifupi komanso msinkhu wake, zinali zazitali masitadiya 12,000 (pafupifupi makilomita 2,200), ndipo unali ndi mpanda wautali mikono 144, kapena kuti mamita 64. Mzinda weniweni sungakhale waukulu choncho chifukwa ungakhale waukulu kuwirikiza nthawi 14 kuposa dziko la Israel la masiku ano, ndipo ungakhale wautali makilomita 560 kupita m’mwamba. Pajatu masomphenya a m’buku la Chivumbulutso anaperekedwa mwa zizindikiro. Ndiye kodi miyezo imeneyi ikutiuza chiyani za Yerusalemu Watsopano wakumwamba?
8. Kodi mfundo zotsatirazi zikutanthauza chiyani? (a) mpanda wa mzindawo unali wautali mikono 144, (b) muyezo wa mzindawo unali masitadiya 12,000, (c) m’litali, m’lifupi ndiponso msinkhu wa mzindawo zinali zofanana ndendende.
8 Mpanda wa mzindawo, womwe ndi wautali mikono 144, ukutikumbutsa mfundo yakuti mzindawu wapangidwa ndi anthu 144,000 amene Mulungu amawaona kuti ndi ana ake auzimu. M’litali, m’lifupi ndi msinkhu wa mzindawo zinali zofanana, ndipo muyezo wake unali masitadiya 12,000. Nambala ya 12 imene ikupezeka pa muyezo umenewu, imagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa m’maulosi a m’Baibulo, kuimira gulu lokonzedwa mwadongosolo. Choncho Yerusalemu Watsopano ndi gulu limene linakonzedwa mwadongosolo kwambiri kuti likwaniritse cholinga chamuyaya cha Mulungu. Yerusalemu Watsopano, pamodzi ndi Mfumu Yesu Khristu, ndi gulu limene likupanga Ufumu wa Yehova. Taona kale kuti m’litali mwa mzindawo, m’lifupi mwake, ndi msinkhu wake zinali zofanana. Mofanana ndi zimenezi, Malo Oyera Koposa a m’kachisi wa Solomo, omwe munali zinthu zimene zinkaphiphiritsira kuti Yehova ali mmenemo, analinso ofanana m’litali, m’lifupi ndi msinkhu wake. (1 Mafumu 6:19, 20) Choncho m’pake kuti Yerusalemu Watsopano amene Yohane anaona, yemwe ndi wowala chifukwa cha ulemerero wa Yehova, anali wamkulu kuposa Malo Oyera Koposa aja ndiponso m’litali, m’lifupi ndi msinkhu wake zinali zofanana. Mbali zake zonse n’zofanana ndendende. Mzinda umenewu ulibe mbali iliyonse yokhota kapena yopotoka.—Chivumbulutso 21:22.
Unamangidwa ndi Miyala Yamtengo Wapatali
9. Kodi Yohane anafotokoza kuti mzindawo unamangidwa ndi zinthu ziti?
9 Yohane anapitiriza kufotokoza mzindawo kuti: “Mpandawo unali womangidwa ndi mwala wa yasipi, ndipo mzindawo unali womangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. Maziko a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse: maziko oyamba anali amwala wa yasipi, achiwiri wa safiro, achitatu wa kalikedo, achinayi wa emarodi, achisanu wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto, ndipo a 12, wa ametusito. Komanso zitseko za pazipata 12 zija zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinali ngale imodzi. Ndipo msewu waukulu wa mumzindawo unali wopangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi.”—Chivumbulutso 21:18-21.
10. Kodi mfundo yakuti mzindawo unamangidwa ndi yasipi, golide komanso “miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse,” ikutanthauza chiyani?
10 Mzindawu unamangidwadi mogometsa kwambiri. Pomanga mzindawu sanagwiritse ntchito zinthu zachabechabe zapadziko lapansi ngati dothi kapena miyala wamba, koma anaumanga ndi yasipi, golide woyenga bwino, komanso “miyala yamtengo wapatali ya mitundu yonse.” Miyala imeneyi ikuimiradi zinthu zomangira zakumwamba, ndipo ndi yamtengo wapatali kuposa zinthu zilizonse zomangira nyumba. Kale likasa la pangano linakutidwa ndi golide woyenga bwino, ndipo m’Baibulo kawirikawiri golide amaimira zinthu zabwino komanso zamtengo wapatali. (Ekisodo 25:11; Miyambo 25:11; Yesaya 60:6, 17) Yerusalemu Watsopano yense komanso misewu yake ikuluikulu, inamangidwa ndi “golide woyenga bwino woonekera ngati galasi.” Zimenezi zikusonyeza kuti ndi wokongola mogometsa kwambiri komanso wamtengo wapatali.
11. N’chiyani chidzachititse kuti amene akupanga Yerusalemu Watsopano adzakhale onyezimira kwambiri ndiponso oyera mwauzimu?
11 Palibe munthu amene angayenge golide wabwino chonchi. Koma Yehova ndi Woyenga Wamkulu. Iye wakhala pansi ngati “woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeretsa siliva.” Amayenga anthu okhulupirika a Isiraeli wauzimu ndipo amachotsa zodetsa zonse mwa iwo n’kuwayeretsa “ngati golide ndi siliva.” Anthu amene ayengedwa ndi kuyeretsedwadi, ndi okhawo amene adzapange Yerusalemu Watsopano. Mwanjira imeneyi Yehova akumanga mzindawu pogwiritsa ntchito anthu amene ndi onyezimira kwambiri chifukwa chakuti ndi oyera mwauzimu.—Malaki 3:3, 4.
12. Kodi mfundo zotsatirazi zikusonyeza chiyani? (a) maziko a mzindawo anakongoletsedwa ndi miyala 12 yamtengo wapatali, (b) zitseko za zipata za mzindawo zinali ngale.
12 Maziko a mzindawu nawonso ndi okongola kwambiri chifukwa chakuti anawakongoletsa ndi miyala 12 yamtengo wapatali. Zimenezi zikutikumbutsa za mkulu wa ansembe wachiyuda amene pa masiku a zikondwerero ankavala efodi wokhala ndi miyala yosiyanasiyana 12 yamtengo wapatali, yofanana ndi imene yafotokozedwa pa Chivumbulutso 21:18-21. (Ekisodo 28:15-21) Ndithudi, sikuti zimenezi zangofanana mwangozi. Koma zikusonyeza kuti Yerusalemu Watsopano adzagwiranso ntchito za wansembe, ndipo Yesu, amene ndi Mkulu wa Ansembe wapamwamba, ndiye “nyale” yake. (Chivumbulutso 20:6; 21:23; Aheberi 8:1) Komanso madalitso a utumiki wa Yesu monga mkulu wa ansembe, adzafika kwa anthu kudzera mwa Yerusalemu Watsopano. (Chivumbulutso 22:1, 2) Chitseko chilichonse mwa zitseko 12 za zipata za mzindawo, chinali ngale yokongola kwambiri. Zimenezi zikutikumbutsa fanizo la Yesu pamene anayerekezera Ufumu ndi ngale yamtengo wapatali. Aliyense wolowa pazipata za mzindawu adzakhala atasonyeza kuti amakondadi kwambiri zinthu zauzimu.—Mateyu 13:45, 46; yerekezerani ndi Yobu 28:12, 17, 18.
Mzinda Wowala
13. Kodi kenako Yohane ananena chiyani chokhudza Yerusalemu Watsopano, ndipo n’chifukwa chiyani mzindawo sunafunikire kachisi weniweni?
13 Pa nthawi ya Solomo, kachisi wa ku Yerusalemu ndi amene anali wamkulu kwambiri mumzindawu kuposa nyumba iliyonse. Kachisiyu anamangidwa paphiri la Moriya kumpoto kwa mzindawo, omwe anali malo okwera kwambiri mumzinda wonsewo. Nanga bwanji za Yerusalemu Watsopano? Yohane anati: “Sindinaone kachisi mumzindawo, pakuti Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ndiye anali kachisi wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kachisi wake. Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, pakuti ulemerero wa Mulungu unauwalitsa, ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:22, 23) Kunena zoona, mumzindawu simunafunike kumangamo kachisi weniweni. Zili choncho chifukwa kachisi wakale wa Ayuda ankachitira chithunzi kachisi wamkulu wauzimu. Ndipo kachisi wauzimuyu wakhalapo kuchokera pamene Yehova anadzoza Yesu kukhala Mkulu wa Ansembe mu 29 C.E. (Mateyu 3:16, 17; Aheberi 9:11, 12, 23, 24) Komanso pakachisi wakale panali gulu la ansembe amene ankapereka nsembe kwa Yehova poimira anthu. Komatu onse amene akupanga Yerusalemu Watsopano ndi ansembe. (Chivumbulutso 20:6) Ndiponso nsembe yaikulu, yomwe ndi moyo wangwiro umene Yesu anali nawo ali padziko lapansi, inaperekedwa kamodzi kokha ndipo sipadzafunikanso ina. (Aheberi 9:27, 28) Kuwonjezera pamenepo, aliyense wokhala mumzindawu angathe kufika kwa Yehova payekha.
14. (a) Kodi n’chifukwa chiyani sipakufunika dzuwa ndi mwezi kuti ziziunikira Yerusalemu Watsopano? (b) Kodi ulosi wa Yesaya unaneneratu chiyani chokhudza gulu la Yehova la m’chilengedwe chonse, ndipo Yerusalemu Watsopano akukhudzidwa bwanji ndi zimenezi?
14 Pamene ulemerero wa Yehova unadutsa pafupi ndi Mose paphiri la Sinai, unachititsa kuti nkhope ya Mose iwale kwambiri moti anachita kuiphimba kuti Aisiraeli ena asaione. (Ekisodo 34:4-7, 29, 30, 33) Ndiye kodi mukuganiza kuti mzinda womwe ukuwala nthawi zonse chifukwa cha ulemerero wa Yehova, ungakhale wowala bwanji? Usiku sungakhalepo mumzinda umenewu, ndipo sungafunike dzuwa lenileni kapena mwezi. Mzindawu ungakhale wowala mpaka kalekale. (Yerekezerani ndi 1 Timoteyo 6:16.) Yerusalemu Watsopano ndi wowala kwambiri mwanjira imeneyi. Ndithudi, mkwatibwi ameneyu pamodzi ndi Mkwati wake amene ndi Mfumu, anakhala likulu la gulu la Yehova la m’chilengedwe chonse. Ndipo gulu limeneli likuimira “mkazi” wa Yehova, yemwe ndi “Yerusalemu wam’mwamba.” Ponena za gulu limeneli, Yesaya analosera kuti: “Dzuwa silidzakhalanso lokuunikira masana, ndipo mwezi sudzakuunikiranso. Kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale, ndipo Mulungu wako adzakhala kukongola kwako. Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzapitanso kumdima. Pakuti kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale, ndipo masiku ako olira adzakhala atatha.”—Yesaya 60:1, 19, 20; Agalatiya 4:26.
Kuwala Kounikira Mitundu ya Anthu
15. Kodi ndi mawu ati a m’buku la Chivumbulutso onena za Yerusalemu Watsopano omwe ali ofanana ndi ulosi wa Yesaya?
15 Ulosi womwewu unanenanso kuti: “Mitundu ya anthu idzatsata kuwala kwako, ndipo mafumu adzatsata kunyezimira kwako.” (Yesaya 60:3) Buku la Chivumbulutso likusonyeza kuti mawu amenewa akukhudzanso Yerusalemu Watsopano. Bukuli limati: “Mitundu ya anthu idzayenda mwa kuwala kwake, ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo. Zipata zake sizidzatsekedwa n’komwe masana, ndipo usiku sudzakhalako. Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo.”—Chivumbulutso 21:24-26.
16. Kodi “mitundu ya anthu” imene idzayende mwa kuwala kwa Yerusalemu Watsopano ndi iti?
16 Kodi “mitundu ya anthu” imene ikuyenda mwa kuwala kwa Yerusalemu Watsopano ndi iti? Amenewa ndi anthu amene poyamba anali mbali ya mitundu ya anthu a m’dziko loipali, ndipo atsatira kuwala komwe kukuchokera mumzinda waulemerero wakumwamba umenewu. Mbali yaikulu ya anthuwa ndi a khamu lalikulu, amene atuluka kale “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse” ndipo akulambira Mulungu usana ndi usiku pamodzi ndi Akhristu odzozedwa. (Chivumbulutso 7:9, 15) Yerusalemu Watsopano adzatsika kuchokera kumwamba ndipo Yesu adzagwiritsa ntchito makiyi a imfa ndi Manda poukitsa akufa. Zimenezi zikadzachitika a khamu lalikulu adzagwirizana ndi anthu oukitsidwawa, omwe adzakhalepo mamiliyoni ambirimbiri. Iwo adzakhala ochokera ‘m’mitundu ya anthu,’ ndipo adzayamba kukonda Yehova ndi Mwana wake, yemwe ndi Mwamuna wa Yerusalemu Watsopano, wokhala ngati Mwanawankhosa.—Chivumbulutso 1:18.
17. Kodi “mafumu a dziko lapansi” amene ‘adzabweretse ulemerero wawo’ mu Yerusalemu Watsopano, ndani?
17 Nanga “mafumu a dziko lapansi” amene ‘adzabweretse ulemerero wawo mumzindawo’ ndani? Mafumu amenewa si mafumu enieni a padziko lapansi, chifukwa monga gulu, iwo adzawonongedwa pa Aramagedo polimbana ndi Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 16:14, 16; 19:17, 18) Kodi mafumu amenewa akuimira anthu otchuka a m’dzikoli amene adzakhale mbali ya khamu lalikulu, kapena kodi ndi mafumu oukitsidwa amene adzagonjere Ufumu wa Mulungu m’dziko latsopano? (Mateyu 12:42) Ayi si choncho, chifukwa chakuti ulemerero wa mafumu amenewo unali wa padziko lapansi ndipo pa nthawiyi udzakhala utatha kalekale. Choncho “mafumu a dziko lapansi” amene adzabweretse ulemerero wawo mu Yerusalemu Watsopano ayenera kuti ndi a 144,000. Iwo ‘anagulidwa . . . kuchokera mu fuko lililonse, chinenero chilichonse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse’ kuti alamulire monga mafumu pamodzi ndi Mwanawankhosa, Yesu Khristu. (Chivumbulutso 5:9, 10; 22:5) Iwo adzabweretsa mumzindawu ulemerero umene Mulungu anawapatsa, ndipo zimenezi zidzawonjezera kuwala kwa mzindawo.
18. (a) Ndani amene sadzalowa mu Yerusalemu Watsopano? (b) Kodi ndani okha amene adzaloledwe kulowa mumzindawo?
18 Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Koma chilichonse chosapatulika, ndi aliyense wochita zonyansa ndiponso wabodza, sadzalowa mumzindawo. Amene adzalowemo ndi okhawo olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:27) Chilichonse choipitsidwa ndi dziko la Satanali sichingakhale mbali ya Yerusalemu Watsopano. Ngakhale kuti zipata za mzindawu zidzakhala zotsegula nthawi zonse, “aliyense wochita zonyansa ndiponso wabodza” sadzaloledwa kulowamo. Mumzinda umenewu simudzapezeka aliyense wampatuko kapena wa mu Babulo Wamkulu. Ndipo aliyense wofuna kudetsa mzindawu poyesa kusocheretsa anthu amene adzakhale mumzindawu pa nthawi imene iwo adakali padziko lapansi, sadzapambana. (Mateyu 13:41-43) A 144,000 okha, “olembedwa mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa,” ndi amene pamapeto pake adzalowe mu Yerusalemu Watsopano.b—Chivumbulutso 13:8; Danieli 12:3.
Mtsinje wa Madzi a Moyo
19. (a) Kodi Yohane ananena chiyani, zimene zikusonyeza kuti anthu adzapeza madalitso kudzera mwa Yerusalemu Watsopano? (b) Kodi “mtsinje wa madzi a moyo” unayamba liti kuyenda, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?
19 Anthu padziko lapansi adzalandira madalitso ambiri kudzera mwa Yerusalemu Watsopano wokongolayu. Izi n’zimene Yohane anaona kenako. Iye anati: “Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo, oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa. Mtsinjewo unali kudutsa pakati pa msewu waukulu wa mumzindawo.” (Chivumbulutso 22:1, 2a) Kodi “mtsinje” umenewu unayamba liti kuyenda? Popeza kuti mtsinjewu ukuchokera “kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa,” ndiye kuti unayamba kuyenda tsiku la Ambuye litayamba mu 1914. Zinthu zochititsa chidwi zimene mngelo amene analiza lipenga la 7 analengeza, zinachitika pa nthawi imeneyi. Iye analengeza kuti: “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika.” (Chivumbulutso 11:15; 12:10) M’nthawi yamapeto ino, mzimu ndi mkwatibwi akhala akuitana anthu a maganizo abwino kuti adzamwe madzi a moyo kwaulere. Anthu otere adzapitirizabe kupeza madzi ochokera mumtsinje umenewu mpaka pamapeto a dziko loipali. Ndipo kenako, adzapitiriza kumwa madzi amenewa m’dziko latsopano, Yerusalemu Watsopano ‘akadzatsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu.’—Chivumbulutso 21:2.
20. N’chiyani chikusonyeza kuti ena mwa madzi a moyo alipo kale?
20 Aka si koyamba kuti anthu apatsidwe mwayi wolandira madzi a moyo. Pamene Yesu anali padziko lapansi, ananena za madzi opatsa moyo wosatha. (Yohane 4:10-14; 7:37, 38) Komanso Yohane anali atatsala pang’ono kumva mawu oitana mwachikondi, akuti: “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: ‘Bwera!’ Aliyense wakumva anene kuti: ‘Bwera!’ Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Ngakhale panopa anthu akuitanidwa kudzamwa madzi, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti ena mwa madzi a moyo alipo kale. Koma m’dziko latsopano, madzi amenewa adzayenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu, kudzera mu Yerusalemu Watsopano, ndipo madziwo adzapanga mtsinje waukulu.
21. Kodi “mtsinje wa madzi a moyo” ukuimira chiyani, ndipo masomphenya a Ezekieli a mtsinje umenewu akutithandiza bwanji kudziwa zimenezi?
21 Kodi “mtsinje wa madzi a moyo” umenewu n’chiyani? Madzi enieni ndi ofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi moyo. Munthu angathe kukhala ndi moyo kwa milungu ingapo popanda chakudya, koma ngati atakhala osamwa madzi angafe pa mlungu umodzi wokha. Madzi timawagwiritsanso ntchito poyeretsa zinthu ndipo ndi ofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi moyo wathanzi. Choncho madzi a moyo ayenera kuti akuimira zinthu zofunika kwambiri kuti anthu akhale ndi moyo komanso thanzi labwino. Mneneri Ezekieli nayenso anaonetsedwa masomphenya a “mtsinje wa madzi a moyo” umenewu, ndipo m’masomphenya akewo, anaona kuti mtsinjewo unkayenda kuchokera m’kachisi ndipo unakathera mu Nyanja Yakufa. Kenako panachitika chinthu chozizwitsa kwambiri. Madzi a m’nyanja imeneyi, omwe sanali abwino komanso munalibe chamoyo chilichonse, anasintha n’kukhala abwino kwambiri ndipo munadzaza nsomba. (Ezekieli 47:1-12) Zoonadi, mtsinje wa m’masomphenyawu unathandiza kuti m’nyanja yakufayi, imene munalibe chamoyo chilichonse mukhale zinthu zamoyo. Zimenezi zikutsimikizira kuti mtsinje wa madzi a moyo ukuimira zinthu zimene Mulungu wapereka kudzera mwa Yesu Khristu zothandiza kuti anthu amene anali ngati akufa adzapeze moyo wangwiro. Madzi a mumtsinje umenewu ndi “oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo,” kusonyeza kuti zinthu zothandiza anthu zimene Mulungu wapereka n’zosadetsedwa komanso n’zoyera. N’zosiyana ndi “madzi” akupha komanso odzaza ndi magazi, a m’Matchalitchi Achikhristu.—Chivumbulutso 8:10, 11.
22. (a) Kodi mtsinjewu ukuchokera kuti, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenera? (b) Kodi n’chiyani chikukhudzana ndi madzi a moyo, ndipo n’chiyani chikupanga mtsinje wophiphiritsawu?
22 Mtsinjewu ukuchokera “kumpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa.” Zimenezi n’zoyenera chifukwa chakuti nsembe ya dipo ndiyo maziko a zinthu zopatsa moyo zimene Yehova amapereka. Ndipo Yehova anapereka dipo limeneli chifukwa chakuti “anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Madzi a moyo akukhudzananso ndi Mawu a Mulungu, ndipo mawu amenewa m’Baibulo amatchedwanso madzi. (Aefeso 5:26) Komabe, mtsinje wa madzi a moyo si choonadi chokha, koma ukupangidwa ndi zinthu zina zonse zimene Yehova amapereka chifukwa cha nsembe ya Yesu, kuti anthu omvera awomboledwe ku uchimo ndi imfa n’kupatsidwa moyo wosatha.—Yohane 1:29; 1 Yohane 2:1, 2.
23. (a) N’chifukwa chiyani m’pake kuti mtsinje wa madzi a moyowu ukudutsa pakati pa msewu waukulu wa mu Yerusalemu Watsopano? (b) Kodi ndi lonjezo liti limene Mulungu anachita ndi Abulahamu, lomwe lidzakwaniritsidwe madzi a moyo akadzayamba kuyenda ochuluka?
23 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, anthu adzalandira madalitso onse obwera chifukwa cha dipo. Zimenezi zidzachitika kudzera mwa Yesu yemwe ndi mkulu wa ansembe pamodzi ndi ansembe ake aang’ono okwana 144,000. M’pake kuti mtsinje wa madzi a moyowu ukudutsa pakati pa msewu waukulu wa mu Yerusalemu Watsopano. Yerusalemu Watsopanoyu wapangidwa ndi Isiraeli wauzimu, amene pamodzi ndi Yesu, akupanga mbewu yeniyeni ya Abulahamu. (Agalatiya 3:16, 29) Choncho madzi a moyowa akadzayamba kuyenda ochuluka, kudutsa pakati pa msewu waukulu wa mumzinda wophiphiritsawu, “mitundu yonse ya padziko lapansi” idzakhala ndi mwayi wonse wopeza madalitso kudzera mwa mbewu ya Abulahamu. Zimenezi zikadzachitika, lonjezo limene Yehova anachita ndi Abulahamu, lidzakwaniritsidwa lonse.—Genesis 22:17, 18.
Mitengo ya Moyo
24. Kodi kenako Yohane anaona chiyani kumbali zonse za mtsinje wa madzi a moyo, ndipo zimenezi zikuimira chiyani?
24 Madzi a mumtsinje wa m’masomphenya a Ezekieli anayamba kuthamanga kwambiri, ndipo mneneriyu anaona kuti m’mbali zonse za mtsinjewu munamera mitengo yosiyanasiyana ya zipatso. (Ezekieli 47:12) Koma kodi Yohane anaona chiyani? Iye anati: “Kumbali iyi ya mtsinjewo ndi kumbali inayo, kunali mitengo ya moyo yobala zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inali kubala zipatso mwezi uliwonse. Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu.” (Chivumbulutso 22:2b) “Mitengo ya moyo” imeneyi iyeneranso kuti ikuimira gawo lina la zinthu zimene Yehova amapereka zothandiza anthu omvera kuti adzapeze moyo wosatha.
25. Kodi Yehova adzapereka zinthu zambiri ziti kwa anthu okhulupirika m’Paradaiso wa padziko lonse?
25 Apatu n’zoonekeratu kuti Yehova adzapereka zinthu zambiri kwa anthu omvera. Anthuwa sikuti azidzangomwa madzi otsitsimulawo, koma nthawi zonse azidzathyolanso ndi kudya zipatso zokoma zosiyanasiyana m’mitengo imeneyi. Zikanakhalatu bwino kwambiri ngati makolo athu oyambirira aja akanakhutira ndi zipatso ‘zooneka bwino’ zimene Mulungu anawapatsa m’Paradaiso, m’munda wa Edeni. (Genesis 2:9) Koma tsopano dziko lonse lapansi lidzakhalanso Paradaiso, ndipo Yehova ‘adzachiritsa mitundu ya anthu,’ pogwiritsira ntchito masamba a mitengo yophiphiritsayo.c Masamba ophiphiritsawa ndi amphamvu kwambiri kuposa mankhwala alionse azitsamba kapena amtundu wina amene akupezeka masiku ano. Masamba ochiritsawa adzathandiza kwambiri anthu okhulupirira kuti akhale ndi matupi angwiro komanso kuti akhale angwiro mwauzimu.
26. Kodi n’kutheka kuti ndani amene ali m’gulu la mitengo ya moyo, ndipo n’chifukwa chiyani zili choncho?
26 N’kutheka kuti a 144,000 amene ndi mkazi wa Mwanawankhosa, ali m’gulu la mitengo imeneyi, yomwe izidzalandira madzi okwanira ochokera mumtsinjewo. Pamene ali padziko lapansi, anthu amenewa amapindula ndi zinthu zothandiza anthu kudzapeza moyo zimene Mulungu amapereka kudzera mwa Yesu Khristu. N’zochititsa chidwi kuti mwaulosi, abale a Yesu odzozedwa ndi mzimu amenewa amatchedwa “mitengo ikuluikulu ya chilungamo.” (Yesaya 61:1-3; Chivumbulutso 21:6) Iwo abereka kale zipatso zambiri zauzimu zimene zikuthandiza kuti Yehova atamandidwe. (Mateyu 21:43) Ndipo mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, iwo adzathandiza popereka nawo zinthu zosiyanasiyana zochokera kwa Mulungu ‘zochiritsa mitundu ya anthu’ ku uchimo ndi imfa pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo.—Yerekezerani ndi 1 Yohane 1:7.
Usiku Sudzakhalakonso
27. Kodi Yohane anatchula madalitso ena ati amene anthu omwe ali ndi mwayi wolowa mu Yerusalemu Watsopano amalandira, ndipo n’chifukwa chiyani akunena kuti “sikudzakhalanso temberero”?
27 Ndithudi, palibe mwayi winanso waukulu kuposa kukalowa mu Yerusalemu Watsopano. Inde, ndi mwayi waukulu kuti anthu onyozeka komanso opanda ungwiro atsatire Yesu kumwamba n’kukakhala nawo m’malo aulemerero amenewa. (Yohane 14:2) Yohane anafotokoza ena mwa madalitso amene anthu amenewa adzasangalale nawo pamene ananena kuti: “Sikudzakhalanso temberero. Koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa udzakhala mumzindamo, ndipo akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulika kwa iye. Iwo adzaona nkhope yake, ndipo dzina lake lidzakhala pamphumi pawo.” (Chivumbulutso 22:3, 4) Ansembe a ku Isiraeli wakale atayamba kuchita zinthu mwachinyengo, Yehova anawatemberera. (Malaki 2:2) Komanso Yesu ananena kuti “nyumba” yopanda chikhulupiriro ya ku Yerusalemu inasiyidwa ndi Mulungu. (Mateyu 23:37-39) Koma mu Yerusalemu Watsopano ‘simudzakhalanso temberero.’ (Yerekezerani ndi Zekariya 14:11.) Onse amene adzakhale mmenemo amakumana ndi mayesero amene ali ngati moto padziko lapansi pano, ndipo akapambana mayeserowo, ‘amavala kusawonongeka ndiponso kusafa.’ Yehova akudziwa kuti anthu amenewa, mofanana ndi Yesu, adzapitiriza kumutumikira mokhulupirika ndipo sadzam’pandukira. (1 Akorinto 15:53, 57) Komanso “mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa” udzakhala mumzindawu, ndipo zimenezi zidzachititsa kuti mzindawu ukhale wotetezeka kwamuyaya.
28. N’chifukwa chiyani anthu amene adzapange Yerusalemu Watsopano adzalembedwe dzina la Mulungu pamphumi pawo, ndipo akuyembekezera mwayi uti wapadera kwambiri?
28 Mofanana ndi Yohane, anthu onse amene adzakhale mumzinda wakumwambawu ndi “akapolo” a Mulungu. Choncho dzina la Mulungu linalembedwa moonekera bwino pamphumi pawo, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti anthu amenewa ndi a Mulunguyo. (Chivumbulutso 1:1; 3:12) Iwo amaona kuti ndi mwayi wapadera kwambiri kukatumikira Mulungu kumwamba, monga mbali ya Yerusalemu Watsopano. Pamene Yesu anali padziko lapansi, analonjeza olamulira am’tsogolowa mwayi wapadera kwambiri. Iye anati: “Odala ndi anthu oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu.” (Mateyu 5:8) Akapolo amenewa adzasangalala kwambiri kuona Yehova maso ndi maso ndi kumulambira.
29. N’chifukwa chiyani Yohane ananena kuti “usiku sudzakhalakonso” mu Yerusalemu Watsopano wakumwamba?
29 Yohane anapitiriza kuti: “Komanso, usiku sudzakhalakonso. Sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwa Yehova Mulungu adzawaunikira.” (Chivumbulutso 22:5a) Mofanana ndi mzinda uliwonse padziko lapansi, mzinda wakale wa Yerusalemu unkadalira kuwala kwa dzuwa masana, ndipo usiku unkadalira kuwala kwa mwezi ndi nyale. Koma zounikira zimenezi sizidzafunikira mu Yerusalemu Watsopano wakumwamba chifukwa Yehova weniweniyo ndi amene azidzaunikira mzindawu. Mophiphiritsa, mawu akuti “usiku” angatanthauze tsoka kapena kuchoka kumbali ya Yehova. (Mika 3:6; Yohane 9:4; Aroma 13:11, 12) Koma m’malo aulemerero ndi owala mmene muli Mulungu wamphamvuyonse simungakhale usiku woterewu.
30. Kodi Yohane anati chiyani pomaliza kufotokoza masomphenya osangalatsawa, ndipo buku la Chivumbulutso likutitsimikizira chiyani?
30 Yohane anamaliza kufotokoza masomphenya osangalatsawa ponena za akapolo a Mulunguwa kuti: “Ndipo adzalamulira monga mafumu kwamuyaya.” (Chivumbulutso 22:5b) Pofika kumapeto kwa zaka 1,000, madalitso onse obwera chifukwa cha dipo adzakhala ataperekedwa, ndipo Yesu adzapereka mtundu wa anthu angwiro kwa Atate wake. (1 Akorinto 15:25-28) Koma sitikudziwa kuti Yehova adzapereka ntchito yotani kwa Yesu ndiponso a 144,000 pambuyo pa zimenezi. Komabe buku la Chivumbulutso likutitsimikizira kuti iwo adzapitiriza kuchita utumiki wopatulika kwa Yehova mpaka muyaya.
Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’Chivumbulutso
31. (a) Kodi mapeto a masomphenya a Yerusalemu Watsopano adzakhala otani? (b) Kodi Yerusalemu Watsopano adzachita chiyani kwa anthu ena okhulupirika?
31 Buku la Chivumbulutso likusonyeza kuti kukwaniritsidwa kwa masomphenya a Yerusalemu Watsopano, yemwe ndi mkwatibwi wa Mwanawankhosa, ndi mapeto osangalatsa, ndipo zimenezi n’zoyenereradi. Akhristu onse a m’nthawi ya Yohane, amene uthenga wa m’buku la Chivumbulutso unkapita kwa iwo poyamba, ankayembekezera kudzalowa mumzinda umenewu ndi matupi auzimu omwe sangafe, kuti akalamulire limodzi ndi Yesu Khristu. Akhristu odzozedwa amene adakali ndi moyo padziko lapansi masiku ano, nawonso akuyembekezera zimenezi. Choncho masomphenya a m’buku la Chivumbulutso adzafika pachimake penipeni, onse amene ali m’gulu la mkwatibwi akadzapita kumwamba kukakumana ndi Mwanawankhosa. Kenako, kudzera mwa Yerusalemu Watsopano, mtundu wa anthu udzalandira madalitso obwera chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu, moti pamapeto pake anthu onse okhulupirika adzalandira moyo wosatha. Mwanjira imeneyi mkwatibwi, yemwe ndi Yerusalemu Watsopano, adzagwira nawo ntchito yokonza dziko lapansi latsopano lolungama limene lidzakhalepo kwamuyaya. Iye adzathandizira mokhulupirika Mkwati wake yemwenso ndi Mfumu pogwira ntchito imeneyi. Zonsezi zidzabweretsa ulemerero wonse kwa Mulungu wathu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.—Mateyu 20:28; Yohane 10:10, 16; Aroma 16:27.
32, 33. Kodi taphunzira chiyani m’buku la Chivumbulutso, ndipo tiyenera kuchita chiyani ndi mtima wathu wonse?
32 Tikusangalala kwambiri pamene tatsala pang’ono kumaliza kuphunzira buku la Chivumbulutso. Taona kuti zonse zimene Satana ndi mbewu yake akhala akuchita pofuna kusokoneza komaliza atumiki a Mulungu, zidzalephereratu ndipo Yehova adzawonongeratu adani onse popereka chiweruzo chake cholungama. Babulo Wamkulu adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso mpaka kalekale. Kenako magulu enanso oipa a dziko la Satanali adzawonongedwa kotheratu. Ndiyeno Satanayo ndi ziwanda zake adzaponyedwa kuphompho ndipo pamapeto pake adzawonongedwa. Kenako Yerusalemu Watsopano adzalamulira limodzi ndi Khristu kuchokera kumwamba. Pa nthawiyi, akufa adzaukitsidwa ndipo anthu adzaweruzidwa. Pamapeto pake anthu amene adzakhalenso angwiro adzasangalala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Buku la Chivumbulutso lafotokoza zonsezi ndi masomphenya ochititsa chidwi kwambiri. Masiku ano, zimenezi zikutilimbikitsa ‘kulengeza uthenga wabwino wosatha monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.’ (Chivumbulutso 14:6, 7) Kodi mukugwira nawo ntchito yaikuluyi mwakhama?
33 Tsopano ndi mitima yoyamikira, tiyeni tikambirane mawu omaliza a m’buku la Chivumbulutso.
[Mawu a M’munsi]
a Mfundo yakuti mzindawo unayezedwa “malinga ndi muyezo wa munthu, umene ulinso wofanana ndi muyezo wa mngelo” mwina ikugwirizana ndi mfundo yakuti mzindawo wapangidwa ndi a 144,000, omwe poyamba anali anthu koma anasintha n’kukhala zolengedwa zauzimu, zofanana ndi angelo.
b Onani kuti “mumpukutu wa moyo, umene ndi wa Mwanawankhosa,” muli mayina a anthu 144,000 okha, omwe ndi Isiraeli wauzimu. Choncho mpukutu umenewu ndi wosiyana ndi “mpukutu wa moyo” umene watchulidwa m’mbuyomu, mmenenso muli mayina a anthu amene adzakhale ndi moyo padziko lapansi.—Chivumbulutso 20:12.
c Mawu akuti “mitundu ya anthu” nthawi zambiri amatanthauza anthu amene sali m’gulu la Isiraeli wauzimu. (Chivumbulutso 7:9; 15:4; 20:3; 21:24, 26) Choncho palembali, mawuwa sakutanthauza kuti anthu adzapitiriza kukhala m’mitundu yosiyanasiyana pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000.