Madzi Opatsa Moyo Wosatha
“Koma amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu mpang’ono pomwe, ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi otumphuka mwa iye opatsa moyo wosatha.”—YOHANE 4:14.
‘NDINANGOONA kuseri kwa mwezi kwatulukira kanthu kobulungira, kooneka ngati mwala wokongola wamtengo wapatali kwambiri, wokhala ndi mwina mwa buluu ndi mwina moyera, kakutuluka pang’onopang’ono kuchokera mu thambo lakuda bii.’—Anatero Edgar Mitchell, wasayansi ya zakuthambo pofotokoza momwe anaonera dzikoli ali m’mlengalenga.
N’chiyani chimachititsa dziko lathuli kukhala lokongola chonchi mpaka kuchititsa munthuyu kunena mawu osonyeza kugomawa? Madzi, amene ndi mbali yaikulu ya dziko lathuli, ndi amene amachititsa zimenezi. Madzi amapangitsa dziko lathuli kukhala lokongola; komanso amathandiza kuti zolengedwa zikhale ndi moyo. Ndipotu mbali yaikulu ya thupi lathu ndi madzi. N’chifukwa chake buku lina linati: “[Madzi] ndi ofunika kwambiri pa moyo, amathandiza kwambiri zomera ndi nyama zomwe.”—Encyclopædia Britannica.
Madzi satha padzikoli chifukwa chakuti madzi amene tawagwiritsa ntchito akayeretsedwa timadzawagwiritsanso ntchito nthawi ina. Buku lina linati: “Pafupifupi kadontho kalikonse ka madzi kamene timagwiritsa ntchito kamabwerera m’nyanja.” Bukuli linapitiriza kuti: “Madzi akatenthedwa ndi dzuwa kunyanja amasanduka nthunzi ndipo amapita kumwamba. Kenako amagwa monga mvula. Choncho madzi amagwiritsidwa ntchito mobwerezabwereza. Satha ntchito.” (The World Book Encyclopedia) Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, Baibulo linanena zimenezi motere: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” Kayendedwe ka madzi kameneka n’kodabwitsadi kwambiri.—Mlaliki 1:7.
Popeza kuti madzi ndi moyo komanso amapangidwa modabwitsa zedi, n’zosadabwitsa kuti Baibulo limawatchula maulendo oposa 700. Nthawi zambiri Baibulo limayerekezera madzi ndi Mawu a Mulungu, chifukwa chakuti zonse ndi zofunikira kwambiri pamoyo komanso zimayeretsa zinthu.—Yesaya 58:11; Yohane 4:14.
Baibulo Lili ndi Mphamvu Yoyeretsa
Aisiraeli ankadziwika kuti anali anthu aukhondo kwambiri chifukwa chakuti ankakonda kusamba komanso kuchapa. Analinso ndi mwambo wosamba m’mapazi polowa m’nyumba. (Luka 7:44) Aisiraeli ankagwiritsanso ntchito madzi pamwambo wawo kuti akhale oyera. Ansembe otumikira pa chihema ankafunika kusamba ndi kuchapa zovala zawo nthawi zonse. (Eksodo 30:18-21) Patapita nthawi, pakachisi wa ku Yerusalemu, Solomo anapanga “thawale” lamkuwa limene munkalowa madzi okwana malita 44,000. Madziwa anali okwanira kusamba ndi kuyeretsera zinthu mogwirizana ndi Chilamulo. (2 Mbiri 4:2, 6) Kodi zimenezi zikuwakhudza bwanji Akhristu masiku ano?
Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Yesu anayeretsa mpingo wachikhristu “ndi madzi mwa mawuwo.” Monga madzi amene amayeretsa thupi, choonadi cha Mawu a Mulungu chimayeretsa makhalidwe athu ndi moyo wathu wauzimu. Choncho, ophunzira a Khristu amakhala ‘oyera ndi opanda chilema.’ (Aefeso 5:25-27) N’chifukwa chake, onse ofuna kukondedwa ndi Mulungu ayenera kuyesetsa kukhala “opanda thotho, opanda chilema” mwakuthupi ndiponso mwauzimu. (2 Petulo 3:11, 14) Kodi Mawu a Mulungu amatithandiza bwanji kuchita zimenezi?
Anthu amene amafuna kusangalatsa Yehova Mulungu amamwa madzi auzimu mwa kuphunzira Baibulo nthawi zonse. Zimene akuphunzirazo zikawakhudza mtima, amayesetsa kuchita zimene Baibulo limanena zakuti: “Sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu.”—Aroma 12:2.
Kudziwa chifuniro cha Mulungu molondola kumathandiza anthu amenewa kuzindikira kuti zochita ndi maganizo awo zili ndi mathotho ofunika kuwachotsa. Akamagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo, Mawu a Mulungu amakhala ngati madzi chifukwa ‘amawasambitsa n’kukhala oyera’ ndipo amachotsa ngakhale machimo aakulu.—1 Akorinto 6:9-11.
Zimenezi n’zimene zinachitikira mnyamata wina wa ku Spain dzina lake Alfonso. Iye ankagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndipo anali chigawenga choopsa. Iye anati: “Ndili ndi zaka 18, moyo wanga sunali wosangalatsa chifukwa cha zimene ndinkachitira thupi langa komanso zimene ndinkachitira anthu ena. Motero, ndinkaona kuti ndine wodetsedwa.
“Kusukulu kwathu kunali mtsikana wina wa msinkhu wanga, waukhondo komanso wofatsa ndipo anali wosiyana kwambiri ndi ana ena. Mtsikana ameneyu ndiye anandithandiza kusintha khalidwe. Nthawi ina anandipempha kuti ndidzapite ku mpingo wa Mboni za Yehova. Kenako ndinayamba kuphunzira Baibulo n’kukhala paubwenzi ndi Mulungu. Pasanathe chaka, ndinasiyiratu makhalidwe anga oipa aja ndipo ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova. Nditasintha, makolo ambiri ankandipempha kuti ndiwathandizire ana awo omwe ankakonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.”
Madzi Opatsa Moyo Wosatha
Nthawi ina Yesu anauza mayi wachisamariya, yemwe ankatunga madzi pachitsime cha Yakobo, za “madzi amoyo.” Iye anati: “Amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu mpang’ono pomwe, ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi otumphuka mwa iye opatsa moyo wosatha.” (Yohane 4:10, 14) Mawu a Yesu amenewa akusonyeza kuti “madzi amoyo” akuimira zimene Mulungu wakonza kuti tikhale ndi moyo, zomwe zafotokozedwa m’Mawu ake, Baibulo. Chifukwa cha zimenezi, n’zotheka kuti anthu adzakhale ndi moyo wosatha. Mbali yofunika kwambiri ya madzi ophiphiritsa amenewa ndi nsembe ya dipo ya Yesu Khristu. Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Alfonso, yemwe tamutchula kale uja, anaona kuti “madzi amoyo” ochokera kwa Mulungu ndi ofunika kwambiri. Ponena za anzake ena amene anapitirizabe moyo wa uchigawenga ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, iye anati: “Mkulu wanga ndi anzanga onse anamwalira. Kuphunzira Mawu a Mulungu kunandipulumutsa. Ndili ndi moyo mpaka lero chifukwa cha zinthu zauzimu zimene Yehova amapereka.” Komanso, chifukwa cha zimene Alfonso waphunzira, iye akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza.—2 Petulo 3:13.
Tonse Tikuitanidwa
Buku lomaliza la Baibulo, limanena za “mtsinje wa madzi a moyo, oyera ngati kulusitalo, ukuyenda kuchokera ku mpando wachifumu wa Mulungu, ndi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 22:1) Mtsinjewu ukuimira zimene Mulungu wakonza n’cholinga chakuti anthu adzakhalenso ndi moyo wangwiro ngati umene Adamu ndi Hava anali nawo poyamba.
Atafotokoza za mtsinjewu, nkhaniyi ikupitiriza kupempha kuti: “Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Masiku ano, mawu amenewa akulengezedwa padziko lonse. Chaka chilichonse, Mboni za Yehova m’mayiko oposa 235 zimathera maola oposa 1 biliyoni pothandiza anthu kuphunzira mawu a m’Baibulo opatsa moyo.
Kodi muli ndi ludzu la madzi a moyo? Mukamamwa madzi oyera, kapena kuti mukamaphunzira za Mlengi wathu komanso mukamagwiritsa ntchito zinthu zimene watipatsa, inunso mungakhale m’gulu la anthu amene ‘akudzisungira okha maziko abwino a tsogolo lawo, kuti akagwire zolimba moyo weniweniwo.’—1 Timoteyo 6:19.
[Mawu Otsindika patsamba 14]
Mofanana ndi madzi amene amayeretsa thupi, choonadi cha m’Baibulo chimatha kuyeretsa makhalidwe ndi moyo wathu wauzimu
[Bokosi/Zithunzi patsamba 15]
MALO OTUNGA MADZI M’NTHAWI ZA M’BAIBULO
M’nthawi za m’Baibulo, anthu ankafunika kugwira ntchito zolimba kuti apeze madzi abwino akumwa. Cha ku Beereseba, Abulahamu ndi Isake anakumba zitsime kuti azikhala ndi madzi okwanira banja lawo ndi ziweto zawo.—Genesis 21:30, 31; 26:18.
Nthawi zambiri zitsime zosaya zimauma m’nthawi yotentha. Kuti anthu azikhala ndi madzi nthawi zonse ankafunika kukhala ndi zitsime zakuya. (Miyambo 20:5) Chitsime china ku Lakisi chinali chakuya mamita 44. Chitsime chinanso ku Gibeoni chinali chakuya mamita oposa 25 ndipo chinali chachikulu mamita 11 pakamwa pake. Pokumba chitsimechi anafukula miyala yokwana matani 3,000. Mayi wachisamariya yemwe anabwera kudzatunga madzi pa chitsime cha Yakobo anauza Yesu kuti: ‘Chitsimechi n’chozama.’ N’kutheka kuti anthu ankafunika kuponya chingwe cha mamita 23 kuti apeze madzi pachitsimechi.—Yohane 4:11.
Kale anthu a ku Middle East, analinso ndi zitsime zikuluzikulu zomwe ankasungiramo madzi a mvula, yomwe inkagwa kuyambira mwezi wa October mpaka April. Ankakumba ngalande kuchokera ku phiri kuti madzi amvulawo azikalowa m’zitsime zimenezi. Aisiraeli anakumba zitsime zikuluzikulu kuti azisungiramo madzi amenewa.—2 Mbiri 26:10.
Kutunga madzi pa chitsime ndi ntchito yaikulu. Akazi monga Rebeka ndiponso mwana wa Yetero ankagwira ntchito yabwino, yotungira madzi banja ndi ziweto zawo tsiku lililonse.—Genesis 24:15-20; Eksodo 2:16.
[Chithunzi patsamba 15]
Alfonso masiku ano, akulalikira Mawu a Mulungu