Mutu 44
Mmene Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso Akukukhudzirani
1. (a) Kodi mngelo uja anatsimikizira Yohane kuti chiyani ponena za malonjezo onse osangalatsa a m’buku la Chivumbulutso? (b) Kodi ndani amene ananena kuti “ndikubwera mofulumira,” ndipo ‘adzabwera’ nthawi iti?
PAMBUYO powerenga za Yerusalemu Watsopano, amene wafotokozedwa mosangalatsa kwambiri m’Baibulo, mwina mungafunse kuti: ‘Kodi zinthu zosangalatsa chonchizi zingachitikedi?’ Yohane akuyankha funso limeneli potiuza mawu otsatira amene mngelo uja ananena. Iye anati: “Kenako anandiuza kuti: ‘Mawu awa ndi odalirika ndiponso oona. Yehova, Mulungu wopereka mauthenga ouziridwa a aneneri, anatumiza mngelo wake kudzaonetsa akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa. Ndipo taonani! Ndikubwera mofulumira. Wodala ndi aliyense wosunga mawu a ulosi a mumpukutu uwu.’” (Chivumbulutso 22:6, 7) Malonjezo onse osangalatsa amene ali m’buku la Chivumbulutso adzakwaniritsidwadi. Mngeloyo, amene ankalankhula m’dzina la Yesu, ananena kuti Yesu akubwera posachedwapa, kapena kuti “mofulumira.” Pamenepa ayenera kuti akunena za nthawi imene Yesu adzabwere “ngati mbala” kudzawononga adani a Yehova, n’kubweretsa madalitso osangalatsa amene afotokozedwa m’masomphenya a m’buku la Chivumbulutso. (Chivumbulutso 16:15, 16) Choncho tiyenera kukhala moyo wogwirizana ndi mawu a “mumpukutu uwu,” kapena kuti m’buku la Chivumbulutso, kuti pa nthawiyo tidzatchedwe odala.
2. (a) Kodi Yohane anatani pambuyo poona masomphenya ochititsa chidwi a m’buku la Chivumbulutso, ndipo mngelo uja anamuuza kuti chiyani? (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mawu amene mngelo uja ananena, akuti “Samala!” ndiponso akuti, “Lambira Mulungu”?
2 Pambuyo poona masomphenya ochititsa chidwi kwambiriwa, m’pomveka kuti Yohane anagoma kwambiri. Iye anati: “Ine Yohane, ndine amene ndinali kumva ndi kuona zinthu zimenezi. Ndipo nditamva ndi kuona, ndinagwada n’kuwerama kuti ndilambire pamapazi a mngelo amene anali kundionetsa zinthu zimenezi. Koma iye anandiuza kuti: ‘Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako amene ndiwo aneneri, ndi wa anthu amene akusunga mawu a mumpukutu umenewu. Lambira Mulungu.’” (Chivumbulutso 22:8, 9; yerekezerani ndi Chivumbulutso 19:10.) Chenjezo loletsa kulambira angelo, limene laperekedwa kawiri m’buku la Chivumbulutso, linali lapanthawi yake m’masiku a Yohane. Izi zinali choncho chifukwa zikuoneka kuti anthu ena ankalambira angelo, kapena ankanena kuti aona masomphenya apadera ochokera kwa angelo. (1 Akorinto 13:1; Agalatiya 1:8; Akolose 2:18) Masiku ano, chenjezoli likutsindika mfundo yakuti tiyenera kulambira Mulungu yekha basi. (Mateyu 4:10) Sitiyenera kuipitsa kulambira koyera polambira munthu wina aliyense kapena chinthu china chilichonse.—Yesaya 42:5, 8.
3, 4. Kodi mngelo uja anapitiriza kumuuza chiyani Yohane, ndipo Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi achita chiyani pomvera mawu a mngeloyu?
3 Yohane anapitiriza kuti: “Anandiuzanso kuti: ‘Usatsekere mawu a ulosi a mumpukutu uwu, pakuti nthawi yoikidwiratu yayandikira. Amene akuchita zosalungama, achitebe zosalungama, ndipo wochita zonyansa apitirizebe kuchita zonyansazo. Koma wolungama achitebe chilungamo, ndipo woyera apitirizebe kuyeretsedwa.’”—Chivumbulutso 22:10, 11.
4 Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi masiku ano akumvera mawu a mngelo uja, ndipo sanatsekere mawu a ulosiwu. Mwachitsanzo, mu Nsanja ya Olonda yoyambirira yeniyeni [Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence (July 1879)] munali ndemanga zofotokozera mavesi ambiri a m’buku la Chivumbulutso. Monga tinaonera m’mutu woyambirira wa buku lino, pa zaka zambiri zapitazi, Mboni za Yehova zafalitsa mabuku ena othandiza anthu kumvetsa buku la Chivumbulutso. Tsopano m’buku lino tikufotokozera onse okonda choonadi maulosi ochititsa chidwi a m’buku la Chivumbulutso ndiponso mmene maulosiwo akukwaniritsidwira.
5. (a) Kodi chingachitike n’chiyani ngati anthu atasankha kusamvera machenjezo ndi malangizo a m’buku la Chivumbulutso? (b) Kodi anthu ofatsa ndi olungama ayenera kuchita chiyani?
5 Ngati anthu sakufuna kumvera machenjezo ndi malangizo a m’buku la Chivumbulutso, asiyeni achite zimene akufuna, chifukwa mngelo uja anati: “Amene akuchita zosalungama, achitebe zosalungama.” Ngati anthu asankha kuchita zinthu zonyansa zimene zafala m’dziko lolekerera makhalidwe onyansali, adzafa chifukwa cha zochita zawo zonyansazo. Posachedwapa, Yehova apereka chiweruzo ndi kuwonongeratu adani ake onse, ndipo woyambirira kuwonongedwa akhala Babulo Wamkulu. Anthu ofatsa ayenera kuchita khama pomvera mawu a mneneri Zefaniya akuti: “Bwerani kwa Yehova, . . . Yesetsani kukhala olungama, yesetsani kukhala ofatsa. Mwina mungadzabisike pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Zefaniya 2:3) Koma anthu amene anadzipereka kale kwa Yehova, mngelo uja akuwalimbikitsa kuti: “Wolungama achitebe chilungamo, ndipo woyera apitirizebe kuyeretsedwa.” Anthu anzeru amadziwa kuti zosangalatsa zakanthawi za uchimo sizingafanane ndi madalitso osatha amene anthu ochita chilungamo komanso oyera adzasangalale nawo. Baibulo likutilimbikitsa kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akorinto 13:5) Munthu aliyense adzalandira mphoto malinga ndi zimene wasankha kuchita pa moyo wake.—Salimo 19:9-11; 58:10, 11.
6. Kodi Yehova anati chiyani polankhula komaliza mu ulosiwu, kwa anthu owerenga buku la Chivumbulutso?
6 Tsopano Yehova, Mfumu yamuyaya, analankhula komaliza mu ulosiwu, kwa anthu owerenga buku la Chivumbulutso. Iye anati: “Taonani! Ndikubwera mofulumira, ndipo mphoto ndili nayo, yoti ndipereke kwa aliyense malinga ndi ntchito yake. Ine ndine Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto. Odala ndiwo amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndiponso kuti akalowe mumzindawo kudzera pazipata zake. Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu, amene amachita zamizimu, adama, opha anthu, opembedza mafano, ndi aliyense wokonda kulankhula ndi kuchita zachinyengo.”—Chivumbulutso 22:12-15.
7. (a) Kodi Yehova ‘akubwera mofulumira’ kudzachita chiyani? (b) N’chifukwa chiyani atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu sadzakhala ndi gawo lililonse mu Yerusalemu Watsopano?
7 Apanso, Yehova Mulungu akutsindika mfundo yakuti iye ndi mfumu yamuyaya ndiponso kuti pamapeto pake, adzakwaniritsa zolinga zake zimene wakhala nazo kuyambira pachiyambi penipeni. Iye ‘akubwera mofulumira’ kudzapereka chiweruzo ndipo adzapereka mphoto kwa anthu amene akumufunafuna ndi mtima wonse. (Aheberi 11:6) Mfundo zake zolungama n’zimene zidzamuthandize kudziwa amene akuyenera kulandira mphoto komanso amene akuyenera kulangidwa. Atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu akhala akuchita zinthu ngati “agalu opanda mawu,” ndipo amalekerera makhalidwe oipa amene Yehova wawafotokoza palembali. (Yesaya 56:10-12; onaninso mawu a m’munsi pa Deuteronomo 23:18.) Iwo ‘amakonda’ kuphunzitsa zinthu zabodza ndiponso kuchita zinthu zachinyengo ndipo safuna ngakhale pang’ono kumvera malangizo a Yesu opita ku mipingo 7 ija. Choncho, iwo sadzakhala ndi gawo lililonse mu Yerusalemu Watsopano.
8. (a) Kodi ndani okha amene ali ndi “ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo,” ndipo zimenezi zikutanthauza chiyani? (b) Kodi a khamu lalikulu ‘achapa bwanji mikanjo yawo’ ndipo ayenera kuchita chiyani kuti akhalebe oyera pamaso pa Mulungu?
8 Akhristu odzozedwa amenedi “achapa mikanjo yawo” kuti akhale oyera pamaso pa Yehova, ndi okhawo amene ali ndi “ufulu wa kudya zipatso za m’mitengo ya moyo.” Zimenezi zikutanthauza kuti iwo amapatsidwa mphamvu ndi ulamuliro woti adzalandire moyo umene sungafe m’malo awo kumwamba. (Yerekezerani ndi Genesis 3:22-24; Chivumbulutso 2:7; 3:4, 5.) Anthu amenewa akamwalira, amaukitsidwa n’kukalowa mu Yerusalemu Watsopano. Angelo 12 aja amawalola kuti alowe, koma salola kuti mumzindawu mulowe munthu aliyense amene amanena mabodza kapena amene amachita zinthu zodetsa, ngakhale kuti iye amanena kuti ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba. Nawonso a khamu lalikulu amene ali padziko lapansi “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa,” ndipo ayenera kupitiriza kukhala oyera pamaso pa Mulungu. Iwo angachite zimenezi popewa makhalidwe oipa amene Yehova akuwafotokoza palembali. Komanso, iwo ayenera kumvera malangizo amene Yesu anapereka m’mauthenga ake 7 opita ku mipingo ija.—Chivumbulutso 7:14; Chivumbulutso chaputala 2 ndi 3.
9. Kodi Yesu analankhula mawu otani, ndipo uthenga wake komanso buku lonse la Chivumbulutso, choyamba zikupita kwa ndani?
9 Yehova atatha kulankhula, Yesu nayenso analankhula. Iye ananena mawu olimbikitsa anthu a mtima wabwino owerenga buku la Chivumbulutso, kuti: “Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kudzachitira umboni zinthu izi kwa inu, kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.” (Chivumbulutso 22:16) Zoonadi, mawuwa kwenikweni ndi ‘othandiza mipingo.’ Uthenga umenewu choyamba ndi wopita ku mpingo wa Akhristu odzozedwa padziko lapansi. Zonse zimene zili m’buku la Chivumbulutso choyamba zikupita kwa Akhristu odzozedwa, amene adzakhale mu Yerusalemu Watsopano. Ndipo kudzera mwa mpingo umenewu, nawonso a khamu lalikulu ali ndi mwayi womvetsa mfundo zosangalatsa za choonadi za mu ulosiwu.—Yohane 17:18-21.
10. N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti iye ndi (a) “muzu ndi mbadwa ya Davide”? (b) “nthanda yonyezimira”?
10 Yesu Khristu anapatsidwa udindo woulula masomphenya a m’buku la Chivumbulutso kwa Yohane. Kenako Yohaneyo anaulula masomphenyawo ku mpingo. Yesu ndi “muzu [komanso] mbadwa ya Davide.” Iye anabadwira m’banja la Davide monga munthu, choncho ndi woyenera kukhala Mfumu ya Ufumu wa Yehova. Ndipo iye adzakhalanso “Atate Wosatha” wa Davide, choncho adzakhala “muzu” wa Davide. (Yesaya 9:6; 11:1, 10) Iye ndiye Mfumu ya m’banja la Davide yomwe idzakhalapo mpaka kalekale komanso yomwe singafe, ndipo adzakwaniritsa pangano la Yehova kwa Davide. Komanso iye ndi “nthanda yonyezimira” imene inanenedweratu m’masiku a Mose. (Numeri 24:17; Salimo 89:34-37) Iye ndi “nthanda” imene inatuluka n’kuchititsa kuti m’bandakucha ufike. (2 Petulo 1:19) Zinthu zonse zachinyengo zimene Babulo Wamkulu, yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu, wayesera kuchita sizinalepheretse nthanda yaulemereroyi kutuluka.
Nenani Kuti: “Bwera!”
11. Kodi tsopano Yohane ananena mawu otani oitana anthu onse, ndipo ndani amene angabwere atamva kuitanako?
11 Tsopano Yohane nayenso analankhula. Poyamikira ndi mtima wonse zinthu zonse zimene anaona ndi kumva, iye anati: “Mzimu ndi mkwatibwi akunenabe kuti: ‘Bwera!’ Aliyense wakumva anene kuti: ‘Bwera!’ Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Madalitso obwera chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu sadzapita kwa a 144,000 okha, chifukwa apa Yohane akuitana anthu onse. Mzimu wa Yehova umagwira ntchito mwa anthu a m’gulu la mkwatibwi, ndipo mothandizidwa ndi mzimuwu, iwo akupitiriza kulengeza uthenga womveka bwino kwambiri wakuti: ‘Imwani madzi a moyo kwaulere.’ (Onaninso Yesaya 55:1; 59:21.) Aliyense amene ali ndi ludzu la chilungamo akuitanidwa kuti “abwere” adzalandire madalitso ochokera kwa Yehova. (Mateyu 5:3, 6) Anthu onse amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko lapansi, omwe akubweradi atamva kuitana kwa Akhristu odzozedwa, ndi amwayi kwambiri.
12. Kodi anthu a khamu lalikulu achita chiyani atamva mawu oitana opezeka pa Chivumbulutso 22:17?
12 Kuyambira chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, anthu ambiri a khamu lalikulu, amene akuwonjezerekawonjezerekabe, akhala akubwera ‘atamva’ kuitana kumeneku. Mofanana ndi akapolo anzawo odzozedwa, iwo achita zinthu zowapangitsa kuti akhale oyera pamaso pa Yehova. Iwo akulakalaka nthawi imene Yerusalemu Watsopano adzatsike kumwamba n’kubweretsa madalitso ku mtundu wa anthu. Anthu a khamu lalikulu amva uthenga wolimbikitsa kwambiri wa m’buku la Chivumbulutso ndipo akunena nawo mawu oti “Bwera!” Koma sikuti iwo akungonena mawu amenewa, chifukwa akugwira ntchito mwakhama posonkhanitsira anthu ku gulu la Yehova ndi kuwaphunzitsa kuti nawonso azilengeza nawo uthenga wakuti: “Aliyense wakumva ludzu abwere.” Choncho chiwerengero cha anthu a khamu lalikulu chikupitiriza kukwera. Panopa anthu oposa 7 miliyoni a m’gulu limeneli m’mayiko 236 padziko lonse, akugwira ntchito yoitana anthu kuti “amwe madzi a moyo kwaulere.” Iwo akugwira ntchito imeneyi limodzi ndi Akhristu odzozedwa a m’gulu la mkwatibwi osakwana 12,000.
13. Kodi Yesu anapereka chenjezo lotani?
13 Kenako, Yesu analankhulanso ndipo anati: “Ine ndikuchitira umboni kwa aliyense wakumva mawu a ulosi wa mumpukutuwu, kuti: Wina akawonjezera pa zimenezi, Mulungu adzamuwonjezera miliri yolembedwa mumpukutuwu. Ndipo wina akachotsa kalikonse pa mawu a mumpukutu wa ulosi umenewu, Mulungu adzachotsa gawo lake pa zolembedwa mumpukutuwu, kutanthauza kuti sadzamulola kudya zipatso za m’mitengo ya moyo, ndipo sadzamulola kulowa mumzinda woyerawo.”—Chivumbulutso 22:18, 19.
14. Kodi Akhristu odzozedwa amauona bwanji “ulosi” wa m’buku la Chivumbulutso?
14 Akhristu odzozedwa ayenera kuuza anthu za “ulosi” wa m’buku la Chivumbulutso. Iwo sayenera kubisa ulosiwu kapena kuwonjezerapo chilichonse. Ndipo uthenga wa mu ulosiwu uyenera kulengezedwa poyera, kuchokera “pamadenga.” (Mateyu 10:27) Popeza kuti buku la Chivumbulutso ndi louziridwa ndi Mulungu, kodi ndani angalimbe mtima kusintha mawu amene Mulungu walankhula yekha ndi kuwatumiza kudzera mwa Yesu Khristu, yemwe panopa ndi Mfumu yomwe ikulamulira? Ndithudi munthu wochita zimenezi sayenera kudzalandira mphoto ya moyo, ndipo ayenera kulandira nawo miliri imene idzagwere Babulo Wamkulu komanso dziko lonse lapansili.
15. Kodi mawu amene Yesu ananena akuti iye “akuchitira umboni zinthu zimenezi,” ndiponso akuti ‘akubwera mofulumira,’ akutanthauza chiyani?
15 Tsopano Yesu ananena mawu omaliza olimbikitsa, akuti: “Amene akuchitira umboni zinthu zimenezi akuti, ‘Inde, ndikubwera mofulumira.’” (Chivumbulutso 22:20a) Yesu ndi “mboni yokhulupirika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Choncho ngati akuchitira umboni masomphenya a m’buku la Chivumbulutso, ndiye kuti masomphenyawa ndi oona. Yehova Mulungu ndi Yesu akutsindika mobwerezabwereza kuti akubwera “mofulumira,” kapena kuti posachedwapa, ndipo palembali Yesu akunena mawu amenewa kachisanu. (Chivumbulutso 2:16; 3:11; 22:7, 12, 20) Iwo ‘akubwera’ kudzapereka chiweruzo kwa hule lalikulu lija, kwa “mafumu” a ndale ndiponso kwa anthu ena onse amene amatsutsana ndi “ufumu wa Ambuye wathu [Yehova] ndi wa Khristu wake.”—Chivumbulutso 11:15; 16:14, 16; 17:1, 12-14.
16. Popeza mwadziwa kuti Yehova Mulungu ndi Yesu akubwera mofulumira, kodi muyenera kutsimikiza kuchita chiyani?
16 Kudziwa kuti Yehova Mulungu ndi Yesu akubwera mofulumira, kuyenera kukulimbikitsani “kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” (2 Petulo 3:12) Ngakhale kuti zinthu za m’dziko la Satanali zingaoneke ngati zokhalitsa, zangokhala zakanthawi chabe. Ndipo zinthu zomwe zingaoneke ngati zikuyenda bwino pansi pa ulamuliro wa kumwamba, kumene kukuimira olamulira a dzikoli amene ali m’manja mwa Satana, nazonso n’zosakhalitsa. Zinthu zonsezi zichoka posachedwapa. (Chivumbulutso 21:1) Koma zinthu zokhalitsa sitingazipeze kwina kupatulapo kwa Yehova, mu Ufumu wake wolamulidwa ndi Yesu Khristu, ndiponso m’dziko latsopano limene iye walonjeza. Choncho musamaiwale mfundo imeneyi.—1 Yohane 2:15-17.
17. Kodi muyenera kuchita chiyani poyamikira mfundo yakuti Yehova ndi woyera?
17 Chotero zimene mwaphunzira m’buku la Chivumbulutso muyenera kuzigwiritsa ntchito kwambiri pa moyo wanu. Kodi pamene munaphunzira za masomphenya ofotokoza za kumwamba kumene Yehova amakhala, simunagome ndi ulemerero waukulu ndiponso kuyera kwa Mlengi wathu? (Chivumbulutso 4:1–5:14) Ndi mwayitu waukulu kwambiri kutumikira Mulungu wotero. Chifukwa choyamikira kwambiri mfundo yakuti Mulungu ndi woyera, muyenera kutsatira mosamala malangizo amene Yesu anapereka ku mipingo 7 ija. Choncho muyenera kupewa zinthu monga kukonda kwambiri chuma, kulambira mafano, chiwerewere, kukhala wofunda mwauzimu, magulu ampatuko, kapena chinthu china chilichonse chimene chingapangitse kuti Yehova asavomereze utumiki wanu. (Chivumbulutso 2:1–3:22) Mawu amene mtumwi Petulo analembera Akhristu odzozedwa akugwiranso ntchito kwa anthu a khamu lalikulu. Iye anati: “Khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse.”—1 Petulo 1:15, 16.
18. Kodi muyenera kugwira nawo ndi mtima wonse ntchito yotani, ndipo n’chifukwa chiyani ntchito imeneyi ikufunika kugwiridwa mwachangu masiku ano?
18 Komanso, kudziwa zimenezi kukulimbikitseni kuchita khama kwambiri pamene mukulengeza “za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima, ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu.” (Yesaya 35:4; 61:2) Kaya ndinu a kagulu kankhosa kapena a khamu lalikulu, yesetsani kugwira nawo ndi mtima wonse monga momwe mungathere, ntchito yolengeza za kukhuthulidwa kwa mbale 7 za mkwiyo wa Yehova, zimene zili ndi mauthenga a Mulungu oweruza dziko la Satanali. Pa nthawi yomweyomweyo, gwirani nawo ntchito yosangalatsa yolengeza za uthenga wabwino wosatha wonena za Ufumu wa Yehova ndi wa Khristu wake, womwe unakhazikitsidwa. (Chivumbulutso 11:15; 14:6, 7) Gwirani ntchito imeneyi mwachangu. Komanso, pozindikira kuti tili m’tsiku la Ambuye, anthu ambiri amene padakali pano sanayambe kutumikira Yehova ayenera kuyamba kugwira nawo ntchito yolengeza uthenga wabwino. Tikuwapempha anthu amenewa kuti afike podzipereka kwa Mulungu n’kubatizidwa. Kumbukirani kuti “nthawi yoikidwiratu ili pafupi.”—Chivumbulutso 1:3.
19. Kodi mtumwi Yohane, yemwe anali wokalamba, anamaliza buku la Chivumbulutso ndi mawu oti chiyani, ndipo inu mukuti chiyani pomva mawu amenewa?
19 Choncho tikugwirizana ndi Yohane popemphera kuchokera pansi pa mtima kuti: “Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.” Ndipo mtumwi wokalambayu anawonjezera kuti: “Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu Khristu kukhale ndi oyerawo.” (Chivumbulutso 22:20b, 21) Ndipo kukoma mtima kwakukulu kukhalenso ndi nonsenu amene mukuwerenga buku lino. Khalani ndi chikhulupiriro kuti mapeto osangalatsa a masomphenya a m’buku la Chivumbulutso ali pafupi. Khalani ndi chikhulupiriro chimenechi kuti nanunso mudzathe kunena nafe limodzi mochokera pansi pa mtima kuti, “Ame.”
[Chithunzi patsamba 314]
“Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu . . . ”
[Chithunzi patsamba 315]
“Odala ndiwo amene . . . akalowe mumzindawo kudzera pazipata zake”