Tizithandiza Abale a Khristu Mokhulupirika
“Pa mlingo umene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munachitira ine amene.”—MAT. 25:40.
1, 2. (a) Kodi Yesu anafotokoza mafanizo ati kwa ophunzira ake? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi tikambirana mafunso ati ofunika kwambiri okhudza fanizo la nkhosa ndi mbuzi?
YESU anafotokozera Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane fanizo la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, anamwali 10 ndiponso la matalente. Pomaliza, anafotokoza fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Iye ananena za nthawi imene “Mwana wa munthu” adzaweruze “mitundu yonse ya anthu.” Ophunzira ake ayenera kuti anachita chidwi kwambiri ndi fanizoli. Mu fanizoli Yesu anafotokoza za gulu la anthu amene ali ngati nkhosa ndi lina la anthu ngati mbuzi. Koma pali gulu lina lofunika kwambiri lomwe analitchula kuti “abale” a “mfumu.”—Werengani Mateyu 25:31-46.
2 Atumiki a Yehova akhala akuchita chidwi ndi fanizoli chifukwa limafotokoza zimene zidzachitikire anthu m’tsogolomu. Yesu anafotokoza zimene zidzachititse kuti anthu ena apeze moyo wosatha ndipo ena awonongedwe. Choncho kuti tikapeze moyo wosatha tiyenera kumvetsa bwino fanizoli ndi kutsatira mfundo zake. Ndiyeno tingafunse kuti: Kodi Yehova wakhala akutithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la fanizo la nkhosa ndi mbuzi? N’chifukwa chiyani tinganene kuti fanizoli likusonyeza kufunika kwa ntchito yolalikira? Kodi ndani ayenera kulalikira? Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okhulupirika kwa “mfumu” ndiponso ‘abale ake’?
KODI TASINTHA BWANJI MMENE TIMAFOTOKOZERA FANIZOLI?
3, 4. (a) Kodi tiyenera kudziwa zinthu ziti zofunika zokhudza fanizo la nkhosa ndi mbuzi? (b) Kodi Nsanja ya Olonda ya 1881 inafotokoza bwanji fanizoli?
3 Kuti timvetse bwino fanizo la nkhosa ndi mbuzi tiyenera kudziwa zinthu zitatu zofunika. Tiyenera kudziwa anthu otchulidwa, nthawi ya chiweruzo komanso zifukwa zimene zingachititse munthu kukhala nkhosa kapena mbuzi.
4 Nsanja ya Olonda ya 1881 inanena kuti “Mwana wa munthu,” kapena kuti “mfumu,” ndi Yesu. Ophunzira Baibulo oyambirira ankaganiza kuti mawu oti “abale anga” amaimira anthu amene adzalamulire ndi Khristu komanso anthu ena onse amene adzakhala angwiro padzikoli. Iwo ankaganiza kuti nkhosa ndi mbuzi zidzalekanitsidwa pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Ankaganizanso kuti anthu adzaweruzidwa kuti ndi nkhosa chifukwa chotsatira lamulo la Mulungu la chikondi.
5. Kodi m’ma 1920, Yehova anathandiza bwanji anthu ake kumvetsa fanizoli?
5 Kumayambiriro kwa m’ma 1920, Yehova anathandiza anthu ake kumvetsa fanizoli. Nsanja ya Olonda ya October 15, 1923, sinasinthe zoti “Mwana wa munthu” ndi Yesu. Koma inafotokoza kuchokera m’Malemba kuti abale a Khristu ndi okhawo amene adzalamulire naye kumwamba. Inanenanso kuti nkhosa zikuimira anthu amene adzakhale padzikoli n’kumalamuliridwa ndi Ufumu wa Khristu. Koma kodi inanena kuti nkhosa ndi mbuzi zidzalekanitsidwa liti? Nkhaniyi inafotokoza kuti abale a Khristu adzakhala akulamulira kumwamba pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1,000. Choncho inanena kuti pa nthawiyo sangathandizidwe kapena kunyalanyazidwa ndi anthu padzikoli. Ndiyeno inati nkhosa ndi mbuzi zidzalekanitsidwa Ulamuliro wa Zaka 1,000 usanayambe. Inanenanso zoti anthu adzaweruzidwa kuti ndi nkhosa chifukwa chakuti amamvera Yesu monga Ambuye wawo komanso amakhulupirira kuti Ufumu udzathetsa mavuto.
6. Kodi zimene tinkadziwa pa fanizoli zinasintha bwanji m’ma 1990?
6 Izi zinachititsa anthu a Yehova kuganiza kuti anthu akuweruzidwa kukhala nkhosa kapena mbuzi m’masiku otsiriza ano. Ankaonanso kuti anthuwo akuweruzidwa chifukwa cha zimene amachita akamva uthenga wabwino. Koma m’ma 1990 tinasintha zimene tinkaganizazo. Mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995 munali nkhani ziwiri zimene zinafotokoza kufanana pakati pa mawu a Yesu pa Mateyu 24:29-31 (Werengani.) ndi pa Mateyu 25:31, 32. (Werengani.)a Ndiyeno nkhani yoyamba inanena kuti kuweruza nkhosa ndi mbuzi kudzachitika m’tsogolo. Inati kudzachitika chisautso chachikulu chotchulidwa pa Mateyu 24:29, 30 chikadzayamba ndiponso Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake. Nkhaniyo inanenanso kuti amenewa adzakhala mapeto a dziko loipali ndipo pa nthawiyo Yesu adzaweruza anthu onse.
7. Kodi masiku ano tikudziwa chiyani pa fanizo la nkhosa ndi mbuzi?
7 Masiku ano tikudziwa bwino tanthauzo la fanizo la nkhosa ndi mbuzi. “Mwana wa munthu,” kapena kuti “mfumu,” ndi Yesu. Mawu oti “abale anga” akuimira abale ndi alongo odzozedwa amene adzalamulire ndi Khristu kumwamba. (Aroma 8:16, 17) “Nkhosa” ndi “mbuzi” zikuimira anthu ochokera m’mitundu yonse. Iwo si odzozedwa ndi mzimu woyera. Nanga kodi anthuwo adzaweruzidwa pa nthawi iti? Izi zidzachitika chakumapeto kwa chisautso chachikulu chimene chikubwera posachedwapa. Kodi anthuwo adzaweruzidwa kuti ndi nkhosa kapena mbuzi pa zifukwa ziti? Iwo adzaweruzidwa chifukwa cha zimene achitira abale a Yesu padziko lapansi. Panopa mapeto a dzikoli ali pafupi kwambiri. Choncho timayamikira kwambiri kuti Yehova wakhala akutithandiza kumvetsa tanthauzo la mafanizo otchulidwa pa Mateyu chaputala 24 ndi 25.
FANIZOLI LIKUSONYEZA KUFUNIKA KWA NTCHITO YOLALIKIRA
8, 9. N’chifukwa chiyani Yesu amaona kuti anthu amene ali ngati nkhosa ndi ‘olungama’?
8 Mu fanizo la nkhosa ndi mbuzi, Yesu sanatchule ntchito yolalikira. Ndiyeno n’chifukwa chiyani tinganene kuti fanizoli likusonyeza kufunika kwa ntchitoyi?
9 Choyamba, tiyenera kukumbukira kuti zimene Yesu ankanenazi ndi fanizo chabe. Iye sankanena zosiyanitsa nkhosa zenizeni ndi mbuzi zenizeni. Choncho sankatanthauza kuti nkhosa zikuimira anthu amene adzachitedi zinthu monga kupereka chakudya ndi zovala kwa abale akewo, kuwasamalira kapena kukawaona kundende. M’malomwake, ankatanthauza mtima umene anthuwo angasonyeze abale ake. Yesu amaona kuti anthu amene ali ngati nkhosa ndi ‘olungama.’ Amatero chifukwa chakuti amazindikira kuti Yesu ali ndi gulu la odzozedwa padzikoli ndipo iwo amathandiza odzozedwawo mokhulupirika m’masiku otsiriza ano.—Mat. 10:40-42; 25:40, 46; 2 Tim. 3:1-5.
10. Kodi nkhosa zingasamalire bwanji abale a Khristu?
10 Chachiwiri, tiyenera kukumbukira kuti Yesu ankafotokoza chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a dziko loipali. (Mat. 24:3) Chakumayambiriro, Yesu ananena kuti mbali ina ya chizindikirochi ndi yoti uthenga wabwino wa Ufumu “udzalalikidwa padziko lonse lapansi.” (Mat. 24:14) Ndiyeno asananene fanizo la nkhosa ndi mbuzi, ananena fanizo la matalente. Mu nkhani yapita ija, tinanena kuti Yesu anapereka fanizo la matalente pofuna kusonyeza kuti ‘abale ake’ odzozedwa ayenera kugwira mwakhama ntchito yolalikira. Pa nthawi ino ya kukhalapo kwa Yesu, odzozedwa ochepa amene adakali padzikoli ali ndi ntchito yaikulu kwambiri. Iwo ayenera kulalikira kwa anthu a “mitundu yonse” mapeto asanafike. Ndiyeno fanizo la nkhosa ndi mbuzi limasonyeza kuti odzozedwawa azithandizidwa. Choncho tingasamalire abale a Khristu amenewa powathandiza pa ntchito yolalikirayi. Ndiyeno kodi tingawathandize bwanji? Kodi tizingowapatsa zinthu zina ndiponso kuwalimbikitsa basi?
KODI NDANI AYENERA KULALIKIRA?
11. Kodi tingafunse funso liti, ndipo n’chifukwa chiyani tingalifunse?
11 Masiku ano, pali Akhristu 8 miliyoni ndipo ambiri mwa iwo si odzozedwa. Choncho sali m’gulu la akapolo odzozedwa amene anapatsidwa matalente. (Mat. 25:14-18) Ndiyeno funso n’kumati, ‘Kodi anthu amene sanadzozedwe ndi mzimu woyera ayeneranso kugwira nawo ntchito yolalikira?’ Inde. Tiyeni tione zifukwa zake.
12. Kodi tikuphunzira chiyani pa mawu a Yesu pa Mateyu 28:19, 20?
12 Yesu anauza ophunzira ake onse kuti azilalikira. Yesu ataukitsidwa anauza ophunzira ake kuti akaphunzitse anthu kuti azisunga “zinthu zonse zimene” iye anawalamulira. Chinthu chimodzi chimene anawalamulira n’chakuti azilalikira. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Choncho ophunzira onse a Khristu, kaya akuyembekezera kukalamulira kumwamba kapena kudzakhala padzikoli, ayenera kulalikira.—Mac. 10:42.
13. Kodi masomphenya amene Yohane anaona akusonyeza chiyani? Fotokozani.
13 Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti odzozedwa pamodzi ndi a nkhosa zina ayenera kugwira ntchito yolalikira. Yesu anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya osonyeza “mkwatibwi” akuitana anthu kuti “amwe madzi a moyo kwaulere.” Mkwatibwiyu akuimira odzozedwa 144,000 omwe adzalamulire ndi Khristu kumwamba. (Chiv. 14:1, 3; 22:17) Madzi a moyowa akuimira zimene Yehova wachita kuti amasule anthu ku uchimo ndi imfa pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Khristu. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16; 1 Yoh. 4:9, 10) Mfundo yofunika kwambiri mu uthenga umene timalalikira ndi yokhudza dipolo komanso mmene lingathandizire anthu. Odzozedwa akutsogolera pa ntchito yolalikira uthengawu. (1 Akor. 1:23) M’masomphenyawo, Yohane anaonanso anthu ena amene sali m’gulu la mkwatibwi. Nawonso anauzidwa kuti anene kuti: “Bwera!” Iwo anamvera n’kumaitananso anthu ena kuti amwe madzi a moyo. Gulu lachiwirili ndi la anthu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli. Choncho buku la Chivumbulutso likusonyeza kuti anthu onse amene avomera ‘kubwera’ ali ndi udindo wolalikira.
14. Kodi tingamvere bwanji “chilamulo cha Khristu”?
14 Anthu onse otsatira “chilamulo cha Khristu” ayenera kulalikira. (Agal. 6:2) Yehova amafuna kuti atumiki ake onse azimvera malamulo ake. Kumbukirani kuti anauza Aisiraeli kuti: “Lamulo lililonse ligwire ntchito mofanana kwa mbadwa ndi kwa mlendo wokhala pakati panu.” (Eks. 12:49; Lev. 24:22) N’zoona kuti Akhristu sayenera kutsatira Chilamulo cha Mose. Koma tonsefe, kaya ndife odzozedwa kapena ayi, tiyenera kutsatira “chilamulo cha Khristu.” Zonse zimene Yesu anaphunzitsa zili m’chilamulo chimenechi. Ndipo mfundo yofunika imene Yesu anaphunzitsa ndi yakuti otsatira ake ayenera kukondana. (Yoh. 13:35; Yak. 2:8) Njira yabwino kwambiri imene timasonyezera kuti timakonda Yehova, Yesu ndiponso anzathu ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu.—Yoh. 15:10; Mac. 1:8.
15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti otsatira onse a Khristu ayenera kumvera lamulo lake?
15 Yesu ankatha kuuza anthu ochepa zinthu zokhudza anthu ambiri. Mwachitsanzo, iye anachita pangano la Ufumu ndi ophunzira ake 11 okha. Koma odzozedwa onse 144,000 ali m’panganoli. (Luka 22:29, 30; Chiv. 5:10; 7:4-8) N’chimodzimodzinso ndi lamulo loti otsatira ake azilalikira. Iye ataukitsidwa anaonekera kwa anthu ochepa okha n’kuwauza lamulo limeneli. (Mac. 10:40-42; 1 Akor. 15:6) Koma ophunzira ake onse m’nthawi ya atumwi anazindikira kuti ayenera kumvera lamuloli ngakhale kuti iwo kunalibe pamene Yesu ankalipereka. (Mac. 8:4; 1 Pet. 1:8) Masiku anonso, Yesu sanauze mwachindunji Akhristu 8 miliyoni kuti azilalikira. Koma onsewa amazindikira kuti ayenera kukhulupirira Khristu ndiponso kugwira ntchito yolalikira.—Yak. 2:18.
TIYENERA KUKHALA OKHULUPIRIKA PANOPA
16-18. (a) Kodi a “nkhosa zina” angathandize bwanji abale a Khristu? (b) N’chifukwa chiyani ayenera kuchita zimenezi panopa?
16 Panopa Satana akulimbana kwambiri ndi odzozedwa omwe adakali padzikoli. Iye awonjezera kuchita zimenezi chifukwa “kanthawi kochepa” kamene watsala nako kakutha. (Chiv. 12:9, 12, 17) Ngakhale kuti odzozedwawa akuvutitsidwa ndi Satana, iwo akuchitabe khama kwambiri potsogolera ntchito yolalikira padziko lonse. N’zosakayikitsa kuti Yesu akuwathandiza kugwira ntchitoyi.—Mat. 28:20.
17 A “nkhosa zina” akuwonjezeka ndipo amaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza abale a Khristu pa ntchito yolalikira ndiponso m’njira zina. Mwachitsanzo, amapereka ndalama ndiponso kuthandiza pomanga Nyumba za Ufumu, malo a msonkhano ndi maofesi a nthambi. Iwo amamveranso abale amene amasankhidwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azitsogolera m’gulu la Yehova.—Mat. 24:45-47; Aheb. 13:17.
18 Posachedwapa, angelo adzasiya kugwira mphepo zowononga kuti chisautso chachikulu chiyambe. Zimenezi zidzachitika odzozedwa onse omwe ali padzikoli atadindidwa chidindo chomaliza. (Chiv. 7:1-3) Ndiyeno Aramagedo isanayambe, odzozedwa onse adzatengedwa kupita kumwamba. (Mat. 13:41-43) Choncho, anthu onse omwe akufuna kudzaweruzidwa ngati nkhosa ayenera kuthandiza abale a Khristu mokhulupirika panopa.
a Kuti mumve zonse werengani nkhani yakuti “Kodi Mudzaima Motani ku Mpando wa Chiweruzo?” ndiponso yakuti “Kodi Nkhosazo ndi Mbuzizo Zili ndi Mtsogolo Motani?” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995.