Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi Akristu ena odzozedwa adzapulumuka ‘chisautso chachikulu’ kudzakhala pa dziko lapansi m’dziko latsopano asanatengedwe kupita kumwamba?
Kunena mwa gogogo, Baibulo silimanena tero.
Kwa nthaŵi yaitali Akristu akhala okondweretsedwa m’mwaŵi umene Mulungu waufutukulira kwa iwo. (Machitidwe 1:6) Chimenecho chakhala chowona makamaka m’nthaŵi yathu chiyambire kukhazikitsidwa kwa Ufumu. (Mateyu 24:3, 24, 34) Popeza kuti mapeto a dongosolo ili loipa adzabwera m’nthaŵi yawo, Akristu azizwa kuti kaya ena odzozedwa ndi mzimu angakhale ndi moyo kupyola ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu’ ndi kudzatumikira padziko lapansi kwa kanthaŵi asanalandire mphotho yawo yakumwamba. (Chibvumbulutso 16:14) Baibulo silimanena kuti izi zidzachitika, komabe zitsanzo zina ndi maulosi zatengedwa kusonyeza kuti ichi chingachitike. M’malo mokhala oumirira, tingadikire kudzawona mmene Mulungu adzasamalirira zinthu.
Zochitika zina Zabaibulo zimakhala ndi zofanana nazo pambuyo pake pakati pa anthu a Mulungu. Mwachitsanzo, timadziŵa kuti Yona anali m’chinsomba chachikulu kwa usana utatu ndi usiku utatu. Anthu ena angawone chimenecho kungokhala chitsanzo cha chipulumutso chaumulungu, koma Yesu anati chinali chitsanzo chaulosi cha mmene iye akakhalira m’manda kwa nyengo yofananayo chiukiriro chake chisanadze. (Yona 1:17; Mateyu 12:40) Inde, chokumana nacho cha Yona chinali chiphiphiritso chaulosi. Momvekera, atumiki a Mulungu ayang’ana ku maulosi ndi mbiri zakutizakuti za m’Baibulo kuwona ngati izi zimasonyeza mmene Yehova adzachitira nawo.
Monga chitsanzo chokhudza ulosi wa Baibulo, The Watch Tower ya December 15, 1928, inafotokoza Mika 5:2-15. Bukhu la Mika linafotokoza za kusakaza Samariya kochitidwa ndi ‘Asuri’ ndi kubwerera kwa Ayuda kuchokera ku ndende ya ku Babulo. (Mika 1:1, 5-7; 4:10) Koma inaloza ku zochitika zapambuyo pake, monga ngati kubadwa kwa Mesiya m’Betelehemu. (Mika 5:2) Mika analosera kuti pambuyo pa chipulumutso chawo kuchokera kwa “Asuri,” “otsala a Yakobo” adzakhala ‘ngati mame ochokera kwa Yehova’ ndipo “ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa.” (Mika 5:6-8) The Watch Tower inathirira ndemanga iyi: “Zimenezi zingaonedwe monga chisonyezero chakuti ena a otsalira adzakhala padziko lapansi ngakhale Harmagedo itamenyedwa ndipo pa nthaŵi imeneyo adzakhala ndi ntchito ina yowonjezereka yochita m’dzina la Ambuye ndi ku chitamando chake ndi ulemerero.” Onani chinenero chodzichepetsa, cholingalira chogwiritsiridwa ntchito kusonyeza kuthekera kumeneku: “Zimenezi zingawonedwe monga chisonyezero.”
Kodi bwanji ponena za mbiri ya m’Baibulo imene ingafanane ndi kupulumuka koteroko padziko lapansi? Chitsanzo chimodzi chimene chaperekedwa chimakhudza Nowa ndi banja lake. Nowa wawonedwa kukhala akuimira Yesu m’nthaŵi ino yamapeto. (Genesis 6:8-10; Mateyu 24:37) Monga momwe Nowa anatsogozera mkazi wake ndi ana awo atatu ndi azipongozi awo kupyola mapeto a dongosolo lakale limenelo, Kristu adzapereka utsogoleri kwa gulu lake la mkwatibwi la otsalira ndi awo amene akhala ana a “Atate Wosatha,” Yesu. Mkazi wa Nowa anapulumuka Chigumula ndi kukhala ndi phande m’kukonzanso kulambira kowona padziko lapansi loyeretsedwa. Kufanana nako kungakhale kupulumuka kuloŵa m’dziko latsopano kwa otsalira a gulu la mkwatibwi.—Yesaya 9:6, 7; 2 Akorinto 11:2; Chibvumbulutso 21:2, 9.a
Mbiri zina Zabaibulo zawonedwanso kukhala zikulingalira kuti odzozedwa ena angadzakhale ndi moyo kuloŵa m’dziko latsopano. Mwachitsanzo, Yeremiya anapulumuka kuwonongedwa kwa Yerusalemu; “munthu” wokhala ndi zolembera anatsala kuwona ntchito yakuphayo asanapite kukapereka lipoti lake.—Ezekieli 9:4, 8, 11.
Ndemanga zonena za kuthekera kwakuti odzozedwa ena angapulumuke kuloŵa m’dziko latsopano zapangidwa ndi zolinga zabwino ndiponso ndi chiunikiro cha zochitika Zabaibulo poyesera kumvetsetsa maulosi kapena zitsanzo zimene zingakhale ndi kukwaniritsidwa kwa mtsogolo. Ngati zidzachitika kuti palibe wodzozedwa amene adzasiyidwa pa dziko lapansi, sipadzakhala chifukwa chokhalira wosakhutira. Tavomereza kale kuti nkhani Zabaibulo zimamvedwa bwino lomwe ndi kupita kwa nthaŵi. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya January 15, 1982, inafotokozanso Mika 5:6-9 ndipo inalongosola kuti “otsalira a Aisrayeli auzimu sanafunikire kuyembekezera kufikira pambuyo pa . . . Harmagedo kuti akhale ngati ‘mame’ otsitsimutsa kwa anthu.” Kufotokoza kumeneku kunaperekanso kuthekera kwakuti otsalira angapulumuke nkhondo yaikulu ya Mulungu ndipo kwa kanthaŵi “adzapitiriza kukhala monga ‘mame’ otsitsimutsa kwa ‘khamu lalikulu’ la ‘nkhosa zina.’” Komabe, tikuwona kuti kupita kwa nthaŵi ndi kuwonjezeka kwa kuwala kwauzimu kungakulitse ndi kusintha kumvetsetsa kwathu kwa ulosi kapena madrama a Baibulo.—Miyambo 4:18.
Tikudziŵa kuti Baibulo limagwirizanitsa ‘kudza kwa Mwana wa munthu’ ndi ‘kusonkhanitsidwa kwa osankhidwa ku mphepo zinayi.’ (Mateyu 24:29-31) Ndiponso, mkati mwa “kufikanso kwa Ambuye” m’ulamuliro Waufumu, odzozedwa ogona m’imfa akuukitsidwira ku moyo kumwamba. (1 Atesalonika 4:15, 16) Anthu osindikizidwa chizindikiro ameneŵa ali kumeneko kuti adzakhale mbali ya mkazi wa Mwanawankhosa. Kodi zimenezo zidzachitika liti?
M’bukhu la Chibvumbulutso, mwamsanga pambuyo pakuti Yohane walongosola za kupha kwa Mulungu mkazi wachigololo wachipembedzo, Babulo Wamkulu, iye akulongosola za “ukwati wa Mwanawankhosa.” “Mkazi” wonyansa, wachiŵereŵere wachotsedwa padziko, ndipo tikuwona “mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa” ‘wovala bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.’ (Chibvumbulutso 18:10; 19:2, 7, 8; 21:9) Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu kuli mbali ya chisautso chachikulu. (Mateyu 24:21; Chibvumbulutso 7:14) Chotero chingalingaliridwe kuti ena a gulu la mkwatibwi adzapulumuka chisautso chachikulu monga umboni wa chivomerezo ndi chitetezo cha Yehova. (Zefaniya 2:3; yerekezerani ndi Mateyu 24:22.) Motero ngati iwo adzapulumutsidwa pa dziko lapansi, iwo adzakhala pompano kufikira Mulungu atasankha kuwatengera kumwamba.
Komabe, kalongosoledwe ka m’Chibvumbulutso sikali m’ndondomeko yosamalitsa. Ndipo uku sindiko kuti otsalira ochepa a odzozedwa adzafunikira kutsogoza zinthu m’dziko latsopano, popeza kuti iwo aphunzitsa kale mamiliyoni a Akristu okhulupirika amene adzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi. Mofananamo, Mulungu angatengere kumwamba odzozedwa ake mwamsanga pambuyo pa kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, kukhazikitsa maziko kuti “ukwati wa Mwanawankhosa” uchitike. Mwakutero oyera mtima onse akakhala ndi phande limodzi ndi Kristu ‘m’kulamulira mitundu ndi ndodo yachitsulo’ m’kuikumbutsa za chisautso chachikulu. (Chibvumbulutso 2:26, 27; 19:11-21) Ngati mmenemo ndi mmene Mulungu adzasamalira zinthu, anthu onse 144,000 adzakhala ndi Yesu ‘kuchita ufumu pamodzi ndi Kristu zaka chikwi.’—Chibvumbulutso 20:4.
Nchabwinodi kuti anthu a Mulungu ngosangalatsidwa kwambiri m’kusunzumira kuwona mmene adzatsogozera ndi kufupa atumiki ake. (Yerekezerani ndi 1 Petro 1:12.) Ichi chikusonyeza chidaliro chawo chakuti chifuniro chake chidzachitidwa. Ngakhale kuti sitingakhale ndipo sitiyenera kukhala oumirira ponena za tsatanetsatane, tingayang’ane kutsogolo ndi chidwi ku zimene zidzachitika.
[Mawu a M’munsi]
a Yerekezerani ndi You May Survive Armageddon Into God’s New World, masamba 61, 292, 351; “Your Will Be Done on Earth,” tsamba 347; The Watchtower ya May 1, 1942, tsamba 133. (Zonsezi nzofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.)