-
“Gwirabe Mwamphamvu Chimene Uli Nacho”Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
-
-
17 Mu 1918, ‘sunagoge wa Satana’ wa masiku ano anayamba kutsutsa kwambiri Akhristu odzozedwa, ngati mmene zinachitikira ndi mpingo wolimba wa ku Filadefiya. Atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, amene ankanena kuti ndi Ayuda auzimu, mwaukathyali ananyengerera olamulira kuti ayambe kuzunza Akhristu oona. Komabe Akhristu oonawo anayesetsa ‘kusunga mawu onena za kupirira kwa Yesu.’ Choncho popeza kuti iwo anathandizidwa mwauzimu kapena kuti anapatsidwa “mphamvu zochepa” zomwe zinawathandiza kwambiri, anapirira ndipo analimbikitsidwa kuti alowe pakhomo limene linali litawatsegukira. Kodi khomo limeneli linawatsegukira motani?
‘Khomo Lotseguka’
18. Kodi Yesu anapereka udindo kwa ndani mu 1919, ndipo amene anapatsidwa udindowo akufanana bwanji ndi mtumiki wokhulupirika wa Hezekiya?
18 M’chaka cha 1919, Yesu anakwaniritsa lonjezo lake ndipo anavomereza gulu laling’ono la Akhristu odzozedwa enieni kuti akhale “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Akhristu amenewa anapatsidwa mwayi wofanana ndi umene mtumiki wokhulupirika Eliyakimu anali nawo m’nthawi ya Mfumu Hezekiya.d Ponena za Eliyakimu, Yehova anati: “Ndidzaika makiyi a nyumba ya Davide paphewa pake. Iye akatsegula palibe amene azidzatseka ndipo akatseka palibe amene azidzatsegula.” Eliyakimu ankachita zinthu zofunika kwambiri potumikira Hezekiya, mwana wa m’banja lachifumu la Davide. Mofanana ndi zimenezi, masiku ano Akhristu odzozedwa ali ndi “makiyi a nyumba ya Davide” paphewa lawo, kutanthauza kuti apatsidwa udindo woyang’anira zinthu zapadziko lapansi za Ufumu wa Mesiya. Yehova walimbikitsa atumiki akewa kuti akwanitse udindo umenewu ndipo wachulukitsa mphamvu zawo zochepa kuti akwanitse kugwira ntchito yaikulu yolalikira padziko lonse.—Yesaya 22:20, 22; 40:29.
19. Kodi Akhristu odzozedwa anachita zotani pokwaniritsa utumiki umene Yesu anawapatsa mu 1919, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
19 Kuyambira mu 1919 kupita m’tsogolo, Akhristu odzozedwa amene adakali ndi moyo padziko lapansi akhala akutsanzira Yesu pogwira mwakhama ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse. (Mateyu 4:17; Aroma 10:18) Poona zimenezi, ena amene anali m’Matchalitchi Achikhristu, omwe ndi sunagoge wa Satana wa masiku ano, anabwera kwa Akhristu odzozedwawa ndipo analapa. Iwo ‘anagwada ndi kuweramira’ Akhristu amenewa posonyeza kuti akuvomereza udindo umene kapolo wokhulupirikayu ali nawo. Chotero nawonso anayamba kutumikira Yehova limodzi ndi Akhristu odzozedwa achikulire. Anthu amenewa anapitiriza kubwera mpaka pamene chiwerengero chonse cha Akhristu odzozedwa, amene ndi abale ake a Yesu, chinakwanira. Tsopano, “khamu lalikulu la anthu, . . . lochokera m’dziko lililonse” likubwera ‘kudzagwada ndi kuweramira’ kapolo wodzozedwayu. (Chivumbulutso 7:3, 4, 9) Kapolo ameneyu pamodzi ndi khamu lalikulu apanga gulu limodzi la Mboni za Yehova.
-
-
“Gwirabe Mwamphamvu Chimene Uli Nacho”Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
-
-
25. Kodi Mkhristu aliyense masiku ano angagwiritsire ntchito bwanji mfundo zimene zili m’malangizo amene Yesu anapereka ku mpingo wa ku Filadefiya?
25 Uthenga umenewu uyenera kuti unalimbikitsa kwambiri Akhristu okhulupirika a ku Filadefiya. Ndipo uthengawu ulinso ndi mfundo zothandiza kwambiri kwa Akhristu odzozedwa masiku ano, mkati mwa tsiku la Ambuye. Koma mfundo zimene zili mu uthengawu n’zofunikanso kwa Mkhristu aliyense, kaya ndi wodzozedwa kapena wa nkhosa zina. (Yohane 10:16) Aliyense wa ife ayenera kupitiriza kubala zipatso za Ufumu ngati mmene anachitira Akhristu a ku Filadefiya. Tonsefe tili ndi mphamvu zochepa zotithandiza kukwanitsa kutumikira Yehova m’njira inayake. Choncho tiyeni tigwiritse ntchito mphamvu zimenezi. Ngati tikufuna kuwonjezera utumiki wathu pa ntchito yokhudza Ufumu, tiyeni tikhale tcheru kuti tilowe pakhomo lililonse la mwayi wa utumiki limene lingatitsegukire. Ndipo tingathenso kupemphera kuti Yehova atitsegulire khomo limenelo. (Akolose 4:2, 3) Tikamatsanzira Yesu pa nkhani ya kupirira ndiponso tikamachita zinthu mogwirizana ndi dzina lake, tidzasonyeza kuti ifenso makutu athu akumva zimene mzimu woyera wa Mulungu ukunena ku mipingo.
-