Mutu 12
“Gwirabe Mwamphamvu Chimene Uli Nacho”
FILADEFIYA
1. Kodi uthenga wa Yesu wa nambala 6 unapita kumpingo umene unali mumzinda uti, ndipo dzina la mzindawo limatanthauza chiyani?
KUKONDA ABALE ndi khalidwe labwino kwambiri. Zikuoneka kuti Yesu ankaganizira khalidwe limeneli pamene ankapereka uthenga wake wa nambala 6. Uthenga umenewu unkapita kumpingo wa mumzinda wa Filadefiya ndipo dzina limeneli limatanthauza “Kukonda Abale.” Yohane amene anali wokalamba, ankakumbukirabe zimene zinachitika zaka zoposa 60 m’mbuyomo, pamene Petulo anauza Mbuye wake Yesu katatu konse kuti amamukonda kwambiri. (Yohane 21:15-17) Koma kodi Akhristu a ku Filadefiya ankakonda abale awo? Zikuoneka kuti ankawakonda.
2. Kodi mzinda wa Filadefiya unali wotani, ndipo mumzindawu munali mpingo wotani? Nanga Yesu anati chiyani kwa mngelo wa mpingo umenewu?
2 Mzinda wa Filadefiya wa m’nthawi ya Yohane unali wotukuka ndipo unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 50 kum’mwera chakum’mawa kwa mzinda wa Sade (kumene panopa kuli mzinda wa Alasehir m’dziko la Turkey). Koma chimene chinali chochititsa chidwi mumzindawu chinali chakuti mpingo wachikhristu umene unali kumeneko unali wolimba. Akhristu kumeneko ayenera kuti anasangalala kwambiri kulandira mtumiki amene anabwera kumpingo wawo, mwina pochokera ku Sade. Mu uthenga umene mtumikiyu anawabweretsera munali malangizo amphamvu. Koma choyamba uthengawo unasonyeza kuti wachokera kwa munthu wamphamvu komanso waudindo waukulu. Munthu waudindoyo anati: “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Filadefiya, lemba kuti: Izi ndi zimene akunena woyerayo, amene ali woona, yemwe ali ndi kiyi wa Davide. Iye amene amati akatsegula palibe wina amene angatseke, ndipo akatseka palibe wina amene angatsegule.”—Chivumbulutso 3:7.
3. N’chifukwa chiyani m’pake kuti Yesu akutchedwa “woyera,” ndipo n’chifukwa chiyani tinganene kuti iye ndi “woona”?
3 M’mbuyomo, Yohane anamva Petulo akuuza Yesu Khristu ali padziko lapansi, kuti: “Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha. Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.” (Yohane 6:68, 69) Popeza kuti Yehova Mulungu ndi woyera kwambiri kuposa wina aliyense, ndiye kuti Mwana wake wobadwa yekha nayenso ndi “woyera.” (Chivumbulutso 4:8) Komanso Yesu ndi “woona.” Mawu achigiriki (a·le·thi·nosʹ) amene anawamasulira kuti “woona” palembali amatanthauza chinthu chenicheni osati chachinyengo. Choncho potengera tanthauzo limeneli, Yesu ndi kuwala kwenikweni komanso chakudya chenicheni chochokera kumwamba. (Yohane 1:9; 6:32) Iye ndi mtengo wa mpesa weniweni. (Yohane 15:1) Komanso Yesu ndi woona chifukwa chakuti ndi wodalirika ndipo nthawi zonse amanena zoona. (Onani Yohane 8:14, 17, 26.) Choncho Mwana wa Mulungu ameneyu ndi woyeneradi kukhala Mfumu ndiponso Woweruza.—Chivumbulutso 19:11, 16.
“Kiyi wa Davide”
4, 5. Kodi “kiyi wa Davide” anali wogwirizana ndi pangano liti?
4 Yesu ali ndi “kiyi wa Davide.” Pogwiritsa ntchito kiyi ameneyu, iye “akatsegula palibe wina amene angatseke, ndipo akatseka palibe wina amene angatsegule.” Kodi “kiyi wa Davide” ameneyu n’chiyani?
5 Yehova anachita pangano la ufumu wosatha ndi Mfumu Davide ya Isiraeli. (Salimo 89:1-4, 34-37) Davide ndi anthu ena a m’banja lake anayamba kukhala pampando wachifumu wa Yehova ku Yerusalemu kuyambira m’chaka cha 1070 B.C.E., mpaka m’chaka cha 607 B.C.E. Koma kenako Mulungu anapereka chiweruzo pa ufumuwo chifukwa chakuti unayamba kuchita zinthu zoipa. Choncho Yehova anayamba kukwaniritsa ulosi wake wopezeka pa Ezekieli 21:27 wakuti: “Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu [kapena kuti Yerusalemu wapadziko lapansi]. Ufumu umenewu [kapena kuti ndodo yachifumu ya mafumu a m’banja la Davide] sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga, ndipo ndidzaupereka kwa iye.”
6, 7. Kodi “amene ali woyenerera mwalamulo” anaonekera liti ndipo anaonekera bwanji?
6 Kodi “amene ali woyenerera mwalamulo” ameneyu anaonekera liti ndipo anaonekera bwanji? Nanga anapatsidwa bwanji ndodo yachifumu ya ufumu wa Davide?
7 Patapita zaka pafupifupi 600, namwali wina wachiyuda dzina lake Mariya, amene anali mbadwa ya Mfumu Davide, anatenga pakati mwa mphamvu ya mzimu woyera. Mulungu anatumiza mngelo Gabirieli kuti akauze Mariya kuti adzabereka mwana wamwamuna, ndipo adzam’patse dzina lakuti Yesu. Gabirieli ananenanso kuti: “Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake. Iye adzalamulira monga mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya, moti ufumu wake sudzatha konse.”—Luka 1:31-33.
8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali woyenerera kulowa ufumu wa Davide?
8 Yesu atabatizidwa mumtsinje wa Yorodano ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera mu 29 C.E., anasankhidwa kuti adzakhale Mfumu ya m’banja la Davide. Yesu anapereka chitsanzo chabwino polalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu ndipo analamulanso ophunzira ake kuti azigwira ntchito imeneyi. (Mateyu 4:23; 10:7, 11) Yesu anadzichepetsa mpaka analolera kuphedwa pamtengo wozunzikirapo. Zimenezi zinasonyeza kuti analidi woyenerera kulowa ufumu wa Davide. Yehova anaukitsa Yesu ndipo anam’patsa thupi lauzimu limene silingafe, komanso anamuika pamalo apamwamba kudzanja lake lamanja kumwamba. Kumeneko Yesu anapatsidwa mphamvu zonse za ufumu wa Davide. Posachedwapa iye agwiritsira ntchito mphamvu zimenezi ‘popita kukagonjetsa anthu pakati pa adani ake.’—Salimo 110:1, 2; Afilipi 2:8, 9; Aheberi 10:13, 14.
9. Kodi Yesu amagwiritsira ntchito bwanji kiyi wa Davide potsegula ndiponso kutseka?
9 Panopa Yesu wagwiritsira ntchito kiyi wa Davide potsegulira anthu mwayi wolandira madalitso a Ufumu wa Mulungu. Kudzera mwa Yesu, Yehova wapulumutsa Akhristu odzozedwa ku “ulamuliro wa mdima” padziko lapansi n’kuwasamutsira “mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa.” (Akolose 1:13, 14) Yesu amagwiritsiranso ntchito kiyi ameneyu potchingira aliyense amene wasonyeza kusakhulupirika kuti asalandire madalitso amenewa. (2 Timoteyo 2:12, 13) Yesu, amene sadzachoka pampando wachifumu wa Davide mpaka kalekale, amathandizidwa ndi Yehova. Choncho palibe aliyense amene angamulepheretse kugwiritsa ntchito kiyiyo m’njira imeneyi.—Yerekezerani ndi Mateyu 28:18-20.
10. Kodi Yesu analimbikitsa bwanji mpingo wa ku Filadefiya?
10 Mawu a Yesu opita kwa Akhristu a ku Filadefiya ayenera kuti anali olimbikitsa kwambiri chifukwa chakuti iye anali munthu waudindo waukulu. Iye anayamikira mpingowo kuti: “Ndikudziwa ntchito zako. Taona! Ndakutsegulira khomo pamaso pako, limene wina sangalitseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa, ndiponso kuti unasunga mawu anga. Ndikudziwanso kuti wakhala wokhulupirika ku dzina langa.” (Chivumbulutso 3:8) Akhristu a mumpingowu ankagwira ntchito mwakhama, ndipo khomo linawatsegukira. Mosakayikira khomo limeneli linali la mwayi wautumiki. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 16:9; 2 Akorinto 2:12.) Choncho, Yesu analimbikitsa mpingowo kuti ugwiritsire ntchito mokwanira mwayi wolalikira. Akhristuwo anapirira komanso anasonyeza kuti anali okonzeka kupitiriza kugwira “ntchito” zina mu utumiki wa Yehova, ngati mzimu wa Mulungu utawathandiza. (2 Akorinto 12:10; Zekariya 4:6) Iwo anamvera zimene Yesu anawalamula ndipo sanakane Khristu, kaya ndi mawu kapena ndi zochita zawo.
“Iwo Adzakugwadira”
11. Kodi Yesu analonjeza Akhristu kuti adzawapatsa madalitso otani, ndipo lonjezo limeneli linakwaniritsidwa bwanji?
11 Choncho Yesu anawalonjeza kuti adzawapatsa madalitso. Iye anati: “Taona! Anthu ochokera m’sunagoge wa Satana, amene amanama kuti ndi Ayuda pamene si Ayuda, ndidzawachititsa kuti abwere kudzagwada ndi kuwerama pamapazi ako. Ndipo ndidzawachititsa kudziwa kuti ndimakukonda.” (Chivumbulutso 3:9) Mofanana ndi Akhristu a ku Simuna, mwina Akhristu a mpingo umenewu ankavutitsidwa ndi Ayuda akumeneko. Yesu ananena kuti Ayuda amenewa ndi ‘sunagoge wa Satana.’ Komabe, ena mwa Ayudawa anali atatsala pang’ono kuzindikira kuti zimene Akhristu ankalalikira zokhudza Yesu zinali zoona. Mwina iwo anabwera “kudzagwada ndi kuwerama” m’njira imene Paulo anaifotokoza pa 1 Akorinto 14:24, 25, moti analapa n’kukhala Akhristu. Iwo anazindikira chikondi chachikulu chimene Yesu anasonyeza popereka moyo wake chifukwa cha ophunzira ake.—Yohane 15:12, 13.
12. N’chifukwa chiyani Ayuda a m’sunagoge wa ku Filadefiya ayenera kuti anadabwa atamva kuti ena a iwo ‘adzagwada ndi kuweramira’ Akhristu akumeneko?
12 Ayuda a m’sunagoge wa ku Filadefiya ayenera kuti anadabwa atamva kuti ena mwa iwo ‘adzagwada ndi kuweramira’ Akhristu akumeneko. Mosakayikira mumpingo wa ku Filadefiya munali Akhristu ambiri omwe sanali Ayuda. Choncho Ayudawo akanayembekezera kuti Akhristuwo ndi amene akuyenera ‘kugwada ndi kuweramira’ Ayudawo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yesaya analosera kuti: “Mafumu [omwe si achiyuda] adzakhala okusamalira [osamalira Aisiraeli], ndipo ana awo aakazi adzakhala okuyamwitsira ana ako. Iwo adzakugwadira mpaka nkhope zawo pansi.” (Yesaya 49:23; 45:14; 60:14) Nayenso Zekariya anauziridwa kulemba kuti: “M’masiku amenewo, amuna 10 [omwe si Ayuda] ochokera m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwira chovala cha munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zekariya 8:23) Inde, anthu a mitundu ina ndi amene ankayenera kugwada ndi kuweramira Ayuda, osati Ayudawo kuweramira anthu a mitundu ina.
13. Kodi ndi Ayuda ati amene anayenera kuona kukwaniritsidwa kwa maulosi opita kwa Aisiraeli?
13 Maulosi amenewo ankapita ku mtundu umene Mulungu anausankha. Pa nthawi imene maulosiwa ankanenedwa, mtundu wa Isiraeli ndi umene unali wosankhidwa ndi Mulungu. Koma Ayuda atakana Mesiya, nayenso Yehova anawakana. (Mateyu 15:3-9; 21:42, 43; Luka 12:32; Yohane 1:10, 11) M’malomwake, pa Pentekosite mu 33 C.E., iye anasankha Isiraeli weniweni wa Mulungu, yemwe ndi mpingo wachikhristu. Anthu a mumpingo umenewu ndi Ayuda auzimu ndipo anachita mdulidwe weniweni, wa mumtima. (Machitidwe 2:1-4, 41, 42; Aroma 2:28, 29; Agalatiya 6:16) Choncho, chinthu chimodzi chokha chimene Ayuda enieni akanachita kuti akhalenso paubwenzi ndi Yehova chinali kukhulupirira Yesu, yemwe ndi Mesiya. (Mateyu 23:37-39) Zikuoneka kuti ena mwa Ayuda a ku Filadefiya anali pafupi kuchita zimenezi.a
14. Kodi malemba a Yesaya 49:23 ndi Zekariya 8:23 akwaniritsidwa bwanji mwapadera m’nthawi yathu ino?
14 M’nthawi yathu ino, ulosi ngati wa pa Yesaya 49:23 ndi pa Zekariya 8:23 wakwaniritsidwa mwapadera kwambiri. Anthu ambiri alowa pakhomo lotseguka la utumiki wa Ufumu chifukwa chakuti Akhristu odzozedwa akugwira mwakhama ntchito yolalikira.b Ambiri mwa anthu amenewa atuluka m’Matchalitchi Achikhristu amene amanama kuti ndi Isiraeli wauzimu. (Yerekezerani ndi Aroma 9:6.) Anthu amenewa akupanga khamu lalikulu, ndipo akuchapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa pokhulupirira magazi ansembe a Yesu. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Iwo amamvera Ufumu wa Khristu ndipo akuyembekezera kudzalandira madalitso a Ufumuwo padziko lapansi pompano. Tinganene kuti iwo amabwera kwa Akhristu odzozedwa, omwe ndi abale ake a Yesu, ‘kudzagwada ndi kuwaweramira’ chifukwa chakuti ‘anamva kuti Mulungu ali ndi iwo.’ Anthuwa amatumikira odzozedwawo ndipo amagwirizana nawo chifukwa onse ali pa ubale wapadziko lonse.—Mateyu 25:34-40; 1 Petulo 5:9.
“Ola la Kuyesedwa”
15. (a) Kodi Yesu anawalonjeza chiyani Akhristu a ku Filadefiya, ndipo anawalimbikitsa kuchita chiyani? (b) Kodi Akhristuwo ankayembekezera kudzalandira “mphoto” yotani?
15 Yesu anapitiriza kunena kuti: “Popeza unasunga mawu onena za kupirira kwanga, inenso ndidzakusunga pa ola la kuyesedwa, limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Ndidzakusunga pa ola limene likubwera kudzayesa okhala padziko lapansi. Ndikubwera mofulumira. Gwirabe mwamphamvu chimene uli nacho, kuti wina asakulande mphoto yako.” (Chivumbulutso 3:10, 11) Ngakhale kuti Akhristu a m’nthawi ya Yohane sanakhalebe ndi moyo mpaka kudzafika m’tsiku la Ambuye (lomwe linayamba mu 1914), iwo sankakayikira kuti Yesu adzabwera, ndipo zimenezi zinawapatsa mphamvu kuti apitirizebe kulalikira. (Chivumbulutso 1:10; 2 Timoteyo 4:2) Iwo ankayembekezera kukalandira “mphoto” ya moyo wosatha kumwamba. (Yakobo 1:12; Chivumbulutso 11:18) Ngati anakhalabe okhulupirika mpaka imfa, ndiye kuti analandiradi mphoto imeneyo.—Chivumbulutso 2:10.
16, 17. (a) Kodi “ola la kuyesedwa, limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu” n’chiyani? (b) Kodi zinthu zinali bwanji kwa Akhristu odzozedwa pamene “ola la kuyesedwa” linkayamba?
16 Koma kodi “ola la kuyesedwa” n’chiyani? Sitikukayikira kuti Akhristu a ku Asia amenewo anapitiriza kuzunzidwa kwambiri ndi ufumu wa Roma.c Komabe, ola la kuyesedwa limeneli linakwaniritsidwa kwambiri mu ola la kupetedwa ndi kuweruzidwa limene linayamba m’tsiku la Ambuye, ndipo linafika pachimake kuyambira m’chaka cha 1918 mpaka m’tsogolo. Cholinga cha mayesero amenewa n’chofuna kudziwa amene ali kumbali ya Ufumu wa Mulungu ndiponso amene ali kumbali ya dziko la Satanali. Mayeserowa ndi a nthawi yochepa kapena kuti “ola” limodzi lokha, koma sanathebe. Choncho tisaiwale kuti tili mu “ola la kuyesedwa” kufikira ola limeneli litatha.—Luka 21:34-36.
17 Mu 1918, ‘sunagoge wa Satana’ wa masiku ano anayamba kutsutsa kwambiri Akhristu odzozedwa, ngati mmene zinachitikira ndi mpingo wolimba wa ku Filadefiya. Atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, amene ankanena kuti ndi Ayuda auzimu, mwaukathyali ananyengerera olamulira kuti ayambe kuzunza Akhristu oona. Komabe Akhristu oonawo anayesetsa ‘kusunga mawu onena za kupirira kwa Yesu.’ Choncho popeza kuti iwo anathandizidwa mwauzimu kapena kuti anapatsidwa “mphamvu zochepa” zomwe zinawathandiza kwambiri, anapirira ndipo analimbikitsidwa kuti alowe pakhomo limene linali litawatsegukira. Kodi khomo limeneli linawatsegukira motani?
‘Khomo Lotseguka’
18. Kodi Yesu anapereka udindo kwa ndani mu 1919, ndipo amene anapatsidwa udindowo akufanana bwanji ndi mtumiki wokhulupirika wa Hezekiya?
18 M’chaka cha 1919, Yesu anakwaniritsa lonjezo lake ndipo anavomereza gulu laling’ono la Akhristu odzozedwa enieni kuti akhale “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Akhristu amenewa anapatsidwa mwayi wofanana ndi umene mtumiki wokhulupirika Eliyakimu anali nawo m’nthawi ya Mfumu Hezekiya.d Ponena za Eliyakimu, Yehova anati: “Ndidzaika makiyi a nyumba ya Davide paphewa pake. Iye akatsegula palibe amene azidzatseka ndipo akatseka palibe amene azidzatsegula.” Eliyakimu ankachita zinthu zofunika kwambiri potumikira Hezekiya, mwana wa m’banja lachifumu la Davide. Mofanana ndi zimenezi, masiku ano Akhristu odzozedwa ali ndi “makiyi a nyumba ya Davide” paphewa lawo, kutanthauza kuti apatsidwa udindo woyang’anira zinthu zapadziko lapansi za Ufumu wa Mesiya. Yehova walimbikitsa atumiki akewa kuti akwanitse udindo umenewu ndipo wachulukitsa mphamvu zawo zochepa kuti akwanitse kugwira ntchito yaikulu yolalikira padziko lonse.—Yesaya 22:20, 22; 40:29.
19. Kodi Akhristu odzozedwa anachita zotani pokwaniritsa utumiki umene Yesu anawapatsa mu 1919, ndipo zotsatira zake zinali zotani?
19 Kuyambira mu 1919 kupita m’tsogolo, Akhristu odzozedwa amene adakali ndi moyo padziko lapansi akhala akutsanzira Yesu pogwira mwakhama ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse. (Mateyu 4:17; Aroma 10:18) Poona zimenezi, ena amene anali m’Matchalitchi Achikhristu, omwe ndi sunagoge wa Satana wa masiku ano, anabwera kwa Akhristu odzozedwawa ndipo analapa. Iwo ‘anagwada ndi kuweramira’ Akhristu amenewa posonyeza kuti akuvomereza udindo umene kapolo wokhulupirikayu ali nawo. Chotero nawonso anayamba kutumikira Yehova limodzi ndi Akhristu odzozedwa achikulire. Anthu amenewa anapitiriza kubwera mpaka pamene chiwerengero chonse cha Akhristu odzozedwa, amene ndi abale ake a Yesu, chinakwanira. Tsopano, “khamu lalikulu la anthu, . . . lochokera m’dziko lililonse” likubwera ‘kudzagwada ndi kuweramira’ kapolo wodzozedwayu. (Chivumbulutso 7:3, 4, 9) Kapolo ameneyu pamodzi ndi khamu lalikulu apanga gulu limodzi la Mboni za Yehova.
20. N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova ziyenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kutumikira Mulungu mwakhama makamaka masiku ano?
20 Masiku ano, a Mboni za Yehova amadziwa kuti akuyenera kugwira mwachangu ntchito yolalikira imene apatsidwa, ndipo amachita zinthu mogwirizana chifukwa amakondana kuchokera pansi pa mtima ngati mmene Akhristu a ku Filadefiya ankachitira. Posachedwapa, dziko loipa la Satanali lidzawonongedwa pa chisautso chachikulu. Tiyeni tiyesetse kuti pa nthawi imeneyo, tidzapezeke tili ndi chikhulupiriro cholimba komanso tikutumikira Mulungu mwakhama, kuti mayina athu asadzafafanizidwe m’buku la moyo la Yehova. (Chivumbulutso 7:14) Tiyeni tiziganizira mozama malangizo a Yesu opita kumpingo wa ku Filadefiya kuti tigwirebe mwamphamvu mwayi wathu wa utumiki, n’cholinga choti tidzalandire mphoto ya moyo wosatha.
Madalitso Amene Opambana pa Nkhondo Amalandira
21. Kodi Akhristu odzozedwa masiku ano ‘asunga bwanji mawu onena za kupirira kwa Yesu,’ ndipo akuyembekezera madalitso otani?
21 Akhristu odzozedwa masiku ano ‘asunga mawu onena za kupirira kwa Yesu,’ kutanthauza kuti iwonso apirira potsatira chitsanzo chake. (Aheberi 12:2, 3; 1 Petulo 2:21) Choncho iwo alimbikitsidwa kwambiri ndi mawu otsatira a Yesu opita kumpingo wa ku Filadefiya. Yesu anati: “Wopambana pa nkhondo, ndidzamuika kukhala mzati m’kachisi wa Mulungu wanga, ndipo sadzachokamonso.”—Chivumbulutso 3:12a.
22. (a) Kodi Mulungu wa Yesu kachisi wake n’chiyani? (b) Kodi Akhristu odzozedwa amene apambana pa nkhondo amakhala bwanji zipilala m’kachisi ameneyu?
22 Kukhala mzati m’kachisi wa Yehova ndi mwayi waukulu kwambiri. Mu Yerusalemu wakale, anthu ankapita kukachisi kukalambira Yehova. Kamodzi pa chaka, mkulu wa ansembe ankalowa ‘m’Malo Oyera Koposa,’ mmene munali kuwala kozizwitsa kumene kunkaimira kuti Yehova ali m’chipinda chimenecho. Iye ankalowa mmenemo kuti akapereke nsembe ya magazi a nyama. (Aheberi 9:1-7) Pa ubatizo wa Yesu, kachisi wina anakhazikitsidwa. Kachisi ameneyu ndi dongosolo lolambirira Yehova, lomwe lili ngati kachisi wamkulu wauzimu. Malo opatulikitsa a kachisi ameneyu ali kumwamba, kumene moyenerera Yesu anakaonekera “pamaso pa Mulungu.” (Aheberi 9:24) Yesu ndi Mkulu wa Ansembe, ndipo anangopereka nsembe imodzi yokha imene inaphimbiratu machimo onse. Nsembe imeneyi ndi magazi amene Yesu anakhetsa monga munthu wangwiro. (Aheberi 7:26, 27; 9:25-28; 10:1-5, 12-14) Akhristu odzozedwa akamatumikira Mulungu mokhulupirika pamene ali padziko lapansi, amakhala ansembe aang’ono m’bwalo la padziko lapansi la kachisi ameneyu. (1 Petulo 2:9) Koma akapambana pa nkhondo, nawonso amalowa m’malo opatulikitsa a kumwamba ndipo amakhala zipilala zosasunthika za dongosolo lolambirira Mulungu lokhala ngati kachisi lija. (Aheberi 10:19; Chivumbulutso 20:6) Mosakayikira, iwo “sadzachokamonso” m’kachisi ameneyu.
23. (a) Kodi kenako Yesu analonjeza chiyani kwa Akhristu odzozedwa opambana pa nkhondo? (b) Kodi Akhristu opambana pa nkhondo akalembedwa dzina la Yehova ndiponso la Yerusalemu watsopano zimatanthauza chiyani?
23 Yesu anapitiriza kunena kuti: “Ndidzamulemba dzina la Mulungu wanga, ndiponso dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano, wotsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga. Ndidzamulembanso dzina langa latsopano.” (Chivumbulutso 3:12b) Inde, opambana pa nkhondo amenewa analembedwa dzina la Yehova, Mulungu wawo komanso Mulungu wa Yesu. Zimenezi zikusonyezeratu kuti Yehova ndi Yesu ndi anthu awiri osiyana ndipo sali mbali ya milungu itatu mwa mulungu mmodzi, ngati mmene anthu ena amanenera. (Yohane 14:28; 20:17) Zolengedwa zonse ziyenera kuona kuti odzozedwa amenewa ndi atumiki a Yehova ndiponso mboni zake. Iwo analembedwanso dzina la Yerusalemu watsopano, womwe ndi mzinda umene ukutsika kuchokera kumwamba. Mzindawu ukutsika kuchokera kumwamba, kutanthauza kuti ulamuliro wake ukubweretsa madalitso kwa anthu onse okhulupirika. (Chivumbulutso 21:9-14) Akhristu onse padziko lapansi, omwe ndi nkhosa za Mulungu, adzadziwa kuti odzozedwa opambana pa nkhondowa ndi nzika za Ufumu, womwe ndi Yerusalemu wakumwamba.—Salimo 87:5, 6; Mateyu 25:33, 34; Afilipi 3:20; Aheberi 12:22.
24. Kodi dzina latsopano la Yesu likuimira chiyani, ndipo limalembedwa bwanji pa Akhristu odzozedwa okhulupirika?
24 Pomaliza, odzozedwa opambana pa nkhondowa analembedwa dzina latsopano la Yesu. Dzina limeneli likuimira udindo watsopano komanso wapadera umene Yehova anapatsa Yesu. (Afilipi 2:9-11; Chivumbulutso 19:12) Palibe amene akudziwa dzinali, kutanthauza kuti palibe amene anagwirapo ntchito zokhudzana ndi udindo umenewu kapena amene anapatsidwa udindo wapadera ngati umenewu. Koma Yesu akalemba dzina lake pa abale ake okhulupirika, abale akewo amakhala naye paubwenzi wapadera kumwambako ndipo amathandizana naye pa udindo wakewo. (Luka 22:29, 30) N’zosadabwitsa kuti Yesu anamaliza uthenga wake wopita kwa odzozedwawo pobwereza mawu ake olimbikitsa akuti: “Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.”—Chivumbulutso 3:13.
25. Kodi Mkhristu aliyense masiku ano angagwiritsire ntchito bwanji mfundo zimene zili m’malangizo amene Yesu anapereka ku mpingo wa ku Filadefiya?
25 Uthenga umenewu uyenera kuti unalimbikitsa kwambiri Akhristu okhulupirika a ku Filadefiya. Ndipo uthengawu ulinso ndi mfundo zothandiza kwambiri kwa Akhristu odzozedwa masiku ano, mkati mwa tsiku la Ambuye. Koma mfundo zimene zili mu uthengawu n’zofunikanso kwa Mkhristu aliyense, kaya ndi wodzozedwa kapena wa nkhosa zina. (Yohane 10:16) Aliyense wa ife ayenera kupitiriza kubala zipatso za Ufumu ngati mmene anachitira Akhristu a ku Filadefiya. Tonsefe tili ndi mphamvu zochepa zotithandiza kukwanitsa kutumikira Yehova m’njira inayake. Choncho tiyeni tigwiritse ntchito mphamvu zimenezi. Ngati tikufuna kuwonjezera utumiki wathu pa ntchito yokhudza Ufumu, tiyeni tikhale tcheru kuti tilowe pakhomo lililonse la mwayi wa utumiki limene lingatitsegukire. Ndipo tingathenso kupemphera kuti Yehova atitsegulire khomo limenelo. (Akolose 4:2, 3) Tikamatsanzira Yesu pa nkhani ya kupirira ndiponso tikamachita zinthu mogwirizana ndi dzina lake, tidzasonyeza kuti ifenso makutu athu akumva zimene mzimu woyera wa Mulungu ukunena ku mipingo.
[Mawu a M’munsi]
a M’nthawi ya Paulo, Sositene, amene anali mtsogoleri wa sunagoge wa Ayuda ku Korinto, anakhala m’bale wachikhristu.—Machitidwe 18:17; 1 Akorinto 1:1.
b Magazini a Nsanja ya Olonda, amene amafalitsidwa ndi Akhristu odzozedwa, akupitiriza kusonyeza kufunika kogwiritsira ntchito mpata umenewu mwamsanga ndi kugwira nawo mokwanira ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, onani nkhani yakuti “Sangalalani ndi Ntchito Yopanga Ophunzira” mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2009, komanso yakuti “Khalani Maso” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2009, ndi yakuti “Khalani ‘Achangu pa Ntchito Zabwino’” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2009. Pa avereji, m’chaka cha 2010 panali anthu okwana 1,132,861 amene anachita utumiki wa upainiya.
c Buku lina linanena kuti: “Zipolowe zimene ansembe achikunja ankayambitsa, zinachititsa kuti mafumu adziwe zambiri zokhudza Chikhristu. Ansembewo ankayambitsa zipolowezo chifukwa cha mantha poona kuti Chikhristucho chinkafalikira mofulumira. Choncho Trajan [98-117 C.E.] anakakamizika kukhazikitsa malamulo amene cholinga chake chinali kuthetsa pang’onopang’ono kufalikira kwa ziphunzitso zatsopano zimene zinkasintha anthu n’kuwachititsa kuyamba kudana ndi kulambira milungu. Pa nthawi imene Pliny Wamng’ono anali bwanamkubwa wa dera la Bituniya [limene kumpoto kwake linachita malire ndi chigawo cha Asia cholamuliridwa ndi Aroma], ankafunikira kuweruza nkhani zambiri zovuta zokhudzana ndi Chikhristu chimene chinkafalikira mofulumira kwambiri. Komanso ankafunikira kuthetsa mkwiyo umene anthu achikunja am’derali anali nawo chifukwa cha kufalikira kwa Chikhristucho.”—McClintock and Strong’s Cyclopedia (Volume X, page 519).
d Dzina lakuti Hezekiya limatanthauza kuti “Yehova Amalimbikitsa.”
[Bokosi patsamba 63]
Anthu Ambiri Akuthandizidwa Kuti Agwirizane ndi Akhristu Odzozedwa
Mwa Akhristu odzozedwa 144,000 amene adzalamulire mu Ufumu wa kumwamba, zikuoneka kuti amene adakali ndi moyo padziko lapansi ndi pafupifupi 11,000. Komanso khamu lalikulu likuwonjezeka ndipo panopa m’khamu limeneli muli Akhristu oposa 7,300,000. (Chivumbulutso 7:4, 9) Kodi n’chiyani chachititsa kuti khamu limeneli liwonjezeke kwambiri chonchi? Sukulu zosiyanasiyana za Mboni za Yehova zathandizira kwambiri kuti khamuli liwonjezeke. Sukulu za Mboni zimenezi zimathandiza anthu kuti azikhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu. Izi n’zosiyana kwambiri ndi maseminale a Matchalitchi Achikhristu amene salemekeza Baibulo koma amangophunzitsa nzeru za anthu. Sukulu za Mbonizi zimathandiza anthu kuti aone mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo kuti akhale ndi makhalidwe oyera komanso abwino ndiponso kuti azitumikira Mulungu modzipereka. Kuyambira mu 1943, mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova padziko lonse, umachita Sukulu ya Utumiki wa Mulungu m’nyumba yawo ya Ufumu. Anthu mamiliyoni ambiri amaphunzira nawo m’sukulu imeneyi mlungu uliwonse, ndipo maphunziro a m’Baibulo amenewa amakhala ofanana padziko lonse.
Mboni za Yehova zakhalanso zikuchita Sukulu ya Utumiki wa Ufumu kuyambira mu 1959. Sukulu imeneyi imaphunzitsa akulu a mpingo komanso atumiki othandiza. Ndipo kuyambira mu 1977 abale ndi alongo ambiri aphunzitsidwa mu Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Mofanana ndi Akhristu a ku Filadefiya, Akhristu amenewa amalalikira nthawi zonse potumikira Yehova. Sukulu Yophunzitsa Utumiki imene panopa ikudziwika kuti Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira, inayambika mu 1987 kuti iziphunzitsa abale kuchita utumiki wapadera padziko lonse.
Sukulu yapadera kwambiri pa sukulu zonse za Mboni za Yehova ndi Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo. Kuyambira mu 1943 sukulu imeneyi, yomwe ili ku New York State, imaphunzitsa makalasi awiri a amishonale pafupifupi chaka chilichonse. Atumiki onse a Yehova amene aphunzitsidwa m’sukuluyi ndi oposa 7,000, ndipo amatumizidwa m’mayiko osiyanasiyana kuti akakhale amishonale. Akhristu amene anamaliza maphunziro awo m’sukuluyi atumikirapo m’mayiko oposa 100 ndipo m’mayiko ambiri mwa amenewa, iwo anathandiza kuti ntchito ya Ufumu iyambike. Panopa patha zaka zoposa 60 kuchokera pamene sukuluyi inayamba, ndipo ena mwa amishonale oyambirira akupitirizabe utumiki wawo. Iwo akuthandizana ndi amishonale atsopano pa ntchito yokulitsa gulu la Yehova padziko lonse, ndipo gululi lakuladi mochititsa chidwi kwambiri.
[Tchati patsamba 64]
Mu 1919 Yesu, amene panopa akulamulira monga mfumu, anatsegulira Akhristu khomo la mwayi wa utumiki. Akhristu ambiri odzipereka, amene akuchulukirachulukirabe, akugwiritsa ntchito mwayi umenewu.
1918 14 3,868 591
1928 32 23,988 1,883
1938 52 47,143 4,112
1948 96 230,532 8,994
1958 175 717,088 23,772
1968 200 1,155,826 63,871
1978 205 2,086,698 115,389
1988 212 3,430,926 455,561
1998 233 5,544,059 698,781
2008 236 6,829,455 732,912
2010 236 7,224,930 844,901
[Mawu a M’munsi]
e Manambala ali pamwambawa ndi maavereji apamwezi.
f Manambala ali pamwambawa ndi maavereji apamwezi.
[Tchati patsamba 65]
A Mboni za Yehova amagwira ndi mtima wonse ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, onani kuchuluka kwa maola amene anakhala akugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu Baibulo komanso kuchuluka kwa anthu amene anaphunzira nawo Baibulo panyumba pawo kwaulere.
Maola Othera Maphunziro
Polalikira a Baibulo
Chaka (Chaka Chonse) (Avereji ya Pamwezi)
1918 19,116 Sizinalembedwe
1928 2,866,164 Sizinalembedwe
1938 10,572,086 Sizinalembedwe
1948 49,832,205 130,281
1958 110,390,944 508,320
1968 208,666,762 977,503
1978 307,272,262 1,257,084
1988 785,521,697 3,237,160
1998 1,186,666,708 4,302,852
2008 1,488,658,249 7,133,760
2010 1,604,764,248 8,058,359
[Chithunzi patsamba 59]
Kiyi wachiroma wa m’nthawi ya atumwi