Khalani Omvera Pamene Mapeto Akuyandikira
“Anthu adzamvera [Silo].”—GENESIS 49:10.
1. (a) Kodi kale nthaŵi zambiri kumvera Yehova kunafuna kuchita chiyani? (b) Kodi Yakobo analosera chiyani zokhudza kumvera?
NTHAŴI zambiri kumvera Yehova kunafuna kumvera anthu amene anali kumuimira. Ena mwa anthu amene anamuimira anali angelo, makolo akale, oweruza, ansembe, aneneri, ndi mafumu. Mpando wachifumu wa mafumu a Israyeli unatchedwanso mpando wachifumu wa Yehova. (1 Mbiri 29:23) Koma n’zomvetsa chisoni kuti olamulira ambiri a Israyeli sanamvere Mulungu, zimenezi zinabweretsa mavuto kwa iwo ndi anthu amene anali kuwalamulira. Koma Yehova sanasiye anthu ake okhulupirika opanda chiyembekezo. Anawalimbikitsa ndi lonjezo lakuti adzaika Mfumu yopanda chinyengo, imene anthu olungama adzakondwera kuimvera. (Yesaya 9:6, 7) Yakobo, kholo lakale, ali pafupi kumwalira analosera za wolamulira wam’tsogolo ameneyu kuti: “Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena [chibonga cha, NW] wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.”—Genesis 49:10.
2. Kodi “Silo” amatanthauza chiyani, ndipo ulamuliro wake udzaphatikizapo ndani?
2 “Silo” ndi liwu la Chihebri limene limatanthauza kuti “Mwini Wake.” Inde, Silo anali kudzakhala ndi ufulu wonse wolamulira, monga mmene ndodo yachifumu ikusonyezera, ndiponso mphamvu yolamula monga mmene ikuimiridwa ndi chibonga cha wolamulira. Ndiponso ufumu wake sudzakhala wa ana a Yakobo okha koma “anthu” onse. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Yehova analonjeza Abrahamu. Anati: “Mbewu zako zidzagonjetsa chipata cha adani awo; m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:17, 18) Yehova anasonyeza amene anali “mbewu” imeneyi mu 29 C.E. pamene anadzoza Yesu wa ku Nazarete ndi mzimu woyera.—Luka 3:21-23, 34; Agalatiya 3:16.
Ufumu Woyamba wa Yesu
3. Kodi Yesu analandira ulamuliro wotani atapita kumwamba?
3 Yesu atapita kumwamba, sanatenge ndodo yachifumu nthaŵi yomweyo ndi kuyamba kulamulira anthu padziko lapansi. (Salmo 110:1) Komabe, iye analandira “ufumu” pamodzi ndi anthu amene anali kumumvera. Mtumwi Paulo anafotokoza chimene ufumuwu uli pamene analemba kuti: ‘[Mulungu] anatilanditsa ife [Akristu odzozedwa ndi mzimu] ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutiloŵetsa m’ufumu wa Mwana wa chikondi chake.’ (Akolose 1:13) Kulanditsa kumeneku kunayamba pa Pentekoste wa 33 C.E. pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa otsatira a Yesu okhulupirika.—Machitidwe 2:1-4; 1 Petro 2:9.
4. Kodi ophunzira oyambirira a Yesu anasonyeza bwanji kumvera, ndipo Yesu anawatcha ndani monga gulu?
4 Monga “atumiki m’malo mwa Kristu,” ophunzira odzozedwa ndi mzimu momvera anayamba kusonkhanitsa ena amene anali kudzakhala a “mudzi womwewo” mu ufumu wauzimuwo. (2 Akorinto 5:20; Aefeso 2:19; Machitidwe 1:8) Ndiponso, ameneŵa anafunika kukhalabe ‘omangika mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho’ kuti Mfumu yawo, Yesu Kristu iwayanje. (1 Akorinto 1:10) Monga gulu, anthu ameneŵa anapanga gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kapena gulu la mdindo wokhulupirika.—Mateyu 24:45; Luka 12:42.
Anadalitsidwa Chifukwa Chomvera “Mdindo” wa Mulungu
5. Kodi Yehova waphunzitsa bwanji anthu ake kuyambira kale?
5 Yehova nthaŵi zonse wapereka aphunzitsi kwa anthu ake. Mwachitsanzo, Ayuda atabwerako ku Babulo, Ezara ndi amuna ena oyenerera sanangoŵerengera chabe anthu Chilamulo cha Mulungu, koma ‘anatanthauzira’ chilamulocho, ‘kuwazindikiritsa’ Mawu a Mulungu.—Nehemiya 8:8.
6, 7. Kodi gulu la kapolo lapereka bwanji chakudya chauzimu panthaŵi yake kudzera m’Bungwe lake Lolamulira, ndipo n’chifukwa chiyani kugonjera gulu la kapolo n’koyenera?
6 M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, nkhani ya mdulidwe itabuka mu 49 C.E., bungwe lolamulira la gulu la kapolo loyambirira linapenda nkhaniyi mwapemphero ndipo linagamula mogwirizana ndi Malemba. Atalengeza m’kalata zimene anagamula, mipingo inamvera malangizowo ndipo Mulungu anaidalitsa kwambiri. (Machitidwe 15:6-15, 22-29; 16:4, 5) N’chimodzimodzinso masiku ano. Kapolo wokhulupirika kudzera m’Bungwe lake Lolamulira wafotokoza bwino nkhani zofunika kwambiri monga kusaloŵerera m’ndale kwa Akristu, kupatulika kwa magazi, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi fodya. (Yesaya 2:4; Machitidwe 21:25; 2 Akorinto 7:1) Yehova anadalitsa anthu ake chifukwa chomvera Mawu ake ndi kapolo wokhulupirika.
7 Mwa kugonjera gulu la kapolo, anthu a Mulungu amasonyezanso kugonjera Mbuyeyo, Yesu Kristu. Kugonjera kumeneku n’kofunika kwambiri masiku ano chifukwa cha kukula kwa ulamuliro wa Yesu monga mmene unanenera ulosi wa Yakobo umene anaunena ali pa bedi limene anamwalirira.
Silo Akhala Wolamulira Woyenera wa Dziko Lapansi
8. Kodi ulamuliro wa Kristu unakula motani ndipo liti?
8 Yakobo analosera kuti “anthu adzamvera” Silo. Inde, Kristu sanali kudzalamulira Israyeli wauzimu yekha. Kodi anali kudzalamuliranso ndani? Lemba la Chivumbulutso 11:15 limayankha kuti: ‘Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.’ Baibulo limavumbula kuti Yesu analandira ulamuliro umenewo pamene “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” zaulosi, ‘nthaŵi za akunja’ zinatha mu 1914.a (Danieli 4:16, 17; Luka 21:24) Panthaŵiyo, “kukhalapo” kwa Kristu monga Mfumu ya Umesiya kunayamba, pamodzi ndi nthaŵi yake ‘yochita ufumu pakati pa adani ake.’—Mateyu 24:3, NW; Salmo 110:2.
9. Kodi Yesu anachita chiyani atalandira Ufumu wake, ndipo zimenezi zakhudza bwanji anthu, makamaka ophunzira ake?
9 Ntchito yoyamba imene Yesu anachita atalandira ufumu inali yogwetsera “pansi kudziko” Satana yemwe ndi chimake cha kusamvera, pamodzi ndi ziŵanda zake. Kuyambira nthaŵi imeneyo, mizimu yoipa imeneyi yayambitsa mavuto omwe sanachitike n’kale lonse kwa anthu, kuwonjezera pa kulimbikitsa zinthu zimene zachititsa kumvera Yehova kukhala kovuta kwambiri. (Chivumbulutso 12:7-12; 2 Timoteo 3:1-5) Ndipotu, anthu amene Satana amawafuna kwambiri kumenya nawo nkhondo yauzimu ndi odzozedwa a Yehova, “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu,” pamodzi ndi anzawo a “nkhosa zina.”—Chivumbulutso 12:17; Yohane 10:16.
10. Kodi ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi uti wa m’Baibulo kumene kukutsimikizira kulephera kwa Satana m’nkhondo yake yolimbana ndi Akristu oona?
10 Komabe, Satana adzalephera chifukwa lino ndi “tsiku la Ambuye,” ndipo palibe chingam’lepheretse Yesu ‘kulakika.’ (Chivumbulutso 1:10; 6:2) Mwachitsanzo, iye adzaonetsetsa kuti kusindikizidwa chizindikiro komaliza kwa Aisrayeli auzimu a 144,000 kwachitika. Ndiponso adzateteza “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:1-4, 9, 14-16) Komabe ameneŵa, mosiyana ndi anzawo odzozedwa, adzakhala anthu omvera a Yesu a padziko lapansi. (Danieli 7:13, 14) Kukhalapo kwawo pa dziko lapansi masiku ano kukutsimikizira kuti Silo alidi Wolamulira wa “Ufumu wa dziko lapansi.”—Chivumbulutso 11:15.
Ino Ndiyo Nthaŵi ‘Yomvera Uthenga Wabwino’
11, 12. (a) Kodi ndani okha amene adzapulumuka pamene dongosolo la zinthu lino likutha? (b) Kodi anthu amene amatengera “mzimu wa dziko lapansi” amakhala ndi makhalidwe otani?
11 Onse amene akufuna moyo wosatha ayenera kuphunzira kumvera, chifukwa Baibulo limafotokoza mosapita m’mbali kuti “iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu” sadzapulumuka tsiku la Mulungu lobwezera chilango. (2 Atesalonika 1:8) Komabe, dziko la masiku ano loipali ndi mtima wake wosamvera malamulo ndi mfundo za m’Baibulo zimachititsa kumvera uthenga wabwino kukhala kovuta kwambiri.
12 Baibulo limafotokoza mtima wosamvera Mulungu umenewu kuti ndi “mzimu wa dziko lapansi.” (1 Akorinto 2:12) Pofotokoza mmene zimenezi zikukhudzira anthu, mtumwi Paulo analembera Akristu oyambirira a ku Efeso kuti: ‘Munayenda kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; amene ife tonsenso tinagonera pakati pawo kale, m’zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo.’—Aefeso 2:2, 3.
13. Kodi Akristu angakwanitse bwanji kukaniza mzimu wa dziko lapansi, ndipo pangakhale zotsatira zabwino ziti?
13 N’zosangalatsa kuti Akristu a ku Efeso sanakhale akapolo a mzimu wosamvera mpaka kale. M’malo mwake, iwo anakhala ana omvera a Mulungu mwa kugonjera mzimu wake ndi kututa chipatso chake chabwino chochuluka. (Agalatiya 5:22, 23) Chimodzimodzinso masiku ano, mzimu wa Mulungu, womwe ndi mphamvu yaikulu kwambiri m’chilengedwe chonse, ukuthandiza anthu ambiri kumvera Yehova, ndipo zotsatira zake n’zakuti iwo angakhale ndi “chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro.”—Ahebri 6:11; Zekariya 4:6.
14. Kodi Yesu anachenjeza bwanji Akristu onse okhala m’masiku otsiriza za mavuto enieni amene adzayesa kumvera kwawo?
14 Kumbukiraninso kuti tikuthandizidwa kwambiri ndi Silo, amene pamodzi ndi Atate wake sadzalola kuti mdani wina aliyense, kaya ziŵanda kapena anthu, ayese kumvera kwathu mopitirira malire amene tingathe kupirira. (1 Akorinto 10:13) Ndipotu, potithandiza pa nkhondo yathu yauzimu, Yesu anafotokoza mavuto enieni angapo amene tingakumane nawo m’masiku otsiriza ano. Anachita zimenezo kudzera m’makalata asanu ndi aŵiri, amene anapereka m’masomphenya kwa mtumwi Yohane. (Chivumbulutso 1:10, 11) Kunena zoona, makalatawa anali ndi malangizo ofunika kwambiri kwa Akristu kalelo, koma anali kudzagwira ntchito kwambiri ‘m’tsiku la Ambuye’ kuyambira mu 1914. Ndiyetu n’koyenera kuti titchere khutu ku mauthenga ameneŵa.b
Peŵani Mphwayi, Chiwerewere, ndi Kukonda Chuma
15. N’chifukwa chiyani tifunika kupeŵa mavuto amene anakhudza mpingo wa ku Efeso, ndipo tingachite bwanji zimenezo? (2 Petro 1:5-8)
15 Kalata yoyamba ya Yesu inapita ku mpingo wa ku Efeso. Atauyamikira mpingowo chifukwa cha kupirira, Yesu anati: “Koma ndili nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya chikondi chako choyamba.” (Chivumbulutso 2:1-4) Masiku anonso, Akristu amene poyamba anali achangu ataya chikondi cholimba chimene anali nacho kwa Mulungu. Kutaya chikondi koteroko kungafooketse ubale wa munthuyo ndi Mulungu ndipo afunika kuukonza mwamsanga. Kodi angatani kuti akhalenso ndi chikondi choterocho? Angatero mwa kuphunzira Baibulo nthaŵi zonse, kupezeka pamisonkhano, kupemphera, ndi kusinkhasinkha. (1 Yohane 5:3) N’zoona kuti zimenezi zimafuna “changu chonse,” komatu n’koyenera kutero. (2 Petro 1:5-8) Ngati mutadzipenda moona mtima mupeza kuti chikondi chanu chazirala, konzani vutolo mwamsanga, pomvera langizo la Yesu lakuti: “Kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba.”—Chivumbulutso 2:5.
16. Kodi ndi zinthu zowononga mwauzimu ziti zimene zinali m’mipingo ya ku Pergamo ndi ku Tiyatira, ndipo n’chifukwa chiyani mawu amene Yesu anawauza ndi oyenerera masiku ano?
16 Akristu a ku Pergamo ndi ku Tiyatira anawayamikira chifukwa cha kukhulupirika kwawo, kupirira kwawo, ndi changu chawo. (Chivumbulutso 2:12, 13, 18, 19) Komabe, iwo anasonkhezeredwa ndi anthu ena amene anasonyeza mzimu woipa wa Balamu ndi Yezebeli, amene mwa kuchita chiwerewere ndi kulambira Baala anaipitsa Aisrayeli akale. (Numeri 31:16; 1 Mafumu 16:30, 31; Chivumbulutso 2:14, 16, 20-23) Koma bwanji nanga masiku ano, ‘m’tsiku la Ambuye’? Kodi tikuonanso zinthu zoipitsa zoterezi? Inde. Chiwerewere ndicho chifukwa chachikulu chimene anthu ambiri a Mulungu akuchotsedwera mu mpingo. Ndiyetu n’kofunika kwambiri kuti tipeŵe kucheza ndi anthu onse kaya a mumpingo kapena omwe sali mumpingo amene angatiipitsire makhalidwe. (1 Akorinto 5:9-11; 15:33) Amene akufuna kukhala anthu omvera Silo adzapeŵanso zosangalatsa zoipa pamodzi ndi zolaula za m’mabuku kapena za pa Intaneti.—Amosi 5:15; Mateyu 5:28, 29.
17. Kodi maganizo ndi mtima wa anthu a ku Sarde ndi ku Laodikaya zinasiyana bwanji ndi mmene Yesu anaonera moyo wawo wauzimu?
17 Mpingo wa ku Sarde sanauyamikire m’pang’ono pomwe kupatulapo anthu ochepa chabe. Mpingowu unali ndi “dzina,” kapena kuoneka kuti unali wamoyo, koma kuchita mphwayi ndi zinthu zauzimu kunazika mizu moti kwa Yesu mpingowu unali “wakufa.” Kumvera kwawo uthenga wabwino kunali kwa mwambo basi. Koma ndiye anawadzudzula bwanji! (Chivumbulutso 3:1-3) Mpingo wa ku Laodikaya unalinso chimodzimodzi. Unadzitukumula kuti unali wolemera mwa kunena kuti, “ndine wolemera.” Koma kwa Kristu, mpingowu unali “watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa.”—Chivumbulutso 3:14-17.
18. Kodi munthu angapeŵe bwanji kukhala wofunda mwauzimu pamaso pa Mulungu?
18 Masiku ano, anthu ena amene kale anali Akristu okhulupirika akhalanso osamvera chimodzimodzi. Mwina alola mzimu wa dziko lapansi kufooketsa changu chawo, ndipo motero afunda mwauzimu pankhani ya phunziro la Baibulo, pemphero, misonkhano yachikristu, ndiponso utumiki. (2 Petro 3:3, 4, 11, 12) N’kofunika kwambiri kuti anthu oterowo amvere Kristu mwa kusunga chuma chauzimu, inde, ‘kugula kwa Kristu golidi woyengeka ndi moto.’ (Chivumbulutso 3:18) Chuma chenicheni chimenechi chimaphatikizapo kukhala ‘ochuluka mu ntchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawira ena.’ Mwa kusunga zinthu za mtengo wapatalidi zimenezi, ‘timadzikundikira tokha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti tikagwire moyo weniweniwo.’—1 Timoteo 6:17-19, NW.
Anawayamikira Chifukwa cha Kumvera Kwawo
19. Kodi Yesu anayamikira ndi kulangiza zotani Akristu a ku Smurna ndi ku Filadelfeya?
19 Mipingo ya ku Smurna ndi ku Filadelfeya ndi zitsanzo zabwino kwambiri za kumvera, chifukwa m’makalata amene Yesu anawalembera munalibe chidzudzulo chilichonse. Yesu anauza anthu a mumpingo wa ku Smurna kuti: ‘Ndidziŵa chisautso chanu, ndi umphaŵi wanu (komatu muli achuma).’ (Chivumbulutso 2:9) Anasiyanatu kwambiri ndi a ku Laodikaya amene anadzitama ndi chuma chawo cha kudziko pomwe kwenikweni anali osauka! Koma Mdyerekezi sanasangalale kuona ena akukhulupirika ndi kumvera Kristu. N’chifukwa chake Yesu anachenjeza kuti: “Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, Mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.” (Chivumbulutso 2:10) Mofananamo, Yesu anayamikira anthu a ku Filadelfeya kuti: ‘Munasunga mawu anga [kapena kuti munandimvera], osakana dzina langa. Ndidza msanga; gwirani chimene muli nacho, kuti wina angalande korona wanu.’—Chivumbulutso 3:8, 11.
20. Kodi anthu ambirimbiri masiku ano asunga bwanji mawu a Yesu ndipo achita zimenezo ngakhale kuti pakhala mavuto otani?
20 ‘M’tsiku la Ambuye’ kuyambira mu 1914, otsalira okhulupirika pamodzi ndi anzawo a nkhosa zina, omwe tsopano akukwana mamiliyoni angapo, asunganso mawu a Yesu mwa kutumikira mwachangu ndi kukhalabe okhulupirika. Mofanana ndi abale awo a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, ena avutika chifukwa cha kumvera kwawo Kristu, ngakhale kuponyedwa m’ndende ndi m’misasa ya ukaidi. Ambiri asunga mawu a Yesu mwa kukhalabe ndi ‘diso la kumodzi’ ngakhale kuti akukhala ndi anthu okonda chuma ndi adyera. (Mateyu 6:22, 23) Inde, pamalo alionse ndiponso n’zochitika zilizonse, Akristu oona amapitirizabe kukondweretsa mtima wa Yehova chifukwa cha kumvera kwawo.—Miyambo 27:11.
21. (a) Kodi ndi udindo wauzimu uti umene gulu la kapolo lidzapitiriza kukwaniritsa? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufunadi kumvera Silo?
21 Pamene tikuyandikira chisautso chachikulu, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ali wotsimikiza mtima kusasiya kumvera Mbuyeyo, Kristu. Zimenezi zikuphatikizapo kukonzera banja la Mulungu chakudya chauzimu cha panthaŵi yake. Ndiyetu tiyeni tipitirize kuyamikira gulu la Yehova labwino kwambiri ndi zimene limatipatsa. Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikugonjera Silo, amene adzapereka moyo wosatha kwa anthu onse omumvera.—Mateyu 24:45-47; 25:40; Yohane 5:22-24.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve za “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri” mwatsatanetsatane, onani mutu 10 m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b Kuti mumve mwatsatanetsatane za makalata onse asanu ndi aŵiri, onani buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, kuyambira pa tsamba 33.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi Yesu anali kudzagwira ntchito yotani monga mmene Yakobo analoserera ali pa bedi limene anamwalirira?
• Kodi timavomereza bwanji kuti Yesu ndiye Silo, ndipo tiyenera kupeŵa mzimu wotani?
• Kodi ndi malangizo ati othandiza masiku ano amene ali m’makalata amene analembera mipingo isanu ndi iŵiri ya m’Chivumbulutso?
• Kodi tingatsanzire bwanji anthu a m’mipingo yakale ya ku Smurna ndi ku Filadelfeya?
[Zithunzi patsamba 18]
Yehova amadalitsa anthu ake chifukwa chomvera “mdindo” wokhulupirika
[Chithunzi patsamba 19]
Mavuto amene Satana amabweretsa amachititsa kumvera Mulungu kukhala kovuta
[Zithunzi patsamba 21]
Kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova kumatithandiza kuti timumvere