Mutu 17
Kubweranso kwa Kristu—Kodi Kuwoneka Motani?
1. (a) Kodi Kristu anapereka lonjezo lotani? (b) Kodi pali kufunika kotani kwa kubweranso kwa Kristu?
“NDIDZABWERANSO.” (Yohane 14:3) Yesu Kristu anapereka lonjezo limeneli kwa atumwi ake pamene anali nawo usiku wotsatiridwa ndi imfa yake. Mwina mwake mudzavomereza kuti sipanakhale kufunika kokulirapo kwa mtendere, thanzi ndi moyo zimene kubweranso kwa Kristu m’mphamvu Yaufumu kudzathetsa kwa anthu. Koma kodi Kristu akubweranso motani? Kodi ndani amene akumuwona, ndipo m’njira yotani?
2. (a) Pamene abweranso, kodi Kristu akutengera kuti atsatiri ake odzozedwa, kuphatikizapo atumwi ake, kukakhala? (b) Kodi iwo kumeneko akukhala ndi matupi a mtundu wotani?
2 Pa kubweranso kwake, Kristu sakudza kudzakhala padziko lapansi. M’malo mwake, awo amene ayenera kulamulira monga mafumu limodzi naye akutengedwa kukakhala naye kumwamba. Yesu anauza atumwi ake kuti: “Ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.” (Yohane 14:3) Motero, pamene Kristu abweranso, awo amene akutengeredwa kumwamba akukhala anthu auzimu, ndipo iwo akuwona Kristu m’thupi lake lauzimu laulemerero. (1 Akorinto 15:44) Koma kodi ena a anthu, amene sakupita kumwamba, akuwona Kristu pamene abweranso?
CHIFUKWA CHAKE IYE SAKABWERANSO MONGA MUNTHU
3. Kodi ndiumboni Wabaibulo wotani umene umasonyeza kuti anthu sazawonanso Kristu?
3 Usiku umodzimodziwo Yesu anapitiriza kunena kwa atumwi ake kuti: “Katsala kanthawi. Ndipo dziko lapansi silindiwonanso Ine.”(Yohane 14:19) Dziko lapansi” limatanthauza anthu. Motero Yesu panopa mwachimvekere ananena kuti anthu padziko lapansi sakamuwonanso pambuyo pa kukwera kwake kumwamba. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipo ngati tizindikira Kristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.”—2 Akorinto 5:16.
4. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Kristu akubweranso monga munthu wauzimu wosawoneka wamphamvu?
4 Komabe anthu ambiri amakhulupirira kuti Kristu adzabweranso m’thupi laumunthu limodzimodzilo m’limene iye anaphedwa, ndi kuti awo onse okhala ndi moyo padziko lapansi adzamuwona. Komabe, Baibulo limanena kuti Kristu akubweranso mu ulemerero limodzi ndi angelo onse, ndi kuti iye akukhala “pachimpando cha kuwala kwake.” (Mateyu 25:31) Ngati Yesu akanati adze ndi kukhala pansi monga munthu pampando wachifumu wapadziko lapansi, iye akanakhala wotsikirapo m’malo koposa angelo. Koma iye akudza monga wamphamvu koposa ndi waulemerero koposa ana auzimu a Mulungu onsewa ndipo chifukwa cha chimenecho ngwosawoneka, monga momwedi iwo aliri.—Afilipi 2:8-11.
5. Kodi nchifukwa ninji Kristu sakabweranso m’thupi laumunthu?
5 Ndiponso, koposa zaka 1,900 zapitazo kunali kofunika kwa Yesu kudzitsitsa ndi kukhala munthu. Iye anafunikira kupereka moyo wake waumunthu wangwiro monga dipo kwa ife. Yesu pa nthawi ina anakufotokoza motere: “Mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.” (Yohane 6:51) Yesu motero anapereka thupi lake lanyama mu nsembe kaamba ka anthu. Kodi nsembe imeneyo ikakhala ikugwira ntchito kwautali wotani? Mtumwi Paulo akuyankha kuti: “Tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.” (Ahebri 10:10) Atapereka thupi lake kaamba ka moyo wa dziko lapansi, Kristu sakadalitenganso ndi kukhala munthu kachiwiri. Kaamba ka chifukwa chachikulu chimenecho kubweranso kwake sikungakhale m’thupi laumunthu limene iye analipereka nsembe kamodzi kwatha.
THUPI LANYAMA SILITENGEREDWE KUMWAMBA
6. Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri amakhulupirira kuti Kristu anatengera thupi lake lanyama kumwamba?
6 Komabe, anthu ambiri amakhulupirira kuti Kristu anatengera thupi lake lanyama kumwamba. Iwo amasonyeza chenicheni chakuti pamene Kristu anaukitsidwa kwa akufa, thupi lake lanyama silinalinso m’manda. (Marko 16:5-7) Ndiponso, pambuyo pa imfa yake Yesu anawonekera kwa ophunzira ake m’thupi lanyama kuwasonyeza kuti iye anali wamoyo. Pa nthawi ina Iye anachititsa mtumwi Tomasi kupisa dzanja lake mu una wam’nthinthi Mwake kotero kuti Tomasi akakhulupirire kuti Iye adaukitsidwadi. (Yohane 20:24-27) Kodi zimenezi sizimatsimikizira kuti Kristu anaukitsidwa wamoyo m’thupi limodzimodzilo m’limene iye anaphedwera?
7. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti Kristu anapita kumwamba monga munthu wauzimu?
7 Ayi, sizikutero. Baibulo nlomvekera bwino kwambiri pamene limati: “Kristu anafa kamodzi kwatha ponena za machimo . . . , iye akumaphedwa m’thupi lanyama, koma akumakhalitsidwa wamoyo mu mzimu.” (1 Petro 3:18, NW) Anthu okhala ndi matupi anyama ndi mwazi sangakhale kumwamba. Ponena za chiukiriro cha kumoyo wakumwamba, Baibulo limati: “Lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. . . . thupi ndi mwazi sizingathe kulowa ufumu wa Mulungu.”(1 Akorinto 15:44-50) Anthu okha auzimu okhala ndi matupi auzimu angakhale kumwamba.
8. Kodi nchiyani chimene chinachitikira thupi laumunthu la Kristu?
8 Chabwino, pamenepa, kodi nchiyani chimene chinachitikira thupi lanyama la Yesu? Kodi ophunzirawo sanapeze manda ake apululu? Iwo anatero, chifukwa chakuti Mulungu anachotsa thupi la Yesu. Kodi nchifukwa ninji Mulungu anachita zimenezi? Kunakwaniritsa zimene zidalembedwa M’Baibulo. (Salmo 16:10; Machitidwe 2:31) Motero Yehova anawona kukhala koyenera kuchotsa thupi la Yesu, monga momwe iye adachitira kale ndi thupi la Mose. (Deuteronomo 34:5, 6) Ndiponso, ngati thupilo likadasiyidwa m’manda, ophunzira a Yesu sakanamvetsetsa kuti iye adaukitsidwa kwa akufa, popeza kuti pa nthawi imeneyo iwo sanazindikire mokwanira zinthu zauzimu.
9. Kodi kunatheka motani kuti Tomasi apise dzanja lake pa chironda m’thupi losandulizidwa la Yesu woukitsidwayo?
9 Koma popeza kuti mtumwi Tomasi anali wokhoza kupisa dzanja lake mu una m’nthiti mwa Yesu, kodi zimenezo sizikusonyeza kuti Yesu anaukitsidwa kwa akufa m’thupi limodzimodzilo limene linakhomeredwa pa mtengo? Ayi, pakuti Yesu anangosanduka kapena anangovala thupi lanyama, monga momwe angelo adachitira kale. Kuti akhutiritse maganizo Tomasi za amene Iye anali, Iye anagwiritsira ntchito thupi lokhala ndi mauna azironda. Iye anawonekera, kapena anawoneka kukhala, munthu weniweni, wokhoza kudya ndi kumwa, monga momwedi anachitira angelo amene Abrahamu anachereza pa nthawi ina. —Genesis 18:8; Ahebri 13:2.
10. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Yesu anavala matupi anyama osiyanasiyana?
10 Pamene Yesu anawonekera kwa Tomasi m’thupi lofanana ndi m’limene iye anaphedwa, Iye anavalanso matupi osiyanasiyana powonekera kwa atsatiri Ake. Motero Maliya wa Magadala poyamba anaganiza kuti Yesu anali wakumunda. Pa nthawi zina ophunzira ake sanamzindikire poyamba. M’zochitika zimenezi sikanali kawonekedwe kake ka iye mwini kamene kanatumikira kumdziwikitsa, koma anali mawu ena kapena kachitidwe kamene iwo anazindikira.—Yohane 20:14-16; 21:6, 7; Luka 24:30, 31.
11, 12. (a) Kodi Kristu anachoka padziko lapansi mu mkhalidwe wotani? (b) Motero tiyenera kuyembekezera kubweranso kwa Kristu mu mkhalidwe wotani?
11 Kwa masiku 40 pambuyo pa chiukiriro chake, Yesu anawonekera m’thupi lanyama kwa ophunzira ake (Machitidwe 1:3) Ndiyeno ananyamuka kupita kumwamba. Koma ena angafunse kuti: ‘Kodi angelo awiri amene analipo sanauze atumwi kuti Kristu “adzadza momwemo monga munamuwona alinkupita kumwamba”?’ (Machitidwe 1:11) Inde, iwo anatero. Koma wonani kuti iwo anati “momwemo,” osati m’thupi limodzimodzilo. Ndipo kodi mkhalidwe wa kuchoka kwa Yesu unali wotani? Unali wakachetechete, wopanda kudziwonetsera poyera. Atumwi ake okha anakudziwa. Dziko silinakudziwe.
12 Lingalirani mmene Baibulo limafotokozera mmene Yesu anasiyira atumwi ake pa ulendo wake wakumwamba: “Ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwawo.” (Machitidwe 1:9) Motero pamene Yesu anayamba kulowa kumwamba mtambo unambisa ku maso enieni a atumwi ake. Chifukwa cha chimenecho, Yesu wochokayo anakhala wosawoneka kwa iwo. Iwo sanathe kumuwona. Ndiyeno anakwera kumwamba m’thupi lake lauzimu. (1 Petro 3:18) Motero kubweranso kwake kukakhalanso kosawoneka, m’thupi lauzimu.
MMENE AKUWONEDWERA NDI DISO LIRILONSE
13.Kodi tiyenera kumva motani kanenedwe kakuti “diso lirilonse lidzawona” Kristu pamene adza ndi mitambo?
13 Pamenepa, kodi ndimotani mmene tingamvere mawu a Chivumbulutso 1:7? Pamenepo mtumwi Yohane akulemba kuti: “Tawonani adza ndi mitambo; ndipo diso lirilonse lidzampenya Iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse apadziko adzamlira Iye.” Panopo Baibulo likutchula kuwona, osati ndi maso enieni, koma m’lingaliro la kuzindikira kapena kumva. Motero, pamene munthu amva kapena azindikira chinthu, iye anganene kuti, ‘Ndikuwona.’ Baibulo, kunena zowona, limatchula “maso a kuzindikira kwanu.” (Aefeso 1:8, King James Version) Motero kanenedweko “diso lirilonse lidzampenya Iye” kamatanthauza kuti munthu aliyense pa nthawi imeneyo adzamva kapena kuzindikira kuti Kristu wafika.
14. (a) Kodi ndani amene akutanthauzidwa mwakuti “amene anampyoza”? (b) Kodi nchifukwa ninji kudzakhala chisoni chachikulu pamene aliyense potsirizira pake azindikira kufika kwa Kristu?
14 Awo amene “anapyoza” kwenikweni Yesu salinso amoyo padziko lapansi. Motero iwo amaphiphiritsira anthu amene, mwa kuvulaza atsatiri amakono a Kristu, akutsanzira khalidwe la anthu a m’zaka za zana loyamba amenewo. (Mateyu 25:40, 45) Nthawi idzafika posachedwapa yakuti Kristu aphe anthu oipa oterowo. Iwo achenjezedweratu za zimenezi. Pamene kupha kumeneku kuchitika, iwo “adzawona” kapena kuzindikira chimene chirinkuchitika. Ndipo chisoni chawo chidzakhaladi chachikulu!
KODI KRISTU AKUBWERANSO KUDZIKO LAPANSI?
15. Kodi liwulo “kubwera” kawirikawiri limagwiritsiridwa ntchito m’njira yotani?
15 Kubwerera sikumatanthauza nthawi zonse kuti munthuyo amapita kumalo enieni. Motero anthu odwala amanenedwa kukhala ‘akubwerera ku thanzi.’ Ndipo wolamulira wapapitapo anganenedwe kukhala ‘akubwerera ku ulamuliro.’ M’njira yofananayo, Mulungu anauza Abrahamu kuti: “Ndidzabwera kwa iwe, pakufika nyengo yake, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” (Genesis 18:14; 21:1) Kubwereranso kwa Yehova kunatanthauza, osati kubwerera kwenikweni, koma kutembenuzira maso ake kwa Sara kuchita zimene iye adalonjeza.
16. (a) Kodi Kristu akubweranso kudziko lapansi m’njira yotani? (b) Kodi Kristu anabweranso liti, ndipo kodi nchiyani chimene chinachitika pa nthawi imeneyo?
16 M’njira imodzimodziyo, kubweranso kwa Kristu sikumatanthauza kuti iye akubweranso kwenikweni kudziko lapansili. M’malo mwake, kumatanthauza kuti iye amatenga ulamuliro Waufumu kulinga ndi dziko lapansili ndi kutembenuzira maso ake ku ilo. Iye sakufunikira kusiya mpando wake wachifumu wakumwamba ndi kutsikira kwenikweni kudziko lapansi kuti achite zimenezi. Monga momwe tawonera m’mutu wapitawo, umboni Wabaibulo umasonyeza kuti m’chaka cha 1914 C.E. nthawi ya Mulungu inafika yakuti Kristu abwerenso ndi kuyamba kulamulira. Kunali pa nthawi imeneyo pamene mfuu inamvedwa kumwamba: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mpha mvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake.”—Chivumbulutso 12:10.
17. Popeza kuti kubweranso kwa Kristu nkosawoneka, kodi iye anaperekanji kotero kuti tikathe kudziwa kuti iye adabweranso?
17 Popeza kuti kubweranso kwa Kristu nkosawoneka, kodi pali njira yotsimikizirira kuti kwachitikadi? Inde, iripo. Kristu mwiniyo anapereka “chizindikiro” chowoneka mwa chimene tingadziwire kuti iye wafika mosawoneka ndipo mapeto a dziko ayandikira. Tiyeni tipende “chizindikiro” chimenecho.
[Chithunzi patsamba 142]
Kristu anapereka thupi lake kukhala nsembe. Iye sakadalitenganso ndi kukhala munthu kachiwiri
[Zithunzi pamasamba 144, 145]
Kodi nchifukwa ninji Maliya wa Magadala anayesa Yesu kukhala wakumunda pambuyo pa chiukiriro chake?
Kodi ndim’thupi lanyama lotani limene Yesu woukitsidwayo anapempha Tomasi kupisa dzanja lake?
[Chithunzi patsamba 147]
Kristu anayenera kubweranso mu mkhalidwe umodzimodziwo umene iye anachokera padziko lapansi. Kodi iye anachoka mu mkhalidwe wotani?