-
Kodi Mulungu Ndi Ndani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
2. Kodi Baibulo limatiuza zotani zokhudza Yehova?
Baibulo limatiuza kuti pa milungu yonse imene anthu amailambira, Yehova yekha ndiye Mulungu woona. N’chifukwa chiyani tikutero? Pali zifukwa zambiri. Yehova ndi wolamulira wamkulu, ndipo iye yekha ndi “Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” (Werengani Salimo 83:18.) Iye ndi “Wamphamvuyonse,” kutanthauza kuti ali ndi mphamvu zochitira chilichonse chimene wasankha. Iye ndi amene ‘analenga zinthu zonse,’ zakumwamba ndi zapadziko lapansi. (Chivumbulutso 4:8, 11) Mosiyana ndi wina aliyense, Yehova alibe chiyambi komanso alibe mapeto.—Salimo 90:2.
-
-
Tingatani Kuti Mulungu Azisangalala Ndi Kulambira Kwathu?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
Yehova amafuna kuti tizilambira iye yekha chifukwa ndiye Mlengi wathu. (Chivumbulutso 4:11) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kukonda ndi kulambira iye yekha basi, popanda kugwiritsa ntchito mafano, zithunzi kapena chifaniziro china chilichonse.—Werengani Yesaya 42:8.
Yehova amafuna kuti tizimulambira m’njira “yoyera ndi yovomerezeka.” (Aroma 12:1) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kumvera malamulo ake pa moyo wathu. Mwachitsanzo, anthu amene amakonda Yehova amamvera ndi kutsatira malamulo ake pa nkhani yokhudza ukwati. Ndipo amayesetsa kupewa makhalidwe omwe amaika moyo pangozi monga kusuta fodya, kugwiritsa ntchito mankhwala molakwika kapenanso kumwa mowa mwauchidakwa.a
-