Mtendere Potsirizira!—Pamene Mulungu Alankhula
“Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.”—YESAYA 9:7.
1. Pamene atsogoleri a dziko mosalekeza akulankhula ponena za mtendere, kodi ndi chiyani chomwe chakhala chikuwonedwa mu mbiri ya mtundu wa anthu?
ATSOGOLERI adziko mosalekeza amalankhula ponena za mtendere, ndipo anthu mwachisawawa amanena kuti amaukhumba iwo. Koma, mkhalidwe lerolino umatikumbutsa ife za zimene mneneri Yeremiya ananena: “Tinayang’anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo tawona kuwopsyedwa!” (Yeremiya 8:15) Kwenikweni, kuyambira pamene Kaini anapha Abele, dziko silinakhale konse ndi mtendere weniweni koma lokanthidwa ndi chiwawa. Ndipo zaka zathu za zana la 20 zakhala m’badwo wachiwawa chochuluka kuposa mibadwo yonse pamene nkhondo zachititsa chifupifupi imfa mamiliyoni zana. Mu nthawi yathu, 97 peresenti ya anthu onse a padziko lapansi yakhala italowetsedwamo mu chifupifupi nkhondo imodzi. Chotero, pamene atsogoleri a dziko akulankhula ponena za mtendere, iwo atsogolera anthu awo mu tsoka limodzi motsatizana ndi linzake.
2. Kodi ndi chochitika cha kuwonjezeka kwa chiwawa chiti chomwe chikuwonedwa mu mitundu yonse?
2 Ku chiwawa chonsecho kuyenera kuwonjezeredwa chiwerengero cha tsiku ndi tsiku cha upandu. Mwachitsanzo, mu United States, chaka chiri chonse chifupifupi anthu 20, 000 amaphedwa. Akazi oposa 80, 000 amagwiriridwa chigololo, ndi kugwiriridwa chigololo kwambiri kosachitiridwa ripoti. Chifupifupi akazi mamiliyoni 2 anamenyedwa kwadzawoneni ndi mwamuna amene amakhala naye. Ndipo chifupifupi gawo lachinayi la nyumba zonse zakhala minkhole ya mtundu uliwonse wa upandu. Ripotilo likumaliza: “Ife takhala chitaganya cha chiwawa cha dzawoneni.”Mkhalidwewo uli wofanana m’maiko ena ambiri.
3. Kodi ndi chiwawa chiti chokulirapo chomwe chingachitidwe ku banja la munthu tsopano?
3 Komabe, zonsezo siziri kanthu kuyerekezedwa ndi chiwawa chomwe chikanachitidwa lerolino ndi zida za nyukiliya. Ziripo zambiri za izo zokwanira kupha nzika iriyonse ya padziko lapansi kuwirikiza nthaŵri 12! Dokotala ananena kuti: “Mankhwala amakono sangapereke chiri chonse kwa minkhole ya kuwombana kwa nyukiliya.” Nchifukwa ninji ayi? Wina anayankha: “Adokotala ambiri, anamwino, ndi odziwa kukonza zinthu adzakhala ataphedwa . . . zipatala zidzakhala zitawonongedwa. Chotero padzakhala ochepa kwambiri osiyidwa omwe adzakhala ndi chidziŵitso chokwanira ndi zida za kupulumutsira aliyense.”
4, 5. (a) Kodi ndi ndemanga yotani imene chofalitsidwa chimodzi chinapanga ponena za kusoweka kwa mtendere mu nthawi yathu?(b) Kodi ndimotani mmene yemwe anali kale nduna ya boma mofananamo anachitira ndemanga?
4 Ponena za kusoweka kwa mtendere mu nthawi yathu, nkhani yaikulu mubukhu lachaka la Encyclopedia Britannica inali ndi mutu wakuti: “Dziko Lathu logawanikana—Chiwopsyezo cha chipolowe cha Dziko Lonse.” Iro linati: “Itapita 1945 malingaliro akuti ‘kupita patsogolo’ anali mwanjira ina yake osapeweka konse ndi kuti mtsogolo mwa dziko la makono mukanakhala mwachigwirizano ndi chimvano analingaliridwa. ” Koma malingaliro amenewo, iro linati, “anatsimikizira kukhala osocheretsa kotheratu,” kuwonjezera: “Chomwe chachitika m’malo mwake . . . chiri chakuti dziko liri mwakachetechete koma mosakhazikika likubwerekedwa ndi kugawanika kwa pang’onopang’ono. Maiko ambiri amene chigwirizano chawo cha khalidwe ndi uzimu chinawonedwa kukhala chosanunkha kanthu akhala akusweka pakati. . . [mu] miyambo, mafuko, chipembedzo, [mipatuko],. . . magulu amizinda, magulu akupha, machitachita a uchigawenga, nkhondo za chiweniweni, ndi magulu a zikondwerero za iwo eni ang’ono ndi amisala.”
5 Mofananamo, yemwe anali kale nduna yapamwamba ya boma mu United States ananena kuti: “Zinthu zimene zimapangitsa kusakhazikika kwa dziko lonse ziri kupeza chipambano chapamwamba cha mu mbiri pa mphamvu zomwe zikugwira ntchito kaamba ka kugwirizana kolinganizika. Mapeto osapeweka a kundandalitsa kopatulidwa kuli konse kwa zochitika za dziko lonse kuli kwakuti phokoso la mayanjano, kusakhazikika kwa ndale zadziko, mavuto a za chuma, ndi kuwombana kwa mitundu yonse moyenerera adzakhala ofalikira mkati mwa nthawi yotsalira ya zaka za zana lino.” Iye akumaliza: “Chiwopsyezo chomwe chikuyang’anizana ndi mtundu wa anthu, mwachidule, chiri . . . chipolowe cha dziko lonse.”
‘Alendo Ochokera Mlengalenga’
6. Kodi ndimotani mmene mkonzi wa nyuzipepala analongosolera kawonedwe kamene alendo ochokera mlengalenga angachite ponena za dziko lerolino?
6 Mkayang’anidwe ka zonsezi, mkonzi analemba mu nyuzipepala ya ku Cleveland: “Ngati alendo akanafika sabata lamawa kuchokera kumlalang’amba wakutali, kodi tikanawauza iwo kuti tikanafunikira kudzipha ndi cholinga chofuna kukhazikitsa upamwamba wa chikomyunizimu kapena chikapitalizimu? Kodi tikanawalongosolera kuti ife tinali mitunduyo imene inadzigawanitsa kukhala mitundu, ndi kuti mitundu imeneyo inalumbiritsidwa kuti iphane wina ndi unzake m’mapwando anthawi ndi nthawi okhetsa mwazi? Kodi tikanalongosola motani kuti talola ena a mtundu wathu kufa ndi njala ndipo ena kulowa m’mkhalidwe woluluzika ndi waumbuli chifukwa chakuti kupangidwa kwa imfa yaunyinji kunali koyambirira kwa ife? Alendo ochokera ku mlalang’amba wakutali amenewo mowonadi adzatilongosola ife kumbuyoko monga abulutu. . . . Tingadandaule kuti ifenso tapanga zinthu zaluso zambiri ndi kukhulupirira mu chiweruzo cholungama. Iwo angamwetulire mwachison ndi kuchoka kuphulika kusanachitike.”
7, 8. (a) Kodi ndi alendo amphamvu ati amene akupanga kufufuza kwa mtundu wa anthu? (b) Kodi nchifukwa ninji iwo ali pano?
7 ‘Komabe,’ ena anganene kuti, ‘palibe “alendo ochokera mlengalenga” amene akupanga mafufuzidwe otero.’ Ayi, osati kuchokera mu mlengalenga wa kuthupi. Koma kwa zaka zina tsopano, alendo amphamvu, anzeru zapamwamba akhala akupenda mosamalitsa zimene mtundu wa anthu wakhala ukuchita kwa iwo wokha ndi ku dziko lapansi. Mkuwonjezerapo, iwo akuwona ku icho kuti uthenga womvekera bwino ukuperekedwa “kuphulika kusanachitike.”
8 Kodi ndani amene ali alendo amphamvu amenewo omwe akhala akupanga kuyendera kotero pa mtundu wa anthu? Mawu a Mulungu amatiuza ife kuti iwo ali oimira a Mulungu m’mabwalo amizimu, angelo okhulupirika, amene iye anawatumiza ku dziko lapansi kudzalizonda. Ponena za zolengedwa zauzimu zimenezi, Masalmo 103:20 amanena kuti: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; ndi a mphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake.” Angelo amphamvu amenewa mobwerezabwereza akutchulidwa mu Baibulo. Mwachitsanzo, pa Mateyu mutu 25 ulosi ponena za nthawi yathu umanena mu versi 31 ndi 32: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake; ndipo adzasonkhanitsa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.”
9. Kodi ndi mbali iti imene Kristu Yesu akuchita mkati mwa kuyendera kwa mtundu wa anthu kumeneku?
9 “Mwana wa munthu” ameneyo ali woimira wamkulu wa Mulungu, Yesu Kristu. Pambuyo pa kuukitsidwa kwake kupita kumwamba, iye anadikira kuti Yehova ampatse ntchito yapadera imeneyi. Monga mmene Masalmo 110:1 amalongosolera iyo, Yehova anati kwa iye: “Khalani pa dzanja la manja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.”Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumasonyeza kuti nthawi ya Mulungu ya kutumiza cholengedwa chake chauzimu champhamvu mkachitidwe inabwera mu chaka cha 1914.
10. Kodi ndi angelo angati amene angakhale ndi Kristu pamene akuthandiza mu ntchito ya kulekanitsa?
10 Koma iye sadzabwera yekha, popeza Mateyu 25:31 amanena kuti “angelo onse” adzakhala ndi iye. Kodi iwo angakhale ochuluka motani? Chivumbulutso 5:11 chikunena kuti: “Ndipo ndinawona, ndipo ndinamva mawu a angelo ambiri pozinga mpando wachifumu [wa Mulungu]. . . ndipo mawerengedwe awo anali zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi.”Zikwi khumi ndi 10, 000. Zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi ndi 10, 000 kuchulukitsa 10, 000, chiwonkhetso cha angelo mamiliyoni 100! Komabe, Chivumbulutso chikulankhula m’mkhalidwe wa pulula, wa “zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi” za angelo akutumikira Mulungu. Kunena kuti mazana amamiliyoni, mwinamwake mabiliyoni kapena owonjezereka. Pansi pa chitsogozo cha Kristu, zolengedwa zauzimu zimenezi zikuthandiza oimira a Mulungu pa dziko lapansi mkulekanitsa mtundu wa anthu mu magulu awiri, gulu limodzi kaamba ka “chiwonongeko chotheratu,” ndipo lina kaamba ka “moyo wosatha.”—Mateyu 25:46; onaninso Mateyu 13:41, 42.
“Mbiri Yabwino Yosatha”
11. Kodi nchiyani chimene chiri “mbiri yabwino yosatha” yomwe mphamvu za angelo zikuchirikiza pa nthawi ino?
11 Kodi ndi uthenga weniweni uti umene alendo aungelo amenewa akuchirikiza padziko lapansi panthawi ino? Chivumbulutso 14:6 chimatidziwitsa ife: “Ndipo ndinawona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo uthenga wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uli wonse wa fuko ndi manenedwe ndi anthu.” Kodi nchiyani chimene chiri “mbiri yabwino yosatha” imeneyi? Iyo iyenera kukhala vogwirizana ndi chimene Yesu ananena kuti chidzakhala chimodzi cha zitsimikiziro zambiri zakuti tikukhala mu masiku otsiriza. Pa Mateyu 24:14 iye analengeza: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa mu dziko lonse lapansi [lokhalidwa ndi anthu NW] ukhale umboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.
12, 13. (a) Kodi ndi chiyani chimene chiri ulamuliro wa Ufumu? (b) Kodi nchifukwa ninji uthenga wa Ufumu uli mbiri yabwino koposa?
12 Ufumu wa Mulungu uli boma lakumwamba lomwe lidzalamulira padziko lonse lapansi pambuyo pa kuchotsedwa kwa maulamuliro a anthu alipowa. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Mfumu yake iri Kristu Yesu, ndipo iye ali ndi olamulira anzake limodzi naye. (Chivumbulutso 14:1-4; 20:4) Ufumu umenewo uliumene unalankhulidwa pa Danilei 7:14 m’mawu awa: “Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzawonongeka.”
13 Nchifukwa ninji uthenga ponena za ulamuliro wa Ufumu uli mbiri yabwino yotero, mbiri yabwino koposa? Chifukwa udzabweretsa dziko latsopano, kakhazikitsidwe katsopano ka mtundu wa anthu. Pansi pa Ufumu wa Mulungu mtundu wa anthu udzalandira madalitso ozizwitsa kotero kuti Masalmo 37:11 amanena za awo amene adzakhalako panthawiyo “Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Inde, “Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.” (Masalmo 29:11) Lerolino, Ufumuwo usanatenge ulamuliro wa zochita zonse za dziko lonse lapansi, mbiri yabwino ya ulamuliro wake wokhazikika, wamtendere mmanja mwa “Kalonga wa Mtendere” ikulalikidwa mu mitundu yonse. Ichi chikuchitidwa ndi atumiki a padziko lapansi a Mulungu pansi pa chitsogozo cha Kristu ndi angelo.—Yesaya 9:6, 7.
14. (a) Kodi ndi njira imodzi iti imene motsimikizirika tingazindikirire atumiki a Mulungu a padziko lapansi? (b) Kodi ndimotani mmene dalitso lotsimikizirika la Yehova lakhalira pa iwo?
14 Kodi ndani amene ali atumiki amenewa a Mulungu a padziko lapansi? Chabwino, kodi ndani okha amene mokhazikika amaitanira pa anthu ndi mbiri yabwino ya Ufumu? Ngakhale otsutsa amawazindikira iwo monga Mboni za Yehova. Tsopano oposa mamiliyoni atatu amphamvu, mathayo olengeza Ufumu amenewo akuwonjezereka mofulumira. Chaka chapita, atumiki atsopano a mbiri yabwino 225, 868 anakhazikitsidwa. Ndipo mu chaka chimodzi chimenecho, mipingo yatsopano ya Mboni za Yehova 2, 461 inakhazikitsidwa padziko lonse, avereji yoposa 6 pa tsiku liri lonse, kupanga chiwonkhetso cha mipingo 52, 177 mu maiko 208. Indedi, ulosi wa pa Yesaya 60:22 ukuwona kukwaniritsidwa kwake: Yehova akufulumiza ntchito yake yolalikira ndi yosonkhanitsa “m’nthawi yake.” Ndipo tsopano iri nthawi imeneyo!
15. Kodi ndi ati omwe ali maziko kaamba ka kuweruzira anthu lerolino?
15 Mmene anthu amavomerezera ku mbiri ya ulamuliro wa Ufumu ali maziko akudziwira kuti kaya iwo adzapatulidwa kaamba ka “chiwonongeko chosatha” kapena kaamba ka “moyo wosatha” mu dziko latsopano. Ambiri amavomereza monga mmene anachitira awo olongosoledwa pa 2 Mbiri 36:15, 16: “Yehova . . . anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo . . . koma ananyodolo mithenga ya Mulungu, napeputsa mawu ake, naseka aneneri ake, mpaka ukali wa [Yehova, NW] unaukira anthu ake.” Koma ena amavomereza mwa chiyanjo ndi kubwera pansi pa chinjirizo la Yehova. Koma wondimvera ine [nzeru yeniyeni], adzakhala wosatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”-Miyambo 1:20, 33; Mateyu 25:34-46.
Makamu Akumwamba ku Ntchito
16. Kodi ndimotani mmene Mulungu posachedwapa adzalankhulira kwa mtundu wa anthu wosamvera?
16 Pasanapite nthawi yaitali, ntchito yolalikira ya atumiki a Yehova idzamalizidwa ku mlingo umene iye anakhazikitsa. Kuleza mtima kwake ndi mtundu wa anthu wosamvera kudzafika ku mapeto ake. Uthenga wa mtendere umene iye wakhala akulankhula kwa mtundu wa anthu m’mbadwo uno udzasintha. M’malo mwake, “pomwepo adzalankhula nawo mu mkwiyo wake, nadzawaopsya m’ukali wake.” (Masalmo 2:5) Monga mmene Yehova iye mwini akulongosolela: “Pakuti ndanena mu nsanje yanga ndi m’moto wa kuzaza kwanga.” (Ezekieli 38:19) Kenaka iye adzapatsa Yesu Kristu chizindikiro cha kuyendetsa makamu ake akumwamba ku ntchito motsutsana ndi dziko iri loukira ndi losayeruzika.
17. Kodi ndimotani mmene mphamvu ya mngelo mmodzi yekha inasonyezedwera?
17 Chimene makamu amenewa adzakwaniritsa chingawonedwe ndi chimene chinachitika kwa Asuri pamene nthaŵi ya Mulungu inafika ya kuchita motsutsana ndi iwo. Mafumu Achiŵiri 19:35 amanena kuti: “Ndipo kunali usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka nakantha m’misasa ya Asuri zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu . . . onsewo ndi mitembo.” Chimenecho ndi kokha chimene mngelo m’modzi yekha anachita! Zimene zikwi khumi kuchulukitsa zikwi khumi za iwo adzakwaniritsa posachedwapa zidzakhala zochititsa mantha kwambiri.
18. Kodi chiwonongeko chidzakhala chokwanira bwino motani pa mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu?
18 Yeremiya 25:31-33 amalongosola chimene chidzachitika m’mawu awa: “Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa adzawapereka kulupanga, ati Yehova. Yehova wa makamu atero, tawonani, zoipa zidzatuluka ku mtundu kunka ku mtundu, ndipo namondwe adzauka kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.”
19. Kodi ndi zinthu zowonjezereka ziti zimene Chivumbulutso mutu 19 umawonjezera?
19 Chivumbulutso mutu 19 chimalongosola ndimotani mmene Yehova adzakwaniritsira zonsezi. Iri mwanjira ya kupanga Mfumu yake Yesu Kristu kupita ku ntchito ndi, monga mmene versi 14 likunenera, “Magulu ankhondo okhala m’mwamba anamtsata iye.” Kenaka versi 17 ndi 18 likunena kuti: “Ndipo ndinawona mngelo alikuima m’dzuwa; ndipo anapfuula ndi mawu akulu akunena ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: Idzani kuno, sonkhanani pa phwando la Mulungu wamkulu, kuti mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitawo, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi ang’ono ndi akulu.” Ndipo maversi 19 kufika ku 21 akulongosola ponena za chiwonongeko cha magulu onse a anthu chifukwa anakana kumvera pamene Mulungu analankhula kupyolera mwa athenga ake a padziko lapansi.
20. Kodi nchifukwa ninji dziko iri silingathe pangozi ya nyukiliya?
20 Chotero, nthawi idzafika posachedwapa ya Mulungu ya kubweretsa kumapeto chiwawa chonsechi, kugawanika kwa dongosolo ladziko. Koma mapeto amenewo sadzakhala kudziwononga kwaumwini kupyolera mu nkhondo ya nyukiliya pakati pa mitundu. Ngati chimenecho chitachitika, olungama adzathedwa psyiti limodzi ndi oipa. Komabe, “kuphulika” kwa Mulungu motsutsana ndi dziko iri sikudzakhala konga ngati kumeneko, koma kudzakhala kosankha. Padzakhala opulumuka kulowa mu dziko latsopano. Monga mmene Miyambo 2:21, 22 imanenera: “Pakuti owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”
21. Kodi ndi mafunso owonjezereka ati amene adzalingaliridwa mu nkhani yathu yotsatira?
21 Kodi nchifukwa ninji dziko iri lafika ku mkhalidwe umenewo kumene chiwonongeka chadziko lonse chimenechi chayandikira? Kodi sikuli kosatheka kuti zoyesayesa za posachedwapa za mtendere za atsogoleri a dziko zidzabala zipatso, kotero kuti dongosolo la kachitidwe ka zinthu iri lingasungidwe? Ndipo ngati tikufuna kukhala pakati pa “owongoka mtima” ndi “olungama” amene adzapulumuka kulowa mu dziko latsopano ndi kupitirizabe kukhala ndi moyo, kodi ndimotani mmene tingadzisungire ife eni mu nthawi iyi yofunika kwambiri m’mbiri yonse ya munthu? Nkhani yathu yotsatira idzalingalira mafunso amenewa.
Kodi Mayankho Anu ndi Otani?
◻ Kodi ndimotani mmene kusoweka kwa mtendere kwakhalira kowonekera, makamaka mu nthawi yathu?
◻ Kodi ndimotani mmene mphamvu za angelo zikulowetsedweramo mu ntchito ya kulekanitsa mtundu wa anthu lerolino?
◻ Kodi nchifukwa ninji uthenga wa Ufumu uli “mbiri yabwino yosatha”?
◻ Kodi ndi pa maziko ati pamene anthu adzaweruzidwira kaamba ka moyo kapena kaamba ka imfa?
[Chithunzi patsamba 13]
Ntchito ya Mboni za Yehova ikuchirikizidwa ndi mphamvu zaungelo.