Mutu 2
Kodi Anthu Angadzetse Mtendere Wosatha ndi Chisungiko?
1. Kodi ndimafunso otani amene tifunikira kufunsa, ndipo chifukwa ninji?
KUTI CHIYEMBEKEZO chikhale ndi tanthauzo lirilonse, chiyenera kuzikidwa pa zenizeni, ndi chowonadi. Ziyembekezo zonyenga zimangochititsa anthu kusawona zenizeni. Chifukwa chake, tifunikira kufunsa kuti: Kodi tikuzindikira bwino lomwe mmenedi mavutowo aliri akulu amene ayenera kuthetsedwa kudzetsa mtendere wowona ndi chisungiko? Kodi tikuzindikira mmene mkhalidwewu wafikira kukhala wofulumira? Kodi pali umboni uliwonse wakuti zothetsera za anthu zikakhala zolingana ndi ukulu wa ntchitoyo?
2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji kufunafuna mtendere ndi chisungiko kulidi kofulumira kwambiri lerolino? (b) Kodi ndiziwopsezo zina ziti zimene ziripo ku moyo padziko lapansi?
2 Kwazaka zikwi zambiri anthu afunafuna mtendere wosatha ndi chisungiko, mosaphula kanthu. Koma tsopano mkhalidwewo ngwofulumira koposa chifukwa cha chiwopsezo cha nkhondo yanyukliya. Lipoti la ku Canada linachenjeza kuti: “Palibe chinthu chonga nkhondo yanyukliya yokhoza kupambanidwa chifukwa chakuti ziyambukiro zake zapambuyo zingakhale zowopsa kwambiri kotero kuti opulumuka akanasirira akufa.”3 Akumasonyeza chifukwa chake, katswiri wasayansi yopenda za m’mwamba Carl Sagan anafotokoza kuti: “Tsopano pali zida zankhondo zanyukliya zoposa 50 000, . . . zokwanira kufafaniza Ahiroshima miliyoni imodzi.” Iye anawonjezera kuti: “Palibe chikaikiro chakuti kutsungula kwathu kwa dziko lonse kungawonongedwe.”4
3 Ndiponso, ziwopsezo zina zikuwopseza moyo padziko lapansi. Chimodzi ndicho kuipitsidwa kwa padziko lonse lapansi kwamtunda, mpweya, ndi madzi. China ndicho kuchulukitsitsa kwa chiwerengero cha anthu limodzi ndi njala yake yotsagana nako, nthenda, ndi chipolowe.
4. Kodi ndimotani mmene mkhalidwe wa anthu lerolino wafotokozedwera?
4 Ponena za ziwopsezo zosiyanasiyana zimene anthu tsopano akuyang’anizana nazo, gulu lamtendere mu Norway linati: “Mkhalidwe wa mitundu yonse lerolino ngwophatikizapo mavuto aakulu okantha pafupifupi mbali zonse za zochita za anthu: za chuma ndi za makhalidwe a anthu, za ndale zadziko ndi za nkhondo, zauzimu ndi zamakhalidwe.” Ilo linawonjezera kuti: “Chiwawa chikuwonjezereka ndipo kugwiritsira ntchito chikakamizo ndiko chiwiya cha njira yochitira zinthu ndipo makambitsirano akhala owanda. . . . Kulingana pakati pamtendere ndi nkhondo kwafikira kukhala paupanndu mowonjezerekawonjezereka.”5 Kodi izi zikutsogolera kuti? Mlembi wamkulu wa UN anachenjeza kuti: “Tikuyandikira mochititsa mantha ku chipolowe chatsopano cha m’mitundu yonse.”6
Dziko Lopanda Nkhondo mwa Zoyesayesa za Anthu?
5. Kodi nchiyani chimene mbiri yakale imasonyeza ponena za kukhoza kwa anthu kuthetsa nkhondo?
5 Kodi pali chifukwa chokhulupiririra kuti anthu angathetse nkhondo? Mogwirizana ndi mbiri, pakhala zaka zowerengeka za apa ndi apo pamene dziko lapansi iri linali lopandiratu nkhondo. M’zaka za zana la20 zino zokha, pafupifupi anthu mamiliyoni 100 aphedwa m’nkhondo! Palibe kaya Chigwirizano cha Amitundu chamakedzana kapena Mitundu Yogwirizana yalerolino imene yakhoza kuimika kuphana uku.
6. Kodi kuwopa nkhondo yanyukliya ndiko maziko abwino amtendere?
6 Koma kodi kuwopa chiwonongeko cha zida zankhondo za nyukliya sikudzasintha zimenezi? Kodi kuwopa kokwanira zida zankhondo za nyukliya sikunadzutsidwe kalero mu 1945 pamene mabomba a atomu anafafaniza mizinda iŵiri ya Ajapani? Eya, kuyambira nthawiyo kuunjika zida zankhondo za nyukliya zamphamvu kwambiri kwakula kuŵirikiza nthawi chikwi. Ndipo kuyambira 1945 chabe anthu oyerekezeredwa kukhala 35 000 000 aphedwa m’nkhondo ndi m’zipanduko zophatikizapo maiko oposa 100. M’chaka chimodzi chaposachedwapa mitundu 45 inaphatikizidwa m’nkhondo!7 Ayi, Kuwopa zida za nyukliya sikunaimike nkhondo.
7. Kodi kusaina mapangano a kuleka kupanga zida zankhondo kapena mapangano amtendere kumatsimikiziritsa mtendere wokhalitsa?
7 Zowonadi, mitundu imatero ndipo mwinamwake idzapitirizabe kusaina mapangano oleka kupanga zida zankhondo kapena mapangano a mtendere. Mkati mwa zaka zenizeni mazana ambiri zapita zikwi zambiri za amenewa zasainidwa. Komabe, paliponse pamene lingaliro lankhondo linakhala lamphamvu kwambiri, mapangano amenewa anakhala mapepala opanda ntchito. Mitundu Yogwirizana yalepheranso kuimitsa nkhondo, chifukwa chakuti ngakhale kuli kwakuti pafupifupi maiko onse lerolino ali mbali ya UN, amainyalanyaza mwadala. Chotero kodi kuli kwanzeru kuyembekezera kuti atsogoleri adziko amtsogolo adzasunga mawu awo kwambiri kuposa a m’nthawi zakale?
8. Kodi ndimotani mmene Baibulo lanenera chowonadi ponena za kulephera kwa anthu kupeza mtendere wokhalitsa?
8 Kumbali ina, lingaliro la Baibulo nlogwirizana ndi zochitika za m’mbiri. Iro silimavomereza kuika chiyembekezo chathu m’zoyesayesa za anthu za kubweretsa mtendere. Mmalo mwake, lidaneneratu kalekale kuti zoyesayesa za anthu sizikabweretsa konse mtendere wosatha. Iro linachenjezeratu kuti mwamsanga dongosolo lino lazinthu lisanathe, nkhondo ndi zipolowe zikafalikira padziko lonse, pamene ‘mtundu udzaukirana ndi mtundu ndi ufumu ndi ufumu wina.’ (Luka 21:9, 10, 31; Chivumbulutso 6:1-4) Zochitika za dziko chiyambire 1914 zakwaniritsa maulosi amenewo. Chotero m’malo mwa kudzutsa ziyembekezo zonyenga, Baibulo motsimikiziradi limalengeza kuti: “Njira ya munthu siri mwa iyemwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
Kodi Anthu Angagonjetse Bomba la Chiwerengero cha Anthu?
9-11. (a) Kodi chiwerengero cha anthu cha dziko lapansi chikuwonjezereka mofulumira motani? (b) Kodi ndimkhalidwe wotani umene umakantha ziwerengero zazikulu za anthu?
9 Chiwerengero cha anthu cha dziko lapansi chinafika pa anthu biliyoni imodzi m’zaka za zana la19. Tsopano chiri pafupifupi anthu mabiliyoni asanu,8 pamene biliyoni imodzi yatsopano iriyonse imadza mofulumirirapo kwambiri. Chaka chiri chonse, pafupifupi anthu owonjezereka mamiliyoni 90 amawonjezeredwa! Ndipo unyinji wa kuchuluka kumeneku umangowonjezera mavuto m’zigawo zimene umphawi, njala, ndi nthenda ziri zochuluka kale. Kuwonjezereka kwa chiŵerengero cha anthu uku pa chifukwa chabwino kwatchedwa bomba la chiŵerengero cha anthu. The New York Times inanena kuti: “Kuli kotheka kuti mbali zazikulu za dziko lapansi zidzasandulizidwa kukhala chipululu cha mchenga chifukwa cha kupanikizana kwa chiwerengero cha anthu chosalamulirika ndi umphaŵi mofanana ndi chipiyoyo cha nyukliya.”9
10 Ponena za ukulu wa njala ya dziko lonse, magazine a Time anati: “Vuto la njala lerolino ndilosiyana kwambiri ndi lapita . . . Tsopano pali chakudya chochepa kwambiri m’mbali zochuluka zadziko, chaka chirichonse, kotero kuti 25 peresenti yonse yachiŵerengero cha anthu pa mbulumbwayi nchanjala kapena nchodya mosakwanira.”10 Magwero ena anayerekezera kuti chaka chirichonse makanda mamiliyoni 11 amafa asanathe chaka chimodzi chifukwa cha ziyambukiro zakudya mosakwanira ndi nthenda.
11 Lipoti limodzimodzilo likufotokoza kuti: “Munthu wokwanira mmodzi mwa asanu amakhala mu umphaŵi wotheratu, mkhalidwe wosoŵa chochita kotheratu kotero kuti ngwakupha mwakachetechete.”11 Ndipo izi, inatero The Toronto Star, zinali pambuyo pa msonkhano wa dziko lonse wa chakudya mu Roma zaka zoposa khumi zapita “utanena kuti, mkati mwa zaka khumi, palibe mwana amene adzakagona ndi njala, palibe banja limene likawopera kusoŵa chakudya tsiku lotsatira ndipo palibe mtsogolo mwa munthu mukafupikitsidwa ndi kudya mosakwanira.”12 Ha malonjezo otero anatsimikizira kukhala opanda pake chotani nanga! Zenizeni ziri monga momwe Guardian ya ku Mangalande inanenera kuti: “Dziko liri pamphembenu pa chiwonongeko cha anthu. . . . Maiko onse awona ziyembekezo zawo zamtsogolo zikuzimiririka.”13
12. Kodi kuchepetsa chiwerengero cha ndalama zowonongedwera pa zankhondo kungathetsedi vutolo?
12 Mbali yaikulu ya vutolo, siiri ndi dziko lapansi, koma ndi olamulira ndi anthu ndi makhalidwe awo. Mwachitsanzo, tsopano mitundu imawonongera pafupifupi madola tiriliyoni imodzi (mabiliyoni chikwi) pa zida zankhondo chaka chiri chonse pamene anthu mamiliyoni ambiri akufa ndi ndi njala. Koma ngakhale ngati kuunjika zida zankhondo kochititsa mantha uku kukanalekeka, dongosolo la chuma logaŵanika la dziko likanachita motsemphana ndi chothetsera vutoli chowona chirichonse. Kaŵirikaŵiri, pamene chakudya chiripo, chikhumbo cha mapindu aakulu chimalepheretsa kugaŵiridwa kwake kwa awo amene ali osoŵa. M’maiko ena, maboma amalipira alimi kuti asalime mbewu zakutizakuti chifukwa chakuti kuchuluka kwa dzinthu kungachititse kutsika kwambiri kwa mitengo. Zakudya zambirimbiri zawonongedwadi kuti pasakhale zowonjezereka.
13. Kodi Baibulo linalondola pamene lidaneneratu mikhalidwe imene iriko panthawi ya mapeto adziko?
13 Chotero, mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwake konse kwasayansi, chitaganya chamakono sichinakhale chokhoza kupewa mikhalidwe yeniyeniyo imene Baibulo linaneneratu. Iro molondola linaneneratu kudza kwa “kupereŵera kwa zakudya” kwadzawoneni mkati mwa “mapeto a dongosolo la zinthu” lino.—Mateyu 24:3, 7, NW; Chivumbulutso 6:5-8.
Kodi Anthu Angathe Kupanga Mtendere ndi Dziko Lapansi?
14-16. Kodi vuto la kuipitsa nlokulira motani?
14 Kwa zaka makumi ambiri anthu akhala akumenyana ndi dziko lapansi lenilenilo pa limene akukhala. Iwo achititsa zinyalala za poizoni kuunjikana m’madzi, mu mpweya, ndi m’nthaka. Mutu wankhani m’Toronto Star unalengeza kuti: “Kuipitsa Kuika Dziko Lapansi Pangozi.” Nkhaniyo inati: “Pulaneti Dziko Lapansi laukiridwa mwakupha. Ndipo woukirayo ndiye munthu.” Inanena kuti “poizoni ya kupita patsogolo kwake” tsopano akuwopseza kukhalapo kwake kwenikweniko, ndipo inanenanso kuti: “Asayansi amalingalira kuipitsidwa kwa malo okhala kulikonse kukhala kowopsa mofanana ndi chiwopsezo cha nkhondo yanyukliya.”14
15 Mwachitsanzo, ponena za United States, magazine a Discover amati: “Mankhwala aupandu ndi zitsulo zomwerekera m’dziko lapansi zikuwopseza magwero a pansi panthaka a madzi a mtunduwo. Akatswiri ena a madzi akuchita mantha akuti mwina mwake kuli kale m’mbuyo mwa alendo kupulumutsa nusu ya iwo.”15 M’Mangalande The Observer inanena kuti: Kuipitsa kochititsidwa ndi mankhwala kunali kutaipsa “unyinji wa madzi akumwa ku Mangalande.”16 Ndipo New Scientist inasimba kuti: “Gulu Lazaumoyo Ladziko likunena kuti nthenda zogwirizanitsidwa ndi madzi a litsiro zimapha anthu 50 000 tsiku lirilonse.”17
16 Mu United States kufufuza kwa akatswiri kunavumbula milingo yapamwamba ya nsanganizo za paizoni mu mpweya. The New York Times inasimba kuti: “Matani zikwi zambiri a zinthu zochititsa kensa ndi nsanganizo zina za upandu kwambiri zimatulutsidwira mu mpweya kuchokera ku mafakitale mazana ambiri.”18 Zowonjezeredwa ku izi ndizo mankhwala aupandu oikidwa m’nthaka, mwachitsanzo, monga mankhwala a kupha tizirombo, ndi kulowa mu mtandadza wa chakudya monga zakudya za zifuyo.
17. Kodi kuli kotheka kuti luso lazopangapanga lingathetse vutoli?
17 Kodi luso la zopangapanga lingawonjole? Kodi zimenezo nzotheka, popeza kuti linapanga unyinji wa mavutowo? Bukhu la Environmental Ethics limati: “Luso lazopangapanga liri mtumiki wogwiritsiridwa ntchito kokha mwapang’ono, ndi wosadalirika kwambiri. Pamene lithetsa vuto lina, iro kaŵirikaŵiri limapanga atsopano awiri—ndipo kawirikawiri ziyambukiro zawo zoipa nzovuta kuziwoneratu.”19
18. Kuti alake kuipitsa, kodi nchidziwitso chofunika chotani chimene anthu alibe, koma kodi ndani amene alinacho?
18 Kachiwirinso, Baibulo linaneneratu kusoŵa nzeru kwa munthu m’kugwiritsira ntchito kwake zinthu zambiri za dziko lapansi. Ulosi wa pa Chivumbulutso 11:18 (NW) unalankhula za nthawi pamene Mulungu akafunikira kuchitapo kanthu “kuwononga iwo akuwononga dziko lapansi.” Anthu akuvomereza kuti sakuzindikira mokwanira kucholowana kwa malo okhala a dziko lapansi. Koma Mulungu amadziŵa, popeza anawalenga ndiye. Kodi sikuli kwanzeru kuyang’ana ku Magwero amenewa kaamba ka chothetsera mavuto?
Chisungiko mwa Kuchotsedwa kwa Upandu
19. Kodi ndimantha otani amene anthu ambiri alinawo lerolino, ndipo chifukwa ninji?
19 Kuipitsa kumaika paupandu zofunika zenizeni za kukhalapo kwa anthu. Koma ndiko kuwonjezereka kwa upandu kumene kumachititsa chiŵengero chachikulu cha anthu kuchita mantha. Upandu ukuchotsera anthu owonjezerekawonjezereka chisungiko chawo osati m’mizinda yaikulu mokha komanso m’matauni aang’ono ndi m’madera a kumidzi. Sichuma chokha koma kaŵirikaŵiri thupi la munthuyo ndi moyo zimakhala paupandu.
20, 21. (a) Kodi nchifukwa ninji kupangidwa kwa malamulo atsopano sikungathetse upandu? (b) Kodi kuwonjezereka kwa kulemerera kapena njira zatsopano za kulimbana ndi upandu zingathetse vutolo?
20 Kodi anthu angadzetse chisungiko chenicheni ku maupandu amenewa, mwinamwake mwa kupanga malamulo atsopano? Pali kale malamulo zikwi zambiri m’mabukhu a malamulo adziko. Komabe, amenewa sanaletse upandu. Ndiponso, chisalungamo chozika mizu kwambiri kaŵirikaŵiri chimayambira mkati mwenimweni mwa magulu osungitsa malamulo iwo eniwo. Kusawona mtima kwa akuluakulu antchito za boma kungalepheretse zoyesayesa za kuchirikiza lamulo kowona mtima.
21 Kodi yankho liri m’njira zatsopano zofufuzira ndi kuletsa upandu? Kaamba ka njira yatsopano iriyonse yotulukiridwa, apandu amapeza njira zatsopano zoilakira. Pamenepa, kodi ulemerero wowonjezeredwa udzathetsa vutolo? Kukakhala kulakwa kunena kuti upandu uli kokha pakati pa magulu a anthu olandira ndalama zochepa. Upandu wakuba ndi pensulo nawonso ukukwera. Mwachitsanzo, mu United States chaka chirichonse okwanira mabiliyoni $80 amatayika chifukwa cha upandu wotero. Pafupifupi 30 peresenti ya mabizinesi onse amene amalephera amatero chifukwa cha uwo. South Africa akusimba kuti kuba kwa antchito kunaboloketsa pafupifupi mabizinesi 1 500 m’chaka chimodzi.20
22. Kodi ndiumboni wotani umene umasonyeza kuti kuyesayesa kwa anthu kokha sikungathetse upandu?
22 Kukwera kwa upandu sikuli ku mitundu yoŵerengeka chabe. Kukupezeka kulikonse. Tawonani mitu ya nkhani ina yochokera ku dziko lonse. Brazil: “Kukwera kwa Chiŵerengero cha Upandu.” Canada: “Chiwerengero cha Upandu wa Akazi Chikukwera.” Mangalande: “Upandu wa Ana Wokwera Mosalekeza.” India: “Upandu Wolinganizidwa Ndiwo Indasitale Yaikulu.” Soviet Union: “Soviet Ikuchita Mantha ndi Kuwonjezereka kwa Upandu.”21 Magazine a Maclean’s anafotokoza kuti: “Upandu wa chiwawa mu Detroit ngwofalikira kwambiri kotero kuti ngakhale ambanda nthawi zina amatchulidwa pang’ono pokha ku masamba a kumbuyo a manyuzipepala.”22 Chotero, kukwera kwa upandu ndiko vuto la m’mitundu yonse, ndipo zoyesayesa za anthu zokha sizingathe kukuthetsa. Ngati chothetsera cha anthu chikanakhala chotheka, pambuyo pa nthawi yonseyi ndi kuyesayesa upandu sukanayeneranso kukhala vuto.
23. Kodi zimene Baibulo lidaneneratu ponena za mikhalidwe m’tsiku lathu zakwaniritsidwa?
23 Zimene zikuchitika ziri monga momwedi Baibulo linaneneratu kalekale kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, . . . okonda zokondweretsa munthu osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-4) Yesu ananeneratunso kuti “kuchuluka kwa kusayeruzika” kukakhalako m’nyengo ya mwamsanga Ufumu wa Mulungu usanapange dziko lapansi kukhala malo okhalidwa kokha ndi ‘anthu ofatsa.’ “Kuchuluka kwa kusayeruzika” kumeneko ndiko njira ya moyo m’tsiku lathu.—Mateyu 24:12; 5:5; Salmo 37:29.
Mavuto Aakulu Koposa Onse
24. Ngakhale ngati anthu akanathetsa mavuto onse amene alankhulidwa kufikira panopa, kodi ndiadani aakulu kwambiri ati amene akanatsala?
24 Tiyeni tinene kuti anthu akanatha kuthetsa mavuto ankhondo, umphawi, njala, kuipitsa, ndi upandu. Kodi izi zikakubweretserani mtendere wokwanira ndi chisungiko? Ayi, kanthu kena kakanakhala kakusoŵekabe. Matenda ndi imfa zikakhalakobe monga adani osagonjetseka. Ndithudi, kodi mpumulo kuchokera ku mavuto ena ungatanthauzenji pamene muwona wokondedwa wanu akudwala ndi kufa, kapena mupeza thupi la inumwini likukanthidwa ndi nthenda yakupha?
25, 26. Kodi nziyembekezo zotani zimene ofufuza a za mankhwala amawona ponena za kugonjetsa nthenda?
25 Pamene kuli kwakuti kupita patsogolo kwa mankhwala kwapangidwa, kodi kwatibweretsera ufulu pamatenda ndi imfa? Dokotala wodalirika akuyankha kuti: “Nthenda zopatsirana sizinagonjetsedwe. Zikali chikhalirebe chochititsa imfa chachikulu cha dziko ndipo, muno [mu United States], chochititsa chachikulu cha matenda.”23 Mu Afirika lipoti linanena kuti nthenda iri yowanda kwambiri “kotero kuti pa ana 1 000 obadwa pafupifupi 500 adzafa asanafike zaka 5 zakubadwa.”24 Kuzungulira dziko lonse mamiliyoni mazana ambiri ayambukiridwa ndi nthenda ya malungo, kawodzera, chizuula, khate, ndi nthenda zina. M’maiko ena otukuka, nthenda zamtima zimachititsa pafupifupi theka la imfa zonse, ndipo kensa imachititsa imfa imodzi mwa zisanu. Ndipo The Lancet, magazine a zamankhwala a Britishi, amafotokoza kuti: “Kuzungulira dziko lonse pali odwala chinzonono atsopano okwanira mamiliyoni 250 ndi odwala chindoko atsopano okwanira mamiliyoni 50 chaka ndi chaka. Nthenda zina zopatsirana mwa kugonana zingakhalenso zofalikira kwambiri.”25
26 Wasayansi wina anafotokoza kuti ngati mankhwala ochiritsira kensa angapezeke, nthenda ya mtima, ndi nthenda ya impso, nthenda zina zikanakhala akupha aakulu kwambiri. Iye anati: “Pali kuthekera kochepa kwakuti tidzawonjezera kwambiri nthawi ya moyo kapena kuchedwetsa ukalamba m’nthawi yapafupi mtsogolomo.”26 Ndipo madokotala m’Soviet Union amanena kuti: “Mosasamala kanthu za zipambano zonse m’zamakhwala, mkati mwa mbiri yodziwika utali wa nyengo ya moyo wa munthu yakhalabe yosasintha.”27
27. (a) Kodi ndimawu a Baibulo otani onena za kutalika kwa moyo wa anthu amene akali owonabe lerolino? (b) Kodi nkuti kumene tingaphunzire chifukwa chake moyo wa anthu uli waufupi kwambiri ndi wodzala mavuto?
27 Ha akupitirizabe kukhala owona chotani nanga lerolino mawu a Baibulo pa Yobu 14:1, 2 kuti: “Munthu wobadwa ndi mkazi ngwamasiku oŵerengeka, nakhuta mavuto. Atuluka ngati duŵa, nafota; athaŵa ngati mthunzi, osakhalitsa.” Baibulo limasonyezanso chifukwa cha ichi, ndipo limatchula chochititsa cha mavuto onse a anthu, monga momwe tidzawonera pambuyo pake.
Kodi Mudzayembekezera m’Chiyani?
28-30. Kuti tithetse mavuto oyang’anizana ndi anthu, kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kwambiri kudalira chothetsera cha Mulungu koposa cha anthu?
28 M’kuwona mtima konse, kodi kuli kwanzeru kudalira mwa anthu kuthetsa mavuto oyang’anizana ndi anthu? Kapena kodi kuli kwanzeru kwambiri kuika chidaliro m’chothetsera chimene Baibulo limatchula, ndiko kuti, kuchitapo kanthu kwa Mulungu mwiniyo kudzera mwa boma lakumwamba lolungama?
29 Kalekale wamasalmo wouziridwa analemba mawu awa: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika. Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chiri pa Yehova, Mulungu wake; amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi.”—Salmo 146:3-6.
30 Musaiwale konse kuti mulimonse mmene anthu angakhalire owona mtima kapena mmene angakhalire amphamvu ndi anyonga monga atsogoleri a dziko, iwo onse ali zolengedwa zakufa. Pokhala osakhoza kudzipulumutsa, kodi angapulumutse ena bwanji? Iwo sangathe. Mulungu yekha angathe, kupyolera mwa boma lake la Ufumu.
[Chithunzi patsamba 13]
M’mbiri yonse anthu akhala akudzandira mwakhungu kuchoka ku tsoka limodzi kumka ku linzake—nkhondo, kuwonjezereka kwa upandu, kuipitsa, umphaŵi, ndi ena ambiri. Monga momwedi Baibulo limanenera kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”
[Chithunzi patsamba 21]
“Musamakhulupirira . . . mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye”