“Kuuka Koyamba” Kuli M’kati Panopa!
“Amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba.”—1 ATESALONIKA 4:16.
1, 2. (a) Kodi pali chiyembekezo chotani kwa anthu amene anafa? (b) Kodi n’chifukwa chiyani inuyo mumakhulupirira za kuuka kwa akufa? (Onani mawu a m’munsi.)
“AMOYO adziwa kuti tidzafa.” Zimenezi zinayambika Adamu atangochimwa. Munthu aliyense amene anabadwa kuyambira panthawiyo, wakhala akudziwa kuti tsiku lina adzafa, ndipo anthu ambiri adzifunsapo kuti: ‘Kodi kenaka chimachitika n’chiyani? Kodi anthu akufa ali motani?’ Baibulo limayankha kuti: “Akufa sadziwa kanthu bi.”—Mlaliki 9:5.
2 Choncho, kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa anthu amene anafa? Inde chilipo. Ndipotu, cholinga choyambirira cha Mulungu polenga anthu sichingakwaniritsidwe popanda chiyembekezo chimenechi. Pa zaka zambirimbiri zapitazi, atumiki okhulupirika a Mulungu akhala akukhulupirira lonjezo la Yehova lokhudza Mbewu imene idzawononge Satana ndi kukonzanso zinthu zonse zimene iye anawononga. (Genesis 3:15) Ambiri a anthu amenewa anamwalira. Kuti adzaone kukwaniritsidwa kwa lonjezo limenelo ndi malonjezo ena amene Yehova anapanga, ayenera kudzaukitsidwa kwa akufa. (Aheberi 11:13) Koma kodi n’zotheka? Inde, n’zotheka. Mtumwi Paulo anati: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Paulo nthawi inayake anaukitsa mnyamata wina dzina lake Utiko, amene anagwa kuchokera pa windo la pa nsanjika yachitatu ya nyumba yosanja ndipo “anakam’tola ali wakufa.” Ameneyu anali munthu womaliza pa anthu 9 otchulidwa m’Baibulo omwe anaukitsidwa.—Machitidwe 20:7-12.a
3. Kodi mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 5:28, 29 akulimbikitsani bwanji inuyo panokha, ndipo n’chifukwa chiyani akulimbikitsani choncho?
3 Nkhani za anthu 9 amene anaukitsidwawa zimatipatsa maziko okhulupirira zimene Paulo ananena. Zimatilimbikitsa kuti tisakayikire ngakhale pang’ono zimene Yesu analonjeza zoti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Amenewatu ndi mawu olimbikitsa zedi! Ndipo ndi olimbikitsa kwambiri kwa anthu mamiliyoni ambiri amene okondedwa awo anagona m’tulo ta imfa!
4, 5. Kodi Baibulo limatchula kuuka kuti ndi kuti, ndipo mu nkhani ino tikambirana kuuka kuti?
4 Oukitsidwa ambiri adzakhalanso ndi moyo pa dziko lapansi, lomwe lidzakhale lamtendere mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu. (Salmo 37:10, 11, 29; Yesaya 11:6-9; 35:5, 6; 65:21-23) Komabe, izi zisanachitike, payenera kukhala kuuka kwina kwa akufa. Choyamba, Yesu Khristu anafunika kuukitsidwa kuti akapereke mtengo wa nsembe yake kwa Mulungu m’malo mwathu. Yesu anafa ndipo anaukitsidwa mu 33 C.E.
5 Kenaka, anthu odzozedwa a “Isiraeli wa Mulungu” ayenera kukakumana ndi Ambuye Yesu Khristu mu ulemerero wa kumwamba, kumene ‘azikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.’ (Agalatiya 6:16; 1 Atesalonika 4:17) Kuuka kumeneku kumatchedwa “kuuka koyambirira” kapena “kuuka koyamba.” (Afilipi 3:10, 11; Chivumbulutso 20:6) Kuuka kumeneko kukadzatha, idzakhala nthawi yoti anthu mamiliyoni ambiri aukitsidwire pa dziko lapansi n’chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Choncho, kaya chiyembekezo chathu n’chakumwamba kapena n’chapadziko lapansi, tili ndi chidwi kwambiri ndi “kuuka koyamba.” Kodi kuuka kumeneku ndi kotani? Kodi kudzachitika liti?
“Ndi Thupi Lotani?”
6, 7. (a) N’chiyani chiyenera kuchitika Akhristu odzozedwa asanapite kumwamba? (b) Kodi iwowa adzaukitsidwa ndi thupi lotani?
6 M’kalata yake yoyamba kwa Akorinto, Paulo anafunsa funso lokhudza kuuka koyamba, loti: “Kodi akufa adzaukitsidwa motani? Inde, kodi iwo adzauka ndi thupi lotani?” Kenaka anayankha funsolo motere: “Chimene ubzala sichikhala ndi moyo koma ngati chiyamba chafa. . . . Koma Mulungu amaipatsa thupi monga mwa kufuna kwake . . . Ulemerero wa matupi a kumwamba ndi wina, ndi ulemerero wa matupi a padziko lapansi ndi winanso.”—1 Akorinto 15:35-40.
7 Mawu a Paulo akusonyeza kuti Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera ayenera kufa asanalandire mphoto yawo yakumwamba. Akafa, matupi awo apadziko lapansi amabwerera kunthaka. (Genesis 3:19) Pa nthawi yoikika ya Mulungu, amaukitsidwa ndi thupi loyenererana ndi moyo wa kumwamba. (1 Yohane 3:2) Mulungu amawapatsanso moyo wosafa. Umenewu si moyo umene amapatsidwa akangobadwa, ngati kuti anawapumira mzimu winawake wosafa. “Chokhoza kuwonongeka ichi chidzavala kusawonongeka,” anatero Paulo. Moyo wosafa ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, ‘yovalidwa’ ndi anthu amene adzaukitsidwe pa kuuka koyamba.—1 Akorinto 15:50, 53; Genesis 2:7; 2 Akorinto 5:1, 2, 8.
8. Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu sasankha anthu a 144,000 kuchokera m’zipembedzo zosiyanasiyana?
8 Kuuka koyamba ndi kwa anthu 144,000 okha. Yehova anayamba kuwasankha pa Pentekosite mu 33 C.E., atangoukitsa kumene Yesu. Onse ali ndi “dzina [la Yesu] ndi dzina la Atate wake, pamphumi pawo.” (Chivumbulutso 14:1, 3) Choncho sasankhidwa kuchokera m’zipembedzo zosiyanasiyana. Onse ndi Akhristu, ndipo amanyadira kutchedwa ndi dzina la Atate wathu, Yehova. Akaukitsidwa, amapatsidwa ntchito kumwamba. Chiyembekezo chodzatumikira Mulungu m’njira yachindunji ngati imeneyo chimawasangalatsa kwambiri.
Kuli M’kati Panopa?
9. Kodi malemba a Chivumbulutso 12:7 ndi 17:14 amatithandiza bwanji kudziwa nthawi imene kuuka koyamba kukuchitika?
9 Kodi kuuka koyamba kudzachitika liti? Pali umboni wamphamvu woti kuli kale m’kati panopa. Mwachitsanzo, tayerekezerani machaputala awiri a Chivumbulutso. Choyamba, onani Chivumbulutso chaputala 12. Pamenepa timawerenga kuti Yesu Khristu limodzi ndi angelo ake oyera, atangopatsidwa kumene ufumu, akumenya nkhondo ndi Satana ndi ziwanda zake. (Chivumbulutso 12:7-9) Monga momwe magazini ino yasonyezera kwa nthawi yaitali, nkhondo imeneyo inayamba mu 1914.b Koma taonani kuti lemba limeneli silikusonyeza kuti pali aliyense wa otsatira odzozedwa a Khristu amene ali ndi Yesu pa nkhondo yakumwamba imeneyo. Tsopano onani chaputala 17 cha Chivumbulutso. Pamenepo timawerenga kuti “Babulo Wamkulu” akadzawonongedwa, Mwanawankhosa adzagonjetsa mitundu. Kenaka lembalo limapitiriza kuti: “Komanso oitanidwa aja, osankhika, ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa limodzi naye.” (Chivumbulutso 17:5, 14) Anthu “oitanidwa aja, osankhika, ndi okhulupirika” ayenera kukhala ataukitsidwa kale kuti athe kukhala ndi Yesu pa kugonjetsedwa komaliza kwa dziko la Satana. Choncho n’zomveka kunena kuti odzozedwa amene akufa Armagedo isanachitike akuukitsidwa pakati pa 1914 ndi Armagedo.
10, 11. (a) Kodi akulu 24 ndi ndani, ndipo kodi mmodzi wa iwo anaulula chiyani kwa Yohane? (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?
10 Kodi tinganene nthawi yeniyeni imene kuuka koyamba kunayamba? Mfundo yochititsa chidwi yotithandiza kutero ikupezeka pa Chivumbulutso 7:9-15, pamene mtumwi Yohane anafotokoza masomphenya ake a “khamu lalikulu limene munthu sanathe kuliwerenga.” Mmodzi wa akulu 24 anauza Yohane za amene khamu lalikululo linali kuimira. Komanso akulu 24 amenewa akuimira olowa ufumu anzake a Khristu okwana 144,000 mu ulemerero wawo kumwamba.c (Luka 22:28-30; Chivumbulutso 4:4) Yohane nayenso anali ndi chiyembekezo chokakhala kumwamba, koma popeza kuti panthawi imene mkuluyo ankalankhula naye, iye anali akadali munthu pa dziko lapansi, m’masomphenyawa Yohane ayenera kuti ankaimira odzozedwa amene ali pa dziko lapansi omwe sanalandire mphoto yawo ya kumwamba.
11 Ndiyeno kodi tikuphunzirapo chiyani pa mfundo yakuti mmodzi wa akulu 24 anamudziwitsa Yohane za amene akuimira khamu lalikulu? Tikuphunzirapo kuti n’zotheka kuti anthu oukitsidwa a m’gulu la akulu 24 amagwira nawo ntchito yodziwikitsa mfundo za choonadi cha Mulungu masiku ano. N’chifukwa chiyani imeneyi ili mfundo yofunika? Chifukwa choti mu 1935 m’pamene atumiki odzozedwa a Mulungu pa dziko lapansi anadziwitsidwa molondola za khamu lalikulu. Ngati mmodzi wa akulu 24 anagwiritsidwa ntchito kudziwikitsa choonadi chofunika chimenecho, ndiye kuti anayenera kukhala ataukitsidwira kumwamba m’chaka cha 1935, kapena chakachi chisanafike, koma osati pambuyo pake. Motero tingati zimenezi zikusonyeza kuti kuuka koyamba kunayamba nthawi inayake pakati pa 1914 ndi 1935. Koma kodi n’zotheka kupereka yankho lachindunji kuposa pamenepa?
12. Fotokozani chifukwa chake mwezi wa April m’chaka cha 1918 ukhoza kukhala nthawi yomwe kuuka koyamba kunayamba.
12 Tsopano tatiyeni tiganizire nkhani za m’Baibulo zimene tinganene kuti n’zogwirizana. Yesu Khristu anadzozedwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu yam’tsogolo mu October m’chaka cha 29 C.E. Zaka zitatu ndi theka pambuyo pake, mu April m’chaka cha 33 C.E., anaukitsidwa monga munthu wauzimu wamphamvu. Choncho, kodi sizingakhale zomveka kunena kuti popeza Yesu analongedwa ufumu mu October m’chaka cha 1914, ndiye kutinso kuuka kwa otsatira ake odzozedwa okhulupirika kunayamba zaka zitatu ndi theka pambuyo pake, mu April m’chaka cha 1918? N’kutheka kuti umu ndi mmene zililidi ndipotu izi n’zochititsa chidwi. Ngakhale kuti sitingatsimikizire zimenezi mwachindunji m’Baibulo, sizikusemphana ndi malemba ena amene amasonyeza kuti kuuka koyamba kunayamba nthawi ya kukhalapo kwa Khristu itangoyamba kumene.
13. Kodi lemba la 1 Atesalonika 4:15-17 limasonyeza bwanji kuti kuuka koyamba kuyenera kuti kunayamba kuchitika kumayambiriro kwa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu?
13 Mwachitsanzo, Paulo analemba kuti: “Pakuti tikukuuzani izi mwa mawu a Yehova kuti, ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye [osati pa mapeto a kukhalapo kwake], sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. Chifukwa Ambuye iye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula ya mawu a mkulu wa angelo, ndi lipenga la Mulungu. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba. Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwo, tidzatengedwa m’mitambo kukakumana ndi Ambuye mu mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.” (1 Atesalonika 4:15-17) Choncho Akhristu odzozedwa amene anafa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu isanafike ndiwo anayamba kuukitsidwira ku moyo wakumwamba. Anayamba kutero anthu amene anali ndi moyo pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu asanayambe. Zimenezi zikutanthauza kuti kuuka koyamba kuyenera kuti kunayamba kumayambiriro kwa kukhalapo kwa Khristu, ndipo kukupitirirabe “panthawi ya kukhalapo kwake.” (1 Akorinto 15:23) Kuuka koyamba sikukuchitika nthawi imodzi, koma kukutenga nthawi yaitali.
“Aliyense wa Iwo Anapatsidwa Mkanjo Woyera”
14. (a) Kodi masomphenya olembedwa mu Chivumbulutso chaputala 6 akukwaniritsidwa liti? (b) Kodi pa Chivumbulutso 6:9 pakusonyezedwa chiyani?
14 Taonaninso umboni womwe uli mu Chivumbulutso chaputala 6. Chaputala chimenechi chimanena za Yesu atakwera kavalo monga Mfumu yomwe ikupita kukagonjetsa ena. (Chivumbulutso 6:2) Mitundu ya anthu ili m’kati momenyana nkhondo yadzaoneni. (Chivumbulutso 6:4) M’malo ambiri muli njala. (Chivumbulutso 6:5, 6) Milili ikusakaza anthu mosaneneka. (Chivumbulutso 6:8) Zinthu zonse zimene ananeneratuzi zikugwirizana bwino kwambiri ndi zomwe zakhala zikuchitika pa dziko lapansi kuyambira mu 1914. Koma pali chinthu chinanso chimene chikuchitika. Tiyeni tione zomwe zikuchitika pa guwa la nsembe. Pansi pake pali “miyoyo ya iwo amene anaphedwa chifukwa cha mawu a Mulungu, ndi chifukwa cha ntchito yochitira umboni imene anali nayo.” (Chivumbulutso 6:9) Popeza “moyo wa nyama ukhala m’mwazi,” miyoyo yomwe ili pansi pa guwa la nsembelo kwenikweni ikuimira magazi a atumiki okhulupirika a Yesu amene anaphedwa chifukwa chochitira umboni molimba mtima ndiponso mwakhama.—Levitiko 17:11.
15, 16. Fotokozani chifukwa chake mawu a pa Chivumbulutso 6:10, 11 akunena za kuuka koyamba.
15 Mofanana ndi magazi a Abele wolungama uja, magazi a Akhristu ofera chikhulupiriro amenewa akulilira chilungamo. (Genesis 4:10) “Anafuula ndi mawu okweza, amvekere: ‘Mudzalekerera kufikira liti, Inu Ambuye Wamkulukulu, woyera ndi woona, osaweruza ndi kubwezera okhala padziko lapansi chifukwa cha magazi athu?’” Kodi kenaka pakuchitika chiyani? “Aliyense wa iwo anapatsidwa mkanjo woyera, nawauza kuti apumulebe kanthawi pang’ono, kufikira chitakwaniranso chiwerengero cha akapolo anzawo, ndi abale awo amene anali pafupi kuphedwa monganso iwo anaphedwa.”—Chivumbulutso 6:10, 11.
16 Kodi tingati mikanjo yoyera imeneyi anaipereka kwa magazi omwe anali pansi pa guwa la nsembe aja? Ayi! Mikanjoyo inaperekedwa kwa anthu amene magazi awo anakhetsedwa mophiphiritsira pa guwa la nsembelo. M’dzina la Yesu, anthuwa anapereka miyoyo yawo monga nsembe ndipo tsopano anaukitsidwa n’kukhala anthu auzimu. Tikudziwa bwanji zimenezo? Cha kumayambiriro kwa buku la Chivumbulutso, timawerenga kuti: “Iye amene agonjetsa adzavekedwa malaya akunja oyera. Ndipo sindidzafafaniza konse dzina lake m’buku la moyo.” Kumbukiraninso kuti akulu 24 anali “ovala malaya akunja oyera, ndi akolona achifumu agolide [anali] pa mitu pawo.” (Chivumbulutso 3:5; 4:4) Choncho pambuyo poti nkhondo, njala, ndi milili zayamba kuvutitsa anthu padziko, anthu akufa a m’gulu la 144,000, oimiridwa ndi magazi a pansi pa guwa la nsembe aja, anaukitsidwira ku moyo wakumwamba ndipo anavekedwa mikanjo yoyera yophiphiritsira.
17. Kodi anthu omwe analandira mikanjo yoyera ‘amapuma’ m’lingaliro lotani?
17 Anthu oukitsidwa kumene amenewo ayenera ‘kupumula.’ Ayenera kudikira moleza mtima kufika kwa tsiku la Mulungu lobwezera. “Akapolo anzawo,” omwe ndi Akhristu odzozedwa amene akadali pa dziko lapansi, ayenera kusonyeza kukhulupirika kwawo poyesedwa. Nthawi yopereka chiweruzo cha Mulungu ikadzakwana, ‘kupuma’ kuja kudzatha. (Chivumbulutso 7:3) Pa nthawi imeneyo, oukitsidwawo adzathandizana ndi Ambuye Yesu Khristu kuwononga oipa, kuphatikizapo anthu amene anakhetsa magazi a Akhristu osalakwa.—2 Atesalonika 1:7-10.
Tanthauzo Lake kwa Ife
18, 19. (a) Kodi pali zifukwa zotani zimene munganenere kuti kuuka koyamba kuli m’kati panopa? (b) Kodi mukumva bwanji chifukwa chomvetsa bwino kuuka koyamba?
18 Mawu a Mulungu satchula deti lenileni la kuuka koyamba, koma amasonyeza kuti n’kotenga nthawi yaitali, ndipo n’kochitika pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. Oyamba kuukitsidwa ndi Akhristu odzozedwa amene anafa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu isanayambe. M’nthawi yonse ya kukhalapo kwa Khristu ino, Akhristu odzozedwa akamaliza mokhulupirika moyo wawo wa pa dziko lapansi amasinthidwa “m’kuphethira kwa diso” n’kukhala zolengedwa zauzimu zamphamvu. (1 Akorinto 15:52) Kodi odzozedwa onse adzalandira mphoto yawo yakumwamba nkhondo ya Armagedo isanayambe? Sitikudziwa. Zimene tikudziwa n’zoti pa nthawi yoikika ya Mulungu, a 144,000 onse adzapezeka ataima pa Phiri la Ziyoni lakumwamba.
19 Tikudziwanso kuti ambiri mwa a 144,000, panopo ali kale limodzi ndi Khristu. Ndi ochepa okha omwe atsala pa dziko lapansi pano. Umenewu ndi umboni wamphamvu kwambiri wakuti nthawi ya chiweruzo cha Mulungu ikuyandikira kwambiri! Posachedwapa, dongosolo lonse la dziko la Satana liwonongedwa. Satanayonso adzatsekeredwa kuphompho. Kenaka, kuuka kwa anthu onse kudzayamba, ndipo pa maziko a nsembe ya dipo ya Yesu, anthu okhulupirika adzakonzedwa n’kufika pa ungwiro wofanana ndi umene Adamu anataya. Ulosi wa Yehova wolembedwa pa Genesis 3:15 ukukwaniritsidwa mosangalatsa kwambiri. Ndithudi, ndi mwayi wapadera kwambiri kukhala ndi moyo mu nthawi ino.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziwe za anthu ena 8 amene anaukitsidwa, onani 1 Mafumu 17:21-23; 2 Mafumu 4:32-37; 13:21; Maliko 5:35, 41-43; Luka 7:11-17; 24:34; Yohane 11:43-45; Machitidwe 9:36-42.
b Kuti muone umboni wa m’Malemba woti kukhalapo kwa Khristu kunayamba mu 1914, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? masamba 215-218, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
c Mfundo zokhudza mmene timadziwira kuti akulu 24 akuimira Akhristu odzozedwa pa udindo wawo kumwamba, mungazipeze m’buku la Revelation—Its Grand Climax At Hand! tsamba 77, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Kodi Mungafotokoze?
Kodi malemba otsatirawa amatithandiza bwanji kuzindikira nthawi ya “kuuka koyamba”?
• 1 Akorinto 15:23; 1 Atesalonika 4:15-17
[Zithunzi patsamba 26]
Kodi ndi kuuka kotani kumene kukuchitika anthu ena onse asanayambe kuukitsidwa kwa akufa?
[Chithunzi patsamba 29]
Kodi anthu ena amene anali m’tulo ta imfa anapatsidwa mkanjo woyera m’njira yotani?