Kodi Tsiku la Ambuye Lidzatanthauzanji kwa Inu?
“Pita nugonjetse pakati pa adani ako.”—SALMO 110:2, “NW.”
1-3. (a) Nchifukwa ninji chiyambi cha tsiku la Ambuye chakhala nthaŵi ya kukanthana, ndipo nziti zomwe zakhala zina za zipambano za Yesu? (b) Ndimotani mmene Yesu “adzatsirizira kugonjetsa kwake”?
KUMBUYOKO mu 1914, Yesu anakhzikitsidwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, ndipo tsiku la Ambuye linayamba. Mwamsanga, Mfumu yatsopano inayang’anizana ndi chitsutso chachiwawa kuchokera kwa Satana Mdyerekezi ndi oimira ake pano padziko lapansi. (Salmo 2:1-6) Chotero zaka zoyambirira zimenezi za tsiku la Ambuye zakhala nthaŵi ya kukanthana mu imene Yesu wapitirizabe ‘kugonjetsa pakati pa adani ake.’—Salmo 110:2, NW.
2 Kugonjetsa kwa Mfumu yatsopano kwakhala kosangalatsa. Pambuyo pa 1914, Satana anayesera “kulikwira” Ufumu wobadwa chatsopanowo koma, m’malomwake, anachotsedwa kumwamba momvetsa manyazi. (Chivumbulutso 12:1-12) Iye kenaka ‘anamenya nkhondo’ ndi otsalira a odzozedwa, koma anali wosakhoza kuchinjiriza kuimirira’ kwawo mu 1919 kapena kulandira kwawo “kampukutu” kuchokera ku dzanja la Yesu Kristu. (Chivumbulutso 10:8-11; 11:11,12; 12:17) Iye mofananamo anali wopanda mphamvu kuchinjiriza kusonkhanitsidwa kwa otsalira a 144,000 ndi kusonkhanitisidwa kwa khamu lalikulu (kuchokera m’mitundu yonse), omwe amapereka “utumiki wopatulika usana ndi usiku mu kachisi [wa Yehova].”—Chivumbulutso 7:1-3, 9-15.
3 Ndithudi, chiyambire 1914 Yesu wapitirizabe ‘kugonjetsa.’ Mosasamala kanthu za chimenecho, zambiri ziyembekezera kuchitika. Yesu afunikirabe “kutsiriza kugonjetsa kwake.” Iye afunikirabe kutenga kachitidwe m’kuchotsa kuwonekera kulikonse kwa dongosolo la zinthu la dziko la Satan. (Chivumbulutso 6:1, 2; 19:11-21) Kodi nchiyani chimene kachitidwe ka m’mbiri kameneka kadzatanthauza kaamba ka ife monga aliyense payekha?
Kuvulidwa Kwapoyera kwa Babulo Wamkulu
4. Ndimotani mmene chipembedzo chonyenga chalongosoledwera mu Chivumbulutso?
4 Kuwonongedwa kwa dziko la Satan kuyambika ndi mapeto a chipembedzo chonyenga. Chivumbulutso chimalongosola ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga—kuphatikizapo Chikristu cha Dziko—kukhala mkazi wachigololo, Babulo Wamkulu, yemwe ali ndi unansi ndi mafumu a dziko lapansi ndipo apangitsa mtundu wa anthu kuledzera ndi chigololo chake. Iyemwini ali woledzeranso—mowukira—kuchokera ku kumwa mwazi, mwazi wa atumiki a Mulungu. (Chivumbulutso 17:1-6) Chivumbulutso chimalongosolanso mapeto a mkazi wachigololo wonyansa wakale ameneyu, ndipo tingamvetsetse bwino kwambiri chimene ichi chidzatanthauza ngati tilingalira chimene chinachitika kwa mkazi wina wachigololo wa chipembedzo yemwe anakhalako kumbuyoko m’zana lachisanu ndi chiŵiri Nyengo Yathu ino isanadze.
5, 6. Nchifukwa ninji Yerusalemu wosakhulupirika anatchedwa mkazi wachigololo, ndipo ndi chiweruzo chotani chimene ichi chinabweretsa pa iye kuchokera ku dzanja la Yehova?
5 Mkazi wachigololo ameneyo anali mzinda wa Yerusalemu. Iwo unayembekezeredwa kukhala malo apakati a kulambira kwa Yehova padziko lapansi, koma Mulungu anati kwa iye: “Wapalamula nawo mwazi wako waukhetsa.” (Ezekieli 22:4) Iye anayembekezeredwanso kukhala woyera mwauzimu, koma anachita chiogololo iyemwini mwa kugwirizana ndi mitundu. “[Ha mmene ndakwiyira molimbana ndi iwe, NW]” Yehova anatero kwa iye, “pakuchita iwe izi zonse, ndizo ntchito za mkazi, wachigololo wouma m’maso!”—Ezekieli 16:30; 23:1-21; Yakobo 4:4.
6 Talingalirani, kenaka, chiweruzo cha Yehova pa mkazi wachigololo ameneyu: “Chifukwa chake tawona ndidzasonkhanitsa mabwenzi ako onse [mitundu] amene wakondwera nawo ndi onse unawakonda . . . , ndi kuvula unaliseke wako kuti awone umaliseke wako onse. Ndipo adzatentha nyumba zako ndi moto.” (Ezekieli 16:37, 39, 41; 23:25-30) Mbiri yakale iri ndi zimene zinachitika. Ababulo anabwera mu 607 B.C.E. ndipo anavula Yeruslameu wamaliseke. Anthu ake ndi chuma chake zinatengedwa ku Babulo. Mzindawo unawonongedwa, kachisi anatenthedwa, ndipo dziko linasiidwa lopasulidwa.—2 Mbiri 36:17-21.
7. Nchiyani chomwe chidzakhala mapeto a Babulo Wamkulu?
7 Chinachake chofananako chidzachitika kwa Babulo Wamkulu. Chivumbulutso chimachenjeza kuti: “Izi [“mafumu” amakono, kapena olamulira kwa amene Babulo Wamkulu wachita nawo dama lauzimu] zidzadana ndi mkazi wachigololoyo nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama zake nizidzampsyereza ndi moto.” (Chivumbulutso 17:2, 16) Kuchokera ku chitsanzo cha Yerusalemu wakale, timadziŵa chimene ichi chidzatanthauza. Chipembedzo chonyenga chidzawonongedwa ndi maboma a mitundu omwe kale ‘anamkonda’ iye. Chuma chake chidzakhadzulidwa, ndipo iye adzatenthedwa, kuwonongedwa kotheratu. Chimaliziro choyenera ku gulu lonyansa!
Miyamba Idetsedwa
8. Ndi mtundu wotani wa nthaŵi umene chisautso chachikulu chidzakhala kaamba ka mtundu wa anthu?
8 Ndi kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, tidzakhala titalowa mu “chisautso chachikulu” choloseredweratu ndi Yesu. (Mateyu 24: 21; Chivumbulutso 7:14) Kulankhula za nthaŵi imeneyo, Chivumbulutso chimanena kuti: “Ndipo panali chivomezi chachikulu ndi dzuŵa linada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi; ndi nyenyezi zam’mwamba zinagwa padziko.” (Chivumbulutso 6:12, 13) Chivomezi chachikulu chimenechi chiri “kugwedezeka kwakukulu” mu “dziko la Israyeli” kumene Ezekieli analosera. (Ezekieli 38:18, 19: Yoweli 3:14-16) Chiri chiwonongeko chomalizira cha dongosolo la zinthu loipa ili. Kodi chinachake chidzachitika ku dzuwa lenileni, mwezi, ndi nyenyezi panthaŵi imeneyo?
9, 10. Nchiyani chomwe Ezekieli analosera m’nkhani ya Igupto, ndipo ichi chinakwaniritsidwa motani?
9 Ezekieli, akumachenjeza ponena za kugwa komadza kwa mnansi wamkulu wa kum’mwera wa Israyeli, Igupto, ananena kuti: “Ndipo pakukuzima iwe [Farao] ndidzaphimba thambo ndi kudetsa nyenyezi zake. Ndidzaphimba dzuŵa ndi mtambo, ndi mwezi sudzawonetsa kuwala kwake. Ndidzakudetsera miyuni yonse yakuwunikira kuthambo—ndi kuchititsa mdima pa dziko lako,’ ati [Mfumu, NW] Ambuye Yehova.”—Ezekieli 32:7,8.
10 Pamene Farao ndi makamu ake anagwa, m’mwamba mwenimweni simunade. Koma mtsogolo mwa Igupto munakhala mwakuda. Monga mmene wophunzira wa Baibulo C. F. Keil akudziŵitsira, “chiyambukiro cha mdima [pa kugwa kwa Farao] chiri choimira chiphiphiritsira cha mkhalidwe wopanda chiyembekezo kotheratu.” Wotsirizika ku nthaŵi zonse monga mphamvu ya dziko yodziimira pa yokha, Igupto analamuliridwa ndi mphamvu yadziko imodzi pambuyo pa inzake! Lerlino, lokulira la gawo la mphamvu zadziko zakale za Ufarao likulamuliridwa ndi mitundu ya chiArab.
11. (a) Nchiyani chomwe chaphiphiritsiridwa ndi chimene cinachitika ku Igupto? (b) Ndimotani mmene mtsogolo mudzakhala mwakuda kotheratu kaamba ka dziko la Satana pa chisautso chachikulu?
11 Koma Keil anawona tanthauzo lowonjezereka mu ulosi wa Ezekieli. Iye akulemba kuti: “Kugonjetsedwa kwa mphamvu yadziko imeneyi [Iguopto] kuli malaulo ndi kuyambika kwa kugonjetsedwa kwa mphamvu zadziko zirizonse zopanda umulungu pa tsiku la chiweruzo chotsirizira.” Ichi chiri, m’tsatanetsatane, chowona. Monga momwe Chivumbulutso chasonyezera, pa chisautso chachikulu ziyembekezo zosakhala zaumulungu za mtundu wa anthu zidzakhala zakuda monga momwe zinaliri zija za Igupto. Chidzakhala monga ngati kuti dzuŵa silinapereke kuwala patsiku ndipo mtambo wa usiku unalibe kuwunika kotentha kulikonse kuchokera ku mwezi ndipo wopanda bwenzi aliyense, nyenyezi zotwanima. Awo omwe amakana kulemekeza Mfumu ya Yehova adzatha popanda ngakhale kuikidwa kwaulemu pamene Wokwera pa kavalo woyera atsiriza kugonjetsa kwake. (Chivumbulutso 19:11, 17-21; Ezekieli 39:4, 17-19) Nchosadabwitsa kuti anthu opanda umulungu adzalirira kwa “mapiri ndi matanthwe: ‘Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wawo, ndipo akhoza kuima ndani?”—Chivumbulutso 6:16, 17; Mateyu 24:30.
Nkhondo Yopita Patsogolo!
12. Ndimotani mmene Satana walongosolera udani wake wa Yesu Kristu mkati mwa tsiku la Ambuye?
12 Bwanji, ngakhale ndi tero, ponena za Akristu mu nthaŵi zimenezi? Chabwino, iwo ayambukiridwa mokulira ndi mkhalidwe wa nkhondo wosatha pakati pa Satana ndi Wokwera pa kavalo woyera. Popeza kuti Satana wakhala wosakhoza kufikira pa Yesu mwaumwini, iye watulutsa magwero otheratu aukali wake pa otsalira a odzozedwa ndipo—posachedwapa kwenikweni—pa khamu lalikulu la nkhosa zina lomwe lasonkhanitsidwa kuzungulira iwo. Monga mmene Yesu anachenjezera, awa akhala “ozondedwa ndi amitundu kaamba ka dzina [lake].” (Mateyu 24:9) Satana wagwiritsira ntchito chida chirichonse chomwe ali nacho, kuphatikizapo kuwukira kwa gulu, kuika m’ndende, kuzunza, ndi kupha, kumenyana molimbana ndi iwo.—2 Timeteo 3:12.
13. Ndimotani mmene Satana wagwiritsira ntchito chinyengo mu mkhalidwe wake wa nkhondo motsutsana ndi anthu a Mulungu?
13 Satana wagwiritsiranso ntchito mwaluso chinyengo. (Aefeso 6:11) Mwa kugwiritsira ntchito “mphamvu za chuma chonyenga,” iye wayesa ena kufooka kapena ngakhale kuleka utumiki wawo wopatulika. (Mateyu 13:22; 1 Timoteo 6:9, 10) Ena wawakokera mu mkhalidwe woipa ndi chisembwere. (1Akorinto 5: 1, 2) Ambiri ali pansi pa chididikizo chokulira chifukwa cha “zodera nkhaŵa za moyo,” ndipo Satana akutenga mwaŵi wa ichi kuyesera ‘kuwatopetsa.’ (Luka 21:34) M’nkhani zina, iye wagwiritsira ntchito kukanthana kwaumunthu kapena zikhoterero zowukira kuchotsa chisamaliro ku “zinthu zofunika kwenikweni.”—Afilipi 1:10; 1 Akorinto 1:11, 12; Yakobo 4:1-3.
14, 15. Ndimotani mmene tingagonjetsere m’kumenyana kwathu motsutsana ndi Satana?
14 Ndiponso, Akristu afunikira kulimirira chipiriro mkati mwa tsiku la Ambuye. Ena alephera, ndipo kulephera kulikonse kwakhala kupambana kwakung’ono kwa Satana. (1 Petro 5:8) Koma ochulukira alabadira lonjezo la Yesu lakuti: “Koma iye wakupirira kufikira chimaliziro yemweyo adzapulumutsidwa.” (Mateyu 24:13, NW) Ndi thandizo lochokera kwa Yehova, iwo agonjetsa ndipo abweretsa chisangalalo ku mtima wake.—Miyambo 27:11; 1 Yohane 2: 13, 14.
15 Motsimikizirika, palibe ndi mmodzi yense wa ife amene afuna kupatsa Satana chikhutiritso cha kutiwona ife tikuleka! Chotero, tiyeni titsatire uphungu wa Paulo ndi kudzikonzekeretsa ife eni ndi chowonadi, chilungamo, ndi chikhulupiriro—kulalikira mbiri yabwino ndi changu ndi kuphunzira kusunga chikhulupiriro chathu cholimba. Tiyeninso tipemphere mokhazikika ndi kukhala ogalamuka. Mwanjirayo, tidzakhala “opanda chifukwa mu tsiku la Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Akorinto 1:8; Aefeso 6:10-18; 1 Atesalonika 5:17; 1 Petro 4:7) M’mwalomwake, tsiku la Ambuye lidzakhala magwero a madalitso olemerera kaamba ka ife.
Mathayo Odabwitsa a Utumiki
16. Nchifukwa ninji Yohane sanauzidwe kulemba chimene mabingu asanu ndi aŵiri ananena, ndipo kodi ichi chinatanthauzanji kaamba ka Akristu odzozedwa mu 1919?
16 Pa Chivumbulutso 10:3, 4, Yohane akunena kuti iye anamva “mabingu asanu ndi aŵiri” akufuula mawu awo. Iye anafuna kulemba chimene anamva, koma iye akusimba kuti: “Ndinamva mawu ochokera kumwamba nanena: ‘Sindikiza nacho chizindikiro zimene adalankhula mabingu asanu ndi aŵiri, ndipo usazilembe.’” Motsimikizirika, siinali nthaŵi kaamba ka chidziŵitso choterocho kuti chitulutsidwe. M’malomwake, Yohane anauzidwa kutenga mpukutu waung’onowo ndi kudya. Mabingu asanu ndi aŵiri amawonekera kuimira kulongosola kotheratu kwa zifuno za Yehova. (Salmo 29:3; Yohane 12:28, 29; Chivumbulutso 4:5) Kumbuyoko mu 1919, pamene Akristu odzozedwa mophiphiritsira anadya mpukutu waung’onowo, siinali nthaŵi kaamba ka iwo kukhala ndi kumvetsetsa kotheratu kwa zifuno za Yehova. (Yerekezani ndi Danieli 12: 8, 9) Koma iwo anapita patsogolo mopanda mantha ndi kumvetsetsa kumene anali nako ndipo anadzitsimikizira iwo eni kukhala oyenera kaamba ka kuwunikira kotsatira.
17. Kodi ndi zinthu zina zatsopano ziti zimene Yehova wapereka kwa anthu ake m’zaka chiyambire 1919?
17 Kenaka, mkati mwa zaka, iwo anapatsidwa kumvetsetsa komvekera bwino kopita patsogolo kwa chifuno cha Yehova. Mwachitsanzo, iwo anadzazindikira kuti nkhosa za m’fanizo la Yesu zinali, ngakhale Armegedo isanadze, kulekanitsidwa kuchokera ku mbuzi. (Mateyu 25:31-46) Iwo anawona kuti kubadwa kwa Ufumu mu 1914 kunali m’kukwaniritsidwa kwa Chivumbulutso mutu 12. Iwo anabwera ku chiyamikiro chozama cha kufunika kwa dzina la Yehova, ndipo anaphunzira amene kamu lalikulu la Chivumbulutso mutu 7 ali ndithudi. Ndi chidaliro chotani nanga chimene zivumbulutso zopita patsogolo zimenezi zinapereka kwa anthu a Mulungu!—Miyambo 4:18; 2 Petro 1:19.
18. Ndi mathayo autumiki apadera otani amene anthu a Yehova agawanamo mkati mwa tsiku la Ambuye, ndipo ndi kugalamuka kotani kumene ichi chimamangirira m’mitima yathu?
18 Panthaŵi imodzimodziyo, Yehova anaikiza kwa atumiki ake a padziko lapansi ndi thayo lapadera la utumiki. M’masomphenya okulira, Yohane anawona angelo akulalikira mbiri yabwino yosatha kaamba ka mtundu wa anthu, kulengeza kugwa kwa Babulo Wamkulu, ndi kuchenjeza molimbana ndi kulandira chizindikiro cha chirombo. (Chivumbulutso 14:6-10) Pamene angelo mosakaikira anawoneratu mathayo autumiki aumulungu amenewa, anali anthu, Mboni za Yehova padziko lapansi, amene kwenikweni analankhula mauthenga amenewa kwa mtundu wa anthu. Yohane anawonanso Yesu akututa “zotuta zadziko lapansi.” (Chivumbulutso 14:14-16) Koma chakhala kupyolera m’kulalikira Ufumu ndi ntchito yopanga ophunzira ya nzika za Yesu padziko lapansi kuti iye watuta zotutazi. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Ndi mwaŵi wotani nanga umene iwo uliri wa kugawana ndi angelo ndi Yesu Kristu iyemwini m’mathayo autumiki a kufunika koteroko! M’kuchita tero, timadzimva ife eni mowonadi m’chigwirizano ndi gulu lalikulu la Yehova, losawoneka la zolengedwa zauzimu zokhulupirika.
Chinjirizo Laumulungu
19. (a) Nchiyani chimene chidzakhala kaindeinde wa nkhalwe ya Satana kulinga kwa anthu a Mulungu? (b) Ndani yemwe adzagonjetsa potsirizira pake, m’kukanthana kwa pakaindeinde?
19 Pamene mapeto a dziko lino ayandikira, Satana adzaika chitsenderezo chowonjezerekawonjezereka pa Akristu. Kaindeinde wa kuwukira kwake akulongosoledwa mu Ezekieli mutu 38 ndi 39, kumene iye mwa ulosi akutchedwa Gogi wa Magogi. Mogwirizana ndi ulos wouziridwa umenewu, Satana adzapanga kuwukira kotheratu kuyesera kuwononga anthu a Mulungu kosatha. Kodi iye adzapambana? Chivumbulutso chikuyankha: “Nyanga khu [“mafumu,” amakono kapena olamulira] . . . zidzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye ndi Mfumu wa mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, koma oitanidwa ndi osakhika ndi okhulupirika.” (Chivumbulutso 17:12, 14) Akristu okhulupirika adzakhala otsimikizira za chilakiko ngati iwo akhala okhulupirika kwa Mfumu yawo yaikulu, yogonjetsa. Magwero a Gogi adzawonongedwa kotheratu.—Ezekieli 39:3, 4, 17-19; Chivumbulutso 19:17-21.
20. Ndi madalitso otani amene tsiku la Ambuye lidzabweretsa kwa Akristu okhulupirika pa chisautso chachikulu?
20 Chotero, tsiku la Ambuye limtanthauza chipulumutso kaamba ka anthu a Mulungu. Awo a odzozedwa omwe adzakhalabe ndi moyo monga anthu pa chisautso chachikulu adzakhala ndi malo awo akumwamba atatsimikiziridwa, ndipo adzagamulapo mosagwedezeka kutsiriza njira ya moyo wawo mokhulupirika. (Chivumulutso 7:1-3; 2 Timoteo 4:6-8) Khamu lalikulu lidzapulumukanso, ndipo Yesu “adzawatsogolera ku akasupe a amadzi amoyo. Ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.” (Chivumbulutso 7:14, 17) Ndi mphoto yabwino chotani nanga kaamba ka kupirira kokhulupirika!
21. Nchiyani chomwe chidzachitika padziko lapansi mkati mwa tsiku la Ambuye pamuyo pa chisautso chachikulu?
21 Tsopano tsiku la Ambuye likulowa m’mbali yodabwitsa: Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu Yesu. (Chivumbulutso 20:6, 11-15) Mtsinje wa madzi amoyo, woloseredwa ponse paŵiri mu Chivumbulutso ndi Ezekieli, udzayenda kuchokera ku mpando wachifumu wa Yehova kupita ku mtundu wa anthu, ndipo awo akumwa ku iwo adzaukitsidwa pang’onopang’ono ku ungwiro waumunthu. (Ezekieli 47:1-12; Chivumbulutso 22:1, 2) Hade idzachotsedwamo chirichonse, ndipo mabiliyoni a awo omwe anafa adzakhalanso ndi mwaŵi wakumwa madzi amenewa.—Yohane 5:28, 29.
22. Ndi zochitika za m’mbiri zotani zimene zikuyembekezera mtundu wa anthu pamapeto a Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Kristu?
22 Pamapeto pa zaka chikwi, mtundu wa anthu udzakhala utabweretsedwa ku ungwiro. Idzakhala nthaŵi yoyenera chotani nanga kaamba ka Satan kupanga kuwonekera kwake kotsirizira pa malo a padziko lapansi! Kachiŵirinso iye adzayesera kunyenga mtundu wa anthu, ndipo ena adzamutsatira iye, ngakhale pamenepo. Awa mwapadera akutchedwa “Gogi ndi Magogi” popeza kuti adzawonetsera mzimu woipa wofananawo wonga uja wosonyezedwa ndi ‘khamu la Gogi’ mu ulosi wa Ezekieli. Koma mzimu wawo wowukira udzachotsedwa ku nthaŵi zonse pamene iwo, limodzi ndi Satana iyemwini ndi ziwanda zake, adzaponyedwa m’nyanja yophiphiritsira ya moto. (Chivumbulutso 20:7-10; Ezekieli 39:11) Mtsogolo modalitsika mowonadi mukuyembekezera awo omwe akhala okhulupirika kupyola chiyeso chotsirizira chimenecho, ndipo kenaka mtundu wa anthu wopangidwa wangwirowo udzakhala umodzi ndi gulu lolungama la chilengedwe chonse cha Yehova. Yehova Mulungu iyemwini adzakhala “zonse mu zonse”!—1 Akorinto 15: 24, 28; Chivumbulutso 20:5.
23. M’chiyang’aniro cha nthaŵi yomwe tikukhalamo, ndi uphungu wotani wa Paulo womwe uli woyenera kaamba ka aliyense wa ife kuwulabadira?
23 Ndi madalitso osayerekezeka otani nanga, kenaka, omwe akutiyembekezera ngati tipirira! Kumbukirani, tsiku la Ambuye tsopano liri mkati. Zinthu zodabwitsa zayamba kale kuchitika. Oyenerera, chotero, ali mawu a Paulo: “Tisaleme akuchita zabwino, popeza m’nyengo yake tidzatuta tikapanda kulema.” (Agalatiya 6:9) Tiyeni ndithudi “tisaleme pakuchita zabwino” m’tsiku iri la Ambuye. Ngati tipirira, tsiku limeneli lidzabweretsa mapindu osatha kwa aliyense wa ife.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi ndi iti yomwe iri mbali yoyamba ya kuwonongedwa kwa dziko la Satana?
◻ Ndimotani mmene Yesu “adzatsirizira kugonjetsa kwake” kwa adani ake?
◻ Ndimotani mmene Satana wamenyera molimbana ndi Mboni za Yehova mkati mwa tsiku la Ambuye?
◻ Ndi madalitso ozizwitsa otani amene anthu a Mulungu asangalala nawo chiyambire 1919?
◻ M’chiyang’aniro cha kumene tiri m’nyengo ya nthaŵi, nchiyani chomwe inu mwagamulapo kuchita mwaumwini?
[Chithunzi patsamba 16]
Tsoka la Yerusalmeu wakale limasonyeza chimene chidzachitika posachedwapa kwa Babulo Wamkulu