Kodi Ufumu wa Mulungu Ukadzabwera Udzachotsa Zinthu Ziti?
“Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”—1 YOH. 2:17.
1, 2. (a) Kodi dzikoli likufanana bwanji ndi chigawenga chimene achiweruza kuti chikaphedwe? (Onani chithunzi choyambirira.) (b) Kodi anthu ndi angelo adzamva bwanji dzikoli likadzawonongedwa?
PAMENE asilikali akundende zina ankapita ndi zigawenga kumalo ena ankanena kuti: “Mtembo ukuyenda.” Koma munthuyo ankaoneka wathanzi bwinobwino. Ndiye n’chifukwa chiyani asilikaliwo ankanena zimenezi? N’chifukwa chakuti munthuyo anali ataweruzidwa kuti aphedwe ndipo ankapita naye kokamupha. Choncho zinali ngati wafa kale.a
2 Dziko loipali lili ngati chigawenga chimene chaweruzidwa kuti chiphedwe. Nthawi yoti dzikoli liwonongedwe yangotsala pang’ono ndipo sizingalephereke. Paja Baibulo limati: “Dziko likupita.” (1 Yoh. 2:17) Koma pali kusiyana pakati pa kuwonongedwa kwa dzikoli ndi kuphedwa kwa chigawenga chija. Chigawenga chikamakaphedwa, anthu ena amatsutsa kuti munthuyo sayenera kuphedwa ndipo ena amaona kuti mlandu wake sunaweruzidwe mwachilungamo. Koma amene waweruza dzikoli kuti liwonongedwe ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse ndipo ndi wachilungamo. (Deut. 32:4) Nthawi yoti dzikoli liwonongedwe ikadzakwana, palibe amene adzatsutse kapena kukayikira kuti Mulungu waweruza mwachilungamo. Likadzawonongedwa, anthu ndi angelo adzasangalala kwambiri ndipo adzaona kuti chilungamo chachitika. Mavuto onse adzathera pomwepo.
3. Tchulani magulu 4 a zinthu zimene zidzachoke Ufumu wa Mulungu ukadzabwera.
3 Koma kodi tikamati “dziko likupita” timatanthauza kuti chomwe chikupita n’chiyani? Zinthu zimene zimaoneka ngati zokhalitsa m’dzikoli ndi zimene zidzapite. Uthenga umenewu ndi wosangalatsa kwambiri ndipo ndi mbali ya “uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mat. 24:14) Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zimene zidzapite Ufumu wa Mulungu ukadzabwera. Zinthuzi tiziika m’magulu 4 awa: anthu oipa, mabungwe amene amachita zoipa, makhalidwe oipa komanso zinthu zina zoipa. Pokambirana gulu lililonse tizipeza mayankho a mafunso awa: (1) Kodi zinthuzo zikutikhudza bwanji masiku ano? (2) Kodi Yehova adzachita chiyani? (3) N’chiyani chidzalowe m’malo?
ANTHU OIPA
4. Kodi zochita za anthu oipa zimatikhudza bwanji?
4 Kodi zochita za anthu oipa zimatikhudza bwanji? Mtumwi Paulo ananeneratu kuti masiku ano adzakhala “nthawi yapadera komanso yovuta.” Iye analembanso kuti “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.” (2 Tim. 3:1-5, 13) Kodi inuyo mwaonapo umboni wa zimenezi? Ambirife tavutikapo chifukwa cha zochita za anthu achiwawa, okwiya komanso achiwembu. Ena amachita kuonetsera kuipa kwawo pomwe ena amachita mwakabisira. Ngakhale zitakhala kuti anthu oterewa sanatichitire zoipa mwachindunji, zochita zawo zimatikhudzabe ndithu. Mwachitsanzo, timakhumudwa komanso timachita mantha tikamva za zinthu zimene anthu oipa achitira achikulire, ana komanso osauka. Anthu oipa amasonyeza mtima wauchinyama ndiponso wauchiwanda. (Yak. 3:15) Komabe anthu a Mulungufe timadziwa kuti pali uthenga wabwino.
5. (a) Kodi Yehova wapereka mwayi wotani kwa anthu oipa? (b) Kodi anthu oipa amene akukana kusintha zidzawathera bwanji?
5 Kodi Yehova adzachita chiyani? Panopa Yehova wapereka mwayi kwa anthu oipa kuti asinthe. (Yes. 55:7) Sikuti iye waweruza kale munthu aliyense woipa kuti adzaphedwa. Koma dzikoli ndi limene waliweruza kuti lidzawonongedwa. Ndiye kodi anthu amene akukana kusintha zidzawathera bwanji pa nthawi ya chisautso chachikulu? Yehova analonjeza kuti adzawononga dziko loipali. (Werengani Salimo 37:10.) Mwina anthu ena oipa amaganiza kuti iwowo sadzawonongedwa. N’kutheka kuti ali ndi maganizo amenewa chifukwa choti akhala akuchita zoipa koma salangidwa chifukwa amabisala. Mwinanso n’chifukwa choti sakumana ndi zotsatira za zochita zawozo. (Yobu 21:7, 9) Koma paja Baibulo limati: “Maso ake [a Yehova] amayang’anitsitsa njira za munthu, ndipo amaona mayendedwe ake onse. Kulibe mdima wandiweyani woti amene akuchita zopweteka ena abisaleko.” (Yobu 34:21, 22) Choncho palibe amene adzabisale moti Yehova n’kulephera kumuona. Komanso popeza maso ake amaona paliponse, palibe chimene munthu angachite moti n’kumupusitsa. Choncho Aramagedo ikadzatha, tidzayang’ana paliponse pamene pankakhala anthu oipa, koma sadzapezekapo chifukwa adzakhala atawonongedwa.—Sal. 37:12-15.
6. Ndani adzatsale anthu oipa akadzawonongedwa, ndipo n’chifukwa chiyani tinganene kuti umenewu ndi uthenga wabwino?
6 Ndani adzalowe m’malo? Yehova anatilonjeza kuti: “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Baibulo limanenanso kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:11, 29) Kodi “ofatsa” komanso “olungama” amene atchulidwa m’mavesiwa ndi ndani? Ofatsa ndi anthu odzichepetsa amene amalola kuti Yehova aziwaphunzitsa komanso kuwatsogolera. Olungama ndi anthu amene amakonda kuchita zinthu zimene Yehova amaona kuti ndi zolungama. Masiku ano anthu ofatsa komanso olungama ndi ochepa kwambiri poyerekezera ndi anthu oipa. Koma m’dziko latsopano mudzakhala anthu olungama okhaokha. Anthu amenewa ndi amene adzathandize kuti dzikoli likhalenso Paradaiso.
MABUNGWE AMENE AMACHITA ZOIPA
7. Kodi zochita za mabungwe ena zimatikhudza bwanji?
7 Kodi zochita za mabungwe ena zimatikhudza bwanji? Mavuto ambiri a m’dzikoli amayambitsidwa ndi mabungwe osati anthu paokha. Mwachitsanzo, pali zipembedzo zambiri zimene zimanamiza anthu pa nkhani zokhudza Mulungu, Baibulo komanso tsogolo la anthu ndi dzikoli. Ndiye palinso maboma amene amalimbikitsa nkhondo, kusankhana mitundu, kupondereza osauka, ziphuphu komanso kukondera. Makampani ena amawononga zinthu zachilengedwe komanso kubera anthu pa nkhani za malonda. Izi zimachititsa kuti anthu ochepa azilemera kwambiri pomwe ochuluka ali pa umphawi. Choncho n’zosachita kufunsa kuti mabungwe ambiri akuyambitsa mavuto m’dzikoli.
8. Kodi Baibulo limasonyeza kuti n’chiyani chidzachitikire mabungwe omwe panopa akuoneka kuti ndi amphamvu?
8 Kodi Yehova adzachita chiyani? Chisautso chachikulu chidzayamba andale akadzaukira zipembedzo zonse zonyenga. M’Baibulo, zipembedzo zimenezi zimaimiridwa ndi hule ndipo zimatchedwa Babulo Wamkulu. (Chiv. 17:1, 2, 16; 18:1-4) Mabungwe onse a zipembedzo adzawonongedwa. Ndiyeno kodi n’chiyani chidzachitikire mabungwe enawa amene amachitanso zoipa? Baibulo limayerekezera mabungwe amene amaoneka ngati amphamvu panopa ndi mapiri komanso zilumba. (Werengani Chivumbulutso 6:14.) Baibulo linaneneratu kuti maboma onse ndiponso mabungwe amene amagwirizana nawo potsutsa Ufumu wa Mulungu adzawonongedwa. Chimenechi chidzakhala chimake cha chisautso chachikulu. (Yer. 25:31-33) Zikadzatero, ndiye kuti padzikoli padzakhala popanda mabungwe ochita zoipa.
9. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu amene adzakhale nzika za Ufumu wa Mulungu adzakhala gulu logwirizana?
9 N’chiyani chidzalowe m’malo mwa mabungwewa? Kodi pali bungwe kapena gulu lililonse limene lidzakhalepo pambuyo pa Aramagedo? Baibulo limanena kuti: “Pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Pet. 3:13) Maboma amene alipowa ali ngati kumwamba kwakale pomwe anthu ake ali ngati dziko lakale ndipo zonsezi sizidzakhalaponso. Ndiyeno adzalowedwa m’malo ndi kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Mawu oti “kumwamba kwatsopano” akutanthauza boma lakumwamba ndipo “dziko lapansi latsopano” ndi anthu amene adzakhale padzikoli n’kumalamulidwa ndi boma limeneli. Mfumu ya Ufumu umenewu ndi Yesu Khristu ndipo Ufumuwu udzasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo. (1 Akor. 14:33) Choncho anthu amene azidzalamuliridwa ndi Ufumuwu adzakhala gulu logwirizana. Komanso padzakhala anthu amene azidzayang’anira ntchito zosiyanasiyana. (Sal. 45:16) Azidzalandira malangizo kuchokera kwa Khristu ndi a 144,000. Kodi mukuganiza kuti zidzakhala bwanji mabungwe onsewa akadzachoka n’kungotsala gulu limodzi lopanda chinyengo komanso la anthu ogwirizana?
MAKHALIDWE OIPA
10. (a) Tchulani makhalidwe oipa amene amachitika m’dera lanu. (b) Kodi makhalidwewa amakhudza bwanji inuyo ndi banja lanu?
10 Kodi makhalidwe oipa a anthu amatikhudza bwanji? M’dzikoli makhalidwe oipa ali paliponse. Anthu ambiri ndi achiwerewere, achinyengo, achiwawa komanso ankhanza. Makolo amavutika kwambiri polera ana chifukwa cha kuchuluka kwa makhalidwe oipawa. Zosangalatsa zambiri zimalimbikitsa makhalidwe oipa ndipo zimachititsa anthu kuona kuti mfundo za Yehova n’zosathandiza. (Yes. 5:20) Koma Akhristu enieni amayesetsa kuti akhale osiyana ndi anthu a m’dzikoli. Iwo amafuna kukhalabe okhulupirika ngakhale kuti anthu ambiri amanyoza mfundo za Yehova.
11. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachitira mzinda wa Sodomu ndi Gomora?
11 Kodi Yehova adzachita chiyani? Kodi Yehova anachita zotani makhalidwe oipa atachuluka ku Sodomu ndi Gomora? (Werengani 2 Petulo 2:6-8.) Loti ankavutika kwambiri mumtima chifukwa choti anthu amene ankakhala pafupi ndi banja lake anali oipa. Yehova anawononga mizinda iwiriyi ndipo anathetsa zoipa zonse. Zimene anachitazi ndi “chitsanzo cha zinthu zimene zidzachitikire anthu osaopa Mulungu m’tsogolo.” Ngati Yehova anawononga anthu a makhalidwe oipa pa nthawiyo, kodi angadzalekerere anthu amene akuchita zoipa masiku ano?
12. Kodi ndi zinthu ziti zimene inuyo mumafuna kudzachita m’dziko latsopano?
12 N’chiyani chidzalowe m’malo? M’dziko latsopano mudzakhala zinthu zambiri zosangalatsa. Mwachitsanzo, padzakhala ntchito yosintha dzikoli kuti likhale Paradaiso komanso yomanga nyumba zathu ndi za anzathu. Anthu ambiri amene anamwalira adzaukitsidwa ndipo tidzawaphunzitsa mfundo za Yehova komanso zimene Yehovayo wachitira anthu. (Yes. 65:21, 22; Mac. 24:15) Tsiku lililonse tizidzachita zinthu zosangalatsa komanso zolemekeza Yehova.
ZINTHU ZOIPA
13. Kodi zimene Satana, Adamu ndi Hava anachita zabweretsa mavuto ati?
13 Kodi zinthu zoipa zimatikhudza bwanji? M’dzikoli mwadzadza anthu oipa, mabungwe ochita zoipa komanso zinthu zoipa. Tonsefe timakhudzidwa ndi zinthu monga nkhondo, umphawi komanso kusankhana mitundu. Matenda ndi imfa nazonso zimatisowetsa mtendere. Zonsezi zikuchitika chifukwa chakuti Satana, Adamu ndi Hava anapandukira Mulungu. Panopa palibe amene sangakumane ndi mavuto obwera chifukwa cha zimene zinachitikazi.
14. Kodi Yehova adzathetsa mavuto ati?
14 Kodi Yehova adzachita chiyani? Yehova walonjeza kuti adzathetseratu nkhondo. (Werengani Salimo 46:8, 9.) Wanenanso kuti adzathetsa matenda onse. (Yes. 33:24) Nanga bwanji za imfa? Baibulo limanena kuti Yehova adzameza imfa kwamuyaya. (Yes. 25:8) Iye adzathetsanso umphawi komanso zoipa zonse zimene tikuzunzika nazo masiku ano. (Sal. 72:12-16) Yehova adzachotsanso mzimu wa dzikoli womwe uli ngati “mpweya.” (Aef. 2:2) Tikutero chifukwa choti Satana ndi ziwanda zake adzakhala kulibe.
15. Tchulani zinthu zina zimene sizidzakhalapo m’dziko latsopano.
15 Kodi mukuganiza kuti moyo udzakhala wotani Yehova akadzathetsa nkhondo, matenda ndi imfa? Pa nthawiyo kudzakhala kopanda zida za nkhondo, asilikali, sitima ndi ndege za nkhondo komanso zipilala zokumbukira anthu ophedwa kunkhondo. Sikudzakhalanso zipatala, madokotala, manesi, anthu okhoma mabokosi, mamotchale, manda kapenanso adzukulu okumba manda. Anthu achiwembu sadzakhalaponso moti sikudzakhala makampani a zachitetezo, ma alamu, apolisi ndipo mwina sitidzakhalanso ndi maloko kapena makiyi. Choncho sipadzakhalanso chilichonse chotidetsa nkhawa.
16, 17. (a) Kodi zinthu zidzakhala bwanji kwa anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo? Perekani chitsanzo. (b) Kodi tingatani kuti tisadzapite dziko loipali likamadzapita?
16 Kodi moyo udzakhala wotani mavuto onse akadzatha? Kunena zoona sitingamvetse mmene zidzakhalire. Anthufe takhala m’dziko loipali kwa nthawi yaitali moti mavuto tangofika powazolowera. Tili ngati anthu amene amakhala pafupi ndi siteshoni ya sitima moti angozolowera phokoso lake kapena anthu amene amakhala pafupi ndi kumtaya moti angozolowera fungo loipa. Anthu amene amakhala pamalo otere amazindikira kuti anali pa mavuto, pa nthawi imene vutolo latha.
17 N’chiyani chidzalowe m’malo mwa nkhawa zimene timakhala nazo masiku ano? Lemba la Salimo 37:11 limanena kuti anthu “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” Kodi inuyo mumamva bwanji mukawerenga mawu amenewa? Zimenezitu n’zimene Yehova adzatichitire. Choncho tiyeni tizichita zonse zimene tingathe kuti tisachoke m’gululi komanso kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova m’masiku ovutawa. Muziganizira kwambiri zimene Yehova watilonjeza ndipo musamakayikire kuti zidzachitika. Muziuzanso anthu ena zinthu zimenezi. (1 Tim. 4:15, 16; 1 Pet. 3:15) Mukamatero, simudzapita dziko loipali likamadzapita. Koma mudzakhala ndi moyo wosangalala mpaka kalekale.
a Ndimeyi ikufotokoza zimene zinkachitika kundende zina za ku United States zaka zam’mbuyomu.