“Tsiku la Ambuye”
“NDINAGWIDWA ndi mzimu tsiku la Ambuye.” (Chibvumbulutso 1:10) Ananena motero mtumwi Yohane wokalambayo, wosonyezedwa pamwambapo, m’mutu woyamba wa bukhu Labaibulo la Chibvumbulutso. Mawu ake amatithandiza kudziŵa nthaŵi yakukwaniritsidwa kwa masomphenya ochititsa mantha amene iye akupitiriza kufotokoza.
Komabe, sionse amene amavomereza kumasulira kumeneku kwa Chibvumbulutso 1:10. Mwachitsanzo, wotembenuza Baibulo Wachijeremani wotchedwa Jörg Zink amalimasulira motere: “Ndinadzazidwa ndi mzimu woyera—panali pa Sande.” Komabe, matembenuzidwe ambiri Abaibulo amatembenuza mawu Achigiriki akuti teiʹ ky·ri·a·keiʹ he·meʹrai kukhala “tsiku la Ambuye.” Koma ambiri m’mawu amtsinde amanena kuti iwo amaloza ku Sande. Kodi ichi ncholondola?
Bukhu lazilozero Lachikatolika Lachijeremani lotchedwa Herders Bibelkommentar, likufotokoza kulingalira kokhala kumbuyo kwa ganizo limeneli pamene limati: “[Pa Chibvumbulutso 1:10] chilozero pano chikupangidwa osati ku Tsiku Lachiweruzo Chomalizira, limene mofananamo limadziŵika kukhala ‘Tsiku la Ambuye’, koma ku tsiku lenileni la mlungu. Akristu oyambirira anayamba kusunga tsiku loyamba la mlungu monga tsiku lawo lalikulu la mautumiki atchalitchi kuyambira pakati pa zaka za zana loyamba. (Machitidwe 20:7; 1 Akor. 16:2)” Komabe, malemba aŵiri ogwidwa mawu ndi bukhu lazilozerolo samatsimikizira mwanjira iriyonse kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba analiwona tsiku loyamba la mlungu kukhala “tsiku lawo lalikulu la mautumiki atchalitchi.”
Lemba loyambalo la Machitidwe 20:7, limangosimba kuti Paulo, mabwenzi ake oyendayenda, ndi Akristu ochokera ku Troa anasonkhana pamodzi pa tsiku loyamba la mlungu kaamba ka chakudya. Popeza kuti Paulo akachokapo tsiku lotsatira ndipo sakaŵawonanso iwo kwa nthaŵi yaitali, anapeza mwaŵi pachochitikacho kulankhula nawo mwatsatanetsatane.
Lemba lachiŵirilo la 1 Akorinto 16:2, linalimbikitsa Akristu a ku Korinto kusunga ndalama pa “tsiku loyamba la sabata yense” kotero kuti akhale nkanthu kokapereka kwa awo osoŵa m’Yudeya. Katswiri wotchedwa Adolf Deissmann akupereka lingaliro lakuti tsiku limeneli liyenera kukhala linali tsiku lamalipiro. Mulimonse mmene zinaliri, lingaliro loperekedwa ndi Paulo linali lothandiza, popeza kuti ndalama zikakhoza kutha mkati mwa mlungu.
Kulibe kulikonse m’Baibulo kumene kukunenedwa kuti Akristu m’nyengo ya atumwi analiwona tsiku loyamba la mlungu, tsopano lotchedwa Sande, kukhala mtundu wa sabata Yachikristu, tsiku lopatulidwa kwenikweni kaamba ka misonkhano yawo yokhazikika yakulambira. Panali kokha pambuyo pa imfa ya atumwi pamene tsiku la Sande linadzalingaliridwa mwanjirayi nilidzatchedwa “tsiku la Ambuye.” Izi zinali mbali ya mpatuko wonenedweratu ndi Yesu ndi atumwi ake enieniwo.—Mateyu 13:36-43; Machitidwe 20:29, 30; 1 Yohane 2:18.
Nangano, kodi “tsiku la Ambuye” nchiyani? Mawu apatsogolo ndi apambuyo a Chibvumbulutso 1:10 amasonya kwa Yesu monga Ambuye yemwe ali mwiniwake wa tsikulo. Mawu a Mulungu amadziŵikitsa mawu onga ngati “tsiku la Ambuye wathu Yesu Kristu” kukhala nthaŵi ya chiweruzo cha anthu ndi kubwezeretsedwa kwa Paradaiso.—1 Akorinto 1:8; 15:24-26; Afilipi 1:6, 10; 2:16.
Chotero, Hans Bruns, m’matembenuzidwe ake okhala ndi cholembedwa chomasulira, Das Neue Testament (Chipangano Chatsopano), ngwolondola ponena kuti: “Ena amakhulupirira kuti [Yohane] pano akulankhula za tsiku la Sande, koma kuli kothekera kwenikweni kuti iye akuloza ku Tsiku la Ambuye lodabwitsa, limene kwenikweni likulozedwako m’kufotokoza kwake kotsatira.” W. E. Vine akuti: “‘Tsiku la Ambuye’ . . . liri Tsiku Lake lachiweruzo chosonyezedwa padziko.” Bukhu la Fritz Rienecker lotchedwa Lexikon zur Bibel (Lexicon ya Baibulo) limanena kuti “tsiku la Ambuye” mowonekera limaloza ku “tsiku lachiweruzo.”
Kumvetsetsa kolondola kwa mawu akuti “tsiku la Ambuye” kumatithandiza kumvetsetsa bukhu lonse la Chibvumbulutso. Kuwonjezerapo, umboni ngwakuti tsikulo linayambika kale. Pamenepa, nkofunika chotani nanga kwa ife ‘kumva mawu aulosi a Chibvumbulutso ndi kusunga zolembedwamo’!—Chibvumbulutso 1:3, 19.
[Chithunzi patsamba 27]
Kalongosoledwe komvekera bwino ndiponso kamakono ka vesi lirilonse m’bukhu la Chibvumbulutso kaperekedwa m’bukhu la “Revelation—Its Grand Climax At Hand!” Bukhu lothandiza kuphunzira Baibulo limeneli limapezeka tsopano m’zinenero 33