Khamu Lalikulu la Olambira Oona—Lachokera Kuti?
“Taonani, khamu lalikulu, . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.”—CHIVUMBULUTSO 7:9.
1. Kodi nchifukwa ninji masomphenya aulosi m’Chivumbulutso amatisonkhezera kukhala ndi chidwi lerolino?
CHAKUMAPETO kwa zaka za zana loyamba C.E., mtumwi Yohane anaona masomphenya a zochitika zodabwitsa mogwirizana ndi chifuno cha Yehova. Zina za zinthu zimene anaona m’masomphenyawo zikukwaniritsidwa panthaŵi inoyo. Zina zidzakwaniritsidwa mtsogolomu posachedwapa. Zonsezi zaloza kukukwaniritsidwa kwa chifuno chachikulu cha Yehova cha kuyeretsa dzina lake pamaso pa chilengedwe chonse. (Ezekieli 38:23; Chivumbulutso 4:11; 5:13) Ndiponso, zimaphatikizapo ziyembekezo za moyo wa aliyense wa ife. Kodi zili choncho motani?
2. (a) Kodi nchiyani chimene mtumwi Yohane anaona m’masomphenya ake achinayi? (b) Kodi ndi mafunso otani onena za masomphenya ameneŵa amene tidzalingalira?
2 Mu mpambo wachinayi wa masomphenya a Chivumbulutso, Yohane anaona angelo atagwira mphepo zowononga kufikira atasindikiza chizindikiro “akapolo a Mulungu wathu” pamphumi zawo. Ndiyeno anaona zochititsa chidwi koposa—“khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” logwirizana m’kulambira Yehova ndi m’kulemekeza Mwana wake. Yohane anauzidwa kuti ameneŵa anali anthu amene akatuluka m’chisautso chachikulu. (Chivumbulutso 7:1-17) Kodi ndi ayani amene akufotokozedwa kukhala “akapolo a Mulungu wathu”? Ndipo kodi ndi ayani amene adzapanga “khamu lalikulu” la opulumuka chisautso? Kodi mudzakhala mmodzi wa iwo?
Kodi ndi Ayani Amene Ali “Akapolo a Mulungu Wathu”?
3. (a) Pa Yohane 10:1-18, kodi Yesu anafanizira motani unansi wake ndi otsatira ake? (b) Kodi nchiyani chimene Yesu anatheketsa kwa nkhosa zake mwa imfa yake yansembe?
3 Pafupifupi miyezi inayi imfa yake isanachitike, Yesu anadzitcha iye mwini kukhala “mbusa wabwino” ndipo otsatira ake monga “nkhosa” zimene akatayira moyo wake. Anatchula mwapadera za nkhosa zimene iye anapeza m’khola lophiphiritsira ndipo pambuyo pake zimene anazisamalira kwambiri. (Yohane 10:1-18)a Mwachikondi, Yesu anataya moyo wake kaamba ka nkhosa zake, akumapereka mtengo wa dipo umene unafunika kuti ziwonjoledwe ku uchimo ndi imfa.
4. Kodi ndani amene ali oyamba kusonkhanitsidwa monga nkhosa mogwirizana ndi zimene Yesu panopo ananena?
4 Komabe, asanachite zimenezo, Yesu mwiniyo monga Mbusa Wabwino anasonkhanitsa ophunzira. Oyambirira anadziŵikitsidwa kwa iye ndi Yohane Mbatizi, “wapakhomo” wa m’fanizo la Yesu. Yesu anali kufunafuna anthu amene akalandira mwaŵi wa kukhala mbali ya ‘mbewu ya Abrahamu’ ya chiungwe. (Genesis 22:18; Agalatiya 3:16, 29) Iye anakulitsa chiyamikiro cha Ufumu wakumwamba m’mitima yawo, ndipo anawatsimikizira kuti akawakonzera malo m’nyumba ya Atate wake wakumwamba. (Mateyu 13:44-46; Yohane 14:2, 3) Moyenerera iye anati: “Kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.” (Mateyu 11:12) Awo amene anamtsatira kotero kuti apeze chonulirapo chimenecho analidi mkati mwa khola limene Yesu ananena.
5. (a) Kodi ndani amene ali “akapolo a Mulungu wathu” otchulidwa pa Chivumbulutso 7:3-8? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti ena ambiri adzagwirizana ndi Israyeli wauzimu m’kulambira?
5 Pa Chivumbulutso 7:3-8, awo amene amapitabe patsogolo mwachipambano ku chonulirapo chimenecho cha kumwamba amatchedwanso kuti “akapolo a Mulungu wathu.” (Onani 1 Petro 2:9, 16.) Kodi 144,000 otchulidwa pamenepo ali Ayuda akuthupi okha? Kodi awo amene ali m’khola lophiphiritsira la m’fanizo la Yesu ali Ayuda okha? Kutalitali; iwo ndiwo ziŵalo za Israyeli wauzimu wa Mulungu, iwo onse amagwirizana ndi Kristu kupanga mbewu yauzimu ya Abrahamu. (Agalatiya 3:28, 29; 6:16; Chivumbulutso 14:1, 3) Ndithudi, potsirizira pake nthaŵi ikafika pamene chiŵerengero chake chenicheni chikakwanira. Ndiyeno nchiyani chimene chikatsatira? Monga momwe Baibulo linali litaneneratu, enanso—khamu lalikuludi—akagwirizana ndi Aisrayeli auzimu ameneŵa m’kulambira Yehova.—Zekariya 8:23.
“Nkhosa Zina”—Kodi Ndizo Akristu Akunja?
6. Kodi Yohane 10:16 amatchulanso za kukhalapo kwa chiyani?
6 Atatchula za khola limodzi pa Yohane 10:7-15, Yesu anatchulanso gulu lina, akumati: “Nkhosa zina ndili nazo, zimene sizili za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Yohane 10:16) Kodi ndi ayani amene ali “nkhosa zina” zimenezo?
7, 8. (a) Kodi nchifukwa ninji lingaliro lakuti nkhosa zina zili Akristu Akunja lili lozikidwa pa maziko olakwika? (b) Kodi ndi umboni wotani wonena za chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi umene uyenera kuyambukira kuzindikira kwathu amene ali a nkhosa zina?
7 Othirira ndemanga ambiri a Dziko Lachikristu ali ndi lingaliro lakuti nkhosa zina zimenezi ndizo Akristu Akunja ndi kuti awo okhala m’khola lotchulidwa poyambirirapo ndiwo Ayuda, amene anali pansi pa pangano la Chilamulo, ndi kuti magulu onsewo amapita kumwamba. Komatu Yesu anabadwa ali Myuda ndipo motero anali pansi pa pangano la Chilamulo. (Agalatiya 4:4) Ndiponso, awo amene amaona nkhosa zina kukhala Akristu Akunja amene anadzafupidwa moyo wakumwamba amalephera kulingalira za mbali ina yofunika ya chifuno cha Mulungu. Pamene Yehova analenga anthu oyamba ndi kuwaika m’munda wa Edene, anadziŵikitsa bwino lomwe kuti chifuno chake chinali chakuti dziko lapansi lidzazidwe ndi anthu, kuti lonse limene likhale paradaiso, ndi kuti osamalira ake aumunthu akhale ndi moyo kosatha—pamaziko akuti anayenera kulemekeza ndi kumvera Mlengi wawo.—Genesis 1:26-28; 2:15-17; Yesaya 45:18.
8 Pamene Adamu anachimwa, chifuno cha Yehova sichinathetsedwe. Mwachikondi Mulungu anapanga makonzedwe kaamba ka mbadwa za Adamu kuti zikhale ndi mwaŵi wa kulandira chimene Adamu analephera kuyamikira. Yehova ananeneratu kuti akautsa mombolo, mbewu, mwa amene madalitso adzaperekedwa kumitundu yonse. (Genesis 3:15; 22:18) Lonjezolo silinatanthauze kuti anthu onse abwino padziko lapansi adzatengedwera kumwamba. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Asanalankhule za fanizo lolembedwa pa Yohane 10:1-16, Yesu anali atangouza kumene ophunzira ake kuti Atate wake anakonda kupatsa “kagulu ka nkhosa” kokha Ufumu wakumwamba. (Luka 12:32, 33) Chotero pamene tiŵerenga za fanizo la Yesu lonena za iye mwini monga Mbusa Wabwino amene ataya moyo wake kaamba ka nkhosa zake, kukakhala kulakwa kusalingalira za unyinji wa awo amene Yesu amawaika m’chisamaliro chake chachikondi, anthu amene amakhala nzika zapadziko lapansi za Ufumu wake wakumwamba.—Yohane 3:16.
9. Kalelo mu 1884, kodi nchiyani chimene Ophunzira Baibulo anazindikira kukhala chizindikiro cha nkhosa zina?
9 Kalelo mu 1884, Watch Tower inadziŵikitsa nkhosa zina kukhala anthu amene adzapatsidwa mwaŵi wa kukhala ndi moyo padziko lapansi pansi pa mikhalidwe imene idzakwaniritsa chifuno cha pachiyambi cha Mulungu. Ophunzira Baibulo oyambirira amenewo anazindikira kuti zina za nkhosa zina zimenezi zikakhala anthu amene anakhalako ndi kumwalira utumiki wapadziko lapansi wa Yesu usanachitike. Komabe, panali mfundo zina zimene sanamvetsetse bwino. Mwachitsanzo, iwo analingalira kuti kusonkhanitsidwa kwa nkhosa zina kukachitika odzozedwa onse atalandira mphotho yawo kumwamba. Chikhalirechobe, iwo anazindikiradi kuti nkhosa zina sizinangokhala Akristu Akunja okha. Mwaŵi wa kukhala mmodzi wa nkhosa zina ngwotseguka kwa Ayuda ndi Akunja omwe, kwa anthu amitundu yonse ndi mafuko.—Yerekezerani ndi Machitidwe 10:34, 35.
10. Kuti ife tikhale awo amene Yesu amaonadi kukhala nkhosa zake zina, kodi nchiyani chikufunikira kwa ife?
10 Kuti ayenerane ndi mafotokozedwe operekedwa ndi Yesu amenewo, nkhosa zina ziyenera kukhala anthu amene, mosasamala kanthu za fuko kapena mtundu, amazindikira Yesu Kristu kukhala Mbusa Wabwino. Kodi zimenezo zimaphatikizaponji? Iwo ayenera kusonyeza kufatsa ndi kufunitsitsa kutsogozedwa, mikhalidwe imene ili ya nkhosa. (Salmo 37:11) Monga momwe zilili kwa kagulu ka nkhosa, iwo ayenera ‘kudziŵa mawu’ a mbusa wabwino ndi kusadzilola iwo eni kupatutsidwa ndi anthu ena amene angafune kuwanyenga. (Yohane 10:4; 2 Yohane 9, 10) Ayenera kuzindikira kufunika kwa zimene Yesu anachita potaya moyo wake kaamba ka nkhosa zake ndi kusonyeza chikhulupiriro chokwanira m’makonzedwe amenewo. (Machitidwe 4:12) Ayenera ‘kumvetsera’ mawu a Mbusa Wabwino pamene awalimbikitsa kupereka utumiki wopatulika kwa Yehova yekha, kufuna choyamba Ufumu, kulekana ndi dziko, ndi kusonyeza chikondi chodzimana kwa wina ndi mnzake. (Mateyu 4:10; 6:31-33; Yohane 15:12, 13, 19) Kodi mukuyenererana ndi mafotokozedwe amenewo a awo amene Yesu amaona kukhala nkhosa zake zina? Kodi mukufuna kutero? Ha, ndi unansi wamtengo wapatali chotani nanga umene umatsegukira onse amene amakhaladi nkhosa zina za Yesu!
Kulemekeza Ulamuliro wa Ufumu
11. (a) M’chizindikiro cha kukhalapo kwake, kodi nchiyani chimene Yesu anafotokoza ponena za nkhosa ndi mbuzi? (b) Kodi abale amene Yesu anatchula ndani?
11 Miyezi ingapo atapereka fanizo limene lili pamwambapa, Yesu analinso ku Yerusalemu. Pamene anakhala pa Phiri la Azitona akumaona dera la kachisi mmunsi, anapatsa ophunzira ake tsatanetsatane wa ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu.’ (Mateyu 24:3, NW) Kachiŵirinso iye analankhula za kusonkhanitsidwa kwa nkhosa. Pakati pa zinthu zina, iye anati: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.” M’fanizo limeneli, Yesu anasonyeza kuti awo amene akuyang’anizana ndi Mfumuyo adzaweruzidwa pamaziko a mmene anachitira kwa “abale” ake. (Mateyu 25:31-46) Kodi ndani amene ali abale ameneŵa? Iwo ndiwo Akristu obadwa ndi mzimu amene chifukwa cha chimenecho ali “ana a Mulungu.” Yesu ndiye Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu. Chifukwa chake, iwo ali abale a Kristu. Iwo ali “akapolo a Mulungu wathu” otchulidwa pa Chivumbulutso 7:3, osankhidwa pakati pa mtundu wa anthu kukakhala ndi phande ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba.—Aroma 8:14-17.
12. Kodi nchifukwa ninji njira imene anthu amachitira ndi abale a Kristu ili yofunika kwambiri?
12 Njira imene anthu ena amachitira ndi oloŵa nyumba a Ufumu ameneŵa njofunika kwambiri. Kodi mumawaona monga momwe Yesu Kristu amachitira ndipo monga momwe Yehova amachitira? (Mateyu 24:45-47; 2 Atesalonika 2:13) Mkhalidwe wamaganizo wa munthu kulinga kwa odzozedwa ameneŵa umasonyeza mkhalidwe wake wamaganizo kulinga kwa Yesu Kristu mwiniyo ndi kulinga kwa Atate wake, Mfumu Yachilengedwe Chonse.—Mateyu 10:40; 25:34-46.
13. Kodi ndi kufikira kumlingo wotani umene Ophunzira Baibulo mu 1884 anazindikirira fanizo la nkhosa ndi mbuzi?
13 M’kope lake la August 1884, Watch Tower inasonyeza molondola kuti “nkhosa” za m’fanizo limeneli ndizo awo amene aikiridwa chiyembekezo cha moyo wangwiro padziko lapansi. Kunazindikiridwanso kuti fanizolo liyenera kukhala logwira ntchito pamene Kristu akulamulira pampando wake wachifumu wakumwamba waulemerero. Komabe, panthaŵiyo iwo sanazindikire bwino nthaŵi imene akayamba ntchito yolekanitsa yofotokozedwa pamenepo kapena kuti ikatenga nthaŵi yautali wotani.
14. Kodi ndimotani mmene nkhani yaikulu ya msonkhano wachigawo mu 1923 inathandizira Ophunzira Baibulo kuzindikira nthaŵi imene fanizo laulosi la Yesu lidzakwaniritsidwa?
14 Komabe, mu 1923, m’nkhani yaikulu ya msonkhano wachigawo, J. F. Rutherford, amene panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society, anafotokoza za nthaŵi ya kukwaniritsidwa kwa fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Chifukwa ninji? Mwapang’ono pokha, chifukwa chakuti fanizolo limasonyeza kuti abale a Mfumuyo—ena a iwo—akakhalabe ali padziko lapansi. Pakati pa anthu, ali otsatira ake obadwa ndi mzimu okha amene akatchedwadi kuti abale ake. (Ahebri 2:10-12) Ameneŵa sadzakhala padziko lapansi m’Zaka Chikwi zonse, akumapereka mpata kwa anthu wa kuwachitira zabwino m’njira zimene Yesu anafotokoza.—Chivumbulutso 20:6.
15. (a) Kodi ndi zochitika ziti zimene zinathandiza Ophunzira Baibulo kudziŵa molondola nkhosa za fanizo la Yesu? (b) Kodi ndimotani mmene nkhosazo zaperekera umboni wa kuzindikira kwawo Ufumu?
15 M’nkhani imeneyo mu 1923, panali kuyesayesa kudziŵikitsa awo amene amayenerera mafotokozedwe a Ambuye a nkhosa ndi mbuzi amene anapangidwa, komano mfundo zina zinafunikira kumveketsedwa bwino kuti tanthauzo lonse la fanizolo lidziŵike. Mkati mwa zaka zotsatira, mwapang’onopang’ono Yehova anadziŵikitsa mfundo zimenezi zofunika kwa atumiki ake. Mu 1927, zimenezi zinaphatikizapo kuzindikira bwino kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ali gulu lonse la Akristu odzozedwa ndi mzimu okhala padziko lapansi; ndiponso mu 1932, anazindikira za kufunika kwa kudzigwirizanitsa mopanda mantha ndi atumiki odzozedwa a Yehova, monga momwe Yonadabu anachitira ndi Yehu. (Mateyu 24:45; 2 Mafumu 10:15) Panthaŵiyo, pamaziko a Chivumbulutso 22:17, onga nkhosa ameneŵa analimbikitsidwa mwachindunji kukhala ndi phande m’kutengera uthenga wa Ufumuwo kwa ena. Chiyamikiro chawo pa Ufumu Waumesiya chinawasonkhezera osati kungosonyeza kukoma mtima kwaumunthu kulinga kwa odzozedwa a Ambuye komanso kupatulira miyoyo yawo kwa Yehova mwa Kristu ndi kukhala oyanjana kwambiri ndi odzozedwa ake, akumakhala ndi phande mwachangu mu ntchito imene akuchita. Kodi inu mukuchita zimenezo? Kwa awo amene akuchita zimenezo, Mfumuyo idzati: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Pamaso pawo paikidwa chiyembekezo cha moyo wosatha wangwiro mu Ufumuwo padziko lapansi.—Mateyu 25:34, 46.
“Khamu Lalikulu”—Likumka Kuti?
16. (a) Kodi ndi malingaliro olakwa ati amene Ophunzira Baibulo oyambirira anali nawo ponena za amene ali namtindi wamkulu, kapena khamu lalikulu, la pa Chivumbulutso 7:9? (b) Kodi ndiliti ndipo ndi pamaziko otani pamene lingaliro lawolo linawongoleredwa?
16 Panthaŵi ina atumiki a Yehova anakhulupirira kuti namtindi wamkulu (kapena, khamu lalikulu) wa pa Chivumbulutso 7:9, 10 anali wosiyana ndi nkhosa zina za pa Yohane 10:16 ndi nkhosa za pa Mateyu 25:33. Chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti “akuimirira ku mpando wachifumu,” kunalingaliridwa kuti iwo akakhala kumwamba, osati pamipando yachifumu, akumalamulira monga oloŵa nyumba anzake a Kristu, koma monga okhala m’malo achiŵiri patsogolo pa mpando wachifumu. Analingaliridwa kukhala Akristu achikhulupiriro chocheperapo, anthu amene sanasonyeze mzimu weniweni wa kudzimana. Mu 1935 lingaliro limenelo linawongoleredwa.b Kupenda Chivumbulutso 7:9 mothandizidwa ndi malemba onga ngati Mateyu 25:31, 32 kunasonyeza bwino lomwe kuti anthu okhala padziko lapansi pano angakhale ‘ataimirira ku mpando wachifumu.’ Ndiponso kunasonyezedwa kuti Mulungu alibe miyezo iŵiri ya kukhulupirika. Onse amene akufuna kukhala ndi chivomerezo chake ayenera kusunga umphumphu kwa iye.—Mateyu 22:37, 38; Luka 16:10.
17, 18. (a) Kodi nchiyani chimene chinachititsa chiwonjezeko chachikulu, kuyambira 1935, cha chiŵerengero cha oyembekezera moyo wosatha padziko lapansi? (b) Kodi ndi m’ntchito yofunika yotani imene a khamu lalikulu akukhalamo ndi phande mwachangu?
17 Kwa zaka zambiri anthu a Yehova analankhula za malonjezo a Mulungu onena za dziko lapansi. Chifukwa cha zimene anayembekezera kuchitika kalelo m’ma 1920, iwo analengeza kuti “Mamiliyoni Okhala ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse.” Komano panthaŵiyo panalibe mamiliyoni amene analandira makonzedwe a Mulungu a moyo. Pakati pa ochuluka amene analandira choonadi, mzimu woyera unawapatsa chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Komabe, kusintha kwakukulu, makamaka pambuyo pa 1935 kunachitika. Sichinali chifukwa chakuti The Watchtower inanyalanyaza chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi. Kwa zaka makumi ambiri atumiki a Yehova analankhula za zimenezi ndipo anafunafuna awo amene anayenerera mafotokozedwe a Baibulowo. Komabe, panthaŵi yoyenera ya Yehova, anatsimikizira kuti ameneŵa adzisonyeza poyera.
18 Zolembedwa zimene zilipo zikusonyeza kuti kwa zaka zambiri ofika pa Chikumbutso ochuluka anadya zizindikiro. Koma mkati mwa zaka 25 pambuyo pa 1935, chiŵerengero cha ofika pa Chikumbutso cha chaka ndi chaka cha imfa ya Kristu chinawonjezeka mofulumira kuŵirikiza zana limodzi kuposa chiŵerengero cha awo amene anali kudya. Kodi anthu enaŵa anali ayani? Oyembekezera kukhala ziŵalo za khamu lalikulu. Mwachionekere, nthaŵi ya Yehova ya kuwasonkhanitsa ndi kuwakonzekeretsa kupulumuka chisautso chachikulu chimene chili patsogolopa inali itafika. Monga momwe kunanenedweratu, iwo achokera mu “mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Iwo akukhala ndi phande mwachangu mu ntchito imene Yesu ananeneratu pamene anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka kufotokozedwa kwatsatanetsatane kwatsopano kwa makola ankhosa a Yohane chaputala 10, onani Nsanja ya Olonda ya August 1, 1984, masamba 10-21, 30, 31.
b The Watchtower, ya August 1 ndi 15, 1935.
Kodi Ndemanga Yanu Njotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji masomphenya a m’Chivumbulutso chaputala 7 amatisonkhezera kukhala ndi chidwi mwapadera?
◻ Kodi nchifukwa ninji nkhosa zina za pa Yohane 10:16 sizili Akristu Akunja okha?
◻ Kodi choonadi nchotani kwa awo amene amayenerera mafotokozedwe a Baibulo a nkhosa zina?
◻ Kodi ndimotani mmene fanizo la nkhosa ndi mbuzi limasonyezera za kulemekeza ulamuliro wa Ufumu?
◻ Kodi nchiyani chimene chimasonyeza pamene nthaŵi ya Yehova inafika ya kusonkhanitsa khamu lalikulu la pa Chivumbulutso 7:9?