NKHANI YOPHUNZIRA 21
Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakhudza Tsogolo Lanu
“Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.”—CHIV. 22:20.
NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi anthu onse ayenera kusankha pankhani yofunika iti?
MASIKU ano anthu akuyenera kusankha pa nkhani yofunika kwambiri. Kodi iwo adzasankha kukhala ku mbali ya Yehova Mulungu monga woyenera kulamulira chilengedwe chonse, kapena adzasankha kukhala ku mbali ya Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wake komanso wankhanza? Palibe amene anganene kuti sali kumbali iliyonse. Zimene aliyense angasankhe zidzakhudza tsogolo lake mpaka kalekale. (Mat. 25:31-33, 46) Pa “chisautso chachikulu,” adzaikidwa chizindikiro choti apulumutsidwe kapena kuwonongedwa.—Chiv. 7:14; 14:9-11; Ezek. 9:4, 6.
2. (a) Kodi lemba la Aheberi 10:35-39 limatilimbikitsa kuchita chiyani? (b) Kodi buku la Chivumbulutso lingatithandize bwanji?
2 Werengani Aheberi 10:35-39. Ngati mwasankha kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Yehova, mwasankha bwino kwambiri. Tsopano ndinu ofunitsitsa kuthandiza ena kuti nawonso asankhe bwino. Mungathe kugwiritsa ntchito mfundo za m’buku la Chivumbulutso kuti muwathandize. Buku lochititsa chidwili limafotokoza zomwe zidzachitikire otsutsa Yehova, koma limafotokozanso madalitso omwe anthu amene ali kumbali yake adzapeze. Tingachite bwino kuganizira mfundo za choonadi zimenezi. Kuchita izi kudzatithandiza kukhala otsimikiza kuti tipitirizabe kutumikira Yehova. Kuwonjezera pamenepo, tingathe kugwiritsa ntchito mfundo zimene taphunzira kuthandiza ena kuti asankhe kutumikira Yehova ndiponso asasiye.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Munkhaniyi tikambirana mafunso awa: Kodi n’chiyani chidzachitikire omwe ali kumbali ya ulamuliro wa Mulungu? Nanga n’chiyani chidzachitikire anthu omwe amasankha kukhala kumbali ya chilombo chofiira kwambiri chofotokozedwa m’buku la Chivumbulutso?
ZIMENE ZIDZACHITIKIRE ANTHU OKHULUPIRIKA
4. Kodi mtumwi Yohane anaona Yesu ali ndi gulu liti kumwamba?
4 M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona magulu awiri a anthu omwe ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova ndipo adzalandira moyo wosatha. M’gulu loyamba muli anthu 144,000. (Chiv. 7:4) Iwo anatengedwa padziko lapansi kuti akakhale ndi Yesu mu Ufumu wake kumwamba. Limodzi ndi iye adzalamulira dziko lonse lapansi. (Chiv. 5:9, 10; 14:3, 4) Yohane anawaona m’masomphenya ataimirira ndi Yesu pa Phiri la Ziyoni kumwamba.—Chiv. 14:1.
5. Kodi n’chiyani chichitikire a 144,000 posachedwapa?
5 Kwa zaka zambiri, anthu ochuluka akhala akusankhidwa kuti akhale m’gulu la a 144,000. (Luka 12:32; Aroma 8:17) Koma Yohane anauzidwa kuti ochepa mwa anthu amenewa adzakhala adakali ndi moyo padzikoli m’masiku otsiriza. Chisautso chachikulu chisanayambe, anthu amenewa omwe ndi “otsala,” adzadindidwa “chidindo” chomaliza chosonyeza kuti Yehova wawavomereza. (Chiv. 7:2, 3; 12:17) Kenako mkatikati mwa chisautso chachikulu adzatengedwa kupita kumwamba kuti akakumane ndi anzawo a 144,000, omwe anamwalira ali okhulupirika. Kumeneko iwo azikalamulira limodzi ndi Yesu mu Ufumu wa Mulungu.—Mat. 24:31; Chiv. 5:9, 10.
6-7. (a) Kodi Yohane anaonanso gulu liti, nanga tikuphunzira chiyani za gululi? (b) N’chifukwa chiyani odzozedwa omwe ali padzikoli komanso a “khamu lalikulu” ayenera kuchita chidwi ndi zomwe zili pa Chivumbulutso 7?
6 Pambuyo poona gulu lopita kumwamba, Yohane anaona “khamu lalikulu.” Mosiyana ndi a 144,000, gulu lachiwirili chiwerengero chake sichikudziwika. (Chiv. 7:9, 10) Kodi tikuuzidwa zotani zokhudza gulu limeneli? Yohane anauzidwa kuti: “Amenewa ndi amene atuluka m’chisautso chachikulu, ndipo achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa.” (Chiv. 7:14) “Khamu lalikulu” limeneli likadzapulumuka pa chisautso chachikulu, lidzakhala padzikoli ndipo lidzasangalala ndi madalitso ochuluka.—Sal. 37:9-11, 27-29; Miy. 2:21, 22; Chiv. 7:16, 17.
7 Kaya tasankhidwa kuti tidzapite kumwamba kapena tidzakhale padzikoli, kodi timadziona kuti tili m’gulu la anthu amene zomwe zafotokozedwa pa Chivumbulutso 7 zidzawachitikire? Tizidziona choncho. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri kwa magulu awiri a atumiki a Mulungu amenewa. Tidzakhala ndi chimwemwe chochuluka chifukwa choti tinasankha kukhala kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Kodi buku la Chivumbulutso limatiuzanso zinthu ziti zokhudza chisautso chachikulu?—Mat. 24:21.
ZIMENE ZIDZACHITIKIRE OMWE AMATSUTSA MULUNGU
8. Kodi chisautso chachikulu chidzayamba bwanji, nanga chidzakhudza bwanji anthu ambiri?
8 Monga mmene nkhani yapita ija inafotokozera, posachedwapa maboma a m’dzikoli adzaukira Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonse zonyenga. (Chiv. 17:16, 17) Ichi chidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu. Kodi zimenezi zidzachititsa kuti anthu ambiri ayambe kulambira Yehova? Ayi. M’malomwake, Chivumbulutso chaputala 6 chimasonyeza kuti panthawi yovutayi, anthu omwe satumikira Yehova adzafunafuna chitetezo kwa andale komanso amalonda a m’dzikoli omwe amayerekezeredwa ndi mapiri. Chifukwa choti iwo sadzakhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu, Yehova adzawaona kuti ndi otsutsa.—Luka 11:23; Chiv. 6:15-17.
9. Kodi anthu a Yehova adzachita bwanji zinthu mosiyana ndi ena pa chisautso chachikulu, nanga zotsatira zake zidzakhala zotani?
9 Kunena zoona, atumiki a Yehova adzachita zinthu mosiyana kwambiri ndi ena panthawi yovuta ya chisautso chachikulu. Iwo adzakhala gulu lokhalo lomwe lizidzatumikira Mulungu padzikoli ndipo azidzakana kukhala kumbali ya “chilombo.” (Chiv. 13:14-17) Zimenezi zidzakwiyitsa kwambiri anthu omwe amatsutsa Yehova. Zotsatira zake n’zakuti mgwirizano wa mayiko udzaukira anthu a Mulungu padziko lonse. Baibulo linaneneratu kuti zimene mayiko adzachitezi ndi kuukira kwa Gogi wa ku Magogi.—Ezek. 38:14-16.
10. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 19:19-21, kodi Yehova adzatani anthu ake akadzaukiridwa?
10 Kodi Yehova adzatani ndi kuukira kwankhanza kumeneku? Iye amatiuza kuti: “Mkwiyo wanga udzatulukira m’mphuno mwanga.” (Ezek. 38:18, 21-23) Pa Chivumbulutso 19 amafotokoza zimene zidzachitike pambuyo pake. Yehova adzatumiza Mwana wake kuti akateteze anthu ake komanso kugonjetsa adani awo. Yesu adzamenya nkhondoyi pamodzi ndi ‘magulu a nkhondo amene ali kumwamba,’ omwe ndi angelo okhulupirika komanso a 144,000. (Chiv. 17:14; 19:11-15) Kodi zotsatirapo za nkhondoyi zidzakhala zotani? Anthu komanso mabungwe omwe amatsutsa Yehova adzawonongedweratu.—Werengani Chivumbulutso 19:19-21.
NKHONDO IKADZATHA PADZAKHALA UKWATI
11. Kodi n’chiyani chomwe chidzakhale pachimake pa zochitika za m’buku la Chivumbulutso?
11 Tangoganizani mmene anthu okhulupirika padzikoli adzamvere akadzapulumuka pakuwonongedwa kwa adani a Mulungu. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri. Ngakhale kuti kumwamba kudzakhala chisangalalo Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, pali chinthu chinanso chomwe chidzachititse kuti chisangalalocho chiwonjezereke kwambiri. (Chiv. 19:1-3) Kudzakhala “ukwati wa Mwanawankhosa,” womwe udzakhala pachimake pa zochitika za m’buku la Chivumbulutso.—Chiv. 19:6-9.
12. Monga mmene lemba la Chivumbulutso 21:1, 2 likusonyezera, kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzachitika liti?
12 Kodi ukwatiwu udzachitika liti? A 144,000 onse adzakhala atapita kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Komatu iyi siidzakhala nthawi ya ukwati wa Mwanawankhosa. (Werengani Chivumbulutso 21:1, 2.) Ukwatiwu udzachitika pambuyo poti nkhondo ya Aramagedo yamenyedwa ndipo adani onse a Mulungu awonongedwa.—Sal. 45:3, 4, 13-17.
13. Kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzatanthauza chiyani kwenikweni kwa Yesu ndi odzozedwa?
13 Kodi ukwati wa Mwanawankhosa udzatanthauza chiyani kwa Yesu ndi odzozedwa? Mofanana ndi ukwati womwe umagwirizanitsa mwamuna ndi mkazi, ukwati wophiphiritsawu udzachititsa kuti Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu agwirizane ndi a 144,000, omwe ndi “mkwatibwi” wake. Kumeneku kudzakhala kukhazikitsidwa kwa boma latsopano lomwe lidzalamulira dzikoli kwa zaka 1,000.—Chiv. 20:6.
MMENE MZINDA WOKONGOLA UMAKHUDZIRA TSOGOLO LANU
14-15. Kodi pa Chivumbulutso 21 amayerekezera a 144,000 ndi chiyani? (Onani chithunzi chapachikuto.)
14 Kenako pa Chivumbulutso 21 amayerekezera a 144,000 ndi mzinda wokongola kwambiri womwe ukutchedwa “Yerusalemu Watsopano.” (Chiv. 21:2, 9) Mzindawu uli pa miyala 12 ya maziko yomwe yalembedwa “mayina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” N’chifukwa chiyani Yohane anachita chidwi ndi zimenezi? Chifukwa chakuti anaona dzina lake litalembedwa pa umodzi wa miyalayo. Umenewutu unali mwayi waukulu kwambiri.—Chiv. 21:10-14; Aef. 2:20.
15 Palibe mzinda wooneka ngati umenewu. Unali ndi msewu waukulu wopangidwa ndi golide woyenga bwino, mageti 12 a ngale, makoma ndi maziko okongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali komanso mzindawu unayezedwa bwino kwambiri. (Chiv. 21:15-21) Komabe pakuoneka kuti pakusowekera chinachake. Taonani zimene kenako Yohane akutiuza: “Sindinaone kachisi mumzindawo, pakuti Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ndiye anali kachisi wake, komanso Mwanawankhosa ndiye kachisi wake. Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, pakuti ulemerero wa Mulungu unauwalitsa, ndipo nyale yake inali Mwanawankhosa.” (Chiv. 21:22, 23) Anthu omwe adzakhale mbali ya Yerusalemu Watsopano azidzakhala ndi Yehova. (Aheb. 7:27; Chiv. 22:3, 4) Choncho Yehova ndi Yesu ndiwo kachisi wa mzindawu.
16. Kodi n’chiyani chomwe chidzachitikire anthu mu Ulamuliro wa Zaka 1000 wa Ufumu wa Mulungu?
16 Odzozedwa amasangalala kwambiri akamaganizira za mzinda umenewu. Koma nawonso amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli amachita chidwi ndi mzindawu. Mu Ulamuliro wa Zaka 1000 wa Ufumu wa Mulungu, Yerusalemu Watsopano adzabweretsa madalitso osaneneka. Yohane anaona madalitsowa akuyenda ngati “mtsinje wa madzi a moyo.” Kumbali zonse za mtsinjewo kunali “mitengo ya moyo” yomwe inali ndi masamba “ochiritsira mitundu ya anthu.” (Chiv. 22:1, 2) Anthu onse omwe adzakhale ndi moyo padzikoli adzakhala ndi mwayi wopindula ndi zinthuzi. Pang’ono ndi pang’ono anthu onse omvera adzathandizidwa kuti akhale angwiro. Sikudzakhalanso kudwala, kumva kupweteka kapenanso kulira chifukwa cha mavuto.—Chiv. 21:3-5.
17. Mogwirizana ndi Chivumbulutso 20:11-13, kodi ndi ndani adzasangalale ndi madalitso mu Ulamuliro wa Zaka 1000?
17 Kodi ndi ndani adzasangalale ndi madalitso amenewa? Poyamba ndi khamu lalikulu lomwe lidzapulumuke pa Aramagedo komanso ana omwe angadzabadwe m’dziko latsopano. Koma pa Chivumbulutso 20 palinso lonjezo lakuti akufa adzaukitsidwa. (Werengani Chivumbulutso 20:11-13.) “Olungama” okhulupirika omwe anamwalira limodzi ndi “osalungama” amene sanapatsidwe mwayi wophunzira za Yehova, adzaukitsidwa padzikoli. (Mac. 24:15; Yoh. 5:28, 29) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti aliyense adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo padzikoli pa nthawi ya Ulamuliro wa Zaka 1000? Ayi. Anthu oipa omwe anakana mwayi wotumikira Yehova pa nthawi imene anali ndi moyo, sadzaukitsidwa. Iwo atapatsidwa mwayi anasonyeza kuti sanali oyenera kukhala ndi moyo m’Paradaiso.—Mat. 25:46; 2 Ates. 1:9; Chiv. 17:8; 20:15.
MAYESERO OMALIZA
18. Kodi zinthu zidzakhala bwanji padzikoli zaka 1000 zikamadzatha?
18 Zaka 1000 zikamadzatha, anthu onse padzikoli adzakhala ali angwiro. Palibe munthu yemwe adzakhale ndi uchimo womwe tinatengera kwa Adamu. (Aroma 5:12) Temberero la uchimo wa Adamu lidzakhala litachotsedweratu. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu onse padzikoli ‘adzakhalanso ndi moyo’ monga angwiro kumapeto kwa zaka 1,000.—Chiv. 20:5.
19. N’chifukwa chiyani padzafunike mayesero omaliza?
19 Timadziwa kuti Yesu anakhalabe wangwiro pamene Satana ankamuyesa. Koma kodi anthu onse omwe adzakhale angwiro pa nthawiyo adzakhalabe okhulupirika Satana akadzapatsidwa mwayi wowayesa? Aliyense adzayankha yekha funso limeneli Satana akadzamasulidwa kuphompho pambuyo pa zaka 1000. (Chiv. 20:7) Anthu omwe adzakhale okhulupirika pa mayesero omalizawa adzalandira moyo wosatha komanso adzasangalala ndi ufulu weniweni. (Aroma 8:21) Anthu otsutsa adzawonongedwa mpaka kalekale limodzi ndi Mdyerekeziyo komanso ziwanda zake.—Chiv. 20:8-10.
20. Kodi mukumva bwanji mukaganizira za maulosi osangalatsa opezeka m’buku la Chivumbulutso?
20 Kodi mukumva bwanji pambuyo pokambirana mwachidule zimene zili m’buku la Chivumbulutso? Kodi si zosangalatsa kudziyerekezera mulipo pa nthawi imene maulosi onsewa azidzakwaniritsidwa? Kodi sizikukuchititsani kukhala wofunitsitsa kuitanira ena kuti azilambira nafe Mulungu woona? (Chiv. 22:17) Chifukwa chosangalala ndi zinthu zochititsa chidwi zomwe zichitike m’tsogolozi, mtima wathu umatilimbikitsa kulankhula zomwe mtumwi Yohane ananena pomwe anati: “Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.”—Chiv. 22:20.
NYIMBO NA. 27 Ulemerero wa Ana a Mulungu Udzaonekera
a Iyi ndi nkhani yomaliza pa nkhani zitatu zomwe zikufotokoza buku la Chivumbulutso. Monga mmene tionere munkhaniyi, anthu omwe apitirize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova adzakhala ndi tsogolo labwino, koma amene amatsutsa ulamuliro wa Mulungu adzawonongedwa mochititsa manyazi.