Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Malinga ndi mmene ayenera kugwirira ntchito, kodi pali kusiyana pakati pa mawu a m’Baibulo akuti “nkhosa zina” ndi “khamu lalikulu”?
Inde kulipo, ngakhale kuti sitiyenera kusamala mopambanitsa za kugwiritsira ntchito mawu kapena kukhumudwa ngati wina agwiritsira ntchito mawuwo mowasinthanitsa.
Akristu ambiri amadziŵa bwino malemba amene timapezapo mawu ameneŵa. Limodzi la iwo ndi Yohane 10:16. Pamenepo Yesu anati: “Nkhosa zina ndili nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga, ndipo zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” Liwu linalo, “khamu lalikulu,” limapezeka pa Chivumbulutso 7:9. Timaŵerenga kuti: “Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimilira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo.”
Choyamba tiyeni tipende Yohane 10:16. Kodi nkhosa zinazo ndani? Chabwino, tingachite bwino kukumbukira kuti otsatira a Yesu okhulupirika onse amatchedwa nkhosa. Pa Luka 12:32, iye anatcha ophunzira ake omwe akapita kumwamba kuti “kagulu ka nkhosa.” “Nkhosa” za “kagulu ka nkhosa” zidzakhala mbali ya Ufumuwo kumwamba. Komabe, palinso ena, aja amene ali ndi chiyembekezo chosiyana ndi chimenecho, amene Yesu amawaonanso kukhala nkhosa.
Tingaone zimenezi mu Yohane chaputala 10. Atalankhula za nkhosa, monga atumwi ake amene anawaitana ku moyo wakumwamba, Yesu anawonjezera m’vesi 16 kuti: “Nkhosa zina ndili nazo, zimene siziri za khola ili; izinso ndiyenera kuzitenga.” Mboni za Yehova zadziŵa kwa nthaŵi yaitali kuti m’vesili Yesu anali kulankhula za anthu amene ali ndi chiyembekezo cha moyo wa pa dziko lapansi. Okhulupirika ambiri m’nthaŵi zakale Chikristu chisanakhale, onga Abrahamu, Sara, Nowa, ndi Malaki, anali ndi chiyembekezo chotero. Motero tingawaphatikize bwino lomwe pa “nkhosa zina” za pa Yohane 10:16. Mkati mwa Zaka Chikwi, mboni zimenezo za m’nthaŵi yakale Chikristu chisanakhale zidzaukitsidwa ndipo panthaŵiyo zidzaphunzira ndi kulandira Kristu Yesu, zikumakhala “nkhosa zina” za Mbusa Wabwino.
Timadziŵanso kuti chiyambire pamene chiitano cha onse cha kagulu kopita kumwamba chinatha, mamiliyoni akhala Akristu oona. Ameneŵanso ali oyenera kutchedwa “nkhosa zina,” popeza kuti sali mbali ya “kagulu ka nkhosa.” M’malo mwake, nkhosa zina lerolino zikuyang’ana kutsogolo kupitirizabe ndi moyo mpaka kuloŵa m’paradaiso wa pa dziko lapansi.
Tsopano, kodi tinganenenji za amene ali “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9? Chabwino, onani pa vesi 13, ndi funso lakuti, “Ndiwo ayani, ndipo achokera kuti?” Timapeza yankho pa Chivumbulutso 7:14: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.” Motero “khamu lalikulu” ndilo aja amene atuluka, kapena amene apulumuka chisautso chachikulu. Monga momwe vesi 17 likunenera, iwo ‘adzatsogoleredwa ku akasupe a madzi a moyo’ pa dziko lapansi.
Komabe, nkomveka kuti ameneŵa asanapulumuke chisautso chachikulu choyandikiracho, ayenera choyamba kukhala atayeretsa zovala zawo m’mwazi wa Mwanawankhosa, ndi kukhala olambira oona. Chifukwa chake, ngakhale kuti Chivumbulutso 7:9 chikulongosola khamu limeneli pambuyo pa chisautso chimenecho, tingagwiritsire ntchito liwu lakuti “khamu lalikulu” kwa onse amene ali ndi chiyembekezo cha kukhala pa dziko lapansi amene akupereka utumiki wopatulika kwa Yehova tsopano, kutatsala pang’ono kuti chisautso chachikulu chiulike ndi kuukira chipembedzo chonyenga kwa mitundu.
Mwachidule, tingakumbukire “nkhosa zina” kukhala liwu lalikulu, loloŵetsamo atumiki a Mulungu onse okhala ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi. Limaphatikizapo gulu locheperapo la onga nkhosa lerolino amene akusonkhanitsidwa monga “khamu lalikulu” lokhala ndi chiyembekezo cha kupulumuka amoyo chisautso chachikulu choyandikiracho. Akristu okhulupirika ambiri amene alipo ndi moyo lerolino ali a “nkhosa zina,” ndiponso ali a “khamu lalikulu.”
Nkofunika kubwereza kuti, ngakhale kuti nkofunika kudziŵa bwino kusiyana kwa mawuŵa, sikofunika kwa Mkristu aliyense kukhala wosamala mopambanitsa za mmene mawu ayenera kugwiritsiridwa ntchito—kumene kungatchedwe kupenda mawu konkitsa. Paulo anachenjeza za ena amene anali ‘otukumuka’ ndi okonda “makani a mawu.” (1 Timoteo 6:4) Ngati aliyense wa ife adziŵa kusiyana kokhala pakati pa mawu ena, nzabwino zimenezo. Komabe, sitifunikira kusuliza ena, cha mumtima kapena ndi mawu, ngati angagwiritsire ntchito mawu a m’Baibulo mosalondola kwenikweni.