Mutu 21
Miliri ya Yehova pa Matchalitchi Achikhristu
Masomphenya 5—Chivumbulutso 8:1–9:21
Nkhani yake: Kulira kwa malipenga 6 mwa malipenga 7
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Kuyambira nthawi imene Khristu Yesu anaikidwa pampando wachifumu mu 1914 mpaka pa chisautso chachikulu
1. Kodi chinachitika n’chiyani Mwanawankhosa atamatula chidindo cha 7?
ANGELO aja adzapitirizabe kugwira mwamphamvu “mphepo zinayi” mpaka anthu 144,000 a Isiraeli wauzimu atadindidwa chidindo ndiponso anthu a khamu lalikulu atayenerera kupulumuka. (Chivumbulutso 7:1-4, 9) Komabe, mphepo yamkunthoyi isanawombe padziko lapansi, chiweruzo choopsa cha Yehova padziko la Satanali chiyenera kulengezedwa. Pamene Mwanawankhosa ankamatula chidindo chomaliza cha 7, Yohane ayenera kuti anali ndi chidwi kuti aone zimene zichitike. Ndiyeno iye akutiuza zimene anaona, kuti: “[Mwanawankhosa] atamatula chidindo cha 7, kumwamba kunangoti chete! pafupifupi hafu ya ola. Kenako ndinaona angelo 7 ataimirira pamaso pa Mulungu, ndipo anapatsidwa malipenga 7.”—Chivumbulutso 8:1, 2.
Nthawi Yopemphera Kuchokera Pansi pa Mtima
2. Kodi n’chiyani chinachitika pa nthawi yophiphiritsa yokwana hafu ya ola, imene kumwamba kunakhala chete?
2 N’zochititsa chidwi kuti kumwamba kunangokhala chete, chifukwa hafu ya ola ndi nthawi yaitali kwambiri ngati munthu akudikirira chinachake kuti chichitike. Pa nthawiyi, ngakhale zamoyo zimene zinkatamanda Mulungu mosalekeza, zinasiya kaye. (Chivumbulutso 4:8) Chifukwa chiyani? Yohane anadziwa chifukwa chake ataona zinthu zina zimene zinachitika m’masomphenyawa. Iye akutiuza kuti: “Mngelo wina anafika ndi kuimirira kuguwa lansembe. Iye anali ndi chiwiya chofukiziramo chagolide, ndipo anamupatsa zofukiza zambiri kuti azipereke nsembe limodzi ndi mapemphero a oyera onse paguwa lansembe lagolide, limene linali pamaso pa mpando wachifumu. Pamenepo, utsi wa zofukizazo unakwera pamaso pa Mulungu kuchokera m’dzanja la mngeloyo limodzi ndi mapemphero a oyera.”—Chivumbulutso 8:3, 4.
3. (a) Kodi kufukiza zofukiza kukutikumbutsa chiyani? (b) Kodi cholinga cha hafu ya ola imene kumwamba kunakhala chete n’chiyani?
3 Zimenezi zikutikumbutsa zimene zinkachitika kale m’nthawi ya Ayuda. Iwo ankafukiza zofukiza tsiku ndi tsiku kuchihema ndipo patapita zaka, ankafukiza kukachisi wa ku Yerusalemu. (Ekisodo 30:1-8) Pa nthawi yofukiza zofukizazo, Aisiraeli amene sanali ansembe ankadikira panja pa malo opatulika n’kumapemphera, mwina chamumtima, kwa Mulungu amene utsi wa zofukizazo unkapita. (Luka 1:10) Apa tsopano Yohane anaona zofanana ndi zimenezi zikuchitika kumwamba. Zofukiza zimene mngelo akufukiza zinaperekedwa limodzi ndi “mapemphero a oyera.” Ndipotu m’masomphenya ena a m’mbuyomu, tinaona kuti zofukiza zikuimira mapemphero amenewo. (Chivumbulutso 5:8; Salimo 141:1, 2) Choncho zikuoneka kuti nthawi yophiphiritsa imene kumwamba kunakhala chete inapereka mpata woti mapemphero a oyera amene ali padziko lapansi amvedwe.
4, 5. Kodi ndi zinthu zapadera ziti zimene zinachitika m’mbuyomu zimene zikutithandiza kudziwa nthawi yomwe ikuimiridwa ndi nthawi yophiphiritsa yokwana hafu ya ola, imene kumwamba kunakhala chete?
4 Kodi tingathe kudziwa nthawi imene zimenezi zinachitika? Inde tingadziwe, tikaona bwinobwino masomphenya onsewa komanso zinthu zapadera zimene zinachitika chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye. (Chivumbulutso 1:10) Kuyambira mu 1918 mpaka mu 1919, zimene zinachitika padziko lapansili zikugwirizana kwambiri ndi zimene zatchulidwa m’masomphenya a pa Chivumbulutso 8:1-4. Kwa zaka 40 chaka cha 1914 chisanafike, Mboni za Yehova, zimene zinkadziwika kuti Ophunzira Baibulo pa nthawiyo, zinakhala zikulengeza molimba mtima kuti nthawi za Akunja zidzatha m’chaka cha 1914. Zinthu zoopsa zimene zinachitika m’chaka chimenechi zinasonyeza kuti iwo ankanena zoona. (Luka 21:24, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu; Mateyu 24:3, 7, 8) Koma ambiri mwa iwo ankakhulupiriranso kuti mu 1914 adzatengedwa kuchoka padziko lapansili kupita kukalandira cholowa chawo kumwamba. Zimenezi sizinachitike. M’malomwake, pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, iwo anazunzidwa kwambiri. Pa October 31, 1916, Charles T. Russell, yemwe anali pulezidenti woyamba wa Watch Tower Society, anamwalira. Kenako pa July 4, 1918, Joseph F. Rutherford, yemwe anali pulezidenti watsopano wa bungwe la Watch Tower Society, pamodzi ndi anzake 7 amene ankatsogolera nawo bungweli, anatumizidwa kundende ya ku Atlanta, m’chigawo cha Georgia, ataweruzidwa molakwa kuti akhale m’ndende kwa zaka zambiri.
5 Tsopano Akhristu odzozedwa oona mtima anaima mitu. Iwo ankadzifunsa kuti: “Kodi Mulungu akufuna kuti tichite chiyani tsopano? Kodi titengedwa liti kupita kumwamba?” Choncho, m’magazini ya Nsanja ya Olonda yachingelezi ya May 1, 1919, munali nkhani ya mutu wakuti, “Kodi N’chiyani Chichitike Popeza Ntchito Yokolola Yatha?” Nkhaniyi inasonyeza kuti Akhristuwo sankadziwa chochita ndipo inalimbikitsa Akhristu okhulupirika kuti apitirizebe kupirira. Nkhaniyi inanena kuti: “Tikukhulupirira kuti tsopano ntchito yokolola anthu a m’gulu la ufumu yatha. Anthu onsewo adindidwa chidindo ndipo khomo latsekedwa.” Pa nthawi yovutayi, mapemphero ochokera pansi pa mtima a Akhristu odzozedwa ankakwera kumwamba mofanana ndi utsi wa zofukiza zambiri ndipo mapempherowo ankamvedwa.
Anaponya Moto Kudziko Lapansi
6. Kodi chinachitika n’chiyani kumwamba nthawi yokhala chete ija itatha, ndipo n’chiyani chinachititsa zimenezi?
6 Yohane akutiuza kuti: “Koma nthawi yomweyo, mngeloyo anatenga chiwiya chofukiziramo chija, n’kudzazamo moto umene anapala paguwa lansembe, ndi kuuponyera kudziko lapansi. Ndiyeno kunagunda mabingu, kunamveka mawu, ndipo kunachita mphezi ndi chivomezi.” (Chivumbulutso 8:5) Nthawi yokhala chete ija itatha, mwadzidzidzi kunachitika zinthu zina zochititsa chidwi. Zinthuzo ziyenera kuti zinachitika chifukwa cha mapemphero a oyera. Izi zili choncho chifukwa moto umene unapalidwa paguwa la nsembe zofukiza ndi womwe unayambitsa zimenezi. Kale kwambiri mu 1513 B.C.E., paphiri la Sinai panachitika zinthu zosiyanasiyana zomwe zinkasonyeza kuti Yehova waika maganizo ake onse pa anthu ake. Zina mwa zinthuzo zinali chivomezi chimene chinagwedeza phirilo, phokoso lalikulu, moto, mabingu ndi mphezi. (Ekisodo 19:16-20) Motero zinthu zofanana ndi zimenezi, zomwe Yohane ananena, zikusonyezanso kuti Yehova anaika maganizo ake onse pa atumiki ake padziko lapansili. Koma zimene Yohane ankaonazi sizinali zenizeni. Zinali zizindikiro chabe. (Chivumbulutso 1:1) Choncho kodi zinthu zophiphiritsazi monga moto, mabingu, mawu, mphezi ndiponso chivomezi zikutanthauza chiyani masiku ano?
7. (a) Kodi Yesu anakoleza moto wotani wophiphiritsa padziko lapansi pa nthawi ya utumiki wake? (b) Kodi abale auzimu a Yesu anakoleza bwanji moto m’Matchalitchi Achikhristu?
7 Pa nthawi inayake, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndinabwera kudzakoleza moto padziko lapansi.” (Luka 12:49) Zoona, iye anakolezadi moto. Popeza Yesu ankalalikira mwakhama, iye anathandiza Ayuda kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi nkhani yofunika kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti Ayudawo ayambe kutsutsana mwamphamvu, zomwe zinali ngati moto woyaka pakati pawo. (Mateyu 4:17, 25; 10:5-7, 17, 18) Mu 1919, abale auzimu a Yesu padziko lapansi, omwe anali kagulu kakang’ono ka Akhristu odzozedwa amene anapirira mayesero osiyanasiyana pa nthawi ya nkhondo yoyamba ya padziko lonse, anakoleza moto ngati umenewu m’Matchalitchi Achikhristu. Mu September chaka chomwechi, zinaonekeratu kuti mzimu wa Yehova ukugwira ntchito pa anthu ake a Mboni okhulupirika amene anachokera m’madera osiyanasiyana n’kudzasonkhana ku Cedar Point, Ohio, m’dziko la United States. Joseph F. Rutherford, yemwe anali atangotulutsidwa kumene m’ndende ndiponso milandu yonse yomwe ankamuzenga itatsala pang’ono kuthetsedwa, analankhula molimba mtima kwa anthu omwe anasonkhana pamsonkhanowo. Iye anati: “Pomvera lamulo la Mbuye wathu, ndiponso pozindikira mwayi ndi udindo umene tili nawo womenya nkhondo yolimbana ndi ziphunzitso zolakwika, zimene zaika anthu pa ukapolo kwa nthawi yaitali, ntchito yathu yaikulu idakali yolengeza za kubwera kwa ufumu waulemerero wa Mesiya.” Pamenepatu nkhani yaikulu, kapena kuti yoyaka ngati moto, inali yokhudza Ufumu wa Mulungu.
8, 9. (a) Kodi J. F. Rutherford anafotokoza kuti anthu a Mulungu anali ndi mtima wotani ndiponso ankalakalaka kuchita chiyani m’zaka zovuta za nkhondo? (b) Kodi moto unaponyedwa bwanji kudziko lapansi? (c) Kodi mabingu, mawu, mphezi ndi zivomezi zachitika bwanji padzikoli?
8 Ponena za mavuto amene anthu a Mulungu anali atakumana nawo chaposachedwa, M’bale Rutherford anati: “Adani athu anatiukira mwankhanza kwambiri moti nkhosa zambiri zokondedwa za Ambuye zinangoima chilili, podabwa ndiponso posowa chochita, uku zikupemphera ndi kudikirira kuti Ambuye azionetse chifuniro chake. . . . Koma ngakhale kuti tinakhumudwitsidwa kwakanthawi, tinkalakalaka kwambiri kulengeza uthenga wa ufumu.”—Onani Nsanja ya Olonda yachingelezi ya September 15, 1919, tsamba 280.
9 M’chaka chomwecho cha 1919, zimene ankalakalaka zija zinatheka. Gulu laling’ono la Akhristu akhamali linakhala ngati likuyaka moto mwauzimu ndipo linayamba kugwira ntchito yolalikira padziko lonse. (Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 5:19.) Moto unaponyedwadi kudziko lapansi, kutanthauza kuti Ufumu wa Mulungu unakhala nkhani yaikulu kwambiri, ndipo zili chonchobe mpaka pano. Nthawi yokhala chete inatha ndipo kunayamba kumveka mawu amphamvu olengeza momveka bwino uthenga wa Ufumu. Machenjezo ochokera m’Baibulo, omveka mwamphamvu ngati kugunda kwa mabingu, anayamba kulengezedwa. Mofanana ndi kuwala kwa mphezi, mfundo za choonadi zinayamba kuwala kuchokera m’Mawu aulosi a Yehova. Komanso mofanana ndi mmene chivomezi champhamvu chimagwedezera zinthu, uthengawu unagwedeza mwamphamvu zipembedzo zonse. Akhristu odzozedwa anaona kuti panali ntchito yaikulu imene inkafunika kugwiridwa. Ndipo mpaka masiku ano, ntchito imeneyi ikupitirizabe kukula padziko lonse kumene kuli anthu, zimene zikubweretsa ulemerero kwa Mulungu.—Aroma 10:18.
Kukonzekera Kuliza Malipenga
10. Kodi angelo 7 anakonzekera kutani, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
10 Yohane anapitiriza kunena kuti: “Angelo 7 okhala ndi malipenga 7 aja, anakonzekera kuliza malipengawo.” (Chivumbulutso 8:6) Kodi kuliza malipengawo kukutanthauza chiyani? Kale ku Isiraeli, anthu ankaliza malipenga ngati chizindikiro chosonyeza masiku ofunika kwambiri kapena zinthu zina zake zapadera. (Levitiko 23:24; 2 Mafumu 11:14) Mofanana ndi zimenezi, kulira kwa malipenga kumene Yohane anali atatsala pang’ono kumva kunali chizindikiro chosonyeza nkhani yofunika kwambiri yokhudza moyo ndi imfa.
11. Kuyambira mu 1919 mpaka 1922, kodi Akhristu odzozedwa anatanganidwa ndi ntchito yokonzekera chiyani?
11 Pamene angelo ankakonzekera kuliza malipengawo, sitikukayikira kuti ankaperekanso malangizo othandiza pokonzekera kugwira ntchito yolalikira padziko lapansi. Kuyambira mu 1919 mpaka mu 1922, Akhristu odzozedwa omwe anali atalimbikitsidwa, anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yokonzanso zinthu kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino. Anatanganidwanso ndi ntchito yomanga nyumba zosindikizira mabuku. Mu 1919, magazini ya The Golden Age, yomwe imadziwika ndi dzina lakuti Galamukani! masiku ano, inayamba kufalitsidwa monga “Magazini Yonena Zoona, Yopereka Chiyembekezo, Ndiponso Yolimbitsa Chikhulupiriro.” Magazini imeneyi inakhaladi ngati lipenga chifukwa inathandiza kwambiri kuulula zimene zipembedzo zonyenga zinkachita polowerera m’ndale.
12. Kodi kulira kwa lipenga lililonse kukulengeza chiyani, ndipo zimenezi zikutikumbutsa chiyani chimene chinachitika m’nthawi ya Mose?
12 Monga momwe tionere, kulira kwa lipenga lililonse kunkalengeza za kubwera kwa miliri yoopsa kwambiri yowononga magawo ena a dziko lapansi. Ina mwa miliri imeneyi ikutikumbutsa za miliri imene Yehova anatumiza polanga Aiguputo m’nthawi ya Mose. (Ekisodo 7:19–12:32) Yehova anatumiza miliriyi poweruza mtunduwo, ndipo inathandiza kuti anthu a Mulungu atuluke mu ukapolo. Miliri imene Yohane anaona inakwaniritsa cholinga chofanana ndi chimenechi. Komabe, miliri imeneyi ndi yophiphiritsa ndipo ikuimira chiweruzo cholungama cha Yehova.—Chivumbulutso 1:1.
Kodi “Gawo Limodzi mwa Magawo Atatu” N’chiyani?
13. Kodi chinachitika n’chiyani angelo ataliza malipenga anayi oyambirira, ndipo zimenezi zikubweretsa funso lotani?
13 Monga mmene tionere kutsogoloku, angelo ataliza malipenga anayi oyambirira, miliri inagwera pa “gawo limodzi mwa magawo atatu” a dziko lapansi, a nyanja, a mitsinje ndi akasupe a madzi, ndiponso a dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. (Chivumbulutso 8:7-12) Gawo limodzi mwa magawo atatu la chinthu limakhala lalikulu ndithu, koma si chinthu chonsecho. (Yerekezerani ndi Yesaya 19:24; Ezekieli 5:2; Zekariya 13:8, 9.) Choncho, kodi “gawo limodzi mwa magawo atatu” limene likuyenera kwambiri kuwonongedwa ndi miliri imeneyi, ndi liti? Anthu ochuluka padziko lapansili anapusitsidwa ndiponso kuchititsidwa khungu ndi Satana pamodzi ndi mbewu yake. (Genesis 3:15; 2 Akorinto 4:4) Zili ngati mmene Davide ananenera, kuti: “Onse apatuka, ndipo onsewo ndi achinyengo. Palibe aliyense amene akuchita zabwino, palibiretu ndi mmodzi yemwe.” (Salimo 14:3) Ndithudi, mtundu wonse wa anthu ukhoza kudzalandira chiweruzo choopsa. Koma makamaka gawo limodzi la anthu ndi limene lili ndi mlandu waukulu chifukwa likanatha kupewa mlandu umenewu. Limeneli ndi “gawo limodzi mwa magawo atatu.” Kodi “gawo limodzi mwa magawo atatu” limeneli n’chiyani?
14. Kodi gawo limodzi mwa magawo atatu lophiphiritsa limene Yehova analipatsa uthenga wamphamvu wokhudza miliri, n’chiyani?
14 Gawo limeneli ndi Matchalitchi Achikhristu. M’zaka za m’ma 1920, pafupifupi munthu mmodzi pa anthu atatu alionse padziko lonse ankati ndi Mkhristu. Anthu a mpatuko omwe anachoka m’Chikhristu choona ndi amene anayambitsa Matchalitchi Achikhristu, ndipo Yesu ndi ophunzira ake analosera za mpatuko waukulu umenewu. (Mateyu 13:24-30; Machitidwe 20:29, 30; 2 Atesalonika 2:3; 2 Petulo 2:1-3) Atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu amati ali m’kachisi wa Mulungu ndipo amanena kuti iwowo amaphunzitsa mfundo zogwirizana ndi Chikhristu choona. Koma ziphunzitso zawo n’zosiyana kwambiri ndi choonadi cha m’Baibulo, ndipo akupitiriza kuchita zinthu zonyozetsa dzina la Mulungu. M’pake kuti Matchalitchi Achikhristu akuimiridwa ndi gawo limodzi mwa magawo atatu, ndipo akulandira uthenga wamphamvu wochokera kwa Yehova wokhudza miliri yomwe idzawagwere. Gawo limeneli, lomwe ndi gawo limodzi mwa magawo atatu la anthu onse padzikoli, likuyeneradi kulangidwa ndi Mulungu, osati kuchitiridwa chifundo.
15. (a) Kodi lipenga lililonse linalizidwa m’chaka chimodzi basi? Fotokozani. (b) Kodi ndani amene akuthandiza Akhristu odzozedwa polengeza uthenga wokhudza chiweruzo cha Yehova?
15 Mogwirizana ndi malipenga amene angelo aja anawaliza motsatizana, kuyambira mu 1922 mpaka mu 1928 pamisonkhano yokwana 7 pankakhala zigamulo zapadera zosiyanasiyana. Koma malipenga aja sanalizidwe m’zaka zokhazi basi. Pamene tsiku la Ambuye likupitirira, gulu la Yehova likupitiriza kuulula mosapita m’mbali zinthu zoipa zimene Matchalitchi Achikhristu akuchita. Uthenga wokhudza chiweruzo cha Yehova uyenera kulalikidwa padziko lonse kwa anthu a mitundu yonse, ngakhale kuti m’mayiko osiyanasiyana anthu amadana ndi anthu a Mulungu amene akulengeza uthengawu ndipo amawazunza. Ndiyeno mapeto a dziko la Satanali adzafika uthengawu ukalalikidwa padziko lonse m’mitundu yonse ya anthu. (Maliko 13:10, 13) N’zosangalatsa kuti khamu lalikulu likuthandiza Akhristu odzozedwa polengeza mopanda mantha uthenga wachiweruzo, womwe ndi wofunika kwambiri padziko lonse.
Gawo Limodzi mwa Magawo Atatu a Dziko Lapansi Linapsa
16. N’chiyani chinachitika mngelo woyamba ataliza lipenga lake?
16 Yohane analemba za angelo aja kuti: “Mngelo woyamba analiza lipenga lake. Atatero, panaoneka matalala ndi moto, zosakanikirana ndi magazi. Zimenezi zinaponyedwa kudziko lapansi. Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansi linapsa. Kuwonjezera pamenepo, gawo limodzi mwa magawo atatu a mitengo linapsa, komanso zomera zonse zobiriwira zinapsa.” (Chivumbulutso 8:7) Izi zikufanana ndi mliri wa 7 umene unagwera Aiguputo. Koma kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife masiku ano?—Ekisodo 9:24.
17. (a) Kodi mawu akuti ‘dziko lapansi’ opezeka pa Chivumbulutso 8:7 akutanthauza chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansili, lomwe ndi Matchalitchi Achikhristu, linapsa, ikutanthauza chiyani?
17 M’Baibulo, nthawi zina mawu akuti “dziko” amatanthauza anthu. (Genesis 18:25) Popeza mliri wachiwiri ukukhudza nyanja, imenenso imatanthauza anthu, mawu akuti ‘dziko lapansi’ ayenera kuti akutanthauza dongosolo la anthu lochitira zinthu looneka ngati lolimba. Satana ndi amene wakhazikitsa dongosolo limeneli ndipo latsala pang’ono kuwonongedwa. (2 Petulo 3:7; Chivumbulutso 21:1) Mliri womwe unachitika ukusonyeza kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansili, lomwe ndi Matchalitchi Achikhristu, likupsa ndi mkwiyo wotentha wa Yehova. Atsogoleri ake, omwe amaoneka okwezeka ngati mitengo pakati pa anthu ena onse m’matchalitchiwa, akupsa ndi uthenga womwe ukulengezedwa wokhudza chiweruzo choopsa cha Yehova. Ndipo anthu mamiliyoni ambirimbiri omwe ali m’Matchalitchi Achikhristu, ngati angapitirize kugwirizana ndi matchalitchiwa, adzakhala ngati udzu wowauka ndi moto, kutanthauza kuti Mulungu adzawaona kuti ndi ofota mwauzimu.—Yerekezerani ndi Salimo 37:1, 2.a
18. Kodi uthenga wokhudza chiweruzo cha Yehova unalengezedwa bwanji pamsonkhano umene unachitika mu 1922 ku Cedar Point?
18 Kodi uthenga wachiweruzo umenewu unalengezedwa bwanji? Sunalengezedwe pogwiritsa ntchito mabungwe ofalitsa nkhani, omwe ali mbali yadzikoli ndipo nthawi zambiri amanyoza “kapolo” wa Mulungu. (Mateyu 24:45) Uthengawu unalengezedwa m’njira yapadera kwambiri pamsonkhano wachiwiri wosaiwalika wa anthu a Mulungu womwe unachitika pa September 10, 1922, ku Cedar Point, m’chigawo cha Ohio, m’dziko la United States. Mogwirizana komanso mosangalala, anthu omwe anasonkhana pamsonkhanowu anavomereza chigamulo cha mutu wakuti, “Zimene Atsogoleri a Dzikoli Ayenera Kuchita” (A Challenge to World Leaders). Uthenga womwe unali m’chigamulochi unachenjeza dziko lophiphiritsa la masiku ano mosapita m’mbali, kuti: “Tikulimbikitsa anthu a mitundu yonse padziko lapansi kuti apereke umboni wotsimikizira kuti angakwanitsedi kubweretsa bata ndi mtendere padziko lapansi, komanso kuthandiza anthu kuti azikhala mosangalala. Ena mwa anthu amene tikuwalimbikitsa kupereka umboniwa ndi atsogoleri ndi olamulira, atsogoleri onse a matchalitchi onse a padziko lapansi, anthu awo pamodzi ndi amene amagwirizana nawo, komanso akuluakulu a zamalonda ndi a ndale. Akalephera kupereka umboni, tikuwalimbikitsa kuti amvere umboni umene ife tikupereka monga mboni za Ambuye, ndipo anene ngati umboni wathu uli woona kapena wabodza.”
19. Kodi anthu a Mulungu anapereka umboni wotani ku Matchalitchi Achikhristu wokhudza Ufumu wa Mulungu?
19 Akhristuwo anapereka umboni wakuti: “Tikukhulupirira ndipo tikulengeza kuti ufumu wa Mesiya ndi umene udzathetseretu mavuto onse a anthu, udzabweretsa mtendere padziko lonse lapansi komanso udzathandiza anthu kuti akhale ndi moyo wabwino, womwe anthu a mitundu yonse akuulakalaka. Tikukhulupirira ndi kulengezanso kuti anthu amene amagonjera mwakufuna kwawo ulamuliro wake wolungama, womwe wayamba kale, adzalandira madalitso osiyanasiyana monga mtendere wosatha, moyo, ufulu ndiponso adzakhala ndi chimwemwe chomwe sichidzatha.” M’masiku ovuta ano, maboma a anthu, makamaka a m’Mayiko Achikhristu, akulephera mochititsa manyazi kuthetsa mavuto padziko lapansili. Ndipo zimene atsogoleri a dzikoli akuyenera kuchita zija, zikulengezedwabe mwamphamvu kuposa mmene zinalili mu 1922. Choncho, m’pake kuti Ufumu wa Mulungu wokha, womwe wolamulira wake ndi Khristu wopambana pa nkhondo, ndi umene udzathetse mavuto onse a anthu.
20. (a) Kodi mpingo wa Akhristu odzozedwa unagwiritsa ntchito chiyani polengeza uthenga wachiweruzo mu 1922 komanso m’zaka zotsatira? (b) N’chiyani chinachitikira Matchalitchi Achikhristu lipenga loyamba litalira?
20 Pogwiritsa ntchito zigamulo, timapepala, timabuku, magazini, mabuku komanso nkhani za onse, mpingo wa Akhristu odzozedwa unapitiriza kulengeza uthenga umenewu ndi mauthenga ena. Lipenga loyamba litalira, Matchalitchi Achikhristu anamenyedwa ndi matalala ouma kwambiri. Zinaululika kuti matchalitchiwa ali ndi mlandu wamagazi chifukwa cholowerera mu nkhondo m’zaka za m’ma 1900, ndipo zinaoneka kuti matchalitchiwa akuyenera kulandira chiweruzo cha mkwiyo woyaka moto wa Yehova. Akhristu odzozedwa, amene kenako anayamba kuthandizidwa ndi khamu lalikulu, akupitiriza kulengeza uthenga wogwirizana ndi kulira kwa lipenga loyamba. Uthenga umenewu ukuthandiza anthu kudziwa kuti Yehova amaona kuti Matchalitchi Achikhristu ndi oyenera kuwonongedwa.—Chivumbulutso 7:9, 15.
Ngati Phiri Loyaka Moto
21. N’chiyani chinachitika mngelo wachiwiri ataliza lipenga lake?
21 “Kenako mngelo wachiwiri analiza lipenga lake. Ndipo chinachake chokhala ngati phiri lalikulu chinaponyedwa m’nyanja chikuyaka moto. Moti gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja, linasanduka magazi. Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zamoyo zimene zili m’nyanja zinafa. Komanso gawo limodzi mwa magawo atatu a ngalawa, linasweka.” (Chivumbulutso 8:8, 9) Kodi zinthu zoopsazi zikuimira chiyani?
22, 23. (a) Kodi ndi chigamulo chiti chimene sitikukayikira kuti chinaperekedwa chifukwa cha kulira kwa lipenga lachiwiri? (b) Kodi “gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja” likuimira chiyani?
22 Tingamvetse bwino zimenezi tikaona zimene zinachitika pamsonkhano umene anthu a Yehova anachita mu 1923, pa August 18 mpaka 26, ku Los Angeles, m’chigawo cha California, m’dziko la United States. Loweruka masana, J. F. Rutherford anakamba nkhani yamutu wakuti “Nkhosa ndi Mbuzi.” M’nkhaniyi, m’baleyu anafotokoza momveka bwino kuti “nkhosa” ndi anthu olungama amene adzalandire dziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu. Kenako chigamulo chimene chinaperekedwa chinaulula chinyengo cha “atsogoleri a zipembedzo za mpatuko ndi cha ‘anthu ofunika kwambiri pa nkhosa zawo,’ omwe ndi anthu olemera m’dzikoli komanso andale otchuka.” Chigamulochi chinalimbikitsa “khamu la anthu okonda bata ndi mtendere amene ali m’matchalitchi . . . kuti achoke m’matchalitchi osalungamawa, amene Ambuye anawatchula kuti ‘Babulo,’” ndipo akonzekere “kulandira madalitso a ufumu wa Mulungu.”
23 N’zosakayikitsa kuti kulira kwa lipenga lachiwiri n’kumene kunachititsa kuti chigamulo chimenechi chiperekedwe. Anthu amene m’kupita kwa nthawi anamvera uthenga umenewu anadzipatula pagulu la anthu oipa. Yesaya anafotokoza anthu oipawa motere: “Koma anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuwinduka, imene ikukanika kukhala bata, imene madzi ake akuvundula zomera za m’nyanjamo ndiponso matope.” (Yesaya 57:20; 17:12, 13) Choncho, m’pake kuti “nyanja” ikuimira anthu okonda ziwawa ndi osamvera amene amayambitsa zipolowe ndiponso amapanga magulu ofuna kusintha zinthu. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 13:1.) Koma nthawi ikubwera pamene “nyanja” imeneyo sidzakhalaponso. (Chivumbulutso 21:1) Panopa, pamene mngelo waliza lipenga lachiwiri, Yehova akulengeza uthenga wake wachiweruzo pa gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja, limene ndi anthu osamvera amenenso ali m’Matchalitchi Achikhristu.
24. Kodi chinthu chooneka ngati phiri lalikulu loyaka moto chomwe chinaponyedwa m’nyanja chikuimira chiyani?
24 Chinthu chinachake chooneka ngati phiri lalikulu loyaka moto chinaponyedwa “m’nyanja” imeneyi. M’Baibulo, mawu akuti “phiri” nthawi zambiri amatanthauza maulamuliro. Mwachitsanzo, Baibulo limayerekezera Ufumu wa Mulungu ndi phiri. (Danieli 2:35, 44) Ufumu wa Babulo, womwe unali wowononga kwambiri, unasanduka “phiri lotenthedwa ndi moto.” (Yeremiya 51:25) Koma chinthu chooneka ngati phiri chimene Yohane anaona, chikupitirizabe kuyaka. Moyenerera, kuponyedwa kwake m’nyanja kukuimira mmene nkhani yokhudza ulamuliro inakhalira yaikulu kwambiri pakati pa anthu, makamaka m’Mayiko Achikhristu, nkhondo yoyamba yapadziko lonse ili mkati komanso itatha. Mwachitsanzo, ku Italy, Mussolini anayambitsa ulamuliro wankhanza. Nakonso ku Germany, Hitler anayambitsa ulamuliro wankhanza wa chipani chake cha Nazi, ndipo mayiko ena nawonso anayambitsa maulamuliro osiyanasiyana amene ankayendera mfundo yoti boma liziyendetsa lokha ntchito zonse zokhudza malonda. Ku Russia, zinthu zinasintha kwambiri pamene chipani cha Bolshevik chinalanda boma n’kuyambitsa ulamuliro watsopano wachikomyunizimu. Zimenezi zinachititsa kuti atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu akhale opanda mphamvu m’dziko limeneli, ngakhale kuti poyamba anali ndi mphamvu zambiri m’boma.
25. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti anthu anapitiriza kulimbana pa nkhani yokhudza ulamuliro, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha?
25 Ulamuliro wankhanza wa ku Italy ndi ku Germany unatha pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, komabe anthu anapitiriza kulimbana pa nkhani yokhudza ulamuliro. Ndipo anthu amene ali ngati nyanja anapitirizabe kuwinduka poyesetsa kukhazikitsa maulamuliro atsopano ofuna kusintha zinthu. Mwachitsanzo, patapita zaka zambiri kuchokera mu 1945, maulamuliro amenewa anakhazikitsidwa m’mayiko ambiri monga ku China, Vietnam, Cuba, ndi ku Nicaragua. Ku Greece, asilikali anayesa kukhazikitsa ulamuliro wawo wankhanza, koma zinthu sizinawayendere bwino ndipo ulamulirowo unatha. Ku Kampuchea (Cambodia), boma linkafuna kukhazikitsa ulamuliro wankhanza kuti liziyendetsa lokha ntchito zonse za malonda m’dzikolo. Zimenezi zinachititsa kuti anthu oposa mamiliyoni awiri aphedwe.
26. Kodi ‘phiri loyaka moto’ likupitiriza bwanji kuchititsa mafunde pakati pa anthu omwe ali ngati nyanja?
26 ‘Phiri loyaka moto’ limeneli likupitirizabe kuchititsa mafunde pakati pa anthu omwe ali ngati nyanja. Mavuto okhudzana ndi kulimbirana ulamuliro akuchitikabe m’mayiko ena a ku Africa kuno, ku North ndi ku South America, ku Asia ndiponso kuzilumba zina za m’nyanja ya Pacific. Nkhani yolimbirana ulamuliroyi yakula kwambiri m’Mayiko Achikhristu, kapena m’mayiko amene amishonale a Matchalitchi Achikhristu amayambitsa nkhani zofuna kusintha boma. Mwachitsanzo, m’mayiko ena ansembe achikatolika anafika mpaka polowa nawo m’magulu a zigawenga oukira boma ofuna kusintha ulamuliro. Pa nthawi yomweyomweyi, magulu a alaliki achipulotesitanti ku Central America ankalimbana ndi magulu oukira boma amene iwo ankawaona kuti “ndi ankhanza ndiponso ofunitsitsa kulanda boma.” Koma mafunde onsewa, omwe akuchitika pakati pa anthu amene ali ngati nyanja, sanathandize anthu kukhala mwa bata ndi mtendere.—Yerekezerani ndi Yesaya 25:10-12; 1 Atesalonika 5:3.
27. (a) Kodi mfundo yakuti “gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja,” linasanduka magazi ikutanthauza chiyani? (b) Kodi ‘gawo limodzi mwa magawo atatu a zamoyo za m’nyanja zinafa’ motani, nanga chidzachitike n’chiyani pa “gawo limodzi mwa magawo atatu a ngalawa”?
27 Kulira kwa lipenga lachiwiri kunasonyeza kuti anthu amene amalowerera mu nkhondo ndi m’mikangano yofuna kusintha boma m’malo mogonjera Ufumu wa Mulungu, ali ndi mlandu wamagazi. Makamaka Matchalitchi Achikhristu, omwe ndi “gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja,” afiira ngati magazi. Mulungu amaona kuti zamoyo zonse m’gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja imeneyi n’zakufa. Mabungwe awo onse ofuna kusintha zinthu amene akuyenda ngati ngalawa pa gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja adzawonongedweratu. Komabe, n’zosangalatsa kwambiri kuti anthu mamiliyoni ambiri angati nkhosa tsopano amvera chenjezo lofanana ndi kulira kwa lipenga ndipo achoka m’gulu la anthu amene adakali m’nyanja yowinduka. Nyanja imeneyi ili ndi mlandu wamagazi ndiponso imalimbikitsa anthu kuti azikonda kwambiri dziko lawo.
Nyenyezi Inagwa Kuchokera Kumwamba
28. Kodi chinachitika n’chiyani mngelo wachitatu ataliza lipenga lake?
28 “Tsopano mngelo wachitatu analiza lipenga lake. Ndipo nyenyezi yaikulu yoyaka ngati nyale inagwa kuchokera kumwamba. Inagwera pa gawo limodzi mwa magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe a madzi. Dzina la nyenyeziyo ndi Chitsamba Chowawa. Choncho gawo limodzi mwa magawo atatu a madzi linakhala lowawa, ndipo anthu ambiri anafa ndi madziwo chifukwa anali owawa.” (Chivumbulutso 8:10, 11) Apanso malemba ena a m’Baibulo angatithandize kudziwa mmene lembali likukwaniritsidwira m’tsiku la Ambuye.
29. Kodi “nyenyezi yaikulu yoyaka ngati nyale” ikuimira chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tikutero?
29 M’mitu ya m’mbuyomu, taona kale zimene nyenyezi imaimira m’mauthenga a Yesu opita kumipingo 7. M’mauthenga amenewa, nyenyezi 7 zimaimira akulu a m’mipingo.b (Chivumbulutso 1:20) “Nyenyezi,” kapena kuti akulu odzozedwa pamodzi ndi Akhristu onse odzozedwa, mwauzimu amakhala m’malo awo a kumwamba kuyambira pa nthawi imene anadindidwa chidindo ndi mzimu woyera ngati chikole chotsimikizira kuti adzalandira cholowa chawo kumwamba. (Aefeso 2:6, 7) Komabe, mtumwi Paulo anachenjeza kuti pakati pa anthu okhala ngati nyenyezi amenewa padzatuluka anthu a mpatuko ndiponso oyambitsa magawano, amene adzasocheretsa nkhosa. (Machitidwe 20:29, 30) Akulu osakhulupirikawo adzachititsa kuti pakhale mpatuko waukulu, ndipo iwo adzakhala “munthu wosamvera malamulo,” yemwe adzadzikweze kuti afanane ndi Mulungu pakati pa anthu. (2 Atesalonika 2:3, 4) Zimene Paulo anachenjezazi zinayamba kuchitika pamene atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anayamba kuonekera. M’pake kuti gulu la atsogoleri limeneli likuimiridwa ndi “nyenyezi yaikulu yoyaka ngati nyale.”
30. (a) Kodi Yesaya ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti mfumu ya ku Babulo yagwa kuchokera kumwamba? (b) Kodi mawu akuti ‘kugwa kuchokera kumwamba’ angatanthauze chiyani?
30 Yohane anaona nyenyezi imeneyi ikugwa kuchokera kumwamba. Kodi nyenyeziyo inagwa motani? Zimene zinachitikira mfumu ya ku Babulo zikutithandiza kumvetsa mmene inagwera. Yesaya analankhula mawu opita kwa mfumu imeneyi, kuti: “Wagwa kuchokera kumwamba, wonyezimirawe, iwe mwana wa m’bandakucha! Wadulidwa n’kugwera padziko lapansi, iwe amene unali kupundula mitundu.” (Yesaya 14:12) Ulosi umenewu unakwaniritsidwa pamene mzinda wa Babulo unagonjetsedwa ndi asilikali a Koresi. Ndipo mwadzidzidzi, mfumu yake yomwe inali wolamulira wamphamvu kwambiri padziko lonse, inachotsedwa pa udindowo mochititsa manyazi kwambiri. Choncho, mawu akuti ‘kugwa kuchokera kumwamba’ angatanthauze kuchotsedwa pa udindo waukulu n’kukhala munthu wonyozeka.
31. (a) Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anagwa liti kuchokera m’malo awo “akumwamba”? (b) Kodi n’chifukwa chiyani madzi amene atsogoleri a zipembedzo amapereka ali ngati “chitsamba chowawa,” ndipo anthu ambiri amene alandira madzi amenewa chawachitikira n’chiyani?
31 Anthu ena atachoka m’Chikhristu choona n’kukhala atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, anagwa kuchokera m’malo awo okwezeka “akumwamba” amene anatchulidwa ndi Paulo pa Aefeso 2:6, 7. M’malo mopereka madzi abwino a choonadi kwa anthu awo, iwo anapereka “chitsamba chowawa,” chomwe ndi ziphunzitso zabodza. Zina mwa ziphunzitso zimenezi ndi zakuti anthu oipa amakapsa kumoto, zoti kuli malo otchedwa puligatoliyo, zoti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, ndiponso zoti Mulungu analemberatu zilizonse zimene zimachitika pa moyo wa munthu. Komanso iwo anachititsa kuti anthu azimenya nkhondo m’malo mowalimbikitsa kuti akhale atumiki a Mulungu amakhalidwe abwino. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Anthu amene anakhulupirira mabodza amenewa anadyetsedwa poizoni wauzimu. Zimene zinawachitikira n’zofanana ndi zimene zinachitikira Aisiraeli osakhulupirika a m’nthawi ya Yeremiya. Ponena za Aisiraeli amenewa, Yehova anati: “Ndiwadyetsa chitsamba chowawa ndipo ndiwamwetsa madzi apoizoni. Chifukwa kuchokera mwa aneneri a ku Yerusalemu mpatuko wafalikira m’dziko lonse.”—Yeremiya 9:15; 23:15.
32. Kodi zinadziwika liti kuti Matchalitchi Achikhristu agwa mwauzimu kuchokera kumwamba, ndipo n’chiyani chinachititsa kuti kugwa kumeneko kuonekere bwino?
32 M’chaka cha 1919, zinadziwika kuti atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anagwa mwauzimu kuchokera kumwamba chifukwa sanasankhidwe kuti aziyang’anira zinthu zokhudza Ufumu. M’malomwake, kagulu kochepa ka Akhristu odzozedwa komwe kanali padziko lapansi, n’komwe kanasankhidwa kuti kagwire ntchito imeneyi. (Mateyu 24:45-47) Mu 1922, kugwa kumeneko kunaonekera bwino kwambiri pamene Akhristu odzozedwawa anayambanso ntchito yapadera youlula mosapita m’mbali chinyengo cha atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu.
33. Kodi chinyengo cha atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu chinaululidwa bwanji pamsonkhano umene unachitika m’chaka cha 1924, ku Columbus, Ohio, m’dziko la United States?
33 Mwachitsanzo, chigamulo chimene chinaperekedwa pamsonkhano wina chinaulula mosapita m’mbali chinyengo cha Matchalitchi Achikhristu. Magazini ya The Golden Age inanena kuti umenewu “unali msonkhano wofunika kwambiri wa Ophunzira Baibulo kuposa uliwonse umene unachitikapo.” Msonkhano umenewu unachitika m’chaka cha 1924, pa July 20 mpaka 27, ku Columbus, m’chigawo cha Ohio. Sitikukayikira kuti chigamulo champhamvuchi chinaperekedwa motsogoleredwa ndi mngelo amene analiza lipenga lachitatu, ndipo anthu onse amene anali pamsonkhanowo anagwirizana nacho. Kenako, mfundo za m’chigamulochi zinalembedwa m’timapepala tokwana 50 miliyoni tomwe tinagawidwa kwa anthu. Mutu wa timapepalato unali wakuti Atsogoleri a Zipembedzo Akuzengedwa Mlandu (Ecclesiastics Indicted). Kamutu kena pakapepalako kanali kakuti, “Kusiyana kwa Mbewu Yolonjezedwa ndi Mbewu ya Njoka.” Kapepalako kanaulula mosapita m’mbali chinyengo cha atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu pa nkhani ngati kudzipatsa mayina aulemu, kulolera anthu otchuka ochita za malonda ndiponso atsogoleri a ndale kukhala ndi mphamvu kwambiri m’tchalitchi, kufunitsitsa kulemekezedwa, ndiponso kukana kulalikira uthenga wa Ufumu wa Mesiya. Kapepalako kanatsindikanso mfundo yakuti Mkhristu aliyense wodzipereka anapatsidwa udindo ndi Mulungu wolengeza ‘tsiku lobwezera la Mulungu wathu ndi kutonthoza anthu onse olira.’—Yesaya 61:2.
34, 35. (a) Kuyambira pamene mngelo wachitatu anayamba kuliza lipenga lake, kodi mphamvu za atsogoleri a zipembedzo zakhudzidwa bwanji? (b) Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu ali ndi tsogolo lotani?
34 Kuyambira pamene mngelo wachitatu anayamba kuliza lipenga lake, mphamvu za atsogoleri a zipembedzo zikucheperachepera moti pofika pano, ndi atsogoleri ochepa okha amene adakali ndi mphamvu zochuluka, ngati zimene anali nazo kwa zaka zambirimbiri m’mbuyomo. Chifukwa cha ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova, anthu ambiri azindikira kuti ziphunzitso zochuluka zimene atsogoleri a zipembedzo amaphunzitsa zili ngati “chitsamba chowawa,” kapena kuti poizoni wauzimu. Komanso, m’mayiko a kumpoto kwa Ulaya, mphamvu za atsogoleri a zipembedzo zatsala pang’ono kutheratu, ndipo m’mayiko ena, boma linaika malamulo okhwima ochepetsa mphamvu zawo. Ndiponso mbiri ya atsogoleri a zipembedzo yaipa kwambiri m’mayiko achikatolika a ku Ulaya ndi ku America chifukwa cha zochita zawo zoipa pa nkhani zokhudza chuma, ndale ndiponso makhalidwe. Mphamvu zawo zipitiriza kuchepa kwambiri ndipo posachedwapa, adzawonongedwa pamodzi ndi zipembedzo zina zonse zonyenga.—Chivumbulutso 18:21; 19:2.
35 Koma Yehova apitirizabe kugwetsera miliri pa Matchalitchi Achikhristu. Mwachitsanzo, taonani zimene zinachitika mngelo wachinayi ataliza lipenga lake.
Mdima
36. Kodi chinachitika n’chiyani mngelo wachinayi ataliza lipenga lake?
36 “Ndiyeno mngelo wachinayi analiza lipenga lake. Atatero, gawo limodzi mwa magawo atatu a dzuwa linakanthidwa. Chimodzimodzinso gawo limodzi mwa magawo atatu a mwezi, ndi a nyenyezi. Zinatero kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a zimenezi lichite mdima, ndi kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a usana lisalandire kuunika, chimodzimodzinso usiku.” (Chivumbulutso 8:12) Mliri wa 9 umene unagwera Aiguputo unali mdima weniweni, osati wophiphiritsa. (Ekisodo 10:21-29) Koma kodi mdima umene Yohane anaonawu, womwe ndi wophiphiritsa, ukuimira chiyani?
37. Kodi mtumwi Petulo ndi mtumwi Paulo anafotokoza bwanji moyo wauzimu wa anthu omwe sanali mumpingo wachikhristu?
37 Mtumwi Petulo anauza okhulupirira anzake kuti iwo anali mu mdima wauzimu asanakhale Akhristu. (1 Petulo 2:9) Nayenso Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “mdima” pofotokoza moyo wauzimu wa anthu omwe sanali mumpingo wachikhristu. (Aefeso 5:8; 6:12; Akolose 1:13; 1 Atesalonika 5:4, 5) Nanga bwanji anthu a m’Matchalitchi Achikhristu omwe amati amakhulupirira Mulungu ndiponso amati analandira Yesu kukhala Mpulumutsi wawo?
38. Kodi mngelo wachinayi ataliza lipenga lake anaulula chiyani chokhudzana ndi “kuwala” kwa m’Matchalitchi Achikhristu?
38 Yesu ananena kuti Akhristu oona adzadziwika ndi zipatso zawo, ndipo anthu ambiri amene amati ndi otsatira ake adzakhala “anthu osamvera malamulo.” (Mateyu 7:15-23) Tikaona zipatso za gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko, lomwe ndi Matchalitchi Achikhristu, palibe angatsutse zoti matchalitchiwa ali mu mdima wauzimu wandiweyani. (2 Akorinto 4:4) Matchalitchiwa ali ndi mlandu waukulu chifukwa amanena kuti amatsatira Khristu. Choncho, m’pomveka kuti mngelo wachinayi alize lipenga lake n’kuulula kuti m’Matchalitchi Achikhristu mulibe “kuwala” koma muli mdima, ndipo ziphunzitso zawo ndi zachibabulo osati zachikhristu.—Maliko 13:22, 23; 2 Timoteyo 4:3, 4.
39. (a) Kodi chigamulo chimene anthu a Yehova anavomereza pamsonkhano mu 1925 chinafotokoza bwanji mfundo yakuti kuwala kwa m’Matchalitchi Achikhristu n’kwachinyengo? (b) Kodi gulu la Yehova linaululanso chiyani mu 1955?
39 Mogwirizana ndi zimene mngeloyu analengeza, chikhamu cha anthu a Mulungu chinachita msonkhano ku Indianapolis, m’chigawo cha Indiana, m’dziko la United States, pa August 29, 1925. Pamsonkhanowu, anthuwo anavomereza chigamulo chosapita m’mbali cha mutu wakuti, “Uthenga Wopatsa Chiyembekezo” (Message of Hope), ndipo anavomerezanso kuti chigamulochi chifalitsidwe m’kapepala. Kachiwirinso, timapepala toposa 50 miliyoni ta uthenga umenewu tinaperekedwa kwa anthu m’zinenero zingapo. Kapepalaka kanafotokoza kuti anthu akhala akunamizidwa ndi kuwala konyenga kwa akuluakulu a zamalonda, atsogoleri a ndale, ndi atsogoleri a zipembedzo, ndipo chifukwa cha kunamizidwako, “anthuwo ali mu mdima wandiweyani.” Kanasonyezanso kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungathandize anthu kuti “adzalandire madalitso osiyanasiyana, monga kukhala mwamtendere, kukhala ndi moyo wosasowa kanthu, kukhala ndi thanzi labwino, moyo, ufulu ndiponso chimwemwe chosatha.” Panafunika kulimba mtima kwambiri kuti kagulu kochepa ka Akhristu odzozedwa kalengeze uthenga ngati umenewu wodzudzula gulu lalikulu kwambiri la Matchalitchi Achikhristu. Koma kagulu ka Akhristuwa kakhala kakuchita zimenezi mosalekeza kuyambira kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1920 mpaka pano. Chaposachedwapa, mu 1955, chinyengo cha atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu chinaululidwanso padziko lonse kudzera m’kabuku kamutu wakuti, Kodi Ndani Amene Ali “Kuwala kwa Dziko”? Amene Ali M’Matchalitchi Achikhristu Kapena Amene Ali M’Chikhristu Choona? (Christendom or Christianity—Which One Is “the Light of the World”?) Masiku ano, chinyengo cha Matchalitchi Achikhristu chikuonekera poyera moti anthu ambiri m’dzikoli akuchita kuona okha zimenezi. Koma anthu a Yehova sanasiye kuulula kuti matchalitchi amenewa ndi ufumu wa mdima.
Chiwombankhanga Chimene Chikuuluka
40. Kodi kulira kwa malipenga anayi kwasonyeza kuti Matchalitchi Achikhristu ndi otani?
40 N’zoonadi kuti kulira kwa malipenga anayi oyambirirawa kwachititsa kuti Matchalitchi Achikhristu aonekere poyera kuti ndi omvetsa chisoni ndiponso akuchititsa kuti anthu awo adzawonongedwe. Ndipo zadziwika kuti gawo lake la “dziko” n’loyenerera kulandira chiweruzo cha Yehova. Zadziwikanso kuti maboma andale oyesa kusintha zinthu amene ali m’Mayiko Achikhristu ndi m’mayiko ena akuchititsa kuti anthu azilephera kulambira Mulungu. Kulira kwa malipengawa kwachititsanso kuti atsogoleri a zipembedzo aonekere poyera kuti anagwa kuchokera kumwamba, komanso aliyense akutha kuona bwino kuti Matchalitchi Achikhristu ali mu mdima wauzimu wandiweyani. Apa zikuonekeratu kuti Matchalitchi Achikhristu ndi amene ali mbali yoipa kwambiri ya dziko la Satanali.
41. Kodi Yohane anaona ndi kumva chiyani mngelo wachinayi atamaliza kuliza lipenga lake?
41 Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zinaululidwa? Tisanayankhe funso limeneli, mngelo wachinayi atamaliza kuliza lipenga lake, panapita kaye nthawi pang’ono mngelo wotsatira asanalize lipenga lake. Yohane anafotokoza zimene anaona pa nthawiyi, kuti: “Ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga chikuuluka pafupi m’mlengalenga, chikulankhula ndi mawu okweza kuti: ‘Tsoka, tsoka, tsoka kwa okhala padziko lapansi, chifukwa cha malipenga otsalawo, amene angelo atatuwo atsala pang’ono kuwaliza!’”—Chivumbulutso 8:13.
42. Kodi chiwombankhanga chimene chikuuluka chingaimire chiyani, ndipo chikulengeza uthenga wotani?
42 Chiwombankhanga chimauluka m’mwamba kwambiri moti anthu a m’dera lalikulu amatha kuchiona. Chili ndi maso akuthwa kwambiri ndipo chimatha kuona patali zedi. (Yobu 39:29) Chimodzi mwa zamoyo zimene zinazungulira mpando wachifumu wa Mulungu, zomwe ndi akerubi, chinali ngati chiwombankhanga chimene chikuuluka. (Chivumbulutso 4:6, 7) Sitikudziwa ngati chiwombankhanga chomwe chimaulukacho chinali kerubi ameneyu kapena mtumiki wina wa Mulungu, woona patali. Koma chiwombankhangacho chinalengeza mofuula uthenga wamphamvu wakuti: “Tsoka, tsoka, tsoka”! Choncho, anthu onse okhala padziko lapansi ayenera kukhala tcheru pamene angelo akuliza malipenga atatu otsala aja, ndipo kulira kwa lipenga lililonse kukugwirizana ndi tsoka lililonse mwa masoka atatuwa.
[Mawu a M’munsi]
a Mosiyana ndi zimenezi, lemba la Chivumbulutso 7:16 limasonyeza kuti khamu lalikulu silidzapsa ndi kutentha kwa mkwiyo wa Yehova.
b Ngakhale kuti nyenyezi 7 zimene zili m’dzanja lamanja la Yesu zikuimira oyang’anira odzozedwa a mumpingo wachikhristu, akulu ambiri m’mipingo yoposa 100,000 padziko lonse ali m’gulu la khamu lalikulu. (Chivumbulutso 1:16; 7:9) Kodi iwo ali ndi udindo wotani? Akuluwa amaikidwa ndi mzimu woyera kudzera mwa Akhristu odzozedwa, omwe ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Motero, tinganene kuti akuluwa akutsogoleredwa ndi dzanja lamanja la Yesu chifukwa iwonso ndi abusa ake aang’ono. (Yesaya 61:5, 6; Machitidwe 20:28) Iwo amathandiza “nyenyezi 7” chifukwa amatumikira kumene kulibe abale odzozedwa oyenerera.
[Tchati patsamba 139]
Madzi a M’Matchalitchi Achikhristu Anadziwika Kuti Ali Ngati Chitsamba Chowawa
Zikhulupiriro za Zimene Baibulo
Matchalitchi Achikhristu Limanenadi
Dzina la Mulungu ndi Yesu anapemphera kuti
losafunika: “Kugwiritsa dzina la Mulungu liyeretsedwe.
ntchito dzina lenileni la Petulo ananena kuti:
Mulungu mmodzi yekhayo . . . “Aliyense woitana padzina
sikoyenera ngakhale pang’ono kwa la Yehova adzapulumuka.”
anthu onse a m’Matchalitchi (Machitidwe 2:21; Yoweli 2:32;
Achikhristu.” (Mawu oyamba Mateyu 6:9; Ekisodo 6:3;
a Baibulo lachingelezi la Chivumbulutso 4:11; 15:3; 19:6)
Revised Standard Version)
Pali milungu itatu Baibulo limanena kuti Yehova
mwa Mulungu mmodzi: ndi wamkulu kuposa Yesu ndipo
“Atate ndi Mulungu, iye ndi Mulungu ndiponso
Mwana ndi Mulungu, ndiponso mutu wa Khristu.
Mzimu Woyera ndi Mulungu, (Yohane 14:28; 20:17;
komabe sikuti iwo ndi Milungu itatu 1 Akorinto 11:3)
koma ndi Mulungu mmodzi.” Mzimu woyera
(The Catholic Encyclopedia, ndi mphamvu ya Mulungu
lofalitsidwa mu 1912) yogwira ntchito.
Munthu ali ndi mzimu Munthu alibe mzimu
umene suufa: “Munthu umene suufa.
akamwalira, Munthu akamwalira,
mzimu ndi thupi saganiza kapena
lake zimasiyana. kumva chilichonse
Thupi lake . . . limawola . . . ndipo amabwerera kufumbi
Koma mzimu wa munthu suufa.” kumene anachokera.
(What Happens After Death, (Genesis 2:7; 3:19;
buku la Akatolika) Salimo 146:3, 4;
Anthu oipa akamwalira Malipiro a uchimo ndi imfa,
amakapsa kumoto: osati moyo wozunzika kumoto.
“Malinga ndi chikhulupiriro (Aroma 6:23) Anthu akufa
chachikhristu, anthu amene ali m’Manda sadziwa
amakazunzika kumoto chilichonse,
mpaka kalekale.” koma adzaukitsidwa.
(The World Book Encyclopedia, (Salimo 89:48;
lofalitsidwa mu 1987) Yohane 5:28, 29; 11:24, 25;
“Dzina lakuti Nkhoswe Wamkazi Mkhalapakati yekhayo
[mkhalapakati wamkazi] pakati pa Mulungu
limagwiritsidwa ntchito ndi anthu ndi Yesu.
ponena za Amayi Athu.” (Yohane 14:6; 1 Timoteyo 2:5;
(New Catholic Encyclopedia, Aheberi 9:15; 12:24)
lofalitsidwa mu 1967)
Makanda ayenera kubatizidwa: Anthu omwe ayenera
“Kuyambira kale kwambiri kubatizidwa ndi okhawo
Tchalitchi chakhala amene akhala ophunzira
chikupereka Sakalamenti la a Yesu ndipo aphunzitsidwa
Ubatizo kwa makanda. Mwambo kumvera malamulo ake.
umenewu sikuti wangokhala Kuti munthu ayenerere
wogwirizana ndi malamulo chabe, kubatizidwa,
koma timaphunzitsidwanso ayenerakumvetsa Mawu a
kuti ndi wofunika kwambiri kuti Mulungu ndi kusonyeza
munthu adzapulumuke.” chikhulupiriro.
(New Catholic Encyclopedia, (Mateyu 28:19, 20;
lofalitsidwa mu 1967) Luka 3:21-23;
M’matchalitchi ambiri Akhristu onse
mumakhala magulu a m’nthawi ya atumwi
awiri a anthu, anali atumiki ndipo
gulu la atsogoleri ankalalikira uthenga wabwino.
ndiponso gulu (Machitidwe 2:17, 18;
la anthu wamba. Aroma 10:10-13; 16:1)
Nthawi zambiri atsogoleriwo Mkhristu ayenera
amalandira malipiro ‘kupereka kwaulere,’ osati
chifukwa cha ntchito kumalandira malipiro.
yawo ndipo amakwezedwa (Mateyu 10:7, 8)
pamwamba pa anthu wamba Yesu analetsa mwamphamvu
popatsidwa mayina aulemu, kugwiritsira ntchito
monga akuti “Abusa,” mayina aulemu achipembedzo.
“Abambo,” kapena (Mateyu 6:2; 23:2-12;
“Abambo Mfumu.” 1 Petulo 5:1-3)
Mafano, zifaniziro, Akhristu ayenera kuthawa
ndi mitanda zimagwiritsidwa mtundu uliwonse
ntchito polambira: wa kupembedza mafano,
“Mafano a . . . Khristu, ngakhale kugwiritsira
Virigo Amayi a Mulungu, ndi ntchito mafano monga
a oyera ena ayenera . . . zinthu zongothandizira
kusungidwa m’matchalitchi polambira Mulungu.
ndi kupatsidwa ulemu (Ekisodo 20:4, 5; 1 Akorinto 10:14;
woyenerera.” 1 Yohane 5:21)
(Mfundo imene bungwe Iwo amalambira Mulungu
la Council of Trent osati ndi zinthu zooneka
linagwirizana [1545-63]) ndi maso koma motsogoleredwa
ndi mzimu ndi choonadi.
Anthu a m’matchalitchi Yesu analalikira
amaphunzitsidwa kuti kuti Ufumu wa Mulungu
Mulungu adzakwaniritsa ndi womwe udzathetse
zolinga zake kudzera mavuto onse a anthu,
mwa anthu a ndale. osati anthu a ndale.
Kadinala Spellman (Mateyu 4:23; 6:9, 10)
asanamwalire ananena kuti: Iye anakana kulowerera ndale.
“Pali njira imodzi yokha (Yohane 6:14, 15)
imene ingabweretse Ufumu wake suli mbali
mtendere . . . , njira ya dzikoli,
yaikulu imeneyi choncho otsatira akenso
ndi demokalase.” sayenera kukhala mbali ya dzikoli.
Anthu olemba nkhani (Yohane 18:36; 17:16)
amafalitsa zomwe zipembedzo Nayenso Yakobo anachenjeza
zikuchita polowerera za kuchita ubwenzi
ndale za m’dzikoli ndi dzikoli. (Yakobo 4:4)
(ngakhale kuchita nawo
zionetsero zofuna
kusintha zinthu).
Amanenanso kuti zipembedzozi
zikugwirizana ndi bungwe la
United Nations n’kumaliona
kuti ndi “chinthu chokhacho
chimene chingabweretse
mgwirizano ndi mtendere.”
[Chithunzi patsamba 132]
Zidindo 7 zitamatulidwa, malipenga 7 analizidwa
[Chithunzi patsamba 140]
“Zimene Atsogoleri a Dzikoli Ayenera Kuchita” (A Challenge to World Leaders) (1922)
Chigamulo chimenechi chinathandiza kulengeza mliri umene Yehova adzagwetsere “kudziko lapansi”
[Chithunzi patsamba 140]
“Chenjezo kwa Akhristu Onse” (A Warning to All Christians) (1923)
Chigamulo chimenechi chinathandiza polengeza kwa anthu ambiri uthenga wa chiweruzo choopsa cha Yehova pa “gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja”
[Chithunzi patsamba 141]
“Atsogoleri a Zipembedzo Akuzengedwa Mlandu” (Ecclesiastics Indicted) (1924)
Kapepala kameneka kanagawidwa kwa anthu ambiri ndipo kanathandiza anthu kudziwa kuti “nyenyezi,” yomwe ndi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, yagwa
[Chithunzi patsamba 141]
“Uthenga Wopatsa Chiyembekezo” (Message of Hope) (1925)
Chigamulo chosapita m’mbali chimenechi chinagwiritsidwa ntchito pothandiza anthu kudziwa kuti m’Matchalitchi Achikhristu mulibe kuwala kwa choonadi koma muli mdima