Mutu 22
Tsoka Loyamba Linali Dzombe
1. Kodi ndani amene ankalengeza uthenga mngelo aliyense akaliza lipenga lake, ndipo lipenga lachisanu linalengeza chiyani?
MNGELO wachisanu anakonzekera kuliza lipenga lake. Pa nthawiyi, angelo anayi anali ataliza kale malipenga awo ndipo miliri inayi inali itagwera kale pagawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansi. Gawo limeneli ndi Matchalitchi Achikhristu, ndipo Yehova amaliona kuti ndi loipa kwambiri. Kulira kwa malipengawo kunachititsa kuti matchalitchiwa aululike kuti akudwala matenda akayakaya. Mngelo aliyense ankati akaliza lipenga lake, anthu nawonso ankalengeza uthenga padziko lonse. Koma tsopano, mngelo wachisanu anali atatsala pang’ono kulengeza tsoka loyamba, lomwe linali loopsa kwambiri kuposa miliri taona ija. Tsokali linali lokhudza mliri wa dzombe lochititsa mantha. Komabe, tiyeni tikambirane kaye malemba ena amene angatithandize kumvetsa bwino mliriwu.
2. Kodi ndi buku liti la m’Baibulo limene limafotokoza mliri wa dzombe wofanana ndi umene Yohane anaona, ndipo dzombelo linakhudza bwanji Aisiraeli akale?
2 M’Baibulo, buku la Yoweli, lomwe linalembedwa m’zaka za m’ma 800 B.C.E., limafotokoza za mliri wa tizilombo. Tina mwa tizilombo timeneti tinali dzombe lofanana ndi limene Yohane anaona. (Yoweli 2:1-11, 25)a Yoweli analosera kuti dzombeli lidzasowetsa mtendere kwambiri Aisiraeli onse ampatuko, komanso lidzachititsa Ayuda, aliyense payekha, kuti alape n’kuyambanso kukondedwa ndi Yehova. (Yoweli 2:6, 12-14) Iye analoseranso kuti pa nthawiyo, Yehova adzatsanulira mzimu wake pa “chamoyo chilichonse,” ndipo zizindikiro zoopsa ndi zodabwitsa zidzachitika “tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanafike.”—Yoweli 2:11, 28-32.
Mliri wa M’nthawi ya Atumwi
3, 4. (a) Kodi ulosi wa pa Yoweli chaputala 2 unakwaniritsidwa liti, ndipo unakwaniritsidwa bwanji? (b) M’nthawi ya atumwi, kodi n’chiyani chinali ngati mliri wa dzombe, ndipo mliriwo unapitiriza kuchitika mpaka liti?
3 Ulosi wa pa Yoweli chaputala 2 unakwaniritsidwa koyamba m’nthawi ya atumwi. Pa Pentekosite mu 33 C.E., mzimu woyera unatsanulidwa pa Akhristu n’kuwadzoza ndi kuwapatsa mphamvu. Zimenezi zinawathandiza kuti alankhule “zinthu zazikulu za Mulungu” m’zinenero zambiri, ndipo chikhamu cha anthu chinasonkhana. Polankhula ndi chikhamu cha anthu odabwawo, mtumwi Petulo anagwira mawu ulosi wa pa Yoweli 2:28, 29 ndipo anafotokoza kuti zimene anthuwo ankaona zikukwaniritsa ulosiwu. (Machitidwe 2:1-21) Koma palibe umboni wosonyeza kuti pa nthawiyo panali mliri wa dzombe lenileni, lomwe linkasowetsa anthu ena mtendere ndiponso kuchititsa kuti anthu ena alape.
4 Ndiyeno kodi m’nthawi ya atumwi panali mliri wophiphiritsa? Inde, unalipo. Mliriwu unayamba chifukwa cha ntchito yolalikira, yomwe Akhristu omwe anali atangodzozedwa kumene ndi mzimu woyera, ankagwira mwakhama kwambiri.b Yehova anagwiritsa ntchito Akhristu amenewa poitana Ayuda omwe ankamvetsera uthenga wawo, kuti alape ndi kulandira madalitso ochokera kwa iye. (Machitidwe 2:38-40; 3:19) Anthu omwe analabadira analandiradi madalitso ochuluka kwambiri. Koma kwa anthu omwe sanalabadire, Akhristu a m’nthawi ya atumwi anakhala ngati mliri wa dzombe lowononga kwambiri. Kuchokera ku Yerusalemu, Akhristuwa anafalikira m’madera onse a ku Yudeya ndi ku Samariya. Posapita nthawi, anafalikira paliponse, ndipo ankasowetsa mtendere Ayuda osakhulupirira polengeza za kuuka kwa Yesu, ndiponso zinthu zina zambiri zokhudzana ndi kuukako. (Machitidwe 1:8; 4:18-20; 5:17-21, 28, 29, 40-42; 17:5, 6; 21:27-30) Mliri umenewu unapitiriza kuchitika mpaka pa “tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha” mu 70 C.E., pamene Yehova anabweretsa asilikali achiroma n’kuwononga Yerusalemu. Amene anapulumuka pa nthawiyi anali Akhristu okhawo omwe ankasonyeza chikhulupiriro poitana pa dzina la Yehova.—Yoweli 2:32; Machitidwe 2:20, 21; Miyambo 18:10.
Mliri wa Dzombe Masiku Ano
5. Kodi ulosi wa Yoweli wakhala ukukwaniritsidwa bwanji kuyambira mu 1919?
5 Zingakhale zomveka kuyembekezera kuti ulosi wa Yoweli ukwaniritsidwe komaliza m’nthawi ya mapeto ino. Ndipotu ulosiwu wakhala ukukwaniritsidwadi. Mwachitsanzo, pamsonkhano umene Ophunzira Baibulo anachita m’chaka cha 1919 pa September 1 mpaka 8, ku Cedar Point, m’chigawo cha Ohio, ku United States, zinaonekeratu kuti mzimu wa Yehova unatsanulidwa pa iwo. Zimenezi zinathandiza anthu a Yehova kuti ayambitse ntchito yapadera yolalikira padziko lonse lapansi. Pa anthu onse amene ankati ndi Akhristu, ndi Ophunzira Baibulo okhawa amene ankalalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu, wonena kuti Yesu waikidwa pampando wachifumu kumwamba. Iwo ankagwira ntchitoyi pokwaniritsa ulosi, ndipo zimenezi zinali ngati mliri wosowetsa mtendere kwambiri kwa anthu a m’Matchalitchi Achikhristu.—Mateyu 24:3-8, 14; Machitidwe 1:8.
6. (a) Kodi Yohane anaona chiyani mngelo wachisanu ataliza lipenga lake? (b) Kodi “nyenyezi” imene yatchulidwa palembali ikuimira ndani, ndipo n’chifukwa chiyani zili choncho?
6 Buku la Chivumbulutso, lomwe linalembedwa patapita zaka pafupifupi 26 Yerusalemu atawonongedwa, limafotokozanso za mliri umenewu. Kodi bukuli limawonjezera mfundo ziti pa zimene Yoweli ananena? Kuti tidziwe zimenezi, tiyeni tione zimene Yohane analemba. Iye anati: “Kenako mngelo wachisanu analiza lipenga lake. Ndipo ndinaona nyenyezi imene inagwera kudziko lapansi kuchokera kumwamba. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi wa dzenje lolowera kuphompho.” (Chivumbulutso 9:1) “Nyenyezi” imeneyi ndi yosiyana ndi nyenyezi yotchulidwa pa Chivumbulutso 8:10, yomwe Yohane anaona ikugwa. Pa nthawi ino, iye anaona “nyenyezi imene inagwera kudziko lapansi kuchokera kumwamba.” Nyenyeziyi tsopano ili ndi ntchito yapadera yoti ichite yokhudzana ndi dziko lapansili. Kodi nyenyeziyi ndi cholengedwa chauzimu kapena munthu weniweni? M’mavesi akutsogoloku, Baibulo linanena kuti yemwe ali ndi “kiyi wa dzenje lolowera kuphompho” amene watchulidwa palembali anaponya Satana “m’phompho.” (Chivumbulutso 20:1-3) Choncho, iye ayenera kuti ndi cholengedwa chauzimu champhamvu kwambiri. Pa Chivumbulutso 9:11, Yohane akutiuza kuti dzombe lili ndi ‘mfumu, yomwe ndi mngelo wa phompho.’ Mavesi awiri onsewa ayenera kuti akunena za munthu mmodzi, chifukwa n’zoonekeratu kuti mngelo yemwe ali ndi kiyi wa dzenje lolowera kuphompho uja ayeneranso kukhala mngelo wa phompho. Ndipo nyenyezi iyenera kuti ikuimira Mfumu yoikidwa ndi Yehova, popeza Akhristu odzozedwa amavomereza mngelo mmodzi yekha, yemwe ndi Yesu Khristu, kuti ndiye Mfumu.—Akolose 1:13; 1 Akorinto 15:25.
7. (a) Kodi chinachitika n’chiyani “dzenje lolowera kuphompholo” litatsegulidwa? (b) Kodi kuponyedwa “kuphompho” kumatanthauza chiyani, ndipo ndani amene anakhalamo kwa nthawi yochepa?
7 Yohane anapitiriza kufotokoza zokhudza nyenyeziyo, kuti: “Pamene inatsegula dzenje lolowera kuphompholo, utsi ngati wa m’ng’anjo yaikulu unatuluka m’dzenjemo, ndipo dzuwa ndi mpweya zinada ndi utsi wa m’dzenjewo. Mu utsiwo, munatuluka dzombe n’kubwera padziko lapansi. Dzombelo linapatsidwa ulamuliro wofanana ndi umene zinkhanira za padziko lapansi zili nawo.” (Chivumbulutso 9:2, 3) Malemba akasonyeza kuti cholengedwa chilichonse kapena munthu waponyedwa “kuphompho,” zimatanthauza kuti sangachite chilichonse, kapenanso kuti ndi wakufa. (Yerekezerani ndi Aroma 10:7; Chivumbulutso 17:8; 20:1, 3.) Chakumapeto kwa nkhondo yoyamba yapadziko lonse, gulu lochepa la abale a Yesu linakhala nthawi yochepa “m’phompho” limeneli (1918 mpaka 1919), ndipo anthu a m’gulu limeneli sankatha kuchita chilichonse mwauzimu. Koma mu 1919, pamene Yehova anatsanulira mzimu wake pa atumiki ake omwe anali atalapa, iwo anasonkhana ngati dzombe n’kuyamba kugwira mwakhama ntchito yolalikira.
8. Kodi mfundo yakuti dzombe linatulukira pamodzi ndi “utsi” wambiri ikutanthauza chiyani?
8 Monga mmene Yohane anaonera, dzombe lija linatuluka pamodzi ndi “utsi ngati wa m’ng’anjo yaikulu.”c Zinthu zangati zimenezi zinachitika mu 1919. Zinthu zinawadera Matchalitchi Achikhristu ndiponso anthu onse m’dzikoli. (Yerekezerani ndi Yoweli 2:30, 31.) Akhristu odzozedwa omwe anali ngati dzombewo atatulutsidwa m’phompho, unali umboni woti atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu agonja. Atsogoleriwa ndi omwe anakonza chiwembu chofuna kuthetseratu ntchito yolalikira za Ufumu, ndiponso amakana Ufumu wa Mulungu. Umboni wosonyeza kuti Matchalitchi Achikhristu anakutidwa ndi utsi wakuda kwambiri, unayamba kuonekera pamene gulu langati dzombelo linapatsidwa ndi Mulungu udindo wolengeza mwamphamvu uthenga wachiweruzo, ndipo gululo linayamba kuchitadi zimenezi. “Dzuwa” la Matchalitchi Achikhristu, limene likuimira mfundo yakuti iwo amaoneka ngati gulu lodziwa zinthu zauzimu molondola, linada ngati nthawi ya kadamsana. Ndipo “mpweya” unada chifukwa cha kulengezedwa kwa uthenga wachiweruzo wa Mulungu, umene unasonyeza kuti mulungu wa Matchalitchi Achikhristu ndi “wolamulira wa mpweya” wa dzikoli.—Aefeso 2:2; Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19.
Dzombe Lozunza
9. Kodi dzombeli linalandira malangizo otani omenyera nkhondo?
9 Kodi dzombeli linalandira malangizo otani omenyera nkhondo? Yohane akutiuza kuti: “Ndipo linauzidwa kuti lisawononge zomera za padziko lapansi, kapena chilichonse chobiriwira, kapena mtengo uliwonse, koma livulaze anthu okhawo amene alibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo. Dzombelo silinaloledwe kupha anthuwo, koma linauzidwa kuti liwazunze miyezi isanu. Ndipo kuzunzika kwawo kunali kofanana ndi mmene munthu amazunzikira akalumidwa ndi chinkhanira. M’masiku amenewo, anthuwo adzafunafuna imfa, koma sadzaipeza. Adzalakalaka kufa, koma imfa izidzawathawa.”—Chivumbulutso 9:4-6.
10. (a) Kodi mliriwu makamaka ukupita kwa ndani, ndipo unawakhudza bwanji? (b) Kodi anthuwo akuzunzika motani? (Onaninso mawu a m’munsi.)
10 Mliriwu sukupita choyamba kwa “zomera,” zomwe ndi anthu wamba, kapena kwa ‘mitengo ya padziko lapansi,’ yomwe ndi anthu awo otchuka. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 8:7.) Dzombelo linauzidwa kuwononga anthu okhawo amene alibe chidindo cha Mulungu pamphumi pawo. Anthuwa ndi a m’Matchalitchi Achikhristu, omwe amati anadindidwa chidindo koma zochita zawo n’zosiyana kwambiri ndi zimene amanenazi. (Aefeso 1:13, 14) Choncho, uthenga wozunza womwe dzombe la masiku anoli limalengeza, choyamba unapita kwa atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu. Atsogoleri odzikuzawa ayenera kuti anazunzika kwambiri mumtima mwawo atamva uthenga wosapita m’mbaliwu. Dzombeli linkalengeza kuti atsogoleriwo akulephera kutsogolera nkhosa zawo kupita kumwamba ndipo iwonso sadzapita kumwamba.d N’zoonadi, “munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake.”—Mateyu 15:14.
11. (a) Kodi dzombe laloledwa kuti lizunze adani a Mulungu kwa nthawi yotalika bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani tinganene kuti nthawi imeneyi si yaifupi? (b) Kodi adani a Mulungu akuzunzika mpaka pati?
11 Dzombeli linazunza anthuwo kwa miyezi isanu. Kodi tinganene kuti imeneyi ndi nthawi yochepa kwambiri? Ayi, si nthawi yochepa tikaganizira za dzombe lenileni, chifukwa dzombe limodzi limatha kukhala ndi moyo kwa miyezi isanu. Choncho, dzombe lamasiku anoli limazunza adani a Mulungu pa nthawi yonse imene lili ndi moyo. Ndipotu dzombeli limazunza kwambiri anthuwo moti amalakalaka atangofa. N’zoona kuti tilibe umboni wosonyeza kuti anthu omwe amazunzidwa ndi dzombeli anayesapo kudzipha. Koma mawu a pavesili akungotithandiza kumvetsa kuti anthuwo akuzunzika modetsa nkhawa kwambiri, mofanana ndi munthu amene akulumidwa mobwerezabwereza ndi zinkhanira. Kuzunzika kumeneku n’kofanana ndi kumene Yeremiya analosera ponena za Aisiraeli osakhulupirika omwe anagonjetsedwa ndiponso kubalalitsidwa ndi asilikali a ku Babulo. Aisiraeliwo ankaona kuti ndi bwino kufa kusiyana ndi kukhala moyo.—Yeremiya 8:3; onaninso Mlaliki 4:2, 3.
12. N’chifukwa chiyani dzombeli laloledwa kungozunza mwauzimu atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, osati kuwapha?
12 N’chifukwa chiyani dzombeli laloledwa kungozunza mwauzimu atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, osati kuwapha? Limeneli ndi tsoka loyamba limene likuulula bodza ndi chinyengo cha Matchalitchi Achikhristu, koma m’tsogolomu, pamene tsiku la Ambuye likupitirira, iwo adzaululidwa mosapita m’mbali kuti ndi akufa mwauzimu. Pa nthawi ya tsoka lachiwiri, m’pamene gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu adzaphedwe.—Chivumbulutso 1:10; 9:12, 18; 11:14.
Dzombe Lokonzekera Nkhondo
13. Kodi dzombeli linkaoneka bwanji?
13 Dzombelo linali ndi maonekedwe oopsa kwambiri. Yohane analifotokoza kuti: “Dzombelo linali kuoneka ngati mahatchi okonzekera nkhondo. Pamitu pawo panali zisoti zagolide zooneka ngati zachifumu. Nkhope zawo zinali ngati nkhope za amuna, koma tsitsi lawo linali ngati la akazi. Mano awo anali ngati a mikango. Pachifuwa pawo panali zotetezera zokhala ngati zachitsulo. Ndipo phokoso la mapiko awo linali ngati phokoso la magaleta okokedwa ndi mahatchi ambiri omwe akuthamangira kunkhondo.”—Chivumbulutso 9:7-9.
14. N’chifukwa chiyani mmene Yohane anafotokozera dzombe lija zikugwirizana ndi gulu la Akhristu, lomwe linalimbikitsidwanso mu 1919?
14 Zimenezi zikuimira bwino gulu la Akhristu okhulupirika omwe analimbikitsidwanso mu 1919. Mofanana ndi mahatchi, Akhristu odzozedwawo anakonzekera nkhondo, ndipo anali ofunitsitsa kumenyera nkhondo choonadi m’njira imene mtumwi Paulo anafotokoza. (Aefeso 6:11-13; 2 Akorinto 10:4) Yohane anaona kuti pamitu pawo panali zisoti zagolide zooneka ngati zachifumu. Sizikanakhala zoyenera kuti iwo avale zisoti zenizeni zachifumu chifukwa samayamba kulamulira adakali padziko lapansi. (1 Akorinto 4:8; Chivumbulutso 20:4) Koma mu 1919, iwo anali atayamba kale kuoneka ngati mafumu. Pa nthawiyo, anali atakhala abale a Mfumu, ndipo zisoti zawo zakumwamba zinali zitasungidwa kuti adzawapatse ngati atapitiriza kukhalabe okhulupirika mpaka mapeto.—2 Timoteyo 4:8; 1 Petulo 5:4.
15. Kodi zinthu za dzombe zotsatirazi zikuimira chiyani? (a) zodzitetezera pachifuwa zachitsulo, (b) nkhope ngati za amuna, (c) tsitsi ngati la akazi, (d) mano ngati a mikango, (e) kuchita phokoso lalikulu.
15 M’masomphenyawa, dzombe linali ndi zodzitetezera pachifuwa zachitsulo, zomwe zikuimira chilungamo chosagwedezeka. (Aefeso 6:14-18) Linalinso ndi nkhope za amuna, zomwe zikuimira chikondi, popeza munthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, yemwe ndi chikondi. (Genesis 1:26; 1 Yohane 4:16) Tsitsi lawo linali lalitali ngati la akazi, zomwe zikusonyeza bwino mfundo yoti amagonjera Mfumu yawo, imene ndi mngelo wa phompho. Ndipo mano awo anali ofanana ndi a mkango. Mkango umakhadzula nyama ndi mano ake. Kuyambira mu 1919, Akhristu odzozedwa anayambanso kudya chakudya chauzimu chotafuna, chomwe makamaka chinali choonadi chonena za Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Yesu Khristu, “Mkango wa fuko la Yuda.” Popeza mkango umaimira kulimba mtima, panafunika kulimba mtima kwambiri kuti Akhristu odzozedwawa adye ndi kugaya chakudya cholimbachi, chomwe ndi uthenga wosapita m’mbali. Panafunikanso kulimba mtima kuti alembe uthengawu m’mabuku ndi kuwafalitsa padziko lonse. Dzombe lophiphiritsali lakhala likuchita phokoso lalikulu, ngati “phokoso la magaleta okokedwa ndi mahatchi ambiri omwe akuthamangira kunkhondo.” Potsanzira chitsanzo cha Akhristu a m’nthawi ya atumwi, Akhristu odzozedwawa sanakhale chete.—1 Akorinto 11:7-15; Chivumbulutso 5:5.
16. Kodi mawu akuti dzombe lili ndi “michira ndi mbola ngati zinkhanira,” akutanthauza chiyani?
16 Pali zambiri zimene zikuchitika pogwira ntchito yolalikirayi kuwonjezera pa kulankhula mawu enieni. Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Dzombelo linali ndi michira ndi mbola ngati zinkhanira. M’michira yawoyo ndi mmene munali ulamuliro wawo wovulaza anthuwo kwa miyezi isanu.” (Chivumbulutso 9:10) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Akhristu a Mboni za Yehova akamagwira ntchito yawo yolalikira za Ufumu, polankhula mawu enieni ndiponso kugwiritsa ntchito mabuku, amapereka uthenga wamphamvu wochokera m’Mawu a Mulungu. Uthenga wawo uli ndi mbola ngati za zinkhanira chifukwa iwo amachenjeza anthu za tsiku la Yehova lobwezera adani ake limene latsala pang’ono kufika. (Yesaya 61:2) Dzombe lonse lauzimu limene lilipoli lisanafe, ntchito yomwe linapatsidwa ndi Mulungu, yolengeza uthenga wachiweruzo cha Yehova, iyenera kutha. Uthenga womwe dzombeli likulalikira umavulaza anthu onse amene amanyoza Mulungu mouma mtima.
17. (a) Kodi n’chiyani chinalengezedwa pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo mu 1919, chomwe cholinga chake chinali kuwonjezera ululu wa uthenga umene ankalalikira? (b) Kodi atsogoleri a zipembedzo akhala akuzunzidwa bwanji, ndipo iwo achita chiyani pobwezera?
17 Gulu la dzombe limeneli linasangalala kwambiri pamene magazini yatsopano, yomwe inkatchedwa kuti The Golden Age, inatulutsidwa pamsonkhano wawo mu 1919. Magaziniyi inali yoti izituluka pa milungu iwiri iliyonse ndipo cholinga chake chinali kuwonjezera ululu wa uthenga umene ankalalikira.e Magazini ya nambala 27, yomwe inatuluka pa September 29, 1920, inaulula chinyengo cha atsogoleri a zipembedzo omwe ankazunza Ophunzira Baibulo ku United States kuyambira mu 1918 mpaka mu 1919. M’zaka za m’ma 1920 ndi m’ma 1930, magazini ya The Golden Age inazunza kwambiri atsogoleri a zipembedzo. Magaziniyi inachita zimenezi potulutsa nkhani komanso zithunzi zoseketsa zojambula pamanja zimene zinkaulula chinyengo chawo polowerera ndale. Magaziniyi inkaulula makamaka chinyengo cha atsogoleri achikatolika amene anapanga mgwirizano ndi olamulira ankhanza a ku Italy ndi ku Germany. Pobwezera, atsogoleri a zipembedzo ‘anayambitsa mavuto mwa kupanga malamulo’ ndiponso ankayambitsa ziwawa zoukira anthu a Mulungu.—Salimo 94:20.
Olamulira a Dzikoli Anachenjezedwa
18. Kodi panali ntchito yotani yoti dzombe ligwire, ndipo linachita chiyani potsatira kulira kwa lipenga lachisanu?
18 Dzombe lamasiku ano linali ndi ntchito yoti ligwire. Mwachitsanzo, panafunika kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Panafunikanso kuulula chinyengo, ndiponso kufufuza nkhosa zosochera. Pamene dzombeli linkagwira ntchito zimenezi, anthu m’dzikoli anakakamizika kukhala maso n’kumamvetsera uthenga wawo. Potsatira kulira kwa malipenga a angelo aja, Akhristu odzozedwa akupitirizabe kulengeza poyera kuti Matchalitchi Achikhristu ndi oyenera kulandira chilango chokhwima cha Yehova. Potsatira kulira kwa lipenga lachisanu, uthenga wachiweruzo umenewu unatsindikidwa pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo umene unachitika mumzinda wa London ku England, pa May 25 mpaka 31, 1926. Pamsonkhanowu panaperekedwa chigamulo chakuti “Umboni kwa Olamulira a Dzikoli,” ndiponso panali nkhani ya onse yamutu wakuti, “Chifukwa Chake Maulamuliro Amphamvu Padzikoli Akugwedezeka Komanso Njira Yothetsera Mavutowa,” yomwe inakambidwa muholo yotchedwa Royal Albert. Tsiku lotsatira, mawu onse a m’chigamulochi, komanso a m’nkhaniyi anasindikizidwa m’nyuzipepala ina yotchuka kwambiri ya ku London. Kenako gulu la dzombeli linafalitsa chigamulochi padziko lonse m’timapepala tokwana 50 miliyoni, ndipo zimenezi zinazunzadi atsogoleri a zipembedzo. Patapita zaka zambiri, anthu a ku England ankasimbabe za uthenga wopweteka wa m’kapepala kameneka.
19. Kodi dzombe lophiphiritsa linalandira chida china chiti cholithandiza kumenya nkhondo, ndipo chidacho chinanenapo zotani pa chikalata cha ku London?
19 Pamsonkhano umenewu, dzombe lophiphiritsa linalandira chida china cholithandiza pomenya nkhondo. Chidachi chinali buku lachingelezi la mutu wakuti Deliverance (Kulanditsidwa). Zina mwa zinthu zimene zinali m’bukuli zinali mfundo za m’Malemba zotsimikizira kuti boma lolamuliridwa ndi ‘mwana wamwamuna,’ lomwe ndi Ufumu wakumwamba wa Khristu, linakhazikitsidwa mu 1914. (Mateyu 24:3-14; Chivumbulutso 12:1-10) Komanso bukuli linagwira mawu chikalata chimene chinafalitsidwa ku London mu 1917 ndipo chinasainidwa ndi atsogoleri 8 a zipembedzo, omwe anthu ankawaona kuti “anali m’gulu la akatswiri kwambiri padziko lonse pa nkhani ya kulalikira.” Atsogoleriwo anali a zipembedzo zina zikuluzikulu pa nthawiyo (Baptist, Congregational, Presbyterian, Episcopalian ndi Methodist). Chikalatachi chinanena kuti “mavuto amene akuchitikawa akusonyeza kuti nthawi za Akunja zafika kumapeto,” ndiponso kuti “tikuyembekezera kuti Ambuye akhoza kuonekera nthawi ina iliyonse.” N’zoonadi, atsogoleri a zipembedzowo anazindikira kuti zinthu zomwe zikuchitika m’dzikoli ndi chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu. Koma kodi iwo anachitapo chilichonse? Buku lakuti Deliverance likutiuza kuti: “Chochititsa chidwi kwambiri pa nkhaniyi n’chakuti anthu omwewo amene anasaina chikalata chija, patapita nthawi anasintha maganizo ndipo anayamba kukana umboni wotsimikizira kuti tili m’nthawi ya mapeto a dzikoli, yomwenso ndi nthawi ya kukhalapo kwachiwiri kwa Ambuye.”
20. (a) Kodi atsogoleri a zipembedzo asankha kuchita chiyani pa nkhani ya dzombe ndi Mfumu yake? (b) Kodi Yohane ananena kuti ndani amene akutsogolera gulu la dzombe, ndipo dzina lake ndani?
20 M’malo molengeza za kubwera kwa Ufumu wa Mulungu, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu asankha kukhala kumbali ya dziko la Satana. Iwo sakufuna kugwirizana ndi gulu la dzombe ndi Mfumu yake. Yohane ananena za Mfumu imeneyi kuti: “Dzombelo lili ndi mfumu. Mfumuyo ndiye mngelo wa phompho. M’Chiheberi, dzina lake ndi Abadoni [kutanthauza “Chiwonongeko”], koma m’Chigiriki ali ndi dzina lakuti Apoliyoni [kutanthauza “Wowononga”].” (Chivumbulutso 9:11) Popeza Yesu ndi “mngelo wa phompho” ndiponso “Wowononga,” iye anagwetseradi tsoka pa Matchalitchi Achikhristu, lomwe ndi miliri yowononga. Koma sikuti zinathera pomwepa ayi.
[Mawu a M’munsi]
a Yerekezerani Yoweli 2:4, 5, 7 ndi Chivumbulutso 9:7-9. Lemba la Yoweli 2:4, 5, 7 likuyerekezera dzombeli ndi mahatchi, anthu, amuna, ndiponso likusonyeza kuti dzombeli likuchita phokoso lofanana ndi la magaleta okokedwa ndi mahatchi. Yerekezeraninso Yoweli 2:6, 10 ndi Chivumbulutso 9:2, 5. Lemba la Yoweli 2:6, 10 likufotokoza ululu ndi zinthu zina zoopsa zimene anthu adzamve ndi kuona zobwera chifukwa cha dzombeli.
b Onani nkhani yakuti “Tsiku la Yehova Layandikira,” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1998.
c Lembali silingagwiritsidwe ntchito pofuna kutsimikizira kuti kuphomphoko kunali moto, ngati kuti phompholo ndi malo amene anthu ena amati anthu oipa amakapsa. Yohane ananena kuti anaona utsi wakuda kwambiri umene unali “ngati,” kapena kuti wofanana ndi utsi wa m’ng’anjo yaikulu. (Chivumbulutso 9:2) Iye sananene kuti anaona moto weniweni m’phomphomo.
d Mawu akuti “kuzunzika,” anawamasulira kuchokera kumawu enaake achigiriki (ba·sa·niʹzo), omwe nthawi zina amagwiritsidwa ntchito ponena za kuzunzidwa kwenikweni. Koma mawuwa angagwiritsidwenso ntchito ponena za kuzunzika m’maganizo. Mwachitsanzo, palemba la 2 Petulo 2:8, timawerenga za munthu wolungama Loti, kuti “anali kuzunzika” chifukwa cha zinthu zoipa zimene ankaona mu Sodomu. Nawonso atsogoleri a chipembedzo a m’nthawi ya atumwi anazunzika m’maganizo, ngakhale kuti chifukwa chimene ankazunzikira chinali chosiyana ndi cha Loti.
e Dzina la magazini imeneyi linasinthidwa mu 1937 n’kukhala Consolation (Chitonthozo), ndipo mu 1946, dzinali linasinthidwanso n’kukhala Galamukani!
[Chithunzi patsamba 143]
Kulizidwa kwa lipenga lachisanu kunabweretsa tsoka loyamba pa masoka atatu
[Chithunzi patsamba 146]
Mivi yako yakuthwa idzalasa mitima ya adani a Mfumu. (Salimo 45:5) Mawu amenewa anali pansi pa chithunzi choseketsachi, chomwe chinali chimodzi chabe pa zithunzi zambiri zomwe zinatuluka m’zaka za m’ma 1930 ndipo zinavulaza “anthu okhawo amene alibe chidindo cha Mulungu”
[Zithunzi patsamba 147]
Holo ya Royal Albert. Buku la Deliverance linatulutsidwa pamsonkhano umene unachitikira muholo imeneyi, komanso chigamulo chakuti, “Umboni kwa Olamulira a Dzikoli” chinavomerezedwa muholo yomweyi