Mutu 23
Tsoka Lachiwiri Linali Makamu a Asilikali Okwera Pamahatchi
1. Ngakhale kuti atsogoleri a zipembedzo ayesetsa kuti awononge dzombe, kodi chachitika n’chiyani, ndipo mfundo yakuti masoka enanso awiri akubwera ikusonyeza chiyani?
KUYAMBIRA mu 1919, zomwe dzombe lophiphiritsa likuchita poulula chinyengo cha Matchalitchi Achikhristu zikusautsa kwambiri atsogoleri amatchalitchiwo. Atsogoleriwo ayesetsa kuwononga dzombe limeneli koma alephera ndipo dzombeli likupitirizabe kuwasautsa kwambiri. (Chivumbulutso 9:7) Ndipo si zokhazo, chifukwa Yohane analemba kuti: “Tsoka limodzilo linapita. Koma masoka ena awiri anali kubwera pambuyo pa zimenezi.” (Chivumbulutso 9:12) Masoka enanso osowetsa mtendere anali atatsala pang’ono kugwera Matchalitchi Achikhristu.
2. (a) Kodi chinachitika n’chiyani mngelo wa 6 ataliza lipenga lake? (b) Kodi ‘mawu amodzi ochokera panyanga za paguwa lansembe lagolide’ akuimira chiyani? (c) N’chifukwa chiyani lembali latchula angelo anayi?
2 Kodi tsoka lachiwiri linachokera kuti? Yohane analemba kuti: “Kenako mngelo wa 6 analiza lipenga lake. Ndipo ndinamva mawu amodzi kuchokera panyanga za paguwa lansembe lagolide lokhala pamaso pa Mulungu. Mawuwo anauza mngelo wa 6 amene anali ndi lipengayo kuti: ‘Masula angelo anayi omangidwa amene ali kumtsinje waukulu wa Firate.’” (Chivumbulutso 9:13, 14) Angelowo anamasulidwa potsatira mawu amene anamveka kuchokera panyanga za paguwa lansembe lagolide. Guwa lansembe lagolideli ndi guwa la nsembe zofukiza, ndipo taona kawiri konse m’mbuyomu kuti zofukiza zimene zili m’mbale zagolide za paguwali, zikuimira mapemphero a oyera. (Chivumbulutso 5:8; 8:3, 4) Choncho mawu amodzi amenewa akuimira mapemphero a oyera onse padziko lapansi. Iwo amapempha Yehova kuti awapulumutse n’cholinga choti apitirize kugwira ntchito mwamphamvu monga “amithenga” ake. Ndipotu mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “angelo” palembali amatanthauza kuti “amithenga.” Nanga n’chifukwa chiyani pali angelo anayi? Zikuoneka kuti nambala yophiphiritsayi ikusonyeza kuti angelowa adzachita zinthu mwadongosolo kwambiri ndipo adzafika paliponse padziko lapansili.—Chivumbulutso 7:1; 20:8.
3. Kodi angelo anayi ‘anamangidwa motani kumtsinje waukulu wa Firate’?
3 Kodi angelo amenewo ‘anamangidwa motani kumtsinje waukulu wa Firate’? Kalelo mtsinje wa Firate unali malire akumpoto chakum’mawa a dziko limene Yehova analonjeza Abulahamu. (Genesis 15:18; Deuteronomo 11:24) Zikuoneka kuti angelowa anamangidwa kuti asadutse m’malire a dziko limene Mulungu anawapatsa, kapena kuti malo awo ogwirira ntchito padziko lapansi. Iwo analepheretsedwa kuchita mokwanira utumiki umene Yehova anawapatsa. Mtsinje wa Firate unadutsa m’mphepete mwa mzinda wa Babulo, ndipo mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E., Aisiraeli anakhala akapolo mumzinda umenewu kwa zaka 70, ali “omangidwa . . . kumtsinje waukulu wa Firate.” (Salimo 137:1) Pamene chaka cha 1919 chinkafika, n’kuti Aisiraeli auzimu nawonso ali omangidwa komanso ali achisoni ndipo ankapempha Yehova kuti awatsogolere.
4. Kodi angelo anayiwa ali ndi ntchito yotani, ndipo akuchita chiyani pokwaniritsa ntchitoyi?
4 N’zosangalatsa kuti kenako Yohane ananena kuti: “Angelo anayiwo anamasulidwa. Iwo anali okonzekera kuti pa ola, tsiku, mwezi, ndi chaka chimenecho, aphe gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu.” (Chivumbulutso 9:15) Yehova amasunga nthawi kwambiri. Zinthu zonse zimene akufuna kuchita anazipatsa nthawi yoti azichitire ndipo amazichitadi pa nthawi yake. Choncho amithenga amenewa anamasulidwa pa nthawi yoyenera kuti agwire ntchito imene anafunika kugwira. M’pake kuti iwo anasangalala kwambiri atamasulidwa mu ukapolo mu 1919, ndipo anali okonzeka kugwira ntchito yawo. Iwo sankafunikira kungozunza chabe “gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu,” koma ankafunikiranso kuti pamapeto pake “aphe gawo” limeneli. Izi zikugwirizana ndi miliri imene inachitika angelo ataliza malipenga anayi oyambirira aja. Miliri yoyamba ija inagwera pa gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansi, a nyanja ndiponso a zamoyo za m’nyanja. Inagweranso pa gawo limodzi mwa magawo atatu a akasupe a madzi, a mitsinje komanso a dzuwa, mwezi ndi nyenyezi. (Chivumbulutso 8:7-12) Koma angelo anayiwa anachita zambiri. Iwo ‘anapha,’ kutanthauza kuti anaulula mosapita m’mbali kuti Matchalitchi Achikhristu ndi akufa mwauzimu. Iwo akhala akuchita zimenezi kudzera m’mauthenga achiweruzo amene akhala akulengeza kuyambira mu 1922 mpaka pano.
5. Kodi lipenga la 6 lokhudza Matchalitchi Achikhristu linalira bwanji mu 1927?
5 Kumbukirani kuti mngelo wakumwamba uja anali atangoliza kumene lipenga la 6. Potsatira kulira kwa lipengali, msonkhano wa nambala 6 pa misonkhano yamayiko imene Ophunzira Baibulo ankachita chaka chilichonse, unachitikira mumzinda wa Toronto, ku Ontario, m’dziko la Canada. Nkhani zimene zinakambidwa Lamlungu pa July 24, 1927 zinaulutsidwa m’nyumba 53 zoulutsira mawu pa nthawi imodzi ndipo zoterezi zinali zisanachitikepo n’kale lonse. N’kutheka kuti anthu mamiliyoni ambirimbiri anamvetsera uthenga umenewo. Choyamba, chigamulo champhamvu chinanena mosapita m’mbali kuti Matchalitchi Achikhristu ndi akufa mwauzimu, ndipo kenako anthu anapemphedwa kuti: “M’nthawi yachisokonezo ino, Yehova Mulungu akupempha anthu onse kuti atuluke ‘m’Matchalitchi Achikhristu’ ndi kuwasiyiratu . . . ; [ndipo] anthuwo adzipereke ndi mtima wonse kwa Yehova Mulungu, kwa Mfumu imene iye waisankha ndiponso ku ufumu wake.” Nkhani ya onse imene inakambidwa pambuyo pa chigamulochi inali ndi mutu wakuti “Ufulu kwa Anthu Onse.” Monga mwa nthawi zonse, M’bale J. F. Rutherford anakamba nkhani imeneyi mogwira mtima kwambiri, ndipo zimenezi zinali ngati “moto, utsi, ndi sulufule” zimene kenako Yohane anaona m’masomphenyawa.
6. Kodi Yohane anawafotokoza bwanji makamu a asilikali okwera pamahatchi amene iye anaona?
6 “Ndipo chiwerengero cha makamu a asilikali okwera pamahatchi, chinali miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda. Chimenechi ndicho chiwerengero chawo chimene ndinamva. Mahatchi ndi okwerapowo ndinawaona motere m’masomphenyawo: Anavala zoteteza pachifuwa zofiira ngati moto, zobiriwira ngati mwala wa huwakinto, ndi zachikasu ngati sulufule. Mitu ya mahatchiwo inali ngati mitu ya mikango, ndipo m’kamwa mwawo munali kutuluka moto, utsi, ndi sulufule. M’kamwa mwawomo munalinso kutuluka miliri itatu iyi: Moto, utsi, ndi sulufule. Gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu anaphedwa.”—Chivumbulutso 9:16-18.
7, 8. (a) Kodi makamu a asilikali okwera pamahatchi amene akuthamanga ndipo akuchita phokoso kwambiri, akutsogoleredwa ndi ndani? (b) Kodi makamu a asilikali okwera pamahatchi akufanana bwanji ndi dzombe limene takambirana kale lija?
7 Zikuoneka kuti makamu a asilikali okwera pamahatchiwo ankathamanga akuchita phokoso kwambiri ndipo ankatsogoleredwa ndi angelo anayi aja. Zimenezitu zinali zochititsa mantha kwambiri. Kodi mukanatani zikanakhala kuti makamu a asilikali okwera pamahatchiwo akuthamangitsa inuyo? Mukanachita mantha kwambiri ngakhale ndi maonekedwe awo okha. Koma kodi mwaona kuti makamu a asilikali okwera pamahatchiwa akufanana ndi dzombe limene takambirana kale lija? Dzombe lija linkaoneka ngati mahatchi ndipo makamu a asilikaliwa anakwera pamahatchi. Zimenezi zikusonyeza kuti dzombe komanso makamu a asilikaliwa, akumenya nkhondo ya Mulungu. (Miyambo 21:31) Dzombe lija linali ndi mano ngati a mikango, ndipo mahatchi a asilikaliwo analinso ndi mitu ngati ya mikango. Choncho magulu onse awiriwa akuchita zinthu mogwirizana ndi Yesu Khristu, yemwe ndi Mkango wolimba mtima wa fuko la Yuda. Iye ndi Mtsogoleri wawo, mkulu wa gulu lawo lankhondo, komanso Chitsanzo chawo.—Chivumbulutso 5:5; Miyambo 28:1.
8 Dzombe komanso makamu a asilikali okwera pamahatchiwo akugwira ntchito ya Yehova yopereka chiweruzo. Mwachitsanzo, dzombeli linatuluka mu utsi umene ukuimira tsoka ndiponso moto wowononga Matchalitchi Achikhristu, ndipo m’kamwa mwa mahatchiwo munkatuluka moto, utsi ndi sulufule. Dzombeli linali ndi chodzitetezera pachifuwa chachitsulo, kutanthauza kuti mitima yawo inali yotetezedwa chifukwa chakuti sankalola chilichonse kuwalepheretsa kuchita chilungamo. Asilikali okwera pamahatchiwo nawonso anavala zodzitetezera pachifuwa ndipo chodzitetezera pachifuwa chilichonse chinali ndi mtundu wofiira ngati moto, wobiriwira ngati utsi ndi wachikasu ngati sulufule, zomwe zikuimira uthenga wa chiweruzo choopsa umene ukutuluka m’kamwa mwa mahatchiwo. (Yerekezerani ndi Genesis 19:24, 28; Luka 17:29, 30.) Komanso dzombe lija linali ndi michira ngati ya zinkhanira imene linkagwiritsa ntchito poluma ndi kuzunza adani awo, koma mahatchiwo anali ndi michira ngati njoka imene ankagwiritsa ntchito poluma ndi kupha adani awo. Zikuoneka kuti makamu a asilikali okwera pamahatchiwa anapitiriza kugwira mwakhama ndi kumalizitsa ntchito imene dzombe lija linayamba.
9. Kodi makamu a asilikali okwera pamahatchi akuimira chiyani?
9 Nanga kodi makamu a asilikali okwera pamahatchi akuimira chiyani? Akhristu odzozedwa anayambitsa ntchito yolengeza za chilango chimene Yehova adzapereke pa Matchalitchi Achikhristu, yomwe inali ngati kulira kwa malipenga ndipo iwo anali ndi ulamuliro ‘woluma ndi kuvulaza’ anthu a m’matchalitchiwo. Choncho, tingayembekezere kuti gulu lomweli lingagwiritsidwenso ntchito ‘pakupha,’ kapena kuti polengeza mosapita m’mbali kuti Matchalitchi Achikhristu ndi atsogoleri awo, anaferatu mwauzimu, Yehova anawakana ndipo posachedwapa aponyedwa “m’ng’anjo yamoto,” kutanthauza kuti adzawonongedweratu. Zoonadi, Babulo Wamkulu yense ayenera kuwonongedwa. (Chivumbulutso 9:5, 10; 18:2, 8; Mateyu 13:41-43) Koma Babulo Wamkulu ameneyu asanawonongedwe, Akhristu odzozedwa akugwiritsa ntchito “lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu,” popereka umboni wosonyeza kuti Matchalitchi Achikhristu ndi akufa mwauzimu. Angelo anayi aja komanso okwera pamahatchiwo akutsogolera pa ntchito ya kupha mophiphiritsa “gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu.” (Aefeso 6:17; Chivumbulutso 9:15, 18) Zimenezi zikusonyeza kuti ntchito imeneyi ikuchitika mwadongosolo komanso motsogoleredwa ndi Mulungu, ndipo Ambuye Yesu Khristu ndi amene akuyang’anira gulu lochititsa mantha limeneli la olengeza Ufumu, lomwe likuthamanga kupita kukamenya nkhondo.
Miyanda Iwiri Kuchulukitsa ndi Miyanda
10. Kodi zikutheka bwanji kuti asilikali okwera pamahatchi akhale okwana miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda?
10 Kodi zikutheka bwanji kuti asilikali okwera pamahatchi akhale okwana miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda? Mwanda umodzi ndi 10,000, choncho miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda ikukwana 200 miliyoni.a N’zosangalatsa kuti tsopano pali anthu mamiliyoni ambiri amene akulengeza Ufumu, koma chiwerengero chawo sichikufika 200 miliyoni. Koma kumbukirani zimene Mose ananena pa Numeri 10:36. Iye anati: “Bwererani inu Yehova, kumiyandamiyanda yosawerengeka ya Aisiraeli.” (Yerekezerani ndi Genesis 24:60.) Komabe, m’nthawi ya Mose Aisiraeli analipo pafupifupi mamiliyoni awiri kapena atatu okha. Nanga Mose ankatanthauza chiyani pamenepa? Sitikukayikira kuti iye ankakumbukira kuti Aisiraeli adzachuluka ngati “nyenyezi zakumwamba, monganso mchenga wa m’mphepete mwa nyanja,” kutanthauza kuti adzakhala osawerengeka. (Genesis 22:17; 1 Mbiri 27:23) Choncho iye anagwiritsa ntchito mawu akuti ‘miyandamiyanda’ posonyeza chiwerengero chachikulu chosadziwika. N’chifukwa chake Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu linamasulira vesili kuti: “Bwerani Yehova kwa zikwi zikwi za Israyeli.” Zimenezi zikugwirizana ndi tanthauzo lachiwiri la mawu akuti “mwanda” m’mabuku ena otanthauzira mawu achigiriki ndi achiheberi. Mabukuwa amati mawuwa amatanthauza: “Khamu losawerengeka,” kapena “chikhamu.”—The New Thayer’s Greek-English Lexicon of the New Testament; Gesenius’ A Hebrew and English Lexicon of the Old Testament, lomasuliridwa ndi Edward Robinson.
11. Kodi chinafunika n’chiyani kuti Akhristu odzozedwa akwane miyandamiyanda ngakhale mophiphiritsa?
11 Komabe, Akhristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi pano angopitirira pang’ono 11,000, kungoposa pang’ono mwanda umodzi. Nanga n’chifukwa chiyani akuwayerekezera ndi makamu a asilikali okwera pamahatchi masauzande osawerengeka? Kuti chiwerengero chawo chifikedi miyandamiyanda ngakhale mophiphiritsa, iwo angafunikire ena owathandiza. Ndipo Yehova, mwa kukoma mtima kwake kwakukulu, anapatsa odzozedwawo anthu oti awathandize. Kodi anthu amenewa anachokera kuti?
12, 13. Kodi ndi zinthu zosaiwalika ziti zimene zinachitika kuyambira mu 1918 mpaka mu 1935 zimene zinasonyeza kuti pali anthu ena othandizira Akhristu odzozedwa?
12 Kuyambira m’chaka cha 1918 mpaka mu 1922, Akhristu odzozedwa anayamba kulimbikitsa anthu osautsika powauza nkhani yosangalatsa yakuti “anthu mamiliyoni ambiri amene ali ndi moyo sadzafa.” Mu 1923 zinadziwika kuti nkhosa zotchulidwa pa Mateyu 25:31-34, zidzalandira moyo wosatha padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu. Kabuku kakuti “Ufulu kwa Anthu Onse” (Freedom for the Peoples), kamene kanatuluka pamsonkhano wamayiko mu 1927, kanafotokozanso za chiyembekezo chimenechi. Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, Akhristu amene anali okhulupirika ngati Yehonadabu, komanso anthu onse amene “akuusa moyo ndi kubuula” chifukwa cha kufa mwauzimu kwa Matchalitchi Achikhristu, anadziwika kuti ali m’gulu la nkhosa zophiphiritsa zimenezi, zomwe zikuyembekezera kudzalandira moyo wosatha padziko lapansi pompano. (Ezekieli 9:4; 2 Mafumu 10:15, 16) Polimbikitsa anthu amenewa kuti athawire ‘kumizinda yothawirako’ yamasiku ano, Nsanja ya Olonda yachingelezi ya August 15, 1934, inati: “Anthu onse amene ali ngati Yonadabu amva kulira kwa lipenga la Mulungu ndipo amvera chenjezo ndi kuthawira m’gulu la Mulungu. Iwo akugwirizana ndi anthu a Mulungu ndipo ayenera kukhalabe m’gulu limeneli.”—Numeri 35:6.
13 Mu 1935 anthu ofanana ndi Yonadabu amenewa anaitanidwa kuti akakhale nawo pamsonkhano wa Mboni za Yehova umene unachitikira ku Washington, D.C., m’dziko la United States. Lachisanu pa May 31, J. F. Rutherford anakamba nkhani yake yosaiwalika ya mutu wakuti “Khamu Lalikulu.” M’nkhani imeneyi, iye anasonyeza bwino kwambiri kuti khamu lalikulu lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9 n’chimodzimodzi ndi nkhosa zotchulidwa pa Mateyu 25:33. Iye ananena kuti anthu amenewa ndi odzipereka kwa Mulungu ndipo akuyembekezera kudzalandira moyo wosatha padziko lapansi pompano. Posonyeza kuti khamu lalikulu layamba kusonkhanitsidwa, pamsonkhano womwewo anthu okwana 840 anabatizidwa n’kukhala Mboni zatsopano, ndipo ambiri mwa anthuwa anali a khamuli.b
14. Kodi khamu lalikulu likuthamanga nawo m’gulu la asilikali ophiphiritsa okwera pamahatchi? Nanga kodi gulu la asilikali limeneli linavomereza chiyani mu 1963?
14 Kodi anthu a m’khamu lalikuluwa ali nawo m’gulu la asilikali okwera pamahatchi limene linayamba kuthamanga mu 1922, limenenso linadziwika bwino kwambiri pamsonkhano wa ku Toronto mu 1927? Inde ali nawo, ndipo akutsogoleredwa ndi angelo anayi, omwe akuimira Akhristu odzozedwa. Anthu a m’khamu lalikulu anagwirizana ndi Akhristu odzozedwa povomereza chigamulo cholimbikitsa chimene chinaperekedwa pamsonkhano wakuti “Uthenga Wabwino Wosatha,” umene unachitika padziko lonse mu 1963. Chigamulo chimenechi chinanena kuti posachedwapa dzikoli “ligwedezeka ndi chivomezi cha mavuto apadziko lonse amene sanachitikepo n’kale lonse. Ndipo magulu onse andale komanso zipembedzo zonse, zomwe ndi Babulo wamasiku ano, ziwonongedwa.” Onse pamsonkhanowo anagwirizana ndi mfundo imene inali m’chigamulocho, yakuti “tipitiriza kulalikira kwa anthu amitundu yonse mopanda tsankho ‘uthenga wabwino wosatha’ wonena za Ufumu wa Mulungu, womwe wolamulira wake ndi Mesiya. Uthengawu ndi wonenanso za ziweruzo zake zimene zili ngati miliri imene idzagwere adani ake. Miliriyi idzaperekedwa pofuna kupulumutsa anthu onse amene akufuna kulambira Mulungu m’njira yoyenerera, yemwe ndi Mlengi, motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” Anthu 454,977 amene anafika pa misonkhano yokwana 24 imene inachitika padziko lonse, anavomereza chigamulo chimenechi mosangalala, ndipo anthu oposa 95 pa anthu 100 alionse mwa anthu amenewa anali a khamu lalikulu.
15. (a) Pa anthu onse amene Yehova anawagwiritsa ntchito mu utumiki mu 2010, kodi a khamu lalikulu analipo ochuluka bwanji? (b) Kodi pemphero la Yesu la pa Yohane 17:20, 21 limasonyeza bwanji mgwirizano umene uli pakati pa a khamu lalikulu ndi Akhristu odzozedwa?
15 Khamu lalikulu likupitiriza kugwirizana kwambiri ndi Akhristu odzozedwa pogwetsera miliri pa Matchalitchi Achikhristu. Pa anthu 7,224,930 amene Yehova anawagwiritsa ntchito yolalikira mu 2010, anthu 7,213,728 anali a khamu lalikulu. Ndi mtima wonse, a khamu lalikuluwa akugwirizana ndi Akhristu odzozedwa amene Yesu anawapempherera pa Yohane 17:20, 21 kuti: “Sindikupemphera awa okha, komanso amene amakhulupirira ine kudzera m’mawu awo, kuti onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana, kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife, ndi kuti dziko likhulupirire kuti inu munanditumadi.” Akhristu odzozedwa akutsogoleredwa ndi Yesu, ndipo nawonso akutsogolera a khamu lalikulu amene akugwira nawo mwakhama ntchito yowononga kwambiri mophiphiritsa imene sinachitikepo n’kale lonse. Ndipo onsewa akugwira ntchito imeneyi ngati asilikali okwera pamahatchi aja.c
16. (a) Kodi Yohane anafotokoza kuti pakamwa ndi michira ya mahatchi ophiphiritsa zinali zotani? (b) Kodi Yehova wachita chiyani pothandiza atumiki ake kuti m’kamwa mwawo mukonzekere kuchita utumiki? (c) Kodi mfundo yakuti “michira yawo inali ngati njoka” ikutanthauza chiyani?
16 Asilikali okwera pamahatchiwa ankafunikira zida zomenyera nkhondo. Ndipo n’zosangalatsa kuti Yehova wapereka zida zimenezi. Yohane anafotokoza kuti: “Ulamuliro wa mahatchiwo unali m’kamwa mwawo ndi m’michira yawo, pakuti michira yawo inali ngati njoka, ndipo inali ndi mitu. Zinthu zimenezi anali kuwononga nazo anthu.” (Chivumbulutso 9:19) Yehova wasankha atumiki ake odzipereka ndi obatizidwa kuti agwire ntchito imeneyi. Kudzera mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, m’misonkhano ina ya mpingo ndi m’sukulu zina, Yehova waphunzitsa atumiki amenewa mmene angalalikirire mawu ake, kuti azitha kulankhula mwaluso ndi “lilime la anthu ophunzitsidwa bwino.” Iye waika mawu ake m’kamwa mwawo n’kuwatumiza kuti akalengeze za chiweruzo chake “poyera komanso kunyumba ndi nyumba.” (2 Timoteyo 4:2; Yesaya 50:4; 61:2; Yeremiya 1:9, 10; Machitidwe 20:20) Kwa zaka zambiri, Akhristu odzozedwa komanso a khamu lalikulu akhala akusiyira anthu uthenga woluma mopweteka kwambiri, wofanana ndi “michira.” Iwo akhala akufalitsa uthenga umenewu kudzera m’Mabaibulo ambirimbiri, m’mabuku, m’magazini ndiponso m’timabuku. Anthu amene akuchenjezedwa kuti Yehova ‘adzawawononga,’ amaona ngati kuti asilikali okwera pamahatchiwa alipodi miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda.—Yerekezerani ndi Yoweli 2:4-6.
17. Kodi Akhristu a Mboni za Yehova amene ali m’mayiko omwe ntchito yathu ndi yoletsedwa ndipo sangagawire anthu mabuku athu, akuthamanga nawo pagulu la asilikali okwera pamahatchi? Fotokozani.
17 Gulu la anthu akhama kwambiri pa asilikali okwera pamahatchiwa ndi la abale amene ali m’mayiko omwe Mboni za Yehova n’zoletsedwa. Koma popeza kuti iwo ali ngati nkhosa pakati pa mimbulu, ayenera kukhala “ochenjera ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.” Chifukwa chakuti amamvera Yehova, sangasiye kulankhula za zinthu zimene anaona ndi kumva. (Mateyu 10:16; Machitidwe 4:19, 20; 5:28, 29, 32) Koma kodi tinganene kuti iwo sakuthamanga nawo m’gulu la asilikali okwera pamahatchili chifukwa chakuti alibiretu mabuku oti azifalitsa kapena ali ndi ochepa chabe? Ayi si choncho. Yehova anawapatsa pakamwa ndi ulamuliro kuti athe kufalitsa choonadi cha m’Baibulo. Iwo amachita zimenezi polalikira mwamwayi ndiponso mogwira mtima moti amayambitsa maphunziro a Baibulo ndipo “akuthandiza anthu ambiri kukhala olungama.” (Danieli 12:3) Ngakhale kuti iwo sangasiyire anthu mabuku okhala ndi uthenga wosapita m’mbali, amene ali ngati michira yoluma mopweteka, mophiphiritsa m’kamwa mawo mumatuluka moto, utsi ndi sulufule. Izi zimachitika akamalalikira mosamala kwambiri komanso mochenjera za tsiku limene layandikira kwambiri pamene anthu onse adzadziwe kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.
18. Kodi mabuku athu asindikizidwa m’zinenero zingati, ndipo gulu la asilikali okwera pamahatchi lafalitsa mabuku ochuluka bwanji amene ali ndi uthenga wopweteka ngati mliri?
18 M’mayiko ena, mabuku onena za Ufumu akupitiriza kuvulaza mophiphiritsa Matchalitchi Achikhristu poulula kuti ziphunzitso komanso zochita zawo n’zachibabulo. Pogwiritsa ntchito njira zamakono zosindikizira mabuku, kwa zaka 73 chaka cha 2010 chisanafike, khamu lalikulu limeneli la asilikali okwera pamahatchi, lakhala likusindikiza Mabaibulo, timabuku, magazini ndi mabuku mabiliyoni ambirimbiri m’zinenero zoposa 500. Chiwerengero cha zofalitsa zimenezi n’chachikulu kwambiri kuposa chiwerengero chenicheni cha miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda. Zoonadi, zofalitsa zimenezi, zomwe zili ngati michira, zaluma anthu ndi kuwapweteka kwambiri.
19, 20. (a) Ngakhale kuti uthenga wopweteka ngati miliri kwenikweni ukupita ku Matchalitchi Achikhristu, kodi anthu ena m’mayiko omwe si achikhristu achita chiyani? (b) Kodi Yohane anafotokoza kuti anthu ena onse akupitiriza kuchita chiyani ngakhale kuti amva uthengawo?
19 Cholinga cha Yehova n’chakuti uthenga wake umene uli ngati miliri uphe “gawo limodzi mwa magawo atatu a anthu.” Choncho uthengawu kwenikweni ukupita ku Matchalitchi Achikhristu. Komabe uthengawu wafikanso m’mayiko amene kulibe Matchalitchi Achikhristu, komanso kumayiko ambiri kumene anthu akudziwa bwino za chinyengo cha matchalitchiwa. Kodi anthu a m’mayiko amenewa ayandikira Yehova chifukwa choona kuti miliri yagwera Matchalitchi Achikhristu achinyengowo? Anthu ochuluka achitadi zimenezi. Anthu ambiri ofatsa komanso a mitima yabwino, amene akukhala m’mayiko omwe si achikhristu, akulabadira uthenga wabwino. Koma ponena za anthu ena onse, Yohane anafotokoza kuti: “Koma anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi, sanalape ntchito za manja awo. Sanalape kulambira ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala, ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva, kapena kuyenda. Iwo sanalape ntchito zawo zopha anthu, zamizimu, dama lawo, ngakhalenso umbava wawo.” (Chivumbulutso 9:20, 21) N’zosatheka kuti padziko lonse anthu osalapa ngati amenewo asinthe n’kuyamba kulambira Yehova. Anthu onse amene akupitirizabe kuchita zinthu zoipa adzalandira chilango choopsa cha Yehova pa tsiku lake lalikulu limene anthu onse adzadziwe kuti iye ndiye woyenera kulamulira. Komabe “aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Yoweli 2:32; Salimo 145:20; Machitidwe 2:20, 21.
20 Zimene takambiranazi ndi mbali chabe ya tsoka lachiwiri. Pali zinanso zimene zikuyenera kuchitika tsoka limeneli lisanathe, ndipo tiona zimenezo m’mitu yotsatirayi.
[Mawu a M’munsi]
a Buku lina lothirira ndemanga pa buku la Chivumbulutso, linanenapo za chiwerengero chimenechi cha “miyanda iwiri kuchulukitsa ndi miyanda” kuti: “Kukula kwa manambala amenewa kukutisonyeza kuti ayenera kukhala ophiphiritsa, osati enieni, ndipo zimene zafotokozedwa pambuyo pa manambala amenewa zikugwirizana ndi mfundo imeneyi.”—Commentary on Revelation lolembedwa ndi Henry Barclay Swete.
b Onani mutu 20, tsamba 119 mpaka 126 m’buku lino. Onaninso voliyumu yachitatu ya buku la Vindication, tsamba 83 mpaka 84. Bukuli linafalitsidwa ndi Mboni za Yehova mu 1932.
c Mosiyana ndi dzombe lija, makamu a asilikali okwera pamahatchi amene Yohane anaona, sanavale “zisoti zagolide zooneka ngati zachifumu.” (Chivumbulutso 9:7) Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yakuti a khamu lalikulu, amene akupanga mbali yaikulu ya gulu la asilikali okwera pamahatchi, sakuyembekezera kukalamulira kumwamba mu Ufumu wa Mulungu.
[Chithunzi patsamba 149]
Mngelo ataliza lipenga la 6 kunabwera tsoka lachiwiri
[Zithunzi pamasamba 150, 151]
Angelo anayi akutsogolera khamu lalikulu kwambiri m’mbiri yonse la asilikali okwera pamahatchi amene akuthamanga
[Zithunzi patsamba 153]
Asilikali osawerengeka okwera pamahatchi afalitsa mabuku mamiliyoni osawerengeka ofotokoza nkhani za m’Baibulo
[Zithunzi patsamba 154]
Anthu ena onse sanalape