Mutu 26
Mapeto Osangalatsa a Chinsinsi Chopatulika cha Mulungu
1. (a) Kodi Yohane anatiuza motani za kuthetsedwa kwa chinsinsi chopatulika? (b) N’chifukwa chiyani khamu la angelo linalankhula mokweza mawu?
KODI mukukumbukira mawu amene mngelo wamphamvu uja analengeza mochita kulumbira, omwe akupezeka pa Chivumbulutso 10:1, 6, 7? Iye anati: “Sipakhalanso kuchedwa ayi. Koma m’masiku oliza lipenga la mngelo wa 7, mngeloyo atatsala pang’ono kuliza lipenga lake, ndithu chinsinsi chopatulika cha Mulungu chidzathetsedwa, malinga ndi uthenga wabwino umene anaulengeza kwa akapolo ake, aneneri.” Nthawi ya Yehova yoti lipenga lomalizalo lilizidwe inali itakwana. Nanga kodi chinsinsi chopatulika chinathetsedwa bwanji? Yohane anasangalala kwambiri kutiuza mmene chinathetsedwera. Iye analemba kuti: “Mngelo wa 7 analiza lipenga lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: ‘Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake. Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.’” (Chivumbulutso 11:15) Panali zifukwa zomveka zimene zinachititsa khamu la angelowo kulankhula mokweza mawu ngati kulira kwa mabingu. Uthenga umene angelowo analengeza ndi wofunika kwambiri m’chilengedwe chonse chifukwa ukukhudza zolengedwa zonse zamoyo.
2. Kodi mapeto osangalatsa a chinsinsi chopatulika anafika liti, ndipo anafika bwanji?
2 Tsopano mapeto osangalatsa a chinsinsi chopatulika anafika. Mapeto a chinsinsi chopatulikachi anali aulemerero, ochititsa chidwi kwambiri, ndiponso zolinga zake zonse zinakwaniritsidwa. Mapetowa anafika mu 1914 pamene Ambuye Yehova anaika Khristu pampando wachifumu kuti akhale Mfumu yothandizana naye. Pochita zinthu moimira Atate wake, Yesu Khristu anatenga ulamuliro n’kuyamba kulamulira pakati pa anthu odana naye. Popeza iye ndi Mbewu yolonjezedwa, anapatsidwa Ufumu n’cholinga choti awononge Njoka ndi mbewu yake ndiponso kuti akonzenso dziko lapansili kukhala paradaiso wamtendere. (Genesis 3:15; Salimo 72:1, 7) Monga Mfumu yomwenso ndi Mesiya, Yesu adzakwaniritsa Mawu a Yehova ndi kusonyeza kuti Atate wake okha ndi amene ali “Mfumu yamuyaya,” ndipo akuyenera kulamulira monga Ambuye Wamkulu Koposa “mpaka muyaya.”—1 Timoteyo 1:17.
3. Ngakhale kuti Yehova Mulungu nthawi zonse wakhala Mfumu, n’chifukwa chiyani walola kuti padzikoli pakhale olamulira ena?
3 Popeza kuti Yehova Mulungu wakhala Mfumu nthawi zonse, kodi chinachitika n’chiyani kuti ‘ufumu wa dziko ukhale ufumu wa Ambuye wathu,’ Yehova? N’zoonadi, Yehova Mulungu wakhala Mfumu nthawi zonse, ndipo Asafu yemwe anali Mlevi anaimba kuti: “Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale.” Komanso, wamasalimo wina anati: “Yehova wakhala mfumu! . . . Mpando wanu wachifumu unakhazikika kalekale. Munakhalako kuyambira kalekale.” (Salimo 74:12; 93:1, 2) Komabe popeza Yehova ali ndi nzeru zakuya, iye walola kuti padziko lapansili pakhale olamulira ena. Choncho, anthu akhala ndi nthawi yokwanira yoti aone ngati nkhani imene inanenedwa m’munda wa Edeni, yoti anthu akhoza kudzilamulira okha popanda kudalira Mulungu, ili yoona kapena ayi. Ulamuliro wa anthu walephera mochititsa manyazi. Zimenezi zikugwirizana ndi mawu amene mneneri wina wa Mulungu ananena, akuti: “Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu wochokera kufumbi alibe ulamuliro wowongolera njira ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kungoyambira pamene makolo athu oyambirira anagalukira Mulungu, dziko lonse lapansili kumene kuli anthu lakhala likulamulidwa ndi Satana, “njoka yakale ija.” (Chivumbulutso 12:9; Luka 4:6) Koma tsopano nthawi inali itakwana yoti zinthu zisinthe kwambiri. Yehova pofuna kusonyeza kuti iye yekha ndi amene ali woyenera kulamulira, anayamba kulamulira dziko lapansi m’njira yatsopano, kudzera mu Ufumu wake wa Mesiya.
4. Angelo 7 atayamba kuliza malipenga awo mu 1922, n’chiyani chimene chinatsindikidwa? Fotokozani.
4 Angelo 7 atayamba kuliza malipenga awo mu 1922, Ophunzira Baibulo anachita msonkhano ku Cedar Point, m’chigawo cha Ohio. Pamsonkhanowo, J. F. Rutherford anakamba nkhani yochokera m’malemba, yamutu wakuti, “Ufumu Wakumwamba Wayandikira.” (Mateyu 4:17) Iye anamaliza nkhaniyo ndi mawu akuti: “Choncho bwererani kumunda, inu ana nonse a Mulungu wam’mwambamwamba. Nyamulani zida zanu zankhondo. Khalani ogalamuka, khalani atcheru, gwirani ntchito mwakhama ndipo khalani olimba mtima. Mukhale mboni za Ambuye zokhulupirika komanso zoona. Pitirizani kumenya nkhondo mpaka mbali iliyonse ya Babulo itawonongedwa. Lengezani uthengawu kwina kulikonse. Dziko lonse lidziwe kuti Yehova ndiye Mulungu ndipo Yesu Khristu ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Lero ndi tsiku lalikulu kuposa masiku onse. Onani, Mfumu yayamba kulamulira ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za ufumuwo. Choncho lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi ufumu wake.” Apa anatsindika kwambiri za Ufumu wa Mulungu, womwe wolamulira wake ndi Yesu Khristu, ndipo zimenezi zinalimbikitsa atumiki a Mulungu kuti ayambe kugwira ntchito yaikulu yolalikira za Ufumu. Pogwira ntchitoyi, iwo ankalengezanso ziweruzo zomwe zinkaperekedwa mngelo aliyense pa angelo 7 aja akaliza lipenga lake.
5. Mu 1928, n’chiyani chimene chinachitika pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo chomwe chinatsimikizira kulira kwa lipenga la 7?
5 Kulira kwa lipenga la mngelo wa 7 kunadziwika bwino ndi zimene zinachitika pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo umene unachitika pa July 30 mpaka August 6, 1928, mumzinda wa Detroit, ku Michigan m’dziko la United States. Nyumba zoulutsa mawu zokwana 107 zinaulutsa msonkhanowu pa nthawi imodzi, ndipo nyuzipepala ina (The New York Times) inanena kuti ‘zimenezi zinali zisanachitikepo n’kale lonse ndipo panafunika ndalama zambiri zedi kuti zitheke.’ Pamsonkhanowo panaperekedwa “Chigamulo Chakuti Tipitiriza Kutsutsana ndi Satana Ndipo Tikhalabe Kumbali ya Yehova,” ndipo anthu onse anachivomereza mosangalala. Chigamulochi chinkanena za kugonjetsedwa kwa Satana ndi gulu lake loipa pa Aramagedo, komanso kupulumutsidwa kwa anthu onse okonda chilungamo. Anthu okhulupirika ogonjera Ufumu wa Mulungu anasangalala kwambiri kulandira buku la masamba 368 lamutu wakuti Government (Boma), limene linatuluka pamsonkhanowo. Bukuli linapereka umboni womveka bwino kwambiri wotsimikizira kuti “mu 1914, Mulungu anaika pampando wachifumu Mfumu yake yodzozedwa.”
Yehova Anatenganso Mphamvu
6. Kodi Yohane anafotokoza bwanji chilengezo choti Khristu waikidwa pampando wachifumu mu Ufumu wa Mulungu?
6 Nkhani yakuti Khristu wakhala pampando wachifumu mu Ufumu wa Mulungu inali yosangalatsa kwambiri. Yohane anati: “Ndipo akulu 24 aja, amene anali atakhala pamipando yawo yachifumu pamaso pa Mulungu, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi, ndipo analambira Mulungu ndi mawu akuti: ‘Tikukuyamikani inu Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse, Inu amene mulipo ndi amene munalipo, chifukwa mwatenga mphamvu yanu yaikulu ndi kuyamba kulamulira monga mfumu.’”—Chivumbulutso 11:16, 17.
7. Kodi Yehova Mulungu anatamandidwa bwanji (a) ndi anthu omwe adakali padziko lapansi a m’gulu lophiphiritsira la akulu 24? (b) ndi anthu a m’gulu lophiphiritsira la akulu 24 omwe anaukitsidwa n’kupita kukalandira malo awo kumwamba?
7 Palembali, akulu 24 ndi amene akutamanda Yehova Mulungu, ndipo iwo akuimira abale odzozedwa a Khristu ali m’malo awo kumwamba. Kuyambira mu 1922, Akhristu odzozedwa a m’gulu la 144,000 omwe adakali padziko lapansi, akhala otanganidwa kwambiri ndi ntchito imene inayamba angelo atayamba kuliza malipenga aja. Iwo anamvetsa bwino chizindikiro chotchulidwa pa Mateyu 24:3–25:46. Komabe, ngakhale tsiku la Ambuye litangoyamba kumene, panali mboni zina zomwe ‘zinasonyeza kukhulupirika kwawo mpaka imfa,’ zimene zinali zitaukitsidwa n’kulandira malo awo kumwamba. Pa nthawiyi, mboni zimenezi n’zomwe zinkaimira gulu lonse la a 144,000, ndipo zinagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi potamanda Yehova. (Chivumbulutso 1:10; 2:10) Mboni zonsezi zimayamikira kwambiri Ambuye Wamkulu Koposa chifukwa sanachedwe kubweretsa mapeto osangalatsa a chinsinsi chake chopatulika.
8. (a) Kodi kulizidwa kwa lipenga la 7 kwakhudza bwanji mitundu ya anthu? (b) Kodi mitundu ya anthu yakwiyira ndani?
8 Koma kulizidwa kwa lipenga la 7 sikunasangalatse mitundu ya anthu. Tsopano nthawi yakwana yoti anthu amenewa aone mkwiyo wa Yehova. Yohane anafotokoza kuti: “Koma mitundu ya anthu inakwiya, ndipo mkwiyo wanu unafika. Inafikanso nthawi yoikidwiratu yakuti akufa aweruzidwe, nthawi yopereka mphoto kwa akapolo anu aneneri, ndiponso kwa oyerawo, ndi oopa dzina lanu, olemekezeka ndi onyozeka omwe. Komanso, nthawi yowononga amene akuwononga dziko lapansi.” (Chivumbulutso 11:18) Kuyambira mu 1914 mitundu ya anthu m’dzikoli yakwiyirana yokhayokha, yakwiyira Ufumu wa Mulungu, komanso yakwiyira mboni ziwiri za Yehova zija.—Chivumbulutso 11:3.
9. Kodi mayiko akhala akuwononga bwanji dziko lapansi, ndipo Mulungu wakonza zoti achite chiyani?
9 Kuyambira kale kwambiri, mayiko akhala akuwononga dziko lapansi chifukwa cha nkhondo zomwe akhala akumenya nthawi zonse komanso chifukwa cha kusayendetsa bwino zinthu. Koma kuyambira mu 1914, iwo akhala akuwononga kwambiri dzikoli modetsa nkhawa. Mwachitsanzo, zochita zawo zadyera ndiponso zakatangale zikuchititsa kuti malo ambiri akhale zipululu komanso kuti nthaka iwonongeke kwambiri. Madzi a mvula okhala ndi asidi komanso mitambo yokhala ndi mpweya wakupha zawononga madera ambiri. Zakudya zimene tikudya zikuchokera m’malo owonongeka. Mpweya umene tikupuma ndiponso madzi amene tikumwa, zaipitsidwa kwambiri. Zoipa zochokera m’mafakitale zikupitiriza kuika pangozi zamoyo za pamtunda ndiponso za m’madzi. Pa nthawi inayake, zida zanyukiliya za mayiko amphamvu kwambiri padziko lonse zinkaoneka kuti zikhoza kuwononga chilichonse padzikoli, ndi anthu omwe. Koma n’zosangalatsa kuti Yehova ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ Iye adzaweruza anthu onyada ndiponso osaopa Mulungu, omwe achititsa kuti zinthu ziipe kwambiri padzikoli. (Deuteronomo 32:5, 6; Salimo 14:1-3) Choncho, Yehova wakonza zoti tsoka lachitatu libwere n’kuwononga anthu oipawa.—Chivumbulutso 11:14.
Tsoka kwa Owononga Dziko
10. (a) Kodi tsoka lachitatu n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tikunena kuti tsoka lachitatu lidzakhala loopsa kwambiri?
10 Tsopano tsoka lachitatu latsala pang’ono kubwera. Yehova adzagwiritsa ntchito tsoka limeneli powononga anthu amene akuwononga “chopondapo mapazi” ake, chomwe ndi dziko lathu lokongolali. (Yesaya 66:1) Ufumu wa Mesiya, womwe ndi chinsinsi chopatulika cha Mulungu, ndi womwe udzabweretse tsokali. Adani a Mulungu, makamaka atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, akhala akuzunzidwa ndi masoka awiri oyambirira aja, omwe anayambitsidwa ndi mliri wa dzombe komanso wa asilikali okwera pamahatchi. Koma tsoka lachitatuli, lomwe lidzabweretsedwe ndi Ufumu wa Yehova weniweniwo, lidzakhala loopsa kwambiri. (Chivumbulutso 9:3-19) Tsokali lidzapha anthu onse owononga dzikoli komanso olamulira awo. Zimenezi zidzachitika pa Aramagedo, pamene chiweruzo cha Yehova chidzafike pachimake. Zinthu zidzachitika mogwirizana ndi zimene Danieli analosera, kuti: “M’masiku a mafumu amenewo [olamulira amene akuwononga dziko lapansi], Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” Ufumu wa Mulungu, womwe uli ngati phiri lalikulu, udzalamulira dziko lapansili lomwe lidzakonzedwenso. Komanso Ufumuwu udzasonyeza kuti Yehova yekha ndiye woyenera kulamulira, ndiponso udzabweretsa madalitso osatha kwa anthu.—Danieli 2:35, 44; Yesaya 11:9; 60:13.
11. (a) Kodi ulosiwu ukufotokoza zinthu ziti zosangalatsa zimene zinayamba kuchitika m’tsiku la Ambuye? (b) Kodi Yehova wachita chiyani posonyeza kukoma mtima kwakukulu, wachita zimenezi motani, ndipo ndani amene akupindula nazo?
11 Tsoka lachitatu likamadzachitika, zinthu zina zosiyanasiyana zosangalatsa zidzayamba kuchitika ndipo zidzapitirirabe m’nthawi yonse ya tsiku la Ambuye. Imeneyi idzakhala nthawi yakuti ‘akufa aweruzidwe, nthawi yopereka mphoto kwa akapolo a Mulungu aneneri, ndiponso kwa oyerawo, ndi oopa dzina lake.’ Zimenezi zikutanthauza kuti anthu akufa adzauka. Oyera odzozedwa amene anali atagona kale mu imfa, anaukitsidwa chakumayambiriro kwa tsiku la Ambuye. (1 Atesalonika 4:15-17) Kenako, oyera amene akhala akumwalira tsiku la Ambuye litayamba kale, amaukitsidwa nthawi yomweyo. Koma pali anthu enanso amene adzalandire madalitso. Ena mwa anthu amenewa ndi aneneri akale omwe anali akapolo a Mulungu ndiponso anthu ena onse oopa dzina la Yehova, kaya ali m’gulu la khamu lalikulu limene lidzapulumuke chisautso chachikulu kapena “akufa, olemekezeka ndi onyozeka,” omwe adzaukitsidwe mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Mfumu imene Mulungu waisankha, yomwenso ndi Mesiya, ili ndi makiyi a imfa ndi Manda. Zimenezi zikusonyeza kuti Ufumu wakewo ukutsegula njira yoti iye apereke moyo wosatha kwa anthu onse amene amayesetsa kuchita zinthu zosonyeza kuti akufuna kulandira moyowo. (Chivumbulutso 1:18; 7:9, 14; 20:12, 13; Aroma 6:22; Yohane 5:28, 29) Moyo umenewu, kaya ukhale moyo wakumwamba umene sungafe kapena moyo wosatha padziko lapansi, ndi mphatso imene Yehova waipereka mwa kukoma mtima kwake kwakukulu, ndipo aliyense amene adzailandire ayenera kuthokoza kwambiri.—Aheberi 2:9.
Taonani Likasa la Pangano Lake
12. (a) Malinga ndi Chivumbulutso 11:19, kodi Yohane anaona chiyani kumwamba? (b) Kodi likasa la pangano linkaimira chiyani, ndipo n’chiyani chinalichitikira Aisiraeli atapita ku ukapolo ku Babulo?
12 Yehova akulamulira kudzera mu Ufumu wake wa Mesiya, ndipo akulamulira anthu m’njira yabwino kwambiri. Tingatsimikizire mfundo imeneyi tikaganizira zimene Yohane anaona kenako m’masomphenyawo. Iye akutiuza kuti: “Nyumba yopatulika ya pakachisi wa Mulungu imene ili kumwamba inatsegulidwa, ndipo likasa la pangano lake linaonekera m’nyumba yake yopatulika ya pakachisi. Pamenepo kunachitika mphezi, kunamveka mawu, kunagunda mabingu, kunachita chivomezi, ndipo kunagwa matalala ambiri zedi.” (Chivumbulutso 11:19) M’buku lonse la Chivumbulutso, ndi malo okhawa pamene likasa la pangano la Mulungu likutchulidwa. Likasa linali chizindikiro chooneka kwa Aisiraeli, omwe anali anthu a Yehova, chosonyeza kuti Yehovayo anali pakati pawo. Poyamba, likasali linkasungidwa m’Malo Oyera Koposa m’chihema, ndipo kenako Solomo atamanga kachisi, linkasungidwa m’Malo Oyera Koposa m’kachisiyo. Koma pamene Aisiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo mu 607 B.C.E., Yerusalemu anawonongedwa ndipo likasa la pangano linasowa. Pa nthawiyo, anthu ochokera m’banja la Davide anasiya “kukhala pampando wachifumu wa Yehova monga mfumu.”—1 Mbiri 29:23.a
13. Kodi mfundo yakuti likasa la pangano la Mulungu linaonekera m’kachisi wakumwamba wa Mulungu ikutanthauza chiyani?
13 Tsopano, patapita zaka zoposa 2,600, Likasa linaonekanso. Koma m’masomphenya amene Yohane ankaonawa, Likasali silinali m’kachisi wapadziko lapansi koma linaoneka m’kachisi wakumwamba wa Mulungu. Kachiwirinso, Yehova anayamba kulamulira kudzera mwa mfumu ya m’banja lachifumu la Davide. Koma pa nthawiyi, Mfumuyi, yomwe ndi Khristu Yesu, inaikidwa pampando mu Yerusalemu wakumwamba, ndipo ikupereka ziweruzo za Yehova kuchokera pa malo okwezeka amenewa. (Aheberi 12:22) Tiphunzira mfundo zochuluka zokhudza nkhani imeneyi m’machaputala akutsogoloku m’buku la Chivumbulutso.
14, 15. (a) Kodi ndani yekha yemwe ankaona likasa la pangano ku Yerusalemu, ndipo n’chifukwa chiyani zinali choncho? (b) M’nyumba yopatulika ya pakachisi wakumwamba wa Mulungu, ndani amene amaona likasa la pangano la Yehova?
14 Kale ku Yerusalemu, Aisiraeli onse ngakhalenso ansembe amene ankatumikira pakachisi sankaona Likasa, chifukwa linkakhala m’Malo Oyera Koposa omwe ankatchingidwa ndi nsalu yomwe inali pakati pa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa. (Numeri 4:20; Aheberi 9:2, 3) Mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankaona Likasali akalowa m’Malo Oyera Koposa kamodzi pa chaka, pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Koma pamene nyumba yopatulika ya pakachisi wakumwamba inatsegulidwa, likasa lophiphiritsa silinangoonekera kwa Yesu Khristu yekha, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe wa Yehova. Linaonekeranso kwa ansembe ake aang’ono, omwe ndi a 144,000, ndipo Yohane ali m’gulu limeneli.
15 Anthu amene anaukitsidwa kale kupita kumwamba amaona likasa lophiphiritsali pafupi, chifukwa iwo analandira kale malo awo monga anthu amene ali m’gulu la akulu 24 amene azungulira mpando wachifumu wa Yehova. Ndipo Akhristu odzozedwa omwe ali padziko lapansili athandizidwa ndi mzimu wa Yehova kuti azindikire kuti Yehovayo ali m’kachisi wake wauzimu. Padzikoli pakhalanso pakuchitika zizindikiro zosiyanasiyana zimene zathandiza anthu onse kudziwa zinthu zosangalatsa zimenezi. Mwachitsanzo, m’masomphenya a Yohanewa mukutchulidwanso mphezi, mawu, mabingu, chivomezi ndiponso matalala. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 8:5.) Kodi zizindikiro zimenezi zikuimira chiyani?
16. Kodi zinthu monga mphezi, mawu, mabingu, chivomezi ndiponso matalala, zakhala zikuchitika motani?
16 Kuyambira mu 1914 zipembedzo zochuluka zakhala zikugwedezeka kwambiri. Koma n’zosangalatsa kuti pa nthawi imene “chivomezi” chimenechi chakhala chikuchitika, pakhala pakumvekanso mawu a anthu odzipereka onena za uthenga womveka bwino wa Ufumu wa Mulungu umene unakhazikitsidwa. Machenjezo ochokera m’Baibulo, omveka ngati ‘kugunda kwa mabingu’ aperekedwa. Mofanana ndi kuwala kwa mphezi, kuwala kwauzimu kwathandiza atumiki a Mulungu kuti amvetse bwino mfundo za ulosi wa m’Mawu a Mulungu ndi kuzifalitsa. Uthenga wokhudza chiweruzo choopsa cha Yehova, womwe uli wopweteka ngati “matalala,” wakhala ukuperekedwa kwa Matchalitchi Achikhristu ndiponso zipembedzo zonse zonyenga. Zonsezi zinayenera kuchititsa anthu kuyamba kumvetsera uthengawu. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri, mofanana ndi anthu a ku Yerusalemu m’nthawi ya Yesu, alephera kuzindikira kuti zizindikiro zotchulidwa m’buku la Chivumbulutso zimenezi, zikukwaniritsidwa.—Luka 19:41-44.
17, 18. (a) Kodi Akhristu odzipereka akhala ndi udindo wotani kuyambira pamene angelo 7 aja anayamba kuliza malipenga awo? (b) Kodi Akhristu akuchita zotani pokwaniritsa udindo wawo?
17 Angelo 7 aja akupitiriza kuliza malipenga awo, kusonyeza kuti padziko lapansi pakuchitika zinthu zikuluzikulu zosaiwalika. Akhristu odzipereka ali ndi udindo waukulu woti apitirize kulengeza mauthenga amenewa padziko lonse. Akhristuwa akugwira ntchito imeneyi mwakhama kwambiri. Mfundo imeneyi ikuonekera bwino tikaona maola amene anathera pa ntchito yolalikira pa zaka 25 zapitazi. Mu 1986, iwo analalikira kwa maola 680,837,042, ndipo mu 2010, iwo analalikira kwa maola 1,604,764,248, omwe anali oposa kuwirikiza kawiri maola a mu 1986 aja. Zoonadi, “chinsinsi chopatulika cha Mulungu . . . malinga ndi uthenga wabwino” chikulalikidwa mpaka “kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”—Chivumbulutso 10:7; Aroma 10:18.
18 Tsopano tikambirana masomphenya ena pamene zolinga za Ufumu wa Mulungu zikupitiriza kukwaniritsidwa.
[Mawu a M’munsi]
a Munthu wina wachiroma wolemba mbiri dzina lake Tacitus analemba kuti adani atalanda mzinda wa Yerusalemu mu 63 B.C.E., Cneius Pompeius analowa m’nyumba yopatulika ya pakachisi koma sanapezemo chilichonse. M’kachisimo munalibe likasa la pangano.—Tacitus History, 5.9.
[Bokosi patsamba 173]
Mfundo Zikuluzikulu za M’mauthenga a Ziweruzo za Yehova Omveka Ngati Kulira kwa Malipenga
1. 1922 Cedar Point, Ohio: Pamsonkhanowu atsogoleri a zipembedzo, a ndale komanso a mabizinezi akuluakulu, omwe ali m’Mayiko Achikhristu anapemphedwa kuti avomereze kuti alepheradi kubweretsa mtendere ndi kuthandiza anthu kuti azikhala mosangalala. Msonkhanowu unathandiza anthu kuona kuti Ufumu wa Mesiya wokha ndi umene ungathetse mavuto awo.
2. 1923 Los Angeles, California: Nkhani ya onse yakuti, “Mitundu Yonse ya Anthu Tsopano Ikupita ku Aramagedo, Koma Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa,” inalimbikitsa anthu okonda mtendere okhala ngati nkhosa kuti atuluke m’nyanja yakupha ya mtundu wa anthu.
3. 1924 Columbus, Ohio: Atsogoleri a zipembedzo anazengedwa mlandu chifukwa chodzikweza komanso chifukwa chokana kulalikira za Ufumu wa Mesiya. Akhristu oona ayenera kulalikira za chilango cha Mulungu ndiponso kulimbikitsa anthu amene akumva chisoni ndi zimene zikuchitika m’dzikoli.
4. 1925 Indianapolis, Indiana: Panakambidwa nkhani ya uthenga wopatsa chiyembekezo, yomwe inafotokoza kusiyana kwa mdima wauzimu womwe uli m’Matchalitchi Achikhristu ndi kuwala kwa lonjezo loti Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu kuti akhale ndi mtendere, moyo wosasowa kanthu, thanzi labwino, moyo, ufulu ndiponso chimwemwe chosatha.
5. 1926 London, England: Panakambidwa nkhani imene inali ngati mliri wa dzombe womwe unagwera Matchalitchi Achikhristu ndi atsogoleri ake, n’kuwaulula kuti amakana Ufumu wa Mulungu. Nkhaniyo inafotokozanso kuti boma lakumwamba lakhazikitsidwa.
6. 1927 Toronto, Canada: Anthu anapemphedwa kuchoka m’Matchalitchi Achikhristu n’kudzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova Mulungu, Mfumu yake komanso Ufumu wake. Pempholi linafika patali ngati kuti laperekedwa ndi asilikali okwera pamahatchi.
7. 1928 Detroit, Michigan: Panaperekedwa chigamulo cholimbikitsa anthu kuti apitirize kutsutsana ndi Satana n’kukhalabe kumbali ya Yehova. Chigamulochi chinafotokoza mosapita m’mbali kuti Mfumu yodzozedwa imene Mulungu waisankha, yomwe inaikidwa pampando wachifumu mu 1914, idzawononga gulu loipa la Satana ndi kumasula mtundu wa anthu.
[Bokosi patsamba 175]
Kuwononga Dziko
“Pa masekondi atatu alionse, malo aakulu ngati bwalo la mpira wamiyendo a nkhalango yachilengedwe, amawonongedwa. . . . Kutha kwa nkhalango zachilengedwe kukuchititsa kuti zomera ndi nyama zambirimbiri zithe.”—Illustrated Atlas of the World (Rand McNally).
“Pa zaka 200 zimene anthu akhala m’madera ozungulira [nyanja zikuluzikulu za ku America], nyanjazi zakhala malo aakulu padziko lonse otayirako nyansi za m’chimbudzi.”—The Globe and Mail (Canada).
Mu April 1986, makina opangira magetsi pogwiritsa ntchito mphamvu za nyukiliya anaphulika n’kuyaka moto ku Chernobyl, U.S.S.R. Nyuzipepala ina inati “ngozi yokhudza makina a nyukiliya imeneyi ndi imene inali yoopsa kwambiri . . . chiphulikireni mabomba a nyukiliya ku Hiroshima ndi ku Nagasaki.” Makinawa ataphulika, panatuluka “mpweya wakupha wosatherapo umene unawononga kwambiri mpweya wachilengedwe, nthaka ndi madzi, kuposa mpweya wonse wakupha umene wakhala ukutuluka poyesa zida za nyukiliya ndiponso pakaphulika mabomba a nyukiliya.”—JAMA; The New York Times.
Ku Minamata, m’dziko la Japan, mankhwala oopsa ochokera pafakitale inayake ankathiridwa m’nyanja. Anthu amene ankadya nsomba zomwe zinakhudzidwa ndi mankhwalawa, anadwala matenda otchedwa Minamata, omwe ndi “matenda oopsa kwambiri osachiritsika okhudza ubongo. . . . Pofika [mu 1985] anthu 2,578 m’dziko lonse la Japan ankadziwika kuti anadwala matendawa.”—International Journal of Epidemiology.
[Bokosi patsamba 176]
Mauthenga amphamvu otchulidwa pa Chivumbulutso 11:15-19, angokhala kalambulabwalo chabe wa masomphenya amene ali kutsogoloku. M’chaputala 12 muli mfundo zimene zikufotokoza mwatsatanetsatane uthenga wofunika kwambiri wa pa Chivumbulutso 11:15 ndi 17. Chaputala 13 chikutipatsa chithunzi chotithandiza kumvetsa bwino lemba la Chivumbulutso 11:18, chifukwa chikufotokoza za chiyambi cha gulu la ndale la Satana limene likuwononga dziko lapansili. Chaputalachi chikufotokozanso zochita za gululi komanso mmene lakulira. Chaputala 14 ndi 15 chikufotokoza mwatsatanetsatane ziweruzo zina za Ufumu, zomwe n’zogwirizana ndi kulira kwa lipenga la 7 ndiponso tsoka lachitatu.
[Zithunzi patsamba 174]
Yehova ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi’