Yafika Nthaŵi ya Chiweruzo cha Mulungu
“Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.”—CHIBVUMBULUTSO 14:7.
1. Nchiyani chomwe mitu yotsegulira ya Chibvumbulutso imaphatikiza?
BUKHU la Chibvumbulutso liri ndi maulosi ochititsa nthumazi omwe ali ndi kukwaniritsidwa kwawo m’tsiku lathu. Nkhani yapitayo yalingalira ena a iwo, kuphatikizapo kutsegulidwa kwa zosindikiza zophiphiritsira zisanu ndi chimodzi. Zosindikiza zotsegulidwa zimenezi zimavumbula kukwera kosakaza kwa apakavalo anayi a chibvumbulutso mu “masiku otsiriza” awa. (2 Timoteo 3:1; Chibvumbulutso 6:1-8) Iwo alankhulanso ponena za awo amene adzalamulira ndi Kristu kumwamba ndi awo amene adzapulumuka “chisautso chachikulu” kudzakhala pa dziko lapansi kosatha. Zosindikiza zisanu ndi chimodzi zasonyeza kuti “nthaŵi yoikidwiratu” ya Mulungu ya kupereka chiweruzo “yayandikira.”—Chibvumbulutso 1:3; 7:4, 9-17.
2. Ndimotani mmene malipenga ophiphiritsira asanu ndi aŵiri a Chibvumbulutso mutu 8 ayenera kugwiritsiridwa ntchito?
2 Koma pali chosindikiza chimodzi chowonjezereka, chachisanu ndi chiŵiri. Chibvumbulutso 8:2 chimatiwuza ife chimene chikuvumbulidwa pamene chatsegulidwa kuti: “Ndipo ndinawona angelo asanu ndi aŵiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi aŵiri.” Versi 6 likuti: “Ndipo angelo asanu ndi aŵiri akukhala nawo malipenga [asanu ndi aŵiri] anadzikonzera kuti awombe.” M’nthaŵi ya Baibulo, malipenga ankagwiritsiredwa ntchito kupereka chizindikiro cha zochitika zofunika koposa. M’njira yofananayo, kulira kwa lipenga kusanu ndi kuŵiri kumeneku kuitanira chisamaliro ku kufunika kwa nkhani za kuchita ndi moyo ndi imfa m’nthaŵi yathu. Ndipo pamene angelowa akuyimba malipenga awo, Mboni za umunthu pa dziko lapansi zimatsatira mofananamo kufalitsa mbiri yofunika kwambiri yokwezedwa ndi kulira kwa lipenga lirilonse.
Chimene Kulira kwa Lipenga Kumatanthauza
3. Nchiyani chomwe chiri tanthauzo la kulira kwa malipenga kusanu ndi kuŵiri?
3 Kulira kwa lipenga kumeneko kumatikumbutsa ife za miliri imene Yehova anaitsanulira pa Igupto wakale. Miliri imeneyo inali zisonyezero za chiweruzo cha Yehova pa mphamvu ya dziko yoyamba imeneyo ndi chipembedzo chake chonyenga, koma inatsegulanso njira ya chipulumutso kwa anthu a Mulungu. Mofananamo, kulira kwa lipenga la Chibvumbulutso kuli miliri yamakono, nthaŵi ino pa dziko lonse la Satana ndi chipembedzo chake chonyenga. Iyo siiri, ngakhale ndi tero, miliri yeniyeni koma mauthenga opereka mliri a ziweruzo za Yehova. Iwo akutchulanso njira ya kupulumukira kaamba ka anthu a Mulungu.
4. Ndimotani mmene kulira kwa malipenga kusanu ndi kuŵiri kwapezera kukwaniritsidwa kwawo m’nthaŵi yathu?
4 M’chigwirizano ndi kulira kwa lipenga kusanu ndi kuŵiri kumeneko, zigamulo zolimbana ndi dziko la Satana zinasonyezedwa pa misonkhano yapadera ya pa chaka isanu ndi iŵiri ya anthu a Yehova kuyambira mu 1922 mpaka 1928. Mazana a mamiliyoni a makope a zigamulozo anagawiridwa. Ngakhale kuli tero, kuwombedwa kwa mauthenga otentha amenewa sikunali kotsekeredwa kokha ku zaka zimenezo, koma kwakhala kopitirizabe kupyola masiku otsiriza. Ndipo lerolino kulengezedwa kwawo kuli kwamphamvu mokulira kuposa ndi kalelonse, popeza kuti mamiliyoni a “khamu lalikulu” awonjezera mawu awo ku gulu lochepa la odzozedwa limene linayamba kulalikira kumapeto kwa Nkhondo ya Dziko ya I. (Chibvumbulutso 7:9) Chaka chirichonse tsopano, ndi mphamvu yomawonjezereka ndi ziŵerengero, mamiliyoni amenewa akulengeza kuti dziko la Satana lagwetsedwa kotheratu.
5. Ndani yemwe ali “magawo atatu” a dziko omwe aweruzidwa moipa choyamba, ndipo nchifukwa ninji?
5 Pa Chibvumbulutso 8:6-12, malipenga anayi oyambirira akuyimba. Matalala, moto, ndi mwazi zikutsanulidwa, kutulukapo mu kusakaza kwa “magawo atatu” a dziko. Nchifukwa ninji “magawo atatu” otchulidwa monga mbali yolakwa ya dziko imene imabwera kaamba ka chiweruzo choipa choyambirira? Chifukwa pamene kuli kwakuti dongosolo lonse la Satana liri lonyansa kwa Mulungu, mbali imodzi iri yokulira motero. Mbali iti? Mbali imene inatenga dzina la Kristu pa ilo lokha—Chikristu cha Dziko. Ndipo pamene mauthenga a chiweruzo cha Mulungu anabwera motsutsana ndi iye pamapeto pa Nkhondo ya Dziko ya I, malo a Chikristu cha Dziko nthaŵi imeneyo anakupatira chifupifupi magawo atatu a mtundu wa anthu.
6. Nchifukwa ninji Yehova wasiira Chikristu cha Dziko ku chiwonongeko?
6 Chipembedzo cha Chikristu cha Dziko chiri chipatso cha mpatuko wa zaka 1,900 kuchoka ku Chikristu chowona chimene Yesu ndi ophunzira ake ananeneratu. (Mateyu 13:24-30; Machitidwe 20:29, 30) Atsogoleri a chipembedzo cha Chikristu cha Dziko amadziimira iwo eni monga aphunzitsi a Chikristu, koma ziphunzitso zochotsedwa kotheratu kuchoka ku chowonadi cha Baibulo, ndipo kachitidwe kawo kowononga mopitiriza kabweretsa chitonzo ku dzina la Mulungu. Liwongo lawo la mwazi chifukwa chochirikiza nkhondo za zana lino la 20 lavumbulutsidwa. Chikristu cha Dziko chiri kotheratu mbali ya dongosolo la kachitidwe ka zinthu la Satana. Chotero, iye akulandira mauthenga amphamvu, odzetsa mliri kuchokera kwa Yehova omwe akusonyeza kuti iye sali woyeneretsedwa kudzalandira chiyanjo chaumulungu mwanjira iriyonse. Yehova wasiyira nyumba ya Chikristu cha Dziko ku chiwonongeko motsimikizirika monga mmene anachitira ku nyumba ya Chiyuda ya zana loyamba!—Mateyu 23:38.
Kubwezeretsedwa kaamba ka Kulalikira kwa Dziko Lonse
7, 8. (a) Mu Chibvumbulutso mutu 9, nchiyani chomwe kulira kwa lipenga kwachisanu kumavumbula? (b) Ndani yemwe dzombe limachitira chithunzi?
7 Pa Chibvumbulutso 9:1 mngelo wachisanu akuliza lipenga lake, ndipo masomphenyawo akuvumbula nyenyezi yomwe ikubwera pa dziko lapansi. Nyenyezi imeneyi iri ndi mfungulo m’dzanja lake. Ndi iyo akutsegula dzenje mu limene gulu la dzombe linabindikiritsidwa. Nyenyeziyo iri Mfumu ya kumwamba ya Yehova yoikidwa kumene, Yesu Kristu. Dzombelo liri atumiki a Mulungu, omwe anazunzidwa ndipo mwachiwonekere kuikidwa kunja pamene nduna zawo zowatsogolera zinaikidwa m’ndende mu 1918. Koma Kristu, tsopano mu mphamvu ya Ufumu m’mwamba, akuwamasula iwo kotero kuti angayambenso kulalikira kwawo kwa dziko lonse poyera, zochulukira ku kunyazitsidwa kwa atsogoleri a chipembedzo, omwe anakonzekera kuthetsa ntchito yawo.—Mateyu 24:14.
8 Dzombelo likulongosoledwa mwanjira iyi pa Chibvumbulutso 9:7: “Ndipo mawonekedwe a dzombelo anafanana ndi akavalo okonzeka kukachita nkhondo; ndi pamitu pawo ngati akorona onga agolidi, ndi pankhope pawo ngati pankhope pa anthu.” Versi 10 liwonjezera kuti: “Ndipo liri nayo michira yofanana ndi ya chinkhanira ndi mbola.” Dzombe limeneli likuchitira bwino chithunzi otsalira obwezeretsedwanso olowa m’malo a Ufumu kupitanso mu nkhondo yauzimu kuyambira 1919 kupita mtsogolo. Ndi mphamvu yokonzedwanso, iwo analengeza mauthenga a ziweruzo zoluma za Mulungu, makamaka motsutsana ndi Chikristu cha Dziko chosakaza.
9, 10. (a) Nchiyani chomwe kulira kwa lipenga kwa chisanu ndi chimodzi kumavumbula? (b) Ndani omwe akuphatikizidwa mu akavalo amphamvu zikwi makumi?
9 Kenaka, mngelo wachisanu ndi chimodzi akuwomba lipenga lake. (Chibvumbulutso 9:13) Uku kumavumbula kutulutsidwa kwa gulu lankhondo la pa kavalo. Versi 16 likunena kuti iwo anafikira chiŵerengero cha “zikwi makumi aŵiri zochulukitsa zikwi khumi,” chomwe chimafika ku 200 miliyoni! Ndipo iwo akulongosoledwa mu versi 17 ndi 19 motsatiramu: “Ndi mitu ya akavalo ngati mitu ya mikango; ndipo mkamwa mwawo mutuluka moto ndi utsi ndi sulfure. . . . Michira yawo ifanana ndi njoka.” Magulu ankhondo amenewa akupita patsogolo mwamphamvu pansi pa chitsogozo cha Mfumu, Kristu Yesu. Ndipo iwo ali chiwonetsero chochititsa mantha chotani nanga!
10 Kodi nchiyani chimene akavalo amphamvu amenewa akuimira? Popeza kuti iwo akufika m’chiŵerengero cha mamiliyoni, iwo sangakhale kokha otsalira odzozedwa, kwa amene pa nthaŵi ino pali kokha chifupifupi 8,800 pa dziko lapansi. Zikwi makumi za akavalo zimenezi ziyenera kuphatikizapo “khamu lalikulu” la Chibvumbulutso mutu 7, awo amene ali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi. Mu Baibulo, liwu lakuti “zikwi khumi” kaŵirikaŵiri limalozera ku chiŵerengero chachikulu, chopanda malire. Chotero, akavalo ophiphiritsira amenewa amaphatikiza osati kokha chiŵerengero chomazimiririka cha odzozedwa komanso mamiliyoni omakulakulabe ndi amphamvu a “khamu lalikulu” lomalengeza la “nkhosa zina” omwe akupitiriza ndi ntchito yapoyera yomwe inayambidwa ndi otsalira odzozedwa onga dzombe.—Yohane 10:16.
11. Nchifukwa ninji chikunenedwa kuti “mphamvu ya akavalo iri mkamwa mwawo,” ndipo ndimotani mmene iwo ‘akuipisyira ndi michira yawo’?
11 Chibvumbulutso 9:19 chimalongosola kuti: “Mphamvu ya akavalo iri mkamwa mwawo,” ndipo “ndi [michira yawo] aipsya nayo.” Ndi mwanjira yotani mmene mphamvu iliri mkamwa mwawo? M’chakuti kwa zaka makumi, kupyolera mu Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki ndi misonkhano ina, atumiki a Mulungu aphunzitsidwa mmene angalalikire uthenga wake wa chiweruzo mwa ulamuliro ndi mawu a pakamwa. Ndipo ndi mwa njira yotani mmene iwo amaipsyira ndi michira yawo? M’chakuti iwo agawira zofalitsidwa zozikidwa m’Baibulo mabiliyoni angapo dziko lonse motero, akumasiya kumbuyo uthenga woluma molimbana ndi dziko la Satana. Kwa olimbana nawo, magulu ankhondo apakavalo amenewa ndithudi awoneka monga zikwi makumi kuchulukitsa zikwi makumi.
12. Nchiyani chomwe dzombe lophiphiritsira ndi akavalo ayenera kupitiriza kuchita, ndipo ndi chotulukapo chotani?
12 Chotero, dzombe ndi akavalo ophiphiritsirawo ayenera kulengeza mauthenga a chiweruzo cha Mulungu momvekera ndipo mofuula pamene tsiku lake lakubwezera likuyandikira. Kwa awo owona mtima, mauthenga amenewo ali mbiri yabwino pa dziko lapansi. Koma kwa awo omwe amakonda dziko la Satana, ali mbiri yoipa, popeza kuti imatanthauza kuti dziko lawo posachedwapa lidzawonongedwa.
13. “Tsoka lachitatu” logwirizana ndi kulira kwa lipenga kwa chisanu ndi chiŵiri limaphatikizapo chiyani, ndipo ndimotani mmene ilo liriri “tsoka”?
13 Dzombe lopatsa mliri ndi asilikari apakavalo akulongosoledwa kukhala yoyambirira ndi yachiŵiri ya “matsoka” atatu ogamulidwa mwaumulungu. (Chibvumbulutso 9:12; 11:14) Kodi nchiyani chomwe chiri “tsoka lachitatu”? Pa Chibvumbulutso 10:7 tikuwuzidwa kuti: “Komatu m’masiku a mawu a mngelo wachisanu ndi chiŵiri, . . . pamenepo padzatsirizika chinsinsi [chopatulika] cha Mulungu, monga analalikira kwa akapolo ake aneneri.” Chinsinsi chopatulika chimenechi chimaphatikizapo “mbewu” yolonjezedwa choyamba mu Edeni. (Genesis 3:15) “Mbewu” imeneyo choyambirira iri Yesu komanso imaphatikizapo oyanjana nawo ake odzozedwa omwe adzalamulira ndi iye kumwamba. Chotero chinsinsi chopatulika chimagwirizana ndi Ufumu wa kumwamba wa Mulungu. Ufumu umenewu udzabweretsa “tsoka” lachitatu lolinganizidwa mwaumulungu, popeza udzapereka ziweruzo za Mulungu molimbana ndi dziko la Satana kumathedwe.
Ufumu Wakhazikitsidwa
14. Nchiyani chomwe kulira kwa lipenga kwa chisanu ndi chiŵiri kwa Chibvumbulutso 11:15 kunalengeza?
14 Kenaka zachitika! Chibvumbulutso 11:15 chikunena kuti: “Ndipo mngelo wachisanu ndi chiŵiri anawomba [lipenga lake], ndipo panakhala mawu akulu m’Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova], ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” Inde, chalangezedwa kuti Ufumu wa Mulungu mwa Kristu unakhazikitsidwa m’mwamba m’chaka cha 1914. Ndipo pamene otsalira anabwezeretsedwanso pambuyo pa Nkhondo ya Dziko ya I, iwo anabweretsa mbiri imeneyi kutsogolo.
15. Mu 1922, nchochitika chotani chomwe chinayambitsa kachitidwe katsopano m’kulalikira Ufumu?
15 Pa msonkhano wa mu 1922 wa atumiki a Yehova mu Cedar Point, Ohio, U.S.A., zikwi zopezekapo zinamva chilengezo chochititsa nthumanzi chakuti: “Iri ndi tsiku la masiku onse. Tawonani, Mfumu yayamba kulamulira! Inu muli nthumwi zake zofalitsa. Chotero bukitsani, bukitsani, bukitsani, Mfumu ndi ufumu wake.” Chimenecho chinayambitsa ntchito yaikulu ya kulalikira Ufumu poyera yomwe yaphatikizapo ziweruzo zolengezedwa ndi owomba malipenga aungelo asanu ndi aŵiri. Lerolino, chifupifupi mamiliyoni atatu ndi theka a atumiki a Yehova m’mipingo yoposa 57,000 kuzungulira dziko lonse akuphatikizidwa mu kulalikira Ufumu pa dziko lonse. Zikwi makumi ndithudi!
16. Mu Chibvumbulutso mutu 12, ndi zowunikira zowonjezereka ziti zophatikizapo kumwamba ndi dziko lapansi zomwe zinavumbulidwa ndi kulira kwa lipenga kwa chisanu ndi chiŵiri?
16 Koma mngelo wachisanu ndi chiŵiri ali ndi zowonjezereka zovumbula. Chibvumbulutso 12:7 chimanena kuti kenaka “munali nkhondo m’mwamba.” Versi 9 likutipatsa ife chotulukapo chimenechi cha kachitidwe ka Kristu Mfumu: “Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” Versi 12 likuwonjezera kuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo!” Inde, miyamba inayeretsedwa kuchotsa chisonkhezero cha Satana, chopangitsa cha chisangalalo chachikulu pakati pa angelo okhulupirika. Koma kodi chimatanthauza chiyani kaamba ka mtundu wa anthu? Versi limodzimodzilo likuyankha kuti: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”
17. Nchifukwa ninji kulongosola boma la dziko kukhala “chirombo” mu Chibvumbulutso mutu 13 kuli koyenerera?
17 Chibvumbulutso 12:3 chimalongosola Satana monga ‘chinjoka chachikulu, chokhala nayo mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi,’ wowononga wowopsya monga chinyama. Ichi chimasonyeza kuti iye ali mpangi wa “chirombo” cha ndale zadziko cha pa dziko lapansi cholongosoledwa mu mutu 13, maversi 1 ndi 2. Chirombo chimenecho chirinso ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi, m’kutsanzira Satana. Versi 2 likunena kuti: “Ndipo chinjoka [Satana] [anapereka kwa chirombo, NW] mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.” Kuyerekeza maboma a ndale zadziko monga chirombo kuli ndithudi koyenerera, popeza mu kokha zana lino la 20 anthu, oposa mamiliyoni zana limodzi aphedwa m’nkhondo za mitundu.
18. Nchiyani chomwe chiri chirombo cha nyanga ziŵiri cha Chibvumbulutso 13:11, ndipo ndimotani mmene kachitidwe kake kamathandizira kuchizindikira icho?
18 Chochitika chotsatira mu Chibvumbulutso 13 chimavumbula, monga mmene versi 11 likunenera, “chirombo china chirikutuluka pansi; ndipo chinali nazo nyanga ziŵiri ngati za mwana wa nkhosa, ndipo chinalankhula ngati chinjoka.” Chirombo cha nyanga ziŵiri chimenechi chiri kugwirizana kwa ndale zadziko kwa Anglo-America. Icho chiri chonga mwana wa nkhosa mwakuti chimadzisonyeza kukhala chosawukira, mtundu wokondedwa koposa wa boma. Koma chilankhula ngati chinjoka, monga Satana, ndipo chikutchedwa “chirombo china” chifukwa chakuti machitidwe ake olamulira ali onga chirombo. Icho chimadidikiza kuwopsyeza ndipo ngakhale kugwiritsira ntchito chiwawa pamene mtundu wake wa ulamuliro sulandiridwa. Icho sichimalimbikitsa, kugonjera ku Ufumu wa Mulungu, koma, m’malomwake, kutumikira monga chida cha dziko la Satana. Chimenecho ndicho chifukwa chake versi 14 likunena kuti: “Chisokeretsa iwo akukhala pa dziko.”
19, 20. (a) Nchiyani chomwe umphumphu wa atumiki a Yehova umasonyeza? (b) Ndimotani mmene timadziŵira kuti otsalira odzozedwa motsimikizirika adzapambana pa dziko la Satana?
19 Dziko iri lokhala pansi pa ulamuliro wa Satana liri malo ovuta kukhalamo kwa awo amene, m’chigwirizano ndi lamulo la Yesu kwa Akristu owona, sali mbali ya ilo. (Yohane 17:16) Chotero, ndi chisonyezero chowunikira cha mphamvu ya Yehova ndi madalitso kuti atumiki ake kuzungulira dziko lapansi lerolino akusunga umphumphu mogwirizana kupitirizabe kukweza Yehova ndi njira zake zolungama. Iwo amachita chimenechi moyang’anizana ndi chitsutso chokulira, chizunzo, ndipo ngakhale imfa.
20 Otsalira odzozedwa mwachindunji akhala chandamale cha Satana chifukwa chakuti iwo adzakhala olamulira anzake a Kristu. Koma Chibvumbulutso mutu 14 chimasonyeza kuti chiŵerengero chathunthu cha iwo, 144,000, asonkhanitsidwa mwachipambano ndi Kristu mu mphamvu ya Ufumu. Iwo amamatira mwa umphumphu kwa Mbuye wawo, popeza monga mmene versi 4 lanenera: “Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako”—kuchita ichi mosasamala kanthu za chizunzo cha nkhalwe chimene Satana wabweretsa pa iwo.
Kulandira Ziweruzo za Mulungu Choyamba
21, 22. (a) Ndi zilengezo zotani zimene angelo akupanga pa Chibvumbulutso 14:7, 8? (b) Nchifukwa ninji mngelo akulengeza kugwa kwa Babulo wa chipembedzo pamene iye adakalipo?
21 Pa Chibvumbulutso 14:7 mngelo akufuula kuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.” Ndani amene amalandira chiweruzo cha mphamvu cha Mulungu choyamba? Versi 8 likuyankha kuti: “Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, Wagwa, Babulo Wamkulu amene anamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake!” Pano kwa nthaŵi yoyamba, koma osati yotsirizira, Chibvumbulutso chilankhula za “Babulo Wamkulu,” ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga.
22 Popeza kuti chipembedzo chidakapangabe chisonkhezero m’mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi, nchifukwa ninji mngelo akulengeza kuti Babulo Wamkulu wagwa kale? Chabwino, nchiyani chimene chinatulukapo mu 539 B.C.E. pamene Babulo wakale anagwa koma anali asanawonongedwe kotheratu? Nkulekeranji, popeza kuti atumiki a Yehova omangidwa ukapolo anabwerera ku dziko la kwawo zaka ziŵiri pambuyo pake ndi kubwezeretsa kulambira kowona! M’njira yofananayo, kubwezeretsedwa kwa atumiki a Mulungu ku ntchito yoyambitsidwanso ndi kupita patsogolo kwauzimu komwe kunayamba mu 1919 kuli umboni wowonekera wakuti pa nthaŵiyo, mu 1919, Babulo Wamkulu anakumanizana ndi kugwa kwadzidzidzi monga momwe kwawondedwa ndi Yehova. Iye pamenepo anamuweruzira ku kuchotsedwa kotheratu kwa kutsogolo.
23. (a) Ndimotani mmene njira ikupangidwira kaamba ka kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu? (b) Ndi maulosi owonjezereka otani omwe adzalingaliridwa m’kope lotsatira la Nsanja ya Olonda?
23 Monga chotsogolera ku kuwonongedwa kwake kotheratu komayandikira, Babulo wamakono waloŵa kale m’mavuto ozama. Kuipitsa kwake, chisembwere chokulira, kusawona mtima, ndi kuloŵerera m’ndale zadziko zavumbulidwa kulikonse. Mu mbali zambiri za Europe, anthu oŵerengeka amapita ku tchalitchi. M’maiko ambiri a chisosholizimu, chipembedzo chimalingaliridwa kukhala “mankhwala othetsa ululu a anthu.” Ndiponso, Babulo wamakono amanyazitsidwa m’maso mwa onse okonda Mawu a Mulungu a chowonadi. Chotero iye tsopano akuyembekezera, monga mmene kunaliri, pa mzera wa imfa kaamba ka kuphedwa kwake koyenerera. Inde, “nthaŵi yoikika iri pafupi” kaamba ka zochitika zogwedeza dziko! Ndipo m’kope lotsatira la Nsanja ya Olonda, nkhani ziŵiri zophunziridwa zidzakambitsirana maulosi a mu Chibvumbulutso onena za kuwonongedwa komadza kwa “mkazi wachigololo” wa chipembedzo, limodzinso ndi dongosolo lonse la kachitidwe ka zinthu la Satana.
Ndimotani Mmene Mukayankhira?
◻ Nchiyani chomwe kulira kwa malipenga kusanu ndi kuŵiri komwe kumayambika pa Chibvumbulutso mutu 8 kumatanthauza kaamba ka tsiku lathu?
◻ Nchifukwa ninji Chikristu cha Dziko chikubwera kaamba ka chiweruzo choipa choyamba?
◻ Ndimotani mmene ntchito yolalikira ya otsalira odzozedwa ndi “khamu lalikulu” yalongosoledwera mu Chibvumbulutso mutu 9?
◻ Nchiyani chimene chilengezo cha pa Chibvumbulutso 11:15 chimatanthauza kaamba ka kumwamba ndi dziko lapansi?
◻ Monga kwalongosoledwa pa Chibvumbulutso 14:8, ndimotani mmene Babulo wa chipembedzo anagwera mu 1919, ndipo chimenechi chitanthauzanji kaamba ka iye?